Mpandamachokero Anthology by Bonwell Rodgers
MPANDAMACHOKERO ANTHOLOGY By Bonwell Rodgers
- Page 2 and 3: Mawu Oyamba M’bukuli muli nthano
- Page 4 and 5: Mbalame Yodzimva M’nkhalango ina
- Page 6 and 7: “Mwayankhula bwino pamenepo a Nan
- Page 8 and 9: Osavula zigoba mwavalazo bwanji?”
- Page 10 and 11: Nkhandwe ya Mtima Wangati Kuseri kw
- Page 12 and 13: Galu Apusitsidwa ndi Chithunzithunz
- Page 14 and 15: Mkango Unatenga Zonse Tsiku lina Mk
- Page 16 and 17: Dokowe Apulumutsa Nkhandwe Tsiku li
- Page 18 and 19: Mpandamachokero Kalelo, pamudzi win
- Page 20 and 21: Kusamvana Pakati pa Munthu ndi Njok
- Page 22 and 23: Khoswe Wam’tauni ndi Khoswe Wakum
- Page 24 and 25: ukufuna kubwerera kumudzi nthawi yo
- Page 26 and 27: Monga malipiro a nyama ndatengayi,
- Page 28 and 29: Phunziro: Ndi anthu amatha amene am
- Page 30 and 31: wachita misala, ndipo anatenga ndod
- Page 32 and 33: chinaduka. Kenako anauza Mkangowo k
- Page 34 and 35: Kumachotseratu mbewu yoipa isanamer
- Page 36 and 37: mwamantha ndipo sankayandikira n’
- Page 38 and 39: Phokoso la Mapiri Tsiku lina anthu
- Page 40 and 41: Akalulu Akumana Ndi Mavuto Nthawi i
- Page 42 and 43: Ukakwera M’mwamba Usamatukwane Pa
- Page 44 and 45: Pansi pa Mtima Tsiku lina Gondwa an
- Page 46 and 47: Njoka Yopanda Pabwino Chaka china k
- Page 48 and 49: Ntchentche Yosimbwa Kalelo kunali b
- Page 50 and 51: Nkhandwe Ichezera Dokowe Kalekalelo
MPANDAMACHOKERO

ANTHOLOGY

By Bonwell Rodgers
Mawu Oyamba

M’bukuli muli nthano za ana. Nthano zina ndi zoti

zinalembedwa ndi akatswiri akale kwambiri ndipo

zinamasuliridwa n’kukonzedwa mwina ndi mwina,

pomwe zina ndi za kwathu konkuno ku Malawi.

Nthanozi ndi zazifupi koma zosangalatsa. Wolemba

bukuli anaona kuti anthu ambiri sakonda kuwerenga

nkhani zazitali. Choncho analemba nthano zazifupi

koma zomveka bwino. Nthanozi ndi zoti zikhoza

kugwiritsidwa ntchito pophunzitsa kusukulu,

powerengera ana komanso pocheza. Bukuli

lingathandizenso ana kuphunzira ukadaulo wopinda

komanso kuseweretsa mawu m’Chichewa.

Kuwonjezera apo, nthano zake ndi zokhathamira ndi

nsinjiro za chiyankhulo.

The Series of Rodgers Bounty Books [RBB]

Copyright © January 2015 by Bonwell Rodgers.

All rights reserved. No part of this publication may be reproduced or transmitted in any form or by any means, electronical or

mechanical, including photocopy, recording or any imformation storage and retrieval system, without permission in writing from the

owner.

Requests for permission should be mailed to: Bonwellrodgers91@gmail.com

Phone: 0881813953, 0881831435

Mpandamachokero Anthology

1
Nthano Zokhala ndi Maphunziro

“Tikhoza kuphunzira zambiri ngakhale kuchokera kwa

nyama zakutchire. Chilichonse chili ndi pokomera,

kungoti umafunika kufufuza mosamala kuti upaone

pokomerapo.”

—Anatero Lewis Carrol m’buku lake lakuti, Alice’s

Adventures in Wonderland

Mpandamachokero Anthology

2
Mbalame Yodzimva

M’nkhalango ina munali mbalame yokongola kwambiri

yomwe inkadya moto chifukwa cha kuyerekedwa

kwake. Dzina la mbalameyi linali Pikoko. Mbalameyi

inali yaphunzo chifukwa inkanyoza zinzake zomwe

zinali ndi nthenga zosaonetsa kugulu la anthu.

Inalinso yodzimva komanso yodzikuza zedi. Tsiku lina

mbalame zonse zitakhuta, zinapita pachitsime pomwe

zinkakamwa madzi. Mbalamezi zinkafunika kufola

pamzere kuti zikamwe madziwo. Ndiye chifukwa

chodziona kukongola, mbalame ija yotchedwa Pikoko

inangoyenda kupita kutsogolo n’kudutsa zinzake

zonse zomwe zinafika mofulumira. Mbalameyi

inkayenda monyang’wa ngati sipita kuchumbudzi, ili

palasu palasu palasu mpaka inakafika kutsogolo

kwenikweni. Anzake anaifunsa amvekere: “Chikatere?”

A Pikoko pomva izi anayamba kulavula mwano.

“Mulungutu enafe anatikondera! Kodi mumatichitira

nsanje eti?”

Mbalame zinzake zinadandaula kuti: “Chitsime

n’chimodzi m’mudzi muno, aliyense ayenera

kuchitiridwa mofanana kaya ali ndi nthenga zokongola

Mpandamachokero Anthology

3
kapena ayi, chilungamo chiziyenda ngati madzi!”

Koma mbalame ija inatuzula maso kwinaku

ikutokosera m’mano ndipo kenako inageyanso

chipongwe china cholama.

“Kodi mbalame zosasamba zikudzatani kuno? . . . Inu

a Khwangwala, ngati mumafuna kuchitiridwa zinthu

mofanana ndi enafe ingopitani kumanda! Ndipo

ndimadabwa kuti n’chifukwa chiyani nawonso manda

samaona kuti enafe tili ndi nthenga zokongola?

Tikazitambasula anthu amagwetsa zibwano zawo,

kudabwa kumeneko!”

Nang’omba atamva izi anatsutsa Pikoko. Kumenekotu

ndi kuyankhula kwa ntudzu komanso kogudukira.

Kukongoladi kwa mbalame n’kulinga utaiona

itatsegula pakamwa! Ndikuuzeni pano mosapsatira

mawu achikulire, kukongola kwa nthengaku

sikungakupangitseni kukhala wanzeru! Enafe

tinangoipa maonekedwewa, muntimamu si khalidwe

lake. Komanso tili ndi chikondi chopangitsa munthu

kuiwala kwawo!”

Mbalame zina zonse zinagwedezera mitu

povomerezana ndi a Nang’omba.

Mpandamachokero Anthology

4
“Mwayankhula bwino pamenepo a Nangomba!” Inatero

Nthiwatiwa. A Nthiwatiwa sanadziwe kuti zimene

anachitazo kunali kudzipalasira makala a moto,

ukadziotche weniweni. Pa nthawiyi n’kuti Pikoko

atapsa mtima, ukali ukutulukira mumphuno komanso

m’makutu, kwinaku atafutukura mapiko ake pofuna

kuwaonetsa anzakewo apo panagona kukongola

kwake. Kenako inakoka mtsonyo ikuyangana a

Nang’omba omwe anayandikana ndi a Nthiwatiwa.

Ndiyeno inayamba kulavula chichewa chitalichitali

chothiga ndi phunzo.

“Inu a Nang’omba ndinu chibenga. Nanunso a

Nthiwatiwa muli tiwa ngati nsungwi, zovala

zinakuthawani kalekale. Kodi simunamve kuti

munthu ukamafuna dzino lalikulu umafunika

kuutumba mulomo waukulu woti uvindikirire dzinolo?

Kutalika muli thobo, n’kumalephera kupeza zovala za

msinkhu wanu. Mumabwerekana zovala ndi mwana

wanu kapena? Mbalame zosasambanu mumatha

mawu kwabasi. Kaya n’kusowa khobili logulira

chinkhupule! Miyendo imeneyo ingapulumuke

mutakumana ndi khwekhwe kapena chimvwapula?

Mukamayenda mumangonunkha nkhwema

Mpandamachokero Anthology

5
kunkhwapa, simutisanzitsa inu? Kapena mumafuna

enafe tizichita nseru kuti chakudya m’malunjemu

chizitibwerera kukhosi! Umbombo wamtundu wanji

wofuna muzigalika nokha! Mukamayenda muli mimba

tiyetiye, nthenga zili yaviyavi, n’kumangooneka ngati

kamvuluvulu . . .”

Chipongwe chimenechi chinawafikapo a Nthiwatiwa

moti anayamba kuphulusika. Kenako anati:

“N’chifukwa chiyani anthu omwe muli pabwino

mumayankhula motumbwa?”

Koma a Pikoko anati: “Pajatu chilungamo

n’chipongwe! Kungoti enafe sitibisa mawu. Ena

akamatizolowera timangowamasura!”

Ndiyeno a Mkuta analowererapo n’kuuza a Pikoko

kuti, “Nafenso tikumasureni lero. Khalidwe lanu

limatinyansa, bolanso chimbudzi cha njovu kapena

fungo la dzila lowola.”

“Choka wouma mutu iwe!” Anatero a Pikoko.

“Namalenga ndiye anandinikha kukongolaku. Ngati

mumadziimba mlandu chifukwa cha kusaoneka bwino

kwanuko, mukawasumire makolo anu! Kodi

ndikanena chilungamo ndiye ndisanduke woipa?

Mpandamachokero Anthology

6
Osavula zigoba mwavalazo bwanji?”

Mbalame zonse zinadzuma ndipo ina yomwe inkamwa

madzi inatsamwa. Nthawi yomweyo Kadzidzi yemwe

n’kuti maso ake ali psuu chifukwa chosala tulo, zikope

zili thyo kuthyoka, anati: “A Pikokoo, palibetu

wangwiro padziko lapansi pano. Taonani miyendo

yanuyo!”

Mbalame zonse zinafa nawo nseko ndipo zina

zinangotsala pang’ono kukomoka chifukwa cha

chikhakhali. Zinkaseka miyendo ya a Pikoko yomwe

inali mbuu kutuwa ndipo inkangooneka ngati

zotokosera m’mano. Chifukwa cha manyazi, a Pikoko

anangosamukapo pachitsimepo, koma nyota

itangalula kukhosi.

Phunziro: Si bwino kukhala wodzikuza chifukwa

ngakhale utakhala ndi luso umakhala ndi penapake

pamene umalephera.

Mpandamachokero Anthology

7
Mafunso:

1. N’chifukwa chiyani a Pikoko samafuna kukhala

pamzere?

2. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti a Pikoko

anali wodzikuza?

3. Kodi pakati pa kukongola ndi khalidwe

labwino, chofunika kwambiri n’chiyani?

4. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

8
Nkhandwe ya Mtima Wangati Kuseri kwa

Mphika

Kalekalelo Nkhandwe inapita kukamwa madzi padziwe

lina lomwe linali pafupi ndi phiri. Itafika kumeneko

inaima chakumtunda n’kuyamba kupha ludzu.

Itamwaza maso inaona Nkhosa, nayonso ikumwa

madzi kumunsi kwa dziwelo. Kenako inayamba

kuganiza kuti, “Ndikhozatu kutsuka m’kamwa ndi

kandiwo kameneka. Nditangopeza chifukwa chabwino,

ndikhoza kukaonetsa zakuda ndithu.” Ndiyeno itadya

mutu inayamba kuyankhula mwaukali kwa Nkhosayo

kuti, “N’chifukwa chiyani ukudetsa madzi amene

ndikumwa?” Nkhosayo inayankha kuti, “Ayi, si ine.

Ngati madziwo akubwera akuda kumeneko, vuto si ine

ayi. Nokhanso mukuona kuti madziwa akuchoka

kumeneko n’kumabwera kuno.” Kenako Nkhandwe ija

inati, “Watero, chabwino, nanga n’chifukwa chiyani

unkanditukwana chaka chatha chija nditabwera

kudzamwa madzi kuno?” Nkhosayo inayankhanso

kuti, “Si inenso ameneyo, inetu ndili ndi miyezi isanu

ndi umodzi wokha, moti nthawi imeneyo ndinali

ndisanabadwe.” Itamva zimenezi, Nkhandweyo

inakwiya kwambiri ndipo inati, “Ndilibe nazo ntchito

Mpandamachokero Anthology

9
zimenezo, ngati sunali iweyo ndiye kuti anali bambo

ako.” Itangonena zimenezi inathamangira kunali

Nkhosa kuja n’kuimbwandira, ndipo kenako inaidya.

Phunziro: Munthu woipa sasowa chonamizira.

Amachita chilichonse kuti akwaniritse cholinga chake

ngakhale kupha munthu kumene.

Mafunso

1. Kodi m’nthanoyi ndi nyama iti imene ili yoipa

mtima? N’chifukwa chiyani mwayankha choncho?

2. N’chifukwa chiyani mutu wa nkhaniyi

ukuyerekeza mtima wa nkhandwe ndi kuseri kwa

mphika?

3. Perekani chitsanzo cha munthu woipa mtima

yemwe anachitira mnzake zankhanza, ngakhale

kuti mnzakeyo anali wosalakwa.

4. Kodi nkhaniyi ikutiphunzitsa chiyani?

Mpandamachokero Anthology

10
Galu Apusitsidwa ndi Chithunzithunzi

Tsiku lina Galu anatola nyama ndipo anaipana

n’kumapita nayo kwawo kuti akaidye mwamtendere.

Koma kuti akafike kwawo, ankafunika kuwoloka

mtsinje wina, ndipo kuti awoloke mtsinjewo

ankayenera kudutsa pamlatho waung’ono. Galuyo

atayamba kuwoloka kudzera pamlathowo, anaona kuti

m’madzi mukuoneka chithunzithunzi cha Galu

atanyamula nyama kukamwa kwake. Ataona zimenezi,

anaganiza kuti ameneyo ndi Galu wina. Chifukwa

chosakhutira ndi nyama yomwe anali nayo, Galuyo

anaganiza zolanda nyamayo kuti ikhalenso yake.

Ndiyeno mwamphamvu, analumphira m’madzi muja,

kuti khuvuu! Koma atangotsegula kukamwa kwake,

nyama ananyamula ija inagwera m’madzi ndipo

anaisakasaka koma sanaipeze. Pamenepo m’pamene

anazindikira kuti Galu amaoneka mumtsinje uja

chinali chithunzithunzi chake.

Phunziro: Musalole kutaya zonse zomwe muli nazo kuti

mupeze zinthu zomwe mukuganiza kuti mukhoza

kuzipeza. Kumakhutira ndi zomwe muli nazo.

Mpandamachokero Anthology

11
Mafunso

1. N’chifukwa chiyani Galuyu ankafunanso

kulanda nyama ya Galu amene ankamuona

m’madzi, kodi anali ndi njala?

2. Kodi mukuganiza kuti Galu angachitedi

zimenezi? N’chifukwa chiyani mwayankha

choncho?

3. Kodi nkhaniyi ikutiphunzitsa chiyani?

Mpandamachokero Anthology

12
Mkango Unatenga Zonse

Tsiku lina Mkango unapita kosaka limodzi ndi Agalu

am’tchire atatu. Nyama zimenezi zinasaka, kusaka,

kenako n’kusaka koma sizinagwire kanthu. Ndiyeno

mwamwayi, nyamazi zinasokolotsa Mphalapala ndipo

posakhalitsa zinaigwira n’kuipha. Zitatere, Agalu

am’tchirewo anayamba kunena kuti, “M’pofunika kuti

tonse tigawane nyamayi mofanana.” Koma Mkango

unabangula n’kuuza Agaluwo kuti, “Dulani nyamayi

panayi!” Agalu aja anamveradi zimenezo ndipo

anasenda nyamayo n’kuidula panayi. Kenako Mkango

uja unaima patsogolo pa nyamayo n’kuyamba

kulongosola za kagawidwe kake. Unati: “Mbali

yoyambayi ikhala yanga chifukwa ndine Mfumu ya

Zinyama zonse m’nkhalango muno. Mbali yachiwiriyi

ikhalanso yanga chifukwa ndine ndinayambitsa

ulenjewu. Pomwe mbali yachitatuyi ikhalanso yanga

chifukwa ndinathamangitsa nawo nyamayi. Koma

ponena za mbali yotsalayo, amene ali wolimba mtima

ayerekeze kuigwira aone . . . . ” Atamva zimenezi,

Agalu am’tchirewo anadzuma chapansipansi ndipo

kenako ananyamuka n’kumapita, kwinaku atapanira

michira yawo.

Mpandamachokero Anthology

13
Phunziro: Mukhoza kuthandiza anthu amphamvu

kuchita zinazake, koma simungadye nawo zimene

angapeze.

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani Agalu am’tchire ankathawa

atapanira michira?

2. Kodi mukuganiza kuti Agaluwo ankayenera

kudya nawo nyamayo? N’chifukwa chiyani

mukutero?

3. Kodi nkhaniyi ikutiphunzitsa chiyani?

Mpandamachokero Anthology

14
Dokowe Apulumutsa Nkhandwe

Tsiku lina Nkhandwe inali ndi njala zedi ndipo

inagwira nyama n’kuyamba kuipwepweta

mwankhanza. Koma mwatsoka fupa linaima pammero,

moti inkalephera kulimeza. Nkhandweyo inayamba

kumva ululu woopsa ndipo inkabuula kwinaku

ikupempha nyama zina kuti aithandize. Koma

chifukwa cha khalidwe lake la umadyera mphoto,

nyama zina zinkachita mantha, moti palibe inalimba

mtima kuithandiza. Kenako Nkhandweyo inayamba

kunyengerera aliyense amene inkakumana naye

n’cholinga choti aipulumutse. Inkati, “Ndikupatsani

chilichonse chimene mukufuna ngati mutandichotsa

fupali kukhosiku.” Mwamwayi, Dokowe anavomera

kuti ayesa kuchotsa fupalo, ndipo anaiuza kuti igone

pansi n’kutsegula kukamwa kwake. Dokoweyo

anapisa kukhosi kwa Nkhandweyo ndi mulomo wake

ndipo khosi lake lonse lalitalilo linalowa m’kamwa

mwa Nkhandweyo. Dokoweyo anakwanitsadi kuchotsa

fupalo ndipo Nkhandweyo inayamba kupeza bwino.

Ndiyeno Dokowe anauza Nkhandweyo kuti, “Tsopano

popeza ndachotsa fupali, ndininkhenitu zimene

munalonjeza zija. Pajatu lonjezo linadulitsa mutu wa

Mpandamachokero Anthology

15
nkhuku!” Itamva zimenezi, Nkhandweyo inamwetulira

n’kuonetsa mano ake, ndipo kenako inati,

“Muziyamika a Dokowe. Inuyotu munalowetsa mutu

wanu m’kamwa mwanga n’kuutulutsamo uli

bwinobwino, popanda vuto lililonse. Ndiye mukuti

mukufuna ndikupatseninso mphoto ina kuposa

imeneyo?”

Phunziro: Munthu wadyera sayamika.

Mafunso

1. Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani

Dokowe anathandiza Nkhandwe?

2. N’chifukwa chiyani Dokowe anauza Nkhandwe

kuti imupatse zimene inalonjeza?

3. Kodi mukuganiza kuti Nkhandwe inaperekadi

mphoto kwa Dokowe? N’chifukwa chiyani

mukutero?

4. Tiyerekeze kuti Nkhandweyo inakana kupereka

mphoto kwa Dokowe, kodi tinganene kuti

inalakwa?

5. N’chifukwa chiyani tiyenera kumachitadi

zimene talonjeza?

6. Kodi nkhaniyi ikutiphunzitsa chiyani?

Mpandamachokero Anthology

16
Mpandamachokero

Kalelo, pamudzi wina panali mkamwini wina yemwe

ankasakasaka chifukwa chopitira kwawo. Anthu a

pamudzipo ankakhala naye bwino zedi. Koma kenako

munthuyu anatopa ndi ulemu, ndipo anayamba

kusakasaka chifukwa chochokera pakhomopo. Ndiye

tsiku lina, ana ankaphika masanje ndipo mkamwiniyo

anapita pomwe anawo anakoleza moto wawo

n’kuukodzera. Anawo anayamba kulira ngati kuti wina

wawatsina, moti akuluakulu a pamudzipo anatuluka

m’nyumba kuti akaone chomwe chachitika. Atafunsa

anawo kuti chachitika n’chiyani, anaulula kuti

mkamwiniyo wawazimitsira moto wawo komanso kuti

anachita kuukodzera. Akuluakuluwo anakhumudwa

kwambiri ndipo anapita kunyumba kwa mkuluyo kuti

akamufunse za nkhaniyo. Atafika, mkamwiniyo

anawalandira n’kuwalowetsa m’nyumba. Anthuwo

anapepesa chifukwa chobwera mwadzidzidzi, koma

mkamwiniyo anati, “Ayi, mwafika mwatha.” Ndiye

kenako anawauza kuti, “Tikupunguleni mpweya!”

Zitatero anthu a pamudzipo anayamba kuyala nkhani

yonse. Koma mkamwiniyo atamva zimene anthuwo

ananena, anakwiya kwambiri ndipo anati: “Zoona

Mpandamachokero Anthology

17
mmene ndakuliramu ndingakodzere moto wa ana?

Anthu inutu simukundifuna pamudzi pano. Basi

ndikupita kwathu.” Kenako anamanga nsanza zake

pachitenje, n’kunyamuka kumapita kwawo.

Phunziro: Anthu ena akatopa kukhala pamalo,

amachita kusakasaka chifukwa chochokera.

Mafunso

1. Kodi vuto la mkamwiniyu linali chiyani?

2. Kodi pali umboni wanji wosonyeza kuti anthu a

pamudziwu anali abwino?

3. Kodi mukuganiza kuti mkamwiniyo

ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti,

“tikupunguleni mpweya”?

4. Kodi mwambi wakuti, “mpandamachokero

adakodzera moto wa ana” unayamba bwanji?

5. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

18
Kusamvana Pakati pa Munthu ndi Njoka

Mwana wa Mlimi wina anaponda mchira wa Njoka

mwangozi, ndipo Njokayo inalusa n’kumugagada, moti

anafera pomwepo. Bambo a mwanayo atamva zimenezi

anakwiya zedi, ndipo ananyamula nkhwangwa

n’kuyamba kuthamangitsa Njokayo. Ataipeza

anaponya nkhwangwayo ndipo anaidula mchira.

Zimenezi zinachititsa kuti njokayo ikwiye zedi, moti

inaganiza zokhaulitsa mlimiyo. Inanyamuka n’kupita

m’khola la mlimiyo n’kukaluma ng’ombe zonse, moti

inasiya mlimiyo manja ali m’khosi, ng’ombe zake zonse

zitafa. Koma kenako mlimiyo anaona kuti kubwezera

sikuthandiza, ndipo anaganiza zokambirana ndi

Njokayo kuti akhazikitse mtendere. Choncho tsiku lina

Mlimiyo anauyamba ulendo wopita kwa Njokayo

atatenga kaphoso ka chakudya komanso uchi, ndipo

atafika anaika zinthuzo pauna wa Njoka n’kuodira.

Njoka itatuluka, Mlimiyo anati, “M’bale wanga njoka,

tiye tiiwale zakale. Ndikuona kuti n’zomveka kuti

unalanga mwana wanga atakuchitira chipongwe.

Komanso n’zomveka kuti unapha ng’ombe zanga

utakwiya chifukwa chodulidwa mchira. Komabe,

popeza ndine bambo wa mwana unapha uja,

Mpandamachokero Anthology

19
sindinalakwe kukudula mchira chifukwa monga

ukudziwira, imfa ya mwana imakhala yowawa

kwambiri. Ndiye popeza aliyense wakhutira ndi zimene

wachitira mnzake, tiye tiiwale zakale n’kuyambiranso

kugwirizana.” Pamenepo Njokayo inati: “Ayi,

sindikufuna. Pita nazo uko zinthu zakozo! Ndikudziwa

kuti sungaiwale imfa ya mwana wako, komanso ineyo

sindingaiwale za mchira wanga, womwe iweyo

unaudula mopanda chisoni.”

Phunziro: Nthawi zina zimatheka kukhululukira

munthu, koma osaiwala zomwe anakuchitira.

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani Mlimi anatenga chakudya

komanso uchi popita kukakumana ndi Njoka?

2. N’chifukwa chiyani Njoka inakana kulandira

mphatso zomwe Mlimiyo anapititsa?

3. Kodi zimene Njokayo inachita ndi zabwino?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

20
Khoswe Wam’tauni ndi Khoswe

Wakumudzi

Kalekalelo Khoswe Wam’tauni anapita kukacheza kwa

msuweni wake, yemwe ankakhala kumudzi. Khoswe

Wakumudziyo anasangalala kwambiri ndi zimenezi

moti anamulandira ndi manja awiri mnzakeyo.

Ngakhale kuti analibe zinthu zambiri, Khoswe

Wakumudziyo anayesetsa kukonzera mnzakeyo

chakudya chabwino. Mwachidule tingoti anamupatsa

zonse zomwe akanakwanitsa. Anamupatsa nyemba,

nyama, mabanzi komanso mtedza. Ndiyeno Khoswe

Wam’tauni uja anasolola mphuno yake n’kuyamba

kununkhiza mosonyeza kuti chakudyacho

chikumunyansa, ndipo kenako anati: “Asuweni

sindimakumvetsani. Kodi mumakwanitsa bwanji

kudya chakudya ngati chimenechi? Koma m’pomveka,

kunoko n’kotsalira kwambiri moti simungakwanitse

kupeza zakudya zonona komanso zabwinozabwino

zomwe zimapezeka m’tauni. Tiyeni tipite kwathu

ndikakuonetseni kukoma kwa moyo. Mukakangokhala

sabata imodzi, mukaona kuti moyo womwe

mukukhala kunowu ndi wofanana ndi kukhala

kundende.” Nthawi yomweyo makoswe awiriwo

Mpandamachokero Anthology

21
anauyamba ulendo wopita m’tauni ndipo anafika

usiku kwambiri kunyumba kwa Khoswe Wam’tauni

uja. Kenako Khoswe Wam’tauniyo anati: “Ukuoneka

kuti waweyeseka ndi ulendo, bwanji ndikupatseko

zokhwasulakhwasula? Tabwera kuno!” Kenako

anagwira mnzakeyo dzanja n’kuyamba kumukoka

kupita naye kuchipinda chodyera. Kumeneko anapeza

kuli zinthu zambiri zomwe zinatsala patebulo moti

sanachedwenso ayi, koma kuyamba kudya makeke

komanso zakudya zina zokhetsa dovu, zomwe

anazipeza m’chipindacho. Koma mwadzidzidzi,

anamva agalu akuuwa. Ndiyeno Khoswe Wakumudzi

anafunsa kuti, “Kodi chimenecho n’chiyani?”

Mnzakeyo anayankha kuti, “Aa, usaope. Amenewo ndi

agalu a m’nyumba muno.” Ndiyeno Khoswe

Wakumudziyo anati, “Wati ndisaope? Kwathu

ndimadya mwamtenderetu ine, moti phokoso limenelo

silikundisangalatsa.” Posakhalitsa chitseko

chinatseguka mwamphamvu ndipo Agalu akuluakulu

awiri anatulukira. Makoswe awiriwo atangoona

agaluwo, anayamba kuthawa pofuna kupulumutsa

miyoyo wawo. Kenako Khoswe Wakumudzi anati,

“Msuweni, ine ndikupita kwathu.” Khoswe

Wam’tauniyo anafunsa mnzakeyo kuti, “Bwanji,

Mpandamachokero Anthology

22
ukufuna kubwerera kumudzi nthawi yomweyi?” Koma

Khoswe Wakumudziyo anati, “Inde, ndikupita. Bola

ndizikadya nyemba komanso mabanzi ndili

pamtendere, kusiyana n’kumadya makeke komanso

zinthu zonona ndili ndi mantha.”

Phunziro: “Ndi bwino kumadya chisoso pali mtendere,

kusiyana ndi kumadya nyama uli ndi mantha.”

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani Khoswe Wakumudzi

anapita m’tauni?

2. N’chifukwa chiyani khosweyu anabwerera

kumudzi?

3. Kodi pali kusiyana kotani pakati pa Khoswe

Wakumudzi ndi Khoswe Wam’tauni?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

23
Nkhadwe Inapusitsa Khwangwala

Tsiku lina Nkhandwe inaona Khwangwala akuuluka.

Khwangwalayo anali atapana nyama kukamwa kwake.

Posakhalitsa Khwangwalayo anatera mumtengo wina

ndipo Nkhandwe inaganiza kuti, “Ndikhozatu

kumuyeretsa m’maso ameneyu.” Kenako inanyamuka

n’kupita pafupi ndi mtengo anatera Khwangwala uja

n’kunena kuti, “Muli bwanji Mayi Khwangwala?

Mukuonekatu bwino lero. Mwatchena suti yokongola

zedi, yomwenso ikugwirizana ndi kakolala koyera

komwe kali m’khosi mwanuko. Mukuonekanso kuti

mukhoza kuimba mwanthetemya kuposa mbalame

zina zonse. Ndiponsotu mawu anu amandisangalatsa

zedi, moti mungachite bwino mutandiimbira kanyimbo

mumakonda kuimba kaja, . . . kamene kaja.

Mukangochita zimenezi, nthawi zonse ndizikupatsani

moni waulemu monga Mfumukazi ya Mbalame zonse.”

Khwangwalayo atamva zimenezi anapusitsika ndipo

anatukula mutu wake n’kuyamba kuimba, amvekere

khwaa! khwaa! khwaa! Koma atangochita zimenezi,

nyama inali kukamwa kwake ija inagwera pansi ndipo

Nkhandwe ija inatola n’kunena kuti, “Zikomo

kwambiri mayi. Zimene ndimafuna ndi zimenezi.

Mpandamachokero Anthology

24
Monga malipiro a nyama ndatengayi, ndikupatsani

malangizo oti adzakuthandizeni m’tsogolo.

Mukadzaona munthu akukutamandani pa chifukwa

chosadziwika bwino, mudzadziwe kuti akufuna

kukupondani.”

Phunziro: Osamakhulupirira anthu achinyengo.

Mafunso

1. Kodi ndi ndani amene anali tambwali pakati pa

Nkhandwe ndi Khwangwala?

2. N’chifukwa chiyani Nkhandwe inapempha

Khwangwala kuti amuimbire nyimbo?

3. Nanga n’chiyani chimene chinakopa

Khwangwala kuti aimbedi nyimboyo?

4. Kodi n’zoona kuti Khwangwala analidi

mbalame yokongola komanso yodziwa kuimba?

5. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

25
Mkango Udwala Mwakayakaya

Nthawi ina Mkango unakalamba kwambiri moti

unayamba kudwala mwakayakaya pakhomo la phanga

lake. Mkangowo unkangokhalira kubuula tsiku lonse

ndiponso unkavutika kupuma. Nyama zina za

m’nkhalango zinabwera kudzazonda matendawo koma

popeza Mkango ndi nyama yoopsa, zinaima chapatali

ndithu. Koma zitaona kuti Mkangowo ulibenso

mphamvu komanso kuti moyo wake wangotsala madzi

amodzi, zinayamba kuyandikira pang’onopang’ono.

Zina mwa nyamazo zinayamba kuganiza kuti,

“Tsopano nthawi yakwana yoti tibwezere zonse zimene

Mkango unatichitira.” Ndiyeno Nguluwe inathamanga

n’kukagunda Mkangowo. Kenako Njati nayonso

inadzambatuka n’kukaubaya ndi nyanga zake. Koma

palibe chimene Mkangowo unachita, unangogona

pansi kwala! Choncho, Bulu ataona kuti Mkango

sungachite kanthu, anapita pafupi ndi Mkangowo

n’kuyamba kuvina kwinaku akugwedezera mchira

wake, ndipo kenako anamenya Mkangowo ndi

miyendo yake yakumbuyo. Mkangowo utaona zimenezi

unalira modandaula kuti, “Apa ndiye ndifa kawiri

ndithu. Zoona kumenyedwa ndi ana omwe?”

Mpandamachokero Anthology

26
Phunziro: Ndi anthu amatha amene amalimbana ndi

munthu wamphamvu akamatsirizika.

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani nyamazi zinkayandikira

pang’onopang’ono?

2. N’chifukwa chiyani nyama zina zinaukira

Mkango?

3. Mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Bulu

anapita komalizira?

4. Kodi kubwezera n’kulakwa?

5. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

27
Bulu Komanso Galu

Tsiku lina Mlimi anapita kukaona ana komanso ziweto

zake. Pakati pa nyamazi panali Bulu. Ndiye pamene

Mlimiyo ankapita kumeneku, n’kuti ali limodzi ndi

Galu wake yemwe ankamukonda kwambiri. Galuyo

ankadumphadumpha n’kumanyambita komanso

kugwira mkono wa Mlimiyo. Kenako Mlimiyo anapisa

m’thumba n’kutenga chakudya n’kupatsa Galuyo,

ndipo kenako anakhala pansi n’kuyamba kupereka

malangizo kwa ana ake. Ndiyeno Galuyo analumphira

pamiyendo pa Mlimiyo ndipo Mlimiyo anayamba

kumusisita. Bulu uja ataona zimenezi anasilira

kwambiri moti anadula chingwe chimene

anamumanga nacho n’kuthamangira kwa Mlimiyo kuti

nayenso akachite chimodzimodzi. Mlimiyo ataona

zimenezi anayamba kuseka ndipo Buluyo ankaganiza

kuti zimene akuchitazo zikumusangalatsa. Ndiye

kenako anaganiza zoti alumphire pamiyendo pa

Mlimiyo n’cholinga choti nayenso amusisite. Koma

chifukwa cha kutalika, Buluyo sanakwanepo, moti

miyendo yake inagwira m’mapewa mwa Mlimiyo. Ana a

Mlimiyo ataona zimenezi anaganiza kuti Buluyo

Mpandamachokero Anthology

28
wachita misala, ndipo anatenga ndodo n’kuyamba

kumuumbudza.

Phunziro: Osamangotengera zilizonse zimene ena

akuchita.

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani Bulu anaganiza zotengera

zochita za Galu?

2. Kodi Buluyo anakumana ndi zotani? Nanga

n’chifukwa chiyani anakumana ndi zimenezo?

3. Kodi n’kulakwa kumangotengera zochita za

ena, bola ngati tikuona kuti zikuwayendera bwino?

4. Kodi tikuphunzirapo chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

29
Khoswe Apulumutsa Mkango

Tsiku lina Mkango ukugona, Khoswe anayamba

kuukwerakwera. Zimenezi zinachititsa kuti Mkangowo

udzidzimuke ndipo unagwira Khosweyo n’kutsegula

kamwa lake kuti ungomuponyera m’kamwa

n’kumutafuna. Koma Khosweyo anakuwa n’kuuza

Mkangowo kuti, “Pepani Mfumu yanga,

ndikhululukireni chonde! Ndimvereni chisoni, ndinetu

mwana wamasiye! Mutandisiya wamoyo kano kokha,

ndikhoza kudzakupulumutsani m’tsogolo!” Mkango

utamva zimenezi unafa nalo phwete ndipo unati,

“Usandiseketse m’kamwa, zoona iweyo kuchepa

kumeneku ungandipulumutse?” Posakhulupirira

zimenezi, Mkangowo unamusiyadi Khosweyo. Ndiyeno

patapita nthawi, Mkango uja unagwidwa pamsampha,

ndipo alenje atauona anaganiza zounyamula n’kupita

nawo kwa mfumu yawo. Kenako anaugwira

n’kuukwidzinga pamtengo n’kupita kukasakasaka

ngolo yoti adzaunyamulire. Alenje aja atangochoka,

Khoswe uja anadutsa pafupi ndi pomwe panali

Mkango uja. Ataona mmene Mkangowo

unkandandaulira, anapita pomwepo n’kuchecheta

chingwe chomwe anaumangira chija, ndipo

Mpandamachokero Anthology

30
chinaduka. Kenako anauza Mkangowo kuti, “Si paja

ndinakuuzani kuti ndikhoza kudzakupulumutsani!

Mwaonatu, osamachepetsa kolemera.” Kenako

ananyamuka n’kumapita.

Phunziro: Nthawi zina anthu onyozeka ndi amene

amathandiza kwambiri.

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani Mkango unasiya Khoswe

kuti apite?

2. Kodi Khoswe anathandiza bwanji Mkango?

Nanga n’chifukwa chiyani anauthandiza?

3. Pakati pa Khoswe ndi Mkango, kodi

mukuganiza kuti ndi nyama iti imene

inaphunzirapo kenakake?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

31
Namzeze Achenjeza Mbalame Zina

Nthawi ina Mlimi anapita kukafesa mbewu ya chamba

m’munda wina womwe Mbalame zinkakonda kukatola

zakudya zake. Ndiye Mbalame ina yotchedwa Namzeze

itaona zimenezi, inayamba kuchenjeza mbalame

zinzake zomwe zinkatola zakudya m’mundawo. Inati,

“Samalani ndi munthu uyo!” Mbalame zinazo

zinamufunsa kuti, “Chifukwa? Kodi zimene akuchitazo

ife zikutikhudza?” Iye anayankha kuti, “Munthuyu

akufesa mbewu yoipa. Musayerekeze kusiya nthangala

ngakhale imodzi ya mbewu zimenezi. Mukapanda

kutero, mudzaona zakuda!” Mbalamezo zinkaona kuti

zimene Namzeze ankakambazo ndi za kuntchini

kwadzaza, moti sizinatsatire malangizowo. Koma

patapita nthawi, mbewuzo zinayamba kukula ndipo

mbalamezo zinayamba kuthothola masamba ake

n’kumakamangira zisa. Pamene mbewu zija zinkacha,

mbalame zosamverazo zinagwidwa zili m’zisa

zopangidwa ndi masamba a chamba, omwe zinatenga

m’munda uja. Mbalame zambiri zinasokonezeka ndi

tsokali ndipo sizinkadziwa chifukwa chimene

munthuyo ankatengera zisa zawo. Ndiyeno Namzeze

anaziuza kuti, “Ndinakuuzani chiyani ine?

Mpandamachokero Anthology

32
Kumachotseratu mbewu yoipa isanamere! Mtsinje wa

tinkanenatu unathera mu si izi.”

Phunziro: Kumachotsa mbewu yoipa isanamere, apo

ayi m’tsogolo imadzabweretsa mavuto.

Mafunso

1. Kodi mbewu yoipa imene namzeze ankanena

inali chiyani? N’chifukwa chiyani mukutero?

2. Kodi namzeze anauza mbalame zinzake kuti

zichite chiyani?

3. N’chifukwa chiyani Mlimiyo ankatenga zisa za

mbalamezo?

4. Kodi mungapereke zitsanzo za zinthu zina

zoipa zimene ngati titazilekerera zikhoza

kutibweretsera mavuto?

5. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

33
Achule Afuna Mfumu

Achule ankakhala mosangalala m’dambo lina

lokongola kwambiri. Nthawi zonse ankangokhalira

kusewera. Ankati akadzuka m’mawa, ankayamba

kuwothera dzuwa komanso kudya, ndipo akamva

kutentha, ankakwera pamwala n’kudziponya m’madzi

kuti mphavaa! Ankakhala kukhosi kuli mbee ndipo

palibe chimene chinkawavutitsa. Komatu ukakhala

pabwino, poipa pamakuitana. N’kupita kwa nthawi

Achulewa anayamba kuona kuti moyo umenewu si

wabwino, moti ankafuna atakhala ndi mfumu

komanso malamulo abwino oti aziyendera. Choncho

anaganiza zokapempha kwa Mulungu kuti awapatse

mfumu yoti iziwalamulira. Iwo anati, “Mulungu wathu

wamkulu, titumizireni mfumu yoti izitilamulira

komanso kutipatsa malamulo oti tiziyendera.”

Mulungu atamva zimene Achulewo ananena, anaseka

ndipo anagwetsa chipika chachikulu chomwe

chinagwera m’dziwe lomwe linali m’dambo lija.

Achulewo anachita mantha kwambiri chifukwa cha

phokoso lomwe linamveka pamene chipikacho

chinkagwera m’madzi, moti onse anathawa n’kupita

kumtunda. Kwa masiku ambiri, Achulewo ankakhala

Mpandamachokero Anthology

34
mwamantha ndipo sankayandikira n’komwe chinthu

choopsa chomwe chinagwera m’madzicho. Koma

patapita nthawi, achulewo anaona kuti chinthucho

sichikutakataka. Ndiyeno Achule ena olimba mtima

anapita pafupi ndi chipika chija, moti ena analimba

mtima n’kuchigwira. Komabe, chipikacho

sichinasunthe. Kenako Chule wina, yemwe

ankadziwika kuti ndi wolimba mtima kwambiri,

analumphira pamwamba pachipikacho n’kuyamba

kuvina, ndipo Achule enanso anayamba kuchita

zomwezo. Izi zitachitika, Achulewo anatha mantha

ndipo anayambanso kukhala monga mmene

ankakhalira kale. Anaiwaliratu zoti Mulungu

anawagwetsera chipika, chomwe chinali ngati mfumu

yawo. Achulewo anayamba kuona kuti mfumuyi ndi

yatulo ndiponso kuti ndi yosawayenera, moti

anaganiza zopitanso kwa Mulungu kuti

akapemphenso mfumu ina. Anati, “Tikufuna mfumu

yeniyeni yoti izitilamulira, osati yomwe ikungoliza

mkononoyi!” Zimenezi zinachititsa kuti Mulungu

akwiye ndipo anatumiza Dokowe. Dokoweyo

anayamba kujompha achulewo n’kumawadya.

Achulewo ataona zimenezi, anachita mantha zedi moti

Mpandamachokero Anthology

35
anayamba kulirira Mulungu kuti awachotsere

chilombocho, koma munali m’mbuyo mwa alendo.

Phunziro: Ndibwino kukhala popanda mfumu

n’kumakhala bwinobwino kusiyana ndi kukhala nayo,

koma n’kukhala yankhanza.

Mafunso

1. Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani

Mulungu anatumiza chipika kwa Achule aja,

m’malo mowapatsa mfumu yeniyeni?

2. N’chifukwa chiyani achule anapitanso

kukapempha mfumu ina?

3. Kodi zangati zimene zinachitikira achulewa

zimachitikanso masiku ano?

4. N’chifukwa chiyani Mulungu anawakwiyira?

5. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

36
Phokoso la Mapiri

Tsiku lina anthu a m’mudzi wina anayamba kumva

phokoso loopsa lomwe linkamveka kuchokera

m’Mapiri ena omwe anali pafupi ndi kwawo. Anthuwa

ankaganiza kuti Mapiriwo akubereka ana. M’Mapiriwo

munkatuluka chiutsi, nthaka inkangoti teketeke,

mitengo inkangogwa komanso miyala inkangosweka.

Iwo ankaona kuti pakhoza kuchitika chinachake

choopsa. Anthuwo anasonkhana pamodzi kuti aone

chomwe chitachitike. Anadikira, kudikira n’kudikira,

koma palibe chinachitika. Kenako panachitikanso

chivomerezi china champhamvu kwambiri moti

nthaka inang’ambika pambali pa phiri lina. Anthuwo

anayamba kuyang’ana mwachidwi m’phangalo ndipo

anapitirizabe kudikira. Kenako anangoona kakhoswe

kakang’ono kakuchokera m’phangalo. Kakhosweko

kankapukuta mutu wake ndi timiyendo take

tating’ono. Kenako kanatuluka n’kumalowera kumene

kunali anthu aja. Kungochokera nthawi imeneyo

anthuwo anayamba kunena kuti, “Pakakhala

chiphokoso chachikulu, zotsatira zake zimakhala

zogwetsa mphwayi.” Ndipo ena ankati, “N’chifukwa

chaketu anthu a kum’mawa amanena kuti, ‘Chidebe

Mpandamachokero Anthology

37
chopanda kanthu chimapanga phokoso kwambiri.’

Mpake kuti ena amaganiza kuti, ‘anthu omwe

sayankhulayankhula ndi amene amaganiza

mwaphokoso zedi!”

Phunziro: Nthawi zina anthu amene amalongolola

kwambiri sachita zanzeru.

Mafunso

1. Kodi Anthu ankaganiza kuti chichitike

n’chiyani?

2. Kodi zimene Anthuwo ankayembekezera

zinachitikadi?

3. Kodi tikuphunzirapo chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

38
Akalulu Akumana Ndi Mavuto

Nthawi inayake Akalulu ankazunzidwa ndi zilombo

zina zosadziwika bwinobwino moti ankasowa

kothawira. Zimenezi zinachititsa kuti akangoona

nyama iliyonse azithawa n’kukabisala. Akaluluwa

anafika potopa ndi zimenezi moti tsiku lina anaganiza

zokangodziponya m’madzi n’kufa. Ndiye ataona Njati

zikuthamanga, Akaluluwo anathawira kudziwe lina

kuti akangodziponya m’madzi n’kulekana nawo moyo

wokhala mwamantha. Ndiye atayandikira dziwelo,

anadzidzimutsa Achule ena omwe ankaothera dzuwa

ndipo nthawi yomweyo Achulewo anadziponya

m’madzi. Kalulu wina ataona zimenezo anati, “Aa!

akuluakulu, mavuto amene tili nawo ifewa, bola.

Taonani anzathuwa! Ndaphunzirapo kanthu.

Ukamakumana ndi mavuto, kumakumbukira kuti pali

ena omwe akukumana ndi mavuto onenepa kwambiri

kuposa ako.”

Phunziro: Ukamakumana ndi mavuto, m’malo

mongoganiza zodzipha, ndi bwino kumakumbukira kuti

pali enanso amene akukumana ndi mavuto kuposa

akowo.

Mpandamachokero Anthology

39
Mafunso

1. N’chifukwa chiyani Akalulu ankafuna

kudziponyera m’madzi?

2. N’chiyani chinawapangitsa kusintha maganizo?

3. Kodi ndi nyama ziti zimene mukuona kuti

nazonso zimachita mantha kwambiri zikaona

Achule?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

40
Ukakwera M’mwamba Usamatukwane

Pansi

Mnyamata wina anakwera padenga la nyumba ndipo

atayang’ana pansi, anaona Nkhandwe ikudutsa pafupi

ndi nyumbayo. Nthawi yomweyo anayamba

kuinyogodola amvekere, “Ndiwe chigawenga komanso

kapsala. N’chifukwa chiyani wabwera kuno kunyumba

za anthu amtendere komanso abwino, kodi ulibe

manyazi? N’chifukwa chiyani umakonda kupita

m’malo amene anthu amadziwa kale makhalidwe ako

ochititsa dambisi?” Itamva zimenezi, Nkhandweyo

inayankha kuti, “Ukhoza kundinyoza mmene

ungathere. Zimakhala zophweka kumadzitukumula

komanso kumachita mwano utakwera padenga.

Ndikulakalaka kuti tsiku lina uzidzabwebwetuka

choncho uli pansipa.”

Phunziro: Osamatha mawu zikakhala kuti zinthu

zikukuyendera. Osamachita chipongwe ukakhala malo

otetezeka, chifukwa nthawi ina udzachokapo.

Mpandamachokero Anthology

41
Mafunso

1. Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani

Mnyamatayu ankanyoza Nkhandwe ali padenga la

nyumba?

2. Kodi mukuganiza kuti nthawi zina anthu

amachitadi zangati zimenezi? Perekani chitsanzo.

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

42
Pansi pa Mtima

Tsiku lina Gondwa anaba nkhuku pakhomo lina ndipo

anakalowa nayo kuphanga lake. Atafika kuphangako

anauza ana ake kuti waba nkhukuyo kukhomo

lapafupi. Koma kuti aiwotche, ankafunika moto. Ndiye

Gondwayo anaganiza zotuma mwana wake kuti

akapale moto kukhomo anaba nkhuku lija. Anamuuza

kuti, “Ndikufuna ukapale moto uko. Koma popeza

nkhukuyi taba komweko, asakadziwe kuti tikufuna

kudzawotchera nkhuku. Ndiye ngakhale

akakukakamize, usakaulule kuti motowo

tikudzachitira chiyani. Koma pansi pamtima

uzingodziwa iweyo kuti tikufuna kudzawotchera

nkhuku.” Kenako mwanayo ananyamuka n’kupita

kukapala moto atatenga chiwaya chake. Atafika

kumeneko, anagogoda ndipo ananena chimene

wabwerera. Anthu amene anawapeza kunyumbako

anayamba kumupanikiza ndi mafunso, amvekere,

“Motowo mukufuna mukachite nawo chiyani?”

Mwanayo anayankha kuti, “Anandiuzatu kuti

ndisadzaulule. Amati ndizingodziwa ndekha, pansi

pamtima wanga, kuti tikufuna kukawotchera

nkhuku.” Anthuwo atangomva zimenezi anazindikira

Mpandamachokero Anthology

43
kuti nkhuku yawo waba ndi Gondwa, ndipo

anathamangitsa mwanayo mpaka kukafika paphanga

lija. Kenako anatenga khasu n’kukumba phangalo

ndipo anapha Gondwa ndi ana ake onse.

Phunziro: Palibe chinsinsi padziko lapansi.

Mafunso

1. Kodi mwana wa Gondwa ananena chiyani

atafunsidwa chifukwa chimene anapitira kukapala

moto?

2. Kodi zimene mwanayo ananena zinali zoona

kapena zabodza?

3. Kodi mwanayu analakwitsa kunena zinthu zina

zimene bambo ake anamuuza kuti angozidziwa

yekha? Ndiye tinganene kuti kunena zoona si

kwabwino?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

44
Njoka Yopanda Pabwino

Chaka china kunazizira kwambiri moti madzi ankatha

kuuma gwa ngati mwala. Ndiye munthu wina, yemwe

ankachokera kunkhalango, anaona njoka yakuda

itagona m’mbali mwa nsewu. Njokayo inkaoneka kuti

yangotsala pang’ono kutsirizika chifukwa cha kuzizira.

Kenako munthuyo anaichitira chifundo ndipo anaitola

n’kuiika mujuzi yake kuti imve kutentha. Atafika

kwawo anaiika pafupi ndi moto kuti itenthedwe. Ana a

munthuyo ankangoiyang’ana. Kenako Njokayo

inayamba kumvako bwino, moti inayambiranso

kuyenda bwinobwino. Ndiyeno mwana m’modzi

anaganiza zoti aisisite, koma atangochita zimenezi,

Njokayo inadzutsa mutu wake kuti imulume.

Munthuyo atangoona zimenezo anatenga nkhwangwa

yake n’kudula Njokayo pakati. Kenako anati, “Anthu

ena alibe pabwino inu! Ukhoza kuwachitira chifundo

koma sayamika, moti amalumanso dzanja limene

likuwadyetsa. Munthu woti ndamupulumutsa,

akufunanso kundiphera mwana!”

Phunziro: Anthu oipa alibe pabwino.

Mafunso

Mpandamachokero Anthology

45
1. N’chifukwa chiyani munthu uja anatola Njoka?

2. N’chifukwa chiyani Njokayo inkafuna kuluma

mwana wa munthuyo?

3. Kodi nkhaniyi ikusonyeza kuti munthuyo

anaphunzirapo chiyani pa zimene zinachitikazo?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

46
Ntchentche Yosimbwa

Kalelo kunali bambo wina wadazi. Bamboyo ankati

akamaliza kudya nsima, ankakonda kukhala

pakhonde kuti aphwetse mkhuto wake. Ndiye tsiku

lina kunabwera Ntchentche n’kuyamba kumusokosa

komanso kumuluma dazi lake. Kenako Ntchentcheyo

inatera padazilo ndipo bamboyo anaganiza zoionetsa

mbwadza poiphwanya ndi dzanja lake. Koma m’malo

moti aphwanye ntchentcheyo, anamenya mutu wake,

ndipo anamva ululu wosaneneka. Ntchentcheyo

inapitirizabe kusimbwa, koma pa nthawiyi, nzeru

zinamubwerera bamboyo moti sanalimbane nayo.

Anati, “Umangodzivulaza wekha ukamalimbana ndi

adani oipa.”

Phunziro: Ukamalimbana ndi munthu woipa,

umavutika ndi iweyo.

Mpandamachokero Anthology

47
Mafunso

1. N’chifukwa chiyani munthuyu anadzimenya

m’mutu?

2. N’chifukwa chiyani anaganiza zongosiya

kulimbana ndi Ntchentcheyo?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

48
Nkhandwe Ichezera Dokowe

Kalekalelo Nkhandwe inali pa ubwenzi wa ponda apo

m’pondepo ndi Dokowe. Ndiye tsiku lina Nkhandweyo

inaitana Dokowe kuti akadye nkhomaliro kwawo.

Koma Dokowe atafika, anapeza kuti wangomuphikira

nsuzi ndipo anauika m’mbale yosalowa. Dokoweyo

anayesetsa kuti amwe nsuziwo koma palibe chomwe

anaphulapo. Nsuziwo unkangothera pamlomo wake

wautali. Analimbana nawo kwa nthawi yaitali ndipo

atatopa anangousiya, koma ali ndi njala kwambiri.

Ndiye popeza paja amati, kwa eni kulibe mkuwo, mutu

wa nkhuku n’chiwalo, dokowe sananene chilichonse.

Anazindikira kuti mnzakeyo anachita izi pongofuna

kumucheza basi. Kenako Nkhandwe inati, “Pepani kuti

ndinakuphikirani nsuzi womwe simumaukonda.

Ndikuona kuti udakali nde, mmene unalili.” Koma

Dokowe anayankha kuti, “Usapepese ambwana,

ndathokoza kwambiri chifukwa cha mtima wako

wochereza alendo.” Kenako ananyamuka n’kuona

msana wa njira. Ndiye tsiku lina, Dokowe nayenso

anaitana mnzakeyu kuti akadye kwawo. Itangomva

uthengawu, Nkhandweyo sinachedwechedwe, moti

inauyamba ulendo wa kwa mnzakeyo. Itafika,

Mpandamachokero Anthology

49
inamupeza akumudikirira ndipo inati, “Ndabwera

bwanawe, paja okuluokulu odati kaitana kachita

ujeni, ukachedwa ungakakapeze katabopha!”

Mnzakeyo anaseka kwambiri ndipo kenako

anamulowetsa m’nyumba kuti akadye zakudya

zokoma zomwe anamukonzera. Zakudyazo anaziika

mumtsuko wa kukamwa kwakung’ono, moti

Nkhandwe sikadantha kulowetsa mutu wake n’kudya

chakudyacho. Nkhandweyo inamva kuwawa mumtima

mwake chifukwa cha zimenezi moti inangoyamba

kunyambita kunja kwa mtsukowo. Ndiyeno Dokowe

anati, “Sindipepesa ndi zimene zachitikazi, mwina

ungaphunzirepo kathu. Nkhonya yobwezeratu

imawawa?”

Phunziro: Tizichitira ena zimene ifenso timafuna

atatichitira.

Mpandamachokero Anthology

50
Mafunso

1. Kodi Nkhandwe inachitira bwanji Dokowe

chipongwe?

2. Nanga Dokowe anachita chiyani atazindikira

zimenezi?

3. Mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani tinganene

kuti Nkhandwe ndi Dokowe sanali mabwenzi a

pamtimadi?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

51
Nkhandwe Itola Chigoba

Tsiku lina Nkhandwe inalowa m’chipinda china

chomwe anthu ochita zisudzo ankasungamo zinthu

zawo. Mwadzidzidzi, Nkhandweyo inaona nkhope ya

munthu ikumuyang’ana ndipo inayamba kuchita

mantha. Koma itayang’anitsitsa bwinobwino inaona

kuti chinali chigoba chomwe ochita zisudzo ankavala

akamachita sewero. Ndiyeno Nkhandweyo inati, “Kani

ndi iweyo? Umaonekatu ngati ndiwe munthu

weniweni. Koma n’zomvetsa chisoni kuti ulibe

ubongo.”

Phunziro: Osamapusitsidwa ndi maonekedwe akunja.

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani Nkhandwe inkachita

mantha itaona chigoba?

2. N’chifukwa chiyani Nkhandweyo inauza

chigobacho kuti, “N’zomvetsa chisoni kuti ulibe

ubongo”?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

52
Timba Atengeka Ndi Mbalame Zokongola

Tsiku lina Timba anapita kukawongola miyendo

kumalo amene mbalame zina zokongola kwambiri

zotchedwa Pikoko zinkakonda kukhala, ndipo anatola

nthenga zososoka za mbalamezo n’kuzimangirira

kuchipsepse chake n’kumayenda moyerekedwa,

kwinaku akulowera kumene kunali mbalamezo. Ndiye

mbalamezo zitamuona, zinakwiya kwambiri moti

zinamugwira n’kumuchotsa nthenga anamanga

kuchipsepse zija. Chifukwa cha manyazi, Timbayo

anabwerera kumene kunali mbalame zinzake, zomwe

zinkaona zimene zinkachitikazo zili chapatali.

Anzakewo anamukwiyira kwambiri ndipo anamuuza

kuti, “Si kukongola kwa nthengatu kumene

kumapangitsa mbalame kukhala yabwino, koma

mtima.”

Phunziro: Maonekedwe akunja sanena zambiri za

mtima wa munthu.

Mpandamachokero Anthology

53
Mafunso

1. N’chifukwa chiyani mbalame zokongola

zinazula nthenga pa chipsepse cha Timba?

2. N’chifukwa chiyani anzake a Timba

anakhumudwa ndi zimene mnzawo anachitazi?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

54
Kudzitama Kunaphetsa Chule

Tsiku lina Chule ndi bambo ake anakhala m’mbali

mwa dziwe n’kumawothera dzuwa. Chuleyo anauza

bambo ake kuti, “Bambo, dzulo ndinaona chinthu

chachikulu koopsa. Chinalitu chachikulu, chachikulu

zedi ngati phiri. Chinali ndi nyanga ziwiri zikuluzikulu

pamutu pake, chimchira chachitali komanso

dzimapazi zikuluzikulu.” Kenako bamboyo anati,

“Takhala chete iwe, imene ukunenayotu ndi Ng’ombe

ya mlimi wa pamtundapo. Koma sikuti ndi yaikulu

mmene ikuneneramo, ukungokokomeza iwe!

Yangokhala yaitaliko pang’ono poyerekeza ndi ineyo,

moti nanenso nditadzifufumitsa ndikhoza kufanana

nayo. Dikira uone . . . .” Kenako Chuleyo anakokera

mpweya n’kudzifufumitsa kwambiri. Ndiyeno anafunsa

mwana wakeyo kuti, “Kodi ng’ombeyo inali yaikulu

chonchi?” Mwanayo anayankha kuti, “Ayi, inali

yaikulu kuposa pamenepo.” Chuleyo anapitirizabe

kukokera mpweya ndipo anadzifufumitsa,

n’kudzifufumitsa kenako n’kudzifufumitsa. Ndiyeno

anafunsa kuti, “Nanga bwanji pamenepo?” Mwanayo

anayankhanso kuti, “Ayi, inali yaikulu, yaikulu

kwambiri kuposa pamenepo.” Ndiyetu Chule

Mpandamachokero Anthology

55
wamkuluyo anakoka mpweya, kuukoka, n’kuukoka

moti anafufuma, kufufuma kenako n’kufufuma.

Ndiyeno anati, “Ndikuganiza kuti Ng’ombeyo sinali

yaikulu kuposa apa . . . ” Atangonena zimenezi, nthawi

yomweyo anaphulika.

Phunziro: Kufuna kuoneka wochenjera kumabweretsa

mavuto.

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani chule wamng’ono

ankaganiza kuti waona chilombo chachikulu

koopsa?

2. Mukuganiza kuti n’chiyani chinachititsa kuti

bambo a Chuleyo asonyeze mwana wakeyo kuti

akhoza kufanana ndi chilombocho?

3. N’chiyani chinapangitsa kuti bamboyo

aphulike?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

56
Ubwenzi wa Mkango ndi Kapolo

Tsiku lina kapolo wina anathawa kwawo n’kulowa

m’nkhalango ina. Pamene ankayendayenda

m’nkhalangomo anakumana ndi Mkango womwe

unkabagula. Atangouona anatembenuka n’kuyamba

kuthawa, koma anadabwa atazindikira kuti mkangowo

sukumuthamangitsa. Kenako anaima n’kubwerera

kumene kunali Mkango uja. Pamene ankauyandikira,

mkangowo unamuonetsa dzanja lake lomwe

linkatuluka magazi. Kapoloyo anaona minga yaikulu

yomwe inabaya mwendo wa mkangowo ndipo

unkamva ululu wosaneneka. Kapoloyo anamva chisoni

kwambiri moti anachotsa mingayo n’kumangapo

nsanza. Atangomaliza kuchita zimenezi, Mkangowo

unadzuka n’kuyamba kunyambita kapoloyo ngati

mmene amachitira galu. Kenako unatenga kapoloyo

n’kupita naye kuphanga lake ndipo tsiku lililonse

unkamubweretsera nyama yoti adye. Koma pasanapite

nthawi, Mkangowo komanso kapoloyo anagwidwa ndi

anthu a kumudzi anathawa kuja. Chifukwa choti

kapoloyo anathawa mbuye wake anaweruzidwa kuti

aphedwe pomusiya kuti adyedwe ndi mkango. Kenako

anasiya Mkangowo osaupatsa chakudya kwa masiku

Mpandamachokero Anthology

57
angapo kuti akadzangoumasura, udzapwepwete ndi

mafupa omwe. Mfumu komanso anthu a m’mudzimo

anasonkhana pabwalo lina kuti aone zimenezi

zikuchitika ndipo asilikali anagwira kapolo uja

n’kumapita naye kumene kunali Mkango kuja. Kenako

asilikali anamasula chingwe chomwe anamangira

Mkangowo ndipo unayamba kuthamanga ukubangula

n’kumapita komwe kunali kapolo uja. Koma

Mkangowo utayandikira, unazindikira kuti ndi bwenzi

lake lomwe linamusamalira atavulala. Moti unagona

pansi pafupi ndi kapoloyo n’kuyamba kunyambita

manja ake monga mmene amachitira galu. Mfumu ya

mudziwo inadabwa ndi zimenezi ndipo inaitanitsa

kapoloyo. Kapoloyo anafotokoza zonse zomwe

zinachitika ndipo Mfumuyo inakhululukira kapoloyo.

Mkango ujanso unamasulidwa n’kupita kunkhalango.

Phunziro: Ukamachitira ena zabwino, nawonso

amadzakuthandiza zikadzakusokonekera.

Mpandamachokero Anthology

58
Mafunso

1. N’chifukwa chiyani kapolo anathandiza

Mkango?

2. N’chiyani chinachititsa kuti Mkango ndi

kapoloyo azigwirizana?

3. Kodi mfumu inaphunzirapo chiyani pamene

kapoloyo anafotokoza zimene zinachitika kuti

Mkangowo usamudye?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

59
Mleme Uchenjera Pogona

Pa nthawi ina, zilombo zakuthengo ndi mbalame

zinayambana moti panakonzedwa zoti pachitike

nkhondo. Ndiye mbalame zinayamba kusonkhanitsa

asilikali ake, nazonso zilombo zinayamba kuchita

chimodzimodzi. Koma Mleme unkakana kulowa ku

gulu lililonse. Mbalame zinkati zikauuza kuti ukhale

msilikali unkati: “Inetu ndili m’gulu la zilombo, siine

mbalame.” Komanso zilombo zikauuza kuti, “Bwera

udzalowe gulu lathu,” ankayankha kuti, “Inetu ndine

mbalame, ndiye ndilowa bwanji m’gulu lanu?” Koma

mwamwayi, nkhondo ija inalephereka ndipo mbalame

komanso zilombo zakuthengo zinagwirizana

zokhazikitsa mtendere. Kenako mbalame komanso

zilombo zija zinakonza phwando lokondwerera kuti

nkhondoyo yalephereka. Ndiye mleme unaganiza

zokasangalala nawo ndipo unapita kumene kunali

mbalame koma mbalame zonse zinagwanda. Kenako

unauluka n’kupita kumene kunali zilombo

zakuthengo. Koma nazonso zinamukana ndipo

zinamuuza kuti akapanda kunyamuka zikuonetsa

zakuda. Mlemewo unadandaula kwambiri ndi zimenezi

Mpandamachokero Anthology

60
ndipo unati, “Ukakhala kuti suli m’gulu lililonse,

umakhala wekha.”

Phunziro: Osamafuna anzathu pakakhala pamtendere.

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani Mleme unakana kukhala

m’gulu la mbalame komanso la zinyama?

2. N’chifukwa chiyani mbalame komanso zinyama

zinakana Mleme atabwera kuti adzasangalale

nawo?

3. Kodi tikuphunzira chiyani pamenepa?

Mpandamachokero Anthology

61
Nkhani ya Mbawala ndi Mlenje

Tsiku lina Mbawala inkamwa madzi ndipo inayamba

kugomera chithunzithunzi chake chomwe

chinkaoneka m’madzi. Kenako inati, “Ndi ndani

winanso amene ali ndi nyanga zokongola chonchi

m’nkhalango muno?” Kenako inayang’ana miyendo

yake n’kunena kuti, “Ndimalakalaka ndikanakhala ndi

miyendo yolongosoka yoti izigwirizana ndi nyanga

zamtengo wapatali zomwe zili m’mutu mwangazi.

Zimandiwawa kwambiri ndikaganizira kuti miyendo

yanga ndi yoonda ngati zotokosera m’mano.” Mawu

amenewa ali m’kamwa, kunatulukira mlenje ndipo

anayamba kuithamangitsa. Koma chifukwa choti

miyendo yake ndi yopepuka, Mbawalayo

inangotsomphoka n’kuthawa, moti posapita nthawi

inali patali kwambiri. Mbawalayo inapitirizabe

kuthamanga ndipo inasiya kuyang’ana komwe

imapita, moti inalowa m’ziyangoyango. Chifukwa cha

kukula kwa nyanga zake, inakanirira

m’ziyangoyangozo ndipo mlenje uja anaipeza

n’kungoitola. Mbawalayo inayamba kulira ndipo

mumtima mwake inkati, “N’chifukwa chiyani

timakonda kunyoza zinthu zomwe zimatithandiza

Mpandamachokero Anthology

62
kwambiri, n’kumakonda zinthu zomwe zikhoza kutiika

m’mavuto?”

Phunziro: Zinthu zimene zimaoneka zonyozeka

m’zimene zimatithandiza kuti tikhale ndi moyo.

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani mbawala inkafuna kukhala

ndi miyendo yokongola?

2. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti Mbawala

igwidwe?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

63
Njoka Ipsa Mtima

Tsiku lina njoka inalowa m’nyumba ya munthu wina

momwe munali zitsulo komanso zinthu zina.

Ikuyenda, njokayo inayamba kukandidwa ndi chitsulo

chinachake, moti inapsa mtima n’kuyamba

kuchimenya. Itaona kuti palibe chimene chimachitika

inangosiya kulimbana ndi chitsulocho n’kumapita.

Inkaona kuti ikhoza kungotaya nthawi yake

kumalimbana ndi chinthu chomwe sichimva

kupweteka.

Phunziro: N’kupanda nzeru kumalimbana ndi chinthu

chomwe sichimva kupweteka.

Mafunso

1. Kodi n’chifukwa chiyani njoka inayamba

kumenya chitsulo?

2. Kodi mungapereke chitsanzo cha zimene anthu

amachita zomwe zimakhala ngati kulimbana ndi

chitsulo?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

64
Mitengo Inadzipweteketsa

Tsiku lina munthu wina anapita kunkhalango

nkhwangwa ili m’manja. Munthuyo ankapita

kunkhalangoko kuti akapemphe nthambi ya mtengo

woti aike kunkhwangwa yakeyo, ndipo anauza

mitengo yomwe anaipeza m’nkhalangomo kuti

imuchitire chifundo n’kumupatsa zomwe amafunazo.

Mitengoyo itamva dandauloli, inafunsa munthuyo kuti

akufuna akachite chiyani ndi nkhwangwayo akaika

nthambiyo. Munthuyo anayankha kuti, “Ndikufuna

ndikachitire zinthu zofunika kwambiri.” Popeza

mitengo inali yachifundo, inapatsa munthuyo zomwe

ankafuna. Kenako munthuyo anatenga mtengowo

n’kuika kunkhwangwayo ndipo anayamba kugwetsa

mitengo ya m’nkhalangomo. Mitengoyo itaona zimenezi

inayamba kudandaula kuti sinaganize bwino popereka

kwa mdani wawo chida choti awaphere.

Phunziro: Osamapereka chida kwa mdani wako

chifukwa akhoza kukuphera chomwecho.

Mpandamachokero Anthology

65
Mafunso

1. Kodi mukuganiza kuti mitengo sinkadziwa

chimene munthuyo ankafuna kuchita ndi

nkhwangwa yomwe inali m’manja mwake?

2. Kodi mitengo ikanapewa bwanji mavuto amene

anabwera pambuyo pake?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

66
Galu Akumana ndi Nkhandwe

Nkhandwe inali itatheratu chifukwa cha njala pamene

inakumana ndi Galu wina yemwe ankangodziyendera.

Galuyo anati: “Oo! kodi ndi abwenzi? Inetu

ndinkadziwa kuti moyo wanu wosakhazikikawu

udzakubweretserani mavuto. Mufa ndi njalatu! Bwanji

osamagwira ntchito ngati mmene ndimachitira ine kuti

muzipatsidwa chakudya nthawi zonse?” Nkhandweyo

inati, “Apo ndiye sindingakutsutse m’bale wanga.

Ngati mwayi utapezeka ndikhoza kuchita zomwezo.”

Kenako Galuyo anati, “Tiye tipite kwa abwana anga

ndipo uzikagwira ntchito imene ndimagwira. Ngati

utamakagwira ntchito molimbikira, ukhoza

kudzakhala Nkhandwe yodya bwino.” Kenako nyama

ziwirizi zinauyamba ulendo wopita kunyumba kwa

galu. Koma zili m’njira, Nkhandwe inaona kuti pakhosi

pa Galu panali poperepeseka ndipo inafunsa kuti,

“Kodi khosi lakoli linatani bwanawe?” Galuyo

anayankha kuti, “Aaa, ndi mmene lilili. Pamenepa

m’pamene pamadutsa kolala. Pakolala imeneyo ndi

pamene amakolekapo chingwe chomwe amandimanga

nacho ndikamagwira ntchito usiku. Nthawi zina

chimapana pakhosipa ndithu, n’chifukwa chake

Mpandamachokero Anthology

67
ubweya wina wasosokapo. Koma aa ndi zazing’ono,

ukazolowera monga mmene ndinachitira ineyo.”

Kenako nkhandweyo inati, “Umenewotu ndi moyo

wovuta, kwathu timakhala mwaufulu ife. Basi tionana,

ndikupita kwathu ine.”

Phunziro: Ndibwino kumaonda uli paufulu kusiyana

ndi kumanenepa uli kapolo.

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani Galu ankafuna kuthandiza

Nkhandwe?

2. N’chifukwa chiyani Nkhandwe inaganiza

zokana mwayi wa ntchito womwe Galu

anamupezera?

3. Kodi pali nthano iliyonse yomwe munaimvapo,

yomwe ikugwirizana ndi nkhaniyi?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

68
Ziwalo Ziukira Mimba

Tsiku lina ziwalo za thupi zinakwiya kwambiri.

Ziwalozi zinkaona kuti zimagwira ntchito yotopetsa,

pomwe mimba imangokhala, koma n’kumadya

zakudya zonse. Choncho zinachita msonkhano ndipo

zitakambirana, zinagwirizana kuti zinyanyale ntchito.

Zinanena kuti ziyambiranso pokhapokha mimba

ikavomera kuti izigwira nawo ntchito. Ndiyeno kwa

masiku angapo, mikono inkakana kunyamula

chakudya kupititsa pakamwa. Nalonso kamwa

linkakana kulandira chakudya. Zimenezi zinachititsa

kuti mano azisowa ntchito yoti agwire. Kenako ntchito

zonse zinaimiratu. Koma patatha masiku atatu, ziwalo

zija zinayamba kufooka. Manja ankalephera kusuntha

komanso miyendo inkalephera kuima. Pamapeto pake

ziwalozo zinaona kuti nayonso mimba inkagwira

ntchito yotamandika zedi, ngakhale inali yosaonekera.

Zinaonanso kuti chiwalo chilichonse chimagwira

ntchito yaikulu kuti zinthu ziziyenda bwino.

Phunziro: Mgwirizano umathandiza kuti zinthu

ziyende.

Mpandamachokero Anthology

69
Mafunso

1. Kodi ziwalo zina zija zinkafuna kuti mimba

izichita chiyani?

2. Kodi zinachita chiyani pofuna kukakamiza

mimba kuti nayonso izigwira ntchito?

3. Kodi ziwalo zinazo zinaphunzirapo chiyani?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

70
Mlimi Agwira Gwape Atabisala

Tsiku lina Mlenje ankathamangitsa Gwape ndipo

anam’tengetsa kwambiri moti anangotsala pang’ono

kumugwira. Koma Gwapeyo anathawa n’kukalowa

m’nkhola la mlimi wina n’kudzikwirira ndi zakudya za

Ng’ombe. Miyendo yake yokha ndi imene inkaonekera.

Kenako Mlenje uja anafika pakhomo pa Mlimiyo ndipo

anafunsa mwana wa pakhomopo kuti, “Kodi unaona

Gwape atadutsa apa?” Mwanayo ananena kuti

sanamuone ndipo anayang’anayang’ana m’nkhola

komanso malo ena a pafupi koma sanamupeze.

Ataona kuti zamuvuta, Mlenjeyo anaona msana wa

njira. Kenako Mlimi yemwe anali mwini malowo

anatulukira ndipo atayang’ana m’khola la ng’ombelo

anaona kuti simukuoneka mmene mumaonekera

nthawi zonse. Anayamba kuloza kumene kunali

zakudya za Ng’ombe kuja n’kunena kuti, “Kodi

mitengo ikuoneka pali zakudya za Ng’ombepo ndi ya

chiyani?” Kenako mwana wake uja anapita pamene

panali zakudyazo ndipo atakoka mitengoyo

anangozindikira kuti akukoka Gwape.

Phunziro: Chule anadabwa m’madzi muli mwake.

Mpandamachokero Anthology

71
Mafunso

1. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti Mlimiyu

agwire Gwape?

2. Kodi n’chifukwa chiyani mnyamata uja

komanso Mlenje uja analephera kuona Gwapeyo?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

72
Nkhandwe M’munda wa Mpesa

Tsiku lina Nkhandwe inkayenda m’munda wina ndipo

inafika pamalo ena pomwe panali zipatso za mpesa

zomwe zinkaoneka kuti ndi zakupsa, koma kungoti

zinali zitayanga pamtengo wautali. Itaona mphesazo,

Nkhandweyo inati, “Ndidye mpesazi kuti ndiphe

ludzu.” Kenako inabwerera m’mbuyo n’kudumpha,

koma sinafike pamene panali mpesazo. Inabwereranso

m’mbuyo koma inaphonyanso. Inachita zimenezi

kambirimbiri, koma palibe chomwe inaphulapo.

Kenako inatopa ndipo inanyamuka n’kumapita kwawo

itaimika mphuno zake m’mwamba, kwinaku ikunena

kuti, “Ndikuganiza kuti mphesa zimenezi ndi zowawa.”

Phunziro: Zimakhala zosavuta kumanyoza zinthu

zomwe zakukanika kuzipeza.

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani Nkhandwe inasiya mpesa?

Kodi tinganene kuti simazifuna?

2. N’chifukwa chiyani nkhandweyo inanena kuti

mphesazo zinali zowawa?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

73
Ikakuthawa Imawawa Msuzi

Munthu wina anagwira Njiwa ndipo anasangalala

kwambiri chifukwa ankadziwa kuti nsima ya tsiku

limenelo ikayenda. Koma ali mkati moganiza zimenezi,

Njiwayo inamupulumuka n’kuthawa. Munthuyo

anapsa mtima n’kuyamba kuikuwira Njiwayo

n’kumaiuza kuti, “Iweeeeeeeee, umawawa msuzi!”

Phunziro: Osamanyoza chinthu chikapita.

Mafunso

1. Kodi munthuyu ankaganiza zochita nayo

chiyani Njiwa anagwirayo?

2. N’chifukwa chiyani Njiwayo itamupulumuka

anaikuwira n’kuiuza kuti imawawa nsuzi?

3. Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani

anthu amanyoza chinthu chikapita? Chimakhaladi

kuti ndi choipa? Fotokozani.

4. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

74
Hatchi Akhaulitsa Mphoyo

Kalekalelo Hatchi ndi Mphoyo zinayambana, ndiye

Hatchi anapita kwa Mlenje n’kumupempha kuti

amuthandize kukhaulitsa Mphoyo. Mlenjeyo

anavomeradi, koma anati: “Ngati ukufunadi kuti

ndikuthandize kukhaulitsa mdani wakoyu, uyenera

kumvera zimene nditakuuze. Undilole kuti

ndizikutsogolera komanso ndimangirire chingwe ichi

pakamwa pako kuti ndikakwera pamsana pakopa

ndizichigwira kuti ndisagwe. Komanso ndiike chishalo

ichi pamsana pako n’cholinga choti ndisamamve

kupweteka ndikakhalapo.” Hatchiyo inagwirizana ndi

zimenezi ndipo Mlenjeyo anachitadi zomwe

anapanganazo. Zitatero, mothandizidwa ndi Mlenjeyo,

Hatchiyo inakhaulitsadi Mphoyo ija. Kenako Hatchi

inauza Mlenjeyo kuti, “Popeza zimene timafuna

zatheka, tsikatu pamsana pangapa komanso chotsa

chingwe wandimanga pakamwachi. Chotsanso

chishalo chili pamsanachi.” Koma Mlenjeyo anati,

“Osathamanga magazi a Hatchi, ndikusangalala

kwambiri kukhala pamwamba pano, moti uiwale zoti

nditsikapo.”

Mpandamachokero Anthology

75
Phunziro: Ngati utavomera kuti anthu akugwiritse

ntchito pokwaniritsa cholinga chako, nawonso

amakugwiritsa ntchito pokwaniritsa cholinga chawo.

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani Hatchi inapita kwa Mlenje?

2. N’chifukwa chiyani Mlenje anathandiza Hatchi?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

76
Mbalame Yadyera

Tsiku lina mbalame ina yotchedwa Pikoko inapita kwa

Mulungu kukapempha kuti aipatse mawu anthetemya

oti azigwirizana ndi kukongola kwake. Mulunguyo

atamva pempho la mbalameyi anakana kuichitira

zimene inkafunazo. Koma mbalameyi inakakamirabe

ndipo inauza mulunguyo kuti amuchitire zimene

amafunazo basi. Pofuna kukakamiza Mulunguyo kuti

achite zimene inkafunazo, mbalameyi inauza

Mulunguyo kuti amuchitire chifundo chifukwa

m’mbuyomo mulunguyo anali atanenapo kuti

mbalameyo ndi yokongola komanso yokondedwa

kwambiri kuposa mbalame zonse. Koma Mulunguyo

anaiuza mbalameyo kuti, “Uzikhutira ndi zimene uli

nazo. Sungakwanitse kupeza chilichonse chimene

ukufuna, komanso sungakhale katswiri pa

chilichonse. Kusayamika bwanji, kukongolako

sikumakukwanira?”

Phunziro: Palibe munthu amene amadziwa zonse.

Palibe munthu amene amakhala katswiri pa

chilichonse.

Mpandamachokero Anthology

77
Mafunso

1. Kodi mbalameyi inkafuna kuti Mulungu

aichitire chiyani?

2. N’chifukwa chiyani Mulungu anakana?

3. Kodi tikuphunzirapo chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

78
Chizolowezi Chimabala Mwano

Nkhandwe ina inamva zoti Mkango ndi woopsa

kwambiri komanso kuti ndi Mfumu ya Nyama zonse.

Ulendo woyamba umene Nkhandweyi inakumana

nawo, inachita mantha kwambiri moti inaliyatsa liwiro

n’kukabisala m’nkhalango. Koma itakumananso ndi

Mkangowo ulendo wachiwiri, inaima patali

n’kumauyang’ana ukudutsa. Koma kenako inatha

mantha, ndipo itakumana nawonso ulendo wachitatu,

inayamba kuyenda n’kumapita kumene kunali

Mkangowo ndipo inaufunsa kuti mkazi ndi ana ake ali

bwanji. Inafunsaso Mkangowo kuti, “Kodi

tidzakumananso liti?” Kenako inatembenuka

n’kumapita, kwinaku ikuyendetsa mchira wake

mwamwano.

Phunziro: Ukazolowerana ndi munthu umasiya

kumulemekeza.

Mpandamachokero Anthology

79
Mafunso

1. N’chifukwa chiyani Nkhandwe inachita mantha

itakumana koyamba ndi Mkango?

2. Kodi Nkhandwe inkachitanso mantha

itakumana ndi Mkango ulendo wachitatu?

N’chifukwa chiyani sinkachita mantha? Kodi

Mkangowo unali utasintha?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

80
Munthu Atsutsana ndi Mkango

Tsiku lina Munthu ndi Mkango ankakambirana kuti

wamphamvu ndi ndani pakati pawo. Munthuyo

ankanena kuti anthu ndi amphamvu kwambiri kuposa

Mikango chifukwa ali ndi nzeru zambiri. Ndiyeno

Munthuyo anauza Mkangowo kuti, “Tabwera kuno

ndikuonetse chinthu chinachake kuti umvetse zoti

anthu ali ndi mphamvu zoopsa.” Kenako anatengana

ndi Mkangowo n’kupita nawo pamalo ena, ndipo

anauonetsa chipilala cha Samisoni akukhadzula

kamwa la Mkango ndi manja. Kenako Mkangowo

unati, “Chabwino, koma zimene wandionetsazi si

umboni woti anthu ndi amphamvu kuposa Mikango.

Si, anthu ndi amene anapanga chipilalachi?”

Phunziro: Munthu akhoza kukhotetsa nkhani kuti

igwirizane ndi maganizo ake.

Mpandamachokero Anthology

81
Mafunso

1. Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani

chipilala chinkasonyeza kuti Munthu ndi

wamphamvu kuposa Mkango?

2. Kodi mukuganiza kuti Mkango ukanapanga

chipilalacho, chikanakhala chosiyana ndi

chimenechi? Nanga bwenzi chikuoneka bwanji?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

82
Nyerere Yanzeru

Tsiku lina Chiwala chinkadumphadumpha, muluzi uli

pakamwa ndipo chinkaoneka kuti sichikudandaula

chilichonse. Kenako Nyerere inadutsa itanyamula

thumba la chakudya ndipo inali ili thukuta

kamukamu. Nyerereyi inkagwira ntchito yolemetsayi

chifukwa inkafuna kuti isunge chakudya chambiri

kuphanga lake kuti mvula ikadzayamba kugwa

isadzavutike. Ndiye Chiwala chinafunsa nyerereyo

kuti, “Bwanji osabwera kuti tidzacheze,

ukudzizunziranji chotere ngati kapolo? Sunamvepo

mwambi wakuti, papsa tonola sudziwa mtima

wamoto? Ndani akudziwa ngati mawa tidzukenso?”

Nyerereyo inayankha kuti, “Ndikusonkhanitsa

chakudya choti ndidzadye mvula ikadzayamba.

Nawensotu ungachite bwino kuchitiratu zimenezi

nthawi ikadalipo.” Ndiyeno Chiwalacho chinayankha

mwamwano kuti, “Ndivutikirenji kusunga chakudya

choti ndidzadye mvula ikadzayamba, pomwe panopa

chakudya chilipo kutapa kutaya!” Itamva zimenezi,

Nyerereyo sidayankhe, inangopitirizabe kututira

chakudya kuphanga lake. Pamene mvula inkayamba

Chiwala chinalibe kalikonse ndipo pakhomo pake

Mpandamachokero Anthology

83
panali galu wakuda. Chiwalacho chinkasirira chikaona

Nyerere ikugawana chakudya ndi ana ake ndipo

chinati, “Ukakhala ndi zambiri, ndi bwino kumasunga

zina zoti udzagwiritse ntchito zikadzakuvuta.”

Phunziro: Ukakhala ndi zochuluka kumasungako zina

kuti udzagwiritse ntchito ukadzakumana ndi mavuto.

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani Nyerere inauza Chiwala

kuti chisunge chakudya choti idzagwiritse ntchito

m’nthawi yamvula?

2. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

84
Mtengo ndi Bango

Tsiku lina Mtengo unauza Bango lomwe linamera

pafupi ndi phazi lake kuti, “Mwana iwe, n’chifukwa

chiyani suzika kwambiri mizu yako n’kuimika mutu

wako m’mwamba ngati mmene ndimachitira ine?”

Bangolo linayankha kuti, “Ayi, ndimakhutira ndi

mmene ndilili komanso zomwe ndimakwanitsa

kuchita. Mwina ndimaoneka wofooka, koma ndimaona

kuti ndimatetezeka mwa njira imeneyi.” Mtengo

utamva zimenezi, nkhope yake inachita tsinya ndipo

unati, “Umatetezeka? Iweyotu ndi woonda kwambiri

moti umangokhala ngati uli ndi matenda a

kaliondeonde, kathupi kako kamangoti

lobodolobodooo. Mphepo ikamawomba umangoti

tepatepa. Komansotu ndiwe wosavuta kuzula. Koma

taona ifeyo, amunamuna ogona kukhomo kosatseka.

Ndani angalimbe mtima kuti andizule ndi mitsitsi

yomwe? Komanso ndi ndani amene angalimbe mtima

kuweramitsa mutu wanga pansi?” Mawu amenewa ali

m’kamwa, kunabwera chimphepo champhamvu ndipo

mphepoyo inazula Mtengo uja ndi mitsitsi yomwe moti

Mtengowo unangoti lambaaa, mutu utaloza pansi.

Koma Bango lija linangopindikira kumene kumalowera

Mpandamachokero Anthology

85
mphepo ndipo mphepoyo itadutsa, linadzukanso

n’kukhala tsonga. Kenako linafunsa Mtengo uja kuti,

“Waona, tsopano wamphamvu ndi ndani?”

Phunziro: Osamadzitama.

Mafunso

1. Kodi Mtengo unauza Bango zinthu zotani?

2. N’chifukwa chiyani Bango linkaona kuti ndi

lotetezeka?

3. Kodi mukuganiza kuti kudzitama

kumabweretsa mavuto otani?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

86
Nkhandwe Yatulo

Tsiku lina Nkhandwe inkacheza ndi Mphaka ndipo

inayamba kudzitama n’kumanena kuti imadziwa

kuzemba komanso kuthawa adani ake. Inati:

“Sungakhulupirire, mwina ndingonena kuti ndili ndi

kathumba kosatsegula ka njira zosiyanasiyana zomwe

ndikhoza kugwiritsa ntchito pothawa adani anga.

M’thumba limenelo muli njira zoposa 100 zomwe

ndikhoza kusankha imene ndikufuna kugwiritsa

ntchito.” Koma Mphaka anati, “Ineyo ndili ndi njira

imodzi basi, komabe imandipulumutsa adani anga

akamandithamangitsa.” Nthawi yomweyo panayamba

kumveka phokoso la agalu ndipo linkamveka kuti

likubwera kumene kunali Nkhandwe ndi Mphaka

kuja. Mphaka atamva phokosolo, nthawi yomweyo

anathawira mumtengo n’kukabisala, ndipo anauza

Nkhandweyo kuti, “Ine ndimagwiritsa ntchito njira

imeneyi. Nanga iweyo ugwiritsa ntchito njira iti?”

Kenako Nkhandweyo inayamba kuganizira za njira

yoyamba n’kuona kuti sikugwira. Inaganizira za njira

ina n’kuonanso kuti sikugwira. Inapitirizabe

kuganizira njira zina ndipo pa nthawiyi agalu aja anali

akuyandikira. Kenako Nkhandweyo inasokonezeka

Mpandamachokero Anthology

87
ndipo agaluwo anaigwira moti mwini agaluwo anaipha.

Pamene zimenezi zinkachitika, mphaka uja

ankangoonerera ndipo anati, “Bola kukhala ndi njira

imodzi yothandiza, kusiyana ndi kukhala ndi njira

zambirimbiri zomwe ukungoganiza kuti zikhoza

kukuthandiza.”

Phunziro: Ndi bwino kukhala ndi chinthu chimodzi

chothandiza, kusiyana ndi kukhala ndi zambiri zomwe

sizingakuthandize.

Mafunso

1. Kodi Nkhandwe inauza Mphaka chiyani?

2. N’chifukwa chiyani Nkhandwe inalephera

kuthawa agalu?

3. Kodi tikuphunzirapo chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

88
Mmbulu Inavala Chikopa cha Nkhosa

Pa nthawi ina, Mmbulu unkakhaula ndi njala

chifukwa zinali zovuta kuba Nkhosa. M’busa wa

Nkhosazo anali watcheru kwambiri komanso anali ndi

galu woopsa yemwe sankanyengerera akaona nyama

ina ikuyandikira Nkhosa. Koma tsiku lina, Mmbuluwo

unatola chikopa cha Nkhosa chomwe chinatayidwa,

ndipo inavala chikopacho n’kulowa m’gulu la Nkhosa

zija. Choncho mkazi wa Nkhosa yomwe inaphedwayo,

anayamba kuchita chidwi ndi Mmbuluwo

n’kumaganiza kuti ndi mwamuna wake. Ndiyeno

Mmbuluwo unayamba kulowera kwina, kuchoka pa

gulu la Nkhosalo ndipo Nkhosa yaikaziyo

inkangotsatira. Kenako Mmbuluwo unagwira

Nkhosayo n’kuidya. M’kupita kwa nthawi unazolowera

kuba nkhosa mwa njira imeneyi, moti inadya nkhosa

zambiri m’busa komanso galu uja osadziwa.

Phunziro: Maonekedwe amapusitsa.

Mpandamachokero Anthology

89
Mafunso

1. Kodi Mmbulu unapusitsa bwanji Nkhosa?

2. N’chiyani chinachititsa kuti Nkhosa yaikazi ija

iganize kuti Mmbuluwo ndi mwamuna wake?

3. Mungapereke zitsanzo cha zinthu zina zomwe

zimaoneka ngati ndi zabwino koma zili zoopsa?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

90
Galu Apezeka Modyera Ng’ombe

Tsiku lina Galu anatopa kwambiri ndipo ankafuna

atabako tulo. Ndiye anakalowa m’khola la Ng’ombe

n’kudziponya pamene panali zakudya za ng’ombezo.

Pasanapite nthawi, Galuyo anayamba kuliza

mkonono. Koma pa nthawiyi m’pamene Ng’ombe

inatulukira ili ndi njala zedi ndipo sinachedwenso,

koma kupita pamene panali zakudya zake. Ng’ombeyo

inadzutsa Galu uja n’kumusokonezera maloto ake

okoma. Galuyo anapsa mtima ndi zimenezi ndipo

anayamba kuuwa, wuuuuuuuuu! Uwuuuuu!

Ng’ombeyo imati ikati iyandikire zakudya zakezo,

Galuyo ankauwa kwambiri ndipo ankafuna kuiluma.

Kenako Ng’ombeyo inangomusiya ndipo inanyamuka

n’kumapita kwinaku ikung’ung’udza kuti, “Aa, anthu

ena amakonda kulusira anzawo pa zinthu zomwe

sizingawathandize n’komwe.”

Phunziro: Anthu ena amayambana ndi anzawo pofuna

kuteteza zinthu zomwe sangazigwiritse ntchito

komanso sizingawathandize.

Mpandamachokero Anthology

91
Mafunso

1. Kodi Galu ankagwiritsa ntchito bwanji zakudya

za Ng’ombe zija?

2. N’chifukwa chiyani Ng’ombe inapita pamene

Galu uja anagona?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

92
Fano Lathabwa

Kalekalelo, anthu ena ankalambira miyala komanso

mafano. Ankapempha milungu yawoyi kuti iwadalitse

komanso iwathandize kupeza zimene akufuna pamoyo

wawo. Koma panali munthu wina yemwe anali

kwakwatuke wotheratu. Munthuyu ankapempha

mulungu wake wathabwa kuti amuthandize, koma

palibe chimene chinkachitika. Bambo ake ndi amene

anamupatsa fanolo ngati cholowa. Munthuyu

samatopa kupempha mulungu wakeyo kuti amupatse

mwayi. Anachita zimenezi kambirimbiri, koma

zinkangokhala ngati akulimbana ndi mtunda wopanda

madzi. Tsiku lina, munthuyo anapsa mtima ndi

mulungu wakeyo ndipo anamumenya mwamphamvu

ndi chibakera ndipo mulunguyo anagwa pansi

n’kusweka. Mkati mwa mulunguyo munatuluka

ndalama zambirimbiri ndipo zinangoti mbweee

m’nyumbamo. Munthuyo anangogwira pakamwa

chifukwa chosowa chonena, ndipo anazindikira kuti

bambo ake ndi amene anaika ndalamazo mkati mwa

fanolo.

Phunziro: Kulambira mafano kapena zinthu zina

n’kosathandiza chifukwa zilibe moyo. Sizingakuuze

Mpandamachokero Anthology

93
ngakhale zitakhala kuti munthu wina wabisa chuma

mkati mwake. Lemba la Yesaya 44:14-17 limati: Pali

munthu amene ntchito yake ndi yogwetsa mitengo ya

mkungudza. Iye amasankha mtengo wamtundu

winawake, waukulu kwambiri, n’kuusiya kuti ukule

n’kukhwima pakati pa mitengo ya m’nkhalango. Iye

anabzala mtengo wa paini, ndipo mvula yaukulitsa

kwambiri. Tsopano mtengowo wafika poti munthu

akhoza kuusandutsa nkhuni. Chotero iye watenga

mbali ya mtengowo kuti asonkhere moto woti aziwotha.

Wayatsa motowo n’kuphikapo mkate. Wasemanso

mulungu woti azimugwadira. Mtengowo waupanga

chifaniziro chosema ndipo akuchigwadira

n’kumachilambira. Hafu ya mtengowo waitentha

pamoto. Hafu ina ya mtengowo wawotchera nyama

imene wadya, ndipo wakhuta. Wawothanso moto wake

ndipo wanena kuti: “Eya! Ndafundidwa. Ndaona

kuwala kwa moto.” Koma mtengo wotsalawo

wapangira mulungu, wapangira chifaniziro chake

chosema. Wachiweramira ndi kuchigwadira

n’kumapemphera pamaso pake kuti: “Ndipulumutseni,

pakuti ndinu mulungu wanga.” Munthu ameneyutu ndi

wachaba. Chinthu wapanga yekhacho!

Mpandamachokero Anthology

94
Mafunso

1. Kodi munthuyo ankafuna kuti mulungu

wakeyo amuchitire chiyani?

2. N’chifukwa chiyani munthuyo anapsa mtima?

3. Kodi tinganene kuti mulungu wakeyo

anamuthandizadi?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

95
Msodzi

Tsiku lina Msodzi anatenga chitoliro chake komanso

ukonde wake n’kupita kumtsinje kuti akagwire

nsomba. Atafika kumeneko, anapemphera kuti

nsomba zibwere pamene anaika ukonde wakewo,

koma palibe inabwera kapena kuonetsa mphuno yake

pamwamba pa madzi. Kenako Msodziyo anakokera

ukonde wakeyo chakumtunda ndipo

anapempheranso. Mwadzidzidzi anangoona kuti mu

ukondewo nsomba zayamba kuyenda pamwamba pa

madzi komanso zina zikuphiriphitha, ndipo anati, “Aa,

mwayamba kuvina ine ndikupemphera?” Ndiye

nsomba yokalamba pa zonsezo inati, “Ukagwidwa ndi

munthu wamphamvu, umafunika kumachita zimene

akufuna.”

Phunziro: Osamachita masewera ndi anthu

amphamvu.

Mafunso

1. Msodziyo atagwira nsomba zija ndi ukonde

wake, n’chifukwa chiyani nsomba zinayamba

kuchita zimene msodziyo ankafuna? N’chifukwa

chiyani mukutero?

Mpandamachokero Anthology

96
2. Kodi nsombazo zinkafunadi kuvina?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

97
Mnyamata Wabodza

Kalekalelo kunali mnyamata wina yemwe ankaweta

nkhosa yekhayekha pafupi ndi nkhalango ina

yowirira. Mnyamatayu ankasowa wocheza naye ndipo

ankangokhala yekhayekha tsiku lonse. Ndiye tsiku

lina anapeza nzeru yomuthandiza kuti azisangalalako

komanso kuti anthu azibwera n’kukhala naye pafupi.

Anathamanga kumalowera kumene kunali mudzi

wakwawo kwinaku akukuwa kuti, “Kuli Mikango, kuli

Mikango kunoooooooooo!” Ndiye anthu a m’mudzimo

anathamanga kudzakumana naye ndipo ena a iwo

anaima limodzi naye kwa kanthawi

n’kumamuyankhulitsa, moti panthawiyi

sankasungulumwanso. Zimenezi zinamusangalatsa

kwambiri, moti patapita masiku angapo, anachitanso

chimodzimodzi. Ulendo umenewunso anthu a m’mudzi

uja anabwera ndipo anakhala naye limodzi kwa

nthawi yaitali ndipo mnyamatayo anasangalalanso

kwabasi. Kenako anadzachitanso chimodzimodzi ndipo

anthu a m’mudzi uja anatopa naye ndipo

anam’tulukira kuti akungowapusitsa. Koma tsiku lina

Mikango inatulukadi m’nkhalango ija ndipo inayamba

kugwira Nkhosa zake. Mnyamatayo anayambanso

Mpandamachokero Anthology

98
kukuwa kuti, “Kuli Mikango, kuli Mikango

kunoooooooooo!” Anakuwa kwambiri kuposa

poyamba, koma palibe anabwera. Anthuwo

ankaganiza kuti mnyamatayo akungowanamiza ngati

mmene anachitira maulendo ena aja. Mikangoyo

inadya Nkhosa zambiri ndithu, ndipo itakhuta

inabwerera m’nkhalango muja. Mnyamatayo

anabwerera kumudzi kuja kwinaku akulira ndipo

atafotokoza zimene zinachitika. Ndiyeno munthu wina

wachikulire anamuuza kuti, “Anthu sakhulupirira

munthu wabodza, ngakhale atakhala kuti akunena

zoona.”

Phunziro: Ukamanama anthu amakuzolowera, moti

tsiku lina ukamadzanena zoona,

samakukhulupiriranso.

Mpandamachokero Anthology

99
Mafunso

1. N’chifukwa chiyani mnyamatayu ananena

bodza?

2. Kodi ndi mavuto ena ati amene akanabwera

chifukwa cha bodza la mnyamatayu? Kodi

tinganene kuti moyo wake unali pangozi?

3. N’chifukwa chiyani anthu a m’mudzi uja

sanakhulupirire ulendo womaliza womwe

mnyamatayu ananena kuti kukubwera Mikango?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

100
Mpikisano wa Pakati pa Dzuwa ndi Mphepo

Tsiku lina Mphepo komanso Dzuwa zinkatsutsana

kuti wamphamvu ndi ndani pakati pawo. Mphepo

inauza mnzakeyo kuti, “Inetu ndi wamphamvu zedi,

ndimatha kuyalula denga la nyumba, kuzula mitengo

komanso kugwetsa zinthu zikuluzikulu. Nditati

ndifotokoze zonse zimene ndimachita, iweyo ukhoza

kukalowa n’kutuluka, kenako n’kukalowanso.” Pa

nthawiyi Dzuwa linkangomvetsera zimene mnzakeyo

ankanena. Kenako anaona munthu akudutsa

chapafupi, atavala chipewa. Ndiye Dzuwa linati,

“Eyaaa, ndadziwa chochita tsopano. Kuti tidziwedi

amene ali wamphamvu, tiye tipikisane. Tione amene

angapangitse kuti munthuyo achotse chipewa

chimene wavalacho.” Nthawi yomweyo Mphepo

inasangalala ndipo inati, “Taulutsa zinthuzinthu ife,

ndiye pali chiyani apaaa?” Kenako anagwirizana kuti

iyambe Mphepo kuulutsa chipewacho. Koma Mphepo

imati ikafuna kuulutsa chipewacho, munthuyo

ankangochigwira n’kuchikhazikanso bwinobwino.

Munthuyo ataona kuti Mphepo ikumuvutitsa,

anangomanga chipewacho kuchibwano chake ndi

chigwe. Mphepo inayesa kuulutsa chipewacho koma

Mpandamachokero Anthology

101
inakanika ndipo inatopa kwambiri n’kukhala pansi

kuti ipume. Kenako Dzuwa linalowa m’bwalo. Ndiye

linaomba, n’kuomba ndipo kunja kunatentha zedi.

Zitatero munthu uja anamva kutentha kwambiri ndipo

anamasura chingwe chija n’kuvula chipewa chija.

Kenako anakaima pamthunzi kuti mutu wake

upitidwe mphepo.

Phunziro: Osamadzitama, mwamuna mnzako ndi

pachulu.

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani Mphepo inkaderera

mphamvu za Dzuwa?

2. Kodi tinganene kuti n’kulakwa kumadzitama?

3. Kodi pamapeto pake ndi ndani amene

anapambana?

4. N’chifukwa chiyani Mphepo inalephera

kuulutsa chipewa cha munthu uja?

5. Kodi mukuganiza kuti Dzuwa likuimira

chiyani?

6. Nanga tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

102
Mnyamata wa Zala Zazitali

Mnyamata wina anagwidwa ataba ndalama zambiri

ndipo pofuna kuti ena atengerepo phunziro, mfumu ya

m’deralo inalamula kuti aphedwe. Tsiku loti aphedwe

litafika, mnyamatayo anapempha anthu omwe

ankafuna kumupachikawo kuti amulole kuchita

chinthu chimodzi asanaphedwe. Anapempha kuti

akufuna auze mayi ake zinazake. Anthuwo

anavomera, ndipo mnyamatayo anapita pafupi ndi

mayi akewo n’kuwauza kuti, “Ndikufuna

ndikunong’onezeni.” Mayiyo anaperekeradi khutu lake

kuti mwana wakeyo amunong’oneze, koma mwanayo

analuma khutulo ndipo linangotsala pang’ono

kudukiratu. Anthu onse omwe anabwera

kudzaonerera kuphedwa kwa mwanayo anadabwa ndi

zimenezi ndipo ena ankati mchitidwe umenewu unali

wankhanza zedi. Enanso ankanena kuti munthu

wabwinobwino sangachite zomwe mnyamatayo

anachita. Koma mnyamatayo anati: “Ndachita

zimenezi kuti ndiwakhaulitse. Kungoyambira ndili

mwana ndinkaba zinthu, koma ndikapita kunyumba,

mayiwa ankalandira n’kusunga. M’malo moti

andilangize kapena kundipatsa chilango, ankaseka

Mpandamachokero Anthology

103
n’kunena kuti ‘palibe atadziwe zimenezi.’ Lero

ndiphedwa chifukwa cha iwowa.” Atamva zimenezi,

munthu wina wokonda kupemphera yemwe anali

pamalopo anauza mayiyo kuti, “Mwanayu akunena

zoona. Wafika pamenepa chifukwa inuyo

munamulekerera. Pajatu amati, ‘Langiza mwana

poyamba m’njira yake, ndipo ngakhale akadzakula

sadzachokamo.’”

Phunziro: Kumalangiza komanso kuphunzitsa ana

adakali aang’ono.

Mafunso

1. Kodi mayiwa akanathandiza bwanji mwanayu

ali wamng’ono?

2. Kodi mukuganiza kuti chinkapangitsa mayiyu

kusapatsa mwana wakeyu chilango chinali

chiyani?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

104
Bambo Yemwe Anakwatira Mitala

Kalekalelo, amuna akuloledwa kukwatira akazi ambiri,

bambo wina anakwatira akazi awiri. Wina anali

wamkulu kwambiri kuposa msinkhu wake, ndipo

winayo anali mtsikana. Akazi onsewa ankamukonda

kwambiri ndipo aliyense ankafuna kuti mwamunayo

azioneka mofanana naye. Wamkulu ankafuna kuti

mwamunayo azioneka wachikulire, pomwe wamng’ono

ankafuna azioneka wachinyamata. Ndiye n’kupita kwa

nthawi, mwamuna uja anayamba kukalamba ndipo

tsitsi lake linayamba kuyera. Mkazi wachitsikana uja

anayamba kudana ndi tsitsi la imvilo chifukwa

linkapangitsa kuti azioneka ngati anakwatiwa ndi

mwamuna wamkulu kwambiri, ndipo ankaona kuti

anthu azisokoneza n’kumaganiza kuti ndi bambo ake.

Choncho tsiku lililonse mwamunayo akamagona,

mkaziyo ankapesa tsitsi la mwamunayo n’kuthothola

tsitsi lonse loyera. Koma mkazi wamkulu uja

ankasangalala akaona kuti mwamuna wake wayamba

kuchita imvi ndipo ankaona kuti zimenezi zithandiza

anthu kuti asamaganize zoti mwamuna wakeyo ndi

mwana wake. Choncho m’mawa ulionse mwamunayo

asanadzuke, mkazi wamkuluyo ankathothola tsitsi

Mpandamachokero Anthology

105
lakuda lomwe linali m’mutu mwa mwamuna wakeyo.

Pamapeto pake, tsitsi lonse la mwamunayo linatha

ndipo anasanduka wadazi.

Phunziro: Ukamangomvera aliyense, umasanduka

chitsiru.

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani mkazi wamkulu

ankasangalala mwamuna wake atayamba imvi?

2. Nanga n’chifukwa chiyani mkazi wamng’ono

ankadana nazo?

3. Kodi bamboyu anakumana ndi mavuto otani?

4. Kodi n’zotheka kukhala wokalamba komanso

wachinyamata nthawi imodzi?

5. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

106
Mayi ndi Nkhandwe

“Ndati utontholeee!” Mawu amenewa anayankhula ndi

Mayi wina ataima pazenera lotsegula. M’manja mwake

munali mwana yemwe ankalira mosatonthozeka.

Kenako mwanayo anatonthola ndipo Mayiyo

anachenjeza mwanayo kuti, “Ukayambiranso kulira,

ndikuponyera pazenerapa kuti Nkhandwe ikudye.”

Ndiye zinangochitika kuti pa nthawi imene ankanena

zimenezi, Nkhandwe inali ikudutsa chapafupi ndipo

inamva zomwe mayiyo ananena. Nkhandweyo inaima

pafupi ndi nyumbayo ndipo inayamba kudikira kuti

mwanayo alirenso. Inati, “Lerotu ndiye ndachita

mwayi. Ndikuganiza kuti alira posachedwapa, ana

amakoma kwabasi moti nditsukako m’kamwa lero.”

Nkhandweyo inadikira kwa nthawi yaitali, koma

mwanayo sanalire. Kenako mwana uja anayambiranso

kulira ndipo Nkhandweyo inaima pafupi ndi zenera lija

kwinaku ikugwedezera mchira n’kumadikira kuti

mayiyo aponye mwanayo pawindopo. Koma mayiyo

anangotseka zeneraro n’kuyamba kumuyamwitsa.

Posakhalitsa agalu a pakhomopo anatulukira n’kupeza

Nkhandweyo ili pafupi ndi zeneraro ndipo

Nkhandweyo inayamba kuthawa kwinaku ikunena

Mpandamachokero Anthology

107
kuti, “Anthu ndi osathandiza, n’chifukwa chiyani

nthawi zonse amapereka malonjezo akudziwa kuti

sawakwaniritsa?”

Phunziro: Anthu ambiri amalonjeza akudziwa kuti

sakwaniritsa malonjezowo.

Mafunso

1. Kodi Mayiyu ankafunadi kutaya mwanayo

pazenera?

2. N’chifukwa chiyani Nkhandwe inakhulupirira

zimene Mayiyo ananena?

3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti sikuti panali

ubwenzi uliwonse pakati pa Mayiyo ndi

Nkhandwe?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

108
Msamuko wa Kamba

Tsiku lina Kamba, kapena kuti Fulu, anapeza malo

atsopano ndipo ankafuna kusamukira kumalowo.

Ndiye anapempha mbalame ina yotchedwa Nkhwazi

kuti imunyamule n’kukamusiya kumalowo ndipo

analonjeza kuti aifumbatitsa kenakake. Nkhwaziyo

inavomera ndipo inanyamula Kambayo itagwira

chigoba chake n’kuuluka. Ili m’mwambamo,

Nkhwaziyo inakumana ndi Mphamba. Mphambayo

inauza Nkhwaziyo kuti, “Kambatu ndi ndiwo yokoma

kwambiri.” Koma Nkhwaziyo inati, “Ukunena zoona,

komatu chigoba chakechi n’cholimba ngati mwala.”

Ndiyeno Mphambayo inati, “Utangomuponyera

pamwala uwo, chigobacho chikhoza kusweka, ndipo

ife tikhoza kukhwasula vankati.” Nkhwaziyo inamvera

zimenezi ndipo inasiya Kambayo kuti akagwere

pamwalawo moti chigoba chake chinaphwanyika.

Nkhwazi komanso Mphambayo zinasangalala

kwambiri ndi nyama yokoma yomwe zinadya patsikuli,

moti zinachotsa dalazi.

Phunziro: Osapereka moyo wako m’manja mwa mdani.

Mpandamachokero Anthology

109
Mafunso

1. N’chiyani chimene Kamba analakwitsa?

2. Kodi mukuganiza kuti akanachita chiyani kuti

akafike kunyumba yake yatsopano?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

110
Nkhanu ndi Mwana Wake

Tsiku lina kunacha bwino kwambiri ndipo Nkhanu

inatuluka m’nyumba limodzi ndi mwana wake

n’kupita kukawongola miyendo m’mbali mwa mtsinje.

Koma Nkhanuyo itaona mmene mwana wakeyo

amayendera inati, “Mwana wanga, mayendedwe akowa

sandisangalatsa. N’chifukwa chiyani ukuyenda

cham’mbali? Mpofunika kuti uphunzire kumayenda

mopita kutsogolo. Inetu ndikufuna uziyenda

bwinobwino ngati munthu woti kutsogolo ukukuona.

Sindikufuna uzindichititsa manyazi ndi mayendedwe

ako osalongosokawo.” Koma mwanayo anayankha

kuti, “Chabwino amayi, koma muyambe ndi inuyo

kuchita zimenezi, kuti ineyo ndizitengera chitsanzo

chanu. Anthutu amadabwa akamva munthu akunena

kuti akufuna kusintha dziko, iyeyo akulephera

kudzisintha yekha!”

Phunziro: Osamauza ena kuti achite zomwe iweyo

suchita.

Mpandamachokero Anthology

111
Mafunso

1. Kodi mukuganiza kuti Nkhanu yaikuluyo

inkayenda mopita kutsogolo?

2. N’chifukwa chiyani mwanayo sanagwirizane

ndi zimene kholo lake linanena?

3. Kodi n’zotheka kuthandiza munthu wina

kusintha, ifeyo tikulephera kudzisintha tokha?

4. Kodi tikuphunzirapo chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

112
Bulu Avala Chikopa cha Mkango

Bulu wina anatola chikopa cha Mkango chomwe alenje

anachiyanika padzuwa kuti chiume. Buluyo anavala

chikopacho ndipo anayamba kuyendayenda m’mudzi

wonse. Anthu komanso nyama zimati zikangomuona,

zinkalikumba liwiro, kufuna kupulumutsa moyo.

Buluyo ataona fumbi limene linabwera chifukwa cha

liwiro la anthu komanso nyama, anasangalala

kwambiri ndipo anayamba kukuwa. Nthawi yomweyo

anthu komanso nyama zinamuzindikira ndipo mwini

Buluyo anabwera n’kuyamba kumukutumula. Kenako

kunabwera Galu n’kuuza Buluyo kuti, “Ayi ndithu,

mtima suvala nsanza. Nthawi zina ngakhale nkhuku

ikhoza kumalota itavala nsapato! Komabe unaitha

bwanawe, chifukwa unapusitsa ambiri. Koma

ukudziwa kuti anakutulukira utangotsegula

pakamwa?”

Phunziro: Zovala zimapusitsa, koma zonena za munthu

m’pamene umadziwa ngati ali wanzeru kapena ayi.

Mpandamachokero Anthology

113
Mafunso

1. N’chifukwa chiyani Buluyo anasangalala

pamene anthu komanso nyama zinkathawa?

2. N’chiyani chinachititsa kuti anthu

amuzindikire?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

114
Nkhani ya Mabwenzi a Pamtima

Anthu ena awiri, omwe anali mabwenzi a ponda apo

m’pondepo, anapita kukawongola miyendo

kunkhalango ina, ndipo mwadzidzidzi anakumana ndi

chimbalangondo. Chimbalangondocho chinayamba

kupita kumene kunali anthuwo ndipo anachita

mantha kwambiri. Munthu m’modzi anali kutsogolo

ndipo wina anali m’mbuyo. Munthu anali kutsogoloyo

atangoona kuti chilombocho chikubwera, analumphira

mumtengo n’kubisala ndipo anasiya mnzakeyo ali

pansi pomwepo. Winayo sanalimbanenso n’kuthawa,

koma anangodziponya pansi ndipo nkhope yake

inalowa m’dothi. Chimbalangondocho chinafika pafupi

ndi munthu anagwera pansiyo ndipo chinatsitsa

mphuno yake n’kuyamba kununkhiza mutu wa

munthuyo. Mwamwayi chilombocho sichinamuchite

kalikonse chifukwa chinkaganiza kuti wafa kale, paja

zimbalangondo sizidya kapena kugwira chinthu

chomwe chafa kale. Kenako chinanyamuka

n’kumapita. Chitazimiririka, munthu anali mumtengo

uja anatsika ndipo anafunsa mnzakeyo kuti, “Kodi

bwanawe, chimbalangondo chija chimakunong’oneza

chiyani?” Mnzakeyo anati, “Chinandiuza kuti

Mpandamachokero Anthology

115
ndisamakhulupirire mnzanga amene amandithawa

zikavuta!”

Phunziro: Osamakhulupirira munthu amene

amakukonda zinthu zikakhala zikuyenda bwino, koma

zikavuta amakuthawa.

Mafunso

1. Kodi Chimbalangondocho chinanong’onezadi

munthu anali pansi uja?

2. Kodi munthu anali mumtengo uja akanachita

chiyani akanakhala kuti amamukondadi

mnzakeyo?

3. Kodi tikuphunzira chiyani?

Mpandamachokero Anthology

116
Mapoto Awiri

Tsiku lina mapoto awiri anasiyidwa m’mbali mwa

mtsinje. Poto m’modzi anali wachitsulo ndipo wina

anali wadothi. Ndiyeno mtsinjewo unadzadza madzi

ndipo mapotowo anayamba kuyandama n’kumapita

ndi madzi. Koma poto wadothiyo ankachita mantha

ndipo ankayesetsa kusambira kuti asagundane ndi

mnzakeyo. Poto wachitsuloyo anayamba kudabwa ndi

zimenezi ndipo anakuwira mnzakeyo n’kumuuza kuti,

“Usaope bwanaweee, sikuti ndikugundayi!” Koma poto

wadothiyo anati, “Ndikuopa kuti ndikhoza kugundana

nawe. Inetu ndinapangidwa ndi dothi, moti utati

undigunde kapena ineyo nditati ndikugunde,

ndingavutikebe ndi ineyo.”

Phunziro: Anthu amphamvu ndi ofooka sangayendere

limodzi.

Mpandamachokero Anthology

117
Mafunso

1. N’chifukwa chiyani tinganene kuti poto wadothi

akanaphwanyika mosavuta akanagundana ndi

mnzakeyo?

2. Perekani zitsanzo za zinthu zamphamvu ndi

zofooka zomwe sizingakhalire pamodzi?

3. Kodi tikuphunzirapo chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

118
Ng’ombe Zinayi ndi Mkango

Mkango wina unkazembekerera Ng’ombe zinayi zomwe

zinkadya malo ena. Mkangowo unayesa maulendo

angapo kuti ugwire Ng’ombezo koma unalephera.

Unkati ukafuna kuti uukire Ng’ombe imodzi,

Ng’ombezo zinkalozetsana mbuyo ndipo zinkapezeka

kuti Mkangowo wakumana ndi nyanga za Ng’ombezo.

Zikatere Mkangowo unkachita mantha n’kubwerera.

Koma kenako Ng’ombezo zinayambana ndipo iliyonse

inalowera kwake. Zimenezi zinachititsa kuti Mkango

uja upezerepo mwayi, moti unayamba kugwira

Ng’ombe imodziimodzi mpaka zonse zinatha psiti.

Phunziro: Umodzi ndi mphamvu.

Mafunso

1. N’chiyani chinachititsa kuti Mkango usagwire

Ng’ombe pamene zinkachitira zinthu limodzi?

2. Kodi Ng’ombezo zikanatani kuti zisaphedwe ndi

Mkango?

3. Kodi anthu akagawikana, amakhala

amphamvu kapena ayi?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

119
Mneneri Wabodza

Kalekalelo kunali mneneri wina yemwe ankalosera

zam’tsogolo. Ndiye m’nyengo ina ya mvula, mneneriyu

anaona nyenyezi yachilendo ndipo anayamba kuuza

anthu kuti, “Zaka 100 zikubwera kutsogoloku

kudzachitika tsoka loopsa, anthu ambiri adzamwalira

ndipo mudzi wonsewu udzatheratu.” Mneneriyo

ankanena zimenezi akuyang’ana nyenyeziyo ndipo

anaiwaliratu zoyang’ana pamene ankaponda. Ndiye

mwatsoka, pansi panali mwala moti anapunthwa

n’kugwa, nkhope yake n’kulowa m’matope. Anthu

ataona zimenezi anayamba kumuseka ndipo

anamufunsa kuti, “Kodi inuyo mumakwanitsa bwanji

kumalosera zinthu zomwe zidzachitike zaka 100

kutsogoloku, n’kumalephera kudziwa zimene

zangotsala pang’ono kuchitikira phazi lanu? Ndiye

mukufuna tizikhulupirira bodza bodza lofuka utsi

limene mukutiuzali?”

Phunziro: Kumayamba kaye wachotsa chitsotso cha

m’diso lako kenako cha mnzako.

Mpandamachokero Anthology

120
Mafunso

1. N’chifukwa chiyani anthu aja anayamba

kuseka mneneriyu?

2. Kodi mukuganiza kuti ankakhulupirira kuti

zimene ananenazo zidzachitikadi? Perekani

chifukwa.

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

121
Msodzi Agwira Nsomba Yaing’ono

Tsiku lina msodzi wina anapita kogwira nsomba koma

sanagwire kathu tsiku lonse. Koma chakumadzulo

anagwira kansomba kakang’ono. Kansombako

kanayamba kupempha msodziyo kuti,

“Ndikhululukireni bwana, ndisiyeni ndizipita. Ineyo

ndidakali mwana, ndachepa kwambiri kuti ndidyedwe.

Mukandibwezeretsa m’madzimu ndikula, ndipo

mukhoza kudzandigwira nditanenepa m’tsogolo. Pa

nthawiyo mukhoza kudzandidya ndili wonona

kwambiri.” Koma msodziyo anati, “Ayi, ayi, sindilola.

Ndagwira iweyo lero. Ndani akudziwa ngati

ndingadzakugwiredi m’tsogolomo?”

Phunziro: Osamawerengera zinthu zomwe sunapeze.

Mafunso

1. Kodi mukuganiza kuti nsomba yaing’onoyo

ikanalola kuti idzagwidwenso ndi msodziyu ulendo

wina?

2. N’chifukwa chiyani nsombayo inauza msodziyo

kuti amusiye? Kodi inkanena zoona?

3. Kodi tikuphunzirapo chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

122
Munthu Wadyera Komanso Wansanje

Anthu awiri omwe ankakhala moyandikana nyumba

anapita kwa Mulungu ndipo anapempha Mulunguyo

kuti awapatse zimene akufuna. Mmodzi wa anthuwo

anali wadyera, pomwe winayo anali wansanje. Pofuna

kuwakhaulitsa anthuwa, Mulunguyo anawauza kuti

awapatsa zimene akufuna. Anawauzanso kuti

aziwapatsa zimene akufuna koma anati azipereka

kuwirikiza kawiri zimene m’modzi wapempha. Ndiyeno

munthu wadyera uja anapempha kuti amupatse golide

wodzaza nyumba yake. Pasanapite nthawi anapezadi

golideyo ndipo anasangalala kwambiri. Koma

chisangalalochi sichinakhalitse atazindikira kuti

mnzake wansanje uja wapeza golide wodzadza nyumba

ziwiri. Munthu wansanje uja anamvako bwino

atazindikira kuti mnzake sakusangalala. Koma

ankafuna kuti mnzakeyo akhaule kwambiri, moti

anapempha Mulungu kuti amuchotse mnzakeyo diso

limodzi. Zitatero, Mulungu anamuchotsadi mnzakeyo

diso limodzi, koma zimenezi zinachititsa kuti iyeyo

achotsedwe maso ake onse awiri, moti anakhala

wosaona.

Phunziro: Makhalidwe oipa amabweretsa mavuto.

Mpandamachokero Anthology

123
Mafunso

1. Kodi ndi ndani amene anapezadi zimene

ankafuna?

2. N’chifukwa chiyani anthuwa sankakhutitsidwa

ndi golide amene anali naye?

3. Kodi mungatchule makhalidwe ena oipa amene

amabweretsa mavuto?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

124
Khwangwala Waludzu

Tsiku lina Khwangwala ankafuna kufa ndi ludzu.

Koma mwamwayi anapeza mtsuko wamadzi. Koma

atafika pafupi ndi mtsukowo anapeza kuti madzi ake

anali ochepa ndipo anali pansi penipeni pa mtsukowo

moti sankakwanitsa kuwamwa. Khwangwalayo

anayesetsa kuti amwe madziwo koma analephera moti

kenako anangowasiya n’kutsamira mtsukowo. Koma

kenako nzeru zinamubwerera moti anatola mwala

n’kuponyera mumtsukomo. Anatolanso mwala wina

n’kuponya mumtsukomo ndipo madzi aja anayamba

kukwera. Anapitirizabe kuchita zimenezi mpaka

madziwo anakwera kwambiri ndipo anamwa n’kupha

ludzu lake.

Phunziro: Nyumba imayamba kumangidwa ndi njerwa

imodzi.

Mafunso

1. Kodi chikanachitika n’chiyani zikanakhala kuti

Khwangwalayo anangokhala osachita chilichonse?

2. Kodi n’chifukwa chiyani nthawi zina sibwino

kutaya mtima mwansanga?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

125
Munthu Wam’nkhalango

M’nyengo ina yozizira kwambiri munthu wina

ankayenda usiku m’nkhalango ndipo anasokonekera

n’kumalephera kupeza njira yakwawo. Ndiye pamene

ankayendayenda m’nkhalangomo anakumana ndi

munthu wina yemwe ankaoneka kuti ankakhala

m’nkhalango momwemo. Munthuyo analonjeza kuti

amupatsa malo ogona usikuwo komanso kuti kukacha

amuthandiza kupeza njira yakwawo. Kenako

munthuyo anamutenga n’kumapita naye kwawo koma

munthu anasokonekera uja anaika manja ake

pakamwa n’kumapemerera ndi mpweya wam’kamwa

mwake. Ndiyeno munthu wam’nkhalango uja

anafunsa kuti, “N’chifukwa chiyani mukupanga

zimenezo?” Munthuyo anayankha kuti, “Manja anga

azizidwa ndiye ndikufuna ndiwatenthetse ndi mpweya

wochoka m’kamwa mwanga.” Kenako anafika

kunyumba kwa munthu wam’nkhalango uja ndipo

pasanapite nthawi anabweretsa phala lotentha

kwambiri kuti mnzake uja adye. Ndiye munthu uja

anayamba kudya phalalo ndipo asanaliike m’kamwa,

ankalipemerera kaye. Ataona zimenezi, munthu

wam’nkhalango uja anafunsa kuti, “Nanga mukuchita

Mpandamachokero Anthology

126
zimenezo chifukwa chiyani?” Munthuyo anayankha

kuti, “Phalali ndi lotentha kwambiri ndiye ndikuopa

kuti lindiwaula m’kamwa. Choncho

ndikumalipemerera ndi mpweya wam’kamwa mwanga

kuti lizizire.” Atangomva zimenezi, munthu

wam’nkhalango uja anati, “Basi tulukani m’nyumba

mwanga muno! Munthu wamtundu wanji wotuluka

mpweya wotentha komanso wozizira m’kamwa

mwake.”

Phunziro: Mupeze nokha.

Mafunso

1. Kodi mpweya wa munthuyu unali wotentha

kapena wozizira?

2. Kodi kuchita zinthu zimene tinazolowera

n’kulakwa?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

127
Mazira Agolide

Tsiku lina munthu anapita pachisa cha tsekwe ndipo

anapeza dzira looneka lachikasu komanso lowala.

Atalitola anaona kuti dziralo linkalemera kwambiri

moti anaganiza zolitaya poganiza kuti munthu wina

anaikapo mwala kuti amupusitse. Koma kenako

anasintha maganizo ndipo anapita nalo kunyumba

kwake. Atafika kunyumbako anazindikira kuti dziralo

linali lagolide. Kenako anayamba kumapita kuchisa

cha tsekwe chija m’mawa ulionse, ndipo ankatola

dzira limodzi lagolide. Ankati akatola dzira limodzi,

ankaligulitsa moti n’kupita kwa nthawi anakhala

mponda makwacha. Munthuyo atayamba kulemera,

anayamba dyera moti anaganiza zopeza mazira onse a

tsekweyo nthawi imodzi. Choncho, anapha tsekwe uja

n’kumung’amba pamimba ndipo mkati mwake

sanapezemo kanthu.

Phunziro: Dyera limatayitsa zambiri.

Mpandamachokero Anthology

128
Mafunso

1. Kodi munthu wadyerayu ankaganiza kuti

apeza chiyani mkati mwa tsekwe uja?

2. Kodi anapezadi mazira agolide ambiri atapha

tsekweyo?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

129
Mbalame Yoimba Mokoma

Kafansiyanji wina ankasowa tulo usiku ndipo

ankangomvetsera mbalame ina ikuimba usiku wonse.

Kaimbidwe ka mbalameyo kanamudolola kwambiri

moti usiku wotsatira anagwira mbalameyo kuti

izimuimbira nthawi zonse. Kenako anaiuza mbalameyo

kuti, “Ndiye popeza ndakugwira, uzindiimbira nyimbo

nthawi iliyonse imene ndikufuna.” Koma mbalameyo

inati, “Mbalame za mtundu wathuwutu sizitha kuimba

nyimbo ngati zikukakamizidwa komanso ngati

zitatsekeredwa m’kanyumba.” Ndiye kenako munthu

uja anati, “Ndiye ndikudyatu! Ndinamva zoti mbalame

ngati iweyo mumakoma kwambiri mukakazingidwa

m’mafuta.” Mbalameyo itangomva zimenezi inati, “Ayi,

musandiphe. Ingondisiyani ndipo ndikuuzani zinthu

zitatu zomwe zingakuthandizeni kwambiri kuposa

kudya kathupi kanga kakang’onoka.” Ndiyeno munthu

uja anaimasula n’kuisiya ndipo mbalameyo inaulukira

panthambi yamtengo wina n’kunena kuti,

“Musadzayerekezenso kumvera lonjezo limene munthu

wogwidwa angadzakuuzeni, chimenechi ndi chinthu

choyamba. Chachiwiri, osamataya kapena kusiya

chinthu chokhacho chimene muli nacho ndipo

Mpandamachokero Anthology

130
chachitatu, osamakhalira kudandaula chinthu

chimene ngakhale mutatani simungachipezenso.”

Mbalameyo itangomaliza kunena zimenezi inauluka.

Phunziro: Osalilira chinthu chimene palibe chomwe

ungachite kuti uchipezenso. Osamada nkhawa ndi

zinthu zimene sungazisithe chifukwa ungangotaya

nthawi yako.

Mafunso

1. Kodi ndi malangizo ati amene mbalame

inapereka kwa munthu uja?

2. N’chifukwa chiyani munthuyo analakwitsa

kumvera zimene mbalameyo inamuuza?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

131
Nkhandwe, Nkhuku Komanso Galu

Usiku wina Nkhandwe inkazemberera Nkhuku ndipo

Nkhukuyo itazindikira zimenezi, inauluka n’kukwera

mumtengo moti Nkhandweyo inkalephera kuigwira.

Kenako Nkhandweyo inati, “Musaope a Nkhuku,

ndabweratu kuti ndikuuzeni uthenga wabwino.

Mfumu Mkango yalamula kuti pasapezekenso nyama

yodya inzake kuyambira lero. Inati nyama zonse

ziyenera kumakhala limodzi mogwirizana komanso

mwamtendere.” Ndiyeno Nkhukuyo inati, “Uthenga

wake ndi umenewo eti? Chabwino ndamva! Koma pali

wina amene mwina mungakondenso mutamuuza

uthenga umenewu. Mwina nayenso angasangalale

ataumva.” Nkhukuyo inayamba kuyang’ana

kunyumba komwe inkakhala. Ndiyeno Nkhandwe ija

inafunsa kuti, “Kodi kukubwera chiyani?” Nkhukuyo

inayankha kuti, “Kukubwera Galu wa mbuyanga.”

Nkhandweyo itangomva zoti kukubwera galu,

inatembenuka n’kuyamba kuthawa. Ndiyeno

Nkhukuyo inauza nkhandwe ija kuti, “Kodi

mungamuuzenso Galuyo uthenga mwabweretsa uja?”

Koma Nkhandwe ija inati, “Ndikanakonda

ndikanatero, koma ndikuopa kuti Galuyo akhoza

Mpandamachokero Anthology

132
kundichita zoopsa chifukwa kunalibe pamene Mfumu

Mkango imalengeza zoti pakhale mtendere wa zinyama

zonse.” Nkhukuyo itamva zimenezi inamwetulira

n’kunena kuti, “Nanga ine ndiye ndinaliko?”

Phunziro: Bodza lili ngati matenda, ukhoza kuwabisa

koma pamapeto pake ena amadziwa.

Mafunso

1. Kodi Nkhuku inadziwa bwanji kuti

Nkhandweyo imanama?

2. Kodi Nkhukuyi inaonadi galu wambuyake

akubwera?

3. Kodi ndi makhalidwe oipa ati amene Nkhandwe

inasonyeza m’nkhaniyi?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

133
Munthu Wamanja Lende

Munthu wina ankayendetsa ngolo yake atanyamula

katundu wolemera m’nyengo ina yadzinja. Ngoloyo

inkakokedwa ndi abulu awiri. Chifukwa choti kunali

matope ambiri, matayala a ngoloyo analowa m’matope

n’kutitimira. Ndiyeno munthuyo anayamba kumenya

abulu akewo ndi chikwapu, koma sanakwanitse

kuyenda. Kenako anatopa moti anataya chikwapucho

n’kutsika pangoloyo. Ndiyeno anagwada pansi

n’kupemphera kwa Mulungu kuti amuthandize. Anati,

“Ambuye Mulungu, ndithandizeni chonde pa nthawi

yovutayi.” Koma Mulungu anamuyankha kuti, “Ndiwe

wopusa kwabasi! Tadzuka pamenepo ukakankhe

ngolo yakoyo kuti ichoke m’matopemo!”

Phunziro: Mulungu sangathandize munthu waulesi.

Mpandamachokero Anthology

134
Mafunso

1. Kodi tinganene kuti Mulungu anathandiza

munthuyu? Ngati ndi choncho, n’chifukwa chiyani

mwatero?

2. Kodi Mulungu anauza munthuyo kuti achite

chiyani?

3. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

135
Bambo ndi Mwana Wake Apita Kumsika

Bambo wina ankapita ndi mwana wake kukagulitsa

bulu kumsika. Ndiyeno akuyenda kupita kumsikako,

anakumana ndi munthu wina ndipo anawauza kuti,

“Ndinu opusa kwambiri, bwanji osakwera buluyo?”

Ndiyeno bamboyo anakweza mwana wakeyo pabuluyo

n’kumapitiriza ulendo. Koma kenako anakumananso

ndi gulu la anthu ndipo m’modzi mwa anthuwo anati,

“Taonani mwana waulesiyu, iyeyo wakwera bulu koma

bambo ake akuyenda wapansi!” Bamboyo atamva

zimenezi anauza mwana wakeyo kuti atsike ndipo

anakwerapo iyeyo. Koma asanapite patali anakumana

ndi azimayi awiri ndipo m’modzi anawauza kuti,

“Taonani bambo wopanda nzeruyu wakwera bulu,

mwana wake akuyenda wapansi!” Zitatero, bamboyo

anasowa chochita. Koma kenako anaganiza zoti

angokwera pabuluyo limodzi ndi mwana wakeyo.

Pamene ankachita zimenezi n’kuti atayandikira

kumsika kuja ndipo anthu ena anayamba

kuwalozerana n’kumawanena chipongwe. Bamboyo

anatsika pabuluyo n’kuwafunsa kuti alakwa chiyani.

Koma anthuwo anati, “Kodi mulibe manyazi thunthu

lonselo komanso mwana wanuyo kukwera pamsana

Mpandamachokero Anthology

136
pa bulu wamng’ono ngati ameneyu.” Bambo ndi

mwana wakeyo sanakwerenso buluyo ndipo anaima

kaye n’kuyamba kuganiza zoti achite. Pamapeto pake

anaganiza zodula mtengo n’kumagirira buluyo

n’kumunyamula pamapewa awo. Koma anadabwa

kwambiri kuti anthu ankangowaseka ngati amisala

ndipo posakhalitsa anafika pamlatho wolowera

mumsika ndipo mwendo umodzi wa bulu uja

unamasuka ndipo buluyo anagwa pansi n’kuthawa,

moti sanakwanitsenso kumugwira. Ndiyeno munthu

wina wachikulire, yemwe ankayenda pafupi nawo,

anawauza kuti, “Mutengerepo phunziro, munthu

amene amafuna kusangalatsa onse, sangasangalatse

aliyense.”

Phunziro: Sungakwanitse kusangalatsa aliyense.

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani munthu ndi mwana

wakeyu anamanga buluyo pamtengo?

2. Kodi mawu akuti, “Munthu amene amafuna

kusangalatsa onse, sasangalatsa aliyense”

akutanthauza chiyani?

3. Kodi pali nthano iliyonse imene munaimvapo

imene mukuona kuti ikufanana ndi imeneyi?

Mpandamachokero Anthology

137
4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

138
Munthu Woumira

Kalekalelo panali munthu wina woumira kwambiri

yemwe ankabisa ndalama zake pansi pamtengo

wam’munda mwake. Mlungu ulionse ankapita

pamtengopo n’kukumba ndalamazo, ndipo

ankaziyang’ana kwinaku akunyadira kuti ali ndi

ndalama zambiri. Koma tsiku lina wakuba anamuona

akuchita zimenezi ndipo munthuyu atachoka,

wakubayo anapita kukakumbapo ndalamazo

n’kuthawa nazo. Ndiyeno munthuyu atapitanso kuti

akaone ndalama zake, anapeza kuti zonse zabedwa.

Zitatero anameta tsitsi lake ndipo anang’amba zovala

zake n’kuyamba kulira koopsa. Anthu oyandikana

nawo nyumba atamva kulirako, anabwera kuti

adzaone chimene chachitika. Munthuyo

anawafotokozera zonse zimene zinachitika. Anawauza

kuti anakwirira ndalama zake pansi pamtengowo

ndipo ankabwera mlungu ulionse n’kufukula

ndalamazo moti akaziona mtima wake unkasangalala

zedi. Anthuwo anamufunsa kuti, “Kodi munkatengako

ndalama zina kuti mukagwiritse ntchito?” Munthuyo

anayankha kuti, “Ayi, ndinkangobwera kuti

ndidzazione basi. Ndinkamva bwino kwambiri

Mpandamachokero Anthology

139
ndikaona ndalama zanga zochuluka.” Ndiyeno

anthuwo anamuuza kuti, “Ndiyetu musasiye. Mlungu

ulionse muzibwerabe pamtengopa ndipo

muzingoyerekezera kuti ndalama zanuzo zidakalipobe.

Zimenezi zikuthandizani kwambiri kuti muzisangalala.

Si mwati munkangobwera kudzaziona?”

Phunziro: Kukhala ndi ndalama kapena zinthu zambiri

koma osamazigwiritsa ntchito, n’chimodzimodzi

osakhala nazo.

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani munthu woumirayu

ankakumba ndalama zake nthawi zonse?

2. Kodi akanatani kuti ndalama zake zisabedwe?

3. Kodi akanakhala wanzeru akanachita chiyani

ndi ndalama zakezo?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

140
Nkhandwe ndi Udzudzu

Tsiku lina Nkhandwe inali paulendo ndipo itaoloka

mlatho wina mchira wake unakodwa m’ziyangoyango

moti inkalephera kuchoka. Udzudzu ungapo utaona

zimenezi unakondwera kwambiri ndipo unayamba

kuyamwa magazi a Nkhandweyo popanda

kusokonezedwa ndi mchira wake. Kenako kunabwera

Chisoni ndipo chinamva chisoni kwambiri ndi

Nkhandweyo moti chinapita kuti chikaithandize.

Chinauza Nkhandweyo kuti, “Kodi

ndingakuthandizeko bwanawe pothamangitsa

udzudzu ukukuyamwa magaziwu?” Koma

Nkhandweyo inati, “Zikomo kwambiri pondiganizira

achimwene anga a Chisoni. Koma musatero ayi. Si

mwati mukufuna mungouthamangitsa?” Chisoni

chinavomera ndipo chinafunsa kuti, “N’chifukwa

chiyani simukufuna kuti ndiuthamangitse pomwe

ukukuvutitsani?” Nkhandweyo inayankha kuti,

“Udzudzuwu wangotsala pang’ono kukhuta, ndiye

mukauthamangitsa ukaitana unzake wanjala

kwambiri, moti ubwera n’kudzapopa magazi anga

onse.”

Phunziro: Kumaona patali.

Mpandamachokero Anthology

141
Mafunso

1. N’chiyani chinachititsa kuti Chisoni chimvere

chisoni nkhandwe?

2. N’chifukwa chiyani Nkhandwe inakana

thandizoli?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

142
Nkhandwe Yopanda Mchira

Tsiku lina mchira wa Nkhandwe unakodwa

pamsampha ndipo pamene inkayesetsa kuti ichoke,

mchirawo unaduka. Poyamba Nkhandweyo inkachita

manyazi kupita pamene panali anzake poopa kuti

azimuseka. Koma kenako inalimba mtima

n’kukakumana ndi anzake onse n’kukawauza kuti

akufuna kuwauza nkhani yofunika kwambiri.

Nkhandweyo inauza anzakewo kuti nawonso adule

michira yawo. Nkhandweyi inafotokoza kuti mchira si

wabwino makamaka agalu akamakuthamangitsa.

Inawafotokozeranso kuti ikunena zimenezo chifukwa

imawaganizira komanso kuwakonda kwambiri.

Inanena kuti sikufuna kuti anzakewo azinyamula

pathupi lawo chinthu chomwe sichingawathandize,

koma kungowabweretsera mavuto. Ndiyeno anzakewo

anati, “Tamva ndithu bwanawe, amenewo ndi

maganizodi abwino. Koma tikuona kuti iweyo

sukanaganiza zotiuza kuti tidule michira yathu,

yomwe ndi ziwalo zamtengo wapatali, zikanakhala kuti

wako sunaduke. Tikuona kuti ukungofuna tifanane!”

Phunziro: Osamakhulupirira malangizo ochokera kwa

munthu amene alibe chimene uli nachocho.

Mpandamachokero Anthology

143
Mafunso

1. N’chifukwa chiyani Nkhandwe inkafuna kuti

anzake adule michira yawo?

2. Kodi tinganene kuti inkachita zimenezi

powafuniradi zabwino?

3. Kodi tingadziwe bwanji ngati munthu

akutipatsadi malangizo chifukwa choti akutifunira

zabwino?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

144
Kalulu wa Diso Limodzi

Tsiku lina Kalulu anaphulika diso limodzi ndipo

kungochokera pa tsikulo, zinkamuvuta kuona chinthu

chimene chikubwera kuchokera mbali yomwe diso

linaphulikayo. Ndiye pofuna kupewa mavuto,

Kaluluyu ankakonda kudya pafupi ndi phompho lina

lomwe kumunsi kwake kunali nyanja. Ankati

akamadya diso lake labwinobwino lija linkakhala

kumtunda, pomwe mbali inayo inkaloza kunyanja.

Zimenezi zinkathandiza kuti aziona alenje

akamabwera kudzamugwira ndipo nthawi zambiri

ankathawa. Koma mlenje wina anatulukira kuti

Kaluluyo analibe diso limodzi. Ndiye tsiku lina

anakwera bwato n’kulowa m’nyanja, pansi pachitunda

chomwe kalulu ankadyera paja. Kenako anakoka uta

wake n’kubaya Kaluluyo. Kaluluyo analira kuti, “Mayo

ineeeeeee! Zoonadi, imfa sithawika.”

Phunziro: Ngakhale utayesetsa bwanji koma

sungathawe imfa.

Mpandamachokero Anthology

145
Mafunso

1. Kodi Kalulu anatani kuti asaphedwe ndi

mlenje?

2. Kodi zimenezi zinathandizadi?

3. N’chiyani chinachititsa Kaluluyu kuganiza kuti

akamadyera malo amenewo akhala wotetezeka?

4. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

146
Msonkhano wa Makoswe

Kalekalelo, Mphaka wina ankavutitsa Makoswe

kwambiri. Makoswewo anayamba kudandaula ndipo

anapanga chimsonkhano cha mnzanga ali pati, kuti

agwirizane zoti achite ndi mdani wawoyo. Atakumana,

Khoswe wina wodziwa kuyankhula anaimirira

n’kunena kuti, “Akuluakulu, Mphakayutu

akutisowetsa mtendere, akutizunza kwabasi moti

tikulephera kupeza chakudya choti tidyetse mabanja

athu. Sindikudziwa kuti tipange bwanji ndi chipsinjo

chatigwerachi?” Nkhaniyo inalowa m’bwalo ndipo

makoswewo anayamba kupereka maganizo

osiyanasiyana. Koma kenako, khoswe wina

wamng’ono anaimirira n’kunena kuti, “Mphakayudi

akutisowetsa mtendere. Mungandivomereze kuti

mdani wathuyu amayenda mochenjera kwambiri moti

umangozindikira wakugwira. Ndiye ngati titamamva

phokoso lotichenjeza kuti akubwera, tikhoza

kumamuzemba, ndipo palibe angagwidwe. Choncho

maganizo anga ndi akuti tipeze belu n’kumumangirira

m’khosi. Ndiyeno akamabwera, ifeyo tizimumva,

tikamumva, tizithawa.” Anzakewo anasangalala

kwambiri ndi mfundo anatsitsayi ndipo anayamba

Mpandamachokero Anthology

147
kumuwombera m’manja kwinaku akuimba

malikhweru. Kenako Khosweyo anakhala pansi

akumwetulira ndipo ankaoneka kuti wakukhutira ndi

zomwe wanena. Koma Khoswe wina wachikulire

anaimirira n’kunena kuti, “Maganizowa ndi abwinodi.

Koma kodi ndi ndani amene angalimbe mtima kuti

akamuveke belu?” Makoswewo anayamba

kuyang’anizana ndipo palibe anayankha. Kenako

khoswe wachikulireyo anapitiriza kunena kuti, “Ndi

ndani amene moyo sakuufuna? Maganizo ena

amakhala abwino, koma si onse amakhaladi

othandiza.”

Phunziro: Si maganizo onse amene amakhaladi

othandiza.

Mpandamachokero Anthology

148
Mafunso

1. Kodi tinganene kuti maganizo oveka Mphaka

belu, anali abwino kapena ayi? Ngati ndi choncho,

n’chifukwa chiyani?

2. Kodi mwina n’kutheka kuti Makoswe enawo

ananena zotani zomwe zinali zosatheka kuthetsa

vutolo?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

149
Mpikisano wa Kalulu ndi Kamba

Nthawi inayake Kalulu ankadzitama kuti ali ndi liwiro

kuposa nyama iliyonse. Ankati, “Palibe anayambapo

wandiposa kuthamanga. Ndikati ndiliyatse liwiro,

ndimachita kukhala ngati mphenzi. Ndipo ndikhoza

kukuuzani kuti panopa palibe amene angandipose

kuthamanga. Ngati pali wina akutsutsa, abwere

tipikisane.” Koma kenako Kamba anayankha kuti,

“Chabwino, tiye tipikisane.” Kaluluyo atamva zimenezi

anati, “Musandiseketse a Kamba! Zoona inuyoooo!

Miyendo yake yolowa mkatiyi? Kayendedwe kanunso

kamakhala ngati ka Mbozi, moti ndikhoza kukusiyani

kuti muuyambe ineyo n’kupha kaye tulo. Kenako

ndikhoza kudzuka, kukasamba, kudya, ndiyeno

n’kuyamba kuthamanga, koma ineyo n’kukakhalabe

woyamba kukafika.” Koma Kamba anati, “Ukhala

chete pambuyo poti ndakuchotsa chimbenene. Tiye

tipikisane!” Choncho anapangana mtunda woti

athamange ndipo aliyense anakonzekera kuyambapo

mpikisanowuo. Lipenga la mpikisanowo litangolira,

Kalulu anatsomphoka ngati mwala walegeni ndipo

posapita nthawi sanaonekenso. Koma

atangothamanga pang’ono, anaima kaye kuti abe tulo

Mpandamachokero Anthology

150
pofuna kumutsimikizira Kamba kuti akucheperakaba.

Kamba uja analimbikira kuthamanga moti pamene

Kalulu ankadzuka, Kambayo anali akudutsa pamzere

womaliza ndipo Kalulu sakanakwanitsa kuthamanga

n’kumupitirira. Ndiyeno Kamba anati, “Munthu

wakhama ndi amene amapambana mpikisano.”

Phunziro: Munthu wakhama akhoza kuchita

chilichonse.

Mafunso

1. Kodi pakati pa Kalulu ndi Kamba

chimathamanga kwambiri ndi chiyani? Ndiye

n’chiyani chinapambana pampikisanowu, nanga

n’chifukwa chiyani?

2. Kodi pali zinthu zinanso zimene munthu

amene amachita zinthu modekha komanso

mosathamanga angapambane kuposa wachangu

kwambiri?

3. Kodi tikuphunzirapo chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

151
Gogo Akumana ndi Imfa

Ukalamba umabwera ndi mavuto ambiri ndipo

umapangitsa kuti moyo usamasangalatse. Ndiyeno

kalekalelo, munthu wina anafika potopa ndi ukalamba

chifukwa ankavutika kugwira yekha ntchito

zapakhomo. Ngakhale kuyenda kumene kunkamuvuta

kwambiri. Nthawi zonse ankangokhalira kudandaula

msana, miyendo komanso kuphwanya kwa thupi. Kuti

ayende, ankadalira mgongosera. Ndiye tsiku lina,

anapita kunkhalango kukatola nkhuni zoti aphikire

nandolo. Atamaliza kutola nkhunizo, anazimanga

kamtolo ndipo anasenza n’kumapita kwawo. Koma

kenako nkhunizo zinayamba kumugogoda ndipo

anatopa kwambiri. Atalephera kupirira, anaponya

mtolowo pansi n’kunena kuti, “Sindingakwanitse

kupitirizabe kukhala moyo movutika chonchi!

Ndikanakondwera imfa ikanangobwera

kudzanditenga!” Nthawi yomweyo, imfa inatulukiradi

ndipo inati, “Mayi, ndamva mukutchula dzina langa,

mukundifuna eti? Tsopano ndabweratu, mukufuna

ndikuchitireni chiyani?” Koma gogoyo anati,

“Mwachitadi bwino kubwera. Kodi

Mpandamachokero Anthology

152
mungandithandizeko kusenza mtolowu? Ndikulephera

kuusenza ndekha.”

Phunziro: Zinthu zina zimene timafuna zitachitikadi,

sitingazikonde n’komwe.

Mafunso

1. Kodi munthu wokalambayu ankafunadi kufa?

N’chifukwa chiyani mukutero?

2. Kodi vuto lake linali chiyani kwenikweni?

3. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

153
Kalulu ndi Anzake Ambirimbiri

Kalulu anali nyama yotchuka kwambiri ndipo anali

ndi anzake ambirimbiri. Koma tsiku lina anaona

Nkhandwe zikubwera ndipo anaganiza zopempha

anzakewo kuti amuthandize kuthawa. Ndiye anapita

kwa Bulu n’kumupempha kuti amunyamule pamsana

pake, koma Buluyo anakana ndipo anamuuza kuti

mbuyake wamuuza kuti agwire ntchito inayake.

Anamuuza kuti, “Ndikuganiza kuti utapempha

Ng’ombe ikhoza kukuthandiza.” Kenako anapita kwa

Ng’ombe akumaganiza kuti iopseza Nkhandwezo ndi

nyanga zake. Koma ng’ombe nayonso inati, “Pepa

m’bale wanga, ndinagwirizana ndi chibwenzi changa

kuti tipite koyenda, ndiye ukudziwa kuti mnyamata

safuna kukhumudwitsa njole yake! Ndikuganiza kuti

utapempha Mbuzi ikhoza kukuthandiza mofanana ndi

mmene ine ndikanachitira.” Koma atapitako, Mbuziyo

inamuyankha kuti ikuvutika msana moti inadandaula

kuti ngati itachita zimene amafunazo ndiye kuti sigona

usiku, ingodziputira zina. Kenako inauza Kaluluyo

kuti Nkhosa ikhoza kumuthandiza pa vuto lakelo

ndipo anapitadi kwa Nkhosa. Koma Nkhosayo

inamuuza kuti, “Ndikanakuthandiza m’bale wanga,

Mpandamachokero Anthology

154
koma kungoti vuto lakoli landikulira. Ndakhala

ndikumva kuti Nkhandwe zikumadya Akalulu ndi

Nkhosa zomwe. Ndiye ndikuopa kuti nanenso

ndikhoza kusiyana nalo dziko lapansi.” Kenako Kalulu

anapita kwa mnzake womaliza amene ankaganiza kuti

akhoza kumuthandiza. Mnzakeyo anali Tonde. Koma

Tonde nayenso anakana kumuthandiza poganizira

kuti anzake akuluakulu a Kaluluyo anali atakana

kumuthandiza. Tonde ananena kuti kuvomera

ntchitoyo chikanakhala chipongwe kwa nyama zinazo,

zomwe zinali anzake aponda apo m’pondepo a

Kaluluyo. Pa nthawiyi n’kuti Nkhandwe zija

zitayandikira ndipo Kaluluyo anangoti, phazi thandize,

ndipo mwamwayi anapulumukadi.

Phunziro: Munthu amene ali ndi anthu ambirimbiri

ocheza nawo sakhala ndi anzake enieni.

Mafunso

1. Kodi nyama zomwe Kalulu ankaona kuti anali

anzake apamtima, zinalidi anzake enieni?

2. N’chifukwa chiyani nyamazi sizinkafuna

kuthandiza Kalulu?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

155
Mkango Ugwa M’chikondi

Nthawi ina Mkango unagwa m’chikondi ndi mtsikana

wina wokongola kwambiri ndipo inapita kwa makolo

ake kukafunsira ukwati. Koma anthu a kwawo kwa

mtsikanayo sanadziwe choti anene. Iwo sankafuna

kuti mwana wawo akwatiwe ndi Mkango. Komabe,

ankaopa kuukwiyitsa. Ankadziwa kuti ngati atachita

zinthu mosasamala akhoza kuphedwa. Kenako bambo

a mtsikanayo anati, “Tikuona kuti ndi mwayi waukulu

kuti mwabwera kwathu kuno kudzafunsira banja

monga inuyo Mfumu ya Zinyama zonse. Koma tikuona

kuti mwana wathuyu ndi wamng’ono kwambiri. Ndiye

popeza muzikakhala naye, mukhoza kukamuvulaza

ndi zala komanso mano anuwo. Ndiye timafuna

tikupempheni kuti muwenge zala zanuzo komanso

muzule mano anu akuluakuluwo. Kenako

mudzabwere kudzatenga mtsikanayu kuti akhale

mkazi wanu.” Popeza Mkangowo unakonda kwambiri

mtsikanayo, unachitadi zimene makolowo anapempha.

Unawenga zala zake komanso unachotsa mano ake

akuluakulu. Koma utapita kwa makolo a mkazi uja,

anthu anayamba kuuseka chifukwa cha mmene

unkaonekera komanso chifukwa choti siunkaopsanso.

Mpandamachokero Anthology

156
Phunziro: Chikondi chikhoza kusintha munthu woopsa.

Mafunso

1. Kodi Mkango ukanatani kuti ukwatire

mtsikanayo popanda kuwenga zala komanso

kuchotsa mano ake?

2. Kodi mukuganiza kuti makolo a mtsikanayo

analola kuti Mkango ukwatire mwana wawo,

Mkangowo utawenga zala komanso kuzula mano

ake? N’chifukwa chiyani mukutero?

3. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

157
Kamtolo ka Mitengo

Bambo wina anadwala kwambiri. Atatsala pang’ono

kumwalira, bamboyo anaitanitsa ana ake kuti awauze

mawu omaliza. Zimadabwitsa kuti anthu ambiri

amadikira kaye kuti atsale pang’ono kutsirizika

n’kumanena mawu omaliza, pomwe anali ndi nthawi

yambirimbiri yoti akanachita zimenezo. Mwina

amachita zimenezi popeza paja amati, mawu

oyankhulidwa ndi munthu yemwe akutsirizika ndi

omwe amatsakamira m’khutu. Ndiye bamboyu anauza

wantchito wake kuti abweretse kamulu ka mitengo

komwe anakamanga pamodzi ndipo anauza ana akewo

kuti, “Tathyolani.” Mwana woyamba anayesetsa kuti

athyole koma analephera. Mwana wachiwirinso

anayesa koma analephera. Ndiyeno bamboyo anauza

anawo kuti, “Tsopano masulani mitengoyo. Ndipo

aliyense atenge kamtengo kamodzi.” Anawo atachita

zimenezi, anawauza kuti, “Thyolani.” Anawo anathyola

timitengoto mosavuta ndipo bamboyo anati, “Mwaona

zimene zachitika? Mtengo suvuta kuthyola ukakhala

wokha, koma ikakhala yambiri, imakhala yolimba

kwambiri moti munthu sungaithyole. Nanunso

muphunzirepo kanthu. Dziwani kuti ngati mutayamba

Mpandamachokero Anthology

158
kukangana aliyense n’kuyamba kuchita zake, zinthu

sizidzakuyenderani bwino. Nanunso mukapanda

kusamala anthu adzakuthyolani ndipo mafupa anu

adzalira gobedee!”

Phunziro: Mu umodzi muli mphamvu.

Mafunso

1. Kodi n’chifukwa chiyani zinali zophweka ana

aja kuthyola mtengo umodziumodzi?

2. Kodi tinganene kuti ana a bamboyu anali ngati

mitengo imeneyi chifukwa chiyani?

3. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

159
Mawu Omaliza a Mkango

Nthawi ina Mkango unadwala mwakayakaya ndipo

utatsala pang’ono kufa, unaitana nyama zonse kuti

uziuze mawu omaliza. Unanena kuti izilowa nyama

imodziimodzi kuphanga lake. Choncho Mbuzi inapita

kuphanga la Mkango ndipo inamvetsera kwa nthawi

yaitali mawu omaliza a Mkangowo. Kenako Nkhosa

inakalowa ndipo kenako Ng’ombe nayonso inalowa

kuti ikamve mawu omaliza a Mfumu ya Zilombo zonse.

Phangalo silinkadziwika kuti ndi lalikulu bwanji

chifukwa munali m’dima wa tsokomola

ndingakuponde. Komabe nyamazo zinapitiriza kulowa

m’phangalo. Koma kenako, Mkango uja unayamba

kuchira moti unadzuka n’kuima pakhomo la phanga

lake ndipo unaona Nkhandwe ikudikira panja pa

phangalo. Ndiyeno unafunsa Nkhandweyo kuti,

“N’chifukwa chiyani sukubwera kudzamva mawu anga

omaliza?” Koma poyankha Nkhandweyo inati, “Pepani

mfumu yanga, pansipa pakuoneka mapazi a nyama

monga Mbuzi, Nkhosa komanso Ng’ombe, ndipo

zikuoneka kuti nyamazi zalowa m’phanga lanulo.

Koma sindikuona mapazi a nyamazi zikutuluka.

Zimenezi zinandisokoneza mutu kwambiri, moti

Mpandamachokero Anthology

160
ndinayamba kuchita mantha. Mantha amenewa

akhoza kutha ngati mutatulutsa nyama zonse zomwe

zalowa m’phanga lanulo. Ngati mutatero ndiye

mukhoza kundimasura moti nanenso ndikhoza

kubwera kuti ndidzamve mawu anu omaliza.”

Phunziro: N’zosavuta kugwera m’manja mwa adani

koma zimakhala zovuta kutulukamo.

Mafunso

1. Kodi chinachitika n’chiyani ndi nyama zomwe

zinalowa m’phanga la Mkango lija?

2. Kodi mukuganiza kuti Mkango unkadwaladi?

N’chifukwa chiyani mukutero?

3. N’chifukwa chiyani Nkhandwe inkakayikira zoti

Mkango umadwaladi mwakayakaya?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

161
Ubongo wa Mbawala

Tsiku lina Mkango unagwirizana ndi Nkhandwe kuti

zipite kosaka. Mkangowo unali utatumiza uthenga

kwa Mbawala woiuza kuti nkhandwe ikufuna

kukhazikitsa mtendere ndi Mbawalayo. Ndiyeno

Mbawala itafika pamalo omwe anagwirizana kuti

akakumane, inasangalala kwambiri kuona kuti

Mkango nawonso wabwera monga mkhalapakati wa

mgwirizanowu ndipo inaona kuti yalemekezedwa

kwambiri ndi Mfumu ya Nyama zonse. Mbawalayo

inati, “Ndafika kalekaletu pano, paja a mvula zakale

anati kambalame kolawira ndi kamene kamatola

mphutsi!” Nkhandwe itamva zimenezi inamwetulira

n’kunena kuti, “Komatu khoswe wachiwiri ndi amene

amadya zomwe zili pamsampha! Woyamba amafa

atavuvutidwa ndi msamphawo.” Ali mkati

mokambirana zimenezi, Mkango uja unagwira

Mbawalayo n’kuipha ndipo unauza Nkhandwe ija kuti,

“Chakudya chathu chalero ndi chimenechi. Ndikufuna

kuti uziyang’anira nyamayi, ineyo ndikabe kaye tulo

pang’ono. Ndiye popeza ukudziwa zimene ndimachita

ndi anthu osamvera, usayerekeze n’komwe kukhudza

nyamayi.” Mkangowo unachokadi ndipo Nkhandweyo

Mpandamachokero Anthology

162
inkayang’anira nyamayo. Koma patapita nthawi,

Nkhandweyo inayamba kumva njala. Ndiye itaona kuti

Mkango sukubwera, inaganiza zochotsa ubongo wa

Mbawalayo n’kuudya. Posapita nthawi, Mkango uja

unatulukira ndipo utayang’ana bwinobwino,

unazindikira kuti ubongo wa Mbawalayo

wachotsedwa. Kenako unafunsa Nkhandweyo

mwaukali kuti, “Kodi iwee, ubongo wa nyamayi

wausiya kuti?” Koma Nkhandweyo inayankha kuti,

“Mbawalayitu inalibe ubongo, chifukwa ikanakhala

kuti inali ndi ubongo, sikanabwera pano. Ikanayamba

yaganiza kaye kuti chilengere Mulungu dziko,

zinachitikapo liti Mbawala kupanga mgwirizano ndi

Nkhandwe, mkhalapakati wakenso n’kukhala

Mkango.”

Phunziro: Munthu wanzeru sasowa choyankha.

Mafunso

1. Kodi nzeru za Nkhandwe zinamuthandiza

bwanji kudziwa zoyankha?

2. Kodi mukuganiza kuti Mkangowo

unangoisiyasiya Nkhandweyo?

3. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

163
Mpandamachokero Anthology

164
Nkhwazi Ibayidwa ndi Muvi

Tsiku lina Nkhwazi inkauluka ndipo mwadzidzidzi

inangozindikira kuti yabaidwa ndi muvi moti inavulala

kwambiri. Kenako inayamba kugwa pansi ndipo

magazi ankangoti chuuu kuchucha kuchokera

pamene inabaidwapo. Itayang’ana pamene

inabaidwapo inaona kuti muviwo unali

utamangiriridwa ndi nthenga yake. Ndiye pamene

inkafa inanena kuti, “Nthawi zambiri timapereka kwa

adani athu chida choti atiphere.”

Phunziro: Nthawi zina timapereka kwa adani anthu

chida choti atiphere.

Mafunso

1. Kodi ndi chiyani chimene mwina n’kutheka

Nkhwazi inapereka kwa mdani wake chimene

chinaiphetsa?

2. Kodi mdani wa Nkhwaziyi ndi ndani?

3. Kodi tikuphunzirapo chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

165
Kuwerengera Madzi a Mphutsi

Tsiku lina mtsikana wina ananyamula mtsuko

wodzadza ndi mkaka pamutu pake kuti akagulitse

kumsika. Koma ali m’njira, anayamba kuganizira

zomwe angachite ndi ndalama zomwe angapeze

akagulitsa mkaka womwe anasenzawo. Anati,

“Ndikakangougulitsa, ndikagula nkhuku kwa Angozo.

Nkhukuzo zikakula, zidzayamba kuikira mazira

ambirimbiri ndipo akadzachuluka, ndidzawagulitsa

kwa a Nankhoma. Ndalama zomwe nditadzapeze

ndikadzagulitsa mazirawo ndidzagula diresi yokongola

komanso mpango woti ndizidzavala kumutu.

Ndikuganiza kuti ndikamadzayenda nditavala

zimenezi, anyamata onse azidzangondilondola.

Sindikukayikira kuti Nachisale akadzaona zimenezi

adzachita nsanje. Koma aa, ndizidzangokhala ngati

sizikunditani, sindikundikhudzaaa!

Ndizidzangomuyang’ana cham’mbali kwinaku

ndikuyendetsa mutu wangawu chonchi . . . ” Nthawi

yomweyo mtsuko unali pamutu uja unagwa pansi

n’kusweka, ndipo mkaka wonse unataika. Zitatere

anabwerera kwawo akulira n’kukawauza mayi ake

zomwe zinachitika. Atamva zimene mwana wawoyo

Mpandamachokero Anthology

166
ananena, mayiwo anati, “Mwana wanga,

osamawerengera zinthu zimene sunazipeze.”

Phunziro: Osamawerengera madzi a mphutsi.

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani mtsikanayu ankaganiza

kuti mkaka wodzadza mtsukowo umuthandiza

kuti adzagule diresi komanso mpango?

2. Kodi akanatani kuti asagwetse mtsukowo?

3. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

167
Hatchi ndi Bulu

Tsiku lina Hatchi ndi Bulu zinkayendera limodzi.

Hatchi inkayenda mwamatama pomwe Bulu anali

atanyamula katundu wambirimbiri moti anali

atalemedwa zedi. Bulu anadandaula kuti,

“Ndimalakalaka ndikanakhala ngati iwe. Sugwira

ntchito iliyonse, koma umapatsidwa zakudya zambiri

komanso zonse zimaoneka kuti zimakuyendera

bwino.” Ndiyeno tsiku lotsatira kunayambika

nkhondo, ndipo Hatchiyo inatengedwa n’kupita

kunkhondo moti ili kumeneko inavulala kwambiri

n’kutsala pang’ono kufa. Bulu uja atamva zimene

zinachitikazo anati, “Inetu ndimadzinamiza. Kuli

bwino kumakhala movutika uli pamtendere kusiyana

n’kumadya bwino moyo wako uli pachiswe.”

Phunziro: Moyo ndi wofunika kwambiri kuposa

chilichonse.

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani Bulu ankachitira nsanje

Hatchi?

2. Bulu ananena kuti Hatchi sinkachita

chilichonse. Kodi ankanena zoona? Ngati

Mpandamachokero Anthology

168
sankanena zoona, kodi Hatchi inkagwira ntchito

yanji?

3. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

169
Woliza Lipenga

Tsiku lina munthu woliza lipenga kunkhondo

anayandikira kwambiri adani ndipo anamugwira.

Atangotsala pang’ono kumupha, munthuyo

anapempha anthuwo kuti amuchitire chifundo. Anati,

“Inetu sindimenya nawo nkhondo, ndipo sindinyamula

chida chilichonse. Ndimangonyamula chitolilochi.

Nanga chimenechi ndingaphere munthu ngati? Ndiye

ndichitireni chifundo, musandiphe, chifukwa nanenso

sindipha anthu!” Koma anthuwo anati, “N’zoona kuti

sumenya nawo nkhondo, koma umalimbikitsa

komanso kutsogolera asilikali kuti amenye nkhondo,

ndiye tikupha pa chifukwa chimenechi.”

Phunziro: Tikhoza osachita nawo zoipa, ngati zonena

zathu zimalimbikitsa ena kuchita zimenezo,

n’chimodzimodzi kuti nafenso timachita zinthuzo.

Mpandamachokero Anthology

170
Mafunso

1. N’chifukwa chiyani woliza lipenga ankaganiza

kuti adani akewo samupha?

2. Koma kodi woliza lipengayo akanapangitsa

bwanji kuti adani akewo akumane ndi mavuto?

3. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

171
Katswiri Wolira Nyama Zosiyanasiyana

Pachikondwerero china, katswiri wina woyerekeza

kulira kwa zinyama anaseketsa anthu kwambiri

pamene ankalira nyama zosiyanasiyana. Pomaliza

munthuyo analira ngati nkhumba ndipo anthu

anasangalala kwambiri moti ankaganiza kuti ikulira

ndi nkhumba yeniyeni. Ndiyeno munthuyo anaima

kaye n’kunena kuti, “Kumeneku ndi kulira kwa

nkhumba. Ngati mukukayikira kuti ndimaliradi ndi

ineyo, mawa mudzakhale pomwepo kuti mudzamve

kulira kwa nkhumba yeniyeni.” Anthuwo atamva

zimenezi anaseka kwambiri ndipo tsiku lotsatira

munthu uja anabweranso. Koma pa nthawiyi anabisa

mwana wankhumba ndipo anawerama

n’kumamukoka khutu. Mwana wankhumbayo

anayamba kulira ndipo anthuwo atamva kulirako

anayamba kumugenda n’kumauza munthuyo kuti

asiye. Munthuyo anati, “Ndinu wopusa kwabasi.

N’chifukwa chiyani mumasangalala munthu

akamayerekeza kulira kwa nyama n’kumadana ndi

kulira kwa nyama yeniyeniyo?”

Phunziro: Anthu amasangalala ndi kuyerekezera

chinthu chinachake n’kumadana ndi chinthucho.

Mpandamachokero Anthology

172
Mafunso

1. Kodi katswiriyu ankapanga chiyani chomwe

chinkaseketsa anthu?

2. N’chifukwa chiyani anthu aja anakwiya ataona

kuti imene imalirayo inali nkhumba yeniyeni?

3. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

173
Nkhandwe ndi Mbuzi

Tsiku lina Nkhandwe inkayendayenda m’nkhalango

ndipo mwatsoka inagwera m’mbuna ndipo inkalephera

kutulukamo. Ndiyeno zinachitika kuti Mbuzi

inkadutsa pafupi ndi mbunayo ndipo Mbuziyo itaona

Nkhandweyo inafunsa kuti, “Kodi mukutani

m’menemo?” Nkhandweyo inayankha kuti, “Chaka

chino kukhala chilala choopsa moti madzi azisowa.

Ndiye ndikukumba chitsimechi kuti chilalacho

chikamafika, ndikhale ndili ndi madzi okwanira.

Nawenso dumphira momwemuno tithandizane kuti

tizidzamwera limodzi madziwa.” Mbuziyo itamva

zimenezi inaona kuti umenewo ndi mwayi wake, moti

inalumphiradi m’mbunamo. Kenako Nkhandwe ija

inalumphira pamsana pambuziyo n’kutuluka

m’dzenjemo ndipo inati, “Tionana bwanawe.

Kuyambira lero usadzayerekezenso kumvera

malangizo ochokera kwa munthu yemwe wapanikizika

ndi mavuto.”

Phunziro: Osamakhulupirira malangizo ochokera kwa

munthu amene wapandikizika, akhoza kukhala kuti

akungofuna njira yothawira mavutowo.

Mpandamachokero Anthology

174
Mafunso

1. N’chifukwa chiyani Mbuzi inadumphira

m’dzenje muja?

2. N’chifukwa chiyani Nkhandwe inkafuna kuti

Mbuziyo igwere m’dzenjemo?

3. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

175
Nsikidzi ndi Ana Ake

Munthu wina atatopa kulumidwa ndi Nsikidzi,

anaganiza zotereka madzi kuti azikhaulitse. Kenako

anatenga bulangete lakelo n’kuliika munkhali

n’kutenga madzi obwadamuka n’kuwakhuthulira

momwe munali bulangetelo kuti nsikidzizo zikhaule.

Ndiye zimenezi zitangochitika, Nsikidzi yomwe inali

m’bulangetemo inauza ana ake kuti, “Ana anga,

muyenera kukhala opirira, chifukwa chilichonse

chotentha, pamapeto pake chimazizira. Vuto

lingatenthe bwanji, limakhala ndi mapeto ake.”

Phunziro: Chilichonse chotentha, pamapeto pake

chimazizira. Mavuto angakule bwanji, amakhala ndi

polekezera.

Mafunso

1. Kodi munthu anatani Nsikidzi zitamuvuta zedi?

2. N’chifukwa chiyani Nsikidzi inauza ana ake

kuti “chilichonse chotentha, pamapeto pake

chimazizira”?

3. Kodi ndi zoona kuti vuto lililonse limakhala ndi

pothera?

4. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

176
Nyani ndi Mwana Wake

Nthawi inayake, padziko lapansi panachitika

mpikisano woonetsa ana okongola kwambiri. Ndiye

Nyani atangomva za mpikisanowu, nayenso anatenga

mwana wake n’kuthamangira komweko. Malamulo a

mpikisanowo anali akuti, usanayambe kuchita nawo

mpikisanowo unkafunika kukaonetsa mwana wako

kwa wochititsa mpikisanowo. Ndiye wochititsa

mpikisanowo ataona mwana wa Nyaniyo anaseka

koopsa, ndipo anafunsa Nyaniyo kuti, “Mayi,

mwabweretsachi n’chiyani?” Nyaniyo anayankha kuti,

“Mwana, bwanji?” Wochititsa mpikisanowo anati,

“Nanga bwanji mphunozi?” Akuti ankaseka mphunozo

chifukwa zinkangooneka ngati zochita kuboola ndi

tchizulo. Kenako anapitirizabe kuseka mwachipongwe

kwambiri. Koma kenako Nyaniyo anati, “Inuyo

mukhoza kuseka mmene mungathere. Koma dziwani

kuti kwa ineyo, padziko lonse lapansili palibenso

mwana wina wokongola kwambiri kuposa wangayu!”

Phunziro: Mwana sanyansa mayi wake. Anthu ena

akhoza kumamuona kuti ndi wonyansa, koma kwa

mayi wake ndi wokongola kwambiri.

Mpandamachokero Anthology

177
Mafunso

1. Kodi tinganene kuti Nyani ankaonadi kuti

akhoza kupambana mpikisanowo?

2. N’chifukwa chiyani wochititsa mpikisanowu

anaseka ataona mwana wa Nyaniyo?

3. Kodi nyaniyo anayankha zotani?

4. Kodi wochititsa mpikisanowu analakwitsa

chiyani?

5. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

178
Nkhuku ndi Mwala Wamtengo Wapatali

Tsiku lina Tambala ankayendayenda kwinaku

akusaka chakudya. Kenako anafukula kanthu

kenakake kowala pakati pazinyalala. Ndiyeno anati,

“Ho! ho! Mulungu sapatsa pamanja!” Kenako

anakachotsa pazinyalalapo ndipo anazindikira kuti ndi

kamwala kamtengo wapatali. Ndiyeno anati, “Ukhoza

kukhaladi wamtengo wapatali kwa anthu amene

amakuona ngati mwala wapadera. Koma kwa ineyo,

chinthu chamtengo wapatali ndi deya kapena misere

imene imandithandiza kuti ndikhale ndi moyo!”

Phunziro: Chinthu chimakhala chamtengo wapatali

malinga ndi mmene munthu akuchionera.

Mafunso

1. Kodi mukuganiza kuti tambala ankaganiza kuti

wapeza chiyani?

2. Kodi chinthu chamtengo wapatali chimene

tambalayu ankafunafuna chinali chiyani?

3. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

179
Khoswe ndi Msampha

Bambo wina makoswe anamuvuta zedi ndipo amati

akagula chinthu, Makoswewo ankamubera

n’kukalowetsa kuuna wawo. Tsiku lina makoswewo

anamusautsa kwambiri chifukwa

ankaongoyendayenda padenga moti tulo sadatione.

Zinafika pomukwana kwambiri Makoswewo

atamuboolera zovala zake ndipo anaganiza zothana

nawo. Anayesa kuwathirira tameki, koma palibe ndi

m’modzi yemwe amene anadya. Kenako anaganiza

zotchera misampha. Anaika misampha ingapo

m’nyumbamo ndipo pamsampha uliwonse anaika

chakudya chomwe Makoswewo ankachikonda

kwambiri. Makoswewo ataona zimenezi, anakopeka

kwambiri moti khoswe wina anati, “Tiyeni

tikasangalale ndi chakudya!” Koma mnzake anamuuza

kuti, “Taima kaye bwanawe, wadziwa bwanji kuti

tikasangalala. Kodi munthuyu anayamba wachitazo

zimenezi? Mwinatu akufuna atikole.” Koma Khoswe

wina wadyera kwambiri sanaupeze mtima, moti

anaganiza zotenga chakudya chomwe chinali

pamsampha wina. Atangochigwira, msamphawo

unafwamphuka ndipo unamukang’antha pamimba.

Mpandamachokero Anthology

180
Khosweyo anayamba kulira ndipo anauza anzakewo

kuti, “Chakudyachi ndilibe nachonso ntchito,

mukhoza kuchitenga. Chomwe ndikufuna panopa ndi

kuchoka pamsamphawu.”

Phunziro: Kumaganizira zotsatira za zomwe

mukuchita. Osamangotengeka ndi chilichonse.

Mafunso

1. Kodi khoswe wadyera anatengeka ndi chiyani?

2. Kodi ananena chiyani atapanidwa ndi

msampha?

3. Kodi tinganene kuti sankachifunadi

chakudyacho? N’chifukwa chiyani anasintha

maganizo?

4. N’chifukwa chiyani tiyenera kumaganizira

mavuto amene tingakumane nawo tisanachite

chilichonse?

5. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

181
Nkhani ya Kutha kwa Dziko

Kagiso anali ndi mbuzi ndipo pa nthawiyi n’kuti

itakula ndithu. Ndiye tsiku lina kunabwera anzake

omwe ankakhala moyandikana nawo nyumba

n’kumuuza kuti aphe mbuziyo. Atawafunsa chifukwa

chake, anthuwo anamuuza kuti, “Nkhosa yakoyitu

yanenepa. Tiye tikaiphe kumtsinje. Popeza kunjaku

kwatentha, tikaiphere kumtsinjeko kuti

tikakatenthedwa tizikangolowa mumtsinje

n’kumasambira.” Koma Kagiso anawayankha kuti,

“Ayi, sindikufuna kupha mbuzi yanga.” Koma wina

anamuuza kuti, “Kodi sunamve? Dzikolitu likutha

mawa!” Kagiso anadabwa ndi zimenezi ndipo ataona

kuti akhoza kufa asanadye mbuzi yake, anavomera

zoipha ndipo anaigwira n’kumapita nayo kumtsinje.

Atafika kumeneko anaipha ndipo anayamba kuisenda

chikopa. Anzake aja atayamba kumva kutentha

anavula zovala zawo zonse n’kuyamba kusambira.

Koma Kagiso ankangoti jijirijijiri kukonza mbuzi ija.

Atamaliza kuikonza, anakoleza moto ndipo anayamba

kuiwotcha. Pa nthawiyi n’kuti anzake aja akupanga

chipako cham’madzi. Patapita nthawi, kafungo

kabwino kanayamba kumveka ndipo anzake aja

Mpandamachokero Anthology

182
anatuluka m’madzi muja n’kumuuza kuti, “Koma

ndiye utipha ndi fungotu, tigawireko titsuke

m’kamwa.” Koma atayang’ana pamene panali zovala

zawo anaona kuti palibe ndipo anamufunsa kuti,

“Kodi zovala zathu wazisiya kuti?” Kagiso anayamba

kuzimbaitsa nkhaniyi amvekere, “Inetu ndimadabwa

anthu akamanena kuti zovala. Ndimaona kuti munthu

akavula zimene anavala n’kuziika poteropo,

sizikhalanso zovala, koma zovula.” Anzakewo atamva

zimenezi anakwiya kwambiri ndipo anamuuza kuti,

“Usatitayitse nthawi iweeee! Zovala zathu wazisiya

kuti?” Ndiyeno Kagiso anayankha kuti, “Ndazikolezera

moto!” Atamva zimenezo anzakewo anapsa mtima

kwambiri ndipo anati, “Zoona ungakolezere moto

zovala zathu?” Koma Kagiso anayankha kuti, “Ee, pali

vutoo? Si paja munati dziko likutha mawa, ndiye

mukufunanso zovala zantchito yanji?” Anzakewo

anangoti kukamwa yasaa, ndipo anayamba kuganizira

mmene angayendere kuti akafike kwawo.

Phunziro: Nthawi zina ukamapusitsa mnzako,

umakhalanso ukudzipusitsa wekha.

Mpandamachokero Anthology

183
Mafunso

1. Kodi zimene anzake a Kagiso ankanena, zoti

dziko likutha mawa, zinali zoona? N’chifukwa

chayani mukutero?

2. N’chifukwa chiyani Kagiso anakolezera moto

zovala za anzakewo?

3. Kodi tikuphunzirapo chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

184
Nkhani ya Kalulu ndi Nkhandwe Yatulo

Iyi ndi nkhani ya achikulire a Kalulu ndi Nkhandwe.

Tsiku lina Kalulu ankafuna kupusitsa Nkhandwe

ndipo anaima pafupi ndi mwala wina. Mwalawo

unaima ngati ukufuna kugwa ndipo Kalulu

ankaukankhira m’mwamba. Nkhandwe itaona

zimenezi inafunsa Kalulu kuti, “Achikulire, mukutani

pamenepo?” Ndiyeno Kalulu anaiuza kuti, “Tabwera

mwamsanga bwanawe, mwalawutu ukugwa. Taugwira

kuti ineyo ndikatenge mtengo tidzauimikire.”

Nkhandweyo inavomeradi ndipo Kaluluyo

ananyamuka n’kumapita n’kuisiya Nkhandwe itagwira

mwalawo. Nkhandweyo inachita zimenezi kwa nthawi

yaitali zedi koma Kalulu uja sanabwererenso.

Nkhandweyo inayamba kuitana Kalulu uja ndipo

inkati, “Kodi simunaupezebe mtengowo, mwalawutu

ukundilemera.” Koma kunali zii. Nkhandweyo

itatheratu, inaganiza zosiya mwalawo. Inausiya

mwachanguchangu n’kuchokapo kuti usaigwere.

Koma itachoka, inaona kuti mwalawo sunasunthe.

Ngakhale inaona zimenezi, Nkhandweyo sinatengerepo

phunziro. Tsiku linanso Kalulu anapita kukamwa

madzi padziwe lina ndipo m’madzi munkaoneka

Mpandamachokero Anthology

185
mwezi. Apa anaganizanso zopusitsa Nkhandwe ija

ndipo anaiitana n’kuiuza kuti, “Taona m’madzimo,

pansi pamadzipo, chimenechotu ndi chakudya.”

Ndiyeno Nkhandweyo inati, “Ee, ndachiona, ndi

chakudya chanji?” Kaluluyo anayankha kuti, “Ndi

mtanda wa nsima. Kuteroko ineyo ndayamba kale

kumwa madziwa n’cholinga choti aphwe. Ndiye popeza

ndiwe wamkulu, ukhoza kumaliza madzi atsalawa,

kuti kenako titenge nsimayo tidye. M’bale wanga,

tamwa madziwa kuti timeze kadaunda madzi.”

Nkhandwe yatuloyo inavomeranso zimenezi ndipo

inayamba kumwa madzi aja. Sinazindikire kuti

chimene chimaoneka m’madzicho si nsima koma

mwezi. Kenako kalulu uja anatsanzika n’kumapita.

Nkhandweyo inamwa madziwo mpaka mimba yake

inangoti nguu, kukhuta. Itaona kuti sakuthapo,

inangonyamuka n’kumapita kwawo ndipo usiku wa

tsiku limenelo sinatione tulo chifukwa cha kupweteka

kwa mimba yake.

Phunziro: Osalola kuti munthu akupusitse kawiri.

Mpandamachokero Anthology

186
Mafunso

1. Kodi Kalulu anapusitsa bwanji Nkhadwe?

2. N’chiyani chikusonyeza kuti Nkhandweyo inali

yatulo?

3. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

187
Anyamata Awiri Akumana ndi Wokalamba

Kalekalelo panali anyamata awiri a pachibale.

Anyamatawa anaganiza zoyamba kuyendayenda

padzikoli kuti akafunefune mwayi komanso

chisangalalo. Ali m’njira anaona bambo wina

wachikulire akuyenda patsogolo pawo. Bamboyu anali

ndi ndevu zowirira zedi. Ndiyeno mnyamata wamkulu

anati, “Wamuona bambo uyo? Alitu ndi ndevu zoti

ndikhoza kuzendewera. Ndevu zopangitsa mwana

kufunsa kuti, ‘Ababa pakamwa mpati?’ Mwina

mwachidule ndingoti ali ndi ndevu za ponya mtedza

upaone.” Anyamatawo ankachita chidwi ndi ndevuzo

moti bamboyo anaima n’kuwafunsa kuti, “Mukupita

kuti?” Anyamatawo anamufotokozera chimene

ankafuna ndipo bamboyo anati, “Ndikhozatu

kukuthandizani.” Kenako anapisa m’thumba

n’kutulutsa kajumbo kodzadza ndi ndalama. Kenako

anafunsa anyamatawo kuti, “Ndani amene akufuna

ndalamazi?” Nthawi yomweyo mnyamata wamkulu uja

anayankha kuti, “Ndipatseni ine!” Bamboyo

anamupatsadi ndipo kenako anapisanso m’thumba

n’kutulutsa mwala wamtengo wapatali ndipo

anafunsaso kuti, “Ndani akufuna mwala wamtengo

Mpandamachokero Anthology

188
wapataliwu?” Nthawi yomweyo mnyamata wamkulu

uja anayankhanso kuti, “Ndipatseni ine!” Bamboyo

anamupatsadi. Koma mnyamata wamng’ono uja

sanalandire kanthu. Ndiyeno bambo wachikulireyo

anatula thumba limene ananyamula n’kupempha

anyamata awiriwo kuti, “Ndani amene

atandinyamulire thumbali kuti akandisiyire kwathu?”

Atamva zimenezi, mnyamata wamkulu uja anangoti

duu. Koma wamng’ono uja anapinda malaya ake

n’kusenza thumbalo n’kuuza munthu wachikulireyo

kuti, “Tiyenitu muzinditsogolera.” Bamboyo

anangomwetulira n’kumuuza kuti, “Tenga thumbali

mwana wanga, ndakupatsa kuti likhale lako.

Utengenso zonse zimene zili mkatimo.” Mnyamatayo

atamva zimenezo anati, “Ayi, musatero, ndikungofuna

kukuthandizani basi.” Koma bamboyo anamuuza kuti

wamupatsa monga mphatso. Mnyamatayo atatsegula

thumbalo, sanakhulupirire zimene anaona. Anapeza

kuti thumbalo linali lodzadza ndi miyala yamtengo

wapatali!

Phunziro: Khalidwe labwino ndi limene limapangitsa

munthu kupeza mwayi.

Mpandamachokero Anthology

189
Mafunso

1. Kodi anyamata awiriwa ankafuna chiyani?

2. Kodi anyamatawa anali osiyana bwanji?

3. Ndi uti amene anali wakhalidwe labwino?

N’chifukwa chiyani mukutero?

4. Kodi khalidwe labwino linathandiza bwanji

mnyamata wamng’ono uja kupeza mwayi

waukulu?

5. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

190
Chisoni Chinapha Nkhwali

Kalekalelo Njoka inkafuna kuwoloka mtsinje wina.

Ndiye popeza palibe chimene ikanachita kuti iwoloke

yokha, inapempha Nkhwali kuti aithandize. Nkhwaliyo

inamva chisoni zedi ndi mmene Njokayo inkaonekera

ndipo inavomera kuti ichitadi zimene Njokayo

inkafuna. Inauza Njokayo kuti, “Zizengereze m’khosi

mwangamu!” Kenako inanyamuka n’kuuluka. Itafika

kutsidya, Nkhwaliyo inauza Njokayo kuti, “Bwanawe,

tafikatu. Tsopano ukhoza kutsika kuti uzipita.” Koma

Njokayo inakana kwamtuwagalu kuti sichoka.

Pamapeto pake, chisoni chinachitsa kuti Nkhwali ione

tsoka la nkhuku.

Phunziro: Chisoni nthawi zina chimapweteketsa.

Mpandamachokero Anthology

191
Mafunso

1. N’chiyani chinachititsa kuti njoka ipemphe

thandizo kwa nkhwali

2. Kodi njokayo inayamikira zimene mnzakeyo

anamuchitira?

3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti nkhwali

sinaganize bwino povomera kuthandiza njoka?

4. Kodi nkhwali inakumana ndi zotani pamapeto

pake?

5. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

192
Chisoni Chinaphetsa Wosema Mitondo

Nthawi ina alenje anavumbulutsa gondwa ndipo

anayamba kumuthamangitsa. Alenjewo

anamupezeketsa gondwayo moti anangotsala pang’ono

kumugwira. Gondwayo anayesetsa kukoka phazi

koma sizinam’thandize moti anaganiza zopempha

thandizo kwa munthu wina yemwe ankasema mitondo

m’nkhalangomo. Atatoperatu, gondwayo anapempha

wosema mitondoyo kuti, “Ndithandizeni chonde

ndagwira mwendo wanu. Alenjewa akufuna moyo

wanga, chonde ndipulumutseni!” Wosema mitondoyo

anamva chisoni kwambiri ndipo anauza Gondwayo

kuti amubisa. Koma popeza panalibe malo pafupi

pomwe akanamubisapo, wosema mitondoyo

anangoganiza zomubisa m’kamwa. Alenjewo atafika

anafunsa wosema mitondoyo kuti, “Mwaona Gondwa

atadutsa apa?” Koma wosema mitondoyo anapukusa

mutu posonyeza kuti sanamuone. Ndiyeno alenjewo

atachoka, munthuyo anauza Gondwa uja kuti, “Alenje

ajatu apita, ukhoza kutuluka tsopano!” Koma

gondwayo anayankha kuti, “Tadikirani kaye pang’ono,

muli kenakake kokoma muno!”

Mpandamachokero Anthology

193
Phunziro: Kumaona anthu owathandiza, ena akhoza

kungokubweretsera mavuto.

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani wosema mitondo anaganiza

zothandiza Gondwa?

2. Kodi Gondwa anayamikira zimene munthuyo

anamuchitira?

3. Mukuganiza kuti chinamuchitikira munthuyu

n’chiyani?

4. Kodi nthanoyi ikufanana bwanji ndi ya mutu

wakuti, “Chisoni Chinaphetsa Nkhwali”?

5. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

194
Azimayi Anzeru

Kalekalelo, mfumu ina yamphamvu kwambiri inalanda

mzinda wina. Mfumuyi inalamula kuti amuna onse a

m’mudziwo aphedwe, koma akazi anauzidwa kuti

akhoza kuthawa. Anauzidwanso kuti akhoza kutenga

chilichonse chimene angakwanitse kunyamula.

Azimayiwa atamva izi, anangolowa m’nyumba zawo

n’kukaika amuna awo kumbuyo n’kumathawa nawo.

Mfumuyo itaona zimenezi inafunsa azimayiwo kuti,

“N’chifukwa chiyani mukuchita zimenezi? Si paja

ndinakuuzani kuti muthawe nokha?” Koma azimayiwo

anayankha kuti, “Pajatu munati tikhoza kutenga

chilichonse chimene tingakwanitse kunyamula! Ndiye

kwa ifeyo katundu ofunika kwambiri ndi amene

tanyamulayu!” Mfumuyo inaona kuti zimenezi

n’zomveka, moti inalola azimayiwo kutenga katundu

ananyamulayo, ndipo amuna onse a m’mudziwo

anapulumuka.

Phunziro: Osamaiwala zinthu zofunika kwambiri.

Mpandamachokero Anthology

195
Mafunso

1. N’chiyani chikusonyeza kuti azimayiwa anali

anzeru?

2. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene akanakwanitsa

kunyamula, kupatulapo amuna awo?

3. Kodi anagwiritsa ntchito bwanji mawu a

mfumu kupulumutsa amuna awo?

4. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

196
Mwana Wosamvera

Mayi wina anali ndi mwana wosamvera, mwanayu

sankamva ndi pakamwa pokha, koma am’menye basi.

Nthawi zina amati akamuuza kuti asachite zinazake,

ankakhala ngati wamva, koma zomwe ankachita

pambuyo pake, zinkasonyeza kuti zimene wauzidwazo

zangolowera khutu ili n’kutulukira linalo. Ndiye tsiku

lina mayiyo anauza mwanayo kuti, “Kunjatu kwacha

kalekale, nyamuka uzipita kusukulu, ukachedwatu

aphunzitsi akakubweza!” Koma mwanayo sanamvere

ndipo anapitirizabe kumuuza kambirimbiri, koma ayi

ndithu ankangozikankhira kunkhongo. Ankachita

zinthu ngati kuti kusukuluko ankakaphunzirira mayi

akewo. Koma akakhalanso pakhomo ankawatopetsa

mayi ake chifukwa ankakana kugwira ntchito.

Chinthu chimene ankachidziwa kunali kudya basi.

Ndiye mayiyu atatopa ndi khalidwe la mwanayu,

ananyamuka n’kupita kwa a Chikwapu. Atafika

anawauza kuti, “Mwana wanga akuvuta, kodi

mungakamukwapule kuti apite kusukulu?” Koma a

Chikwapu anakana. Zitatero mayiyo anaganiza zopita

kwa a Moto. Anawafotokozera kuti akufuna kuti a

Motowo akawotche a Chikwapu chifukwa akukana

Mpandamachokero Anthology

197
kukakwapula mwana, ndipo mwana akukana kupita

kusukulu. Koma nawonso a Moto anakana. Mayiyo

anakhumudwa kwambiri ndi zimenezi moti anaganiza

zopita kwa a Madzi. Atafika kumeneko

anawafotokozera kuti, “Pepanitu a Madzi. Ineyo

ndikufuna thandizo lanu. Ndikufuna mukazimitse a

Moto chifukwa akukana kuwotcha a Chikwapu, a

Chikwapu akukana kukwapula mwana, mwana

akukana kupita kusukulu.” Koma nawonso a Madzi

anakana. Kenako mayiyo anapita kwa a Ng’ombe.

Anawafotokozeranso nkhani yonse koma nawonso

anakana. Zitatero, anaganiza zopita kwa M’busa

wang’ombe. M’busayo anawamvetsa mayiwa chifukwa

nawonso anali ndi mwana wovuta ndipo ananyamuka

n’kuyamba kuthamangitsa a Ng’ombe. A Ng’ombe

ataona kuti zavuta, anayamba kuthamangira kumene

kunali a Madzi. A Madzinso ataona kuti amwedwa,

anaganiza zokazimitsa a Moto. A Moto ataona kuti

azimitsidwa, anaganiza zokawotcha a Chikwapu.

Ndipo a Chikwapu ataona kuti zinthu sizili bwino,

anayamba kukwapula mwana ndipo mwana anapita

kusukulu.

Phunziro: Osamamva nkhwangwa ili m’mutu.

Mpandamachokero Anthology

198
Mafunso

1. N’chifukwa chiyani mwana ankakana kupita

kusukulu?

2. Kodi zimene ankachitazi zikanakhudza bwanji

tsogolo lake?

3. N’chiyani chinachititsa kuti apite kusukulu?

4. Kodi nkhaniyi ikusonyeza kuti kulanga mwana

n’kofunika bwanji?

5. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

199
Mwana Wamwano

Pamudzi wina panali mwana wosamvera komanso

waulesi. Makolo ake amati akamutuma ankakana, apo

ayi ankangochokapo n’kupita kukabisala. Ndiye tsiku

lina anamukakamiza kuti apite kumunda ndipo

atafika kumundako, mwanayo anakwera mumtengo

n’kubisala. Mumtengomo munali njoka ndipo njokayo

inamuluma moti anafera pompo. Makolo ataona kuti

mwana wawo sakuoneka, anayamba kumufunafuna

ndipo anamupeza pansi pa mtengo atafa. Atayang’ana

mumtengo, anaona njoka ndipo anadziwa kuti ndi

imene yamuluma. Makolowo ataona izi anati, “Mwana

wathuyu wafa chifukwa cha mwano. Akanamvera

zimene tinamuuza, sakanafa!”

Phunziro: Mwana womvera amakhala ndi moyo

wautali.

Mafunso

1. Kodi mwanayu anali ndi mavuto otani?

2. Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani

atafika kumunda anakwera mumtengo?

3. Kodi anakumana ndi mavuto otani?

4. Kodi akanatani kuti apewe mavuto amenewa?

Mpandamachokero Anthology

200
Bambo ndi Mwana Wake

Tsiku lina bambo wina anakwera sitima limodzi ndi

mwana wake. Sitimayo itangoyamba kuyenda,

mwanayo anayamba kulongolola m’sitimayo ndipo

amauza bambo ake kuti, “Ababa, taonani mitengo

ikuthamanga! Taonaninso nyumbazi, zikuthamangatu

ngati mphenzi!” Bambo akewo anangogwedezera mutu

n’kumusiya. Anthu ena ataona izi anafunsa bamboyo

kuti, “Kodi mwana wanuyu n’koyamba kukwera

sitima?” Koma bamboyo anapukusa mutu. Kenako

mwana uja anayamba kufuntha m’sitimayo, amati

akaona chinthu, amachiyandikira kuti achionetsetse

ndipo anthu ena anayamba kusowa naye mtendere.

Ndiyeno munthu wina anauza bambo a mwanayo kuti,

“Kodi mwana wanuyu mutu wake umagwira?

N’chifukwa chiyani akungokhala ngati anadya matako

a galu?” Ndiyeno bamboyo anayankha kuti, “Si bwino

kupupuluma kuweruza munthu wina usakudziwa

nkhani yonse. Pali mawu akuti, ‘osamaweruza

munthu kuchokera pamene iweyo waima, koma

kuchokera pamene munthuyo waima.’ Mawuwa

amatanthauza kuti kumakhala kulakwa kumaweruza

munthu pongotengera zimene ukuona. Pepani kuti

Mpandamachokero Anthology

201
mwana wangayu akukusowetsani mtendere, koma

ineyo ndikumumvetsa. Mwanayutu anabadwa

wosaona. Kuteroko panopa tikuchokera kuchipatala

komwe anakamuchita opaleshoni ya maso moti

wangoyamba kumene kuona. Chilichonse ndi

chachilendo kwa iyeyu moti n’chifukwa chake

akumangodabwa ndi chilichonse. N’chifukwa

chakenso ineyo sindinamuletse. Ndimaona kuti

akatopa asiya yekha.” Atamva zimenezi, anthuwo

anamumvetsa moti anangogwira pakamwa.

Phunziro: Osamafulumira kuweruza ena usakudziwa

nkhani yonse.

Mafunso

1. Kodi vuto la mwanayu linali chiyani?

2. Kodi tinganene kuti mitengo yomwe ankaona

inkathamangadi?

3. N’chifukwa chiyani anthu ena anayamba

kudabwa naye?

4. Kodi pamene bamboyo anagwedezera mutu

ankatanthauza chiyani? Nanga bwanji pamene

anapukusa mutu?

Mpandamachokero Anthology

202
5. Kodi tinganene kuti anthu a m’sitima ija

analakwitsa kuganiza kuti mutu wa mwanayo

sugwira?

6. Kodi mukuganiza kuti akanatani kuti adziwe

vuto la mwanayo popanda kunena zachipongwe?

7. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

203
Kupulumukira M’kamwa mwa Mbuzi

Tsiku lina anyamata awiri anapeza mbuzi

itamangidwa pamtengo wina ndipo anaganiza zoti

aibe. Atangoyamba kumasula chingwe cha mbuziyo,

mwini wake anabwera ndipo anawafunsa kuti,

“N’chifukwa chiyani mukumasula mbuzi yanga?”

Anthuwo anayamba kuchita mantha. Koma m’modzi

anati, “Tinaona kuti pano palibe msipu wabwino,

ndiye tinaganiza zoti tikaimangirire pamtengo uwo.

Taonani msipu wake ukungoti biriwiribiriwiri,

kukongola. Zoona mbuziyi ife ndi njala msipu uli

m’khonde?” Mwini mbuziyo atamva zimenezi

anawakhulupiriradi. Koma mbuziyo inkadziwa kuti

anthuwo akunama. Ndiye chifukwa choti sitha

kuyankhula, akubawo anapulumukira m’kamwa mwa

mbuzi.

Phunziro: Anthu ena amapulumuka chifukwa cha

bodza.

Mpandamachokero Anthology

204
Mafunso

1. Kodi cholinga cha anyamatawa chinali chiyani?

2. Kodi ankanena zoona pamene ananena kuti

amafuna kumangirira mbuziyo pamene panali

msipu wabwino?

3. Kodi anyamatawa anapulumukira pati?

4. Tiyerekeze kuti munthu wina wapulumuka

mwamwayi galimoto ikufuna kumugunda, kodi

kungakhale kulondola titanena kuti wapulumukira

m’kamwa mwa mbuzi?

Mpandamachokero Anthology

205
Kodi Wochimwa Anali Ndani?

Pa nthawi ina alimi 10 anali paulendo. Ali paulendowo

kunayamba chimvula champhamvu komanso cha

ziphaliwali. Alimiwo ataona kuti mvulayo ikhoza

kuwapweteka, anaganiza zobisala m’kanyumba kena.

Koma atafika m’kanyumbako, anaona kuti

chiphaliwali china chinkangozungulira kanyumbako.

Pamalopo panali chiphokoso choswa makutu, moti

alimiwo anayamba kunjenjemera. Kenako anayamba

kuganiza kuti n’kutheka zoti pakati pawo pali munthu

wina wochimwa kwambiri, yemwe chiphaliwalicho

chikufuna kuti chimuphe. Ndiye anaganiza zopeza

munthuyo kuti amutulutse panja n’cholinga choti

chiphaliwalicho chikamusasanthe. Anachita zimenezi

chifukwa samafuna kuti chiphaliwalicho chiphetse

anthu osalakwa. Alimowo anakambirana zoti akoleke

zisoti zawo pamalo enaake ndipo munthu amene

chisoti chake chitauluke ndi mphepo, ndi amene ali

wochimwa. Atachita zimenezi, chisoti cha mlimi wina

chinauluka ndipo alimi enawo atangoona zimenezi,

anamugwira n’kumuponyera panja mopanda chifundo

m’pang’ono pomwe. Koma munthuyo atangotuluka

panja, chiphaliwalicho chinasiya kuzungulira

Mpandamachokero Anthology

206
kanyumbako ndipo chinamenya denga la kanyumbako

moopsa kwambiri moti alimi 9 anatsala aja anafera

momwemo. Pamenepa m’pamene zinadziwika kuti,

mlimi anamutulutsa uja ndi amene anali wabwino,

ndipo chifukwa cha munthuyo chiphaliwalicho

chinkangozungulira nyumbayo osaiomba. Ndiye

pamene alimi 9 otsala aja anatulutsa mlimiyu,

chiphaliwalicho chinaona kuti mpulumutsi wawo

wachoka, ndipo chinalanga alimi oipa mtimawo mwa

kuwapha. Chinawalanga chifukwa anatulutsa mnzawo

paja, osamuchitira chifundo ngakhale pang’ono.

Phunziro: Usanayambe kuloza kuipa kwa munthu

wina, kumayamba kaye wayeza kuipa kwako.

Mpandamachokero Anthology

207
Mafunso

1. N’chifukwa chiyani alimiwa anaganiza kuti

pakati pawo pali munthu wina wochimwa amene

chiphaliwalicho chinkamufuna?

2. Kodi atamugwira n’kumuponyera panja

chinachitika n’chiyani?

3. Kodi tinganene kuti wochimwa anali ndani

kwenikweni?

4. Kodi mukunganiza kuti chikanachitika

n’chiyani, akanamulola mlimiyu kukhalabe nawo

limodzi?

5. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

208
Mtsuko Wochucha Ndalama

Kalekalelo kunali munthu wina wochakachika, yemwe

anapeza mtsuko waukulu m’munda mwake. Kenako

anayamba kuukumba ndipo atatero anautenga

n’kupita nawo kunyumba kwake. Atafika anauza

mkazi wake kuti autsuke. Koma mkazi wakeyo

atangotsiramo sopo, mtsukowo unayamba kuchucha

sopo wambirimbiri. Amati akakhuthula sopoyo, sopo

winanso amatuluka n’kudzaza mtsukowo. Bamboyo

anayamba kugulitsa sopoyo ndipo mtsukowo

unapitirizabe kutuluka sopo wambiri moti bamboyo

ankapeza ndalama zosaneneka. Koma tsiku lina,

mwangozi, ndalama inagwera mumtsuko uja ndipo

mtsukowo unasiya kuchucha sopo n’kuyamba

kutuluka ndalama. Amati akazichotsamo, zina

zimatulukanso, moti banjali linakhala ndi ndalama

zankhaninkhani, n’kulemera. Ndiye munthuyo anali

ndi bambo ake okalamba kwambiri, womwe ankakhala

kumudzi wina. Bambo akewo analibiretu mphamvu

zoti angadzisamalire, moti mwana wawoyo anawatenga

n’kumakhala nawo. Koma atakhala kwa kanthawi,

munthuyu anayamba kuona kuti bambo akewo ndi

aulesi moti anawauza kuti azigwira ntchito yochotsa

Mpandamachokero Anthology

209
ndalama mumtsuko uja. Koma chifukwa cha

ukalamba, bambowo zinkawavuta kuchita zimenezi

ndipo mwana wawoyo anapsa mtima n’kuyamba

kuwalalatira amvekere, “Ndinu munthu wamanja

lende. N’chifukwa chiyani mukulephera kugwira

ntchito yophwekayi? Pakhomo panotu timayendera

mawu akuti wosagwira ntchito asadye. Ndiye ngati

simukufuna kugwira ntchito, mudziwa chochita.”

Zitatere gogoyo anakhumudwa kwambiri poona kuti

mwana wake weniweni wayamba kumunyoza chifukwa

choti ndi wopeza bwino. Kenako anangotembenuka ali

pintchapintcha kuti atuluke panja. Koma atangotero,

anapunthwa n’kugwera mumtsuko muja ndipo

anafera momwemo. Nthawi yomweyo mtsuko uja

unayamba kutulutsa mitembo yambirimbiri. Amati

akachotsa ina, inkatulukanso ina. Ndalama zonse

zomwe zinatuluka mumtsuko uja zinathera kuika

maliro a bambo ake ndipo ankati akaika lero maliro,

mawanso amakaika ena. Kenako munthuyo anafika

potopa ndi kuika maliro a bambo akewo, moti anaswa

mphikawo ndipo pamene ankauswa n’kuti ali

kwakwatuke wotheratu, wosowa ndi ya mchere

yomwe.

Mpandamachokero Anthology

210
Phunziro: Ukakhala pabwino, usamanyoze ena.

Mafunso

1. N’chiyani chinathandiza munthu wotchulidwa

m’nkhaniyi kutuluka mu umphawi?

2. Kodi anatani atazindikira kuti bambo ake

sangakwanitse kudzisamalira okha?

3. N’chifukwa chiyani anakwiya ataona kuti

bambo akewo amalephera kuchotsa ndalama

mumtsuko uja?

4. Kodi mapeto ake anali otani?

Mpandamachokero Anthology

211
Mphamvu Zobwereka

Nthawi inayake, Nkhandwe inakumana ndi Kambuku.

Kambukuyo atangomuona anatulutsa dzimano zake,

n’kutulutsa zala zake n’kuyamba kuthamangira kunali

Nkhandwe kuja kuti aidye. Koma Nkhandweyo inati,

“Pepani achimwene, taimani kaye! Osamafulumira

kuganiza kuti m’nkhalango muno amphamvu ndinu

nokha. Mphamvu zanutu zikulenga, tikaziyerekeza ndi

zanga. Tiyeni tiyendere limodzi, ndipo inuyo

muziyenda pambuyo panga. Anthu akandiona ineyo

koma osachita mantha, inuyo mundidye. Koma

akandiona n’kuchita mantha, basi mundileke.”

Kambukuyo anagwirizana ndi zimenezi ndipo

Nkhandweyo inayamba kuyenda kulowera

kwinakwake, Kambukuyo akutsatira pambuyo.

Kenako anakumana ndi gulu la anthu ndipo ataona

kuti kukubwera Nkhandwe, koma kumbuyo kwake

kuli Kambuku, nthawi yomweyo analiyatsa liwiro la

mtondo wadooka. Kenako Nkhandwe ija inati,

“Waonatu, ndinali patsogolo ndine, koma anthu

atandiona anachita mantha kwambiri moti

anangotsala pang’ono kudziipitsira!” Kambukuyo

ataona zimenezi anaona kuti mnzakeyodi ndi patali,

Mpandamachokero Anthology

212
moti ananyamuka n’kuyamba kuthawa. Ankaganiza

kuti anthu aja amathawadi Nkhandweyo, osadziwa

kuti mphamvu zake zinali zochita kubwereka.

Nkhandweyo inali itabwereka mphamvu za

Kambukuyo, yemwe anthu aja anamuona akubwera

pambuyo pake.

Phunziro: Osamaopa mphamvu zochita kubwereka.

Mafunso

1. Kodi Nkhandwe inachita chiyani pofuna

kudzipulumutsa?

2. Kodi anthu aja ankathawa chiyani

kwenikweni?

3. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

213
Anzeru Omwe Anali ndi Vuto Losaona

Kalelo kunali anthu ena asanu ndi awiri omwe anali

ndi vuto losaona. Anthuwa anali anzeru kwambiri moti

anthu ankawatayira katsatsa akamva zimene

zinkatuluka pakamwa pawo. Ndiye tsiku lina anthuwa

anaganiza zopita kumalo ena kuti akaone zinyama.

Atafika kumeneko, anapita pamene panali njovu.

Anthu anayi anagwira miyendo ya njovuyo, m’modzi

anagwira chimulomo cha njovuyo, wina anagwira

pamimba ndipo wina anagwira mchira. Ndiye yemwe

anagwira chimulomo uja anayamba kuuza anzakewo

kuti, “Ine ndiganiza kuti njovu imaoneka ngati njoka.”

Koma mnzake amene anagwira kumchira uja

anamutsutsa n’kunena kuti, “Iyayi, imaoneka ngati

chingwe.” Ena amene anagwira miyendo aja

anagwirizana chifukwa anati, “Nonsenu mukunama,

njovu imaoneka ngati mtengo.” Koma amene anagwira

pamimba uja anayamba kunena anzakewo kuti ndi

wopanda nzeru ndipo anati, “Nonsenu ndi a ziwala

m’maso, njovutu imaoneka ngati phiri.” Kenako anthu

onsewo anayamba kukangana moti zinthu zinafika

poipa kwambiri. Munthu wina yemwe ankangoonerera

zimene zinkachitikazo anafika pamalowo ndipo

Mpandamachokero Anthology

214
anawauza kuti, “Aliyense wa inu wangogwira mbali

imodzi ya njovuyi, moti mukanaphatikiza zomwe

nonsenu mukudziwa, mukanatha kudziwa kuti njovu

yonse imaoneka bwanji.”

Phunziro: Palibe amadziwa zonse.

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani anthuwa ankatsutsana?

2. Kodi onsewo ankanama?

3. Kodi akanatani kuti adziwe mmene njovu

imaonekera?

4. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

215
Nkhuku ndi Nkhunda

Kunyumba kwina kunabwera alendo mwadzidzidzi.

Ndiyeno paja kulandira alendo kumaonekera m’mbale,

anthu a pakhomopo anaganiza zowaphikira nsima.

Ndiye popeza anali ndi Nkhunda komanso Nkhuku,

anayamba kukambirana kuti aphe chiyani. Ena ankati

aphe Nkhuku pomwe ena ankati aphe Nkhunda.

Nkhuku itamva zimenezi inayamba kukuwa kuti,

“Koma nkhundayooooo!” Ndipo Nkhunda inkati,

“Mulungu ngwamkulu, Mulungu ngwamkulu,

Mulungu ngwamkulu!” Nkhuku ija inkasokosa

kwambiri moti anthu aja anaiona. Ndiyeno wina anati,

“Bwanji tiphe Nkhuku, chifukwa tikapha Nkhunda,

tipha zambiri.” Nkhukuyo inapitirizabe kukuwa kuti,

“Koma nkhundayooooo!” Ndiye basitu, anthu aja

anayamba kuthamangitsa Nkhuku ija ndipo ataigwira

anaipha, moti maliro ake, alendo aja anadyera nsima.

Phunziro: Osamakankhira anzako mavuto, chifukwa

zimatha kutembenuka.

Mpandamachokero Anthology

216
Mafunso

1. Kodi zimene Nkhuku ndi zimene Nkhunda

imanena m’nkhaniyi kutabwera alendo zikufanana

ndi mmene zenizeni zimalirira?

2. N’chifukwa chiyani eni khomo anaganiza zopha

Nkhuku?

3. Kodi Nkhuku inakankhira bwanji makala

pamalaya a mnzake?

Mpandamachokero Anthology

217
Mankhwala a Banja

M’mudzi wina munali mayi wina, yemwe nthawi zonse

ankangokhalira kudandaula kuti banja lake

silikuyenda bwino. Ankasirira kwambiri akaona

anzake amene anakwatira ndi kumbuyo komwe,

akusangalala ndi mabanja awo. Banja lake linali ndi

vuto limodzi. Mwamuna wake ankangokhalira

kumukutumula ndipo iye ankaona kuti amayesetsa

kumusamalira komanso kuchita zonse zofunika.

Ankati akapita kwa alangizi, ankangomuuza kuti,

“Banjatu n’kupirira, ndiye kaya mwamuna wanu

akumakukunthani, muzingopirira basi. Banja ndiye

limenelo!” Ndiye atatopa ndi nkhanza zimene

mwamuna wake ankamuchitira, anaganiza zopita kwa

munthu wina wodziwa zitsamba kuti akamupatse

mankhwala achikondi. Atafika kwa munthuyo,

anamufotokezera zonse ndipo munthuyo

sanachedwechedwe koma kulowa m’tchire

n’kukathyola kamtengo kenakake. Anamupatsa

mayiyo n’kumuuza kuti, “Mukakakangofika

kunyumba kwanu, musakayankhule chilichonse.

Mukangoika kamtengo aka m’kamwa mwanu

n’kukhala chete. Musakayerekeze kutsegula

Mpandamachokero Anthology

218
pakamwa, chifukwa mukakatero, mankhwalawa

akasuluka.” Mayiyo anauyambadi wakwawo ndipo

atafika anatsatira malangizo anapatsidwa aja.

Mwamuna wake atabwera, anamuphikira nsima

n’kukamupatsa, ndipo mwamunayo anati,

“Ndinakuuza kuti ndili ndi njala?” Mkaziyo atamva

mawu osayamikawo anapsa mtima kwambiri, koma

chifukwa choti anauzidwa kuti asatsegule pakamwa,

sanayankhe chilichonse. Mwamuna uja anadabwa

kwambiri ndi zimenezi, moti anangotenga nsimayo

n’kuyamba kudya. Kungoyambira tsiku limenelo

mwamuna wakeyo sanamumenyenso ndipo patapita

masiku angapo, mayiyo anapitanso kwa munthu

wazitsamba uja kuti akamuthokoze, ndipo

anamufotokozera kuti mankhwala anamupatsa aja

akuthandizadi. Koma munthuyo anati, “Sikuti ndi

mankhwalawo amene akukuthandizani. Ndi mtengo

wachabechabe womwe ndinathyola m’thengomo. Vuto

lanu mayi ndi kulongolola! Mpofunika muphunzire

kuweta lilime lanulo.”

Phunziro: Mavuto ambiri amene timakumana nawo

amayamba chifukwa cha pakamwa.

Mpandamachokero Anthology

219
Mafunso

1. Mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani banja la

mayiyu silinkayenda bwino?

2. Kodi vuto la mayiyu linali chiyani?

3. Kodi mankhwala amene munthu wodziwa

zitsamba uja anamupatsa ndi amene anathandiza

kuti banja lake liziyenda bwino?

4. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala ndi

pakamwa pathu?

Mpandamachokero Anthology

220
“Ndifera Manyazi Mkazi Wanga”

Tsiku lina Aphiri anauza akazi awo kuti, “Mkazi

wanga, zinthu ndiye zativuta. Tipange bwanji kuti

tipeze ufa? Sindingalole kuti ana angawa afe ndi njala

ine ndikuona. Koma ndisanameyi, palibe chimene

ndikuona kuti ndingachite.” Kenako anapukusa mutu

wopanda nyanga. Mkazi wakeyo anavomerezadi

zimene mwamuna wake ananena ndipo

anawalimbikitsa kuti asadandaule. Kenako

mwamunayo anati, “Mkazi wanga, ndaganiza pulani.

Bwanji ineyo ndinyengezere kumwalira? Ndiye uike

mbale pamsewupo. Anthu akamaponya ndalama

zachipepeso, iweyo uzipita kukazichotsamo

n’kukazibisa.” Koma mkaziyo anafunsa mwamuna

wakeyo kuti, “Nanga bwanji anthu akayamba kubwera

pakhomo pano? Kodi ndiwauza chiyani akanena kuti

akupititseni kumotchale? Mukafa ndi kuziziratu inu?”

Bamboyo anati, “Usadandaule ndi zimenezo, ineyo

ndichita zinthu zoti asazindikire kuti ndili moyo. Koma

akanena kuti andipititse kumotchale, iweyo ukane.

Ungowonetsetsa kuti ndalama zomwe zikuponyedwa

m’mbale zikuyenda bwanji. Ineyo ndidzuka mawa

anthu asanaganize zotulutsa maliro panja.”

Mpandamachokero Anthology

221
Mkaziyo anagwirizana ndi maganizowo ndipo

mwamunayo ananamiziradi kumwalira ndipo mkazi

wakeyo anayamba kulira. Mbale inaikidwadi pamsewu

ndipo anthu anayamba kuponyamo. Posakhalitsa

anthu ena anayamba kuyenda m’midzi n’kumatolera

ufa, nkhuni komanso ndalama ndipo akabwera nazo

ankazipereka kwa mayi uja. Ndiyeno m’mawa kutacha,

anthu anayamba kubwera ndipo ena anakagula

bokosi n’kunyamula Aphiri n’kuwaikamo. Koma

atawaika m’bokosimo, Aphiri tulo tidawatenga.

Mkazi uja ankayembekezera kuti mwamuna wake

adzuka. Koma ataona kuti sakudzuka, anapita pafupi

ndi bokosilo n’kuyamba kulira amvekere, “Inu bambo

a Pofera tadzukani chondeeee! Tadzukani inuuu!

Ndimayesa munati mudzuka inu!” Azimayi anabwera

kudzatonthoza mnzawoyo poganiza kuti chisoni

chamugwira. Pamene bamboyo ankadzuka n’kuti

pakhomopo pali namtindi wa anthu ndipo Aphiri

atamva phokoso la anthuwo komanso nyimbo

zachisoni zikuimbidwa, anachita manyazi kuti adzuke.

Mkazi wawo uja anapitirizabe kulira mouza mwamuna

wakeyo kuti adzuke, koma Aphiri anangoti zii. Amati

akamva mkazi wawoyo akulira ankangonena

Mpandamachokero Anthology

222
chapansipansi kuti, “Ndifera manyazi mkazi wanga!”

Posakhalitsa kunabwera adzukulu kuchokera

kumanda ndipo anatenga misomali n’kuyamba

kukhoma bokosilo. Amati akati khoo! Mayi uja amalira

mosatonthozeka, “Amunanga inu dzukani, chonde

tadzukani. Nditani nawo ine anawa?” Kenako

anakhomanso wina kuti khoo mpaka anamaliza.

Anthu ankangoganiza kuti mayiyo akuyankhula

zimenezo chifukwa cha chisoni, osadziwa kuti

akunena nkhaninkhani. Pamapeto pake anthu

ananyamula bokosi lija ndipo Aphiri anakaikidwa

m’manda chifukwa cha manyazi.

Phunziro: Osalola kulowa m’mavuto chifukwa cha

manyazi.

Mpandamachokero Anthology

223
Mafunso

1. Kodi Aphiri ataona kuti zinthu zavuta

panyumba pawo anapanga pulani yotani?

2. Kodi mukuganiza kuti anawerengera mtengo

wake?

3. N’chifukwa chiyani Aphiri ankachita manyazi

kudzuka?

4. N’chifukwa chiyani anthu sanadabwe ndi

mawu amene akazi a Aphiri ankanena akamalira?

5. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

224
Atambwali Sametana

M’mudzi wina munali atsinzina n’tole awiri. Wina

dzina lake linali Paguza ndipo wina anali Saguza.

Tsiku lina Paguza anatenga thumba la mpunga

n’kuikamo mchenga ndipo pamwamba pa mchengawo

anaikapo mpunga n’cholinga choti thumbalo lizikhala

ngati lodzadza mpunga okhaokha. Nayenso Saguza

anatenga mtsuko n’kuthiramo madzi ndipo

pamwamba pamadziwo anathirapo mafuta. Madziwo

ankangoti ndengundengu ngati mafuta ndipo

anasenza mtsukowo n’kumapita nawo kumsika.

Atafika kumeneko, atambwaliwa anakumana ndipo

anagwirizana kuti angosinthana zinthuzo. Paguza

anauza mnzakeyo kuti, “Uwu ndi mpunga

wopunthapuntha, wabwino kwambiri moti

simungapezenso wina yemwe angakugulitseni mpunga

ngati umenewu. Mukakauphika uzikangotuluka

umodziumodzi.” Saguza atamva zimenezo anaona kuti

wapeza munthu watulo, moti sanachedwe koma

kuvomera zoti asinthane ndi mnzakeyo mtsuko

wamafuta. Aliyense anangosenza katundu anapatayo

n’kuuyamba wakwawo. Koma atafika kunyumba

anazindikira kuti apusitsana. Paguza ataona kuti

Mpandamachokero Anthology

225
mnzakeyo wamugulitsa madzi anayamba

kumusakasaka ndipo atamupeza anamufunsa kuti,

“N’chifukwa chiyani wandipusitsa?” Mnzakeyonso

anamufunsa kuti, “Nanga n’chifukwa chiyani iwe

wandigulitsa mchenga?” Atazindikira kuti zawo

n’zimodzi, anayamba kugwirizana kwambiri. Tsiku lina

anapangana kuti apite kukaba kwa mfumu

yam’mudzimo. Atambwaliwa anamva zoti mwana wa

mfumuyo, yemwe anali kutheba, wabwera ndi

chikwama chodzadza ndalama ndipo wapatsa bambo

ake. Atamva zimenezi mitima yawo inkangoti

dyokodyoko, ndipo anagwirizana kuti akumane pakati

pa usiku n’cholinga choti akasowetse chikwamacho.

Kenako anauyamba wa kunyumba kwa mfumuyo.

Mwamwayi pakhomo la mfumuyi panalibe zifuyo

zaukali, moti Paguza anakwanitsa kulowa m’nyumba

ya mfumuyo aliyense osadziwa. Kenako anayenda

monyang’ama n’kukanyamula chikwama chachikulu

chomwe chinali kumutu kwa mfumu yomwe inali

tapatapa ndi tulo. Ndiyeno anafika nacho pazenera la

nyumbayo n’kupatsira Saguza, yemwe anaima panja

pa nyumbayo. Saguza atangolandira chikwamacho

anayamba kuthawa nacho. Atafika kunyumba kwawo,

anasonkhanitsa mudzi wonse ndipo anauza anthu a

Mpandamachokero Anthology

226
pakwawopo kuti ali ndi chikwama chodzadza

ndalama. Koma anawauzanso kuti, “Pali vuto limodzi.

Munthu winawake akundilondalonda. Akufuna

atatenga chikwamachi.” Anapitiriza kunena kuti,

“Ndalamazi zikhoza kupangitsa kuti aliyense pamudzi

pano akhale mponda makwacha. Ndiye mulola kuti

munthu ameneyu atenge ndalamazi?” Anthuwo

atamva zimenezi anapukusa mitu yawo n’kunena kuti,

“Ayi.” Ndiyeno Saguza anati, “Ndikufuna kuti tibise

chikwamachi, Paguza akabwera, mudzamuuze kuti

ndamwalira.” Anthuwo anagwirizana nazo zimenezo

ndipo posakhalitsa anthu anayamba kubuma

amvekere, “Mayi wawaye, tilowera kuti ife, achimwene

athu atsogolaa.” Pakhomopo panayamba kumveka

chiphokoso chachikulu ndipo posapita nthawi

panyumbapo panadzaza anthu. Ndiyeno m’mawa

kutacha, Paguza anatulukira ndipo anafunsa anthu a

pakhomopo kuti, “Wamwalira ndi ndani?” Anthuwo

anamuyankha kuti, “Mnzanu ujatu anatipeza

m’bandakucha ndipo amanena kuti sakumva bwino

moti anatikomokera m’manja, basitu ulendo unali

womwewo.” Koma Paguza atamva zimenezi anayamba

kukayikira ndipo anati, “Anthuwa akundiuza kuti

Saguza wamwalira. Amwalira bwanji atathawa ndi

Mpandamachokero Anthology

227
chikwama chandalama. Akufuna kundiyenda pansi

ameneyu!” Kenako anauza anthu a pakhomopo kuti,

“Ndingakaone mtembo wake?” Anthuwo anamutengadi

n’kumulowetsa m’chipinda chimene munali

mtembowo. Kenako anayamba kuyankhula ndi

mnzakeyo kuti, “Bwanawe, dzuka kuti tingokambirana

bwinobwino?” Koma mnzakeyo anangoti zii. Kenako

Paguza anauza azimayi ena kuti, “Nditerekereni madzi,

awire ngati ososolera nkhuku.” Azimayiwo anachitadi

zimenezo, mosadziwa kuti akufuna achite nawo

chiyani. Madziwo atabwadamuka, azimayiwo

anawatenga n’kupita nawo kwa Paguza. Paguza

analandira madziwo n’kupempha kapu yake

yotungira. Ndiyeno anayamba kuuza mtembowo kuti,

“Ambwana, dzuka zinthu zisanafike poipa! Koma

mnzakeyo sanayankhe. Kenako anatunga madzi

otentha aja pang’ono, n’kumutsira pamwendo kuti

chwaa! Koma mnzakeyo anapirira ndipo sanatekeseke.

Kenako anatunganso ena n’kumuthiranso kuti chwaa!

koma ayi ndithu Saguza sanasunthe. Ndiyeno Paguza

anati, “Bwanawe, dzuka. Uvulalatu!” Koma Saguza

sanayankhe. Kenako Paguza anati, “Nanga mtembo

umamva kuotcha ngati? Kuti nditsimikizire kuti

mnzangayu wapitadi, ndingomukhuthulira madzi

Mpandamachokero Anthology

228
onsewa.” Ndiyeno anangotenga mtsuko uja

n’kukhuthulira mnzakeyo ndipo Saguza analephera

kupirira. Anadzambatuka kwinaku akulira ndipo

mnzakeyo anati, “Ndinakuuzatu ine, ukanangodzuka

nthawi yomwe ija sukanavutika chonchi.” Pa nthawiyi

n’kuti Saguza atayamba kukupuka m’miyendo ndi

m’mikonomu. Zitatero Paguza ndi Saguza

anagwirizana kuti agawane ndalamazo mofanana,

ndipo anakatenga chikwama chija kuti ayambe

kugawana. Koma atangochitsegula, anapeza kuti

munali mapepala okhaokha.

Phunziro: Utambwali umabweretsa mavuto.

Mafunso

1. Kodi Paguza ndi Saguza anali anthu otani?

2. N’chifukwa chiyani anayamba kugwirizana?

3. N’chiyani chikusonyeza kuti onsewa anali

adyera?

4. Kodi pali chilichonse chimene anapindula?

5. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

229
Mutu Wodwala Kansire Adatema Kadzidzi

Kalekale pakati pa mbalame zonse, panali kambalame

kena kakang’ono kotchedwa Kansire, enanso amati

Tchala. Kambalameka kankalemekezedwa ndi

mbalame zonse chifukwa mbalamezo zinkati Kansire

ndi mbalame ya ku mizimu, kapena kuti mbalame

yomvana ndi mizimu.

Kansire amati zipatso ndi zakudya zina zikasowa, iye

amaulukira kumanda kotchedwa Makololo n’kuyamba

kulira. Posapita nthawi m’mitengo yonse kumandako

zipatso zimvekere kuti mbwee! kholophethee! Nthambi

za mitengoyo kuti petaa! kulemedwa ndi zipatso

zikuluzikulu.

Tsopano zimati zikatero, phokoso la mbalame

limachita kuti, buu! Panali mbalame ina imene

inkamveka kwambiri ndi phokoso. Mbalameyi inali

yotchedwa Pumbwa. Pokondwerera zipatso zija

mumtengo wa Kachere inkati, “Mbwe, mbwe, bzolo,

bzolo, zanchulukira! zanchulukira!” Tsopano

mbalamezo zikakhuta, zimatera pansi n’kuyamba

kuyamika mbalame ija yotchedwa Kansire.

Kuyamikako inkatsogolera ndi mbalame ija yomveka

Mpandamachokero Anthology

230
kwambiriyi, Pumbwa. Mbalameyo imati “bzoli! bzoli!

zanchulukira! Ife tiyamika inu Kansire. Lero ife

laponda lamphawi diwa. Tinali padzuwa koma inu

Kansire mwatitoletsa nkhwangwa ndi mpini womwe.

Popanda inu Mfumu Kansire, ife sitikanasambira

m’nkhali monga tachitiramu. Mwa ichi tiyamika,

taphuka chifukwa cha inu mfumu yathu Kansire,”

Anatero Pumbwa poyamika Kansire. “Mawa tibwera

ndi mitolo ya nsembe kuti mupereke kwa mizimu ya

makolo athu,” anatero poyamikira Kansire.

Pumbwa anapitiriza motere, “Pano tikufuna

kukutsimikizirani kuti ndinu mfumu yathu. Enawa

timangowaona chimwendo kong’akong’a, kutalika

chikhosi apoo, kusololokera m’mwamba, koma palibe

chimene adatichitirapo, koma kumangotigogomola ndi

kutinzonzomola pamitu!”

Nthawi yomweyo panamveka mawu ozaza, “Iwe

Pumbwa! thula! Bwanji ukuchitira chipongwe ine?

Kodi kutalika mwendoko ndidakumanani ndine?”

Anatero Nthiwatiwa ali kupalasika ndi ukali, masaya

atatupikana ndi mkwiyo. Mbalame zonse zinangoti

maso pa Nthiwatiwa, yuuu! n’kumangoinyodogola cha

mumtima zili “Ho! Tamuonani gudu wogudukira

Mpandamachokero Anthology

231
zinthu za eni ake. Tachionani chimwendo kutalika

ngati mitengo ya m’masano.” Mmene zimateromo

zimatunguluza maso, lilime lili pamtunda, milomo

zitapambanitsa kupitiriza kunyodola a Nthiwatiwa aja.

“Ine ndikunenetsa pano!” a Nthiwatiwa anatero,

“Mbalame zonse ndinu opusa kwambiri. Mudzaleka liti

kugodomala kotere? Simungatchule kamwana aka ka

Kansire kuti ndi mfumu. Kodi simukudziwa kuti

mfumu ndine Nthiwatiwa? Kodi n’chilungamo

kumalemekeza Kansire, muleka ife amuna ogona

kukhomo kosatseka? Kodi simudziwa kuti Kansire ndi

nthumbidwa? Kodi Kansire ndi ine titati tipandane

angafe ndani?” Anatero Nthiwatiwa poonetsa kunyada.

“Ndiponi mutalemekezako a Mphungu awo, kaya a

Ng’ongwe awo, a Namng’omba kaya a Namntchichi

awo, kapenanso a Kadzidzi awo chifukwa chokula

mutuwo . . . ”

“Ine ndikuthilira ndemanga mawu amenewo!” anatero

a Namn’gomba, “Mbalame nonsenu muli ndi kaduka

kachinangwa! Si zaulemu kumalemekeza kafinye aka

ka Kansire kamene ife timakatchula kuti kandakhuta

kale ayi!” a Namng’omba anatero powonjezera

ndemanga.

Mpandamachokero Anthology

232
“Zoonadi,” anatero Ng’ongwe ali kutsokomola,

chithokomiro cha pakhosi chili tugwaa! kutupikana

ndi ukali. “Ine ndili kuvomereza Namng’omba.

Kamwana aka ka Kansire sikangakhale mfumu a

Nthiwatiwa ali pompano ayi. Kodi ufumuwo alandirira

chifukwa cha ulosi wokhawokhawo? Kodi chidadza ndi

yani choti munthu akakhala wa kumizimu, wotiitanira

mvula tsono, n’kumatinso yemweyo akhale mfumu?”

anatero Ng’ongwe pofunsa mbalame zonse zija.

Mmenemo n’kuti atawatunguluzira maso ali pamtunda

ngati maso a njoka ija yotchedwa mamba, pam’mero

pali dyokhodyokho chifukwa cha ukali. Mbalame

zonse zija zinangotinso maso pa Ng’ongwe kuti yuu!

“Mwaona nokha palibe woyankha, kutsimikiza kuti

sindikunena zambwerera ayi!” anatero Ng’ongwe.

Nthawi yomweyo Ng’ongwe anapisa mutu wake

mphiko lakumanzere. Potulutsa mutu wake, mbalame

zonse zija zinadodoma poona kuti kukamwa kwake

kunali ndudu ya fodya ili fuubaa! utsi umenewo. Utsi

wina unali kutulukira mphuno.

“Kansire ntchito yake ndi ulosi basi osatinso za ufumu

zizimvekera pa dzina lakenso, izo takana

kwamtuwagalu.” Anatero Ng’ongwe ndudu ija

Mpandamachokero Anthology

233
atayamba waitula pansi, koma utsi wina ukutulukabe

m’mphuno pamene anali kuyankhula.

“Kambalame kena ngati Pumbwa, kasasokoneze

Kansire ayi. Mulekeni iye azingolingalira njira zabwino

zomvanirana nazo ndi mizimu ya makolo athu amene

adafa kale basi. Amfumu anthu a Nthiwatiwa ndiwo

amene azilinganiza za ufumu wawo monga

zokonzekera za kumeta unamwali pa nthawi

ikubwerayi ya zinamwali za anyamata ndi

asungwana,” anatero Ng’ongwe popumulira

kuyankhula kuja. Ng’ongwe anatolanso ndudu ija ya

fodya, ndiye tsopano kudangooneka kuti, toloooo! Utsi

umenewo mapiko ake ali kuwombetsa m’mimba

kuonetsa ukali, m’menemo n’kuti maso ali psuu! ngati

wopemereredwa ndi utsi kudzenje.

“Chimene tiyenera kumakumbukira n’choti

tisamaiwale sing’anga wathu Mleme kumuitana kuti

nayenso adzadye nawo phwandoli. Taonani ife

zithokomiro zili tugwaa! chimkhuto chimenecho.

Nanga bwanji taiwala ng’anga yathu? Amfumu

Nthiwatiwa akankhe mthenga kwa Mleme kuti abwere

adzadye nawo ufulu talandirawu . . . azimu atigwera

m’mbale . . . atigwera m’mitengo yathuyi kumasano

Mpandamachokero Anthology

234
kuno,” anateronso Ng’ongwe fodya ali fubafuba utsi uli

kutulukira m’mphuno.

“Wayankhula bwino iwe Ng’ongwe!” anatero

Nthiwatiwa. “Nonsenu musamvere zija amanena

Pumbwa zija ayi. Zija ndi zoyankhula akapasule

okhaokha. Pumbwa sadziwa kuti dziko ndi mafuwa

achita kuchilikiza. Zoyankhula za Pumbwa ndi

zochotsa mafuwa kuti dziko ligwe. Motero, zimene

wayankhula Pumbwa zija aliyense angozithira

kunkhongo. Woyamwa yekhayekha ndi amene

amayankhula zokhuta ngati zimene zija,” Nthiwatiwa

anateronso ali kupenyetsa Pumbwa uja. “Motero tonse

tiyenera kumwazikana koma tonse tidzakumanenso

pano m’mawa dzuwa likutuluka kuti tidzapitirize

kudya madyelerowa.”

M’mawa kutacha dzuwa likutuluka, mbalame zonse

zinali zitasonkhana kale kumasano kuja koma zonse

zinali zitatera pansi zili kwangopenyetsetsa zipatso

m’mitengo muja. Zinali kudikira ulamuliro wa

mbalame ija ya kumizimu yotchedwa Kansire. “Nanga

Kansire ndi Chiuzimbi ali kuti?” Anafunsa motero a

Nthiwatiwa.

Mpandamachokero Anthology

235
“Ife sitikudziwa mfumu,” anatero Kadzidzi chimutu

chake chachikulu chija chili nguninguni kugwedezeka,

masaya ali kweevee! ngati wodwala matenda a

kadukutu. “Tonse tabwera, mphachi (kupatula) awiri

mwatamulawo,” anawonjezera motero Kadzidzi.

Dzidzidzi, mbalame zonse zinamva kukwapulitsa kwa

mapiko a mbalame kuti phururu! phururu!

Posakhalitsa zinaona Chiuzimbi akutulukira ali kutera

pansi, Chiuzimbi chachitali ngati chimchira cha

Nkhwere chili vwandaa! Chilinunda ngati cha kunzi ya

ng’ombe chili pholi! pamsana. “Suyo Chiuzimbi uja

mfumu!” anatero Kadzidzi.

“Eya, ndamuona,” Nthiwatiwa anatero.

“Pepani mfumu ndachedwa kufika!” Anatero

Chiuzimbi.”

“Chifukwa?” Nthiwatiwa anafunsa, maso ali psuu!

mutu uli njenjenje ndi ukali.

“Pepani mfumu ndiye kuti . . . ” anangoyamba motero

Chiuzimbi. “Ndiye kuti chiyani? Kodi iwe Chiuzimbi

umanyadira chimthenga chako chachitalichi? Kapena

umanyadira linundali basi n’kumadziyeseza kuti

ndiwe ng’ombe eti? Ife sitingadikire iwe pano

Mpandamachokero Anthology

236
kutichedwetsa phwando lathuli limene adatipatsa

mlosi wathu Kansire. Kansire pomvana ndi mizimu ya

makolo athu taona m’mitengomu zimene Chisumphi,

kaya Chauta, kaya Mphambe anatipatsa. Kodi

umadziyesa ng’ombe iwe eti?” Anatero Nthiwatiwa

podula pakamwa Chiuzimbi.

“Zachisoni mfumu Kansire wafa?” anatero Chiuzimbi

kuti zonena zake zimveke msanga.

“Ukuti chiyani? Kansire wafa?” Nthiwatiwa anafunsa.

Nthawi yomweyonso panamveka kubuma maliro a

Kansire. Dothi lonse pamalo onsewo linali madzi

khathikhathi ndi misozi yochokera m’maso a mbalame

zija. Nthiwatiwa sanathenso kuyankhula chifukwa cha

phokoso lachisokonezo motere: “Bzolobzolo, bzoii,

mbwembweembwe, gulululu, khurururu, fwakafwaka,

kweeefu, mbirombiro!”

“Nena bwino, ukuti chiyani za Kansire?” Nthiwatiwa

anafunsanso.

“Kansire zoonadi,” anatero Chiuzimbi, “wadwala

pafupi imfa.”

“Khalani chete,” Nthiwatiwa anatero. Chifukwa cha

mawu wotsirizira aja a Chiuzimbi, panali bata kungoti

Mpandamachokero Anthology

237
ziii. “Ndikuti Kansire wadwala pafupi imfa. Usiku

anakomoka katatu.”

“Chabwino, iwe wemwe Chiuzimbi pita kwa sing’anga

wathu Mleme ku Chinsiro ukamuuze za matendawo.

Nonse mubwere pamodzi kuti tonsefe tipitire limodzi

kwa Kansire. Wamva bwino?” anatero Nthiwatiwa.

“Zikomo mfumu,” anatero Chiuzimbi akuuluka kupita

kwa ng’anga ija.

“Zikomooo,” anatero Chiuzimbi.

“Eyaa,” anatero Mleme.

“Koma musavutike n’kundikonzera pokhala ayi.

Ndikhala pachikuni ndatera pano,” Chiuzimbi anatero.

“Kodi n’kwabwino?” Mleme anafunsa.

“Ayi si kwabwino.”

“Chavuta n’chiyani?”

“Matenda kwathuku.”

“Wadwala ndani?”

“A Kumizimu a Kansire.”

Mpandamachokero Anthology

238
“Tsono zikatero n’cho chiyani, atilosere zinthu ndani?”

“Ndimo taonera. Mutu ndithu udawayamba dzana.

Ngakhale amayenda kungoti munthu uja ngolimba.

Mwinanso kuchepa thupi kuwombola. Usiku

anakomoka katatu. Amfumu a Nthiwatiwa atamva ndi

amene anandikankhira nkhongo kunowa, ali basi

muzikabwerera limodzi.”

“Zikomo ndamva. Ine bwenzi n’tabwera ndithu popeza

madzulo ndinalandira mthenga woti kuli phwando,

wosadziwanso kuti n’kumamva zoteronso. Chabwino

dikira pomwepo nditenge lumo lakuthwa loti

tikatemere mankhwala kuti mnzathuyo achire

msanga. Komatu zina leku zina kambu, ine dzinali

ndimangolimva koma titakumana m’malunje, ayi

ndithu sindingawadziwe, mpang’ono pomwe.”

“Aaa! zoonadi?”

“Zoonadi pali agogo kumanda.”

“Tiyeni mukawadziwa lero.”

“Ndakondwanso podzandiitana ine. Koma dzuwa

lisanalowe, Kansireyo akhala atachira.”

“Zoonadi zimenezi?”

Mpandamachokero Anthology

239
“Eee, ine ndimanena zoona zokhazokha. Palibe

ng’anga yoopsa ngati ine m’dziko lonse lino. Ndili ndi

mankhwala anga owopsa kwambiri.”

“Mudakatenga kuti mankhwalawo?”

“Kwathu kudziko la mbewa.”

“Kodi inu ndimayesa kuti kwanu ndi kwathu kudziko

la mbalame. Kodi inu sindinu m’bale wathu?”

“Ndine m’bale wanu.”

“Nanga bwanji mukuti kwanu ndi kwa mbewa?”

“Inenso ndikufunseni. Kodi inu kwanu n’kuti?”

“Ndakuuzani kale kuti kwathu ndi kwa mbalame.”

“Osati kwa ng’ombe?”

“Chifukwa?”

“Nanga inu mwadabwa ndi chiyani poti muziti ndikati

kwathu ndi kwa mbewa mudodoma. Inenso ndili

kudodoma poti mukuti kwanu n’kwa mbalame pomwe

ine ndikuona kuti kwanu n’kwa ng’ombe.”

“Chifukwa chiyani?”

“Achimwene ndikuuzeni. Inu kwanu n’kuwiri: kwa

Mpandamachokero Anthology

240
ng’ombe ndiponso kwa mbalame.”

“Mwaneneranji zimenezi?”

“Taonani chilinundacho! Ine kwathu n’kwa mbewa ndi

mbalame. Tonsefe ndife ofanana tilibe kwathu

kwenikweni ayi. Izi tinazivala mosasankha ayi,

tinangopezeka monga tililimu ndiponso . . . ”

“Pepani sing’anga tiyeni tingakapeze maliro.”

Dzidzidzi, mbaleme zonse ku makololo kuja

zidangoona a Chiuzimbi ndi a Mleme ali kutera pansi

koma maso a Mleme anali pa Kadzidzi gaa, chifukwa

adaona kuti mutu wake unali wotupa. Mleme

mumtima mwake anaganiza kuti mbalame ija

yotchedwa Kansire ndi Kadzidzi uja, poona

kutupikana kwa mutu.

Nthawi yomweyo anatulutsa lumo lakuthwa kwambiri

pamodzi ndi mankhwala ake. Posakhalitsa mbalame

zonse zinaona kuti mutu wa Kadzidzi watemedwa kale

magazi ali psuu, mankhwala ali kupakidwa.

“Pepani sing’anga, ine sindikudwala ayi,” anatero

Kadzidzi.

“Kodi wodwala mutuyo sindiwe?” anafunsa Mleme.

Mpandamachokero Anthology

241
“Ayi sindine.”

“Nanga ndi ndani?”

“Kansire.”

“Ali kuti?”

“Kuchisa chake.”

“Nanga iwe sukudwala?”

“Ayi.”

“Nanga mutuwu unatupa n’chiyani?”

“Siwotupa, ndi mmene ndinabadwira basi, monga

momwe mulili inumu. Mumaoneka ngati mnzathu

mbalame, komanso ena amati ndinu mbewa. Kodi

zikatero chikhale chifukwa choti ife tikutemereni

mankhwala kuti umbewa muli nawowu ukuchokeni?”

“Aaaa, . . . chipongwe choopsa, ndizo

m’mandiyitanira?” anatero Mleme ali kuuluka

kuthawira m’malunje, mbalame zonse zili maso yuu,

kumupenya koma chimutu cha a Kadzidzi chili magazi

psuu.

Phunziro: Si bwino kumaweruza anthu pongotengera

maonekedwe chifukwa maonekedwe amapusitsa.

Mpandamachokero Anthology

242
Mafunso

1. Kodi ndi mbalame iti imene inali yotchuka ndi

phokoso?

2. N’chifukwa chiyani mbalameyi inkaona kuti

ndi bwino kuti Kansire akhale mfumu?

3. Mukuganiza kuti n’chiyani chinachititsa kuti

Chiuzimbi abwere mochedwa?

4. Kodi Kansire sanapite kuphwando lija

chifukwa chiyani?

5. N’chiyani chinachititsa Mleme kuganiza kuti

amadwala mutu ndi Kadzidzi?

6. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

243
Chikumbumtima Chidapha Njovu

Kalekalelo, Njovu inkacheza kwambiri ndi Kalulu.

Tsiku lina inapita kwa Kalulu, n’kumupeza kulibe,

koma inapeza panja patayanikidwa ndiwo. Itaona kuti

palibe aliyense akuona, inaganiza zongoziba. Kenako

Njovu inatenga ndiwozo n’kumapita nazo kwawo.

Kalulu atafika n’kupeza ndiwo zake zitabedwa,

anaganiza zokafunsa bwenzi lake la pamtima Njovu.

Kalulu anafunsa a Njovu kuti, “A Njovu, kodi

mwatenga ndiwo zanga ndinu?” A Njovu anakana kwa

m’tu wagalu, amvekere, “Ndatenga si ine!” Kenako

Kalulu anati, “Koma ngati mwatenga ndinuyo

n’kumakana, chikumbumtima chikuphani!” Kenako

Kalulu anaona msana wa njira. Njovu m’mbuyo muno

inayamba kuda nkhawa kwambiri. Inkaganiza kuti

chikumbumtima ndi nyama yaikulu komanso

yamphamvu kwambiri kuposa iyoyo, choncho

inayamba kukhala mwamantha. Inasiya kutuluka

panja kukafuna chakudya poopa kukumana ndi

chikumbumtima. Masiku anadutsa Njovu ikungogona

nayo njala moti inaonda kwambiri. M’kupita kwa

nthawi Njovu inafa. Apa mawu a Kalulu aja anathera

mu siizi, Njovu inaphedwa ndi chikumbumtima.

Mpandamachokero Anthology

244
Phunziro: Ukachita chinthu choipa chikumbumtima,

chomwe ndi munthu wamkati, chimakuimba mlandu

moti utapanda kuvomereza kulakwa kwako ukhoza

kufa ndi nkhawa.

Mafunso:

1. Kodi chikumbumtima ndi chiyani?

2. Kodi Njovu inkachidziwa chikumbumtima?

3. Kodi n’chiyani chinapha Njovu?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

245
Chifukwa Chake Chule Amakhala M’madzi

Pamudzi wina panali mayi ena odziwa kulikazinga

thobwa. Dzina la mayiwa linali Zenje. Anzawo ena

achilomwe ankangowatchula kuti mayi Nalimata.

Anthu ambiri ankabwekera thobwa la mayiwa moti

anthu sankatha phazi pakhomo pawo. Mwamwayi,

mayi Zenje anali munthu wochereza alendo.

Ankalandira aliyense amene wabwera kudzacheza

ndipo ankamupatsa chipanda cha thobwa kuti

azizilitse kukhosi. Sankasamala ngakhale zitakhala

kuti munthuyo ndi kabwerebwere. Koma panali

munthu wina wopanda pabwino, yemwe ngakhale

mayiwa ankamuchitira zabwino zonsezi,

ankawaberanso thobwa lawo. Munthu ameneyu dzina

lake linali Chule. Ankati mayi Zenje akangochoka

kupita kuchitsime kapena kumsika, iyeyo

ankawalowela m’nyumba n’kuwabera thobwa. Mayi

Zenje akabwera ankadabwa kuti thobwa lawo latsika.

Kenako anazindikira kuti pali tambwali wina yemwe

akumapungula thobwalo ndipo anatsimikiza mtima

zomukhaulitsa. Kuyambira tsiku limenelo

anachenjera, moti anayamba kukhoma chitseko

chawo. Chulenso naye anazindikira kuti amutulukira

Mpandamachokero Anthology

246
ndipo anapeza njira ina yobera thobwalo ngakhale

zitakhala kuti pakhomo ndi pokhoma. Mayi Zenje

ataona kuti kukhoma chitseko sikukuthandiza,

anaganiza zowiritsa kwambiri thobwalo kuti wakubayo

akabwera limuwaule. Ndiyeno anawiritsa thobwa

lomwe anaphika tsikulo n’kuliika pakona la nyumba

yawo. Kenako anadendekera mtsuko wawo n’kumapita

kumadzi. Chule ataona kuti mphaka wachoka, anaona

kuti yakwana nthawi yoti khoswe asangalale. Popeza

pakhomo la nyumba ya mayi Zenje panali potseka,

anapita kuseri kwa nyumbayo n’kukwera pamtondo.

Kenako anasolola bango lake n’kulilowetsa mumtsuko

unali pakona uja kudzera pazenera. Kenako

anayamba kupopa thobwalo ndi mlomo wake. Monga

mwa masiku onse, iye ankayembekezera kumva

kuzuna kwa thobwalo. Koma patsikuli anakumana

nazo. Thobwa lothenthalo linamulowa kukhosi moti

anabuula koopsa. Thobwalo linawauliratu kukhosi

kwake ndipo mawu ake anasinthiratu. Kenako

analumphira pansi ndipo thobwa lija linapitirizabe

kutuluka m’bango lija moti linayamba

kumupungukira pamsana. Msana wonse unatuluka

matuza ndipo nthawi yomweyo anathamangira

kumadzi kuti akadziziziritse. Kungoyambira nthawi

Mpandamachokero Anthology

247
imeneyo, Chule anayamba kukhala m’madzi kuti

asamamve kupweteka kwambiri chifukwa cha matuza

anali pansana pake aja.

Phunziro: Kuba ndi koipa. Kuba ndi kutenga chinthu

cha mwiniwake popanda chilolezo.

Mafunso:

1. Kodi mayi Zenje anali munthu wotani?

2. Kodi anatani atazindikira kuti thobwa lawo

likubedwa?

3. Kodi Chule anasiya kuba thobwa ataona kuti

mayi Zenje akumatseka chitseko chawo?

4. Kodi mayi Zenje anatani pofuna kukhaulitsa

amene ankawabera thobwa lawo?

5. N’chifukwa chiyani mawu a chule anasiya

kumveka bwino?

6. N’chifukwa chiyani Chule amakhala ndi zilonda

pamsana?

7. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

248
Kufulumira Kunena Anathawitsa Likongwe

wa Apongozi

Panali anyamata awiri amene anakwatira banja

limodzi. Wina anakwatira wamkulu wina anakwatira

wamng’ono. Tsiku lina apongozi awo anadwa la

matenda odetsa nkhawa. Atapita kwa sing’anga

anawauza kuti mankhawala amene angathandize kuti

apongoziwo achile ndi mbewa ya Likongwe. Akamwini

awiri aja atamva zimenezi ndiponso pokhala odziwa

kusaka ndi kukumba mbewa, analonjeza kuti apeza

Likongwe amene anali kufunikayo. Tsiku lotsatira

mkamwini wamkulu uja anauza mkamwini

wamng’ono pamodzi ndi anzawo amene amachita

nawo chidyerano kuti apite kokapha Likongwe

chifukwa anali ataona pamene pamalowa Likongwe.

Asanayambe kukumba, mkamwini wamkulu uja anati,

“Amene athawitse Likongwe wa apongoziyu akachoka

pamudzi paja.” Mkamwini wamng’ono pofuna

kusonyeza ulemu kwa mkamwini wamkulu anayamba

kukumba. Pasanapite nthawi, Likongwe anadziwa kuti

zinthu zavuta, kenako anabulika kudzenje lija

n’kulinjika mbali imene kunakhala mkamwini

wamkulu uja. Mkamwini uja chifukwa chamantha

Mpandamachokero Anthology

249
anajowa, osadziwa kuti akupereka mpata woti

Likongwe athawe. Likongwe analowa patchire

osaonekanso. Mankhwala othandizira apongozi

sanapezeke. Tsopano ena anafunsa kuti, “Wathawitsa

Likongwe ndani?” Mkamwini wamkulu anayesetsa

kupepesa koma chifukwa anali atanena kale yekha

kuti amene athawitse Likongweyo achoka pamudzipo,

anakakamizika kuchoka ndi mkazi wake. Mkamwini

wamng’ono ndi amene anapitiriza kukhala pamudzipo.

Phunziro: Osamafulumira kuyankhula chifukwa

umatha kudziika wekha pakona.

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani akamwiniwa ankakumba

Likongwe?

2. Kodi mkamwini wamkulu ananena kuti amene

athawitse Likongwe achita chiyani?

3. Kodi zimene ananenazi zinamubweretsera

mavuto otani?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

250
Mlendo Ndi Mame

Kalekale panali mayi wina dzina lake Nasiketi. Nasiketi

anali kudziwika kwambiri chifukwa cha umbombo.

Tsiku lina anavuula mphale, ndipo atasinja ufa

anaganiza kuti ndiwo zimene adyere nsima tsikulo

zikhale nyama. Anasinjadi ufa wosalala bwino

ndiponso anapezadi nyama yonona bwino imene

anakagula pamudzi woyandikana ndi mudzi wawo. Pa

nthawiyi Nasiketi anali asanataye matsukwa a mphale

ija. Akumaliza kuphika nsima anamva panja munthu

wina akuodira. Poonetsetsa anaona kuti ndi mlendo

amene sanali kumuyembekezera. Apa nzeru

zinamuthera Nasiketi. Ananyamula nsima ndi kuika

pamphika wa nyama uja kenako n’kuika mphika wa

nyama ndi nsima ija pakamwa pa mtsuko umene

munali matsukwa uja. Tsoka ndi ilo nyama ndi nsima

ija zinagwera m’matsukwa muja. Atatuluka panja kuti

akumane ndi mlendo uja, mlendoyo anamuuza kuti,

“Pepani ndi wosakhalitsa, ndimafuna mundigawireko

madzi akumwa.” Mlendoyo atamwa madziwo

ananyamuka n’kumapita.

Phunziro: Umbombo kapena dyera zimawonongetsa

zambiri.

Mpandamachokero Anthology

251
Mafunso

1. Kodi Nasiketi anali ndi khalidwe lotani?

2. Kodi ataona kuti kwabwera alendo anachita

zotani kuti alendowo asadye nawo nsima yake ya

ndiwo nyama?

3. Kodi alendowo anabwera kunyumba kwake

chifukwa chiyani?

4. Kodi mukuganiza kuti Nasiketi anasangalala

ndi nsima ija?

5. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

252
Ukasauka Usamagwira Nyanga

Mkulu wina anakafunsira ntchito kwa bwana

wolemera kwambiri. Kumene ankagwira ntchitoko

anapezako anzake amene anali atakhala kwa nthawi

yaitali ndi bwanayo. Anzakewo anali ndi zinthu

zambiri zimene anapata pa zaka zimene anakhala

akugwira ntchito. Chifukwa chosirira kukhala ndi

katundu ngati wa anzakeyo ndiponso kukhala

wolemera, anaganiza zoti apeze mankhwala. Mumtima

anaganiza kuti mankhwalawo amuthandiza kuti

bwana wake azimukonda, kuti iye akhupuke ndiponso

kuti bwanayo achotse ena mwa anzake ena amene

sankagwirizana nawo. Ngati zimenezi zikanatheka

ndiye kuti iye akanalandira udindo ndiponso

akanamuwonjera malipiro ake. Atapita kwa sing’anga

anapezadi mankhwala amene ankafunawo. Sing’anga

uja popereka mankhwalawo anamuuzitsa kuti

asakagone kwa masiku atatu chifukwa ngati

angakagone ndiye kuti akatupa mimba. Koma tulo ndi

nkhondo timagoneka olira. Tsiku loyamba analimbadi

m’maso osagona. Pamene kunkacha tsiku lachiwiri

tulo tinali titasonkhana, moti amati akati aimirire

sizimatheka. Atakhala pansi kuyambika kwa matenda

Mpandamachokero Anthology

253
kunali komweko. Anzake amene ankafuna kuwalodza

aja atamufunsa anafokotokoza kuti, “Pepani anzanga,

munthune ndimafuna kulemera. Ndiye mankhwala

amene ndinapeza, chizimba chake china n’choti

ndisagone masiku atatu, koma ndalephera

kuchikwaniritsa. Motero thamangani mukamuuze

sing’anga wandipatsa mankhwalawa kuti atsukule

nyangayo n’cholinga choti ine ndikhale ndi moyo.”

Anzake aja atapita anakapeza kuti sing’anga uja anali

atamwalira cha dzana lake moti anthu anali

asanachoke pasiwa. Anzake atabwerako

anamufotokozera mmene ayendera. Chifukwa

chodziwa kuti kwake kwatha anayamba kulira ndipo

polirapo anali kulira mochenjeza kuti, “Abale anga

munthu ukasauka si nzeru kugwira nyanga, taonani

zandichitikira inezi!” Pamenepo anzakewo

anavomerezadi kuti, “Ukasauka usamagwire nyanga.”

Nyanga zimene munthu uja anakatenga ndi zimene

zinam’phetsa.

Mpandamachokero Anthology

254
Phunziro: Anthu ambiri a ku Africa kuno

amakhulupirira zanyanga kapena ufiti, koma ngati

atasukusula akhoza kuona kuti ufiti kulibe. Mwambi

wakuti ukasauka usamagwira nyanga

umangochenjeza kuti zikativuta tisamachite zinthu

zomwe zingatiike m’mavuto kapena kumafunira

anzathu zoipa.

Mafunso

1. N’chifukwa chiyani mkuluyu anapita kwa

asing’anga?

2. Kodi kusakhutira ndi zomwe tili nazo

kungabweretse mavuto anji?

3. Kodi mwambi wakuti ukasauka usamagwira

nyanga umatanthauza chiyani?

4. Kodi tikuphunzira chiyani m’nkhaniyi?

Mpandamachokero Anthology

255
Ulenje Umasimba Wako

Kalekale panali munthu wina amene anapita kuthengo

kukapha nyama. Kumeneko anapha nyama ziwiri.

Pamene ankabwerera kwawo n’kuti kunja kuli

kachisisira ndipo anamva phokoso likumveka m’mudzi

wakwawo. Atafika pamphambano, mwadzidzidzi

anangoona mkango watulukira. Mlenjeyo anachita

mantha kwambiri, koma mkango uja unamuuza kuti,

“Musachite mantha achimwene. Panotu takumana

amuna okhaokha. Kaya inu mukuchokera kuti

ulendowu?” Poyankha munthu uja anati: “Ine

ndikuchokera m’malunjemu ndimakasaka.” Ndiyeno

mkango unati, “Popeza tonse tikuchokera kosaka,

aliyense asaulule mnzake. Ulenje umasimba wako,

osati wamnzako.” Atangosiyana pamenepo, mkango

uja unalowa m’tchire ndipo munthuyo anathamangira

kwawo ali ndi mantha. Kenako anayamba kuuza

anthu kuti wakumana ndi mkango utagwira nyama.

Mkango uja utamva zimenezi, unapita kunyumba kwa

amfumu n’kukagwira mwana wawo n’kumupha.

Kenako unakamuika m’nyumba mwa mlenje uja.

M’mudzimo munayambika chipwirikiti chifukwa cha

kusowa kwa mwanayo ndipo mfumu inalamula kuti

Mpandamachokero Anthology

256
anthu afufuze amene watenga mwana wakeyo.

Atafufuza anapeza mwanayo atafa koma ali m’nyumba

mwa mlenje uja ndipo mfumu inalamula kuti nayenso

aphedwe.

Phunziro: Si bwino kumaulula zinthu zomwe iwenso

wachita nawo, zimabweretsa mavuto.

Mafunso

1. Kodi mkango unkachokera kuti nanga mlenje

uja ankachokera kuti?

2. N’chifukwa chiyani mkango unanena kuti

ulenje umasimba wako?

3. Kodi mlenjeyo analakwitsa chiyani?

4. Nanga anakumana ndi mavuto otani?

5. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

257
Angozo ndi Mwana Wawo

Bambo: Iwe Joni, kodi pulezidenti woyamba m’Malawi

muno anali ndani?

Mwana: Joyce Banda.

Bambo: (Phwaaa! anamuswa khofi) Uzikhala siliyasi

ndi maphunziro ako!

Mwana: Oo! pepani, ndimaona ngati mumafunsa

pulezidenti woyamba wachizimayi.

Bambo: Khala chete chimwana chopanda nzeru iwee!

Ngati zikukuvutani zakupulaimale, ndiye

zakusekondale mukaphula kanthu inu?

Mwana: Chabwino, nanga inu bambo, Abengo ndi

ndani?

Bambo: Mlimi wa fodya.

Mwana: (Phwaaa! naye analipulumutsa lake khofi)

Abengo ndi chibwenzi cha amayi! Muzikhala siliyasi

ndi banja lanu inu!

Bambo: Mwanawe ndiuze zambiri.

Mwana: Khalani chete. Ngati mukulephera kudziwa za

akazanu musanakalambe, nanga mukadzakalamba

Mpandamachokero Anthology

258
ndiye zidzakhala bwanji?

Phunziro: Aliyense amachita bwino mbali inayake.

Mafunso

1. Kodi n’chifukwa chiyani Angozo anamenya

mwana wawo?

2. Kodi makambitsirano a bambo ndi mwanayu

akusonyeza bwanji kuti onse anali ndi nzeru?

3. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

259
Ufulu wa Nkhwere

Tsiku lina Nkhwere zinachoka m’nkhalango n’kufika

pakhonde la sukulu yotchedwa Nfunde. Mtsogoleri wa

Nkhwere anali Goloti. Goloti anasuzumira pawindo

n’kuona mnyamata wina dzina lake Sibo akusewera

m’kalasi ndipo anamuuza kuti: “Iwe Sibo, ife timafuna

kuimba nawo sukulu, kodi aphunzitsi ako ali kuti?”

Sibo anati, “Ine ndinatsiriza kale, tsopano ndine

mphunzitsi.” Koma Goloti anati, “Kodi sudziwa kuti

iwe ndi ife ndi mtundu umodzi? Inuyo munachokera

kwa ife, mumangoona kunyada inuyo. Inu anzathu

mumavala malaya ndi kabudula, ife timangokhala

osavala, kodi mulibe manyazi kumanyoza ife makolo

anu? Pakanapanda ife mukanaoneka inu?” Koma Sibo

anati, “Sindikukudziwani ayi! Inu ndi anyani a

m’tchire!” Koma Goloti anati, “Eee! Mwana uyu

n’ngosaphunzira. Kawerengenso mabuku ako. Ife

tsopano tikufuna ufulu womaimba sukulu pamodzi

ndi inu, ndiponso tizichita zibwenzi ngakhalenso

kukwatirana.”

Sibo: “Chokani anyani inu!”

Goloti: “Eee! Mwana iwe ukuchitira chipongwe makolo

Mpandamachokero Anthology

260
ako, ndithu mukapitiriza kuchita mwano umenewu

mvula simuiona chaka chino.”

Sibo: “Chokani inu! Chokani!”

Goloti: “Ine ndi wapampando wa anzangawa.

Tapangana m’tchire m’dalaka njoka. Ife tonse tikufuna

tibwerere kumudzi kuno, tizidyera pamodzi, ndiponso

tizimwera pamodzi.”

Sibo: “Pakati pa ife ndi inu ayi, chibwenzi

sichingakhalepo. Inu adakusankhirani Fulu kuti

muchite naye ubwenzi.”

Goloti: “Chabwino, tsala bwino, ife tipita kwa Fuluyo.

Koma kawerengenso mabuku. Iwe unachokera mwa

ife. Onani kamwana kosaphunzira, kawerenge

mabuku a Dalawini, akakuuza. Onani umbuli! Funsa

aphunzitsi ako!”

Mpandamachokero Anthology

261
Mafunso:

1. N’chifukwa chiyani nkhwere zinkanena kuti ndi

pachibale ndi Sibo?

2. Kodi munthu ndi nyani ndi zofananadi?

3. Kodi mukuganiza kuti nkhwere italowa

m’kalasi n’kukhala padesiki ingaphunzire

kalikonse?

Mpandamachokero Anthology

262
Ubwenzi wa Nkhumba ndi Nkhosa

Kalekalelo, pakati pa Nkhosa ndi Nkhumba panali

chibwenzi chonyambitana mapazi. Kumene Nkhosa

inkayenda, Nkhumba inkakhala komweko. Anthu onse

ankasilira chibwenzi chosaonekaoneka chotere. Kalulu

nthawi zonse amati akamva za chikondi chotere

sankamva bwino, kumtima kwake kunali nsanje.

Tsiku lina Kalulu ankakambirana ndi mkazi wake

amvekere, “Kodi iwe wamva za chikondi cha Nkhosa

ndi Nkhumba?” Poyankha mkazi wake anati, “Eee!

Anzanutu amenewo. Si zainuzi. M’nyumba

kumangokangana tsiku ndi tsiku. Ndiponso pakhomo

panga pano, ndimangokhalira kulandira milandu.

Kumene mumayendako ntchito ndi bodza komanso

kuchenjeretsa anthu. Mbiri ili buuu! Akuti

kuchenjera! Banja lanunso likukukanikani kusamala!”

Kalulu atamva mawu amenewa anati, “Izo udamvazo

ndi za nsanje. Anthu amachita nsanje ndi ine popeza

ife a Kalulu ndife amuna osati masewera. Mfumu

yamuno m’nkhalango yomveka ngati kulira kwa

mphenzi nthawi ya mvula.”

Tsopano kalulu analowedwa mzimu woyipa.

Mpandamachokero Anthology

263
Ananyamuka nalo liwiro kupita kwa Nkhumba ndipo

anangoti balamanthu! nati, “Moni a Nkhumba! He-e-e!

ati ndili ndi bwenzi! Mwamva kodi?” Kenako a

nkhumba anati, “Zotani? Za bwenzi zotani?” Kalulu

anati, “Suja akuti bwenzi lanu ndi a Nkhosa? Ine

ndathamanga kudzaulula zimene anandiuza.” “Ine

sindifuna kumva chilichonse chokhudza bwenzi langa

Nkhosa, bwenzi lapamtima,” anatero a Nkhumba.

Kenako Kalulu anati, “A Nkhosa amakunenani ati inu

ndinu auve wodya zotoleza m’matope, ati ndinu

msambamatope.”

Tsopano nkhumba inautsa mutu wake kuti imve

zonse.

Kalulu: “Tere amatinso inu ndinu wamatekenya.”

Nkhumba: “Tsopano ndakhulupirira, iwe Kalulu ndiwe

wabwino. Iweyo ukhala bwenzi langa. Uzindiuza zonse

zimene Nkhosa izinena.”

Kalulu: “Chabwino ndavomera chibwenzi chapakati pa

inu ndi ine.”

Nkhumba: “Tsopano pita bwino bwenzi langa. Koma

wosakamuuza Nkhosa kuti ndapanga ulendo

wokamuphwasura iyeyo.”

Mpandamachokero Anthology

264
Kalulu analiyatsa liwiro lopita kwa Nkhosa. Atayipeza

Nkhosa anati:

Kalulu: “O! o! Kodi mulipo? Akadakhala kuti amafa

ndi mjedo, kunena zoona n’kadakupezani mutafa.”

Nkhosa: “Kwagwa chiyani?”

Kalulu: “Ee ho! Ine panjira ndinakumana ndi a

Nkhumba, zimene amanena zosonyeza kuti zija

timamva kuti mumakondana, n’zabodza.”

Nkhosa: “Amati chiyani iyeyo?”

Kalulu: “Amati inu ndinu wanyansi ati sadzadyera

nanu pamodzi popeza muli ndi matenda a mamina

wosatha, amangochucha ngati mtsinje. Msipu wonse

ati inu mudagwetsera mamina mudawononga.”

Nkhosa: “Amatero iyeyo?”

Kalulu: “Iwowo ndithu ndiwo amatero.”

Nkhosa: “Kuyambira lero chibwenzi chachipongwe

chotere chatha. Tsopano iweyo ndiwe bwenzi langa

chifukwa umanena zoona, ndipo ndili pa ulendo

kupita kwa iyeyo kuti ndikamuphulitse.”

Pamene nkhumba inatsiriza kukwera chitunda

Mpandamachokero Anthology

265
chopitira kwa Nkhosa inangoti, gululu yakumana ndi

Nkhumba. Eee, panalitu moto!

Nkhumba: “Bwanji iwe umandinena, lero kuli

ndikupha!”

Nkhosa: “Iwenso umandinena, ndamva kwa kalulu

bwenzi langa. Lero ndikufinya.”

Kupandana kwa awiriwa kunamveka ponseponse

ndipo chibwenzi chinatha. Kalulu anati kwa mkazi

wake: “Suja unkanena kuti chikondi chikundikanika,

n’kumayamikira a Nkhumba ndi a Nkhosa, wamva

tsopano zimene zachitikazi? Heede!

Ndimangokumvetserani!”

Mafunso:

1. Kodi mkazi wa Kalulu ankadandaula chiyani?

2. Kodi khalidwe la Kalulu linali lotani?

3. N’chifukwa chiyani Nkhosa ndi Nkhumba

zinapandana?

4. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

266
Mvundula Madzi

Kalekalelo panali midzi iwiri imene anthu ankamvana.

Anthu ambiri anali kusirira machitidwe a midziyi.

Mayina a midzi anali Mchirawagaru, mwachidule

amati mudzi wa Mchira. Winawo unali mudzi wa a

Zeze.

Pakati pa mudzi wa Mchira ndi wa Zeze, panali

chitsime chotchedwa Namtudza. Chitsimechi chinali

chokumba ndipo chinazunguliridwa ndi mitengo ya

nkhadze cha kumtunda kwake. Kumunsi kwake

kunali mtengo wamango ndipo chakumwera kwake

kunali mtsinje umene udagwera ku Mtema, ku

Phukuto m’mudzi mwa a Mchira modzera kumalo

wotchedwa Danani, mpaka m’chikonde pafupi ndi

Nzama kukaphera mumtsinje wa Namachizi. Kunsi

kwake kunali dziwe lotchedwa Kanyinda.

Chimbalame chotchedwa Mvundulamadzi,

mwachidule amati Vundula chinali kumwera pa

chitsime cha Namtuza, chimwera ku Mtema,

Chimwera pa Chimkonde, mpaka dziwe la Kanyinda.

Mbalameyi inali kuuluka pamwamba pa midzi iwiriyi,

Mchira ndi Zeze, ndipo chifukwa cha kumvana kwa

Mpandamachokero Anthology

267
midzi iwiriyi Vundula sankakondwera ayi. Popeza

Mbalame zotere zimakondwera zikaona chidani,

maliro, ndewu kapena kuzokozana.

Tsiku lina chinagona mumtengo wamkuyu pa

Kanyinda. Mmawa chinalawira kuchitsime cha

Namtunda ndipo chinaona gulu la akazi lasenza

mitsuko kukatunga madzi. Gululi linali la kwa

Mchirawagalu. Atatha kutunga, chimbalamechi

chinalowa pachitsime paja basi n’kudetseratu madzi

aja chimvekere, vu! vu! vu! Ndi mapiko ake aja, phi

phi! phi! Madzi onse kuderatu kuti bii!

Chitatero chingangoti vuuku, bisalu mumtengo wa

Nkhadze. Tsopano akazi a kwa Zeze analipo khumi.

Atafika pachitsime anapeza madzi ali bii! Mtsikana

wina wotchedwa Maleyi anati, “Oo anzathu onani

madzi ada! Komatu akazi a kwa Mchirawagaru atunga

pompano. Basi iwowo ndi amene adetsa madzi.

Akufuna kuti chitsime chikhale chawo chokha.

Tsopano tadziwa, a Mfumu a Mchira akudana ndi a

Zeze, awatuma ndi amfumu kuti adzachite zimenezi!”

Akazi onse anabwerera osatunga madzi mpaka ena

anapita kukatunga kuchitsime cha Namachizi.

Chimbalame chija chitaona zimenezi chinangoti,

Mpandamachokero Anthology

268
“Ehede! Basi zakhala bwino. Tsopano cholinga changa

chakwaniritsidwa.”

Tsiku lina m’mawa chimbalame chija chinasokoloka

m’nthochi za m’madimba a ku Dumbzi, kulawirira ku

Namtunda kukadetsanso madzi akazi a kwa a Zeze

atatunga kale. Pobwera a kwa Mchira anapeza madzi

akuda. Mtsikana wina dzina lake Damalesi anati,

“Onani akazi a kwa Zeze adetsa madzi, awapangira ndi

amfumu awo.” Onse anabwerera ndipo Mbalame ija

pakumva inati, “Eheee, zanga zikuyenda bwino.”

Potsiriza, midzi yonse inadodoma popeza mfumu

ziwirizi zinafunsana pabwalo. Tsopano a Zeze ndi a

Mchira anapangana kukakhalira ku chitsime kuja ndi

nduna zawo. Mmawa kukucha, anaona chimbalame

chabwera m’madzi muja lowu, chimvekere mapiko

tambasulu, chayamba kuvu! kuvu! kuvu!

Onse aja anathamanga ndi uta, basi n’kuchilasa ndipo

chinafera pomwepo. Zitamveka izi, a Zeze ndi a

Mchirawagaru pamodzi ndi anthu awo, anayanjananso

chifukwa anapha mvundula madzi.

Mpandamachokero Anthology

269
Phunziro: Ifenso tiziyamba tapha mvundulamadzi

tisanayambe kudana.

Mafunso:

1. Kodi mbalame yotchedwa Vundula

inkasangalala pakachitika zotani?

2. N’chifukwa chiyani midzi ya a Mchira ndi a

Zeze inadana.

3. Kodi anatani kuti adziwe amene ankadetsa

madzi?

4. Nanga ifeyo tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

270
Chifukwa Chake Ng’ona Imakhala M’madzi

Kalekale dzikoli likali nsoka, panali mfumu ina

yomveka kwambiri m’dziko lotchedwa Peta. Dzina la

Mfumuyi linali Chifuyo.

Dziko la Peta lidali loopsa. Kudali nkhalango ndipo

m’nkhalangoyo mudali zilombo zosiyanasiyana zoopsa,

kuyambira zokwawa mpaka zoyenda. Zimamveka kuti

kunali njoka zowuluka ngati mbalame zomwe

zinkatchedwa Njokambala. Zimamvekanso kuti kunali

mikango yamapiko imene inkatchedwa Mkangombala.

Mfumu chifuyo inali yolimba mtima pogonjetsa

zilombo zonse m’dziko la Peta. Tsiku lina, mfumuyi

inaitanitsa zamoyo zonse zam’tchire. Zitasonkhana

padambo, Mfumu Chifuyo inati, “Ndakondwa kuti a

Njovu, a Mkango, a Njati, a Nyamalikiti kaya a

Kadyansonga, a Mvuwu komanso a Kalulu afika.”

Nthawi imeneyi nyama zonse zinkangopenyetsana

kwinaku zikumangonong’ona. Njovu inati, “Anzathu,

inu a Mkango tasenderani kuno, uzaninso a Njati

akhale pafupi. Kodi a Mvuwu, munthu ameneyu

atisunga muno? Onani chili m’dzanja mwakecho. Kodi

sichija amatiphera nachochi?” Kodi mphamvu

Mpandamachokero Anthology

271
imeneyi, adakayitenga kuti?” A Mkango anati, “Tiyeni

tileke kuyankhula, angaganize kuti tamugalukira.”

Mfumu Chifuyo inati, “Tsiku lina nyama ina inabwera

kudzafunsa mmene ndizikusungirani, ndiye lero

ndaganiza zoti ndiyankhe nkhani imeneyi. Ndikufuna

kukhazikitsa malamulo oti aliyense aziyendera.

Malamulo ake ndi awa: Nyama iliyonse iziyenda

mmene ikufunira. Nyama ya ndewu sikufunika.

Nthawi iliyonse mukhoza kubwera kwa ine

kudzadandaula. Anthu anga sadzapha ngakhale

mmodzi wa inu moti akafuna nyama azipha ziweto za

m’mudzi osati inu ayi.”

Mkango: “Pepani mfumu tikuduleni pakamwa, ine ndi

anzangawa takondwa kwambiri ndi zimene

mwanenazi. Ine ndilape pamaso panu lero. Ngati

mumaona anthu ena akujiwa, kudyedwa, mtsogoleri

wake adali ine. Kuyambira lero, taleka chifukwa taona

mtima wanu wamlerakhungwa.”

Kalulu: “Tonsefe tiyeni pamodzi tikondwere tipereke

kwa Mfumu Chifuyo, Hepu! Hepu!”

Nyama zonse: “Huree! Hureeeeeeeee!”

Tsopano msonkhano utatha nyama zidakondwera

Mpandamachokero Anthology

272
koposa poona kuti ufumu wa Chifuyo udaposa

maufumu akale monga ufumu wa a Mkango

womangokudya nawo anzawo, komanso ufumu wa a

Njovu womangopondereza anzawo monga a Kasenye

ndi a Chule.

Nyama zonse ngakhalenso Njokambala ndi

Mkangombala palali kuvomera kuti Mfumu Chifuyo

adzafere m’manja mwawo.

Mfumu Chifuyo tsopano idaganiza zoika nduna zake.

A Njovu ndi amene anasankhidwa kukhala nduna

yaikulu pakati pa nduna zonse. M’nkhalango mudali

chiphokoso cha chikondwerero cha zimene Mfumu

Chifuyo inachita. Tsopano Njovu inasamuka kuchoka

kunkhalango n’kumakhala kwa Mfumu Chifuyo kuti

ikayambe udindo watsopanowo.

Mwadzidzidzi, padamveka kuti Mfumu Chifuyo idapita

koyendera dziko lake ndipo adakumana ndi

Mkangombala ndi Njokambala ndipo zilombozi

zidayamba nkhondo ndi Mfumu Chifuyo. Mwatsoka

Mfumu Chifuyo sinatenge zida za nkhondo ndye

idalumidwa koopsa. A Njovu atamva zimenezi

anathamanga nakanyamula Mfumu Chifuyo pamsana

pawo kupita nawo kunyumba. Kenako a Njovu

Mpandamachokero Anthology

273
anaitanitsa msonkhano wa nyama zonse:

“Ndakuitanani ndine. Onani Mfumu Chifuyo ili gonee.

Ndiyesa mwamva zimene Njokambala ndi

Mkangombala achita. Mfumu ngati iyi sitidzaionanso.

Taonani ine mpando umene adapatsa ife nyama za

m’tchire! Tidali yani kale ife? Siuja tinkangophedwa?”

Nyama zonse zinali ndi chisoni, nthawi imeneyi n’kuti

Njokambala ndi Mkangombala atanjatidwa kale ali

m’ndende ndiponso mapiko awo atadulidwa kale ndi

asilikali. Panamveka mawu akuti Nduna Njovu

ikufunidwa ndi Mfumu yodwalayo.

Mfumuyo inati, “Iwe Nduna Njovu waona chipongwe

chimene wachita Njokambala ndi Mkangombala. Ine

ndidzayesa kubweretsa mtendere pakati pa anthu ndi

nyama, koma mtendere udzavuta mpaka m’tsogolo.

Kumbukirani udani wa munthu ndi njoka kuyambira

pachiyambi. Ine ndimafuna kukonza chidani chimene

chija, koma ndaona chimene adanena Chauta palibe

munthu akhoza kusintha. Ine ndikafa, iwe monga

nduna yaikulu, udzasankha yani kuti adzalowe ufumu

wanga?” Nthawi yomweyo Mfumu Chifuyo inamwalira

koma mawu amene idasiya anali akuti, Ufumu

umenewu adzatenge ndi Mlenje monga mmene Mfumu

Mpandamachokero Anthology

274
inalili. Njovu sinali Mlenje ndipo inadziwiratu kuti

Ufumu wa Chifuyo sadzalowa ngakhale anali nduna

yaikulu. Koma anawuza anthu kuti alenje onse

akufunika ndipo nyama zonse zisonkhane zidzamve

mawu.

Nyama zonse zinatchera makutu kuti zimve mawu a

Nduna Yaikulu. “Zachisoni, Mfumu yathu imene

timaikonda yapita kumanda kosabwerako. Onani

mpando uwu wachifumu, lero ulibe mfumu yake.

Pomwalira mfumu inandiuza kuti, mfumu yotenga

mpando umenewu ikhale imene ili katswiri pa ulenje.

Nonsenu mukudziwa kuti ine ngakhale kuti ndine

Nduna Yaikulu, sindine mlenje. N’kadakhala wokonda

ufumu sindikadakuuzani za mawu amenewa ayi.

N’kadangokuuzani kuti kuyambira lero ndine Mfumu

Chifuyo. Koma ndikufuna alenje abwere apa!” Nyama

zonse zinakuwa, “Koma Njati! Ayi koma Kalulu, ayi

koma N’gonaa!” “Chabwino onse abwere kuno,” idatero

Njovu.

Tsiku lina Nduna Njovu inasonkhanitsa nyama zonse

mmawa ndipo inati, “Sindikufuna kupereka ufumu

kwa bwenzi langa ayi! Koma amene angaonetse kuti

ndi mlenje, alandira ufumuwu! Paja mukudziwa kuti

Mpandamachokero Anthology

275
pali opikisana atatu: Ng’ona, Njati ndi Kalulu. Mmodzi

wa atatuwa adzakhala mfumu ya tonsefe. Ndiye

kudamboku kwapezeka nyama ziwiri zakufa. Kodi ndi

ndani wasodza chotereyu?” Posachedwa padamveka

mawu, “Ndine Bwana!” Adafulumira kuyankha Ng’ona.

Onse aja, adaomba mmanja, kulemekeza Ng’ona,

ndipo ena amayankhula chonong’ona kuti, “He!

Komatu zadziwikiratu kuti ufumu umenewu autenga

ndi Ng’ona! Chifukwa liwiro lamumchenga lifunika

kuyambira pamodzi. Ng’ona ndiye wapita kale

m’tsogolo!”

Zimenezi Kalulu zidamuwawa mtima chifukwa ena

adayamba kunyoza Kalulu, “Iwe timakukonda,

ndiponso ndiwe wochenjera. Koma lero wangokhala

chitsiru chenicheni, kuchenjera kuja n’kwabodza!

Monga zikhale zoona kuti a Ng’ona n’kutenga ufumu

iwe ulipo?” Adatero a Mbidzi.

Usiku Kalulu adapita kukasaka nyama. Mwamwayi

adapha Ntchefu zitatu nabwera nazo m’mudzi muja

naika pakhomo pa a Njovu. Kenako iye anapita

kukagona, koma popita anadzera kunyumba ya

Mbidzi. “Odi! Odiii!” Kalulu adawodira. “Ndiwe ndani

usiku ngati unooo?” Mbidzi inafunsa. “Ndine Kalulu!

Mpandamachokero Anthology

276
Paja unanena chipongwe, ndapha Ntchefu zitatu,

ndaika kale kwa a Njovu!” Anatero Kalulu. “Wachita

bwino, ka Ng’ona kodi kapose iwe? Ife tikufuna kuti

ufumu uja ukhale wako! Wachita bwino, tionana

mawa.” Anatero Mbidzi.

Mmawa kutacha, Njovu inakusa onse kuti abwere

kunyumba kwake ndipo inafunsa kuti, “Kodi wampha

Ntchefu izi ndi ndani?” Nthawi yomweyo Ng’ona

inaimirira n’kunena kuti, “Ndine Bwana!” Nthawi

imeneyi Kalulu anachedwa kubwera ndipo anadzapeza

anthu akutamanda Ng’ona akuti, “Ayi, inu Bambo

Ng’ona zanu zili kuyenda bwino, ufumuwu wadziwika

kale kuti ndi wanu.” Kalulu adapita kwa Njovu

n’kunena kuti, “Kodi mwaona Ntchefu zimene ndapha

ine usiku?” Njovu inati, “Choka iwee! Kodi ndiwe

munthu wansanje chotere?”

Kalulu adamva Mbidzi ikumufunsa kuti, “Achimwene,

kodi lija mumandiuza madzuloli lidali bodza?

Kuchedwaku ndi manyazi kuti tingakusekeni! Anzanu

a Ng’ona basi akhala mfumu yathu, kwangotsala kuti

awaveke chigwinjiri kaya ndi khoza la mnyanga.”

Posakhalitsa panamveka kuti pali mphekesera yoti

Mfumu Chifuyo sidaphedwe ndi Njokalamba kayanso

Mpandamachokero Anthology

277
Mkangombala, koma idaphedwa ndi anthu a m’mudzi

momwemo ndiye adapanga bodza kuti aziti, Mfumu

Chifuyo idaphedwa ndi zilombo. Chotero Kalulu ndi

nyama zina zidatenga thupi la Mfumu Chifuyo

n’kukayika pakhomo pa Njovu, naliphimba ndi

masamba. Mmawa kutacha, Njovu inaitanitsanso onse

kuti abwere ndipo inafunsa kuti, “Kodi pakati panupa,

ndiyesa mwadziwa kuti madzulo ano tili kuponya

ufumu wa Chifuyo. Iyi ndi nyama yomaliza

kutsimikiza kuti wotereyu ndi mlenje wofunika

kumuveka makoza awiri awa!”

Anthu onse ndi nyama zonse zinayamba kukuwa,

“Ng’ona! Ng’ona! Ng’ona! Ng’oooooooooooooonaaa!”

Kenako njovu inati, “Mvetserani kaye. Kodi wapha

imeneyi ndi ndani?” “Ndinee! Ndine Bwana!” Inatero

Ng’ona.

Ndiyeno Njovu inati, “Tsopano paja ena

akumasokoneza, kodi alipo wina wotsutsa kuti

nyamayi sadaphe ndi Ng’ona? . . . Eya, zayenda bwino

lero palibe mkangano. Madzulo ano nonse mubwere

kuti tidzalonge Mfumu yathu yatsopano a Ng’ona!”

“Ooooooooooooooo!” Phokoso lachikondwerero

linamveka. Ng’ona inati, “Lero lomwe lino potsiriza

Mpandamachokero Anthology

278
phwando, iwe Njovu ukhala nduna yanga yaikulu!”

Wagwira ntchito yako bwino!

Pamene Njovu inachotsa masamba aja anali

pamwamba pa nyamawa, nyama zonse zidati, “O! O!

O! Onani zoopsa! Kodi udapha Mfumu Chifuyo ndiwe

Ng’ona?” Ng’ona imvekere, “Hii! Ndikufa!” Waliwutsa

liwiro kuthawira kumadzi, nangoti pamadzi dyuli!

Mumtima mwake inati, “Koma sindidziwa, zimenezi

zachitika bwanji?” Kuyambira pamenepo Ng’ona

inayamba kukhala m’madzi mpaka lero.

Mafunso:

1. Kodi nduna yaikulu ya mfumu Chifuyo inali

ndani?

2. Kodi mukuganiza kuti Ng’ona inkaphadi nyama

zija?

3. Nanga anzake anatani pofuna kuikhaulitsa?

4. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

279
Mfumu Yomveka Tambala

Kale Tambala anali mfumu yomveka pakati pa

mbalame zonse, ngakhalenso nyama zakutchire.

Palibe wina amachita mwano kapena kusewera ndi

Tambala. Onse ankamuopa popeza panali mbiri yoti

ali ndi moto pamutu pake ndipo wochita naye

masewera akhoza kutenthedwa. Mbiri imati onse

okhudzidwa ndi motowo, basi imfa imakhala yomweyo

mpaka kupserera. Motowo unali wosenzera pamutu.

Ndiponso amati m’mawa kukacha Tambala

ankatsokomola ndipo nthunzi wa motowo inkaonekera

uli katukatu!

Tambala amati akangoti, “Kokolirikooooo

kwaachaaaa!” aliyense ankadzuka. Akadzatinso,

“Kokolirikooo kwaachaaaaa!” aliyense ankayenera

kuyamba ntchito kuopa kuti akachedwa

angadzam’tenthe ndi moto uja woyaka lawilawi

pamutu pake.

Nyama zonse, ndi Mkango womwe, mbalame zonse

mpaka Kalize kapena Ndakulapsa, zonse zinkaopa

Tambala. Mbalame zinanso monga Ngolomi,

Chiwombankhanga, Nthiwatiwa, Kadzidzi, Katawa ndi

Mpandamachokero Anthology

280
zina zinkaopanso Tambala. Ndiponso nyama monga

Njovu, Mvuwu, Njati komanso zina zotero, nazonso

zinkaopanso Tambala.

Mbiri inamveka kuti wina atawupala moto wa pamutu

pa Tambala, motowo sungazime mpaka wopalayo

atamwalira. Anatinso sufunika nkhuni koma

umangoyaka nthawi zonse. Mvula ikamagwa,

ankanenanso kuti suzima ndipo umafanana ndi moto

wa mphenzi woyaka mvula ili pooo!

Tambala akangolira nyama zonse zimautsa ana awo,

“Ana inu, ukani mfumu Tambala akuti amatumiza

moto wake monga wa mphenzi kwa waulesi ndi

wosamvera iye. Ukani konzekani ndithu

mungatitenthetse.”

Tsiku lina nyama zonse zinasonkhana pamodzi.

Kalulu anati, “Anzathu, moto wa Tambalawu

watiwopsa. Kumbukirani mdani wa moto ndi madzi,

tiyeni kwa a Mvuwu wokhala m’madzi tikafunsire

nzeru.” Atafika Kalulu anati, “Moni a Mvuwu, tabwera

kuti mutipatse nzeru za moto wa Tambala. Kodi

tingakaupale bwanji?” A Mvuwu anati, “Ifenso m’madzi

muno tathedwa nzeru mbale wanga! Bwanji

osapempha a Njovuwo kuti akapale?” Koma poyankha

Mpandamachokero Anthology

281
a Njovu anati, “Eee! Ndaniyo, ine n’kadawukonda

moyo, phukusi la moyo sakusungira ndi wina! Bwanji

apite ndi a Nyamalikitiwa?” Koma a Nyamalikiti

poyankha anati, “Ine ndiye toto, kodi mphenzi

pakugwa mumaiwonerera? Hee! Pamakhala zoopsa.

Tonsefe pano n’kutheratu psiti! Moto umene uja akuti

ufanana ndi mphenzi.” Nthiwatiwa anati, “Uja ndi

mdzukulu wanga. Ndipitako ndine. Moto wowopsawo

ndikauwupala.” Nyama zonse zitamva mawuwa zinati,

“Ooo! Wolimba mtima a nthiwatiwaaa!”

Mmawa mwake, Nthiwatiwa inanyamuka ulendo

kupita kwa Mfumu Tambala. Mkazi wake anasenza

chipanda cha mowa. Onse anafika pakhomo pa

mfumu Tambala.

Atafika, Nthiwatiwa inati:

Nthiwatiwa: “Zikomo Mfumu Tambala!”

Tambala: “Eee! Lowani m’nyumba muno. Koma

m’nyumba muno lero sadasesemo, akazi anuwa

analawirira kumunda. Khalani pa chikumbapo.”

Nthiwatiwa: “Ndati ndikawone mdzukulu wanga

mfumu.”

Tambala: “Aa! msatero mfumu sikhalapo popanda

Mpandamachokero Anthology

282
woibereka. Mwachita bwinoo.”

Nthiwatiwa: “Agogo anuwa anakutengerani

kachiphera dzuwa kuti muyese kufewetsa kukhosi.”

Tambala: “Ha! Mwachita bwino agogo, nanga sindiko

kukhala ukuu!”

Tsopano onse anayamba kumwa. Tambala anamwa

kwambiri mpaka anakhuta, nagona tulo pakama

wake. Nthiwatiwa inatenga ndowe yang’ombe naika

pamutu wa Tambala kuti ikolere moto woopsa uja.

Pamene anawona kuti ndowe sikukolera moto,

anayesa kuyikapo udzu, koma zonse zinangoti zii

opanda moto. Tsopano anaika nthenga zake ndipo

anaona kuti sizinapse. Nthiwatiwa inauza mkazi wake

kuti, “Mkazi wanga, wadziwonera wekha, timangowopa

njokaluzi.”

Atabwerera kwawo, anasonkhanitsa nyama zonse ndi

mbalame zomwe, ndipo anati, “Ine ndinapita kuja

munandituma, mboni ndi mkaziyu. Osamaopanso

amene uja. Simoto uli pamutu uja, ndi litcholotcholo

chabe, lidangofiira koma lilibe moto lili zii kuzizira. Ine

ndidalikhudza ndi nthenga zangazi, osapsa.

Ndinayikapo ndowe ya ng’ombe, mpaka udzu, ayi

Mpandamachokero Anthology

283
ndithu osapsa.” Nyama zonse zitamva izi zinati, “Ooo!

Basi mfumu ndiwe!”

Mafunso:

1. Kodi nyama zinkaopa Tambala chifukwa

chiyani?

2. Kodi nyamazi zinkaona kuti litcholotcholo la

Tambala ndi chiyani?

3. Kodi Tambala ankadzutsa athu pogwiritsa

ntchito lipenga lomveka bwanji?

4. N’chifukwa chiyani Nthiwatiwa inanena kuti

ankaopa njokaluzi?

Mpandamachokero Anthology

284
Chifukwa Chake Kadzidzi Amayenda Usiku

Kalekale ku Chitimbe kumene kunali tchire la bango

lokhalokha, Kadzidzi anali mfumu yoopsa. Mbalame

zonse zinkagwadira iyeyo. Tsiku lina Kadzidzi

anaitanitsa msonkhano.

Pamsonkhanowo Kadzidzi anati, “Zikomo kuti

mwabwera mwaunyinji chonchi, ine ndakhala nanu

zaka zambiri muno m’Chitimbe. Palibe wina

amadandaula. Ndamva kuti Mleme komanso

Nthiwatiwa sakufuna kubwera. Ine monga mukudziwa

ndine mfumu, tsopano ndikufuna banja lililonse

lindipatse thumba la chimanga popeza malipiro anga a

ufumu ndi omwewa.” Mbalame zonse zinati, “Zikomo

mfumu! Mulandira zimene mwanenazo. Koma nanga a

Nthiwatiwa ndi a Mleme, kodi muchita nawo chiyani?”

Kadzidzi anati, “Taonani mbali iyo, mukuona chiyani?

Kodi si asirikali anga amenewa? Uyo wamkulu

mimbayo ndiye mkulu wankhondo ndipo dzina lake

ndi Fwipi. Ali kumbuyo kwakeko ndi Soka, nayenso

ndi wodziwa za nkhondo. Onsewa ali ndi mipando,

kaya udindo wa usajeni ali ndi thepe zitatu. Uyo ali

chakunoyo pampandopo dzina lake ndi Apolo,

Mpandamachokero Anthology

285
wachiwiri ndi Zenu, wachitatu ndi Tibo amene ali

womalizira pa ulemu wa ankhondo anga. Ndanena izi

kuti mukamva kuti a Mleme ndi a Nthiwatiwa

zawavuta, mudziwe kuti nkhondo yake ndi imeneyi.”

Inu nonse mukachita mwano, nkhondo ya ine Kadzidzi

ndi imeneyo yolamulidwa ndi Sajeni Fwipi.

Wolamulira ankhondo a Mfumu Kadzidzi, yemwe anali

Sajeni Fwipi, ananyamuka ulendo wopita kwa Mleme.

Atafika, Sajeni Fwipi analamula, “Apolo! Gwira Mleme!

Mleme uyo! Akalimbalimba ipha!” A Mleme adagwidwa

n’kutengeda ukaidi. Kenako anauyamba ulendo

wopita kwa a Nthiwatiwa. Atafika, Sajeni Fwipi

analamula, “Apolo! Gwirani msanga Nthiwatiwa uyoo!

Akachita mwano, iphani!” A Nthiwatiwa nawonso

adagwidwa n’kutengedwa ukaidi, ulendo wopita nawo

kwa Mfumu Kadzidzi.

Mfumu Kadzidzi ndi mbalame zonse panali

kukondwera chifukwa cha kulimba mtima kwa Sajeni

Fwipi, Sajeni Soka, Kopolo Apolo, Kopolo Zenu ndi

Kopolo wang’ono Tibo pobweretsa achipongwe aja,

odzikuza. Atafika nawo panali nkhani.

Mpandamachokero Anthology

286
Kadzidzi: “Kodi iwe Nthiwatiwa, bwanji sunabwere ku

msonkhano? Sukudziwa kuti ine ndine mfumu?”

Nthiwatiwa: “Zimenezo mukudziwa ndinu. Kodi si

paja nyama zomwezi ndi zimene zidaveka ine ufumu?

Kodi amene anakapala moto kwa Mfumu Tambala

ndinuyo? Kodi mbalame zinazi sizikudziwa zimenezi?

Funsani a Njovu kapena a Mvuwu akuuzani za ine!”

Tsopano nkhani inavuta popeza mbalame zonse

zidakumbukira za ufumu wa a Nthiwatiwa.

Mleme: “Ine ndidamva moipa. Msonkhanowu amati

ndi wa mbalame zokhazokha, kodi ine ndine

mbalame? Kodi mbalame imakhala ndi mchira? Kodi

mbalame imakhala ndi makutu? Kodi mbalame

imakhala ndi pakamwa, mphuno ndi maso ngati

mmene ndikuonekera inemu? Nanga miyendo yanga,

kodi ikufanana ndi ya mbalame? Kodi ndili ndi

nthenga ngati mbalame nonsenu? Eeeee?”

Mfumu Kadzidzi idakanika kuyankha mafunso a

Mleme ndipo zinali zochititsa manyazi zedi.

Powafukula a Mfumu Kadzidzi, adasowa chochita

ndipo panali umboni wokwanira wosonyeza kuti a

Nthiwatiwa ndi amene anali Mfumu ya Mbalame

Mpandamachokero Anthology

287
zonse. Ufumu wa a Kadzidzi unali wobera. Akadzidzi

popsa mtima analamula ankhondo ake kuti aphe a

Nthiwatiwa ndi a Mleme. Koma Sajeni Fwipi anati, “Ine

kuyambira lero sindidzakuonaninso ngati mfumu.

Ndiponso Sindingaphe m’bale wanga Mleme ayi.”

Mbaleme zonse zinamuukira Kadzidzi ndipo nthawi

yomweyo anathawira kuthengo. Kuyambira tsiku

limenelo, a Kadzidzi amayenda ndi usiku kuopa

kuonetsedwa mbwadza ndi mbalame zija.

Mafunso

1. Kodi amene anali woyenera kukhala mfumu

anali ndani?

2. N’chifukwa chiyani Nthiwatiwa komanso Mleme

sizinabwere kumsonkhanowu?

3. Kodi zifukwa zimene anapereka zinali

zomveka?

4. N’chifukwa chiyani Kadzidzi amayenda usiku?

5. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

288
Mkango ndi Bulu

Kalekale Mkango utasowa nyama unasiya ana ake

n’kupita kukasaka nyama. Koma Mkango sunasiyire

ana akewo nyama yokwanira. Ndiye popita, unadzera

kwa bwenzi lake Bulu.

“Bwenzi langa, ine ndikupita kosaka, uzindionerako

ana anga,” unatero Mkango. “Kodi mwawasiyira

chakudya chokwanira?” Anafunsa Bulu. “Ayi

n’chochepa, koma sindikakhalitsa,” unayankha

motero Mkango ndipo kenako unauyamba ulendo

wake.

Patapita tsiku limodzi, Bulu anaona kunjira kuli zii.

Patatha Sabata, Bulu mtima sanaupeze poganiza za

ana a bwenzi lake Mkango.

M’mawa wa tsiku lina, Bulu ananyamuka ulendo

wokaona ana a mnzake. Pamene ankatulukira

pamtunda, anadabwa kuona gulu la anyani pakhomo

pa a Mkango, ana a Mkango ali m’manja mwa a

Nkhwere, ndipo anafunsa kuti, “Kodi Anyani inu,

munayamba kukhala ndi ana a Mkango?”

Nyani wamkulu dzina lake Ziyenda anayankha kuti,

“Kodi iwe Bulu wopanda nyanga, iwe ndiye mlonda wa

Mpandamachokero Anthology

289
a Mkango? Ana awa ife tatenga. A Mkango adayamba

kale kudya ana athu. Ndiye lero tidya ana ake,

kuphanga kwathu kotchedwa Dyero kuli phwando

lero!”

Bulu: “Kodi phanga limeneli lili kuti?”

Ziyenda: “Waona phiri lili apolo? Yang’ana

chakum’mawa kwakeko, kumeneko ndiye kuli phanga

lathu, ubwere ndithu udzadye nawo.”

Bulu: “Chabwino ndibwera, komanso mundikomere

mtima ndibwere ndi mwana wanga wodwala.

Asing’anga a Kalulu anati akudwala matenda a njala,

ndiye atadya nawo phwandolo, akhoza kuchira.”

Ziyenda: “Abwere ndithu.”

Bulu: “Kodi kaphedwe ka mwana wa Mkango

mumakadziwa?”

Ziyenda: “Ayi!”

Bulu: “He! Zikundu zanuzi zikhoza kunyeka zilonda,

moti simungamathenso kukhala pansi. Chabwino,

mundidikire ndidzaphe ndine!”

Ziyenda ndi anzake anavomereza kuti amene adzaphe

ana a Mkango ndi Bulu. “Chabwino, tatsogola

Mpandamachokero Anthology

290
kukakonzeka. Udzapeza nkhuni zili ndu! kudikira iwe

ndi mwana wako akudwalayo.”

Pamene Bulu ankabwerera kwawo, anakumana ndi

Mkango.

Mkango: “Kodi m’bale wanga Bulu, watani? Nkhope

yakoyi ngati ndi yokondwa!”

Bulu: “Pepani ndithu kwagwa nkhondo. Ana anu onse

awiri atengedwa ndi Ziyenda ndi anzake, anyani aja

amakhala paseri pa phiri iloo!”

A Mkango atamva zimenezi analira, “Vuuu! Vuuu! Ana

anga ineee! Vuuu!” Koma a Bulu anati, “Musalire,

zonse ndakonza kale.”

Tsopano a Bulu analongosola zonse zimene

zinachitika. Anafotokoza mmene anapezera Anyaniwo

akutenga ana a Mkango. “Pepani bwenzi langa, ine

ndawatchera msampha, lero lomwe ana anu

tikawapeza ali moyo.” A Bulu analongosola zonse

zimene adapangana ndi Anyani aja. “Inuyo

ndikuberekani ngati mwana, ndipo tikafika kumene

kuli ana anu. Tikakafika, mukhoza kukachita

chilichonse chomwe mukuona kuti ndi chabwino!”

Anatero a Bulu.”

Mpandamachokero Anthology

291
Atafika, Bulu anati, “Odi! Odi! Ndafika ndi mwana

wodwala uja!” Ziyenda namuyankha kuti, “Lowani.

Ana a Mkango aja ndi awa. Tikudikira kuti muwaphe

kuti tiyambepo phwando lathu. Mwachitanso bwino

kubwera ndi mwana wanu wodwalayu.”

Nthawi yomweyo Bulu anati: “Dzimvere ntolo mwana

wodwala! Zidze pano n’zatonse! Kadziwa mwini nkhuto

wa Fulu!” Kenako a Mkango anatsika pamsana wa a

Bulu. Anyani ataona kuti ndi Mkango, anadziwa kuti

zinthu zasolobana. Anayesetsa kuthawa koma

zachisoni, onse anagwidwa n’kuphedwa ndi Mkango.

Ndiyendo a Mkango anati, “A Bulu, sindinkadziwa kuti

ndiwe munthu wabwino chonchi! Ndiwe bwenzi langa

la pamtima. Taona ana anga onse ali bwino. Tiyeko

kumudzi ndikakupatse mphatso.”

Atafika kumudzi, Mkango unati, “Kuyambira lero,

uzigona m’nyumba kapena m’khola. Sudzagonanso

pabwalo ngati nyama zina zonsezi.”

Mpandamachokero Anthology

292
Mafunso

1. N’chifukwa chiyani Anyani anagwira ana a

Mkango?

2. Kodi Bulu anawauza zotani?

3. Kodi zinali zoona kuti anyani aja akapha

mwana wa Mkango zikundu zawo zikhoza kunyeka

zilonda?

4. N’chifukwa chiyani Bulu anasiya kukhala

m’tchire?

5. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

293
Nkhuku ndi Nkhumba

Tsiku lina Nkhumba inapita padzala. Nkhumbayi inali

n’cholinga chokatoleza zakudya zotayidwa. Dzala

limeneli linali la nyumba ya a Kamzati pamudzi wa

Mawoneka. Pamene Nkhumba inkapita padzalalo,

Khoswe n’kuti ali pompo kale, ndipo ataiona

Nkhumbayo anabisala. Tsopano Nkhuku inabwera

n’kuyamba kukambirana ndi Nkhumba.

NKhuku: “Kodi Nkhumba, bwanji umavutika ndi

zakudya za m’dzala ngati izi? Sizikutsegula m’mimba?”

Nkhumba: “Inetu ndatha masiku ambiri mbuye wanga

osandipatsa chakudya. Zikumveka kuti njala yalowa

kudziko kuno.”

Nkhuku: “Zoonadi, zimene mwamvazo n’zoona.

Chimanga kulibe, gaganso kulibe.”

Nkhumba: “Nanga iwe mnzanga umadya chiyani?”

Nkhuku: “Ndimadya uchi wozuna.”

Nkhumba: “Kodi uchiwo amakupatsa ndani?”

Nkhuku: “Ine ndine wanzeru, bwenzi langa lina

linandipatsa msampha wokolera njuchi ndipo zimaika

Mpandamachokero Anthology

294
uchi mumsamphawo. Msamphawo umatchedwa

mng’oma. Njuchi zimalowa m’menemo n’kuikamo zisa

za uchi.”

Nkhumba: “M’bale wanga, bwanji ukhale mnzanga?

Ndigawireko uchiwo, taona ine mnzako ndikufa ndi

njala! Taona nthitizi.”

Nkhuku: “Mawa ukonzeke. Koma udzalawire chifukwa

tidzayenda ulendo wautali kuti tikafike kumene kuli

uchiwo. Ndiye popeza mng’omawo uli mumtengo,

ndidzakuuza mmene udzachitire.”

Tsopano Nkhumba inali ndi chimwemwe chodzadza

tsaya itamva zimene nkhuku inamuuza. Koma Khoswe

anabisala uja anamva nkhani yonseyi. Khosweyo

anachita nsanje chifukwa nayenso njala inali

itamuchita kanthu. Zimene ankaba usiku m’nyumba

ya a Kamzati, sizinkapezekanso chifukwa cha njala ija.

Khoswe mumtima mwake anati, “Hee! Tiona, ine

sindingafe ndi njala Nkhumba itapeza mwayi wokadya

uchi. Ndipita nawo komweko. Ndikulakalaka kutacha

msanga kuti nanenso ndikaulawe.”

Mmawa kutacha, Nkhuku ndi Nkhumba zidakumana

padzala paja.

Mpandamachokero Anthology

295
Nkhumba: “Wadzuka bwanji bwenzi langa! Inetu

ndafika kalekale pano. Paja akuluakulu adati, ‘Wamva

m’mimba ndi amene amatsegula chitseko.’”

Nkhuku: “Bwenzi langa, ndasangalala kuti

wandilonjera chonchi. Koma tisachedwe, tiye

tiuyambe. Pajatu ndinati uchiwo uli mumtengo! Ndiye

Nkhumba: “Nanga ine ndikakwera bwanji

mumtengowo. Inetu ndilibe mapiko ngati iwe!"

Nkhuku: “Ayi inu a Nkhumba, musandidule

pakamwa. Ndakuuzani kuti lero mukadya uchi,

musakayikire iyayi. Nzeru zili ndi ine.”

Nkhumba: “Ha! Ha! Ha! Lero kuli kudya!”

Nkhuku: “Tamvera bwenzi langa. Ndikuuziretu, pali

lamulo limodzi. Ine ndi iwe titenga nsungwi yaitali,

ndiye iweyo ulume mbali imodzi, ine mbali inayo. Ine

ndigwira ntchito youluka, ndipo iweyo unyamuka

nawo limodzi. Tikafika mumtengomo, usakalankhule

ndi wina aliyense. Ichi ndi chinsinsi chodyera uchi,

timadya koma osalankhula. Koma wamvetsa za

lamuloli?”

Mpandamachokero Anthology

296
Nkhumba: “Zamveka, ndikuona kuchedwa kwambiri

kuti tinyamuke.”

Pamene ankayankhula izi, Khoswe wa padzala uja

ankangomvetsera. Tsopano Khosweyo anathamanga

kwa bwenzi lake Khoswe wa patsidwi kukafunsa

nzeru. Khoswe wa patsindwi anamuuza kuti,

“Nkhumba imene ija ndi mdani wanga. Iweyo

uwalondole, ndiye popeza wamva kale chinsinsi

chawo, iwe upite n’kukaima patsinde la mtengowo.

Uzikachita zinthu zoti zikamupsetse mtima. Ukaona

akagwa n’kufa.”

Mmawa kutacha, Nkhumba ndi Nkhuku zinayamba

ulendo wawo. Zitafika pamtengo uja, Nkhuku inati:

“Waona, mtengo uja ndi uwu. Mng’oma uja ndi uwo!

Tsopano luma nsungwiyo. Konzeka m’bale wanga,

limba mtima, tiye tsopano!”

Nkhumba itaona kuti yakwera mumtengo inasangalala

kwambiri, ndipo nkhuku inatenga uchi uja n’kuipatsa

Nkhumba ndipo onse anayamba kudya. Mwadzidzidzi,

pansi panamveka mawu a Khoswe, “Ha! Chitsiru iwe

Nkhumba wodya zowola, tsika! Kadye zowola zako

kudzala! Tsika chitsiru iweeee!”

Mpandamachokero Anthology

297
Nkhumba inamva izi, mtima wake unayaka moto

ndipo inaiwaliratu lamulo lija loti asamayankhule

akudya uchi. Kenako inati, “Aaa! Kamwana ngati iwe

sungandichite chipomwe chotere. Kodi ndikudya

zako?” Mawu amenewa ali m’kamwa, nthambi ya

mtengo umene Nkhumba inakhala inakhadzuka ndipo

Nkhumba inakuwa kuti, “Hi! Bwenzi langa ndikufa!”

Nkhumba inagwera pansi kuti phii!

Nkhuku itaona zimene zinachitkazo inati: “Oooo!

Bwenzi langa tsokalo, tsokaloo!”

Kenako Khoswe anapita pamene panagwera Nkhumba

paja n’kunena kuti, “Ndinakuuza ndiwe chitsiru,

tachionani chatsakamuka chili gaada! Chimati chitani

chikadya za m’dzala!”

Nkhumba idagwa ndi chipumi moti mphuno yake

idanyindukiratu. Mphuno ya nkhumba inaonongeka

kwambiri chifukwa cha dyera la uchi komanso

kusamvera malamulo.

Mpandamachokero Anthology

298
Mafunso

1. N’chifukwa chiyani nkhumba inakwera

mumtengo?

2. N’chifukwa chiyani mphuno ya nkhumba ndi

yophwanyika?

3. Kodi dyera komanso kusamvera malamulo

kumabweretsa mavuto otani?

4. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

299
Ng’oma ya Kalulu

Kalulu adali ndi bwenzi lake lapamtima. Bwenzi lakeli

linali Nkhandwe. Tsiku lina Kalulu anaona bwenzi

lakeli likubwera potero. Pa nthawiyi Kalulu ankaotha

moto ndipo n’kuti dzuwa likulowa. Bwenzi lake lija

litafika, Kalulu anakondwa kwambiri ndipo anakonza

zakudya kuti bwenzi lake lisangalale.

Atatha kudya Chakudya, Kalulu anati, “Kodi

mwangotiyendera?” “Ayi bwenzi langa, ine

chandiyedetsa ndi chinthu. Koma ndisanayambe

kulongosola, ndikufuna undiuze mayina a adani ako

onse.” Inatero Nkhandwe. Inkafuna kuti iitane adani a

Kaluluwo kuphwando kuti adzawakhaulitse.

Tsiku la phwandolo litakwana, Njovu, Mkango ndi

Kadyamsonga zidafika kunyumba kwa Kalulu.

Madyerero anayambika, ndiye popeza nthawi idali

itatha, onse adagona. M’mawa kutacha, phwando

linayambanso.

Nkhandwe: Akuluakulu, phwando likayamba, Kalulu

atenga ng’oma iyo n’kuyamba kuimba ndipo tonse

tizivina!

Njovu: Eya! Ilitu ndiye phwando, lochita kuthudzulira

Mpandamachokero Anthology

300
gule! Nanga paphwando pazichita kukhala ngati

pamaliro?

Mkango: Ndipo inuu! Tiyeni timasuledi ziuno! Mwina

zingachoke dzimbiri.

Kadyamsonga: Koma ndiyetu timuponda gule!

Kenako anapatsidwanso nsimba yangati phiri ndipo

akuluakuluwa anakhala moizungulira. Anaipwekeka

koopsa moti onse anakhuta mimba tugululu, ndipo

anapempha Kalulu kuti ayambe kuwaimbira ng’oma.

Kalulu atayamba kuimba ng’omayo, nyama zonse

zinayamba kuthimbwidzika, nthawi yomweyo Njovu,

Mkango ndi Kadyamsonga, adangozindikira kuti

ayamba kumira m’nthaka ngati kuti ali pamadzi.

Pamene Kalulu anaona zimenezi analimikira kuimba

ng’oma ija. Apono ndiye zinthu zinavuta.

Njovu: Iwe Kalulu, tipulumutse, taona tikumira

munthaka.

Mkango: He! Kalulu, pepa, tipulumutse chonde

tikumira m’nthaka.

Kadyamsonga: Pepa! Pepa Kalulu, Kaluluuuu!

Tipulumutse chondeeee!

Mpandamachokero Anthology

301
Kalulu: Hehee! Ndiwedi bwenzi langa Nkhandwe!

Waziona mfitizi, zatha lero! Ndizionetsa polekera.

Nkhandwe: Imbitsa! Imbitsa! Imba m’bale wanga

akhaule amenewa!

Njovu: Mayo! Mayoooooo! Tikufa kunoooo! Kalulu,

ndakweza manja anga ndagonja!

Mafunso:

1. Mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Kalulu

anaitana nyama zija?

2. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti nyamazi

zimire munthaka?

3. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

302
Ubwenzi wa Njovu ndi Mkango

Kalekale kunkhalango yotchedwa Kambirira pafupi ndi

midzi ya m’dziko la Kabango kunali nyama ziwiri

zokondana kwambiri. Nyamazi zinali Mkango ndi

Njovu. Munkhalangoyi munalinso nyama zina zambiri.

Komabe Mkango nthawi zonse unkangokhala

wachisoni chifukwa unali wokalamba moti unkasowa

mphamvu zogwirira nyama. Nthawi zambiri

unkangokhalira kugona nayo njala chifukwa chosowa

chakudya. Mwamwayi unali ndi bwenzi lake Njovu.

Kawirikawiri Njovu inkapereka mphatso ya nyama kwa

Mkango.

Mkango unkatenga chitete m’mamawa kuli mbuu,

ulendo kukaba maungu m’minda ya anthu. Madzulo

unali ulendo kukapereka maunguwo kwa bwenzi lake

Njovu.

Mwatsoka, chaka china kunasowa mvula ndiye

zachisoni, kunali njala ya mtima bi. Tsiku lina Njovu

ndi Mkango anayamba kukambirana. Mkango unati,

“Bwanawe Njovu, ine masiku ano ana anga akufa ndi

njala. Pakadapanda iwe, tonse bwenzi tili mitembo.”

Koma zinthu zafika posauzana chifukwa

Mpandamachokero Anthology

303
chimkukuluzichi chagwedeza aliyense. Koma kaya

chaka chino tigwira mtengo wanji? “Pepa bwenzi

langa. Chimkukuluzi changati chimenechi ine

ndinachionaponso, ndikuganiza kuti pa nthawiyo

n’kuti iwe usanabadwe. Nthawi imeneyo agogo ako

ndidawaona akudya msipu. Ndipo atete anga

ndidawaona ndi maso angawa akudya nyama. Ndiye

zimene zatigwera chaka chinozi ndikuona kuti

zikulondola mapazi omwewo. Ayi, tiona mmene

zithere. Zikomo!” Inatero Njovu.

Atalekana aliyense anaona msana wa njira. Mkango

utayenda pang’ono unadzera njira yachidule yodutsa

m’tchire. Mwadzidzidzi utatulukira pena unangoona

chimunda cha maungu chili thee! Maungu ali

ngundangunda. Nthawi yomweyo unalankhula

chamumtima nuti, “Ndibwerere ndikauze bwenzi langa

kuti laponda diwa la mphawi, kuli maungu uku!”

Mkango unabwereradi ndi liwiro loopsa. Kenako,

unaona Njovu ikupita potero ndipo unati, “Eeeyi, Ima

pomwepo bwenzi langa ndakupezera maungu!”

Pamene Njovu inamva mawu amenewa inatembunuka

niti, “Kodi n’zoona zimenezo?” Kenako Njovu inayamba

ulendo wopita kumene kunali munda wa maungu

Mpandamachokero Anthology

304
kuja. Atafika pamtunda pamene amapenukira

kumatsitso kumene kunali munda kuja, Njovu inaona

kuti ndi zoona, nkhani ya maungu ija inalidi yoona

ndipo inati, “Zikomo ndithu bwenzi langa,

wandipulumutsa! Tsopano ndithamange liwiro loopsa

kuti ndikapeze mtendere, mundipeza.” Mosachedwa

Njovu inaliyatsa liwiro lothyola nalo mitengo.

Zachisoni pamene Njovu inafika pamunda paja inaona

kuti maungu onse anali owola kwambiri. Zitatero

m’maso mwa Njovu munayamba kulengeza misozi.

Pamene Mkango unkafika unadabwa kuti bwenzi lake

likulila ndipo unati: “Kodi bwenzi langa ukulira

chiyani?” Njovu inati, “Taona maungu aja ndi owola

okhaokha.” Mkango unati, “Aaaa, kodi ndizo

zachitika? Pepa kwambiri. Ili ndi tsoka. Mdani wathu

ndi amene wawoletsa maungu amenewa.”

Njovu inabwerera kwawo ili ndi njala ndiponso

chisoni. Ulendo uli mkati, Njovu inapeza Njati yakufa

ili gadaaa. Njovu inati ndikauza bwenzi langa kuti

ndamupezera mwayi.

Njovu inaliyala liwiro kuthamangira Mkango.

Posachedwa inafika nipeza Mkango utagona pansi

ukubuula ndi njala ndipo njovu inati, “Bwenzi langa

Mpandamachokero Anthology

305
dzuka, kodi watani?” Mkango unayankha kuti, “Pepa

bwenzi langa, ine ndinakomoka ndi njala. Tsopano

imfa yafika moti miyendo yanga ali m’kamwa mwa

ng’ona. Sindikhala ndi moyo ayi.” Njovu inati,

“Dzukani tsopano, ndakupezerani chinyama cha Njati

cha mafuta noninoni.”

Mkango utangomva mawuwa, unangoti, mbalanganda!

Kudzuka, ndipo unathamangira kumene kunali Njati

kuja. Utafika, unangopeza ntchentche zokha zili

m’matsekera zili ng’waaaa. Anthu auzimba

anaipezerera nyama ija, n’kutengeratu yonse. Njovu

inati, “Pepa bwenzi langa, ona mapazi a anthu awa.

Atenga nyama ija ife tili m’njira.”

Tsopano Mkango lilime lake linasololoka, dovu

n’kumangochucha ndipo kenako unagwa pansi

n’kukomoka. Posachedwa Njovu inayamba

kunjenjemera. Nayonso inagwa pansi n’kukomoka.

Kenako mumsewu munkadutsa chigulu cha anthu

ochokera kumsika. Anthuwa anali atatenga zitete

zodzaza ndi maungu, nyama, ufa, chimanga, dzombe

ndi zina. Chifukwa cha phokoso, Njovu ndi Mkango

zinatsitsimuka, tsopano anamva kuyankhula. Atautsa

mitu yawo, anaona kuti anthuwo anasenza zinthu

Mpandamachokero Anthology

306
zabwino zokhazokha. Njovu inati, “Bwanawe, tapeza

mwayi tsopano. Tisasauke ayi. Tikhalebe chogona

ngati tafa. Tikhoza kuwalanda zinthu atengazi.

Mkango unati, “Khala chete, tsopano mwayi wathu ndi

umenewu.”

Munthu wina anati, “Anzathu, onani Mkango ndi

Njovu zaphana! Lero tapeza mwayi, tiyeni titule

katunduyu kuti tichekerane nyama zakufazi.”

Anthu onse anatula pansi katundu wawo, nayamba

kuthamangira nyama zija. Mkango ndi Njovu,

zinadzukira pamodzi kuti, mbalanganda, mkango

umvekere, “Vuuu! Vuuu!” nayonse njovu imvekere,

“Kherrrr! Kherrr!” Anthu aja amvekere, “Mayo mayo

mayo ineeeeeee! Tikufa kunoooooo!”

Anthu aja atathawa, Njovu ndi Mkango zinakhala

pansi n’kuyamba kudya zimene anthuwo anasiya.

Mpandamachokero Anthology

307
Mafunso:

1. N’chiyani chikusonyeza kuti njala inali itafika

poipa kwambiri?

2. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Mkango ndi

Njovu zinali mabwenzi okondana kwambiri?

3. Kodi nyamazi zinatani kuti zipeze chakudya?

4. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

308
Kalulu Aphetsa Ana

M’dziko lotchedwa Fukizi munali munthu wina amene

anali wolimbikira kulima mtedza. Munthuyu dzina

lake anali Bikoko.

Mtedza utacha, Bikoko anaona mapazi anyama za

mtchire. Pambuyo, anaona kuti mtedza wake

unayamba kuwonongeka. Nyama zambiri zinali

kuwononga zokolola zake. Nyama zimene

zimawononga sankazidziwa kwenikweni. Motero,

anaganiza kuti akabisale kuti aone nyama zimene

zinali kuwononga zokolola zake. Bambo Bikoko

anakhala m’chisimba chake koma sanaone nyama

iliyonse.

Kalulu anangoti m’munda muja, tulukiru! Maso

mwazumwazu! Kenako anaona mwini munda ali

m’chisimba. Kalulu uja anayenda mochenjera kuopa

kuonedwa ndi mwini munda. Tsopano anatenda

dzungu n’kuliboola, iyeyo n’kulowa m’menemo ndi

kulivundikira bwino kuti wina aliyense asamuone.

Bambo Bikoko anatopa tsopano, ndipo anaganiza

zopita kumudzi kukapumula. Atangochoka, njovu

inafika nitola dzungu lija munali Kalulu, n’kumeza.

Mpandamachokero Anthology

309
Njovu ija ili kuyenda, Kalulu anazindikira kuti ali

m’mimba mwa Njovu ndipo anati, “Lero kuli phwando,

n’kutere zamkati kunona!” Kalulu anatulutsa mpeni

wake n’kudula mtima wa Njovu. Nthawi yomweyo

Njovu inagwa, n’kuferatu.

Tsopano Kalulu ataona kuti Njovu yafa, anatulukira

kukamwa kwake ndipo mosachedwa anatenga mpango

nayinjata nsangamutu.

Nthawi yomweyo Kalulu anaona anthu a uzimba ali

kupha ziwala. Kalulu anakwera pachulu nayamba

kukuwa nati: “He kodi imeneyo ndi nkhuli?” Anthu aja

anamuona Kalulu uja, nayamba kum’thamangitsa,

koma kalulu anazungulira chitsamba, n’kulowa

m’mimba mwa Njovu ija ndipo a uzimba aja atafika

pafupi ndi Njovu, Kalulu anayamba kubuwula. Anthu

aja anayifunsa Njovu ngati inaona Kalulu, koma Njovu

inati: “Pepani abale anga ine sindili bwino ayi. Litsipa

landivuta kwambiri.” Anthu aja anabwerera

osamuowona Kalulu, kenaka, Kalulu anatulukanso,

n’kukwera pachulu chija nati: “Nkhuliyo m’dambomo!”

Kalulu analowanso m’mimba mwa Njovu yakufa ija.

Tsopano anthu aja anatopa naye Kalulu ndipo

anaganiza zoika mlonda kuti aone chinsinsi cha

Mpandamachokero Anthology

310
Kalulu ndipo anaika mlonda pa chitsamba pafupi ndi

Njovu ija. Anthuwo atachoka, Kalulu anatulukanso

n’kukwera pachulu nati, “Nkhuliyo m’dambomo!”

Atatero anakalowanso m’mimba mwa Njovu ija,

mlonda uja akuona zonse zomwe zinkachitika.

Mlondayo anaona kuti polowa m’mimba mwa njovu

analowera pakamwa ndipo anamva Kaluu akubuula

m’mimba mwa Njovumo.

Mlonda uja anaubutsa ulendo kupita kwa anzake aja

nawauza kuti chinsinsi cha Kalulu chimene

anachipenya. Anaulula kuti Kalulu akumathawira

m’mimba mwa Njovu ndipo akumayamba kubuula,

kutiphimba m’maso kuti tiziti ndi Njovu ili kubuula.

Anzake aja anati, “Hi! Talekerera nyama!” Ndipo

ananyamuka n’kupita pamene panali nyama paja

mipeni ili m’manja kukayamba kucheka nyama ya

Njovu. Kalulu atamva kuti anthu aja ayamba kuicheka

Njovu ija, analimbikira kubuula: “Mayo ine! Ha!

Haaaaaaa! Litsipa ine. Litsipa ineee! Nditani inee!

Kandifunireni mankhwala anthu inu! Ndili ndi moyo

anzanga inuu.” Mlonda uja anati, “Bodza, bodza! Ndi

Chikalulu!”

Pamene Kalulu anamva mawu amenewa, basi

Mpandamachokero Anthology

311
anadziwa kuti zake zada. Tsopano anaganiza nzeru

ina. Iye anati, “Tsopano anthu amenewa anditulukira,

ine zimene ndichite, iwo asanandipeze, ndilowe

m’chifu cha Njovuchi.” Kalulu anabisala m’chifu cha

Njovu.

Anthu aja ataiboola Njovu ija m’mimba, anaona kuti

mulibe Kalulu. Bikoko mtsogoleri wawo anati, “Kodi

iwe mlonda, suja umanena kuti m’mimba mwa Njovuyi

muli Kalulu? Nanga ali kuti?” Mlondayo anati,

“Bwana, ntchito yopeza zinsinsi za Kalulu ikadalipo.

Ine ndapusa koma wopusa sadziwika. Uyu Kalulu

timamudziwa tonse.” Bikoko anati, “Chabwino, ine

udziwa ndimakonda chifu cha Njovu, chifukwa

mumakhala maungu ophikika bwino, chitenge upatse

mwana wanga Bwasano uyo, akapereke kwa amake

kuti akaphike.” Chifu chija anachitenga Bwasano

kupita nacho kumudzi.

Ali panjira, mwana uja anamva kuti chifu

chikuyankhula, “Taya! Taya! Fulumira tayaa!”

Bwasano atamva zotere, zinamudodometsa ndipo

anataya chifu chija n’kuyamba kuthawa.

Nthawi yomweyo Kalulu anatuluka, mwana uja

osadziwa, ndipo anathyola masamba a mtengo

Mpandamachokero Anthology

312
wotchedwa kafwito nasunga m’manja. Munthu

akangotafuna masambawa amagona tulo tofa nato

tsiku lathunthu. Kalulu anauza Bwasano kuti, “Bwera

kuno! Bwera kunooo!” Mnyamata uja anacheuka,

ndipo anabwerera.

Kalulu: Kodi umathawa chiyani?

Bwasano: Chifuchi chimayankhula.

Kalulu: Ayi wayamba misala iwe, tenga mankhwalawa

utafune m’kamwa mwakomo ndiye pafunika kuti

upumule, usayendenso ayi, tsopano lowa m’chifumo

ukakhale pansi, ine ndikunyamula. Ine ndine

sing’anga oposa onse. Lowa msanga!

Bwasano analowa m’chifu chija ndipo Kalulu

ananyamula chifucho ulendo kwa mkazi wa Bikoko.

Atayandikira, Kalulu anafunsira za nyumba ya a

Bikoko, ndipo anauzidwa mmene angakafikire

kunyumbako.

Atatulukira pamudzipo anaona nyumba imene inali

ndi chikwere cha nkhunda pabwalo ndiponso panali

mitengo itatu ya naphini, ndiyeno anati, “Monga muja

andiuzira anthu, nyumba ya Bikoko ndi imeneyi.”

Kalulu anaodira, “Odii! Odii!” Mayi onenepa aafupi

Mpandamachokero Anthology

313
koma oyera, atsitsi la nzindo anatulukira koma

nkhope ili yachisoni.

Kalulu: Kodi Mayi, ndinu amayi a kwawo kwa a

Bikoko?

Mayi: Eee!

Kalulu: Bwanji osakondwera ndi chimtengatenga

ndatengachi?

Mayi: Ayi a Kalulu, ine ndili pachisoni chachikulu.

Kuno kuli matenda banja lonse ngakhale inenso

m’thupimu simwanga ayi. Ana athu awiri Diroli ndi

Chisangwi onse ali gonire, moti a Bikoko ndiponso

Bwasano sakudziwa zimenezi. Ndangokhala ndekha,

ndiye ndangoti ndodo mtolo!

Kalulu: Pepani mayi koma limbikirani kuwafunira

zitsamba zonse zili m’tchirezi. Mayi ine ndatumidwa

ndi Bambo Bikoko kudzatula chimtengatengachi. Iwo

akuti mutenge chimtsuko chachikulu ndipo miyikemo

chifuchi osachidulayi. Akuti muli maungu awo ndipo

akufuna apsere m’chifu chomwechi. Anatero

malamulo awo a chifuchi. Ndiponso akuti mundiphere

nkhuku popeza ndanyamula chifu chawochi.

Mpandamachokero Anthology

314
Amayi aja msangamsanga chifu chija anachiika

m’chimphika chachikulu, naika pamoto. Anaphanso

nkhuku naika mumphika waung’ono. Nsima

inaphikidwa ndipo Kalulu anadya nsima ija ndi nyama

ya nkhukhu. Kalulu anasonkhanitsa mafupa onse

n’kusunga ali, “Chimapulumutsa munthu

sichidziwika.” Kenako anauza mayi aja kuti, “Pepani

mayi ine m’thupimu sindikumva bwino, ndimati

ndipemphe malo ogona.”

Nthawi yomweyo mayi uja anatenga nsalu yakuda

n’kumupatsa Kalulu nati, “Bwerani kuno mugone

pamodzi ndi Diroli ndi Chisangwi, iwe ugone pakatipo.

Mungogonera limodzi popeza mphasa yapadera palibe.

Ndadziwa wadwala chifukwa unanyamula katundu

wolemera kwambiri.”

Kalulu anagona pakati paja nafunda nsalu yakuda

koma Diroli ndi Chisangwi anafunda nsalu zoyera.

Amayi aja ali kusonkhezera mphika uja, chimoto chili

lilili! kuyaka, chimphika chija chili, bwata! bwata!

kubwatitsa chifu cha a Bikoko. Nthawi yomweyo a

Bikoko anafika ndipo anafunsa, “Kodi chifu chafika?”

“Zoona, chifu chafika ndi Kalulu,” anayankha motero

amayi aja. “Aa! Chafika ndi Kalulu! Kodi ine ngati

Mpandamachokero Anthology

315
ndinatuma Kalulu, ine ndinatuma Bwasano osati

Kalulu ayi,” anatero a Bikoko. “Hi! zanu izooo, Kalulu

ndiye wabweretsa.” Anayankha motero amayi. “Bwanji

waphika motere chifu changa? Kodi chifu amaphika

osafinya? Mkazi wosadziwa kuphika iwee!” Anazaza

motero a Bikoko. “Ndachita motsata malamulo anu,

anandiuza zimenezi ndi Kalulu,” anayankha motero

mayi aja.

Nthawi imeneyi Kalulu ankamva phokoso lija, tsopano

anasuntha malo, anagona kumbuyo kwa Chisangwi,

ndiye kuti Chisangwi, anali pakati tsopano, nsalu

anatenga yoyera ya Chisangwi ndipo Chisangwi

anamufunditsa yakuda ija ali, “Ee! Tione mmene

zikhalire.”

Bikoko: Tenga mpeni toboole chifuchi tichifinye, kuti

tiphikenso bwino.

Mkazi wa Bikoko: Kodi mukufuna kuona maungu

anuwo?

Bikoko: Maungu ati?

Mkazi wa Bikoko: Akuti muli maungu anu mmenemu

n’chifukwa chake mumati tiphike chotere.

Mpandamachokero Anthology

316
Bikoko: Amatero ndani?

Mkazi wa Bikoko: Inuyo! Kodi chifuchi ndimayesa

chachokera kwa inu? Nanga ine ndikadangochita za

m’mutu mwanga?

Bikoko: Zonse n’zabodza, Kaluluyo wapita kuti

ndimufunse.

Mkazi wa Bikoko: Wadwala, wagona pakati pa Diroli

ndi Chisangwi kuchipinda cha ana, wafunda nsalu

yakuda ija.

Bikoko: Phula mphika! Tenga mpeni ting’ambe,

tiphikenso titafinya.

Bikoko anatenga mpeni nang’amba chifu chija. “Ooo!

Mayo! Mayoo! Mwana wangaaa!” Anaona Bwasano

wophikika atafa kale. Amayi anafunsa, “Kodi

n’chiyani?” Bikoko anati: “Hii! Mwana wapsa! Waphika

Bwasano!” Bambo analira. Amayi anathamanga kuti

akaone, “Mayo! Mayo! Mayo! Nkhondoyoo!” Bikoko

anati, “Patse uta wanga! Lero naye akufanso!” Onse

analowa m’chipinda chija.

Mkazi wa Bikoko: Kalulu ndi uyo ali pakatiyo.

Mlaseni!

Mpandamachokero Anthology

317
Bikoko: Aona polekera lero, ndimukhomerera pansi

ndi muviwu!

Wodwala: Mayo atate mwandipha!

Tsopano Kalulu bzunthu! waliutsa liwiro.

Povundukula nsalu yakuda ija anaona ndi Chisangwi,

ali, thinuuu! thinuuu! kusauka ndi imfa. Bikoko anati,

“Hii! Ndapha mwanaa!” Waliyatsanso liwiro

kuthamangira Kalulu. Tsopano Kalulu anatsekula

liwori lake lomaliza agalu ali taaawaaa! Kalulu anaona

kuti zinthu zavuta popeza agalu ena anamubzola

ndikum’dulizira kutsogolo, Kalulu anatenga mafupa a

nkhuku aja n’kumawatayira, ndiye agaluwo

akadachedwa ndi kulimbirana mafupa iye anangoti

khophe! wapita. Nafenso tiyenera kuchenjera ndi

anthu a maonekedwe ngati a Kalulu.

Mafunso:

1. N’chifukwa chiyani Kalulu analowa m’kati mwa

dzungu?

2. Kodi anapezeka bwanji m’kati mwa chifu?

3. Kodi khalidwe lakeli linaphetsa bwanji ana?

4. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

318
Ubwenzi wa Kalulu ndi Fisi

M’dziko la Nsabwe, munali akazi awiri amene

ankafuna kukwatiwa ndi nyama zam’tchire. Adaganiza

zimenezi chifukwa akaziwa ankaona m’mene akazi

anzawo ankazunzidwira ndi amuna awo. Maina a

akaziwa anali Khumbo ndi Mtimaukanena.

Nyama zam’tchire zinamva za mbiriyi. Posakhalitsa

nyama zamitundumitundu zinayamba kubwera kwa

Nsabwe koma zambiri zinalephera mbeta za akazi

awiri aja. Tsiku lina a Njovu, a Njati ndi a Mkango

adapitira limodzi kukayesa nawo kufunsira mbeta zija.

Njovu: Kodi iwe Mtimaukanena, ine ukandiona,

umandiona bwanji? Sumandigomera? Kodi mwamuna

ukufunayo, amaposa ife a Njovu? Pofuna amuna

muzisankha ife amphamvu, a mangolomera.

Mtimaukanena: Pepani a Njovu. Mtima wanga

sunandiuze kuti ndikuvomereni ukwati ayi.

Njovu: Chabwino, tabwera iwe Khumbo, kodi

ndimayesa kuti mukufuna ife nyama zam’tchire,

tabweratu kwa ife a Njovu. Kodi simukukhutira nane?

Khumbo: Ayi a Njovu, mtima wanga sunakhumbe inu

Mpandamachokero Anthology

319
ayi.

Njovu: Atsikana awirinu, zedi mwataya mwayi, tsiku

ndi tsiku bwenzi mukudya maungu mukanalola ine.

Khumbo: Hoo! Zakuba m’minda mwa enizo! Toto ine

kukwatiwa ndi chimbala! Anthu ambiri anapunduka

chifukwa chakudya zotsirika. Toto ifee!

Tsopano a Njovu anatuluka nauza anzake aja kuti:

“Anzanga, tangovutika, anamwaliwa ndi okongola

koma ndi ovuta. Tangotaya nthawi pachabe kubwera

kuno.” A Mkango anati, “Ine sindingangobwerera

kunjira pokhapokha nane nditayesa mwayi wanga,

zichite kukakanikira komweko.”

Mkango: Odii atsikana, tabwera ife amunamuna, a

Mkango odya nyama tsiku ndi tsiku. Si za aja a Njovu

odya mawungu akuba ayi. A Mtimaukanena,

mukuganiza bwanji za ine? Bwanji ndinkhale

mwamuna wanu?

Mtimaukanena: Pepani a Mkango, mtima wanga za

inu sunanene kuti mukhale mwamuna wanga.

Mkango: Nanga iwe Khumbo? Ukuti bwanji?

Khumbo: Ayi, pepani, mtima wanga sunakukhumbeni

Mpandamachokero Anthology

320
mpang’ono pomwe.

A Mkango anapsa mtima ndipo anangotuluka

m’nyumba muja. Atafika kwa anzake anati,

“Anzanganu, basi tiyeni tizipita kwathu. Ukaona

mtengo wauwisi ukuyaka, nanga wouma n’kutani?

Kwenikweni inu ongodya msipu mumtsinje, ha!

Sangakuwerengereni n’komwe, akhoza

kukangokutukwananiko. Tiyeni tizipita.”

Mbiri inamveka m’mkhalango yonse kuti zinthu

zavuta. Onse akuluakulu atatu akanidwa ndi mbeta

mochititsa manyazi. Kalulu ndi Fisi anawawidwa

mtima. Tsiku lina Fisi ananyamuka kupita kwa akazi

aja.

Fisi: Zikomo! Zikomooo! Tafika ife amuna osaopa

mdima, oyenda usiku ndi usana. Ndabwera

kudzafunsira ukwati nonsenu, ndikufuna ndikhale ndi

akazi awiri. Nanga muli ndi mawu?

Mtimaukanena: Mtima wanga wanena kuti mwamuna

amene ndakhala ndikuyembekeza ndinu. Ndavomera!

Khumbo: Inenso, mtima wanga wafera inuyo basi! Inu

a Fisi ndiye taona kuti mukhale mwamuna wa ife

awiri.

Mpandamachokero Anthology

321
Fisi: Chabwino, ndikukatenga nkhoswe yanga kuti

tigwirizire chinkhoswe. Sindifuna ukwati wachabe,

wongotengana popanda chinkhoswe ngati amachitira

enawa.

Mbiri inamveka m’nkhalango monse kuti Fisi ndiye

amene waloledwa kukhala mwamuna wa akazi awiri

aja. Nyama zonse zinali zododoma popeza Fisi ndi

wakuba, wodya zoola komanso zakufa. Fisi atafika

kwa Kalulu, anafotokoza monga mmene zinayendera.

Kalulu anavomera kukhala nkhoswe ya Fisi.

Tsiku la Chinkhoswe lisanafike, Kalulu anangolawira

kuti akukasamba kumtsinje, koma unali ulendo

wopitakwa akazi aja. Atafika Kalulu anati, “Tamva kuti

mwalola Fisi kuti akhale mwamuna wanu nonsenu.

Akazi opanda nzeru ngati inu sindinawaonepo. Kodi

simudziwa kuti Fisi amadya zoola, zongofa zokha

komanso ndi wauve koopsa? Simudziwa kuti Fisi ndi

bulu wanga?”

Kalulu: Nanga inu mwafera chiyani? Fisi ndi mbala

yoopsa. Amachita mgoneko usiku ulionse. Mbuzi,

nkhumba za anthu zatha phu! Kuti apeze chakudya

chaufulu, ayi, ntchito ndi kuba m’midzimu. Amene uja

ndi bulu wanga. Kodi simukudziwa zimenezi?

Mpandamachokero Anthology

322
Khumbo: Ayi sitidamvepo. Koma inuyo mutitsimikizire

kuti a Fisi ndi bulu wanu. Mukachita zimenezo, ife

tidzasintha mtima ndipo tidzakwatiwa ndi inu a

Kalulu.

Kalulu anabwerera kwa bwenzi lake Fisi. Tsiku la

chinkhoswe linafika, ulendo unali mkati wopita kwa a

Nsabwe. Atatsala pang’ono kufika, anafika pamtsinje

wina. Kalulu anathamangira madzi a mumtsinjewo

n’kuyamba kumwa. Fisi anafunsa, “Kodi ukumwa

madzi nthawi zino bwanji?” Kalulu anayankha kuti,

“Ndiye kuti ndayamba kudwala m’bale wanga,

sindithanso kuyenda ayi. Pepa bwenzi langa,

tifulumire kukatula mbetayi ndiponso lero lomwe

tikagwirire ndithu chinkhoswe. Ine ndine nkhoswe

yako ya kuchimuna. Tsono miyendo yanga, yauma,

sinditha kuyenda. Iwe uyenera kundibereka pamsana

kuti tikafike msanga.”

Fisi anaberekadi Kalulu. Posakhalitsa onse anafika.

Koma atafika pafupi ndi akazi aja Kalulu anauka

n’kuimirira, ndipo anatenga ndodo yake amvekere,

thya! kukwapula a Fisi. “Yenda bulu wanga! Tiye chita

liwiro! Yenda bulu wangaa!” Kenako anayamba kuuza

mbeta zija kuti, “Suja ndidakuuzani madona kuti fisi

Mpandamachokero Anthology

323
ndi bulu wanga!”

Fisi atamva mawu amenewa anangolira, “Uwi!

Uuuuuuuuuuuuuwi! Kalulu ndizo udakonza

zimenezo, tenga akaziwo zako ziyende!” Atatero

anangoti patchire lowu, zii! wapita. Akazi aja anati,

“Zoonadi, a Kalulu samanamayi!” Ndiyeno Kalulu

anati, “Paja ndinakuuzani kuti fisi ndi bulu wanga!

Mwazionera nokhatu!”

Kalulu anakwatira akazi aja, Mtimaukanena ndi

Khumbo. Fisi ndi Kalulu anadana koopsa. Pakati

pawo panali chidani chosamwerana madzi kuopa

kuthirirana mankhwala.

Mafunso:

1. Kodi n’chifukwa chiyani akazi awiri amene

atchulidwa m’nkhaniyi ankafuna kukwatiwa ndi

nyama zakuthengo?

2. Kodi ndi ndani amene anakanidwa mochititsa

manyazi?

3. Nanga atsikanawa anavomera ndani?

4. Kodi Kalulu anachita chiyani pofuna kulanda

akaziwo?

Mpandamachokero Anthology

324
Kuunika ndi Mdima

Tsiku lina Kuunika ndi Mdima kunayamba

kukangana kuti adziwe amene anali wofunika

kwambiri pakati pawo. Kuunika kunayamba

kuyankhula modzigomera kumvekere, “Eee, ndine

patali, zinthu zonse zimasangalala ndikamawala ndipo

ndine wamphamvu zedi kuposa aliyense. Nditangoti

ndisawale kwa masiku angapo zomera zonse zikhoza

kufa. Anthu akhoza kumavala zovala zaziwisi komanso

kumangopunthwa akamayenda. Kodi anthu otsogola

ndi tekinoloje akanalowera kuti kukapala mphamvu

zoti aunikire midzi yawo. Kunena zoona palibe amene

angafikepo pamene ndinafika ine! Sindili ngati inuyo a

mdima. Kuda muli bii ngati makala, moti umadziwa

zoti pali munthu akatsokomola. Anthu alibe nawe

ntchito, n’chifukwa chake amapala moto kwa ine

n’kumaunikira usiku.” Mdima utamva chipongwe

chimenechi unapsa mtima ndipo unauza Kuwala kuti,

“Pakadapanda ine anthu sakanamaliza mkonono,

bwenzi anthu akumwalira ndi tulo. Akuba sakadapata

chawo chuma komanso Afisi akadavutika koopsa

chifukwa cha njala, nanga adakamatola bwanji

zowola. Iwe kuwala ndiwe woyerekedwa. Kodi sudziwa

Mpandamachokero Anthology

325
kuti anthu amadana nawe? Amati umawawaula,

kuwaononga maso komanso kuwayambitsira

matenda. Amakupherera ndi mwafuli, kuvala mandala

komanso ena amakana kuyenda iwe ukamawala.

Zikanakhala kuti ali ndi mphamvu zokuchotsa

paudindo bwenzi atakuchotsa kalekale chifukwa

anatopa nawe.” Kenako mkanganowo unafika povuta

moti mdima unati, “Tiyeko tipandane tione uyo ali

wadzitho komanso wofunika!” “Chabwino bwera

ndikuphofomole uone,” anatero Kuunika. “Iwe

Kuunika, undipeze madzulo kuti ndidzakuchotse

chimbenene! Panopa ndikufuna ndithandize anthu

kuti apeze ufulu wochita zomwe akufuna.

Umawaphera anthu ufulu iwe! Udzamangidwatu,

zoona ungamayalutse anthu olemekezeka!”

“Chabwino, ndibwera!”

Madzulo, Mdima unadikira mpaka kutopa, koma

kuwala sikunatulukire. Unkangoyang’anira kunjira

maso ali psuu! Tsiku lotsatira Kuwala nakonso

kunadikira mpaka madzulo moti nakonso maso

anafiiriratu psuu, koma sunaone mnzake akubwera.

Usiku unayamba kudzitama umvekere, “Amati atani

Kuunika kapolo? Akuchita mantha kuopa

Mpandamachokero Anthology

326
kupandidwa!” Masana nakonso Kuunika kunayamba

kudzitama kumvekere, “Amati achite chiyani kapolo

amene uja Mdima, wandiopatu!”

Tsiku lina atakumana, ndewu inayamba masanasana.

Nthawi ya madzulo, Kuunika kunagonja n’kugwera

pansi kwalaaa! Mdima utaona zimenezi unati,

“Heheeeedeee! Umati uchite chiyani kamwana iwee!”

Pakati pa usiku, ndewu inabadwa, nthawi ya m’mawa

usiku unagonja. Nakonso kuunika kunayamba

kuseka, “Pwitipwitipwiti! Umati uchite chiyani mwana

woonekera matumbo iwee! Pamenepa mpamene

panayambira udani wawo. Kuunika kunadziwa kuti

mwamuna mnzako mpachulu. Mdima nawonso

unaona kuti mnzakeyo mpachulunso, moti mdima

unkati ukaona kuwala akubwera poteropo, unkachoka

n’kupita kwina. Nakonso kuunika kukaona kuti

Mdima ukubwera, kunkasintha njira kapena

kubwerera kwawo kukagona.

Mpandamachokero Anthology

327
Mafunso:

1. Kodi pakati pa kuunika ndi mdima, chofunika

kwambiri ndi chiyani?

2. Kodi ndi pati pamene panayambira udani wa

kuunika ndi kuwala?

Mpandamachokero Anthology

328
Nzeru za Kalulu

M’nkhalango yotchedwa Ngwangwa m’dziko la Fukuto,

munali nyama zosiyanasiyana. Chaka china mvula

inakanika kugwa moti madzi ankasowa. Mkati mwa

m’nkhalango ya Ngwangwa munali chitsime chimodzi

chokha. Mwachidule tingati chitsimechi chimadziwika

ndi dzina loti Mzizime. Chinali chitsime chamadzi

okoma, ozizira bwino komanso ochotsa chipemba.

Nyama zonse zinkapita kuchitsimechi kukamwa

madzi. Nthawi zina zinkapezeka kuti chitsimechi

chaphwa. Pofufuza, nyama zonse zinatsimikiza kuti

anyani ndi amene ankaphwetsa chitsimecho chifukwa

ankamwa madzi moipa kwambiri. Zitatero, Njovu

inaitanitsa nyama zonse kuti zidzamve malamulo a

chitsime cha Mzizime. “Ndati ndinene pano kuti

anyani asiye kumwa nawo madzi a pachitsime

chathuchi. Ndamva zoti anyaniwa ndi amene

akumaliza madzi pachitsimechi. Choncho kuyambira

lero, muonetsetse kuti anyani asamabwere kuno

kudzamwa madzi! Nkhani imene ndinakuitanirani ndi

imeneyi.”

Njovu inapitiriza kunena kuti, “Iwe Mvuwu, Mbidzi,

Mkango, Kadyamsonga ndi Nyamalikiti, imwani

Mpandamachokero Anthology

329
madziwa tsopano tizipita. Koma muonetsetse kuti

nyani asadzaoneke pachitsimechi. Amene adzagwire

mbala zikuba madziwa, ndithu adzalandira mphoto

yaikulu. Ine sindisamala za ufumu wanga ayi. Amene

adzagwire mbala ikuba madziwa adzapatsidwa ufumu

wangawu.”

Kalulu anaimirira n’kunena kuti, “Ine mfumu ndili ndi

njira yogwirira mbala imeneyi. Mundipatse nthawi.

Mawa nyama zonse zisabwere kuchitsime kuno.

Nyama zonse zibwere mkuja, mawa zitsotse osamwa

madzi. Mkuja, nyama zonse zidzapeza mbala imene

ikuba madzi a mu Mzizime. Nonse mudzabwere

kudzaona mbalayo.” Nyama zonse zitamva mawu a

Kalulu, zinakondwera ndipo nkhawa zawo zinayamba

kuchepa.

Kalulu atachoka apo, anatenga nkhwangwa n’kulowa

m’tchire. Atatero, anapeza mtengo ndipo anasema

chifanizo cha munthu. Anatenganso phula la njuchi

ndi ulimbo n’kuyamba kumata thupi lonse la chosema

chija. Atatha, anachinyamula n’kupita nacho

pachitsime chija. Atafika, anatenga chifanizirocho

n’kuchikumbira pansi kuti chiime chilili ngati

munthu.

Mpandamachokero Anthology

330
Atamaliza kuchita zimenezi, Kalulu anapita kwa

bwenzi lake Nyani ndipo anamuuza kuti, “Bwenzi

langa, kodi dzulo unali kuti?” Nyani anayankkha kuti,

“Bwanawe, ine dzulo pamodzi ndi banja langali,

tinakaba madzi kuchitsime china pafupi pomwepa. Ife

satiloleza kumwa madzi kumeneko chifukwa timati

tikapita, chitsime chonse timachiphwetsa. Moti

anatiletsa kuti tisadzamwenso madzi pachitsimecho.”

Kalulu anauza Nyani kuti, “Bwenzi langa, ine

ndabwera kudzakuchenjeza. Nyama zonse zaika

mlonda kuchitsime chija. Mlondayo amafa msanga

akamumenya kumsana kwake. Iwe mawa upite ndi

banja lako kukamwa madzi. Ukasamale kuti mlondayo

asakakupenye. Ndiye ukatulukire kumbuyo kwake

ndipo usakaponde masamba ouma kuti mlondayo

asakamve mtswatswa wako. Ukakafika kalimbe

mtima, ukalikutumule khofi n’kumenya mlondayo,

ukaona kuti nthawi yomweyo akafa. Uvutikirenji ndi

ludzu ngati umachita kufuna kuti uzimwa madzi

ambiri, si ndi mmene unabadwira! Ukakachipanda

khofi, ukachipondenso ndi mwendo mwamphamvu,

ukaona kuti nthawi yomweyo chafa ndipo iwe ukamwa

madzi mtima uli zii.”

Mpandamachokero Anthology

331
Nyani atamva izi anati, “Zikomo bwenzi langa. Wachita

bwino kundipangira nzeru yotereyi, nanga tife ndi

ludzu chitsime chilipo?” M’mawa kwambiri Nyani

pamodzi ndi banja lake analawirira kuchitsime chija.

Atafika pafupi nyani anabanika nalo khofi.

Anatambasula dzanja lamanja ndipo analikutumula

khofi, limvekere m’mutu mwa mlonda uja kuti phwaa!

Pamene nyani ankati achotse dzanja, zachosoni,

linakanirira. Analiponyanso lamanzere khofi kuti

phwaa! Zachisoni linakaniriranso. Tsopano

anamuponda mlonda ndi miyendo yonse iwiri,

zachisoni, miyendo yonse inakanirira. Tsopano nyani

anayankhula, “Aaaa! Koma iwe uli ndi chipongwe eti?

Bwanji ukugwira dzanja langa? Tandisiya msanga!

Ndati undisiye iweee! Kodi sukumvaaaaaaa? Eeee?”

Nthawi yomweyo kunamveka kulira kwa nyama,

nyamazo zimabwera kuchitsimeko kudzamwa madzi!

Kalulu anali m’gulu la nyamazi. Kalulu anati, “A

Njovu, taonani mbala ija iyoooo! yagwidwa. Ine

ndangochepa msinkhu koma taonani mmene

ndagwirira kapolo wanuyooo!” Nyama zonse

zinathamanga, n’kugwira wakubayo. Posakhalitsa,

Njovu inaveka Kalulu ufumu ndipo inati, “Ufumu ndi

Mpandamachokero Anthology

332
wako chifukwa cha nzeru zako!”

Mafunso:

1. N’chifukwa chiyani Njovu inaitanitsa

msonkhano?

2. Kodi anyani analakwa chiyani kuti awakanize

kumwa madzi a pachitsime chija?

3. Nanga n’chifukwa chiyani Kalulu anapusitsa

Nyani?

4. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

333
Phwando la Kalulu ndi Fulu

Kalekalelo, Kalulu ankakonda kutchera misampha.

Nthawi zambiri iye ankati akagwira nyama,

ankagawirako bwenzi la pamtima Fulu. Ankachita

zimenezi akamachoka kowonjola nyama zomwe

zinakodwa m’misampha yake.

Pa nthawiyo, Njovu ndi Mvuwu zinali paubwenzi

wobwerekana nsalu. Kumene kunali Njovu, a Mvuwu

ankapezekanso komweko. Kangapo konse a Ng’ona

anauzapo onsewa kuti, “Koma anzanga inu, ubwenzi

wotere n’ngoipa. Bwanji simumafuna kutayana? Kodi

simudziwa kuti mukadzakumana ndi ngozi mudzafera

pamodzi?” “Hahaha! Mwana iwe ukuti chiyani?

Akuluakulu ngati ife chingationekere n’chiyani?

Sukudziwa kuti ife ndife mphangala zokhazokha?”

anatero Njovu poyankha a Ng’ona. “Kodi mwana iwe,

aliponso wina woposa ife pa mphamvu? Sudziwa eti?”

Anafunsa chotero a Mvuwu.

Tsiku lina Kalulu akuyendera misampha yake, anaona

mapazi a Njovu ndi Mvuwu. Mumtima mwake ali,

“Agalu amenewa tsiku lina tidzaonana. Amenewa ndi

amene akumaba nyama m’misampha yanga, mbala

Mpandamachokero Anthology

334
zakuba!”

Kalulu atabwerera anafika kwa Fulu ali, “Bwenzi langa

pepa, lerotu udyera therere. Mbala zikungoba nyama

zanga m’misampha. Ndikukhulupirira kuti ndi Njovu

ndi Mvuwu, ndaonera mapazi awo. Ndikadakhala ndi

chingwe cholimba ndikadawatchera msampha,

ndikanawaonetsa malodza.” Fulu anati, “Bwenzi langa,

khala chete, ine ndili ndi chingwe chachitali cha

nsambo zopota. Dikira ndikupatse. Ife tikufuna

kumadya nyama tsiku ndi tsiku ndiye sitingalole agalu

amenewa aziba nyama zako ayi.”

M’mawa mwake, Kalulu anatenga chingwe chija

n’kupita nacho pampita wa Njovu ndi Mvuwu.

Atasunzumira potero, anaona Njovu ndi Mvuwu

zikubwera. Kalulu anatenga chingwecho nachinjatirira

ku muzu wa mtengo waukulu umene udatemedwa

ndipo nayenso anachita ngati wadzinjata.

Njovu ndi Mvuwu zitafika zinati, “Oooooooo! watani

mnzathu woyenda?” Kalulu ali “Heeee!

Sindingakuuzeni chifukwa sindifuna kuti anthu ena

akumane ndi zimene ndikukumana nazo ine pano

chifukwa tingachuluke. Komabe poti tonsefe ndife a

mliyenda m’tchire muno, inu nokha ndikuuzani. Koma

Mpandamachokero Anthology

335
mulonjeze kuti simuuza wina ayi!” “Kodi ife umatiyesa

ana eti? Suona mathunthuwa kodi? Tatiuza,

sitikanena kwa aliyense!” anatero Njovu.

Tsopano Kalulu anati, “Monga mwaonera kuti chingwe

chansambo za mkuwa simunachione, chingwe

chimenechi chimapatsa mphamvu, kapena kuti

mangolomera. Mwakuti inu nonsenu kuyambira lero

simungandichite kanthu ayi, mwachepa!” “Aaaaaaa!

Ukuti chiyani?” anafunsa Mvuwu.

“Kodi simukumva? Inu nonsenu pa mphamvu, osati

msinkhu ayi, mwachepa ndipo ndinu makanda

ang’onoang’ono osamera ndi mano omwe! Kapena

ndinene kuti ndinu nthumbidwa!” anatero Kalulu.

Kalulu anapitiriza kunena kuti, “Ngati mukuchita

makani, mawa tiyesane. Inu awiri mugwire chingwe

cha nsambochi mukhale kuseri kwa kaphiri aka, ine

ndikakhala kuseri kwa Phiri ilo. Nonsenu pamodzi

mukakoke chingwechi kuti muone zimene zichitike.”

Njovu inati, “Ha! Ndikangokusiyira Mvuwuyu basi,

akathane nawe. Mwana wakhanda ungachite chiyani

ndi mapiri ngati ano? Taona, kunotu ndi kugomo osati

masewera ukuchita apawa.” Anatero a Njovu

podzitamandira.

Mpandamachokero Anthology

336
M’mawa kutacha, onse anakumana pa kaphiri

kotchedwa Talala. Chingwe cha mkuwa chija

chinayalidwa kuseri ndi kuseri kwa phirilo. Fulu

patsiku limeneli anabwera kudzawonerera

mpikisanowo ndiponso anasankhidwa kukhala

wolamulira mpikisanowo. Kalulu anatenga chingwe

chija nachinjatirira kumtengo waukulu wa mlambe.

Tsopano poyamba, a Njovu anasiyira a Mvuwu okha

kuti akokane ndi Kalulu.

Fulu analamulira motere, “Tsopano aliyense agwire

chingwe! Konzekani, kokaaaaaaa!” Zimene zinaoneka

pamenepo zinali zoopsa. Mvuwu idayesa kuchita

kakalakakala koma inaona kuti Kalulu ali nju! “Pepa

mnzanga Njovu. Nkhondo yakula, Kalulu ujadi ali ndi

mphamvu.” Anayesanso ndithu ndi mphamvu zake

zonse koma Kalulu anali nju! osasunthika. Kenako

Mvuwu inati, “Achimwene a Njovu, tiyeni tithandizane!

Mmenemo Fulu ali, “Koka! Kokaaa!” Pamenepo n’kuti

mbali imene kunali Njovu ndi Mvuwu, mitengo

itawandikawandika, ina itathyokeratu, miyala

inkangogubuduzikagubuduzika, fumbi lili kobooo!

Nthawi imeneyi, Kalulu n’kuti atangokhala pamwala

ali neng’a, akusuta fodya ali phee. A Njovu anayesetsa

Mpandamachokero Anthology

337
kukoka koma kenaka anayamba kumangodzigwera

okhaokha, kenaka kumangogwerana ndi a Mvuwu,

Njovu itaona kuti zavuta inati, “Aaa! Koma n’zoonadi

Kalulu lero kutichititsa manyazi chotere! Mnzanga

Mvuwu, tiyeko tigonje timunyengerere kuti nafenso

atigawireko mphamvu zakezo!”

Tsopano Njovu ndi Mvuwu anakweza manja awo

m’mwamba kusonyeza kugonja. Fulu analamula,

“Chingwe pansi! Yagonja Njovu ndi Mvuwu! Kalulu

wapambanaaa!” Nthawi yomweyo Kalulu anamasula

chingwe chija n’kuchitaya pansi. Onse tsopano

anakwera pamwamba pa phiri la Talala ndipo

atakumana, a Njovu anati, “Aaa! Iwe Kalulu

takhulupirira zija umanenazi. Tsopano madodafe

ndithu tikhale opanda mphamvu? Ayi usatero,

utipatseko mphamvu zakozi!” Kalulu anati, “Tiyeni

nthawi yomwe ino pamalo pompaja kuti

ndikakunjateni. Inu a Njovu tinjata chitamba

chanuchi. Inu a Mvuwu tikunjatani miyendo yanuyi.”

Atatha kuwanjata, Kalulu anawatembenukira

amvekere: “Mwafa lero mafana! Mwafa lero! Mbala inu

mwakhala mukundibera nyama zanga!” Njovu inati,

“Hiii! Tikufa!” Mvuwunso ili, “Mayooo! Tikufa!” Ndiyetu

Mpandamachokero Anthology

338
panali matatalazi. Tsoka ilonso anali atatopa kale

chifukwa cha mpikisano uja. Ndiyetu a Njovu

amvekere khuu! kugwa, nawonso a Mvuwu, khuu!

Kugwa chagada!

Nthawi yomweyo Kalulu anathamanga kukasokolotsa

ana ake amene anawabisa, mpeni uli kumanja ali,

“Lero kuli chiphwando cha nyama yokhayokha.” Fulu

naye ali, “Ine ndiyambira kuchekako Njovuyi. Lero kuli

chiphwando chosasunsa.” Kalulu ndi ana ake pamodzi

ndi Fulu anapanga chiphwando chadzaoneni ndipo

anadya a Njovu ndi a Mvuwu.

Mafunso

1. Kodi ndi ndani ankaba nyama za Kalulu?

2. Kodi chingwe cha mkuwa chinapatsadi

mphamvu Kalulu?

3. N’chifukwa chiyani Njovu ndi Mvuwu

zinagonja?

Mpandamachokero Anthology

339
Chimene Kalulu Amagonera Diso Lili

Tong’o!

Tsiku lina Kalulu akuongola miyendo m’malunje

anamva phokoso la nyama zomwe zinkaoneka kuti

zinali pa chimsonkhano m’nkhalango yotchedwa

Thuma. Pamene Kalulu anaima, anamva dzina lake

likutamulidwa. Iye anadabwa popeza sanalandire

mthenga wa msonkhano wotere. Kenaka anamva

mawu onena za kuuma kwa mitengo ndi udzu. Chaka

chimenecho mvula inapenga moti kunja kudali gwa

chifukwa cha chilala. Udzu, mitengo komanso zomera

zonse zinaumiratu. Chakudya cha nyama zonse

chinkasowa moti m’masiku amenewo nyama

zinkangodya dothi la mdambo. Nyamazi zinkatchula

malo angati amenewa kuti Phukuto.

Kalulu anayamba kupenekera kuti cholinga cha

msonkhanowo chinali kukambirana za njala imene

inali m’kamwam’kamwa. Kalulu anasendera pafupi

ndithu ndipo anadabwa atangoona nyama

zowerengeka zokha, popeza zinali pobisalika. Mawu a

Njovu anali kumveka kuti, “Anzanga nonse mwabwera

pano, njala ndimeneyi. Njala yopanda pothawira yotere

Mpandamachokero Anthology

340
timaitcha chinkukuluzi. Koma ife bwanji kamwana

kaja kamati ndi mfumuka palibe? Ka Kalulu

kameneka ine ndimati ufumu wake uthe lero. Bwanji

sabwera pamavuto ngati awa? Ine ndinam’tumira

mthenga, koma onani sanabwere. N’chifukwa chaketu

ine ndikuti ufumu wake watha lero! Nanga inu

mukuganiza bwanji?” “Indeee! Tiyeni tipungure ufumu

wakewo kuti aone polekera,” nyama zonse zinatero

mwa mabvume.

Zonse ankanena Njovu zoti adatuma mthenga kwa

Kalulu, linali bodza lofuka utsi. Njovu inachita izi

potengera chidani chakale. Inachita dala kuti Kalulu

atsike pampando. Kenako kunatulukira chimoto

chimene anthu a liwamba anatentha, ndipo Kalulu

ataona motowo zinamuvuta popeza motowo

unkalunjika pamene iye anabisala.

Kalulu nzeru zinamuthera popeza amafuna kumva

zonse zimene ankambirana makamaka zothetsa

ufumu wake wa zaka zambiri m’nkhalangomo. Kalulu

anangothawira kunyumba kwake kuti akayambe

wapeza nzeru zina.

Mmawa kutacha Kalulu anatuma mthenga kwa

bwenzi lake Nyani, kuti awonjezere nzeru chifukwa

Mpandamachokero Anthology

341
mumtima adati, “Nzeru umati n’za mnzako si za

wekha. Mutu umodzi susenza tsindwi. Safunsa adadya

phula. Nzeru zayekha adaviika nsima padziwe. Nyama

ya liuma inafa ndi ludzu. Dombolo n’kuwombolana.

Ndiye ine ndiyenera kufunsira nzeru kwa bwenzi

langa.”

Nyani asanafike, Kalulu anaika mphika pamoto

kuphika zikhawo zosakaniza ndi bowa, chifukwa

mkazi ake anali akudwala. “Odii! Odii kumeneko!”

Mawu anamveka. “Lowani,” anatero Kalulu. “Oooo!

Kodi ndi bwenzi langa Nyani! Khala pachitsapa.

Pepatu wandipeza ndikuphika. Alamu ako sakupeza

bwino ayi. Chibayo chidangowati thi! Moti ali

dathidathi! Ndiye n’chifukwa chaketu wandipeza

ndikuphika,” anatero Kalulu. “Pepa mbale wanga!”

anayankha motero Nyani.

“Ndakuitana ndine bwenzi langa,” anayamba nkhani

motero Kalulu. “Kodi kumsonkhano dzulo lija kunali

zotani? Ine sadanditumire mthenga wondidziwitsa.”

“Ehe! Kodi waiwala, pajatu ife awiri ndife odedwa,

inenso sadandiitane. Ndidangomva akuti a Njovu

akuchotserani ufumu. Koma usade nkhawa mawa

ndibwera ndi mankhwala. Malo ako ano

Mpandamachokero Anthology

342
ndidzakonzakonza moti mitengo yonseyi ikhala ya

biriwiri! Udzu onse wawumawu ukhalanso uli

biriwiriwiri! Nyama zonse, zidzakukhumbira kwambiri

n’chifukwa chake nditadzaikemo chinjoka kuti

chizidzaluma nyama zakuba n’kufera pomwepo. Mbali

iyo, ndi mankhwala omwewo, tibowola kasupe wa

madzi ozizira bwino.”

Atamaliza kudya chakudya chawo, Nyani anatsanzika

n’kunyamuka kumapita kwawo. M’mawa kutacha

Nyani anabwera ndi mankhwala ake amene

anawatchula dzina loti Nkhonkha. Atachita

mankhwala aja, panatuluka chinsipu chobiriwira,

mitengo ya zipatso, ndipo madzi anabowoledwa moti

ankangoti popopo!

Mbiri ya mudzi wa Kalulu inamveka ndipo nyama

zambiri zinkabwera kudzaona zodabwitsa ndi

zachilendozo.

Njati: Odii a Kalulu! Tadzaona zozizwitsazi! Zatheka

bwanji?

Kalulu: Ngakhale munathetsa ufumu wanga, koma

mukufa ndi njala!

Njati: Ngati ndine! Ee! Ndi a Njovutu omwe

Mpandamachokero Anthology

343
mukulimbirana nawo ufumuwo!

Mbidzi: Pepa Kalulu ndimwe nawo madzi ndingafe ndi

ludzu!

Nyama zonse zimene zidakaona mudzi wa Kalulu

zinayamba kunyoza mawu amene ananena a Njovu oti

Kalulu ufumu uthe. Njovu atamva zimenezi anachita

manyazi popeza sankalandiranso ngakhale moni kwa

nyama iliyonse.

Nyama zonse tsopano zinaona kuti Kalulu ngakhale

ufumu unamuchokera, koma anali wosangalala

popeza anali kumwa ndi kudya bwino. Mkango ndi

Mvuwu onse anapangana kuti aitanitse msonkhano.

Nyama zonse pamodzi ndi Njovu zinabwera

kudzakambirana za mavuto awo. Potsiriza anaganiza

kuti onse apite kwa Kalulu kukapepesa ndi kufunsira

nzeru kuti dziko libwerere msipu wosilirika ndi

mitengo yobiriwira pamodzi ndi madzi.

Atafika kwa Kalulu, nyama zonse zinanena mavuto

awo mwatsatanetsatane.

Mkango: Bwana Kalulu, ife tabwera kuti

tidzakupepeseni. Tinakulakwirani zedi. Chimunthu

china chachikulu khutu, chidatilakwitsa. Inu ufumu

Mpandamachokero Anthology

344
wanu udalipoooo!

Nyama zonse: Eeee! Indediii! Zoonaaa!

Mkango: Bwana Kalulu, ife ana anu tikomereni mtima

potikonzera nkhalango yathuyi. Taonani madzi

mulibe, msipu mulibe komanso mitengo yayiwisi

mulibe.

Kalulu: Dzikoli silikonzeka! Ngati mukufuna kuti

likonzeke aliyense akaphe amake. Kenako mubwere

kuno mukabwere ndi mitu yawo kuti tidzakonzere

mankhwala! Zamvekaa?

Nyama zonse: Indeeeee! Mawa ife tibwera nayo

mituyo!

Kalulu: Ine kuti ndipeze mukuzionazi ndinayamba

ndapha mayi anga, n’chifukwa chake lero ndili

pabwino!

Nyama zonse zinabalalika kukapha amayi awo

n’kuwadula mitu. Mitu ija isadabwere, Kalulu

ananyamula mayi ake usiku n’kukawabisa mumtengo

mbali ina ya tchire m’nkhalango ya Thuma.

Tsopano m’mawa kutacha, nyama zonse zinabwera

ndi mitu ija. Kalulu anaunjika mituyo n’kuika nkhuni

Mpandamachokero Anthology

345
pamwamba pake ndipo anaitentha mpaka inasanduka

phulusa lokhalokha. Kenako Kalulu anati, “Eyaaa!

Ntchito yanga ndayamba tsopano, pitani kwanu.

Mukhoza kumwa nawo madzi angawa, mukhozanso

kudya msipuwu ndi chilichonse chimene mungakonde

musanapite kwanu!” Nyama zija zinayamba

kulimbirana makamaka zikhawo za dinde, chinkhwisi,

ndekera, nthochi ndi zina zotero.”

Patapita masiku atatu nyama zija zinabweranso

kudzafunsa ngati panali mwayi uja adalonjeza Kalulu.

Kalulu anangowauza kuti phulusa la mitu lija

likugwira ntchito. Anawauzanso kuti, “Tsopano dzikoli

lili pafupi kukonzeka. Koma phulusa la mitu ija

lachepa. Mvula ndi madzi ndimakapempha kwa Azimu

a m’nkhalango ino, ndiwo amene afuna phulusa lina,

lijali lachepa. Tsopano Azimuwo akufuna phulusa lina

la mitu ya atate anu. Motero katengeni mitu ya atate

anu kuti tidzasakanize pamodzi. Zikatero posachedwa

mudzalandira zonse. Dziko lino la Thuma

sikudzakhalanso mavuto ngati amenewa.”

Nyama zonse zinapita n’kukapha atate awo

n’kubweretsa mitu yonse kwa Kalulu. Kalulu anaotcha

mitu ija n’kutenga phulusa. Nyama zija zinapita

Mpandamachokero Anthology

346
Kalulu ananyamula atate ake n’kukawabisa kumalo

kuja anabisa mayi ake. Pamene amachoka kumeneko,

nyama zina zinamuona ndipo zinadodoma popeza

anatenga nsengwa zodyera chakudya.

Kenaka patatha sabata, nyama zonse zija

zinabweranso kwa Kalulu. Kalulu anati, “Zoona

anzanga muli m’mavuto, koma ndinapita kuphanga

kumene kukhala Azimu. Phulusa lija ndinapereka

koma Azimuwo akuti phulusa lija lachepa m’pofunika

kuwonjezera lina la ana anu oyamba, achisamba.

Mukatero sabata lamawa mulandira mvula ndi zonse

zimene mukufuna.”

Nyama zija zitamva mawu amenewa zinayamba

kukhumudwa mumtima, zambiri zinayamba

kung’ung’udza zimvekere, “Anzathu, izitu tipwetekeka

nazo. Kodi tikathanso mtundu umene madziwo

tidzamwa ndi ndani? Taonani umo taphera anthumu!

Zabodza, Kalulu akufuna tithane tokha. Kodi

simunamudziwebe Kalulu? Akhozatu kukhala

akuponya nkhondo ndi ife mobisalira ife osadziwa.

Tiyeni tichenjere!”

Mmawa, nyama zonse zinabwera ndi mitu ya ana awo

achisamba. Kalulu anatenga mitu ija n’kuiotcha ndipo

Mpandamachokero Anthology

347
anatenga phulusa lija. Patapita masiku awiri, nyama

zonse zinabwera. Kalulu anati, “Ine ndabwera

posachedwa kwa Azimu kuja. Phulusa lija ndapereka,

koma akuti pakufunika kuwonjezeranso lina kuti

tsopano likwane bwino n’cholinga choti mvula ibwere

yoopsa, yamkokomo wa madzi. Motero mawa mubwere

ndi mitu ya zitsitsa misepa zanu. Mufulumire!”

Nyama zonse tsopano zinadodoma, zina zinakwiya

koopsa. Fulu, Nkhandwe ndi Fisi anasankhidwa kuti

akhale maso a nyama zonse. Udindo umene anali

nawo ndi kubisalira Kalulu kuti aone mayendedwe ake

chifukwa zochita za Kalulu zinayamba kuwatayitsa

mtima.

Nyama zonse zikupita kwawo, Kalulu analowa

m’nyumba natulukamo ndi phukusi la masamba a

mtengo wa msuku. Waliutsa liwiro kulowera kutchire.

Fisi, Nkhandwe ndi Fulu, analiutsanso lawo liwiro

kumutsatira. Atakweza maso, anaona Kalulu wagwira

chingwe ali kukwera mumtengo, Fulu anati, “Anzanga

mukuona zimene Kalulu akuchita?”

Fisi: Kodi Kaluluyu ndizo amachita?

Nkhandwe: Kodi n’kukhala chiyani chimenechi?

Mpandamachokero Anthology

348
Fulu: Bwino wosakweza mawu angatimve.

Pamene Kalulu anafika patsinde la mtengo, anayamba

kuimba kanyimbo namati, “Mayi! Mayi! Tayire

kachingwe! Mayi! Mayi! Tayire kachingwe!”

Tsopono anangoona chingwe kuchokera m’mwamba

kuti sololokuu! Pansi khwa! Kalulu gwi! Lendee!

kukwera mumtengo. Kalulu atatsika anapita

kunyumba. Fisi anapita patsinde la mtengo uja

nayambanso kuyimba, “Mayi! Mayi! Tayire kachingwe!

Mayi! Mayi! Tayire kachingwe!”

Posakhalitsa anaona chingwe chija kuti, sololokuu!

Pansi chimvekere khwa! Fisi gwi! Lendee! mpaka

anakafika m’mwamba muja kalakatu! Pamene amayi

ndi atate a Kalulu anaona chilombo Fisi, analira,

“Mayo! Mayoo!” Fisi ali “Mwafa lero! Mwafa lero!”

Zitatero, Fisi ndi Nkhandwe anadula mitu ya awiriwa

ndipo anatsika n’kupita kumene kunali nyama zina

zija.

Atafika Fisi anati, “Anzathu, tachita ntchito imene

munatipatsa. Onani mitu iwiri iyi. Kalulu anabisa

amake ndi atate ake kutchire m’mwamba. Ife

tinamulondola, n’kubisala. Posakhalitsa tinaona

Mpandamachokero Anthology

349
chingwe chili kuchoka m’mwamba. Iye atagwira

chingwecho taona wakwera m’mwamba muja. Atatsika

ifenso tinayimba kanyimbo kakeko ndipo tinangoona

chatsika chingwe, ifenso pogwira, taona takwera

m’mwamba muja. Poti tione, taona ndi amake ndi

atate a Kalulu. Atationa basitu kuyambapo kulira. Ife

ii basi, takong’ontha onse!” Nyama zonse zitamva

zimenezi zinati, “Mwagwira ntchitooooooooooo!

Mwagwira ntchitoo!”

Kalulu atamva za nkhaniyi anathawa n’kukamanga

malo atsopano pachitsamba. Kufikira lero amagona

pachitsamba pomwepo maso ali tuzuuu kuopa

milandu imene anapalamula pouza anthu kuti

akufuna mitu yoti apetulire mvula.

Mpandamachokero Anthology

350
Mafunso

1. N’chifukwa chiyani Njovu inaganiza zothetsa

ufumu wa Kalulu?

2. Kodi Kalulu anamva bwanji za nkhaniyi?

3. Kodi mukuganiza kuti Kalulu ankanena zoona

pamene anauza anzakewo kuti akufuna mitu

n’cholinga choti awabweretsere mvula?

4. N’chifukwa chiyani Kalulu amagona diso lili

tuzu?

5. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

351
Mfumu ndi Nyemba Zophika

Kalelo kunali mfumu ina yokalamba kwambiri.

Mfumuyi inali ndi nkhawa kwambiri chifukwa inalibe

mwana woti n’kulowa ufumu wake. Ndiye itaona kuti

chaka chimenecho sigonera, inaganiza zosankha

mwana m’modzi wa mu ufumu wake kuti akhale

mwana wake wodzalowa ufumuwo. Atafufuza m’dziko

lonse anapeza anyamata khumi omwe ankaoneka

okongola komanso a khalidwe labwino. Koma popeza

inkafuna mwana m’modzi yekha inawauza kuti,

“Tsopano chatsala chinthu chimodzi choti muchite

kuti ndipeze mnyamata amene atakhale mwana

wanga.” Kenako anapereka kwa mnyamata aliyense

nyemba imodziimodzi n’kuwauza kuti akaidzale

kunyumba kwawo n’kuisamalira kwa milingu itatu.

Mwana amene adzasamalire bwino mbewu yake

adzatengedwa kukhala mwana wa mfumu!

Anyamatawo atangomva zimenezi analiyatsa liwiro, wa

kwawo kukadzala mbewu yawo. Koma mnyamata wina

anadabwa kwambiri ataona kuti mbewu yake

sikumera. Mnyamatayo anachita chilichonse kuti

imere, koma palibe chinachitika. Anzake aja

anayamba kumuuza kuti akangogula ina n’kuidzala

Mpandamachokero Anthology

352
chifukwa akapanda kutero zimuvuta. Koma makolo a

mwanayo anali oopa Mulungu moti anamuuza kuti

asachite zimenezo.

Kenako tsiku linafika loti apite kwa amfumu aja. Ana

asanu ndi anayi anapezeka kuti mbewu zawo

zinamera. Mfumuyo inayamba kufunsa

m’modzim’modzi kuti, “Kodi mbewu zimene

ndinakupatsani zinamera?” ndipo anyamata onse

anayankha kuti “Inde mfumu yanga.” Kenako

mfumuyo inagwedezera mutu n’kupitanso kwa wina

mpaka inafika pa mnyamata yemwe nyemba yake

sinamere uja. Mnyamatayo ankangonjenjemera ndi

mantha. Mfumu inamufunsa kuti, “Kodi unaitani

nyemba imene ndinakupatsa kuti ukadzale?” Iye

anati, “Ndinaidzala n’kumaisamalira koma sinamere.”

Mfumuyo inagwira mkono wa mnyamatayo n’kupita

naye pamene panali mpando wachifumu n’kunena

kuti, “Nonse ndinakupatsani nyemba zophika, ndiye

zatheka bwanji kuti za enanu zimere? Nanga nyemba

zophika zingamere ngati? Munthu amene ndimafuna

kuti akhale mwana wanga komanso adzakhale mfumu

ndimafuna akhale ndi khalidwe limeneli la kuona

mtima ndipo ndi mwana uyu yekha amene wachita

Mpandamachokero Anthology

353
wino. Enanu zipitani!”

Mafunso:

1. Kodi n’chifukwa chiyani nyemba ya mwana

wina sinamere?

2. Kodi mukuganiza kuti nyemba zimene

anyamata ena asanu ndi anayi aja anadzala zinali

zimene anapatsidwa ndi mfumu ija?

3. N’chifukwa chiyani mwana amene mbewu yake

sinamere uja anasankhidwa kukhala mwana wa

amfumu?

4. Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Mpandamachokero Anthology

354
Angongole

Mayi: Kukabwera angongole aja, uwauze kuti

ndachokapo.

Nyamazawo: Ndiwauze kuti mwapita kuti?

Mayi: Kwa Chinsapo.

Kenako angongole anatulukira ndipo anayamba

kuodira.

Angongole: Odiiiiii. Odi kumenekooo!

Nyamazawo: Eeeee.

Angongole: Mayi ako ali kuti?

Nyamazawo: Achokapo, apita kwa Chinsapo.

Angongole: Abwerako nthawi yanji?

Nyamazawo: Aaaa, dikikirani kaye ndikawafunse.

Angongole: Ukawafunsa bwanji, mmesa wati apita

kwa chinsapo?

Nyamazawo: Ayi, ali m’nyumbamu.

Mpandamachokero Anthology

355
Fisi Anakana Mtsatsi

Mlenje wina anathedwa nzeru ndi chilombo chimene

chinkabwera pakhomo pake n’kumagwira ziweto zake

usiku. Tsiku lina anaganiza zotchera msampha ndipo

usiku umenewo anagona khutu lili panja kuti akamva

chinachake adzuke.

Usikuwo anayamba kumva phokoso. Asuzumire,

anangoona kuti ndi fisi wakodwa pamsampha. Fisiyo

ankayesayesa kuti achokepo. Mlenjeyo ataona izi

anayamba kukuwa amvekere, “Fisi kunoooooooooo!

Bwerani mudzandithandize kuli fisi kunoooooooo!”

Anthu a m’nyumba zoyandikira anatulukadi ndipo

anagwira fisiyo n’kumukwidzinga ndi zingwe. Kenako

anayamba kumuimba mlandu.

Munthu wina anati, “Nkhosa zanga zakhala zikusowa,

ayenera ndi fisi yemweyu amene amandibera.”

Winanso anati, “Ife ndiye mbuzi zathu wamaliza zonse

kudya.”

Panabweranso mayi wina ndipo anati, “Nkhuku zathu

zonse wamaliza kukhwasula ameneyu!”

Ndiyeno nkhalamba ina inati, “Nanenso dzulo

Mpandamachokero Anthology

356
ndinayanika mtsatsi zanga pathandala, ayenera wadya

ndi yemweyu chifukwa zawowa.”

Fisiyo atamva mawu amenewa anati, “Agogo inuyo

ndiye mukunama, bola zimene anena anzanu zija.

Koma za mtsatsizi ndiye ndakukanirani. Inetu

sindidya mtsatsi.”

Phunziro: Fisi angakhale munthu amene akuimbidwa

mlandu. Ngakhale munthu atakhale woipa kwambiri, si

bwino kumangomunamizira zimene sanachite.

Mpandamachokero Anthology

357
Mlenje ndi Mkango

Tsiku lina mlenje wina anapita kutchire kukasaka

nyama ndi agalu ake. Atafika malo ena, agalu akewo

anasokolotsa Sakhwi n’kumugwira, koma mlenjeyo

anawaletsa agaluwo kuti amusiye ndipo Sakhwiyo

anathawa n’kukabisala kuphanga.

Kenako mlenjeyo anapitirizabe kusaka ndipo anafika

pafupi ndi dziwe lina. Pamalowo panali ntchefu moti

agalu ake aja anagwira imodzi n’kuipha. Pamenepo

mlenjeyo anasangalala zedi podziwa kuti tsiku

limenelo akadyera nyama. Koma kenako kunayamba

chimvula choopsa moti mphenzi sizinkati zaomba pati.

Ataona zimenezi anaganiza zolowa m’phanga lina

ndipo atangolowamo anapezamo ana a mkango. Koma

popeza kunali mvula yoopsa, sakanachitira mwina

koma kulowabe m’phangalo. Atangolowa, mkango

ujanso nawo unatulukira. Nawonso unasokoloka

m’tchire chifukwa cha mvulayo. Utafika pakhomo pa

phanga lake unazindikira kuti m’phanga lakelo

mwalowa munthu ndi agalu ake. Mkangowo sunafikire

kulowamo chifukwa unkafuna kuti uonetsetse

bwinobwino ngati mlenjeyo analidi yekha mphangalo.

Kenako unafunsa munthuyo kuti, “Kodi ndiwe ndani

Mpandamachokero Anthology

358
ukupezeka m’phanga langa?”

Munthuyo anayankha mwamatha zedi kuti, “Ndine

munthu mfumu yanga.”

Kenako Mkangowo unati, “Ndiye popeza ndakupeza

m’phanga langa, utenge ntchefu waphayo uwapatse

agalu akowo kuti adye. Kenako iweyo udye agaluwo.

Ineyo ndidya iweyo!”

Munthuyo atamva izi anachita mantha zedi moti

anayamba kunjenjemera komanso kudzikodzera.

Koma mlenjeyo sanadziwe kuti Sakhwi

anamupulumutsa uja anabisala momwemo.

Sakhwiyo anauza mlenjeyo kuti, “N’chifukwa chiyani

mukuchita mantha? Mkangowutu wanena kuti

mutenge ntchefuyi mupatse agaluwa adye, kenako

inuyo mudye agaluwo, ndipo Mkangowo udya inuyo.

Pamapeto pake, ineyo ndidya Mkango ndi ana akewa.”

Mkangowo utangomva zimenezo unachita mantha

kwambiri moti unathawa.

Phunziro: Ndi bwino kumathandiza ena chifukwa

nawenso zikadzakuvuta akhoza kudzakuthandiza.

Mpandamachokero Anthology

359
Bonwell Rodgers

M’bukuli muli nthano za ana. Nthano zina ndi

zoti zinalembedwa ndi akatswiri akale kwambiri

ndipo zinamasuliridwa n’kukonzedwa mwina

ndi mwina, pomwe zina ndi za kwathu konkuno

ku Malawi. Nthanozi ndi zazifupi koma

zosangalatsa.

Mpandamachokero Anthology

360

This book is dedicated to my

beloved brother, Brian. I love

you little brother and am

always by your side.

If I could save time in a

bottle, the first thing that I’d

like to do is to save every day

till eternity passes away, just

to spend them with you.

If I could make days last

forever, if words could make

wishes come true, I’d save

every day like a treasure and

then again, I would spend

them with you—Jim Croce.