14.12.2012 Views

Mankhwala a HIV ndi EDZI - PIH Model Online - Partners in Health

Mankhwala a HIV ndi EDZI - PIH Model Online - Partners in Health

Mankhwala a HIV ndi EDZI - PIH Model Online - Partners in Health

SHOW MORE
SHOW LESS

Create successful ePaper yourself

Turn your PDF publications into a flip-book with our unique Google optimized e-Paper software.

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

Chiyambi

Mankhwala a ma-ARV amaletsa kachirombo ka HIV kuti kasaswane ndikuononga

chitetezo cha m’thupi. Mankhwalawa samachiza EDZI, choncho munthu wodwalayo

afunika kuwamwa moyo wake onse. Mankhwalawa amafunika kuwamwa panthawi

yomweyomweyo tsiku lililonse komanso kutsatira malangizo ake. Azaumoyo a

m’mudzi akamvetsa bwino za mankhwala a HIV/EDZI ndiye kuti sikudzakhala kovuta

kuwalimbikitsa odwala kuti apitirize kumwa mankhwala ndi kupewa makhalidwe

omwe angaike moyo wawo pachiswe. Mutu uno ufotokoza za ma-ARV ndi nkhani

zokhudza kusalekeza kumwa mankhwalawa koma kutsata ndondomeko zake. Mfundo

zokhuza nkhaniyi zapitirizidwa m’gawo 6, lomwe likufotokoza za zovuta zomwe munthu

amakumana nazo akamwa mankhwalawa.

Zolinga

Pakutha pa gawoli ophunzirawa ayenera:

a Kufotokoza kuti mankhwala a ma-ARV amagwira ntchito yoletsa

kachirombo ka HIV kuswana m’thupi la munthu.

b Kufotokoza nthawi yomwe ma-ARV ayenera kumwedwa, kangati pa tsiku,

nthawi yayitali bwanji komanso kuchuluka kwake.

c Kuzindikira mayina a ma-ARV ndi zizindikiro zomwe zimagwiritsidwa

ntchito pa makhadi olandirira mankhwala.

d Kufotokoza kuti ma-ARV afunika kuwasunga pamalo ouma, osawalira

dzuwa, ozizirira komanso posafikira ana.

e Kuzindikira zizindikiro zoonetsa kuti odwala akumwa mankhwala a ARV

mosadukizadukiza, akuchita zinthu zoyenera kuti moyo wawo upitirire

kukhala wathanzi komanso zizindikiro zoonetsa kuti sakuchita zimenezi.

f

Kupereka chitsanzo cha kagwiritsidwe ntchito ka makhadi olandirira

mankhwala.

g Kufotokoza zimene timatanthauza tikati munthu akumwa mankhala

mosadukiza ndi mavuto amene amakhalapo.

Nthawi

1 Hour, 40 Minutes

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera

135

136

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

Mutu Mwachidule

Ntchito Zoti Ziphunzitsidwe Njira Nthawi Zipangizo Zofunikira

1 Mphunzitsi

2 Ali

afotokoza

mfundo zokhudza

ma-ARV, zizindikiro

zimene zili pa makhadi

olandilira mankhwala

ndi kumwa mankhwala

mosadukizadukiza..

awiriawiri,

ophunzirawa apeza

njira zothetsera mavuto

akumwa mankhwala

modukizadukiza omwe

angathe kuchitika.

Kufotokoza kwa

Mphunzitsi

Zokambirana

za M’magulu

Akuluakulu

Kuthandizana

Anthu Awiriawiri

Mfundo Zikuluzikulu

60 Minutes

40 Minutes

• Matchati kapena kudzera pa makina a

kompyuta

• Chipangizo chotulutsa mawu ndi zithunzi

(ngati akugwiritsa ntchito kompyuta)

• Makhadi olandirira mankhwala

• Mankhwala a ma-ARV

• Bukhu la Wazaumoyo wa M’mudzi

• Makhadi olandirira mankhwala

• Ziyelekezo (ikatha ntchito iyi)

• Bukhu la Wazaumoyo wa M’mudzi

• Ma-ARV amagwira ntchito yoletsa kachirombo ka HIV kuti kasaswane m’thupi.

• Munthu amamwa ma-ARV moyo wake onse.

• Anthu amene ali ndi kachirombo ka HIV/EDZI afunika kumwa ma-ARV pa

nthawi yomweyoyomweyo tsiku lililonse motsatira malangizo ake.

• N’zovuta kumwa ma-ARV tsiku ndi tsiku kwa moyo wonse, koma ngati anthu

amene ali ndi HIV/EDZI adukiza kumwa mankhwala, ndiye kuti mankhwalawo

sagwiranso ntchito.

• Ngati odwala amwa mowa kapena mankhwala osokoneza bongo zimachititsa

kuti ma-ARV asamagwire bwino ntchito mthupi.

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera

Ntchito 1

Mankhwala a ma-ARV

Kufotokoza kwa Mphunzitsi

Zokambirana za M’magulu Akuluakulu

Nthawi

60 Minutes

Zolinga

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

a Kufotokoza kuti mankhwala a ma-ARV amagwira ntchito yoletsa kachirombo

ka HIV kuti kasapitirire kuswana m’thupi.

b Kufotokoza nthawi yomwe ma-ARV ayenera kumwedwa, kangati pa tsiku,

kwa nthawi yaitali bwanji komanso kuchuluka kwake.

c Kudziwa mayina a ma-ARV ndi zizindikiro za mankhwalawa zomwe

zimagwiritsidwa ntchito pa makhadi olandirira mankhwala.

d Kufotokoza kuti ma-ARV amafunika kuwasunga pamalo ouma, osawala dzuwa,

ozizirira komanso oti ana sangawafikire.

Kukonzekera

• Sonkhanitsani mankhwala a ma-ARV osiyanasiyana ndi moti muikemo

mankhwalawa monga mabokosi kapena mbale.

• Konzani malo osachepera asanu m’chipindamo kuti pamalo alionse pakhale

anthu asanu kapena ochepera apa. Ikani mankhwala ndi makhadi olandirira

mankhwala pa malo alionse.

Zipangizo Zofunikira

Matchati kapena kudzera pa makina a kompyuta

Chipangizo chotulutsa mawu ndi zithunzi (ngati akugwiritsa ntchito kompyuta)

Makhadi olandirira mankhwala

• Mankhwala a ma-ARV

Bukhu la Wazaumoyo wa M’mudzi

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera 137

138

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

1

2

Ndondomeko

Mankhwala a HIV ndi EDZI

Uzani ophunzirawa kuti gawo lino likufotokoza nkhani za ma-ARV.

Funsani ophunzira kuti:

Kodi inu kapena wina amene mukumudziwa adamwapo mankhwala?

» azimwedwa?

Kodi pali nthawi zake zenizeni zimene mankhwala ena ake a mafunika kuti

Kodi pali malangizo alionse amene amafunika kutsatidwa pakumwa mankhwala ena?

» Izi zili chomwechi chifukwa chiyani?

(Mankhwala osiyanasiyana amagwira nthito m’matupi athu mosiyananso

ndipo ndikofunika kuti ife tisinthe zochita zathu kuti mankhwalawo atithandize

mokwanira.)

3 Fotokozani kuti ma-ARV amaletsa HIV kuswana ndi kupha ma-CD4, omwe

ndi ofunika kwambiri pachitetezo cha m’thupi. HIV ikakaswana imafooketsa

chitetezo cha m’thupi. Ngati munthu amwa ma-ARV moyenera komanso

mosadumphitsadumphitsa, chitetezo cha m’thupi lake chimakhala champhamvu.

Munthu akapezeka ndi kachirombo ka HIV, sikuti amayamba kumwa mankhwala

a ma-ARV nthawi yomweyo. Dokotala kapena namwino pamodzi ndi wazaumoyo

wa m’mudzi angaone nthawi yoti munthuyo ayambe kumwa mankhwala a ma-

ARV malinga ndi nthazi lake.

4

Mutu 5

Mankhwala a HIV ndi EDZI

Partners In Health

Zanmi Lasante

Bo-Mphato Litsebeletsong tsa Bophelo

Inshuti Mu Buzima

Abwenzi Pa Za Umoyo

52

Anthu amene apezeka ndi HIV amakakumana ndi dokotala kamodzi mwezi

ulionse. Ngati sanayambe kumwa ma-ARV adokotala kapena anamwino

amawayeza n’kuona ngati akufunikira kuyamba ma-ARV. Ngati akumwa ma-

ARV dokotala amawayeza kuti aone ngati mankhwalawo akugwira nthito.

Chitetezo cha m’thupi (CD4) chikachepera pa 250, dokotala kapena namwino

amamuyambitsa munthuyo ma-ARV. (Nambalayi ikhonza kusintha mtsogolomu

kufika 350.)

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera

5

6

7

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

Fotokozani kuti pofuna kuletsa kachirombo ka HIV kuti kasaswane, wodwalayo

ayenera kumwa mitundu itatu ya ma-ARV tsiku ndi tsiku. Tili ndi mwayi kuti

ma-ARV ambiri amene tili nawo ku Malawi kuno, anaphatikizamo mitundu

iwiri kapena itatu m’pilisi limodzi kuti munthu asamachite kumwa mapilisi

ambirimbiri. Mapilisi amenewa amatchedwa amphamvu zingapo.

Anthu amene ali ndi HIV akangoyamba kumwa mankhwala afunika kumwa

mankhalawa nthawi yomweyomweyo tsiku lililonse moyo wawo wonse. Uku

ndiko timati kumwa mankhwala kosadukiza. Ngati wodwala alekeza kumwa

mankhwala kapena adumphitsadumphitsa kamwedwe kake, HIV imayamba

kuswana ndi kupha ma-CD4. Ngati odwala ali ndi chizolowezi chomamwa

ndi kulekeza kumwa ma-ARV, kachirombo ka HIV kamene kali m’thupi lawo

kadzatha kulimbana ndi ma-ARV. Zikafika apa timati kachilomboko sikakumva

mankhwala ndipo ndizoopsa kwambiri. Mankhwala a ma-ARV sadzathanso

kugwira nthito yawo monga m’mene amayenera kuchitira.

Fotokozani kuti amayi oyembekezera amene ali ndi HIV amathandzidwa

mosiyana ndi anthu ena. Atha kuyambitsidwa kumwa ma-ARV pofuna kupewa

kuti angapatsire kachirombo ka HIV mwana yemwe akuyembekezerayo. Amayi

oyembekezera amene ali ndi HIV angafunike kupita ku chipatala kangapo pa

mwezi m’malo mwa kamodzi. Wodwala akayamba kumwa ma-ARV dokotala

kapena namwino amakumana ndi wazaumoyo wa m’mudzi pamodzi ndi

wodwalayo n’kuwafotokozera mankhwala amene wodwalayo azimwa, nthawi

yomwera ndiponso kuchuluka kwake. Zimenezi azidzilemba pa pepala kuti

wodwalayo ndi wazaumoyo wa m’mudzi adzitha kukumbukila.

8 Mu ntchito iyi ophunzirawa aphunzira nkhani zokhudza ma-ARV. Ayesetse

kukumbukira zomwe aphunzirazi, komabe mfundozi ziliponso mu Bukhu la

Wazaumoyo wa M’mudzi (gawo 5 tsamba 113).

9

10

Gawani ophunzirawa m’magulu asanu powauza kuti aliyense azitchula

manambala kuchokera 1 mpaka 5 — onse amene anatchula 1 akhale gulu

limodzi, amene anatchula 2 akhalenso gulu lawo mpaka 5. (Yesetsani kuika

munthu amene amatha kulemba ndi kuwerenga kapena wazaumoyo wa m’mudzi

yemwe amadziwa bwino ntchito yake pa gulu lililonse.)

Uzani ophunzirawa kuti pagulu lililonse pali makhadi olandirira mankhwala.

(mtundu ulionse wa ARV uli ndi khadi lake) ndi mapilisi a ma-ARV. Awa

ndi ma-ARV osiynasiyana amene akupezeka m’dziko muno. Apatseni

ophunzirawa nthawi yokwanira kuti awaone makhadi olandirira mankhwala

ndi kufunsa mafunso okhudza makhadiwo. Onetsetsani kuti akutha kuwerenga

makhadiwa. Fotokozani kuti mu gawo 6, aphunzira mavuto amene amadza

munthu akamamwa ma-ARV kotero kuti asadere nkhawa za zimenezi panopa.

Onetsetsani kuti ophunzirawa akumvetsa zomwe zithunzi zomwe zili pa makhadi

olandirira mankhwala zikuimira.

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera 139

140

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

11 Sandutsani ntchitoyi kukhala sewero. Pamene mutchula maina a ma-ARVs,

funsani ma gulu kuti a yang’ane ndi kukweza khadi yolodola ndi pirisi lake.

Gulu loyamba kupeza khadi ndi pirisi mulipatse pointi, ndipo potsiriza

mudzanena opambana. Gulu likapeza pirisi lolondola, funsani magulu enao ngati

akuvomereza kapena ayi. Akapeza pirisi logwirizana ndi khadi lake, onetsani

tchati tsopano lomwe liri ndi izi.

12

13

Abwenzi Pa Za Umoyo

T 30 (Triomune)

Pilisi limeneli anaphatikizamo Sitavudini (D4T) Lamivudini(3TC) ndi Nevirapini

(NVP). Pilisi limeneli limatchedwa T30. Auzeni ophunzira kuti aone mtundu

wake, kaonekedwe ndi kukula kwa pilisili. Nthawi zambiri wodwala amafunika

kumwa pilisi limodzi kawiri pa tsiku: 6 koloko m’mawa ndi 6 koloko madzulo.

Mankhwalawa amaperekedwanso pa milungu iwiri yoyamba kulandira

mankhwala pa gulu la “ Mankhwala oyambira” pomwe wodwala amafunika

kumwa pilisi limodzi m’mawa pa 6 koloko.

Abwenzi Pa Za Umoyo

T 30 (Triomune)

Kuphatikiza mankhwala a Stavudine (d4T), Lamivudine (3TC),

ndi Nevirapine (NVP)

1 pilisi

(T30-d4T 30mg,

3TC-150 mg,

NVP-200mg)

1 pilisi

(d4T-30 mg,

3TC-150mg)

Imwani kawiri patsiku:

M’mawa – 6 koloko

Madzulo – 6 koloko

LS30

Kuphatikiza mankhwala a d4T ndi 3TC

Imwani kawiri patsiku:

M’mawa – 6 koloko

Madzulo – 6 koloko

53

54

LS 30

Mpilisi ili anaphatizamo Sitavudini (D4T) ndi Lamivudini (3TC). Kawirikawiri

mankhwalawa amaperekedwa pa milungu iwiri yoyambirira kumwa mankhwala

pa gulu la mankhwala oyambira, ndipo wodwalayo amamwa madzulo 6 koloko.

Nthawi zina mankhalawa amaperekedwa kwa wodwala akadana ndi ena mwa

mankhwala a gulu la T30. Zikatere dokotala amauza wodwalayo kuti adzimwa

kawiri pa tsiku, 6 koloko m’mawa ndi 6 koloko madzulo ndipo kawiri kawiri

amamupatsanso mankhwala ena otchedwa Efavirenzi.

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera

14

15

16

Abwenzi Pa Za Umoyo

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

Efavirenzi (Efavirenz—EFV)

Auzeni ophunzira kuti aone kaonekedwe ndi kukula kwa pilisili. Kamwedwe

kake: pilisi limodzi (600mg) kamodzi pa tsiku, madzulo 6 koloko. Wodwalayo

ayenera kumwa asanadye kanthu kalikonse.

Abwenzi Pa Za Umoyo

Kombiviri kapena Duoviri (Comibivir or Duovir)

Mpilisi ili muli zidovudini (AZT) ndi Lamivudini (3TC). Kawirikawiri

mankhwalawa amaperekedwa kwa wodwala amene wadana ndi ena mwa

mankhwala a mu T30. Auzeni ophunzira kuti aone mtundu, kukula ndi

kaonekedwe ka pilisili. Kamwedwe kake ndi pilisi limodzi (350/150g) kawiri pa

tsiku, 6 koloko m’mawa ndi 6 koloko madzulo. Kawirikawiri mankhwalawa

amaperekedwa pamodzi ndi Nevirapini.

Abwenzi Pa Za Umoyo

Efavirenzi (Efavirenz—EFV)

1 pilisi

(600 mg akulu

akulu, 200 mg

kwa ana)

Imwani

musanadye

Imwani kamodzi patsiku:

Madzulo – 6 koloko

Kombiviri kapena Duoviri

(Comibivir or Duovir)

Kuphatikiza Zidovudine (AZT) ndi 3TC

1 pilisi

(3TC-150 mg,

AZT-300 mg)

Imwani kawiri patsiku:

M’mawa – 6 koloko

Madzulo – 6 koloko

Nevirapini (Nevirapine—NVP)

1 pilisi

(200 mg)

Imwani kawiri patsiku:

M’mawa – 6 koloko

Madzulo – 6 koloko

55

56

57

Nevirapini (Nevirapine—NVP)

Aauzeni ophunzira kuti aone mtundu, kaonekedwe ndi kukula kwa pilisili.

Kamwedwe kake pilisi limodzi kawiri patsiku, 6 koloko m’mawa ndi 6 koloko

madzulo.

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera 141

142

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

17

18

19

20

Abwenzi Pa Za Umoyo

Lopinaviri/Ritonaviri (Lopinavir/Ritonavir--Lop/r)

Auzeni ophunzira kuti aone mtundu, kaonekedwe ndi kukula kwa pilisili. Ku

Malawi kuno wodwala amapatsidwa mankhwalawa ngati mankhwala a T30 kapena

ena anamusinthila sakumuthandiza. Kamwedwe kake ndi kawiri patsiku, 6 koloko

m’mawa ndi 6 koloko madzulo, koma adokotala ndi amene amanena kuti munthuyo

adzimwa mapilisi angati.

Abwenzi Pa Za Umoyo

Tenofoviri (Tenofovir—TDF)

Auzeni ophunzira kuti aone mtundu, kaonekedwe ndi kukula kwa pilisili. Ku

Malawi kuno wodwala amalandira mankhwalawa ngati mankhwala a T30

kapena ena amene anamusinthira sakumuthandiza. Kamwedwe kake: pilisi

limodzi (300mg) kamodzi patsiku, 6 koloko m’mawa.

Werengetserani mapoinsi ndikulengeza gulu limene lapambana.

Abwenzi Pa Za Umoyo

Lopinaviri/Ritonaviri

(Lopinavir/Ritonavir–Lop/r)

1 pilisi

(Lopinavir

200 mg,

Ritonavir 50 mg)

Imwani kawiri patsiku:

M’mawa – 6 koloko

Madzulo – 6 koloko

Tenofoviri (Tenofovir—TDF)

1 pilisi

(300 mg Tenofovir

Disoproxil

Fumarate )

(245 mg Tenofovir

Disoproxil)

1 pilisi

(480 mg akulu

akulu, kwa ana

zimatengera

zaka zawo)

Imwani kawiri patsiku:

M’mawa – 6 koloko

Madzulo – 6 koloko

Bakitirimu (Bactrim)

Imwani kawiri patsiku:

M’mawa – 6 koloko

Madzulo – 6 koloko

59

60

58

Bakitirimu

Fotokozani kuti anthu ambiri amene ali ndi HIV amafunikanso kumwa

mankhwala ena otchedwa Bakitirimu. Mankhwala amenewa sali m’gulu la ma-

ARV. Amenewa ndi mankhwala othandiza kulimbana ndi matenda ongopezerapo

mwayi kamba ka HIV ndipo amagwira nthito yakupha mabakitiriya.

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera

21

22

23

Abwenzi Pa Za Umoyo

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

Mankhwala Oyambira

Afotokozereni ophunzira kuti pali magulu osiyanasiyana a ma-ARV ndipo

anawapangira anthu osiyanasiyana. Odwala ndi azaumoyo a m’mudzi ayenera

kufunsa a dokotala kapena anamwino ngati sankumvetsa bwino za mankhwala

amene alandira. Odwala ambiri amamwa mankhwala oyambira kwa milungu

iwiri yoyamba. Odwala amene akumwa mankhwala oyambira amamwa pilisi

limodzi la T30 m’mawa 6 koloko ndi pilisi la Ls30 madzulo 6 koloko. Thupi la

wodwala limafunika kuzolowela mankhwala a Nevirapini mu T30. Pakatha

milungu iwiri mankhwala a Nevirapini angawaonjezere m’kuyamba kumamwa

T30 kawiri patsiku, 6 koloko m’mawa ndi 6 koloko madzulo.

Asungeni kutali

ndi ana

Abwenzi Pa Za Umoyo

“Mankhwala Oyambira”

(Starter Pack)

Imwani kwa milungu iwiri

yoyambirira kumwa mankhwala.

Imwani pilisi limodzi la T 30

6 koloko m’mawa –

T 30 = d4T 30mg, 3TC 150 mg, ndi

NVP 200mg.

Imwani pilisi limodzi la

LS 6 koloko madzulo

30

150 mg Lamivudine, 30 mg Stavudine

61

Kusunga Mankhwala

Nenani kuti ma-ARV afunika kusungidwa pamalo amodzi: pouma, posawalira

dzuwa, pozizirira komanso posafikira ana. Afunseni ophunzirawa chifukwa chake

kusunga mankhwala pamalo abwino kuli kofunika.

Idyani chakudya

chopatsa thanzi

Abwenzi Pa Za Umoyo

Kusunga Mankhwala

Asungeni posafi ka

dzuwa ndi kutentha

Kukhala ndi Moyo Wathanzi

Asungeni pouma

Musamwe mowa Musasute fodya

62

63

Kukhala ndi Moyo Wathanzi

Fotokozani kuti anthu amene ali ndi HIV/EDZI atha kukhala ndi moyo wathanzi

nthawi imene akumwa ma-ARV ngati apewa kusuta fodya, osamwa mowa, kudya

zakudya zabwino nthawi zonse, kumayendayenda, kupuma nthawi yokwanira ndi

kuchita nawo zochitikachitika zabwino zomwe anthu ena akuchita.

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera 143

144

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

24

25

26

Gonanani Modziteteza Nthawi Zonse

Abwenzi Pa Za Umoyo

Kugonana Modziteteza

Tsindikani kuti kukhala ndi moyo wathanzi kumakhudzanso makhalidwe omwe

amateteza anthu ena kutenga kachirombo ka HIV. Tsindikani kuti anthu amene

akumwa ma-ARV asagone ndi munthu popanda kudziteteza.

Phindu la Mankhwala a ma-ARV ndi

Kukhala ndi Moyo Wathanzi

Abwenzi Pa Za Umoyo

64

65

Phindu la ma-ARV ndi Kukhala ndi Moyo Wathanzi

Nenani kuti: Izi ndi zithunzi ziwiri za mayi wa ku Rwanda zina lake Solange.

Monga momwe mukuoneramu, pa chithunzi choyambacho mayiyu ndi woonda,

wofooka komanso wodwala. Pa chithunzi chinacho akuoneka wathanzi. Zithunzi

zonsezi Solange anamujambula ali ndi HIV. Afunseni ophunzirawa kuti:

» Kodi mukuganiza kuti mayiyu akuoneka mosiyana pa zithunzi ziwirizi chifukwa

chiyani?

(Chithunzi choyambacho anamujambla asanayambe kumwa ma-ARV.)

Fotokozani kuti pa chithunzi choyambacho Solange anali asanayambe kumwa

mankhwala. Fotokozaninso kuti ntchito yomwe azaumoyo a m’mudzi amagwira

yothandiza odwala kuti adzimwa mankhwala, makamaka ma-ARV, ndiyofunika

kwambiri. Anthu amene ali ndi HIV/EDZI amene akumwa ma-ARV ndipo

akukhala mwansangala atha kukhala ndi moyo wathanzi ndi wautali. Azaumoyo

a m’mudzi atha kuthandiza kuti izi zichitike.

27 Onetsetsani kuti ophunzirawa azipeza mfundozi mu gawo 5 m’ Bukhu la

Wazaumoyo wa M’mudzi kuyambira tsamba 113. Auzeni kuti atha kugwiritsa

ntchito bukhu lawoli mtsogolomu pofuna kuona zina ndi zina zomwe angafune

kuti azidziwe

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera

1

2

3

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

Ntchito 2

Mavuto a Kusamwa Mankhwala Motsata Ndondomeko

Kuthandizana Anthu Awiriawiri

Nthawi

40 Minutes

Zolinga

e Kudziwa zizindikiro zoonetsa kuti odwala sakudumphitsa kumwa ma-ARV

ndi kuti akuchita zinthu zothandiza kuti akhale ndi moyo wathanzi komanso

zizindikiro zoti odwalawo sakutsatira zimenezi.

f Kusonyeza kagwiritsidwe ntchito ka makadi olandirira mankhwala.

g Kufotokoza zimene timatanthauza tikati munthu akumwa mankhala

mosadukiza ndi mavuto amene amakhalapo.

Kukonzekera

• Chitani fotokope mafunso kuti muthe kuwerenga mosachita kuvundukula

masamba a bukhu.

Zipangizo Zofunikira

Makhadi olandirira mankhwala

Ziyezekezo (ikatha ntchito iyi)

Bukhu la Wazaumoyo wa M’mudzi

Ndondomeko

Uzani ophunzirawa kuti akhale awiriawiri ndi kuonetsetsa kuti m’modzi mwa

anthu awiri alionse amatha kulemba ndi kuwerenga.

Auzeni ophunzirawa kuti atsekule Bukhu la Wazaumoyo wa M’mudzi pamene

pali makhadi olandirira mankhwala mu gawo 5 (tsamba 123).

Fotokozani kuti ayeserera kugwiritsa ntchito makhadi olandirira mankhwala

pomvetsera mafunso ndipo iwo achite zinthu zogwirizana ndi zomwe amvazo.

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera 145

146

4

5

6

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

Werengani mafunso mokweza ndi kuwapatsa ophunzirawo mphindi ziwiri zoti

akambirane awiriawiri.

Akatha kukambirana funsolo uzani gulu limodzi kuti lifotokozere anzawo

onse zomwe akambirana. Funsani ngati pali ena amene sakugwirizana ndi

mayankho omwe anzawowo apereka. Fotokozerani ngati pali pena pamene

sipanamveke bwino

Pitirizani mpaka mumalize kukambirana mafunso onse. Onetsetsani kuti gulu

lililonse mwalipatsa mpata wolankhulapo.

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera

koperani kapena dulani

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

T30 (Triomune)

Kuphatikiza mankhwala a Stavudine (d4T), Lamivudine (3TC),

ndi Nevirapine (NVP)

1 pilisi

(T30-d4T 30mg,

3TC-150 mg,

NVP-200mg)

1 pilisi

(d4T-30 mg,

3TC-150mg)

Imwani kawiri patsiku:

M’mawa – 6 koloko

Madzulo – 6 koloko

LS 30

Kuphatikiza mankhwala a d4T ndi 3TC

Imwani kawiri patsiku:

M’mawa – 6 koloko

Madzulo – 6 koloko

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera 147

148

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera

koperani kapena dulanii

koperani kapena dulani

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

Kombiviri kapena Duoviri

(Comibivir or Duovir)

Kuphatikiza Zidovudine (AZT) ndi 3TC

1 pilisi

(3TC-150 mg,

AZT-300 mg)

Imwani kawiri patsiku:

M’mawa – 6 koloko

Madzulo – 6 koloko

Efavirenzi (Efavirenz—EFV)

1 pilisi

(600 mg akulu

akulu, 200 mg

kwa ana)

Imwani

musanadye

Imwani kamodzi patsiku:

Madzulo – 6 koloko

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera 149

150

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera

koperani kapena dulanii

koperani kapena dulani

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

Nevirapini (Nevirapine—NVP)

1 pilisi

(200 mg)

Imwani kawiri patsiku:

M’mawa – 6 koloko

Madzulo – 6 koloko

Lopinaviri/Ritonaviri

(Lopinavir/Ritonavir—Lop/r)

1 pilisi

(Lopinavir

200 mg,

Ritonavir 50 mg)

Imwani kawiri patsiku:

M’mawa – 6 koloko

Madzulo – 6 koloko

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera 151

152

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera

koperani kapena dulanii

koperani kapena dulani

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

Tenofoviri (Tenofovir—TDF)

1 pilisi

(300 mg Tenofovir

Disoproxil

Fumarate )

(245 mg Tenofovir

Disoproxil)

Imwani kawiri patsiku:

M’mawa – 6 koloko

Madzulo – 6 koloko

“Mankhwala Oyambira”

(Starter Pack)

Imwani kwa milungu iwiri

yoyambirira kumwa mankhwala.

Imwani pilisi limodzi la T 30

6 koloko m’mawa –

T 30 = d4T 30mg, 3TC 150 mg, ndi

NVP 200mg.

Imwani pilisi limodzi la

LS 30 6 koloko madzulo

150 mg Lamivudine, 30 mg Stavudine

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera 153

154

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera

koperani kapena dulanii

koperani kapena dulani

1 pilisi

(480 mg akulu

akulu, kwa ana

zimatengera

zaka zawo)

Bakitirimu (Bactrim)

Imwani kawiri patsiku:

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

M’mawa – 6 koloko

Madzulo – 6 koloko

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera 155

156

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera

koperani kapena dulanii

1.

2.

3.

4.

5.

6.

7.

8.

9.

Mutu 5, Ntchito2: Ziyerekezo

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

Ngati wodwala wanu ali pa mankhwala oyambira, kodi mankhwala a Ls30 azimwa

nthawi yanji?

(Madzulo 6 koloko.)

Ngati wodwala wanu akumwa mankhala a T30, kodi azimwa nthawi yanji?

(Kamodzi m’mawa ndi madzulo.)

Wodwala wanu wina akumwa Kombiviri ndipo akufuna kudziwa kuti azimwa

mapilisi angati patsiku, mumuuza kuti chiyani?

(Awiri.)

Muli ndi munthu wodwala amene akumwa Nevirapini. Kodi munthuyu azimwa

mankhwalawa kangati patsiku ndiponso azimwa mapilisi angatiangati?

(Pilisi limodzi kawiri pa tsiku.)

Wodwala wanu wina akumwa Efavirenzi. Kodi azimwa mankhwalawa kangati pa

tsiku?

(Kamodzi.)

Muli ndi munthu odwala amene akumwa Efavirenzi. Pamene inu mukufika

kunyumba kwake m’mawa kukamuona akumwa mankhwalawa mwampeza akudya

buledi. Kodi m’mene zakhalira zithumu pali vuto?

(Inde. Mankhwalawa afunika kumwedwa munthu asanadye kanthu kalikonse.)

Wodwala wanu wina wamwa mankhwala oyambira kwa masiku khumi. Kodi

kwatsala masiku angati kuti amwebe mankwalawa?

(Masiku 4)

Muli ndi munthu wodwala amene amasuta fodya nthawi zonse. Kodi mufunika

kuchitapo kanthu? Ngati mungatero, mungachite chiyani?

(Kusuta fodya kumachititsa kuti mankhwala asamagwire bwino ntchito yake

mokwanira. Wazaumoyo wa m’mudzi afunika ayankhule ndi wodwalayo

ndikupemphanso namwino kuti ayankhule naye.)

Muli ndi wodwala amene nthawi zina amamveka fungo la mowa mukamafika pa

khomo pake. Kodi limeneli ndi vuto? Chifukwa chiyani? Mungachite chiyani pa vuto

limeneli?

(Inde, limeneli ndi vuto. Mowa umachititsa kuti mankhwala asamagwire bwino

ntchito yake. Muyankhule naye wodwalayo komanso pemphani namwino kuti

ayankhule naye.)

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera 157

158

Mutu 5: Mankhwala a HIV ndi EDZI

Zomwe Wazaumoyo wa M’mudzi

Ayenera Kukumbukira

Kukawatengera odwala mankhwala ku chipatala mwenzi ulionse.

Kupita ndi wodwala kuchipatala mwezi uliwonse kukatenga mankhwala.

Kuonetsetsa kuti odwala akusunga mankhwalawo pamalo otetezeka, ouma,

osawalira dzuwa komanso oti ana sangafikire

Kuonetsetsa kuti odwala akulandira ma-ARV a mtundu woyenera.

Kuonetsetsa kuti odwala akumwa ma-ARV awo moyenera.

Kupenyetsetsa odwala kuti aone zizindikiro zoti sakutsatira makhalidwe

abwino owathandiza kuti akhale ndi moyo wathanzi ndi kuwapatsa uphungu

kapena kuwatumiza kuchipatala ngati nkofunika kutero.

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera

Zolembalemba

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera 159

160

Zolembalemba

Bukhu Lophunzitsira Alangizi Azaumoyo a M’mudzi a Bungwe la Abwenzi Pa Za Umoyo: Chisindikizo Choyeserera

Hooray! Your file is uploaded and ready to be published.

Saved successfully!

Ooh no, something went wrong!