13.07.2015 Views

Umodzi Womwe Khristu Anaupempherera - Namikango Bible School

Umodzi Womwe Khristu Anaupempherera - Namikango Bible School

Umodzi Womwe Khristu Anaupempherera - Namikango Bible School

SHOW MORE
SHOW LESS

Create successful ePaper yourself

Turn your PDF publications into a flip-book with our unique Google optimized e-Paper software.

Umodzi Womwe Khristu AnaupemphereraMawu oyamba: Titha kumadziwa malembo, titha kumabatiza anthu ambiri ndi kukhazikitsa malo a mpingoochuruka, koma popanda umodzi, ntchito yonseyo sidzapindula kanthu. M’Moyo wathu wathupi wauchimo,kumakhala kosabvuta kupatukana. Koma mwa Mzimu Woyera wokha ndimo tingathe kusunga umodzi.Mulungu amafuna mpingo utakhala wolimba ndi wangwiro ndikuti ukafikire ndi kuthandiza mizimu yambiriyotayika ndi kuibweretsa kwa Yesu.Cholinga chathu chenicheni mu maphunzirowa ndikufuna kuphunzira za ubwino ndi kufunika kwa umodzi,kumvetsa zomwe Baibulo limaphunzitsa za umodzi ndinso kuphunzira momwe tingathetsere zolimbana ndimakangano pakati pathu ndi kukhala amodzi mwa Khristu.Mutu 1: Umodzi ndi Wofunika Koposa1. Sanafe, Yesu anapempherera umodzi wa omtsatira ake, kuphatikizirapo ifenso lero lino – Yohane17:11,20,21. Kodi Yesu amamva bwanji akamaona ife tikugawanika? Nanga muganiza amamva bwanjiakamaona ife tikuonetsa umodzi?A. Imfa ya Yesu inali pafupi kwambiri. Iye anali ndi kanthawi kochepa kwambiri asanamwalire kotiapemphere. Choncho anayenera kupempherera zinthu zokhazo zomwe zinali zofunikira kwambirim’moyo wake. Umodzi chinali chinthu chofunikira kwambiri pa pemphero lake. Yesu anasiya maloake aulemu kumwamba ndi cholinga chofuna kupulumutsa dziko lapansi. Iye anagwira ntchitomolimbika pa nthawi ya utumiki wake. Anali atatsala pang’ono kukapereka moyo wake pamtanda.Yesu sanafune kuti ntchito yake ndi imfa yake kuti ingopita pachabe. Iye anafuna uthenga wake wachipulumutso ukhale wopambana padziko lonse.B. Zikanakhala bwanji ngati ophunzira a Yesu akadapanda kulemekeza pemphero limeneli? Zikadakhalabwanji ngati wophunzira aliyense akadayambitsa mpingo wake wake wa payekha ndi kupatuka paanzake ena onse. Kodi anthu akadakhulupirira uthenga womwe ophunzirawa akadamalalikira? Kodimuganiza kuti uthenga umenewu bwenzi tikumaumva monga tichitira leromu?C. Yesu anapemphera “kuti dziko likhulupirire.” Kupatukana kwathu kumatchinjiriza anthu kutiasakhulupirire uthenga wabwino. Tiyenera kuonetsa mwa kuchita chikondi ndi mtendere womwetiulalikira. Kodi muganiza ndi anthu angati omwe akadalandira chipulumutso ngati Akhristuakadapanda kugawikana?D. Yesu anati nyumba kapena ufumu uliwonse womwe ugawikana wokha sungaime ayi – Mateyu 12:25.2. Paulo anafuna kuti Afilipi akhalirane mwa mtendere ndi umodzi kuti awalire dziko lapansi monga kuunika– Afilipi 2:14-16. Ngati Afilipi aja sakadasunga umodzi, ndiye kuti utumiki wa Paulo pa uthenga wabwinoukadakhala wopanda phindu. Ngati palibe chikondi ndi mtendere pakati pa Akhristu pamenepo palibensokuunika.3. Baibulo limatilamula ife kuti tisunge umodzi pakati pathu – 1 Akorinto 1:10; Aefeso 4:1-6.A. Umodzi ndi ganizo limene timalipanga. Ndi chinthu chimene timasankha.B. Umodzi wa Chikhristu sutanthauza kuti tonse tikhale ndi ganizo lofanana pa zinthu zazing’onom’Baibulomo. Koma utanthauza kugwirizana mu zikhulupiriro ndi zolinga zazikulu mwa chikondi pawina ndi mnzake ndiponso pa otaika.C. Umodzi wa thupi la Khristu ndi chimodzi mwa zinthu zisanu ndi ziwiri za ziphunzitso zazikulu zachikhulupiriro cha Chikhristu – Aefeso 4:4-6.D. Pamene tigawanikana mosasamalira bwino, ndiye kuti sitimvera malamulo a Khristu ndi Atumwi aja.Umodzi 11/29/12

4. Umodzi ndi wofunika kwambiri chifukwa Mulungu amakonda mpingo wake ndi kudana komansokuweruza omwe amayambitsa mipatuko – Miyambo 6:16-19; Tito 3:10,11; Aroma 16:17,18.Sindikondwera pamene wina abvutitsa ndi kupweteka thupi langa. Ndimakwiya pamene wina asokonezabanja langa ndi kuyambitsa mabvuto. Kugawikana kumaononga ndi kubvulaza thupi la Khristu.Kumasokoneza ndi kugawanitsa banja la Mulungu. Kugawikana kumapunthwitsa anthu otayika ndipokumawalepheretsa kukhulupirira mwa Khristu. Mulungu amawakonda otayikawo. Mulungutu amalikondabanja lake. Choncho chiweruzo chake chimakhala chokhwima kwa omwe amabweretsa kapena kuyambitsamalekano. Tamvetserani momwe Mulungu amaweruzira nkhani za malekano:A. Pamene kulimbana ndikugawanikana kubwera mu mpingo, Akhristu ambiri amapwetekedwa mumtimakapena kusowa mtendere wa mtima ndipo kenako amasiya kutsatira Yesu. Yesutu anatichenjeza kutitisachite zinthu zomwe zingachimwitse anthu ndi kuwapangitsa kusiya kumvera Khristu.Ngati wina apangitsa mmodzi wa aang’ono awa omwe amakhulupirira ine kuti achimwe, kukanakhalabwino kuti woteroyo akolekedwe mkhosi mwake ndi mwala wamphero waukulu ndiumizidwa m'nyanjayakuya kwambiri. Tsoka dziko lapansi chifukwa cha zinthu zomwe zichimwitsa anthu! Ngati dzanjalako kapena phazi lako likuchimwitsa ndi bwino kulidula ndi kulitaya. Pakuti kuli bwino kulowam’moyo wopunduka kapena wopanda dzanja kapena phazi koposa kuponyedwa m'moto wa nthawizonse uli ndi manja kapena mapazi awiri. Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole ndi kulitaya.Kuli bwino kwa iwe kulowa m'moyo ndi diso limodzi koposa kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwam’gehena wa moto – Mateyu 18:6-9.B. Mulungu adzaononga iwo omwe adzaononge kachisi wake. Paulo analemba za anthu omwe anaonongampingo, kachisi wa Mulungu, poyambitsa mipatuko.Kodi simudziwa kuti inu ndinu kachisi wa Mulungu ndikuti Mzimu wa Mulungu akhala mwa inu? Ngatiwina aliyense awononga kachisi wa Mulungu, Mulungunso adzamuononga popeza kachisi wa Mulungundiwopatulika ndipo inu ndinu kachisiyo – 1 Akorinto 3:16,17.Ngati tilimbana ndi kumagawanikana moona osapembedza ndiye kuti tikukana uthenga wabwino womwetiulalika. Ngati timakondana, ndiye kuti anthu onse adzadziwa kuti ndifedi ophunzira a Khristu. Palibe chinthuchomwe chimaphwanya ndikuononga ntchito ya uthenga wabwino koposa malekano athu. Kodi muganizadziko lathuli likadakhala lotani lero ngati Akhristu onse pamodzi akadakhala amodzi ndi ogwirizana ndikumalalikira uthenga wabwino ndi mphamvu zonse?Mafunso okambirana: Nchifukwa chiyani timangolimbikira pa ziphunzitso zina koposa momwe tichitira pa chiphunzitso chaumodzi? Tafotokozani momwe kugawanikana kwalepheretsa ndi kutchinjirizira uthenga wabwino m’dera lanu. Tafotokozani momwe umodzi wolimbikitsira ulaliki wa uthenga wabwino m'chigawo kapena dera lanu.Mutu 2 - Zomwe Baibulo Linena pa za Chiphunzitso cha Umodzi.Mawu oyamba: Baibulo lonse limaphunzitsa za umodzi. Mulungu adalenga mwamuna ndi mkazi ndipo anatiiwo akhale thupi limodzi (Genesis 2). Ndipo Yesu adati, ”Chomwe Mulungu wa chimanga, munthuasachilekanitse” – Mateyu (. Abrahamu anati kwa Loti “Pasakhale kukangana pakati pa iwe ndi ine, pakuti tiriabale” – Genesis 13. Pamene Kora, Datani ndi Abrahamu anayeserera kugawa Israyeli pogalukira Mose ndiAroni, Mulungu anang’amba nthaka ndipo onse ogalukirawo anamezedwa pomwepo. Davide analemba kuti“Zimakhala zosangalatsa kwambiri pamene abale akhala pamodzi mwa umodzi!” – Masalmo 133. Umodzi wathupi la Yesu ndi chiphunzitso chofunikira kwambiri cha m’Chipangano Chatsopano. Tiyenera kumverachiphunzitso chimenechi. Ngati timakhulupirira ndi kuphunzitsa ziphunzitso zinanso za m’ChipanganoChatsopano, tiyeneranso kukhulupirira ndi kuphunzitsa chiphunzitso cha umodzi.1. M’Chipangano Chatsopano, umodzi uli ndi maziko awiri, maziko a uzimu ndi maziko a chiphunzitso.Umodzi 2

A. Pa Aefeso 4:1-3 timawerenga za umodzi wokhazikika pamaziko auzimu.Monga wamndende wa Ambuye, ndi kudandaulirani ine tsopano, kuti muyende molingana ndimoyenera maitanidwe omwe unaitanidwa n awo, ndipo onetsetsani kuti mukudzichepetsandiponso muli ofatsa; khalani opirira; ololerana wina ndi mnzake mwachikondi. Samaliranikwambiri poonetsetsa kuti mukusunga umodzi wa mzimu podzimangirira pa mtendere nthawizonse.Umodzitu ndi wa Mzimu. Kudzichepetsa monga Khristu ndiko kumachititsa kuti umodzi utheke.Chilengedwe chathu chathupi cholakwa chimakonda moyo wopatukana. Tawerengani mndandanda wa“ntchito za thupi” mu Agalatiya 5:19-21. Mukuona kuti madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima,kukhumba zonyansa, zotetana, magawano, mipatuko ndi njiru zaikidwa mu gulu limodzi ndi chigololo,kuledzera ndi nyanga. Theka la machimo omwe atchulidwa mu mndandanda umenewu amapezekapafupifupi m'malekano a mumpingo uliwonse, ndi mukulekana kwa banja liri lonse. Koma tawerenganimndandanda wa “chipatso cha mzimu mu Agalatiya 5:22,23. Umodzi umakhala wosavuta ngati anthuakhala otere.Popanda chipatso cha Mzimu Woyera, chimene chimagonjetsa khalidwe lakale ndi kusintha ife kutitifanane Khristu, sitingathe kusunga umodzi. Ngakhale tigwirizane ndi ziphunzitso zonse, komakhalidwe lathu la kudzikonda lidzapezabe njira ya kutilekanitsa ngati tikuyenda m’thupi. Makolo agulu la chibwezero, limene Mpingo wa Khristu mmene tiri kukhalamo lero, anayetsetsa kugwirizanitsaokhulupirira malembo. Anatisonyeza ife mmene tingagwirizanirane mwa ziphunzitso zenizeni zaBaibulo. Koma sanaphunzitse zambiri za malekano ochitidwa mwa uzimu. Koma tiyenera kuphunzira.B. Mu Aefeso 4:4-6 Paulo ali kutipatsa ife madziko a chiphunzitso cha umodzi. Watchula ziphunzitsozazikulu zisanu ndi ziwiri zimene tiyenera kuzikhulupirira m’malo mwakuti tikhale amodzi.Pali thupi limodzi ndi Mzimu mmodzi—monga momwe munaitanidwa ku chiyembekezochimodzi pamene munaitanidwa—Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi;Mulungu mmodzi ndi Atate wa onse, amene ali pamwamba pa onse ndi mwa onse ndi mkatimwa zonse.Tafanizirani 1 Akorinto 15:1-8 pamene Paulo waika mndandanda wa zinthu zofunika kwambiri muuthengamo.Pakuti chimene ndinalandira ndinapereka kwa inu monga chofunika choyambirira: kutiKhristu anafera zoipa zathu monga mwa malembo, ndikuti anaikidwa, ndikuti anauka pa tsikulachitatu monga mwa malembo, ndi kuti anaonekera kwa Petro, ndi kwa khumi ndi awiriwa.Izi ndi zoonadi zolimba zimene zitipanga ife kukhala monga momwe tiri. Chotsani ngakhale chimodzimwa izo ndipo sitingakhalenso mpingo wa Ambuye. Tiyenera kulandira zonsezo m’malo mwakutitikhale amodzi ndi kulandirana wina ndi mnzake. Tiribe ufulu wakugwirizana ndi wina aliyensewokana ngakhale chimodzi mwa zoonadi zimenezi. Sitingathenso kusiya chimodzi mwa zoonadizimenezi m’malo mwakuti tisunge umodzi.Malembonso akuphunzitsa kuti sitingakhale amodzi ndi Akhristu amene achita mitundu ya uchimoyoipa ndipo sakulapa – 1 Akorinto 5; Mateyu 16:15-20; Aroma 16:17,18.2. Umodzi wakhazikika pa chisomo. Tiri amodzi ndi Mulungu pachifukwa cha chikhululukiro cha chisomochake. Tiri amodzi ndi Iye osati chifukwa ife tiri olungama koma chifukwa zochimwa zathu zakutidwa ndimwazi wa Khristu. M’njira yomweyo, tiri amodzi wina ndi mnzake kupyolera m’chisomo ndichikhululukiro.Mulandirane wina ndi mnzake, monga momwe Khristu anakulandirani inu, m’malo mwakuti tichitireMulungu ulemu. – Aroma 15:7.Mulungu anatilandira ife monga anthu osakonzeka, ndipo momwemonso ife tilandirane wina ndi mnzakemonganso anthu osakonzeka.Umodzi 3

Monga momwe ndakukonderani inu, inunso mukondane wina ndi mnzake – Yohane 13:34.Yesu anatikonda ngakhale tinali wochimwa koteronso tikondane wina ndi mnzake. Umodzitu umadalirachisomo. Mulungu watipatsa ife malamulo ena ndipo tiyenera kuwalemekeza. Komatu nkhani yaChikhristu simalamulo ayi. Koma ndi nkhani ya chikondi, ubale wokhulupirika ndi Mulungu. Kulekanakwakukulu pakati pa Chikhristu ndi zipembedzo zina zonse kuli pa chisomo. Mulungu adzatiweruzapopanda chifundo ngati tiribe chifundo pa ubale wathu ndi anzathu. – Yakobo 2:13.A. Taonani kuti pali ziphunzitso zina zofunika kwambiri zomwe tonse tiyenera kudzikhulupirira ndipongati tipanda kutero sikungatheke kuti tikhale amodzi – Aefeso 4:4-6; 1 Akorinto 15:3-8; 5:1-13.Tiyenera kupatuka pa wina aliyense yemwe akana ziphunzitso zofunikirazi.B. Komanso Baibulo limafotokozera ndi kuzindikiritsa kuti alipo magawo ena ndi nkhani zinazazing’ono zomwe Akhristu okhulupirika ndi oona angathe kumva mosiyana ndikutsatira mosiyanakomabe nakhala amodzi mu mtendere ndi Mulungu, wina ndi mnzake – Aroma 14. Ichitu ndichiphunzitso chofunikira koposa chomwe Baibulo liphunzitsa za umodzi.1) Yesu amati pali malamulo ena omwe amakhala ofunikira kuposanso ena – Mateyu 23:23; 22:35-40; 40:19. Tiyenera kumasamalira malamulo ena onse koma ena ndi ofunika kuwasamalirakwambiri chifukwa ali ndi maziko osiyana ndi ena.2) Ziphunzitso zina zomamveka bwino ndimalemba ake koma zina zimakhala zovuta kumvetsakwake – 2 Petro 3:16. Ziphunzitso zomwe zimakhudza chipulumutso chathu zimakhala zomvekamosavuta. Nkhani zomwe ziri zovuta kutanthauzira kwake kapena kumvetsa, nkhani zomwezimadalira kwambiri pa umunthu wathu wolephera ndi nzeru zathu za umunthu sizingakhalenkhani za chipulumutso kapena zifukwa zoti tilekane.3) Malamulo ena a m’malembo amangokhala ndi cholinga chofuna kufotokozera tanthauzo lokhalaMkhristu ndi mwana wa Mulungu. Malamulo ena amangokhudzidwa ndi nkhani zazing’ono ndizosakhala zakuya kwenikweni. Ziphunzitso za chikondi, ndi chikhulupiriro ndi kukhulupirika ndizomwe ziri zotumikira koposa ziphunzitso zofotokozera za dongosolo la chipembedzo.Kulakwitsa moona pa zakutalika kwa tsitsi lamkazi sikuli kuopsa kwambiri monga zingaopserengati munthu sakhulupirira za “kuuka”. Afarisi anali otanganidwa ndi okhudzidwa kwambiri ndizinthu zooneka kunja kwa thupi ndi mtima monga za miyambo yosiyanasiyana ndi kusambamunthawi zokonzedwa. Yesu anawasonyeza malemba oti, “ndifuna chifundo, osati nsembe ayi –Mateyu 12:1-7; 9:10-13.4) Mulungu amadziwa kuti popeza tiri nako kufooka kwathu kwa umunthu, ndiponso chifukwachoti tonse sitiri okhwima m’chikhulupiriro, sitingathe kuona bwinobwino, ndimvetsa bwinomawu ake. Munkhani zoterozo, iye amangotipatsa mwa chisomo chake ndipo amatilamula ifekuti tiwachitirenso anzathu zomwezo – Aroma 14:1-15; 7. Izi zimakhudzanso nkhani zomwetimakhulupirira ndi kuzolowera kuchita m’mipingo mwathu. Pamene tidzapita kumwambatidzatulukira kuti tonse tidalakwitsa m'zinthu zina zazing’ono zing’ono zomwe tidazikhulupirira.Palibe ndi mmodzi yemwe amamvetsa bwino ndi kumvera malembo onse mwachindunji. Nkhanindi yoti tiri opulumutsidwa mwa chisomo.Nkhani zambiri zomwe timalimbana nazo ndi kumakanganira mpaka kumagawanikana nazomumpingo sinkhani za chipulumutso konse. Koma umodzi ndi nkhani ya chipulumutso. Ichi ndichiphunzitso chofunikira zedi. Komabe palinso choonadi chomwe Baibulo limafotokoza pa zaumodzi chomwe anthu ambiri satha kuchimvetsa. Zitsanzo:(a)(b)Sitiri oyenera ngakhale kulandira mbale wofooka, womangiririka zinthu zazing’onozoti tingathe kuchita nazo kapena osachita nazo.Akhristu omwe ali a maganizo awiri osiyana pa nkhani zimenezi, angathe kukhala nafepamodzibe ngakhale mmodzi wa iwo ali wolakwa. Ichi chitanthauza kuti mu nkhaniUmodzi 4

zomwe mpata umakhalapo pakati pa abale okhulupirika kuti akhale ndi maganizoolekana pa nkhani zina, sizingakhale nkhani za chipulumutso ayi.(c)(d)(e)Pamene mbale asiyana ndi ine pa momwe titanthauzira malembo, sichitanthauza kutiiyeyo saopa Mulungu kapena akuyesetsa kusamveraMulungu mwa muyezo uliwonse.Lamulo la Paulo mu Aroma 14 loti tilorerane limakhudza zambiri zoposa khalidwelakelake la munthu. Kukhulupirira masiku oyera ndi opatulika kunakhudzansomisonkhano ya mipingo zochitika chitika pa nthawi ya chipembedzo.Mbale amene ali womangiridwa ku chikumbumtima chake yemwe amaweruza mbalewake “pochita zoipa” akubweretsa magawano chimodzimodzi monga momwe mbaleyemwe achita zomwe zikhumudwitsa ubale wake womangiririka ku chikumbumtimachake uja. M’mbuyomo takhala tikutsutsa yemwe amayambitsa zinthu zatsopanomonga woyambitsa mipatuko. Uku kunali kulakwa. Mu Aroma 14 sitiphunzira motero.5) Pamene tiwerenga bwino ndi kumvetsa bwino Aroma 14,15 timaloledwa kukhalabe amodzingakhale pali nkhani zina zazing’ono zomwe tikulephera kumva mofanana. Choncho ndimalembo amenewa titha kuona ndi kumvetsa bwino nkhani imeneyi kuti:a.)b.)c.)Mulungu amatilamulira kuti tipitirirebe kugwira ntchito pamodzi chifukwa cha nkhanizofunikira kwambiri zomwe timazimva mofanana ndi kusiya zina zazing’onozing’onozomwe tingathe kuchita popanda izozo kuti Mulungu ndiye aweruze.Ndingathe kugwiri ntchito ndi abale ena mumpingo ngakhale pali zina zomwesitizimva mofanana pa mfundo zina zomwe iwo achita ndi kukhulupirira.Nkhani itha kukhala ndi magawo abwino ndi oipa ngakhale ndiikulupirira koposa.Ngati pafika poti kumasulira kwa umunthu wathu wooka kugwiritsidwa ntchitonkutheka kuti nditha kukhala wolakwa m’chikhulupiriro changa.C. Makolo athu akale pa nthawi yawo yobwezeretsa anasonkhanitsa chiphunzitso cha m'ChipanganoChatsopano cha umodzi m’mawu oti, “M’chikhulupiriro, umodzi; malingaliro, ufulu; m'zonse,chikondi."D. Ngakhale kulekana kwina ndi kofunika chifukwa kumakhudza za ziphunzitso zofunikira, nthawizambiri kulekana kumakhalapo chifukwa sitimvetsa zomwe Baibulo limaphunzitsa za chisomo.1) Chisomo ndi choonadi siziri zinthu zotsutsana china ndi chinzake ayi. Zonsezi zimagwirizanantchito yofotokozera za khalidwe ndi moyo wa Yesu – Yohane 1:14. Yesu anasakaniza chisomochopusa ndi kuleza, pamodzi kukhudzidwa koposa kwa choonadi.2) Paulo anawauza Akhristu kuti “simuli pansi pa lamulo koma pansi pa chisomo.” – Aroma 6:14.Anthu powerenga mawu amenewa amaganiza kuti chisomocho chimatanthauza kuti azichita zirizonse zomwe zingawakomere koma Paulo akukanitsitsa zimenezi. Sitiyenera kumaopa momwechisomo chingakhudzire kumvera kwa pachoonadi. Chisomo nthawi zonse chimapereka kumverakwakukulu kuposa chilamulo chomwe chimangotsamira pa zowerengeka za malamulo akunja kwathupi ndi mtima. Chisomotu chimasintha mitima yathu ndipo chimatipangitsa kukhala omafunakukondweretsa Mulungu.3) Pamene tiwalandira iwo amene tisiyana nawo maganizo pa nkhani zina zazing’ono sikutanthauzakuti tikugwirizana ndi zomwe tikuona ngati iwo akulakwitsa ayi. Sizitanthauza kuti tasiya kumveralemba la m’Baibulo ndi limodzi lomwe. Tiyenera kumakhala osamalira kwambiri potsatiramaganizo athu m’makhalidwe athu ndi kumaphunzitsa ena zomwe tikukhulupirira kuti ndi zomwemalemba akutanthauza.Umodzi 5

Koma ngati sakumvetsabe chomwe tikutanthauza pa nkhani yomwe tikuwauzayo ngati iriyaing’ono, tiyeni tipitirezebe kuwakonda ndi kugwira nawo ntchito pamodzi. Mu Aroma 14timamva kuti tiyenera kusiyira Mulungu kuti aweruze nkhani zina zomwe ife talephera.Kusunga umodzi pakati pathu ndi omwe tisiyana nawo maganizo ndi lamulonso pa lokha, ndichinthu choyenera kuchikhulupirira, ndi gawo la chiphunzitso cha Chipangano Chatsopano.Baibulo limatiphunzitsa kuti anthu onse, kuphatikizapo akulu ampingo angathe ndipo ayenerakumagwira ntchito pamodzi, ndipo sikuti zingatheke kuti azikhala ofanana m’maganizo pa mfundozonse angakumana nazo. Mpingo ungathe kukula koposa anthu zana limodzi (100) popandakulekana maganizo. Koma kuti izi zitheke, pamafunika kuti tikhale ndi luso lozindikira msangankhani zoti titha kulolerana popeza ndi zazing’ono.Mutu 3: Zoyambitsa Kulekana.Nthawi zina m’mudzi mumagwa mliri. Anthu amavutika ndipo ena amafa. Madotolo ndi akatswiri enaamabwera kuti afufuze choyambitsa kapena chomwe chikufalitsa matendawo. Pamene atulukira ndi kumvetsabwino gwero la matendawo, ndi pomwe angathe kuthetsa matendawo ndi kuwatchinjirizanso. Momwemonsongati timvetsa bwino chomwe chimayambitsa kapena komwe kumachokera moyo wolekana, ndi pomwetingathe kuchiza ndi kutchinjiriza bvuto limeneli. Malingana ndi malemba, zoyambitsa kulekana zina ndi:-1. Kukana kukhulupirira zinthu zofunikira kwambiri ndi malamulo a m’Baibulo.A. Yohane analemba kuti Akhristu asamalandire m’nyumba zawo aphunzitsi omwe ankati Yesusanabwera monga munthu wathupi – 1 Yohane 2:22,23; 4:1-3; 2 Yohane 7-11; tawerengani ndipomufanizire 1 Akorinto 13:3; Aefeso 4:4-6; 1 Akorinto 15:3,4; 5:1-13.B. Mulungu satitsutsa ife ngati tidzilekanitsa kwa aphunzitsi onyenga oterewa. Tiri oyenera kupatuka paamenewa.2. Moyo wathu wauchimo “thupi” – Agalatiya 5:19-21; 3 Yohane 9,10. Timanena kuti kupatukana kwathusikuli koyipa chifukwa tichita zomwe malembo anena, koma zoona ndi zoti nthawi zambiri nkhaniimakhala yokanganira ukulu ndi mphamvu, kapena nthawi zina kuwawirana mtima ndi kusakhululukiranachabe.3. Kukonda kuchititsana makani pa zinthu zopanda pake ndi zosamveka – 1 Timoteo 1:3-7; 4:7; 6:3-5,20,21;2 Timoteo 2:15-17,23-26; 4:3,4; Tito 1:10-15; 3:9-11.4. Kusamvetsa bwino zomwe Baibulo liphunzitsa za umodzi – kapena za umodzi weniweni womwe Baibulolimafotokoza – Aefeso 4:16; Aroma 14:1-15; 75. Kukulitsa ndi kulemekeza zinthu zina koposa Khristu ndi mtanda – 1 Akorinto 1:10 – 4:1. Anthu a kuKorinto anagawanikana chifukwa anakhulupirira ndikutsatira kwambiri alaliki koposa Yesu Khristu. Ifemwina tikhoza kumakhulupirira kwambiri ndi kutamanda koposa mlaliki wodziwa kuyankhula bwino,mphunzitsi mwanzeru, dzina, nyumba, chiphunzitso, kapena mwambo. Zonse ndi zomwe zimalekanitsaAkhristu, (Paulo adati Akorinto anayenera kukhala nalo gulu lomwe ankadziwika nalo kuti aonetse ndi utianali wobvomerezeka kwa Mulungu – 1 Akorinto 11:9). Chirichonse (ngakhale chiphunzitso) chomwechimalowetsedwa m’malo mwa Khristu monga nkhani yaikulu, chimakhala fano6. Kukhulupirira malamulo, kukhulupirira kuti timalandira chipulumutso mwa zintchito zabwino zomwetichita koposa chisomo cha mtanda.Moyo wathu wauchimo wathupi, nthawi zonse umafuna kutenga dongosolo la uthenga wa chisomo ndikuusandutsa kuti ukhale monga lamulo chabe, dongosolo lomwe anthu amalandira chipulumutso chifukwachotsatira malamulo chabe. Izitu zinawachitikira ena aja a mumpingo woyamba uja. Taonani Machitidwe15 ndinso kalata ya kwa Agalatiya. Ndipo zakhala zikuchitikanso mumpingo mu mazana mazana a zakakuyambira munthawi ya atumwi. Anthu omwe amalimbana ati pofuna kuteteza dongosolo la malamulo,nthawi zambiri amalakwitsa poganiza kuti, malinga ndi chikhulupiriro chawo, iwo amachita zimenezipofuna kuvutikira uthenga wabwino ndi chikhulupiriro cha Chikhristu, komanso ati amachita zimenezipolimbikitsa uthenga wabwino ndi Chikhristu.Umodzi 6

A. Chipangano Chatsopano chimaphunzitsa kuti palibe yemwe angalandire chipulumutso chifukwachosunga lamulo,, chifukwa palibe ndi mmodzi yemwe, amene amasunga malamulo mwachindunji ndimosamala. Tonse tinachimwa ndipo taperewera mu ulemerero wa Mulungu, komabe timawerengedwaolungama chifukwa Yesu analipira machimo athu ndi mwazi wake pa mtanda – Aroma 3:20-28.B. Kufananiza pakati pa kuweruzidwa mwa lamulo ndi kuweruzidwa mwa chisomoKuyeretsedwa mwa LamuloKuyeretsedwa mwa ChisomoZochita zathu za ife eniKudalira pa ntchito zabwino -Agalatiya 3:10; Yakobo 2:10.Kuchita bwino kwa ife eni.Kutukumuka chifukwa chochita bwinoKulandira chipulumutso “chomwekutipatsa”UkapoloKukhudza zolembedwa zokhazo basiMwa zintchito, zochitikaKuchita bwino chifukwa cholamulidwa-Kungochita ndikutsata zingapo zotizomwetifuna.Onse analepheraZochitidwa ndi MulunguKudalira ntchito yomwe Yesu anachitaKuchita bwino kochokera kwa Mulungu.Kukweza ndi kulemekeza MulunguChipulumutso mphatso yomwe Mulungu ayenerasitinali oyenera kuilandira.UfuluKukhudza mzimu ndi maganizo amkati.Mwa chikhulupiriroKuchita bwino chifukwa moyo wathu watsopanoufuna kutero.Kuchita zonse zabwino zomwe tingatheOnse angalandire.C. Komabe anthu ena amaganizirabe kuti adzalandira chipulumutso posunga bwino malamulo a Mulungu.Mwa chilengedwe chathu, mipatuko imabadwa chifukwa chotsamira pa malamulo. Taonani zina zazinthu zomwe munthu wotsamira pa malamulo amachita:1) Amasankha ena a malamulo a milungu yomwe ndi yodziwika ndi yokondedwa ndi iyeyo kapenaziphunzitso zina za malembo ndi kuzigwiritsa ntchito monga muyezo woonera chikhulupirirokoma panthawi yomweyo akutaya ndi kuiwala malamulo ambiri a Mulungu ndi ziphunzitsozomwe (makamaka zamkati mwa mtima ndi za uzimu).2) Amawatenga onse omwe amasamala bwino malamulo omwe iye anawasankhawa mongaolungama ndi okhulupirika kwa Mulungu ndipo ena onse omwe sasunga zimenezi monga“olakwa” Ichi chitanthauza kuti iwowa amene ali “olungama ndi okhulupirikawa”, sali olakwa.Alibe tchimo. Izi zimaonetsa kulakwitsa posasamala mfundo yoti tonse timalephera kumveraMulungu m'zinthu zambiri chifukwa cha kusadziwa kapena kufooka, ndipo onse ayenera kudalirachisomo.3) Amalimbikira pa malamulo oyang’ana zakunja kwa thupi ndi kumvera kwake kopanda ungwirokoposa malamulo amkati mwa mtima ndi kumvera kwa mkatikati kwa Mulungu.4) Amakhazikitsa maganizo ambirimbiri a anthu ndi miyambo ya anthu monga malamulo enaowonjezedwa pa malamulo a Mulungu – Taonani Mateyu 15:1-20. Ngati munthu ali wotetezekandi kusunga malamulo kwake koposa chisomo, pamenepa, iye amaona kuti zingamuyenderebwino ngati aonjezerabe malamulo ena awiri atatu monga linga lomuteteza, m’malo mongotsataUmodzi 7

ndi kuchita zinthu momveka bwino monga momwe malemba afotokozera. Miyambo inaimaonjezeredwa ndi cholinga choti zioneke zoonadi. Ichitu ndi chifukwa chake mipingo inaipezeka kuti nthawi zonse ikulekana pa mfundo zina zatsopano.5) Amalimbikira za mgwirizano wathu ndi malamulo koposa mgwirizano wathu ndi Mulunguyemwe anapereka malamulowo. Akhristu otsamira kwambiri pa malamulo nthawi zambiriamakhala ofooka pa momwe iwo eni ayendera ndi Mulungu.D. Nchifukwa chiyani moyo wathu wauchimo umakonda kutsatira ndi kusamala malamulo koposachisomo?1) Titha kukhala ndi chipembedzo cholamulidwa ndi ife eni, chokhala ndi dongosololomangoyang’ana ndi kutsamira pa mndandanda wa malamulo osankhika ndi ziphunzitsozokonzedwa. (Pamene munthu ali pa ubale iye ndi Mulungu, zinthu sizikhala pansi paulamuliro wake ayi; Mulungu amatitengerabe ife nthawi zoti zomayeserera ndi kuchitachifuniro chake ku miyoyo yathu.2) Kudalira pa malamulo kumatipatsa moyo wodzitcha apamwamba. Ife tiri okhulupirika ndiomvera ndipo enawo ali olakwa – tafanizirani ndi mawu opezeka pa Luka 18:9-14.3) Zimatipangitsa kuti tidzinyenge tokha poganiza kuti tiri otetezeka. Popeza tikungoyang'ana pazofunikira za Mulungu zowerengeka chabe osati pa zofuna zake zonse, timaona ngati tikuchitabwino pa kumvera.4) Timangolimbikira kuchita zinthu zingapo zoonekera kunja mokhoza (kapena kungosungaziphunzitso zingapo chabe zolondola), osati kusinthika kwa mitima yathu (ntchito ya pamoyowathu wonse yotheka chifukwa cha thandizo la chisomo cha Mulungu chokha basi).5) Pamene tiri pansi pa ulamuliro wa chilamulo timakhala ndi lamulo lochitira chiri chonse ndipositisowanso kuvutika ndi kuganiza. Pamene kwa munthu yemwe ali pansi pa chisomo ayenerakugwiritsa ntchito mfundo zauzimu pofuna kuyankha Mafunso ambiri omwe malembosanafotokozere mwatchutchutchu, ndipo izi zimafunika kuti ife tikhale olimba ndi oganizamozama kwambiri.6) Ndi kosabvuta kusamalira dongosolo la malamulo koposa kusamalira Mulungu amoyo ndiwoopsa.E. Zoopsya Zapadera Zodalira Malamulo1) Zimatamanda kuchita bwino kwa ife eni ndi kumvetsa kwathu ndi kuchotsa chitamandochikwa mwini wake Yesu ndi mtanda – taonani 1 Akorinto 1:31; 2:2.2) Zimatipangitsa kukhala otukumuka ndi onyada m’malo mokhala odzichepetsa. Timakhalaokonzekera kuweruza ndikutsutsa anzathu enanso.3) Zimabereka kugawikana kosiyanasiyana m’thupi la Khristu, kusokoneza pemphero la Ambuyewathu lija la Umodzi. Umodzi pakati pa anthu operewera pa ufumu wa Mulungu umathekamwa chisomo.4) Zimalinganitsa maganizo athu aumunthu ndi chikhalidwe chathu malamulo a Mulungu ndipopotero zmatipangitsa kuti kupembedza kwathu kwa Mulungu kusakhale kobvomerezeka –Mateyu 15:1-20.5) Zimatipatsa nthawi yoti tidzinyengeka poganiza kuti ndifedi omvera Mulungu, potsamirakwambiri pa malamulo pang’ono osankhidwa mosaganizira bwino. (Kodi ndi chiyani chomwechimapangitsa kuti malamulo ochepa amenewa akhale ofunika kuposa ena onsewo? Kodi ndiUmodzi 8

chiyani chimapangitsa kuti nkhani zina za ziphunzitso zikhale ndi mphamvu koposa malamuloake amkatikati mwake?)6) Zimanyalanyaza malamulo a Mulungu pa za mtima ndi mzimu, ndipo amakhala wokhutitsidwandi kungomvera lamulo Lolembedwa popanda kuganizira mzimu ndi cholinga cha lamulolo.7) Timangodzidalira tokha m’malo modalira Mulungu.8) Timalowetsa ubale wathu ku malamulo angapo omwe timawasankha m’malo molimbikitsaubale ndi Mulungu. Timadziwa zambiri za malamulo koposa Mulungu yemwe anaperekamalamulowo.9) Pali malamulo ena omwe timawakonda ndi kuwazolowera ndi maganizo ena, ngakhale akhaleabwino powagwiritsa ntchito monga mwa cholinga cha Mulungu. Amasanduka mafano kwa ifechifukwa amalowa m’malo mwa Ambuye ndi mtanda wa Khristu pa ziphunzitso zathu. Palibelamulo kapena chiphunzitso chomwe chingakhale ndi tanthauzo ngati chiri chongodziimirapachokha pambali pa Umbuye wa Khristu.10) Kudalira ndi kutsamira pa malamulo kumabvala kumvera koperewera kwa Mulungu chifukwakumanyalanyazitsa malamulo ambiri a Mulungu ndipo amangotsala ochepa okha, chifukwakumanyalanyazitsa nkhani za mkatikati za kumvera ndi kulemekeza zakunja zooneka ndimaso. Mwa chisomo, wokhulupirira amakhala wotengeka pomvera Mulungu chifukwa iyeamachita ichi pobvomereza chikondi cha mtanda, ubale wake wa iye ndi Ambuye wake.11) Zikapitirira, kutsamira pa malamulo kumadzapherezera potilekanitsa ife ndi chisomo chaMulungu. “Inu amene muyetsedwa olungama ndi lamulo, mulibe kanthu popezamunasiyanitsidwa ndi Khristu; Mudagwa posiyana nacho chisomo” – Agalatiya 5:4.Simungathe kukhulupirira ntchito zonse za Khristu ngati mukhulupirira kwambiri pa kuchitabwino kwanu kwa inu eni kapena kulungama kwanu. Ntchito ya kukhululukira ndi kuombolainachitika chifukwa cha ochimwa, osati chifukwa cha iwo ali angwiro.Komatu zonsezi sizitanthauza kuti Mulungu alibe nafe ntchito kapena kuti kumvera kwathu kulikosafunika. Cholinga chenicheni cha chisomo ndicho chofuna kukhazikitsa mwa ife moyo wodzadzandi kumvera koposaposa. Monga momwe mkulu wina ananenera, “Mulungu amakukondani mongamomwe muliri komatu amakukondani koposa kotero kuti sangathe kukusiyani pomwe muliripo.”Gawo loyamba: Kusunga Ubale Wabwino.Mutu 4: Umodzi Pakati pa Ogwira NtchitoMawu oyamba: Satana amafuna kugawanitsa ndi kudanitsa anthu. Amafetsa kuwawirana mtima ndi udani.Khristu amafuna kuyanjanitsa ndi kugwirizanitsa anthu. Iye amafetsa mtendere ndi chikondi. Anthu nthawizonse adzakhala ndi maganizo olekana ndi makangano. Ngati zimenezi tingozilekerera osaziperera njirayokonza, zimakwaniritsa zolinga za Satana. Maganizo a Yesu angathe kuthetsa kulekana kwa maganizo pakatipa anthu ndi kugwetsa malinga olekanitsa mabanja, mipingo, achinansi, kuntchito kapena maubale enaosiyanasiyana. Yesu watipatsa mfundo zomwe zingathe kuchiza ndi kubwezeretsa ubale woonongeka. Tiyenitione komwe makangano amachokera ndi chomwe tingachite pa nkhani imeneyi.1. Muzu weniweni wa kulimbana ndi kulakwirana pakati pa anthu ndi kunyada ndi kudzikonda – Mateyu18:1-5.A. Bvuto: Tonse timafuna kudziwa kuti “Kodi wamkulu ndani?” (wopambana, mpondamatiki, wokhoza,wodzisamala, wosiririka, wokondedwa, wa ulamuliro woposa ndi zina zotero). Ngati nthawi zonsendi mangoganizira za ine ndekha, ndiye kuti kulimbana ndi enawo kuyenera kuyambika nthawi inairiyonse.B. Kuthetsa kwake: Kukhala wakufa kuthupi” – Agalatiya 2:20.Umodzi 9

1) Mateyu 18:3,4 – Mudzione ngati kamwana kakang’ono podzifanizira ndi ena.2) Afilipi 2:5-8 – Kutaya ulemu ndi ufulu wanu mwakufuna kwanu.3) Aefeso 5:21 – Kumverana chifukwa choopa ndi kulemekeza Khristu.4) Afilipi 2:3,4 – Muwatenge ena onse monga ofunikira koposa inu.5) Yohane 13:3-17 – Sambitsanani mapazi anu.2. Sitingathe kubwezeretsa ubale womwe taononga – Mateyu 18:6.A. Malipiro kwa olakwayo:1) “Kuli bwino amizidwe m’nyanja yakuya.”2) Mulungu sadzamva pemphero lake – Mateyu 5:23,24; Ahebri 12:14.B. Mtengo kwa ena onse okhudzidwa.1) Abale apabanja – kuwawidwa2) Mpingo – kupatukana3) Osakhulupirira - kukanidwa – Yohane 17:20,21; Afilipi 2:14-16.C. Musalole kukhala woyambitsa udani kapena kukana kuthetsa zolimbana – Aroma 12:18.1) Konzani msanga tolakwika ting’ono-ting’ono pa ubale wanu madzi asanafike mkhosi.2) Pezani njira zothandiza kuti mukonze ubale molumikizana.3) Limbikirani kuonetsa chikondi. Bwezerani chabwino ku choipa – Aroma 12:17,21.4) Musaumirire pa ufulu wanu – mungadzaupezenso.5) Mudzadalitsidwa – Mateyu 5:9.3. Muyenera kuganizira ndi kuthana ndi zonse zoyambitsa maudani ndi kukhumudwitsa – Mateyu 18:7-14.A. Kuganizira gwero la zolakwirana: Kodi inu muli ndi gawo lanji pa kulimbanako? Mateyu 7:1-5.1) Ndi milandu yochepa yomwe wolakwa amakhala mmodzi.2) Yang’anani bwino mopanda kukondera chomwe chakhumudwitsa mnzanu, mwana, kholo,mbale, ndi mlongo wanu.3) Kodi zochita zanga pankhaniyi zimaonjeza bwanji moto wa nkhani?a. Mwina zolakwa zamnzangayo sizachilendo kwenikweni, koma momwe ndazitengerandi momwe muli moonjezera mafuta pa moto.b. Mwina ndimaganizira kwambiri za ufulu wanga.c. Ena sadzasiya kuchimwa. Kuthetsa kwake kuyenera kukhala malingana ndi momwendiitengera nkhaniyo.Umodzi 10

d. Ichi ndicho chinsinsi cha ufulu ndi mtendere.B. Kuchotsa zoyambitsa kulakwirana:1) Kuyankhula (dula dzanja lako, kolowola diso) kumasonyeza changu chochotsera zoyambitsauchimo ndi kulakwirana. Mizimu ikutayika.2) Kudzitamandira ndi kudzikonda kwanga sikuli koyenera.3) Chikondi ndicho chidzalipira mtengo wa mtendere ndi kuyanjananso.a. Yesu analipira msonkho womwe sanayenera – Mateyu 17:24-27.b. “Bwanji osangololera kuti inu mukhale onyengedwayo” – 1 Akorinto 6:1-8.c. Abrahamu anangompatsa Loti mwayi woti iye asankhe malo okhalako poyambirirapopewa kulimbana – Genesis 13:8-11.4) Muthane nazo zolakwiranazo tsopano – musalorele kuti kudzitamandira kwanu ndikudzikonda kwanu kuononge mwana wa Mulungu – Aroma 14:13,15,19,21.4. Tsatirani ndondomeko ya Mulungu yothetsera zolakwirana – Mateyu 18:15-20; 5:23-26.A. Pitani kwa yemwe wakulakwiraniyo ndi kumuuza iyeyo osati ena ayi.1) Timangofuna kuuza wina aliyense chifukwa cha mkwiyo wathu.2) Anthu ambiri amathamangira kuuza akulu a mpingo asanaonane ndi wowalakwirayo.B. Pitani modzichepetsa ndi modekha – Agalatiya 6:1. Mkwiyo umapangitsa kuti munthu winayoayambe kudziteteza ndipo amayamba kudzikonzera njira zodzitchinjiriza nazo.C. Chitani zimenezi mwachangu, mkanganowo usanakule, usanakhudze ena, ndipo mitima isanafikepolimba.1) Timalandira chilango chowawa pokana nzeru ya malemba.2) Kulimbana kumakhala zaka zambiri mwinanso mpaka moyo wawo wonse chifukwa chakunyada.3) Koma ngati pali chikondi chokwanira ndi kukhudzidwa pa moyo wabwino wa pa banja pake,mpingo, kuntchito, anthu atha kupeza njira.5. Khululukani monganso Mulungu anakukhululukirani. – Mateyu 18:21-35.A. Kukhululuka kulibenso china chofaniziridwa nacho, ngati tifuna kupulumutsidwa – Mateyu6:12,14,15.1) Kusakhululuka ndilo “tchimo losakhululukidwa” lomwe tingalichite.2) Nchifukwa chiyani tidzayembekezera kuti Mulungu atichitire ife zomwe sitingachitire enawo?3) Kubwezera kuli kwa Mulungu – Aroma 12:19.B. Kukhululuka ndi “mchitidwe wokhala ndi cholinga” osati wongomverera m’thupi ayi.1) Monganso chikondi, ndi lamulo lachikhalire.Umodzi 11

2) Titha kuganizira zosankha kuchita mchitidwe wokhululuka. Kenako tidzayamba kumva m’thupi.C. Kusakhululuka kumangolekerera ubale ukumangosweka.1) Kuwawirana mtima pakati pa mwamuna ndi mkazi komwe kumangokhala osapezeredwa njirayothetsedwa kumasakaza banja. (Ngakhale kuwawirana mtima kwa kholo, mbale, mlongongakhale wina aliyense).2) Mkwiyo ndi kuwawirana mtima kwathu kumapatsa Satana mwayi m’miyoyo yathu – Yakobo1:20; Aefeso 4:26,27.D. Kukhululukirana kumabwezeretsa ndi kuchiza maubale owonongeka.1) Ngati wina apempha chikhululukiro, tiyenera kutero nthawi yomweyo kuchokera pansi pamtima, popeza nafenso ndi ochimwa.2) Mzimu wokhululukira umakhala wofunikira munthu winayo asanalape.a. Khristu anapempherera iwo omupachika – Luka 23:34.b. Mzimu wokhululukira sufulumiza kuchita choipa – 1 Petro 4:8; 1 Akorinto 13:6,7.c. Pamene munthu mmodzi ali nawo mzimu wokhululukira ndipo abwera poyera,zimapangitsa kuti winayonso abwere poyera.Mawu otsiriza: Pamene tikuchita ndi zolakwirana, tikupemphedwa kuti “tithetse zoipa ndi zabwino.” – Aroma12:20,21. Chabwino chomwe muchita chidzasungunula mtima wa yemwe munali kulimbana nayeyo – 1Samueli 24:26.Umodzi Pakati pa Ogwira NtchitoGawo Lachiwiri: Pamene Ogwira Ntchito Mumpingo Alekana Maganizo.Kodi bvuto lalikulu mumpingo ndiliti? Pa za utumiki? Akulu ambiri amaganiza kuti bvuto lalikulu ndi lamaubale a pakati pa atsogoleri. Mipingo yambiri yaonongeka chifukwa chakulimbana pakati pa akulu ampingokoposa mabvuto ena monga ankhuli yachiwerewere kapena zanyanga ndi ufiti.1. Ogwira ntchito mumpingo ayenera kuphunzira kusamalira ubwino wa ntchito ya Khristu asanaganizire zazofuna zawo, ndiponso ayenera kudziwa ndi kuphunzira bwino magwero a zolimbana ndi kuthana nazozisanafike powasokoneza mwa uzimu, kusokoneza ntchito yawo, kukhumudwitsa ntchito ya mpingokumudzi ndi kumayiko akutali, ndi kulepheretsa kupulumutsidwa kwa miyoyo.Sitingathe kulipira mtengo wa kulakwitsa komwe kungabwere kwa ife ngati tilephera kuchita zimenezi –Luka 17:1-2; Yakobo 3:1.2. Akulu ampingo ayenera kuzindikira gawo la moyo wodzikonda poyambitsa zolimbana. Akulu ampingonawonso ali nalo bvuto limeneli monganso wina aliyense. Amishonale kapena ogwira ntchito ampingonthawi zonse ayenera kumagwira ntchito m'magulu. Tingathe kumanena kuti tikulimbana chifukwa“chofuna kutsata mfundo zokhazikika,” “zotumikira za mudongosolo”, kapena “nkhani zauzimu,”pamene nkhani yeniyeni iri, “kodi wamkulu ndani?” “kodi akulamulira ndani?” pakadakhala palibekudzitukumula, nkhani zinazo bwenzi zitathetsedwa.Mukaika atambala awiri mukhola lankhuku ndiye kuti mukhala nkhondo yafumbi mpaka adziwike mwiniweniweni wolamulira kholalo. Ndi kuganiza kuti palibe kusiyana pankhani ya nkhukuyi. Ku thupi ifensoogwira ntchito mumpingo tiri chomwecho pachilengedwe. Koma izi zisakhale chomwecho kuuzimu. Ndimfundo za Khristui ndi kukhwima mu uzimu kwa Mkhristu kokha komwe kungathe kuthetsa mabvuto aubale wa ogwira ntchito mumpingo. Ine kusagwirizana kudzakhalapobe koma zisafike poti mpakakuononga kapena kufooketsa ntchito ya Mulungu.Umodzi 12

3. Ngakhalenso ophunzira anali kukumana ndi nthawi zina zomwe panali mabvuto osiyana maganizo pakatipawo. Paulo ndi Barnaba anafika poti aliyense amayenda m'njira yake yake, komabe anapitirira kusungandi kusamala ubale wawo monga abale – Machitidwe 15:36-40 (sikukadakhalakotheka kuti athe kufalitsa uthenga wabwino modalilika ngati akadalephera kuyanjana wina ndimnzake). Pamene Petro analakwitsa, Paulo analimbana naye kwambiri – Agalatiya 2:11-14. Koma anthuawiriwa anaconda ndi kulemekezana kwambiri – 2 Petro 3:15.4. Anthu odzikhulupirira okha ndi kudzitukumula, omva za iwo okha, omwe amati akakumana ndimaganizo olekana ndi awo, nkumaona ngati ali pa chiopsezo, asamasankhidwe pa udindo uliwonse mumpingo.Malembo amati “woyang’anira asakhale womva za iye yekha.” (Tito 1:7). Koma akhala “wodzadzidwandi Mzimu Woyera.” (Machitidwe 6:3) mphunzitsi sangathe kutumikira ena ngati iye alibe chipatso chaMzimu Woyera. Umodzi “ndi wa Mzimu” – Aefeso 4:1-3. Posankha a mishonale kapena akulu ampingo,sikokwanira kwa munthu kukhala wodziwa kuyankhula bwino, kukonza zinthu mwadongosolo,utsogoleri, ndi kukhala wodalira kwambiri pa ziphunzitso kokha ayi. Zinthu zonsezi zimakhalazosafunikira ngati wosankhidwayo alibe mzimu wa Khristu – 1 Akorinto 13; Aroma 8:9. Pamenemukuganizira za munthu woti akutsogolereni, tadzifunsani nokha kuti “kodi munthu ameneyi amachitabwanji ndi anthu ena pa nkhani za ntchito za kumpingo? Nanga ku banja kwake?5. Pakati pa Akhristu ndi pakati pa atsogoleri, Yesu watiphunzitsa momwe tingathetsere kusiyana kwathukwa maganizo. Ogwira ntchito ampingo ndi atsogoleri ayenera kumazindikira zakuopsa komwekumakhalapo chifukwa chakusagwirizana pakati pawo popeza kumakhudza ntchito ya uthenga wabwino.Kuopsa kochotsedwa, kutaika kwa nthawi ndi mphamvu, kulephereka kwa mapemphero (Mateyu5:23,24; Ahebri 12:14); Kupunthwitsa omwe akadakhala Akhristu ndinso Akhristu aang’ono ndi ofooka– Yohane 17:21; Afilipi 2:14,15; Luka17:1,2.6. Ogwira ntchito ampingo ayenera kumanga mfundo yoti sadzalola kusiyana maganizo kwawo kutikuononge ntchito ya Mulungu.7. Atsogoleri ndi antchito ampingo ayenera kumatsata mfundo za malemba pokonza maubale osweka.Konzani ubale womwe wangoyamba kuonetsa zizindikiro zoonongeka zisanafike woipitsitsa. - Mateyu18:15-17; Agalatiya 6:1; Mateyu 5:21-26; Aefeso 4:26-27; Yakobo 1:19,20; Mateyu 7:2-5.8. Pewani chirichonse chomwe chimakulakwitsani ndi kuyambitsa zolimbana – Aroma 14:13,19,19,21;Mateyu 18:8,9.9. Pewani kudzitukumula – Aroma 12:16; Afilipi 2:3..10. Musakakamire pa ufulu wanu, Yesu sanachite choncho ayi – Afilipi 2:5-11; 1 Petro 2:21-25; Aroma15:1-3. Paulonso sanatero ayi – 1 Akorinto 4:10-13; 9:19-23; 2 Akorinto 12:15. Tonse timathakumverana wina ndi mnzake ndipo timaphunzitsidwa kutero – Aefeso 5:21.11. Pewani “kuyerekeza zinthu moipa” – kuyerekeza mongoganizira mopanda umboni weniweni – 1Timoteo 6:4; Yohane 7:24.12. Chikondi chimakwirira machimo ochuruka ndi zolakwika za unyinji – 1 Petro 4:8; 1 Akorinto 13:4-7.13. Khululukiranani wina ndi mnzake – Aefeso 4;31,32; Mateyu 18:21-35.14. Sungani chidzalo cha chipatso cha mzimu woyera – Agalatiya 5:22,23; Luka 11:13.15. Sankhani antchito omwe ndi obvomerezeka mogwirizana ndi maganizo a choonadi ndi mfundo zampingo pa ntchito zake. Ngati pali kusamvana mu nkhani zina, kambiranani zimenezi m'kanyumbakomatu popanda abale ena onse.16. Ngati nkhani zake ziri zazikulu mutha kuitana akulu ena odalirika kuti ayese kukuthandizani kukonzaUmodzi 13

zobvutazo. Nthawi zina mutha musiyitsa njira yanji, koma chofunikira kwambiri ndi choti anthu awiriolakwiranawo athetse nkhani yawoyo mwa uzimu ndipo akhaliranenso mwa mtendere pakati pawo komangati apitirirabe kusungirana mkwiyo m’mitima mwawo, chisomo cha Mulungu chiyenera kuchotsedwakwa iwo pa ntchito yawo ya mtsogolo.Takambirana za zosautsa, koma paliponse pamene mzimu wa Khristu uli mwa ogwira ntchito, zosautsa zonsezimathetsedwa zisanafike poipitsitsa. Mautumiki ena omwe amagwiridwa mogwirizana amathekanso, mongaanamchitira Paulo ndi anzake ogwira naye ntchito – Afilipi 3:16-17.Umodzi Pakati pa Ogwira NtchitoGawo Lachitatu: Kumanga Ubale Wabwino Pakati pa Atsogoleri AmpingoMawu oyamba: Mpingo utha kumayenda bwino, koma kenako ntchito imayamba kusokonekera chifukwa chakukangana wina ndi mnzake pakati pa atsogoleri. Ntchito zambiri za pa mpingo zimalowa pansi ndi kuzilalachifukwa cha kukokana komwe kumayambika chifukwa cha ziphunzitso zonyenga. Ife atsogoleri kupyolera mukufooka kwathu, chonde, tisaononge kachisi wa Mulungu. 1 Akorinto 3:16,17.1. Maganizo osiyanasiyana okhudza ubale pakati pa atsogoleri onse a mpingo (woyang’anira ndiwoyang’anira mnzake, woyang’anira ndi mlaliki, woyang’anira ndi mtumiki, ndi ena). Zambiri zamfundo zimenezi, zimathandizanso pa ubale apakati pa Akhristu onse.A. Chitani zonse mosakondera kapena kuyang’ana nkhope – 1 Timoteo 5:21. Aliyense ali nawoanthu omwe amakondwera nawo, komatu izi zisakhudze momwe muchitira ndi anthu enawo.B. Musamuyankhulire munthu mawu omwe simunayenera kumuyankhulira. Ndipo musayankhulechirichonse chokhumudwitsa chomwe chiri chosathandiza.C. Ganizirani ndi kusinkhasinkha zonse zomwe mwakonza ndi mawu omwe mwakonza kuti kodienawo akamva siziwapweteka m’maganizo?D. Musakhale odzitamandira nokha ndi kumva za inu nokha monga opambana – Aroma 12:3,16.E. Muzindikire zomwe zingautse, komanso zofooka za anthu ena pamodzi ndi zomwe amakondamaganizo awo onse. Yesetsani kusamalira zimenezi ngati nkotheka.F. Muzilolera zofooka za anzanu monga momwe mungafunirenso kuloleredwa pa zofooka zanu ndianzanu – Mateyu 6:14,15; Aroma 15:7.G. Zindikirani kufunika kwa mphatso iriyonse ndi luso m’thupi la Khristu – Aroma 12:3-8.Musayembekezere kuti munthu aliyense azingochita bwino nthawi zonse. Yamikirani mphatsoya munthu aliyense pa yekha koposa kumukana kapena kumunyoza chifukwa chakulepherakwake.H. Nthawi zonse perekani ulemu kwa iwo omwe ayenera kuulandira panthawi yake – Aroma 13:7.Khalani achangu potulukira zabwino zomwe ziri mwa anthu ena monganso momwemungachitire ndi zoipa mwayiwo. Mulibe ufulu wodzudzula zolephera, koma muyambemwabweza mangawa oyamikira ndi kulemekeza khalidwe labwino.I. Phunzirani ndi kuzindikira chifukwa chomwe munaonetsera khalidwe la mtundu umenewo kwaanzanu, ndipo muchotseretu moyo woipawo ku mbali yanu. Ichi chidzadalitsa moyo wanu wonsekuchokera pa nthawi yomwe mwa phunzira izi.J. Pa mkangano uliwonse, poyamba, inde movutikira, taonani ndi kufufuza mokhulupirika mbaliyomwe inu mwachititsa kuti mkanganowu ufike pamenepa, chomwe mumachita, ndipo kenakoyambani mwadzikonza inu eni ake – Mateyu 7:1-5.K. Fulumirani kukonza ubale ndi kubwezeretsa mgwirizano pamene kusamvana kungoyambaUmodzi 14

kumene, pamene anthu sanataye mafuno abwino kapena chikhulupiriro mwa wina ndi mnzake.Kukonza kumeneku kukhala chinthu choyamba kuganiziridwa. Ubale umasokonezeka chifukwaife timalolera kuti zitero. Anthu amakhala ogwirizana pamodzi chifukwa amatsimikira kuteromokondweretsa Yesu. Ayenera kutero.L. Ngati pali kusaganizirana bwino pakati panu ndi mnzanu pa nkhani ina, musayembekezere kutimnzanuyo ayambe kubwera kwa inu kudzapepesa. Yesu akuwauza olakwiridwa onse kuti iwoapite – Mateyu 18:15-17. Akumuuza wolakwirayo kuti apite – Mateyu 5:23-25. Palibe“weniweni woti akhale woyamba kupita”. Koma pitani ndi kudzichepetsa konse poopa kutimungaonjezere mabvutowo – Agalatiya 6:1. (Atsogoleri nawonso ayenera kudzichepetsa, lamulolimeneli lodzichepetsa silichotsera atsogoleri ayi). Muyenera kuuza mnzanu kuti “timangoonongantchito ya Mulungu ndi Kupunthwitsa ena ngati tipitirira kusungirana udani. Ine ndifuna kutitiyambe kukhalirana bwino iwe ndi ine. Kodi titani pamenepa?M. Khululukirani moonadi iwo omwe akulakwirani – Mateyu 18:21-35. Mulungusangakukhululukireni ngati inu simukhululukira. Zindikirani kuti kukhululuka sichinthuchongomveka m’thupi ndi m’maganizo mwanu chabe koma ndi chinthu chomwe munthuamachita kusankha kuti achite.N. Lumikizanani ngakhale mnzanuyo sakutero. Khalani okonzekera kulandira mnzanuyo, siyanichitseko chikhale chotsekula nthawi zonse.O. Chitani zabwino ndipo mukhale achifundo ngakhale mnzanuyo akuchitireni zoipa zotani.Musabwezere choipa ndi choipa chinzake, koma ndi chabwino gonjetsani choipacho – Aroma12:17-21.P. Mudzitha kukhala tcheru pofulumira kuona nthawi zomwe ena akumva kuwawa, kayakulimbana, ndiponso pamene akukumana ndi nyengo zowawa, ndipo muonetse mtimawachifundo. Musangokhala omangiririka ku zinthu zanu zokha zokondweretsa inu nokhampakana kuchita kuiwala osatha kuona mabvuto a ena.Q. Ganizirani njira zoonetsera chikondi ndi kuganizira ena. Chikhale cholinga chanu kuti nthawizonse mukhale monga wolimbikitsa ndi wochangamutsa munjira yomwe muyankhulira ndikuchitira.R. Muzikhala ndi maphunziro a Baibulo olongosoka ndinso mapemphero pamodzi ndi atsogoleriena onse. Izi zidzakuikani inu kufupi ndi Mulungu ndiponso pakati pa wina ndi mnzake.S. Khalani ndi nthawi zapadera zomachezerana, kubindikira pamodzi ndinso kusangalala ndiatsogoleri ena (monga mwa chitsanzo, mabanja awiri kuyenderana kumapeto a sabata). Izizimalimbikitsa ubale.T. Zindikirani kuti anthu ena ndi obvuta kumvetsa zinthu. Anthu ena samalola kuti chisomochiwasinthe kwatunthu mumtima mwawo. Zindikirani kuti muyenera kukhala ndi moyowodziletsa ndi wolimba kuti musaonetse kupsa mtima kwanu kwa anthu oterewa ndi cholingachofuna kuwaonetsa chitsanzo chanu chabwino ndi kutinso ntchito ya Khristu isasautsike.Yesetsani kutchinjiriza moyo wanu ndi kuusunga bwino poyambirira pomwe musanapse mtima –Izi zimakhala zosabvutirapoU. Ngati mukukaikira, nthawi zonse tsatirani lamulo labwino ndi loyenera kusungidwa iri:“muzonse, chitirani ena zomwe mungakondwere iwo atakuchitirani.” – Mateyu 7:12;tawerengani ndi kufaniziranso ndi Mateyu 22:39.2. Maganizo ena oti mlaliki achite nawo pankhani ya ubale wake ndi oyang’anira/abusa.A. Alemekezeni abusa ndi mawu ambiri. Ngati mungathe kuwalola kuti akuyang’anireni pa ntchitoUmodzi 15

yomwe mukugwira, teroni. Mutha kuyankhula nawo molimbikira mfundo yanu, koma nthawizonse munjira yaulemu. Ngati muli nawo bvuto, yankhula nawoni abusawo kapena mmodzi waiwo osati kuyamba kumanena za iwo ndi anthu ena.B. Musataye nthawi pomachita zionetsa kukondweretsedwa ndi mmodzi kapena ena a iwo. Izizingathe kuononga ntchito yanu ndi abusawo. Inde malinga ndi chikhalidwe cha munthu, muthakuzolowerana ndi abusa ena mosiyana ndi ena, komabe muyenera kupereka ulemu mofananakwa onsewo. Onanani ndi abusa osiyanasiyana mu nthawi zosiyanasiyana pa nkhani zomwesizisowa abusa onsewo pamodzi.C. Musanyengere abusawo kapena kuwachititsa kuti akukondeni munjira ya dziko kapena mwandale, koma yesetsani kukhala mbale wachilungamo ndi choonadi kwa onsewo.D. Musawapeputse abusa ngati inu munaphunzira bwino Baibulo kuposa iwo. Koma mugawanenawo zinthu zabwino mwa Ambuye pamene mungathe kutero, ndi kuwalimbikitsa kukula muuzimu. Zinthu zomwe mungagawane nawo zitha kukhala mabukhu, maganizo, makaseti a mawua Mulungu, ma autilaini, madongosolo, anthu ndi zina zotere.E. Mlaliki asataye nthawi ndi kulimbana ndi abusa chifukwa cha ulamuliro kaya kukondedwa.Ngati anthu amenewa, abusa ndi mlaliki ali wokhwima mu uzimu wa Khristu, iri silimakhalabvuto kwa iwo. Mwina ngati bvutoli liripo, aliyense wokhudzidwa achite ndi mzimu wake kumbali yake.F. Ziri kwa abusa kuitana alaliki ku misonkhano yawo kapena ayi. Koma sayenera kuitana mlalikiku msonkhano womwe nkhani yake iri kuyang’ana mlalikiyo. Komabe pamene pali ubalewabwino, abusa ambiri amasangalala poitana mlaliki chifukwa chakumvetsa kwake ndi udindowake pa mpingopo. Izi zimakhala zoona pamene abusa ake akuwetadi nkhosa mwa uzimu osatiomangochita misonkhano yongofuna kumanga mfundo wamba. Onsewo ndi ogwira ntchito ampingo, ndipo mlaliki monga wodziwa bwino za nkhosa zapampingopo, angathe kukhalathandizo la mtengo wapatali kwa abusawo popanda kusokoneza dera la udindo wawo.G. Alaliki omwe angosankhidwa kumene ayenera azibweretsa pang’onopang’ono maganizo awoakusintha kwa ntchito zina za mpingo. Perekani nthawi yokwanira musanayambe zina, poonetsaulemu.H. Ngati mpingo umapereka chithandizo kwa mlaliki, mlalikiyo ayenera adzigwiradi ntchitoyo.Popeza nthawi zambiri amagwira popanda woyang’anira, ayenera aziyambitsa yekha ntchitozambiri. Ayenera kumagwira ntchito nthawi yake yonse ngati alandira chithandizo pa zosowazake zonse. Mlaliki asamajombe pa ntchito ya mpingo chifukwa cha ntchito zake zathupi kayabizinesi yake. Nthawi yomweyonso, abusa ayenera kuzindikira kuti kufunika kwa mlalikikumasinthasintha malingana ndi nthawi, choncho sangathe kusunga dongosolo lokhazikika(ngakhale kuli koyenera kuti azisunga dongosolo labwino). Ngati mlaliki ali wodzipereka nthawizonse, abusa asamuimbe mlandu ngati nthawi zina agwira ntchito zapakhomo pake munthawi inyatsiku lomwe kulibe ntchito zazikulu. Ayenera kukumbukira kuti amagwira ntchito munthawizambiri zausiku posawerengera masana ndi zina zotero. Koma izi zisachitike mopitirira.I. Mlaliki ayenera kuchita dongosolo lomadziwitsa abusa pa kusintha kwa madongosolo a ntchitozake monga maulendo opita kwina, maulaliki a nyumba ndi nyumba, ndi zina zotero, ngakhalengati maulendowo anali obvomerezeka. Izi zimathandiza kupewa kusamvetsetsana.J. Ayeneranso kupereka dongosolo lokambirana ndi abusa mfundo ziri zonse zazikulu zomweafuna kuchita, zomwe ziri zoyenera kukambidwa pakati pawo.K. Mlaliki ayenera aphunzire kusunga chisomo pamene mfundo zomwe anakonza zakanidwa ndiabusa. Abusa angathe kumva zinthu mosiyana ndi momwe iye akumvera, komabe munjirairiyonse, palibe yemwe adzingokhalira kuchita zake zokha nthawi zonse. Mlaliki asakhalewowinya ngati mfundo zake sizinamveredwe.Umodzi 16

L. Ngati mbusa mmodzi kapena abusa angapo nthawi zonse angotsutsa kapena kulimbana ndimfundo zonse zomwe mlaliki apereka, pamenepa mlaliki angolimbikira pa mfundo zomwe iwoagwirizana nazozo kuti poteropo ayambe kubwererana pafupi ndi kumvetsanapang’onopang’ono. Kuganizirana zina ndi zina kungathe kuzima ngati mlaliki atsatira njirazobweretsa chiyanjano nayesa mwa choonadi kukondweretsa enawo. “Gonjetsani choipa ndichabwino” – Aroma 12. Musalole maganizo owawa akhazikike mkati mwanu poganizira mbusakapena abusa, chifukwa izi zidzalepheretsa kuti mugwire nawo bwino ntchito.M. Mlaliki ayenera kuyesetsa kumvera zomwe abusa afuna momwe angathere, ndipo ndi mtimawofunadi. Koma ngati ali ndi bvuto lachikumbumtima ndipo sangathe kuchita zomwe iwo afuna,ayenera wachifundo koma moona mtima kufotokoza bwino kwa iwo ndi kupempha kuti ayesekumukomera mtima. Ngati apempha mwa mzimu wabwino, iwonso adzamumvera ndikulemekeza pempho lakelo. Chirichonse chingatheke kukonzedwa pokambirana munjirayabwino popanda kukhumudwitsana.N. Ngati pali bvuto lalikulu pakati pa mlaliki ndi mpingo kapena abusa loti kusiya ntchito yakekungakhale ngati njira yabwino, ayenera kukambirana moona ndimosasuka ndi abusa ndipo iwoonse pamodzi ayesere njira zonse zoti ziwathandize kukonza ndi kuthetsa bvuto lawolo.Chimodzi modzinso ngati bawo abusa ali ndi bvuto longa lomweli ndi alaliki.O. Nthawi zina njira yothandiza imakhala yosiya ntchito – Machitidwe 15:36-41. Ngati mlalikiwaona kuti nkwabwino kupuma ntchito, ayenera kutero popanda kuyambitsa maganizo achabekapena kugawanitsa mpingo. Pa nthawi yobvuta imeneyi, zambiri zidzadalira momwe iyeasungira lirime lake. Ndipo ngakhale kuti abusa ndi mlaliki agwira ntchito zolekana kuyambirapamenepa, iwo ayenerabe ngati nkutheka kusunga ubale weniweni. Ayenera kukhazikitsa ubalendi Chiyanjano asanalekane.P. Pamene mlaliki ndi mpingo alekana, pasapezeke m’modzi wonenanena zambiri kwa akunja ndionse omwe siziwakhudza mosayenera kapena kusiya mbiri yachabe.Q. Mlaliki ayenera apereke nthawi yokwanira kuti mpingo uthe kupeza wantchito wina, ndipompingo uyenera kumpatsa mlaliki nthawi yoti akonze madongosolo atsopano.R. Alaliki ndi abusa ayenera kukhala ndi zolembera za mapangano awo pa zomwe winaangayembekezere kwa wina pofuna kupewa zosagwirizana zina ndi zina.3. Maganizo ena oti abusa achite nawo pankhani ya ubale wawo ndi alaliki.A. Yesetsani kumvetsa ndi kulemekeza maganizo a mlaliki, ngakhale pamene simubvomerezananawo nthawi zonse.1) Nthawi zonse mlaliki amakhala kuti anaphunzitsidwa kuyesetsa kugwiritsa ntchitomalemba mobvomerezeka pofunafuna ndi kukulitsa mizimu yambiri. Nchachidziwikirekuti abusa sangamvere maganizo onse omwe mlaliki angapereke, koma pomangotsutsanthawi zonse ndi kumangonena-nena za maganizowa, abusa amakhumudwitsa ndikugwetsa mphwayi antchito achinyamata abwino ndipo nthawi zambiri kupangitsa kutiasiye ndi kuchoka m’chiyanjano chathu kapena kusiyananso utumiki kwathu. Abusaayenera kupewa msampha wodziona ngati atetezi a zochitika kokha. Abusa nawonso ndiatsogoleri ndipo monga achitira mlaliki ayeneranso kumafunafuna njira zoberekerazipatso.2) Abusa ayenera kubvomereza kuti ndi momwe zimakhalira monga mwa chilengedwe kutimlaliki amakhala ndi maganizo amphamvu, atsopano. Ena. Ena amakhala abwino, enaayi. Abusa ayeneranso kukumbukira kuti kumatheka kuti mbusa akhale ndi maganizoakale otopa, kukhala wozolowera zomwe zomwezo, kuopa kugwira ntchito mwamphamvu, kapena kuwalola kuchepetsa kapena kusiya kumene kulamulira magawo enaantchito yake. Abusa ayenera kukhala ndi maganizo sinthika pa nkhani zimenezi ndiUmodzi 17

zizolowezi zimenezi. Atatero ndiye kuti zidzamuthandiza kugwirizana bwino ndi mlalikindipo zidzamthandiza kubvomereza pamene alaliki akana kulandira maganizo ake.B. Abusa ayenera kulemekeza maphunziro ndi zonse zomwe mlaliki adziwe, mphatso ndi malusoosiyanasiyana a mlaliki. Ngakhale sangathe kubvomera zonse, ayenera adzikhala ndi chidwichomvera moona maganizo akewo. Nati afuna kukonza bwino kapena kukana kumene maganizoamlaliki, ayenera kutero m'njira yoti sikhumudwitsa mlaliki. Kudekha ndi kudzichepetsa ndizofunika kwa abusa monga ziriri kwa Akhristu ena onse.C. Abusa ayenera kuganizira za zosowa za mlaliki pachuma ndi nthawi ndi banja lake. Ayenerakumlimbikitsa kuti aziwauza za zosowa zake momasuka ndi moona. Utumiki wakeumamutengera nthawi yake yokhala ndi banja lake, ndipo abusa ayenera kumamvetsa pamenemlaliki asowa kuchitako zina za kubanja kwake. Abusa ayenera kukonza dongosolo la masikuomwe mlaliki ayenera kupuma ndi nthawi yoti ayendere malo ena monga kupumula.D. Abusa ayenera kukonza dongosolo loti amve maganizo a mlaliki pa za alaliki ena omweangaitanidwe ku misonkhano ndi zokambirana zina. Mlaliki angathe kudziwa zomwe abusaasoweka kuti adziwe pa za kufunika kwa mlaliki woitanidwayo pa ntchito ya pampingopo.E. Ngati mlaliki akulakwitsa, abusa ayenera kumuthandiza modekha koma mwa chimvekere kutiathe kuona zomwe akuchitazo. Ayenera kugwiritsa ntchito njira yomwe ingamulimbikitse, osatinjira yomwe ingamuvulaze m’maganizo.4. Maganizo ena othandiza abusa pamodzi ndi alaliki.A. Ayenera kumalowa ndi kuchita maphunziro pamodzi, kupemphera pamodzi ndi kulowam’bindikiro pamodzi kuti athe kuphunzira ndi kufunafuna cholinga cha Mulungu kuti athekulunzanitsa maganizo ndi mitima yawo ku zolinga ndi njira zofanana.B. Abusa ndi alaliki ayenera kumazidziwa okha, akhale omvetsa zokhumba zawo zomwezingaonetse kudzikonda, ndipo azindikire zonse zomwe zingawafooketse kapena zofooka zawozimene, zamkati mwawo zomwe zingawapangitse kuti akhale odzimva mopitirira kapena kufunaulamuliro mopitirira. Ayenera moganiza bwino ndi mwachangu kuthana ndi zizolowezi zimenezikuti mwina izi zingaononge ntchito ya Yesu ndi kusokoneza mizimu. – 1 Akorinto 3:16,17.C. Umodzi pakati pa abusa ndi alaliki uyenera ukhale woti mpingo wonse uchitire umboni mongachitsanzo chabwino. Ngati pabuka kusamvana pankhani zina, chonde, zimenezi zisadziwike ndiena onse koma zikhale monga chinsinsi pakati pa atsogoleri kufikira njira yothetsera itapezeka.Abusa ayenera kuthandizira mlaliki monga momwe angathere pamaso pa mpingo mongansomomwe mlaliki naye angachitire.5. Maganizo ena othandiza pakati pa mlaliki ndi alaliki enawo.A. Ngati alaliki awiri agwirira ntchito pamodzi, nchachidziwikire kuti zikhala ngati zija za atambalaawiri mkhola limodzi. Amalimbana mpaka mmodzi aoneke wamwamuna. Moyo umenewuwomwe ndi wathupi, wokonda kulimbana, ulibe malo ndi nthawi pakati pa antchito a Yesu ndipouyenera kuthetsedweratu mwa kulapa ndi mzimu woyera. – Agalatiya 5:19-26.B. Mlaliki ayenera kutaya khalidwe lonse la nsanje ndi kaduka pa mlaliki mnzake yemwe ali ndinzeru ndi maganizo oposa mnzakeyo. Iye ayenera kukondwera chifukwa mlaliki mnzakeyoakutha kutumikira Mulungu mwangwiro. Dziwani kuti tonse tiri m’gulu limodzi.C. Mlaliki asataye nthawi yake pomabvutika mumtima chifukwa mlaliki wina akuthandizidwakapena akulemekezedwa bwino, kapena akuchitidwa bwino munjira iriyonse. Mtumiki waMulungu akhale wokhutitsidwa pololera kuti Mulungu akhale wokonza ndi Kulongosola zaulemu ndi thandizo lomwe iye angalandire, ndi bwino kungoganizira kwambiri za ntchito yakeyotengera chipulumutso cha Yesu kwa anthu. Tiyenera kutaya ufulu ndi ulemu wathu mongansoUmodzi 18

adachitira Yesu – Afilipi 2:5-11; Yohane 3:26-30.D. Mlaliki yemwe ndi mlendo pa malopo ayenera kutsogoleredwa m’njira iriyonse yofunikira ndimlaliki wa pamalopo, iye ndi yemwe angalondolere kwa anthu omwe ayenera kuyenderedwa, ndizina zotumikira za uzimu pa mpingopo, ndi zina zotero. Mlaliki wodzachezayo, ngati ali ndimzimu wabwino, amabwera kudzatumikira, ndipo adzabvomera maganizo amlaliki wapamaloyo.Mawu otsiriza: Nkutheka kuti kudzera mu ubale wapakati pa anthu kuposa m’njira iri yonse, atsogoleri ndiwoali ndi mwayi woonetsa dziko zoonadi ndi kukoma kwake kwenikweni kwa ziphunzitso za Ambuye wathuYesu Khristu.Umodzi Pakati pa Ogwira NtchitoGawo Lachinayi: Zomwe Tingachite ndi Zolimbana.Yesu nthawi zonse ankachenjeza ophunzira ake za mabvuto, zotsutsa ndi za mayesero omwe atumiki ake analikudzakomana nawo. Sanayesere ndi pang’ono pomwe kungowaika m'masamba kuti iwo aganize kuti iwoadzakhala akupambana mosabvuta ndi mwa chisangalalo – Mateyu 10:16-42; Luka 9:57-62. Koma iyeanawalonjeza za chisomo ndi thandizo loti adzathe kuchita bwino, ndipo anawaonetsa kuti adziwe kutintchitoyo pamodzi ndi mphoto yakeyo ndi zoyenera kubvutikiridwa. Nkhondo ya uzimu ifanana ndi nkhondozina zonse. Pamakhala kulimbana, zobvuta ndi zoopsa zomwe. Komabe iyenera kukhalapo basi ndipokoyenera. Msirikali aliyense amakhala ndi zolinga ziwiri pa nkhondo yake, choyamba chimakhala chofunakugonjetsa mdani, ndipo chachiwiri kudziteteza kuti asagonjetsedwe.1. Momwe tingachitire ndi zotsutsana.A. Tiyenera kukonzekera kukomana ndi zolimbana – 2 Timoteo 3:12; Luka 6:22-26; Mateyu10:16,34-36; Machitidwe 20:23; 1 Akorinto 16:8,9; Marko 10:29,30; Aefeso 6:10-12; 2 Timoteo2:3; Yohane 3:19; Yohane 15:20.B. Kutsutsana kulipo kwa mitundu ndi mphamvu zosiyanasiyana.1) Kwina ndi komwe mumachita ku kuyamba nokha chifukwa cha kupusa kwanu, kufookakwanu kapena kuchimwa kwanu.2) Kwina ndi komwe kumachokera kwa abale ofooka komabe olimbikira omangiririka kuziphunztso ndi zizolowezi za anthu, kusakhwima kapena kukhala ndi mtima wokhulupirirakwambiri zinthu zadziko. Tawerengani Mateyu 16:21-23; ndipo mufanizire.3) Kwina ndi komwe kumayamba pamene muputa anthu omwe ndi omangiririka kuzolimbana, zofuna zawo ndi osakasaka chisangalalo ndi ulemerero.4) Kwina ndi komwe kumayambitsidwa ndi choipa chomwe chimakhazikika kwa anthu komandi kumaoneka ngati ndi chauzimu.C. Dongosolo lothandiza pochita ndi kugonjetsera zotsutsana pa utumiki wanu wa Yesu.1) Nthawi zonse muyambe ndi kupempha nzeru kwa Mulungu, ndi kukhulupirira Iyeadzaperekadi – Yakobo 1:5-8 (kutsutsa kumatithandiza potipangitsa kuti tidalire Mulungu).2) Yeretsani moyo wanu ndi mtima wanu kuti mukhale okhulupiriradi za Chiyanjano chanundi Yesu ndinso chithandizo chake. “musasiye malo ena alionse, ngakhale kufooka kwinakuli konse kwa mzimu.” – Aefeso 6:10-18; Yohane 14:30.3) Chotsani mwa inu chirichonse cholakwika chomwe chingathe kumayambitsa kapenakuthandizira pa zotsutsana – Machitidwe 24:16; 1 Akorinto 10:31-33; 11:1.Umodzi 19

a. Mwapemphero, moona, fufuzani moyo wanu ndi womwe mumafikira enawo – 2Akorinto 13:5; Mateyu 7:5. Kodi mumangochita zinthu potsatira zomwe thupi ndimaganizo anu afuna mosalingalira bwino, kodi mumachita zinthu mopupuluma, kodimukusowa moyo wa chisomo pa makhalidwe anu, kodi mukusowa kudzichepetsandi kuupeza mtima, kusagwirizana ndi zina, kukondera, kukhulupirira ndi kumvazanu zokha? Kutsutsidwa kumatithandiza kuti tikhale ndi mwayi wokonzanso moyondi khalidwe lathu.b. Ngakhale pamene mnzathuyo watilakwira, tiyeni tidzifulumiza kupeza njirayothetsera bvutolo ife tokha. Kumakhala kobvuta kuti tiwasinthe ena mwa msanganthawi zonse, koma mungathe kudzisintha nokha, kusintha momwe muchitira ndiena akakulakwirani ndinso machitidwe anu pa nthawi yotsutsidwa.4) Khalani msirikali wodalira nkhondo – Aefeso 6:18; Akolose 4:12. Pemphero lawolungama lingathe kuchotsa mapiri a zolimbana – Marko 11:20-25. Pamene muli ndibvuto lalikulu, chitani nalo mwa kusala kudya ndi pemphero (komatu mukhale oupezamtima ndi okhazikika m’maganizo pa kusala kwanuko – chifukwa njirayi iribe tsenga lirilonse.) Mulungu amakonda mapemphero a iwo amene amakonda mpingo ndi mizimu yaotayika ndi ofooka.5) “Pita kwa mbale wako” – Mateyu 18:15-17; 5:25; Aefeso 4:26-27. Musanene kwa enazambiri za yemwe akukutsutsaniyo – yankhula nayeni. Konzani zolimbana zanumwachangu zisanafike poopsa, makamaka pamene mwangoyamba kumene kudabwa,musanayambe kukayikirana koti zinthu zifike pobereka uchimo waukulu. Konzani msangaming’alu ya ubale wanu isanasanduke mipata yaikulu ndi kugwetsa khoma lonse. Komapitani ndi kudekha konse – Agalatiya 6:1. Mapitidwe amenewa amafunika kudzichepetsa.Ngati mutatsatira njira imeneyi yolumikizana ndi mbale wanuyo, kuphatikizana ndikupepesa kwanu, ndiye kuti mbale wanuyo adzakhala ndi mwayi waukulu womvetsamomwe inu mumamukondera. Ngati muchita ndi zolimbana zanu mwathupi osati mwamalemba, ndiye kuti zimangokhala ngati mwapereka mwayi wothira mafuta anyali pa motowa mumtima mwa yemwe mukutsutsana nayeyo. Pewani kutsutsana ndi kulimbana poyera,koma ngati zingatheke zosakhudza mpingo ndi ubale wanu.6) Musalimbane kapena kuchita makani – Mateyu 12:18-21; 2 Timoteo 2:24-26. Gwiritsanintchito kudandaulira mwachikondi ndi choonadi choperekedwa mwa chifatso.Musatengeke mtima ndi kuyamba kuonetsa khalidwe lofanana ndi yemwe akukutsutsaniyolomwe ndi loipa. Musabwezere choipa ndi choipa – Aroma 12:17-20. Musachiyesechosangalatsa ngati mugonjetsa mnzanu molimbana.7) Funani Mzimu Woyera kuti uthandize inu ndi anzanu, chifukwa umodzi ndi wa Mzimu –Aefeso 4:3; Agalatiya 5:22,23; 2 Akorinto 13:14; Luka 11:13.8) “Gonjetsani choipa ndi chabwino” – aroma 12:21. Pemphererani adani anu. Kumbukiranichitsanzo chomwe Ambuye Yesu anaonetsa pamene anazunzidwa ndi kunyozedwa – 1Petro 2:21-25. Perekani ka Mulungu zolinga zanu zonse, nthawi zonse chitani zabwinondipo wongolerani bwino mzimu wanu. Palibe chifukwa chokubvomerani kuchita zoipachifukwa choti winanso akuchita zoipazo. Kuchitidwa zoipa chifukwa choti muli ndimzimu monga wa Ambuye Yesu ndi phunziro lalikulu lomwe mudzayenera kuchita.9) Phunzirani kunena zoona zokhazokha momveka bwino ndi mwachikondi. Aefeso 4:15.Mungathe kuyankhula muli monse mungafunire ngati muyankhula mokhoza ndimwabwino. Yankho loperekedwa modekha limatha kuthetsa kulimbana – Miyambo 15:1.Mzimu amatithandiza kuyankhulana ndi kumvana bwino mothandiza ndi moombolana.10) Zoyambitsa kulimbana zina ndi zoti mutha kungozinyalanyaza ndi kuziiwala ngatimwayesa yesa njira zinazo – Nehemiya 6:1-13.Umodzi 20

11) Ngati abale ali otsamira ndi kukhulupirira kwambiri pa miyambo ya makolo komabekwinaku ali nacho chikondi cha pa Mulungu, ziripo njira zina zomwe inunso mungachitepopanda kuwalakwira, kapena palinso njira ndi nzeru zina zomwe mungathe kukwaniritsazabwino pamene mukudikira ifike nthawi yoti njira itsekuke. Mudziganizira zachikumbumtima cha abale monga momwe mungathere (Ngakhale kuti izi zichitikemolingana ndi udindo wanu pamaso pa Mulungu kuti mukathe kufikira otayikawo munjiraya uzimu.)12) Samalirani pa zomwe mumayankhula kwa anthu pokhuza za omwe amakutsutsani. Ngatisimusamala mungathe kufesa mbewu zamnyozo chifukwa anthutu amamva zinthumwachangu. Mudziwenso kuti zomwe muyankhulazo tsiku lina zidzapeza yemwemukumunenayo.13) Muzolowerane ndi osadziwa ndi ofooka powaphunzitsa modekha ndi mofatsatsirira bwino,kuwadyetsa ndi kuwaonetsera chitsanzo chabwino. Pamene ofookawo ayesera kuchitakobwino, ayamikireni.14) Dandaulirani mfundo zomwe inu ndi okutsutsaniwo mungathe kugwirizana ndipomulimbike kugwira ntchito mu mfundo zimenezi ndi mtima wonse.15) Taphunzirani ndi kuona momwe Yesu ndi ophunzira ake anamchitira ndi nthawi zobvutazomwe anali kutsutsidwa. Kodi ndi nthawi ziti zomwe anali kukana kugonja? Ndipo ndinthawi ziti zomwe anali kulolera kufooka kwa anthu?16) Samalirani mwakuopa Mulungu momwe muweruzira okutsutsani, makamaka pa zokhudzamaganizo awo – Yohane 7:24; Mateyu 7:1-5; Yakobo 2:12,13. samalirani kutimusafulumize kukhulupirira zomwe mumva za miseche yochokera kwa olimbana nanuwo.Fufuzani kokwanira musanagwiritse ntchito zokumvazo.17) Chenjerani kuti pasayambike magulu kapena timabungwe pakati pa abale ndi alongochifukwa chokhala ndi maganizo osiyana pakulimbana. Musakolezere moto pakutsutsanandi kulekana kwa anthu.18) Pezani malangizo kwa oyera mtima odalilika ndi atsogoleri a akulu.19) Musapangitse banja lanu kuti likhale ndi mkwiyo wa pa omwe mutsutsana nawowo kapenampingo chifukwa kayankhulidwe kanu. Phunzirani kupempherera ndi kufunira adani anuzabwino pamodzi ndi banja lanu lonse (pali nkhani zina zoti zimuyenera kukambirana ndiana anu aang’ono ndiponso zina ngakhale aakulu amene).20) Potsiriza, pamene mwa ona kuti kutsutsako kukuchokera mkati weniweni mwa choipa,ndipo mfundo zofunikira kapena mtendere wa ntchito za mpingo ungathe kusokonezeka,iripo tsopano nthawi pamene zonse zalephereka yochotsera choipacho ndi kufotokozeramomveka bwino, posiya matsutso agwere komwe ayenera kugwera – Mateyu 23;Machitidwe 13:6-12; Agalatiya 2:11-13.a. Muyenera mutsikize kuti mukulondola ndi kuti mfundo za mpingo zikuopsezeka.b. Tengani maganizo a anthu a mtima wolondola.c. Mukhale okonzekera kulandira zotsatira zake.d. Yesetsani kupanga zoti zisasokoneze kwambiri mpingo (mwa chitsanzo, ngati musiyautumiki wanu, ndi chanzeru kuchoka ndi kumakasonkhana ku malo ena ampingowomwewo wa Yesu koposa kukhala chida chothandiza kugawa anthu).e. Yesetsani kuti ubale wanu wonse ukhale wosaonongeka kuti ubale wanunso ndiMulungu usaonongekeUmodzi 21

21) Perekani moyo wanu ndi zolinga zanu kwa Mulungu – 1 Yohane 4:4; 1 Petro 2:23;Masalmo 23:5.22) Lolerani kulakwiridwa kapena kulakwira chifukwa cha Mulungu ndi cholinga chake, komaosati chifukwa chofuna kukwaniritsa zolinga zanu. Muzidziwa kusiyana kwake!Mu utumiki, zambiri ndi zosautsa ndi zokhumudwitsa. Komabe zimenezi sizingafanizidwe ndi chisomo chaKhristu Yesu chomwe chaperekedwa kuti chitithandize ngakhale ndi chisangalalo chomwe utumikiwopambana umabweretsa ku mizimu ya anthu.Phunziro 5: Umodzi mu Mpingo wa PamaloGawo 1: Mzimu wa Utumiki wa KhristuChinthu chapamwamba chopusa zonse pa mpingo womwe ndi wogwirizana kapena pa banja ndi moyowotumikira wa Khristu. Mabvuto ambiri m’mipingo ndi m’mabanja amabadwa kukuchokera ku uchimo,kudzikuza, ndi kudzikonda. Akhristu ali nayo njira yamphamvu yothetsera zimenezi kudzera m'moyo wa Yesuwomwe uyenera kumabadwa m’miyoyo yathu. Palibe njira zopezekeratu “za mayankho ododometsa” kumabvuto am’mipingo ndi m’mabanja ndiponso palibe lonjezo lirilonse lomwe lingabweretse kusintha kwazinthu popanda kudzipereka kwa Ambuye kuti atilamule. Koma pokhala pansi pa iye monga Ambuye wathundikutsatira chitsanzo chake, mipingo yathu ndi mabanja athu angathe kukhala ogwirizana monga momweMulungu anakonzera! Mu phunziro loyambali tidzayang’ana za maziko a umodzi, moyo wotumikira wa Yesu.1. Khristu anali nawo ufulu monga Mulungu wokhala kumwamba – Afilipi 2:5-7.; Yohane 1:1,2,14; 17:5.2. Khristu anasiya padera ulemerero wake mwakufuna kwake ndi cholinga chofuna kuti atithandize –Afilipi 2:5-8. “Iye anadzikhuthula yekhaA. Iye anabvomera pa chiyambi pomwe ndi Mulungu kuti adzachita zimenezi - Ahebri 10:4-7;tawerengani Aroma 15:3; 2 Akorinto 8:9; ndipo mufanizire.B. Izi zimafuna mphamvu zambiri koposa kuumirira ufulu wathu.C. Pamene tiri kuphunzira chikondi chosadziganizira wekhachi, cha Khristu, moyo umenewuwotumikirau, tidzatha kukhala ndi khalidwe lomwe mwa njira zina sitikanatha ndi kulikwanitsam’mabanja mwathumo.3. Khristu anakhala wotumikira (kapolo) – Afilipi 2:5-8.A. Pobadwa monga munthu – Yohane 1:14; Mateyu 1:23.B. Ponyamula zolemetsa ndi zosowa za anthu ena – Mateyu 8:1-4; Luka 7:11-15; Yohane 8:2-11;Marko 6:31-34; Mateyu 15:32; Luka 13:10-17; Yohane 5:1-15; Yohane 4:1-38; Luka 22:24-26;Yohane 13:3-17; Luka 23:39-43.4. Yesu anadzichepetsa yekha ndipo anamvera mpaka imfa ya pamtanda – Afilipi 2:8.A. Uku kunali kudzikhuthula kwake kwa Yesu m’moyo wake kwachiwiri.B. Imfa yake inali yodzipereka yekha, kutisenzera zolakwa zathu pamene ife tinali olephera –Yesaya 53:3-6.5. Popeza anataya ulemerero wake wonse kuti apulumutse ena, Mulungu anamukweza iye kopambana ndikumubwezera zonse mochuruka. – Afilipi 2:9-11. Ngakhale pakali pano akutisenzerabe zolakwa zathundi kutipempherera – Ahebri 7:25; 1 Petro 5:7.6. Yesu akutiimiranso ife kumoyo womwewo wodzikhuthula, wotumikira ndi cholinga chofunakupulumutsa.Umodzi 22

A. Kuti tinyamule zolakwa za ofooka ndi kuti tisadzikondweretse tokha – Aroma 15:1-3;tawerengani Machitidwe 20:35; 2 Akorinto 12:15.B. Kuti tikonde ena monganso Khristu anaconda ife – Yohane 13:34; tawerengani 1 Akorinto 13;Yohane 15:13; 10:11.C. Kuti tidzikhuthule ndi kunyamula mtanda wa Khalidwe lofuna kuombola ena – Mateyu16:24,25.1) Njira yekhayo yotsatira nayo Khristu.2) Dzikhuthuleni, osangoti machimo okha – Mateyu 16:24; Aroma 6:6; Agalatiya 2:20.3) Kunyamula mtanda tsiku ndi tsiku – Luka 9:234) Ngati titaya moyo wathu chifukwa cha Yesu ndi cha ena onse, timaupezanso.Mau otsiriza: Kodi ndingathe bwanji kukhala wopulumutsa monga anamchitira Yesu?1. Mthane ndi zoyambitsa kupunthwa ndi kuchimwa m’moyo wanu – Mateyu 18:6-9.2. Lapani ndi kusiya moyo wodziganizira nokha ndi kumaukonza nthawi iriyonse pamene muona kuti ufunakuyambiranso.3. Yang’anani kwa Yesu ndi uthenga wake ndipo pemphani thandizo la Mzimu wake – 2 Akorinto 3:18;Luka 11:13.Kusinthika kwanu kudzathandiza kuti banja lanu lonse lipulumutsidwe ndi kukonzeka. Nthawi zambiri banjalimasinthika chifukwa cha kusinthika kwa munthu mmodzi wapabanjapo.Gawo lachiwiri: Utsogoleri Wotumikira.Mawu oyamba: Yesu anaphunzitsa kuti utsogoleri wa mu ufumu wake ndi wosiyana ndi utsogoleri wa dzikolapansi.Ndipo kunakula kutsutsana mwa iwo, ndani wa iwo ayesedwe wamkulu. Ndipo anati kwa iwo, mafumu a anthuamitundu awachitira ufumu; ndipo iwo amene awachitira ulamuliro anenedwa, ochitira zabwino. Komasipadzatero ndi inu; komatu iye ali wamkulu mwa inu akhale ngati wamng’ono; ndi iye ali woyamba, akhalengati wotumikira. Pakuti wamkuru ndani, iye wakuseyama pachakudya kapena wakutumikirapo? Sindiyewakuseyama pachakudya kodi? Koma ine ndiri pakati pa inu monga ngati wotumikira. – Luka 22:24-27.Koma amene aliyense akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu; ndipo amene aliyenseakafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu; monga mwana wa munthu sanadzakutumikiridwa koma kutumikira ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri. – Mateyu 20:26-28.Wetani gulu la Mulungu liri mwa inu, ndi kuliyang’anira, osati mokakamiza, koma mwa ufulu, kwa Mulungu;osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu; osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhalazitsanzo za gululo. – 1 Petro 5:2,3.1 Yesu ndiye chitsanzo chathu cha utsogoleri wotumikira – Afilipi 2:5-11; Mateyu 20:28; Aroma 15:1-3.A. Momwe amachitira ndi unyinji.B. Anasunga nthawi yoganizira anthu osowa ndipo nthawi zonse ankakhudzidwa kwambiri chifukwa enakoposa momwe ankadziganizirira yekha.C. Ankasamalira osauka, osawerengedwa, akunja ndipo ankapeza nthawi yokhala nawo pamodzi.Umodzi 23

D. Sanadzikweza yekha kapena kutenga maulemu adziko lapansi.E. Ngati anakwiya, chinali chifukwa cha Mulungu, osati chake ayi.F. Kudzichepetsa kwake sikutanthauza kuti anali wofooka ayi. Iye anali mwamuna wolimba koposandinso mphunzitsi wamphamvu yemwe sanaonekepo ndikale lonse. Nthawi zina ankakalipa, komazinali zoonekeratu kuti zinkachitika m’chikondi, osati chifukwa cha iye mwini ayi.G. Pamene anakomana ndi mtanda, anatumikira zosowa zathu koposa zofuna zake za iye mwini. Tonsetikuitanidwa ku moyo woterewu, wokonda ndi kutumikira modzikhuthula – Afilipi 2:5-11; Aroma15:1-3; Mateyu 16:24,25; Yohane 13:1-17,34.2. Akhristu sadzaphunzira utumiki pokhapokhapo atsogoleri awo atawaonetsera utumikiwo monga momweYesu anamchitira – Yohane 17:19.3. Utsogoleri wotumikira sungatheke ku moyo wathu wauchimo wathupi. Ungatheke potsatira moyowatsopano wofanana ndi Khristu womwe umaperekedwa ndi Mzimu Woyera:A. Moyo wathu wathupi wa uchimowo umalamulidwa ndi kudzikonda, ndi kunyada – Agalatiya 5:19-21. Aliyense amafuna kukhala wotsogola, kuti enawo azingotsatira zomwe ife tifuna basi. – Mateyu18:1-4.B. Mzimu woyera amabwereka mwa ife chipatso chatsopano cha moyo wofanana ndi Yesu – Agalatiya2:20.4. Kodi atsogoleri otumikira amaganiza ndi kuchita motani?A. Utsogoleri wotumikira sudzikondweretsa okha koma umafunafuna ulemerero wa Mulungu ndikuonetsetsa kuti ena apeze bwino – 1 Akorinto 4:8a; Aroma 15:1-3; Yohane 3:26-30.B. Umalakalaka ndi kukonzekera kutumikira anthu ndi Mulungu – Ahebri 13:17; 1 Petro 5:4; Yakobo3:7; 1 Timoteo 3:1-7; Tito 1:5-9; 1 Samueli 12:1-3. Mtsogoleri saopa kutumikirana ngati aliwoyeneradi, wosankhidwa munjira yoyenera ndi yobvomerezeka. Mtsogoleri wotumikira saopakupereka malipoti okwanira a chuma cha mpingo kumpingowo. Iye amafunsa anthu kuti aperekemaganizo awo kwa iye pa za ntchito ya pampingopo. Mtsogoleri wofana ndi Yesu amabvomerakudzudzulidwa kothandiza komwe kungathandize utsogoleri wake. Utsogoleri wamtundu umenewuumabweretsa umodzi mumpingo, pamene utsogoleri wofanana ndi wadziko lapansi umabweretsakugawikana mumpingo.C. Utsogoleri wotumikira umapulumutsa.1) Kutumikira mwachikondi, ndi mopanda kudzikonda kumachita bwino, kumawala bwino m’dzikolodzitumikira lokha. Kudzikonda ndi kunyada ndi chizindikiro cha moyo wathupi wa uchimo.2) Anthu analondola Yesu chifukwa anamva mumtima mwawo kuti iwo ofunikira kwa iye. Iye analiwokhudzidwa kwambiri pa za moyo wawo, osati pa za moyo wake.3) Anthu amakopeka ndi kukokeredwa ku moyo wokonda, wosadzikonda ndipo amafuna atakhalandi khalidwe lotere.4) Chikondi chotumikira chimasintha anthu pamene palibe china chirichonse chomwe chingathekuwasintha – Yohane 12:32; 1 Yohane 4:19; 2 Akorinto 5:14; 1 Petro 3:1-6.D. Umathana ndi zolimbana mwa chiombolo.(Satana amagwiritsa ntchito kutsutsana moononga, komaAkhristu odzala ndi chisomo amatenga kutsutsana ngati mwayi wowathandiza kuti aphunzire ndikukula.)Umodzi 24

1) Sutenga kutsutsana mwa iwo okha. Mtsogoleri wotumikira anadzikhuthula. Nthawi zina Yesuankakwiya mwa chifuniro cha Mulungu, koma simunamuona akukwiya mwa chifuniro cha iyemwini. Mtsogoleri wotumikira amaphunzira kuchokera mukudzudzulidwa pa za Madera omweiye ayenera kukonza – Mateyu 7:3-5, ndiponso amaphunzira kungosiya kudzudzula kopandaphindu kupite, chifukwa anali ndi zinthu zambiri zofunika kuti achite poyamba koposa kudzitchawachilungamo. Iye amadziwa kuti onse otsutsana naye si adani ake; Satana, zofooka za munthu,kusadziwa ndiwo ali adani ake.2) Umalumikiza koposa kusiya monga munthu wathupi wa zamdziko angachitire. Mtsogoleriwotumikira sayembekezera kuti munthu winayo ndiye ayambe.3) Pochita ndi wotsutsa, suchita monga mwa nkhondo kuchititsa kuti winayo akane kukambiranandi cholinga chodziteteza. Umafikira mwa chilungamo koma modekha poika njira za chimvano –Agalatiya 6:1,2; 2 Timoteo 2:24-26.4) Pokonza zoonongeka umagwiritsa ntchito dongosolo lomwe Yesu anatipatsa lothetseramakangano mwachangu asanakule ndi kuononga kwakukuru. Cholinga choyambirira sichofunakuweruza ndi kudzudzula ayi koma kuthetsa kusiyana kwa maganizo kuti asachitinso mongamwa chifuniro cha Satana – Mateyu 18:15-17; 5:23,24; Aefeso 4:26-27.E. Mtsogoleri wotumikira amafikirika. Mtsogoleri sachepsa maganizo a ena kapena kukana Mafunsoawo koma amamvetsera ndi kuyankha modekha ndi kudzisunga konse – Yakobo 1:19,20; 3:17;Aefeso 4:29; 2 Timoteo 2:24-26; 1 Petro 3:15; Afilipi 2:3; Akolose 4:6. Tingathe kulimbikitsadongosolo la Mulungu popanda kukhala oweruza aukali.F. Utsogoleri wotumikira umalemekeza ndi kulolera maganizo osiyana ndi ake a ena pa nkhani zinazomwe chifukwa cha umunthu wathu wolephera, sitingathe kuzimvetsa ndi kuzimasulira bwino,zomwe siziri zofunika kwenikweni ku chikhulupiriro chathu. Nkofunika ndipo nkoyenera kutiMkhristu aliyense wokhulupirika ndi wodalilika aone zinthu zimenezi mosiyana. Mtsogoleriwotumikira amadziwa kuti iye wangokhala munthu mmodzi m’gulu la anthu otumikira mofanana,okhulupirira olemekezeka, ndipo sadzakakamiza anzakewo kuti akhulupirire ndi kukhala ndimaganizo onga akewo pa zinthu zomwe zioneka monga zochepera mphamvu, kapena kuti akhale ndimaganizo ofanana ndi ake pa momwe iye amvera Baibulo.G. Utsogoleri wotumikira sulamulira ena kuti atsatire njira yake. Koma mtsogoleri amamvera ndipoamakamba poyera, pofotokozera chifukwa chomwe iye amaganizira munjira yakutiyakuti. Amadziwakuti sichikhala chinthu wamtengo wapatali ngati angomvera mongomukondweretsa koma amveremochokera pansi pa mtima wawo. – 2 Akorinto 3:17. Anthu omwe amatsutsana naye mwachilungamo amalandirabe ulemu wake.H. Umakonda kukopa ndi kudandaulira momwe ungathere koposa kulamula – 2 Akorinto 13:10.Utsogoleri weniweni suchita kupemphedwa m'njira iyiyonse. Umapezeka polandira ulemu wa iwoomwe tiwatsogolera.I. Umakhala ndi chidwi chogawana ntchito yotsogolera ndi kulekera nsakali kwa m’badwo wobwerawo– 2 Timoteo 2:2.1) Mipingo yambiri ikufa chifukwa asogoleri ake onse akula ndipo ayamba njira zawo zawo ndipoakukanika kupereka mwayi kuti anthu aang’ono ndi maganizo a anthu ang’ono abweremumpingo.2) Atsogoleri otumikira nthawi zambiri, ndi cholinga, amaphunzitsa atsogoleri aang’ono ndikumagawana nawo ntchito ndi maudindo kuphatikizapo ufulu woti athandizepo kukonzadongosolo la tsogolo la mpingo (atsogoleri omwe lero akulawa, nawonso ankafuna ufuluwomwewo pamene anali kuyamba kumene).Mawu otsiriza: Maganizo ndi njira za Mulungu ndi zosiyana ndi zathu – Yesaya 55:8,9. Utsogoleri womwecholinga chake ndi kutumikira ndi wamphamvu kuposa utsogoleri wina wamtundu uliwonse womweUmodzi 25

mungaudziwe. Unamthandiza Yesu kusiya chitsanzo chosaiwalika mpaka kalekale padziko lapansi, ndipoudzatithandiza kutsogolera mpingo mwa mphamvu ndi mofuna kubweretsa anthu kuchiombolo, kuti tithekupyola ku zopunthwitsa zomwe sitikanatha kuzidutsa mu njira iriyonse, ndi kuwakopa anthu kuti akhale ndichidwi cholondola ndikutsatira. Kumvetsa zinthu zimenezi nkwamtengo wapatali koposa dongosolo lina lirilonse.Gawo lachitatu: Kupasirana Nsakali: Kumwetulirana Kapena Kuponyerana Nkhondo?(Kupewa Kulimbana kwa Pakati pa Atsopano ndi Akale.)Sauli anamponyera nkondo Davide, chifukwa sanakondwere poganiza kuti Davide adzalowa ufumu wake tsikulina. Herodei anapha unyinji wa makanda a ku Betlehemu pamodzi ndi akubanja kwake komwe posakondwerandi kubvomera ganizo loti iye sadzakhala wolamulira mpaka kale kale, ena adzayeneranso kudzatenga maloake.Kumbali inayi, tiona Eli wansembe wamkulu, mosiyana ndi omwe tamvawa, akudzipereka yekha pophunzitsaSamueli mnyamata kuti adzakhale mtsogoleri wamawa. Eliya adaphunzitsa Elisa kuti adzatenge malo ake ndikupitiriza ntchito yake mtsogolo. Nawonso Elisa ndi Samueli anaphunzitsa pa sukulu yokonzekera aneneriamtsogolo. Mtumwi Paulo analimbikitsa gulu la alaliki ang’onoang’ono ndi aphunzitsi omwe oti adzapitirizekufalitsa uthenga wabwino pamene Paulo amwalira. Anali wokondwera chifukwa cha iwo. Ndipo analikumawapempherera. Kwa Timoteo monga wophunzira wake wopambana, anamlembera kuti, “zonse zomwewandimva ndikulankhula pamaso pa mboni zambiri uikize kwa anthu okhulupirika amene adzakhozakuphunzitsanso ena.”1. Ife omwe tagwira ntchitoyi kwa nthawi yaitali tikadakonda tikupitirizabe kugwira ntchitoyi.Sitikondweretsedwa kumva kapena kuganizira zakufooka kwathu. Koma tsopano taonani tisanazindikire zakuzilala kwa mphamvu zathuku, timafika mundime yoti mphamvu zathu zimayambabe kulowa pansi.Mphamvu zathu zimayamba kulephera. Timayamba kumangobwereza zomwezo zakale m’malomoganizirabe njira zina zatsopano. Timayamba kusowa mphamvu za achinyamata kuti ayeserere ndikuganizira ndi kumanga. Timangoyamba kumayang’ana za m’mbuyo m’malo moyang’ana zamtsogolo.Sitithanso kumvetsa za makono zomwe ndi zofunikira. Timatopa msanga.Choncho tiyenera kusiyira ntchitoyi ku m’badwo winawu. Koma tiri nawo mwayi wosankha njira yakeyochitira zimenezi. Tingathe kusiyira nsakali ya ntchitoyi mwa chisomo ndi mwanzeru kapena tingathekumakana zimenezi ndi kumangokhalira kulimbana ndi achinyamata, kumawatenga ngati adani. Pamenetisankha njira imeneyi mpingo umabvutika ndipo umalipira dipo loopsa kwambiri.2. Mulungu safuna kuti mpingo ugawikane pakati pa mibadwo mibadwo. Monga momwe uthenga wabwinouyanjanitsa ndi kulumikizira mitundu ya anthu yosiyanasiyana, amuna ndi akazi, anthu azikhalidwezosiyana, umalumikiza ndi kuyanjanitsanso aakulu ndi achinyamata m’chikondi cha kwa aliyense ndicholinga. Ngati kukula msinkhu kuli nazo zofooka zake, kuli nachonso chuma chamtengo wapatali, ndichonzeru. Achinyamata ayenera kumvera mwa ulemu malangizo a achikulire. Nawonso achikulire ayenerakulemekeza zolakalaka ndi zofuna za achinyamata. Akulu ndi achinyamata si adani; onsewo ali m’gululimodzi. Mphamvu zawo ndi zofanana.A. Uwu ndi mutu wobvuta ndi wotenga mtima. Komabe ndikhulupirira ndiri nawo ufulu woti ndinenendithu pankhani imeneyi popeza nanenso ndi kuyandikira nthawi yoti ndipume, ndakhala woyang’anirakwa nthawi yaitali ndipo ndaukonda mpingo. Ndakhala ndi kupemphera kuti ndilandire nzeruyolankhula mosasonkhezera moto woyambitsa makangano koma kuti ndithandize ife atsogoleriachikulire kuti tidziunike tokha ndi kukonza malingaliro athu ndipo potero tilandire udindo wathuwauzimu wa kuti tithe kusintha mwa chisomo, ntchito ya Mulungu pakati pa mibadwo ndi misinkhuyosiyana.B. Umenewu ndi udindo wathu chifukwa 1) Ndife okhwima, olimba omwe tiyenera kunyamula zofookaza ochepa mphamvu; ndipo 2) Ndife omwe tikutsogolera ndipo tiri ndi mwayi wosankha momwentchito ipitire patsogolo.C M’mipingo ina atsogoleri akupatsirana bwino nsakali ya utsogoleriyi ndipo anthu aakulu ndiUmodzi 26

achinyamata akugwirira ntchito pamodzi. Koma m’mipingoyo yambiri zafika posukusa ngatisikuonongeka kumene. Pamene kugawikana pakati pa akulu ndi achinyamata ndinso kulimbanakubuka, achinyamata a amakambirana ndi achinyamata anzawo za achikulire ndipo achikulire nawonsoamakambirana ndi achikulire anzawo za achinyamata, ndipo palibe gulu lomwe limayankhula gululinzakelo. Nthawi zambiri amayankhana monga athupi amachitira, molimbana, mopanda moyowololerana wa chikondi monga momwe Akhristu otsogoleredwa ndi Mzimu amachitira.Ndi kumbukira nthawi ina yomwe ndinali kukambirana ndi atsogoleri achikulire ku tauni ina yake,pamene ndinali kuwalimbikitsa kuti asamafulumize kukhulupirira miseche yopanda umboni yonenaogwira ntchito mu mpingo achinyamata, koma alumikizane nawo modekha poopa kuti mwinaachinyamatawo angayambe kusafuna kukhala pafupi ndi iwo. Ngati ife achikulire tipitiriza kukakamiraudindo, ngati tikaniza achinyamata mwayi woti athandize kutsogolera mpingo, ndiye kuti tidzathawitsaachinyamata abwino pamodzi ndi nzeru zawo zomwe zikanadzathandiza mpingo mtsogolo.3. Nchifukwa chiyani zimakubvutani kusiyira nsakali ya utsogoleri kuti muthandizane kutsogolera?Choipitsitsa kwambiri ndi choti mwina kumangokhala kulimbanira ndi kukanirira udindo, zosasiyana ndizomwe Sauli kapena Herodi anaganiza zija. Tonsefe tili nako kufooka koganiza monga mwa thupi. Ngatitizindikira moyo umenewu mwatokha, nkoyenera ndi kofunikira kwambiri kulapa, kudzichepetsa,kufewetsa mitima yathu ndi kusintha mthandizidwa ndi Mulungu! Komabe nditha kuganiza kuti ambiri aatsogoleri athu amakhala ndi cholinga kapena zolinga zabwino zowapangitsa kuti asachite zinthumofulumiza. Zina za zolingazo ndi izi:A. Kukayikira kutuma ena. Mbali ina yakhalidwe limeneli ndi kudzitamandira (“ndine ndekha wodziwabwino”), komanso mbali ina ndi maganizo ongofuna kuti ntchitoyo igwiridwe bwino. Tiyenerakudziwa kuti atsogoleri achinyamata sadzakhwima ndi kulimba ngati sapatsidwa mwayi weniweni wotiaphunzire kutsogolera. Tiyenera kuwapatsa mwayi woti okha aone chochita molakwitsa mongansotinkachitira ife munthawi zathu zoyamba zija. Nthawi zina tidzadzidzimuka Poona mphatso ndi nzeruzomwe sitimayembekezera kuti ali nazo.B. Kukhudzidwa ndi tsogolo la mpingo. Kwa ambiri a ife atsogoleri ampingo achikulire, mpingo wakhalamonga moyo wathu. Tidzalolera kutaya moyo wathu chifukwa cha mpingo. Achinyamata amaonetsazikhulupiriro zina zomwe sitikondwera nazo. Timaiwala kuti nafenso pamene tinali kukula kumenemumpingo tinkachita zomwezo, ndipo zinkatero ndi mibadwo yonse yakumbuyoku.Masiku ano kusintha kukuchitika mowirikiza. Koma m’badwo uliwonse unaziganizira wokhamamvedwe ake a zomwe Baibulo liphunzitsa. Timayesetsa kuphunzitsa ana athu kuti adziopa ndikulemekeza Mulungu kuti akonze okha chikhulupiriro chawo. Timakhumbira atakwera m’mapewaathu ndikudziwa zambiri koposa ife eni, koma taonani akateronso timayambanso kuganiza zina ndikusowa nawo mtendere. Kodi nanga, ngati Mulungu munjira zina, athandiza ana athuwa kutulukiranzeru zina zomwe ife sitinadziwa? Kodi nanga monga Paulo wa ku Tariso titsutsa, ndi kusowetsamtendere pa ntchito yomwe Mulungu waikonza? Kodi nthawi zina timaponya mivi kwa anthu omweMulungu wawasankha?Kukhudzidwa kwathu pa nkhani ya mpingo kumakhala kolimba ngati tidzipereka ndi kukumbukira kutitiri nacho choonadi chonse ndipo maganizo ena onse abwera pamwamba pa chimenechi ndi mongankhamba nkamwa chabe (zakumva). Titha kumalepherabe kumvetsa kwenikweni za zomwe Baibuloliphunzitsa za chisomo ndi zomwe Mulungu atilamulira pa kulemekezana ngakhale pamakhalakusiyana maganizo “pa mfundo zina zazing’ono.” (Aroma 14,15). Nthawi zambiri takhala tikubvutikapolimbana ndi nkhani zazing’ono zoti titha kungozisiya, zomwe sitiyenera kuzitenga mongazoyambirira kuganiziridwa, ngati ndi zofunikira kwambiri pa chikhulupiriro chathu. Inde ndiyenerakumvera chikumbumtima changa, koma lemba liti ndidzatha kupulumutsidwa ngakhale ndalakwitsa pamfundo zina zomwe zagawanitsa okhulupirira. “Mubvomerezane wina ndi mnzake, inde, mongansoYesu anakulandirani inu….” Izi zingapangitse kuti kukhale kosabvuta kukhalirana pamodzi ndiachinyamata omwe ayenera kupatsidwa udindo wotsogolera. Komanso sitiyenera kumangololeramaganizo awo alionse; kuwamvera kwathu sikutanthauza kukhuthula maganizo athu onse ayi; pali zinazoti tidzimusiyira Mulungu.Umodzi 27

C. Kusokoneza pakati pa tanthauzo lenileni la mpingo logwirizana ndi Baibulo, ndi momwe titanthauzirampingo mogwirizana ndi chikhalidwe chathu cha makolo. Pamene Mulungu wamanga zinthu zina kutitisazisinthe, palinso njira zina zambiri zomwe watipatsa mwayi wosankha njira yotikondweretsamalingana ndi nthawi ndi zinthu zotizungulira. Dongosolo la zambiri zomwe mpingo umachita lagonam'gawo limeneli. Pankhani ya ufulu wosankhawu, m’badwo uliwonse umasintha mpingowo kuti uthekugwirizana ndi kuchita bwino mogwirizana ndi zofunikira za nyengo. Ife omwe takula tiyenerakubvomera kuti momwe chikhalidwe chathu chigwirizanira ndi kumvera tanthauzo la mpingochidzatha monganso momwe zakhala zikuchitira ndi mibadwo mibadwo yapitayo. Koma kufunikirakwa mpingo monga mwa malembo kudzapitirirabe ndipo kudzalimbalimbane; zipata za akufasizidzaulaka. Ine ndatengeka ndi kusanalatsidwa ndi chikhulupiriro chopambana ndi kudziperekakomwe kuli mwa m’badwo wa achinyamata.4. Kodi tingasiyirane bwanji nsakaliyi mwa chimwemwe ndi kuchepetsa kulimbana pakati pa achinyamatandi achikulire?A. Titha kumaonjezera atosogoleri ena atsopano mumpingo. Atsogoleri anzeru sadikira mpakana zinthuzifike pofuna kuonongeka chifukwa cha mabvuto autsogoleri. M’malo mwake amalimbikitsa nthawiisanafike, kugwirira ntchito pamodzi ndi achinyamata nthawi zambiri. Choncho kukonzekeratuutsogoleri mwa choonadi kumaimirira mpingo wonse ndiponso maganizo a achinyamata amakhala ndigawo pa zamtsogolo la mpingo.Podziwa kuti atsogoleri sakhwima tsiku limodzi, choncho pamafunika kukhala ndi cholinga chofetsambewu ya atsogoleri amtsogolo ndi akazi awo nthawi isanafike. Ichinso chitanthauza kuti gawo lautsogoleri lomwe liperekedwe kwa achinyamatawo liyenera kukhala leni-leni. Ngati mtsogoleri kapenaatsogoleri akale angodziikirabe okha mphamvu zina, atsogoleri atsopanowo sachedwa kutulukirabvutoli. (choona ndi chakuti, gulu la atsogoleri lakhala ndi mibadwo yosiyana-siyana, ndi nthawizochepa mwinanso osachitika kumene kuti pakhale kugawanikana pakati pa misinkhu yosiyana.)B. Ife omwe tiri achikulire pa zaka tiyenera kumamvera mwa ulemu maganizo a achinyamata ndikumaganizira maganizo awo ngakhale tikulekana ndi maganizo awo. Tinayenera, ndi nthawi yaitaliyomwe takhala padzikoyi, kukhala titadziwa momwe tingachitire modekha ndi moganizira bwino.Koma ngati nthawi zomwe timangowaikira maganizo athu ndi kumangowakhumudwitsa,timangowatalikitsa nafe ndipo m’badwo wawo kukhalanso pafupi nafe. Ndipo ngati achinyamataamveredwa popanda kubvutikira, ndiye kuti kukhala kosabvuta kuti amvere nzeru za achikulire.C. Titha kumabweretsa pang’ono pang’ono kusintha kwa muyezo woyenera mwa pafupipafupi. Apatu ndikutanthauza kusintha kwake kobvomerezeka, kofunikira, kusintha kukhala molingana ndi chikonzerocha Mulungu komwe mpingo wakhala akuchita kuyambira mibadwo yoyambayo mpaka tsopano ndicholinga choti mpingo ukhale wolimba ndi kutha kufikira otayikawo. Ngati sitikonza dongosololomasintha mpingo pang’onopang’ono munjira yoti mpingo uthe kumvetsa, timafika pa ndime yobvutayoti achinyamata amafuna kusintha kochuluka kwa nthawi yomweyo ndipo mwa msanga koposamomwe achikulire angathe kukonza. Nkhondo za pakati pa mibadwo zimauka, Akhristu amachokandipo timaononga mphamvu ya mpingo yoti ukanachita kanthu. Atsogoleri anzeru amakonzeratuzamtsogolo, osati ongochita modzidzimukira.D. Ife atsogoleri aakulu misinkhu titha kulimbikitsa mizimu yathu ndi maganizo athu ndi mapempheropamodzi ndi maphunziro nthawi zonse. Kulimbana kungathe kuyamba nthawi iriyonse pamene anthuachinyamata aposa achikulire pakamvetsedwe ka malemba ndi ubale kwa Mulungu. Ngati ena aatsogoleri achinyamata ali ndi mfundo zoopseza, ambiri a iwo amakhala ndi mtima wolimbika zedi zaMulungu ndi mawu ake. Ife atsogoleri akale nthawi zambiri timangotsamira pa “mfundo zochepa”zomwe tinaphunzira kale m’masiku oyambirira aja, ndipo timangoona ngati basi, potero takwana,palibenso china chomwe tikusowanso monga atsogoleri achikhulupiriro ndi okhulupirika. Ziphunzitsozoyambirira, inde, ngakhale ndi zofunikira, si zilowa m’malo otifikitsa ku moyo wokhwima mwa Yesu.Nthawi zina abusa amaonetsa kulephera ndi kusadziwa malemba. Ndipo mfundo za dzanja, ngakhalezikhale zabwino chotani, si zokhazo zomwe ife atsogoleri tiyenera kudziwa. Kuti tithe kulemekezamisinkhu yonse mumpingo, tiyenera kumvera lamulo la Yesu ndi mtumwi Paulo loti “tiyeneraUmodzi 28

kumvetsa za nthawi yomwe tiri.” Kodi ndiye kuti ndifedi atsogoleri oona ngati tikulephera mongaatsogoleri, kuphunzira ndi kupempherera zobvuta za makono zisanafike poopseza nkhosa zathu.Ine monga munthu ndimakhuzidwa ndi momwe zakale zimabvutira atsogoleri achinyamata. Komatu zomwetibvutika nazo lero ndi zomwe tikubvutika nazo kale. Ngati ena akubvutika ndi zochitika zimenezi, ife akalendi omwe timathandiza kukhazikitsa zimenezi. Zomwe tiwasiyira achinyamata sikuti ndi zoipa kwenikweni.Ayenera kumakumbukira kuti tidawaphunzitsa kukonda Mulungu ndi mawu ake. Koma pamene tikuwasiyiransakali imeneyi, tikhale ndi chidwi chotani choonetsetsa kuti tipewe zomwe zimapangitsa kuti achinyamata ndiongophunzira kumene apunthwe! Tikhale osamala bwanji kuti tipewe mafano akale omwe ankathawitsaachinyamata: kukhulupirira zinthu zosachitika, magawano osafunika ndi osatsatira malemba, kulimbikira pazinthu zazing’ono, kusokoneza pakati pa maganizo athu ndi malemba, kuchititsa kuti ziphunzitso ndizikhulupiriro zikhale amphamvu ndi zofunika kuposa Mulungu mwini.Chitsanzo chopambana ndi chamtengo wapatali chochokera m’Baibulo cha kusiyirana muuni kwabwino ndicha Yohane Mbatizi. Pamene khamu linayamba kusintha ndikuyamba kutsata Yesu, Yohane anakondwera ndizimene Mulungu anali kuchita ndipo anati, “Munthu amalandira zokhazo zomwe iye walandira kuchokera kwaMulungu … Iye ayenera akule; ine ndikhale wamng’ono.”Ndinamva ulaliki wina wosasunthika, wochirimika, wodzipereka ndi chikhulupiriro chonse, akulankhula pamaphunziro zaka zapitazo. Moyo wake ndi chitsanzo chomwe Mulungu amafuna kuchokera kwa atsogoleriaakulu ndi akale. Kwa ogwira ntchito achinyamata ananena mawu otere: “Ifetu tsopano kuno nkukula. Tiyenerakuyang’ana kwa inu kuti mupitirize ntchito. Tilandireni udindowu. Tumikirani Mulungu mokhulupirika.Maganizo anu ena atha kutibvuta ife omwe tiri akale. Komabe musaope kuchita zomwe mukukhulupirira kutiMulungu ndiye afuna kuti inu muchite kuti mubale zipatso. Iye adzakhala nanu monganso wakhala ndi ife.”1. Kulandirira MuuniwoNgati nsakali ya utsogoleri ikapatsidwe kapena kusiyiridwa kuchokera ku mibadwo umodzi kupita kum’badwo winawo payenera pakhale wolandira wofunadi ndinso wopereka wofunadi. Zimadabwitsa kutim’mipingo mwina mulibe anthu ofunadi kulandira katundu wodzipereka wa utsogleri. Kodi zinthu zirichonchi chifukwa chiyani? Ndi chifukwa choti makolol asiya kuphunzitsa ana awo kulakalaka utsogoleriwa Chikhristu kapena kuiona ntchito imeneyi ngati ganizo losiririka labwino? Kapena ndi chifukwa chotisitiphunzitsa ndi kusula atsogoleri ndi cholinga cha mawa? Kapena ndi chifukwa choti anthu athuatanganidwa ndi ntchito zawo zina zapadera? Kapena ndi chifukwa cha zobvuta zosiyanasiyana zomweasogoleri amakumana nazo masiku ano? Kapena ndi chifukwa choti timasasulira zoyeneretsa zam’malemba munjira yomwe Mzimu Woyera sabvomereza?A. Yambani kukonzekera tsopano lomwe. Mtsogoleri amakula pang’ono pang’ono monga mtengowamlambe kuchokera m'chiyambi chaching’ono kwambiri: Makolo omwe moyo wawo wonseumadalira Mulungu ndi kumagawana malemba, mapemphero ndi utumiki pamodzi ndi ana awokuchokera adakali ang’ono. Makolo omwe nthawi zonse sangokhalira kutsutsa alaliki ndi abusa komaamaonetsa kuthokoza pa ntchito zawo ndi kupangita ana awo kuti aganize kuti kukhala mlaliki kapenambusa ndi chinthu cha ulemu. Atsogoleri omwe analimbikitsa achinyamata kuti akule ndi kuphunzira.Makolo achinyamata omwe amaphunzira ndi cholinga choti akule mwayiwo okha. Sukulu za Baibulozingakonze maphunziro a masiku ochepa a atsogoleri ozungulira dziko lino ndinso ena omwe afunakudzakhala atsogoleri. Abusa angathenso kutumiza achinyamata omwe akuonetsa kuti ali ndi tsogololabwino ku uzimu kumaphunziro “a maluso ena.” Ndi kuwalola kuti aphunzirebe pomakhala nawo pamisonkhano ya abusa ndi kumatsagana ndi abusawo ku ntchito zoyendera nkhosa. Oyang’anira waangathe kutuma ophunzirawa ntchito zina.B. Utsogoleritu siwa wina aliyense. Munthu yemwe akhumbira utsogoleri ayenera kuzindikira ndikudziwiratu za kudzipereka nsembe ndi udindo womwe umayenerana ndi utsogoleri. Pamene munthuwina anafuna kutsata Yesu, Yesu anamchenjeza kuti, “nkhandwe ziri napo pogona pawo ndiponsombalame ziri nazo zisa zawo, koma mwana wa munthu alibe poikapo mutu wake.” Woyang’anirayemwe amayang’aniradi adzasiya nthawi yochita zinthu zake yambiri kuti akonze dongosolo la ntchitoya Mulungu ndi kutumikira anthu pa zosowa zawo. Adzasamala pochepetsa ufulu wake kutiasapunthwitse ofooka. Yakobo akutichenjeza, “Musafune kukhala aphunzitsi ambiri a inu, abale anga,Umodzi 29

chifukwa mudziwa kuti ife amene tiphunzitsa tidzaweruzidwa moposa enawo.” Atsogoleri ndiwo alindi udindo ndipo ndiwo adzayankhe kwa Mulungu pa nkhosa zomwe iwo ayang’anira. – Ahebri 13:17.C. Koma Mulungu ndiye amayang’anira iwo omwe alakalaka komanso ali ndi mphatso zamtsogoleri. Iyeamachita izi poyankha mapemphero athu a ogwira ntchito kuti tikolole zipatso. Iye amachita zimeneziD. pamene anthu payekha payekha apemphera kuti Mulungu awagwiritse ntchito monga mwa mphatsozawo.E. Ndi chinthu chofunika kuti okalaka ntchito ya utsogoleri adzichepetse pansi pa ulamuliro wa Mulungu.Ngati oyang’anira ndi atumiki “oyambira kuphunzitsa” anthu omwe akuoneka kuti ali ndi mphatso,tiyenera kumvetsa bwino pamenepa kuti dongosolo limeneli silitanthauza kuti amenewa ndiyeangolowa ndi kukhala atsogoleri. Zotsatira zake ziyenera kusiyidwa m’manja mwa Mulungu. Ndipongati mpingo ufunsidwa kutchula maina a atumiki ndi oyang’anira kuti aonjezedwe ku mpingo, iwoomwe alandira mavoti ochepa, ayenera akukonzekeratu zisanachitike izi kubvomereza zomwe mpingowachita popanda kuwawidwa mtima. Mzimu Woyera ndi amene amapanga abusa mumpingo(Machitidwe 20:28) ndipo imodzi ya njira zomwe amachitira zimenezi ndi yoyankhula kudzerakusankha komwe mpingo umachita.Pamene Mulungu aitana anthu ena kuti akhale atsogoleri, izi zimatsimikizika ku mpingo pamene ayesamoyo ndi khalidwe la iwo omwe aitanidwawo. Ngati wina sanasankhidwe padakali pano, mwinazingatanthauze kuti Mulungu akufuna nthawi yokwanira yoti amukonze munthuyo. Kapena zithakutanthauza kuti Mulungu anampatsa munthuyo mphatso yoti atumikire m’njira zina. Tidziwe kutisimtumiki aliyense amakhala woyang’anira wa mawa. Inde tikudziwa kuti ntchito zonse ziwirizizimakhudzana ndi nzeru za utsogoleri ndi moyo wa chitsanzo, udindo wa woyang’anira ndi wa paokha.Pali atumiki ena abwino omwe sangathe kutumikira bwino ngati akhala oyang’anira, ndiponso paliabusa ena omwe sakanakhoza kukhala atumiki abwino.Popeza zimatenga nthawi yaitali kuti pakhale mtumiki, mlaliki, mphunzitsi ngakhale mbusa, tiyeneratidzikonzekera ndi kuchitiratu dongosolo lero lomwe lino ngati tikufuna kuti tikhale ndi atsogoleri okwanira kumibadwo yakutsogoloyo.Gawo Lachinayi: Momwe Tingachitire ndi Kasinthidwe ka Zinthu.Mawu oyamba: Nkhani ya kusintha kwa zinthu ndi nkhani imodzi yobvuta kwambiri mumpingo ndi ntchitozake, chifukwa kusintha, kaya kwabwino ndi kololedwa komanso kofunika, ndi kobvuta malingana ndichizolowezi ndi chilengedwe cha munthu. Chikhalidwe chathu ndi miyambo yathu ikusintha mofulumirakwambiri moti sizinachitikenso m’mbiri yadziko ndipo zimenezi zikubweretsa mabvuto mumpingo. Mipingoyambiri konsekonse ikusauka ndi makangano. Anthu ena mumpingo amafuna ufulu wosintha kuti mpingo uthekugwirizana ndi kufikira m’maganizo a anthu amakono. Ena amaopa kutaya mpingo ndi choonadi cham’Baibulo chifukwa chakusintha kumeneku, ndipo amalimbalimba ndi kukana kusinthika. Alipo ambiriokhulupirika omwe ndi okonda Mulungu ndi mawu ake ku mbali zonse zakulimbana kumeneku. Komansokumakhalanso ena odzikonda, akhungu ndi aukali ku mbali zonse zakukanganako. Tiyeni tiyese kuonamodekha pa cholinga cha nkhani ya kusintha zinthu mumpingo.1. Kusintha ndi nkhani yamphamvu: ndi nkhani yoopseza ndi yosowetsa mtendere.2. Kusintha kungathe kukhala kwabwino kapena koipa.A. Kusintha kungathe kukhala koononga ngati kuli kusintha kochoka pa zabwino kupita pa zachabe,kapena kusintha ndi zolinga zofuna kudzikondweretsa, kapena kungosintha pofuna kutsatira nkhosa.Ngakhalenso kusintha kwabwino kumaononga nthawi zonse ngati mpingo ungokakamizidwa popandakupatsidwa nthawi yoti umvetse bwino.B. Komanso kusintha ndi kofunika kwambiri. Ndi mbali ya moyo wathu. Popanda kusintha palibe yemweangathe kukula ku uzimu kapena kuthupi. Palibe munthu kapena gulu lomwe lingachize bwino kapenakuthandiza kwambiri. Palibe yemwe akanatha ngakhale kulapa kumene kapena kufika pafupi ndiUmodzi 30

Mulungu ndi cholinga chake. Ndipo mpingo sungathe kufikira anthu a makono osinthika ngati susinthanjira zake zofikira anthuwo.C. Ziripo mfundo zina zoona zenizeni za mpingo zomwe siziyenera kusinthidwa; ndi zomwe zimachititsampingo kuti ukhale monga momwe ulirimo. Ziripo ziphunzitso zina zofunikira kwambiri, zobweretsaumodzi zomwe sizisowanso kukambirana kwa mtundu uliwonse – Aefeso 4:4-6; 1 Akorinto 15:1-4.Mpingo nthawi zonse uyenera kukhala woyera, wokhala ndi makhalidwe a Yesu. Nthawi zonseudzakhala pansi pa ntchito yaikulu yopanga ndi kutuma ophunzira. Udzakhala ndi mangawaopembedza Mulungu ndi kutumikira anthu osowa.D. Koma Mulungu wapereka ufulu wambiri ku mpingo kuti usinthike pamene nthawi ziri kusinthanso,potilola kuti tigwiritse ntchito njira iriyonse, zochitika, ndi mwambo uliwonse. Munthawi zimenezimumpingo wakhala ukusintha kuchokera ku m’badwo uwu kupita ku m’badwo wina ndipo kuchokeraku zaka mazana mazana kufikira zaka mazana ena. Titati tibwerere kumpingo woyamba ija, tingathekudabwa poona kusiyana maganizo komwe kunali pakati pawo, chimodzimodzinso ndi iwowoangadabwe Poona kusiyana maganizo kwa pakati pathu lero.E. Choncho mu zinthu zina kusintha kungaononge cholinga cha Mulungu. Mu zinthu zinanso Mulunguamayembekezera kuti zisinthike kuti ziyende bwino, choncho kusasintha kungaononge cholinga ndichifuniro cha Mulungu.3. Miyambo ya makolo ingathe kukhala yabwino kapena yoipa.A. Miyambo yagawika pawiri:1) Matanthauzidwe ndi magwiritsidwe ntchito a malemba omwe mibadwo yopitayo inasiira anthukuchokera kwa atsogoleri olemekezeka, ndinso2) Miyambo ndi “njira zabwino” zochitira zinthu zomwe tinasiyiridwa ndi makolonso.B. Miyambo ndi ya umunthu, osati uzimu. Iribe ulamuliro ndi mphamvu mofanana ndi mawu a Mulunguayi. Koma chodabwitsa ndi choti timailemekeza pafupifupi ngati mawu a Mulungu amene, mwinansokuipatsa ulamuliro ndi mphamvu ndi kumaisokoneza ndi mawu a Mulungu. Kotero kuti wina akayeserakusinthako miyambo yanuyo, zimachitika ngati wachita kusintha malamulo a Mulungu.C. Miyambonso ndi yofunikira mu njira zambiri. Mpingo uliwonse uli nayo. Imathandiza kusunga nzeruzakale. Imatithandiza kudziwa momwe tingapitirizire mtsogolo ntchito ya Mulungu. Imatipatsa moyowozindikira mtundu wathu ndi chitetezo. Imapereka dongosolo labwino lakagwiridwe ka ntchito.D. Miyambo imafika poononga pamene ifika pa ndime yooneka ngati yofunikira kwambiri ndi kumaonangati ndi kosayenera kuisintha ndi kuikonza pophunzitsa zomwe Baibulo linena, ndipo ndi kumaganizakuti sikwabwino kuisiya pamodzi ndi njira zina zomwe tazolowera ngakhale malinga ndi nthawisizikuthandizanso.E. Ngati miyambo ya anthu iyamba kulepheretsa chiphunzitso cha m’Baibulo kapena utumiki wabwinondinso mafikiridwe a anthu ena, iyenera kusiyidwa (ngatitu tifuna kuti tikhale omvera Mulungu ndikuika chifuniro chake patsogolo). Tidziwe kuti tidzayankha kwa Mulungu ngati tikonda kwambirimiyambo ya makolo athu koposa osochera omwe tiyenera kukawafikira. Yesu anamdzudzula atsogoleriaChiyuda aja chifukwa chonyalanyaza mawu a Mulungu ndi cholinga choti alemekezebe miyamboyomwe makolo awo anawasiyira – Mateyu 15:1-9.4. Mfundo zothandiza pa kagwiritsidwe ntchito ka kusintha zinthu kobvomerezeka ndi Mulungu.A. Mfundo yofunikira kwambiri yomasula nayo kumangiririka ku miyambo ya makolo ndi kuthandizaAkhristu kuti akule m’chikondi cha pa osochera. Pamene tikukhwima m’Chikhristu, tikuphunzira kutikupulumutsa mizimu ndi kofunikira kwambiri koposa mtendere wathu, koposa kudzikondweretsatokha. Timaphunzira kuti njira yeniyeni ya Khristu ndi chikondi, kudzipereka ndi cholinga chofunaUmodzi 31

kupulumutsa – 1 Akorinto 9:19-23; Aroma 15:1-3; Mateyu 16:24,25. Pamene mpingo ulimbikirakufikira osochera ndi kupanga ophunzira, pameneponso mpingo udzalimbikira kufuna kusiyiratumiyambo ndi zizolowezi zomwe zingalepheretse ntchito imeneyi ndi zolinga zimenezi.B. Pezani nthawi yoti muphunzitse mpingo za kusiyana kwa miyambo ya anthu ndi malemba. Nthawizambiri timalimbana chifukwa miyambo imasokonezedwa ndi chiphunzitso cha Mulungu. UpezeniC. mtima ndi kobvuta kuti anthu amvetse bwino zimenezi.D. Chitani mosamala ndi modekha monga momwe mungathere. Ine ngakhale ndi kusintha komweMulungu amakondwera nako, anthu ambiri ali ndi muyezo wawo wachilengedwe womwe angathepanthawi yakuti yakuti. Mulungu amaonetsa kudekha mtima akamachita ndi anthu motere:1) M’malo mosintha zinthu zambiri nthawi imodzi, amayamba pa zofunikira kwambiri.2) Amabweretsa kusintha m’magawo oyenera. Mwa chitsanzo, kuphunzitsa nyimbo imodzi yokhayatsopano pa mwambo ndi nyengo yoperekedwayo.3) Kupitirira kuonjezera atsogoleri ku gulu la atsogoleri ena ndi cholinga, kuchokera kwaachinyamata kuti utsogoleri wampingo ukhale woimiriridwa ndi mibadwo yonse ndi kutinsoutsogoleri usakhale monga chinthu chakale chongokhazikika.E. Thandizani mpingo kukhala wozindikira chifukwa chomwe kusinthika kuyenera kukhalapo.F. Musalole kuti mpingo ukhale womangiririka kumaganizo ofooka kwambiri, mokakamizika malinganandi pamalopo. Kumatheka kuti abale 98 apa malopo abvomereza kuti pakhale kusintha kuti anthuambiri akafikiridwe koma awiri aona kuti sikwabwino. Monga mwachizolowezi timangosiya chifukwacha awiriwa chifukwa malembo ati musakhumudwitse mbale. Tiyenera kukhala ndi mtima wodekhandipo mwa mapemphero kuyesetsa kubweretsa umodzi. Koma ponena zoona Paulo zingatanthauze kutimaganizo ochepa mphamvu ndi ofookawo, akalamulire ntchito za mpingo.Pa kuphunzitsa za kusiyana kwa maganizo, Paulo ananena molimbika kuti sibwino kwa iwo omweakhulupirira pa chinthu china kuti aweruze ena monganso anauzira iwo omwe alibe bvuto ndi chinthuchina kuti asalakwitse enawo. M’mbuyo monsemu sitinaganizire ndi kuzindikira mfundo imeneyi.Paulo anatiphunzitsa kuti tidzisiya kuweruza kwina kuti kukhale m’manja mwa Mulungu ndi kupitirizapamodzi ntchito ya Mulungu. Pa zinthu zina zazing’ono ndi bwino kugonja pa zomwezikanakhumudwitsa winayo. Koma pamene tikuona kuti ntchito ya malemba ingaonongeke yomweikadakhoza kupulumutsa miyoyo 50, ndipo ife tingoganiza chifukwa cha miyoyo iwiri, kodi pamenepandiye kuti tawakondadi anthu makumi asanu aja moyenera? Posaganizira za kudekha ndi kukondakomwe atsogoleri ali nako, nthawi imafika pamene utsogoleri umayenera kungochita chimeneakudziwa kuti ndi chomwe ntchito ya Mulungu ifuna.G. Sizimachitika kawirikawiri kubweretsa kusintha kwa padera mumpingo wakale, wokhulupiriramiyambo. Kuti zitero ndiye kuti mwina pafupifupi mpingowo ungagawike kapena ena ambiriadzachoka. Ndi bwino kukonza dongosolo mpingo watsopano womwe udzalemekeza zolinga zauthenga koposa miyambo ya makolo koma mwa mtendere.Mawu otsiriza: Kusintha zinthu mofunikira ndi chinthu chobvuta, koma tingathe kupirira ndipo kenakokukwanitsa kusinthako ngati atsogoleri ndi Akhristu onse ali odzazidwa ndi moyo wa Khristu.Gawo Lachisanu: Kuchita Mwanzeru Pamene Talekana Maganizo.Mawu oyamba: Werengani 1 Akorinto 3:1-17. Ngakhalenso mipingo yolimba iri nazo “zowawa zakezanthawi zonse.” Nthawi zimene tikumana ndi zolimbana ingakhale monga mwayi wotithandiza kuti tikulemwa uzimu chifukwa timakakamizika kuphunzira ndi kuzidziwa tokha. Kulekana maganizo mumpingokungatithandize kuona zambiri; kumva chinthu mosiyana kumathandiza kukonza, kufananiza, kapenakuonjezerana nzeru wina ndi mnzake.Umodzi 32

1. Kodi zina za zoyambitsa akulimbana ndi kukokana mumpingo wathu ndi ziti?A. Zochitika “zachilendo” kapena “zatsopano” zimayamba kugwiritsidwa ntchito mumpingo ndi iwoamene amafuna zomwe iwo amati kusintha zinthu mwa phindu. Zinthu zatsopano zimenezi zisakhalezosiyana ndi malemba ndi cholinga choyambitsa kutsutsana. Monganso momwe zinthu zosiyana ndizomwe tinazolowera kuchita, zoyambitsidwa mochuluka ndi mwa msangamsanga, zingachitire.B. Kusintha kwa utsogoleri ku guwa nthawi zonse kumayambitsa maganizo abwino ndi oyipa.C. Takhala tikusiyira “nsakali ya utsogoleri” kwa achinyamata, pophunzira kugawana nawo utsogoleri.1) M’badwo uliwonse uyenera kuchita zimenezi.2) Iwo omwe ali achichepere adzaona zina za zinthu mosiyana ndi momwe m’badwo winawoumaonera, monganso momwe ife akalefe tinali nawo maganizo athu pamene tinali achichepere.3) Ngati akalefe sitinapitirire kuphunzira kuti tikule mwa uzimu ndi m’maganizo anzeru, ndiye kutikulekana pakumvetsa kwathu kudzakhala kwakukulu ndiponso kulimbana ndi kutsutsanakudzakhala ku kukulirabe.4) Talera ndi kuphunzitsa achinyamata athu kuchita zinthu zoposa kungolimbana ndi zoganizirazina ndi zina. Tawaphunzitsa iwo kufuna zakuya zauzimu mwa kutsata zolemba. Nthawi zinasizimakhala bwino pamene achita. Komabe timafuna kuti ana athu aimebe pa mapewa athu ndikukula kulabe mu choonadi koposa ife.D. Mipingo ya Khristu yonse pamodzi yafika munthawi zomwe sitikuzindikira kuti kodi ndife yani? Koditiri nacho choonadi chonse, kapena ziripobe zinthu zina zoti tiphunzire?E. Pamalo pomwepo mumpingo pangathe kupezeka anthu amitundu yonse iwiri omwe atsamira pamiyambo ya makolo ndi osasunthika, ndi enanso omwe ndi omasuka ndi okonzekera kusintha nthawizonse ndi cholinga chofuna kuti zinthu zikhale bwino.[ ZOFUNIKA KUONA: Mu mphunziroli, pamene tikunena za “kusintha” tikunena za miyambo yamakolo ndi zina zachilendo zomwe Mulungu watipatsa mpata woti tokha tichitepo chisankho. Komatutiribe ufulu wosintha chirichonse chomwe Mulungu wachikhazikitsa m’malemba.]1) Anthu amaganizo onsewa nthawi zina amaononga. Anthu amaganizo osasunthika aja amati,“uwutu ndiye simpingo. Anthuwa akuusintha. Ukutayika.” Nawo omasuka posintha zinthu ajaamati, “ziripobe zambiri zoti tichite kuti mpingo ufikepo penipeni pa mpingo wa malemba.Bwanji nanga tipitirirebe mtsogolo?”2) Anthu amaganizo onsewa ndi okhulupirika ndipo amamkonda Mulungu.3) Titha kumangwiriza maganizo ndi zomwe malemba atiphunzitsa komabe ndi kumasiyanabe pazinthu zina zazing’ono zoti tiri nawo ufulu wosankha pa kachitidwe kake.Taonani zitsanzo za momwe mipingo imasiyanirana mu machitidwe ake:a. Amaona maimbidwe ndi Amaona maimbidwe ndi machitidwemachitidwe a nyimbo monga a nyimbo monga kuperekachinthu chongopangidwachopereka chamtengo wapatalikapena kuonetsedwa”kwa Mulungu.Amakondwera kuti anthuKudzipereka kwa mitimaYathu, osati za ukatswiriwomwe timauika m’mayi-Ntethemya za kaimbidwe zimaonetsansomtima wa munthu. Nyimbo monga ulalikizimamangirira. Nyimbo zoyimbidwamwa uthetemya ziri chimodzimodzi ndiUmodzi 33

mbidwe athu.”Ulaliki wokonzedwa bwino.b. Amakondwera kuti anthu Amakondwera kuti okhawoambiri agwire ntchitoakukhosi kwabwino atsogolereyotsogolera nyimbonyimbo lamulungu lija.lamulungu lija.”Mulungu sayang’ana zakuja, “Timaika alaliki odziwa ntchitokaya sikome chotani,m'mayimbidwe athu.guwa la Mulungu lija, chonchonsoKutsogolera nyimbo, monga gawolina la kupembedza, sizinasiyane.c. Kuomba m’manja sikuloledwa kuomba m’manja ndi kofunikirandipo sikuli kofunikirandipo kumaloledwa m’nthawim’nthawi zopembedza.Zopembedza.”Kuomba m’manja kusonyeza Kuomba m’manja kwa sinthikaKugonjetsera kapena kuyambiramatanthauzo lake pa chikhalidwekuti ena aone, koma tiri ku chathu chamakono. Ku kusonyezampingo kuti tipembedze Mulungu kukondwa kapena kuthokozaosati kuti tionetse anthumonga momwe zinalili m’Chipanganokapena tiimbire anthu”chakale panthawi yopembedza(nthawi imeneyo Mulungu analamulirakuti anthu aziomba m’manja ndipo iyesanakuone ngati chinthu chosayenera)Ndipo ndikoyenera “kupereka ulemukwa iye womuyenera” ngati iyesalowerera ndi kulandira ulemu waMulungu mwini.d. Panthawi za chipembedzo Magulu ena apadera amaloledwatiyimbe nyimbo za m'bukhu munthawi zina zapadera.lodziwika zokha basi.Anthu ena anadalitsidwa ndiNyimbo zapadera “zimakhala mphatso yokopa ndi kulimbikitsamonga zoyimbiridwa ena.M’mayimbidwe monga momweTonse tikulamulidwa kutialaliki achitira pa guwa. Nyimbotiziyimba pamodzi.imakhala yoimbira wina(Aefeso 5:19; Akolose 3:16) pokhapokhapo ngati maganizo akeali oterowo. Mumpingo woyamba“aliyense anali ndi nyimbomawu ……” (1 Akorinto 14:26).Zikuoneka nati iyeyu ankaimbiraku mpingo monga anali nawo”e. Amaona kuwerenga malembo Amaona kuwerenga malembopa gulu lonse monga chinthu pamodzi pagulu lonse mongachosavomerezeka, zochitidwa chimodzi mmodzi ndi kuimbandi mipatuko.Nyimbo pamodzi mofanana ndikusangalala komwe mpingowoyamba uja unkaimbira.f. Amaona ngati kukweza Amaona ngati kukweza manjamanja m'mwamba ndi njira m’mwamba ndi kusefukira kwaimodzi yoyamba kuchitakuyamikira ndi kukweza Mulungu,ngati anthu opembedzamaganizo m’Chipangano Chatsmofuulaampatuko. pano (1 Timoteo 2:8).g. “Amakonda nyimbo zauthenga Amakonda nyimbo zoyimbidwaUmodzi 34

zakale.””Nyimbo zosazolowerekasizikondweretsa anthu ndiponyimbo zina zimangowadutsaanthu osamva bwino zomweziri m’menemo.”Mwaluso,” zoikiriridwa ukatswiripozikonza,” kapena amakonda“nyimbo zomwe zikuyimbidwamakono.”“Tiyenera kupereka kwa Mulunguzinthu zabwino zomwe tingathe;maimbidwe akhale odzala ndichauzimu chopambana momweTingathere. Nyimbo zikhalezotha kukulumikizidwa bwinoku maganizo a anthu amakono.h. Amafuna mapembezedwe Amafuna ufulu wokwanira kutiolondolezeka bwino, olongosoka athe kuonetsa chisangalalo ndindi odziwika.kuyanjana.”Chipembedzo chichitikemolongosoka ndi moyenera.“Kupembedza kuzichokera mumtima- osati zooneka zokha ayi. Kumasukasikutanthauza chisokonezo.”Zonsezi ndi zizolowezi ndi miyambo yoti tikhoza kusankha kuichita kapena kuisiya. Munkhanizonsezi mbali iri yonse imakhala nacho choonadi chake. Zimenezi ziribe umboni weniweni wamalemba. Koma anthu amabvutika ndi kukhuzidwa ndi nkhani zimenezi koposa nkhani zomweziri zofunikira kwambiri malinga ndi malemba.4) Kodi nafenso tiri nako kusiyana maganizo pa zinthu zazing’ono ngati izi mofanana ndi momwempingo woyamba uja unaliri? Ena amasungabe maphwando apadera ndi masiku monga Sabata,koma ena ayi. Ena ankadya nyama ena ayi – Aroma 14.2 Kodi timachita bwanji pamene tasiyana maganizo?A. Osati:1) Kunyoza omwe ali ndi maganizo osiyana nawo kapena kuwatsutsa ndi zolinga zoipa.2) Kunenanena za zovuta zathu ndi wina aliyense osakhala omwe tinayenera kunena nawo, moterotimangoonjezera ndi kukulitsa kulimbana kwathu.3) Kukana kuganizira ndi kubvomereza maganizo ena.4) Ndale, mphamvu, kulamulira, kunyozetsa, kunenana zoipa ndi okutsutsani, kupatsana mainaachabe (wachilamulo, waufulu, wauzimu, wampatuko)B. Koma mwa:1) Kumvetsa mfundo zina:a. Nthawi zonse padzakhala kusiyana maganizo pa mpingo uliwonsewomweukukula. Padzakhala kulolerana ndi kugwirizana munkhani zinazazing’ono, apo ayi, mpingo udzagawika ndi kukhala m’magulu. Pauloamatiphunzitsa kuti tidzikhala ololerana munkhani zina zazing’ono –Aroma 14,15.Umodzi 35

. Pamene tikukula kusintha kwina kumakhala kofunika. Tiribe ufuluwosintha zomwe zinamangirika ndi malemba, koma pa nkhanizakumasuka tiyenera kusintha kuti tithe kufikira bwino ku khalidelosinthikali (ngati tikufuna kutsatira chitsanzo cha Paulo ndi kufikiramizimu yochuruka – (1 Akorinto 9:19-23). Kusinthika pakokha sikulikoipa kapena kwabwino.c. Kusintha nthawi zonse kumatisautsa. “zakale zomwe zija zinali bwino.”d. Nthawi zina anthu amaukirana wina ndi mnzake chifukwa chosamvetsazomwe mpingo ndi mapembedzedwe ake uliri malingana ndi malemba.e. Kulimbana kwathu m’mipingo nthawi zambri kuli pa momwe timveramalembo osati pa chiphunzitso chenicheni cha malemba.f. Kulimbana kotigawa kumayambika ndi “mbali zonse” zokakamiza kutizisinthe ndi kulimbana pokana kusintha. Cholakwika chimodzi chachikuluchomwe tingachite ndi chodzudzula mbali imodzi yokha ya vutoli.Mu Aroma 14 ndi 15 timaphunzira kuti anthu okhala ku mbali zonsezankhaniyi ayenera kufewetsa zofuna zawo ndi maganizo awo kuti athekusamalirana ndi kukhala amodzi. Uwu ndiwo moyo wa mtanda – Aroma15:1-3. Mpingotu sungathe kukula ndi kuyendera pamodzi popandachimenechi.2) Pomvetsa ndi kubvomereza kuti tiri ndi umunthu wochimwa ndi wodzitamandira.a. Nditha kumafuna kudzikondweretsa ndekha koposa kukondweretsazofunikira za mpingo.b. Nditha kukhala wopanda chidwi chosenza zofooka ndi zosowa za ena.c. Nthawi zina nkhawa zanga za kunyumba kwanga kapena zina zodziwa inendekha kapena kuntchito kwanga ndimazipitiriza ndi kuzilowetsansokumpingo.d. Zolimbana zambiri mumpingo ndi m’mabanja nkhani za “mphamvu” osatizimene zimaonekerazo.3) Pochita zinthu zosagwirizana ndi umunthu m’malo mochita za umunthu pamene titsutsana ndiena.a. Umunthu wathu umatikakamiza kusakomanso ndi anthu omwesitigwirizana nawo. Choncho anthu olekanawo amangopitirirabekulekana.b. Onetsani kupepesa kwanu chifukwa cha umunthu wanu wa uchimopochita zomwe anthu sangaziyembekezere:1. Khalani ndi nthawi yoyanjana ndi omwe simugwirizana mu zambiri.2. Yesetsani kuyamikira ndi kumvetsa maganizo a enawo mosakondera ngakhalesimugwirizana nawo.3. Onetsani zolinga zabwino kwa okutsutsaniwo – 1 Akorinto 13:4-7.4) Yambani mwaganiza bwino kwambiri musanayankhule kapena kuchita.Umodzi 36

a. Tidzayankha mlandu pa mawu onse opanda pake omwe tidzayankhula – Mateyu 12:36-37.b. Mulungu amadana ndi anthu omwe amafetsa mbewu zodanitsa abale – Miyambo 6:19.c. Yesu amapempherera kuti tikhale amodzi kuti dziko likhulupirire kuti Mulungu ndi ameneanamtuma – Yohane 17:20-21.d. Kukanakhala bwino kuti munthu amizidwe m’nyanja yakuya koposa kuchimwitsa mmodziwa aang’ono – Luka 17:1,2.e. Ngati tiononga kachisi wa Ambuye pogawanikana, nayenso adzationonga – 1 Akorinto3:16,17.f. Tiyenera kumadziunika tokha koposa enawo – Mateyu 7:1-5. Mwina chifukwa chakusadziwa, nditha kutsutsa zomwe Mulungu afuna. Nditha kumalimbikitsa zomwe Mulungusafuna. Polimbikira kusunga miyambo ndi zizolowezi nditha kumangofuna maonekedweosati zenizeni zofunikira. Pofunafuna kusintha kwa zinthu nditha kumangofuna kuti ndionemomwe zikhalira m’malo moti zikhale molingana ndikufuna kwa Mulungu kapena kumverakwathu kwa tsiku ndi tsiku. Ngati ndikana kusintha chifukwa cha chiphunzitso chomvekabwino cha malemba, Iye adzandipatsa mphoto. Ngati ndikana kusintha chifukwa chakufunakungokondweretsa maganizo anga ndi zofuna zanga, Mulungu adzandilanga chifukwandalepheretsa ntchito yabwino yobereka zipatso ya mpingo. Nditha kuchita zinthukumpingo zomwe sindinachitepo.4) Pouza zotisautsa zathu kwa wotilakwirayo, ndipo kenako ngati nkofunikira kwaatsogoleri a mpingo – Mateyu 18:15f.a. Popereka kwa enawo chilolezo chomwe ifenso tikadakonda atatipatsa.a. Popita ku tchalitchi ngakhale kuti pali poti dongosolo lomwelikukonzedwalo sitikondwera nalo patokha.bcPoganizira kuti nditha kuupeza mtima ndi kudzibweza ngakhale winaatachita china chomwe ine sindichibvomereza monga cholondola.Pokhala ndi mtima wodekha mwachikondi kwa omwe sagwirizana ndimaganizo anga osintha zinthu.6) Atsogoleri athu pomvetsera mosamala ku maganizo ndi zofunikira zonse mumpingo ndikusankha njira yodekha yomwe idzakhoza kukwaniritsa zosowa za mbali zonse monga momwekungathekere. Mpingo suyenera kukhala ndi maganizo a anthu a mbali imodzi yokha.Abusa oyenera azikhala owonetsetsa ndi odziwa zonse zochitika pa mpingo, akonze ndikugwiritsa ntchito mfundo yodekha yosinthira miyambo ndi zizolowezi, kulemekeza zonsezokhazikitsidwa mwa malemba, kuphunzitsa mpingo kuti uonjezere chidziwitso chake, ndi kuikachitsanzo chabwino cha kulolerana pakati pa atsogoleri okha. Ayenera kumadziwitsiratu mpingokusintha kuli konse kusanachitike.Mawu otsiriza: Palibe chinthu china chomwe mdierekeze angachikonde chopusa kucheptsa ndi kunyozantchito yabwino yomwe ikuchitika m’mipingo. Iye amafuna kuti ife tidziika maganizo athu kwambiri pa zinthuzazing’ono, ndi kutichotsera moyo wodalira Yesu ngati Ambuye wathu, ndinso kutichotsera moyo wofunakukafikira ndi kukachiritsa mizimu. Tiyenera kupereka ulemu wathu wonse kwa Khristu pochita ndi kulekanamaganizo kwathu munjira yoti siting’amba thupi lake, mpingo. Tiyenera kulemekeza atsogoleri athu ampingopamene akuyesetsa kutitsogolera mu umodzi. Ndipo tiyenera kupempherera atsogoleri athu pamodzi ndimpingo wa Khristu.Umodzi 37

Mutu 6: Umodzi ndi Malekano Mumpingo wa Khristu -Yesu anapempherera omtsatira ake kuti akhale amodzi kuti dziko lapansi likamkhulupirire Iye – Yohane 17:20-21. Ntchito yopititsa mtsogolo ufumu wa Mulungu yokhala ikusokonezedwa kwambiri ndi kugawanika pakatipa Akhristu koposa zifukwa zinazo. Ndipo ufumu wa Satana wapindula kwambiri potengera mwayikugawanika kumeneku. Ngati tiri ndi mtima wonga wa Khristu, tidzalakalaka umodzi wapakati pathu ndi anthuena okhulupirira ndipo tidzachita china chirichonse, poyesa yesa kuti pakhale umodzi. M’masiku ano, pamenemipatuko ikuchepera ndipo pali njala yomwe ikukulira yofuna kubwerera ku zoona zokhazokha, nkhaniyotsatira itithandize kuganizira mozama.1. Kodi onse okhulupirira Yesu angathe bwanji kukhala amodzi? M'zaka za m’ma 1800 ku Britain ndi kuAmerica, kunapezeka aphunzitsi ambiri ochokera m’ziphunzitso zosiyanasiyana za mpingo omweanasautsidwa m’mitima yawo chifukwa cha malekano ndi kulimbana pakati pa okhulupirira, omwe anafunakuyanjanitsa okhulupirira onse pobwerera ku ulamuliro umodzi wa malembo achikhulupiriro ndi zochitikaza mpingo. Padali Abner Jones ndi John Wright a gulu la a Baptist; James O’kelley a gulu la a Methodist;ndi Barton W. Stone, Walter Scott, Thomas Campbell ndi mwana wake Alexander Campbell a gulu la aPresbitale. Aliyense wa amenewa payekha payekha anakhumudwa ndi kulimbana ndi kupatukana komwekunalipo pakati pa otsatira Khristu chifukwa cha ziphunzitso. Ndipo aliyense anaona kuti njira yabwinoyoyanjanitsira okhulupirirawa inali yekhayo yobwerera ku ulamuliro wa malembo. Thomas Campbellanayesetsa kugwira ntchito yoyanjanitsa Akhristu a m'gulu la a Presibiteriani omwe anali kulimbana kumpingo wa ku Ayalandi (Irelandi).2. Thomas Campbell, Alexander Campbell ndi Barton W. Stone anali atsogoleri opambana omwe anadziwikanthawi imeneyo pa ntchito yoyesetsa kubwezeretsa chikhulupiriro cha pa malemba ndi kuchita komwe. AThomas Campbell anapita ku America kuchokera ku Scotland. Iye anali pasitala wa mpingo wa aPresibitare, ndipo kudziko la chilendo iye analandiridwa napatsidwa ulamuliro ku mipingo ina yakomwekokomwe iye ankayendera. Campbell anabvutikanso m’maganizo pamene anapeza kuti ku America nakonsokunali magawano ndi magulu omwe anawasiya kwawo ku Scotlandi kuja. Omwe anali a gulu limodzisamalola kuyanjana pamodzi ndi a gulu lina lija ngakhale kuti onse anali a Pulesibitare okhaokha. Ndipom'matauni monse munali magulu odzipatsa maina osiyanasiyana namataya nthawi yawo ndi mphamvuzawo kulimbana wina ndi mnzake, mphamvu zoti anayenera kudzigwirira ntchito yopulumutsira osocherangati mipingo ikanakhala yogwirizana.3. Pamene Campbell anafuna kuyanjana ndi gulu lina lija mwa mgonero, iye anatsutsidwa ndi akulu ampingo. Kenako iye anangoganiza zosiya kugwiritsa ntchito dzina loti “Pulesibitare” nayambakumangotumikira Mulungu wake monga Mkhristu basi popanda kuonjezeranso dzina lina la padera lachipembedzo. Anayamba kuzindikira kuti maina opangidwa ndi anthu ndi zikhulupiriro zake zomwe,zimangolimbikitsa zipupa zamalekano pakati pa magulu otsatira Khristu. Iye anatsimikizika kuti ntchitoyake yonse ikangotsamira pa mphamvu za malemba basi, ndipo anayamba kudandaulira ena onse omweanali m’mipingo kuti asiye kulimbana pakati pawo chifukwa cha miyambo ndi zikhulupiriro zoikidwa ndianthu ndikuti agwirizane pomangoyang’ana pa malembo kuti adziwe komwe akupita ndi choyenerakuchita. Iye analibe cholinga chofuna kuyambitsa mpingo watsopano. Iye anangofuna kuti mipingoisinthike posiya miyambo ndi zizolowezi zomwe inadzipangira ndi kudziunjikira ndipo m’malo mwakeagwirizane ndi kuyanjana pansi pa chiphunzitso ndi machitidwe a atumwi.4. Pamene Thomas anapita ku America, Alexander, mwana wake, anatsala ku Scotland kwa kanthawipamodzi ndi mayi wake ndi ana ena onse. Panthawi imeneyi Alexander anali kuphunzira pa univesite ina.Nayenso, monga bambo wake, anatulukira kuti panali kulekana kwa maganizo mumpingo pa zifukwazazing’ono, ndipo kuti anthu a gulu linalo sanali kulola kuyanjana pa mgonero ndi anthu a gulu linalingakhale onse anali a Pulesibitare okhaokha. Iye anaonanso kuti makonzedwe ndi dongosolo la zochitikaza mumpingo wa a Pulesibitalewu zinali zosiyana kwambiri ndi zomwe iye anaona m’malemba. Pasanapitenthawi Alexander pamodzi ndi ena onse a pa banja lawo anapita kukhala pamodzi ndi Thomasi ku Amerikakuja. Ali ku Amerikako Alexander anayamba kuthandiza bambo ake mu ntchito yodandaulira kuti pakhaleumodzi wosadalira zoikika ndi maganizo a anthu koma zotsamira pa malembo.5. Thomas Campbell analemba bukhu labwino lofotokoza za umodzi pakati pa Akhristu ndi zoyambitsaUmodzi 38

kupatukana. Linatchulidwa “Kunena poyera ndinso kuyankhulira” (Declaration and Address), (onani gawolake ku zoonjezera). Thomas ndi Alexander anaona kuti Baibulo linali chimodzimodzi ku mipingo yonse,koma ziphunzitso ndi zikhulupiriro ndizo zinasiyana. Mipatuko siichokera mu Baibulo limodzi ayi, komaichokera ku zikhulupiriro ndi ziphunzitso zolekanazo zomwe ndi zopangidwa ndi munthu. Mpingouliwonse unali wokonzekera kumvera unzakewo ngati unzakewo ukanasiya zikhulupiriro zake ndiziphunzitso zake ndi kubvomereza za winawo. Koma zonse sizinayenda bwino popeza mpingo uliwonsepawokha unakakamira kugwiritsa zikhulupiriro zake monga zoulamulira.6. Thomas Campbell anayamba kupempha okhulupirira onse kuti ayambe kusiya zikhulupiriro ndiziphunzitso zonse zolembedwa ndi munthu ndi kubwerera ku malemba, omwe ali olandiridwa ndi onse,monga maziko enieni owalamulira ndinso umodzi. Iyenso anapereka maganizo oti anthu asamachitechirichonse mumpingo chifukwa choti atsogoleri awo akale ankachita motero, koma kuti tiwerengenso ndikuphunzira bwino malemba ndi kuchita chirichonse chomwe tichita chifukwa cha mphamvu ndi ulamulirowa malembo.7. Ndipo pamene anapitirira kuphunzira mawu a Mulungu, Thomas ndi Alexander Campbell, mabanja awo,ndi ena omwe ankaphunzira nawo pamodzi anabatizidwa mwa ubatizo weniweni womizidwa. Iwoanazindikira kuti ubatizo wawo wa poyamba wa pamutu sunalingane ndi ubatizo wa mawu a Mulungu,ndipo kuti ubatizo wa pa mutu unali wonga njira za chidule zopangidwa ndi munthu monga chizolowezichabe chomwe chinayamba kuchokera munthawi za atumwi. Anasiyanso kumayang’ana malo ena a dzikokapena bungwe monga boma kapena likulu la mpingo, chifukwa anaona kuti m’mawu a Mulungu mpingouliwonse unali nawo atsogoleri ake osakhalanso pansi pawina aliyense koma pa ulamuliro wa Khristu basi.Anasiya kudalitsa makanda ndi ana aang’ono chifukwa sanapeze ulamuliro kapena chitsanzo chamchitidwe umenewu m’mawu a Mulungu. Anayamba kumayanjana ponyema mgonero wa Ambuye sabatairiyonse pokumbukira imfa ya Khristu tsiku loyamba la Sabata iriyonse chifukwa anaona ndi kuphunzirakuti mpingo woyamba unkatero. Anapitiriza kuphunzirabe ndi kutsatirabe zambiri ziphunzitso ndimachitidwe a mpingo wa Chipangano Chatsopano, ndi kutaya zikhulupiriro ndi ziphunzitso zomweanakhulupirira kuti zinangoonjezedwa ndi anthu m mibadwo yobwera nthawi ya atumwi itapita. Patapitanthawi, Campbell ndi mwana wake anagwirizana ndi Walter Scott ndi Barton W. Stone omwenso nawoanali kulakalaka ndi ntchito yobweretsa umodzi potsamira pa mawu a Mulungu.8. Chiwerengero cha anthu omwe anakhulupirira mfundo zimenezi chinachulukira chulukira ndipo mipingoinabadwa. Zinthu zonga zomwezi zinali kuchitikanso ku Britain. Ntchito yonseyi pamodzi inatchedwa“Ntchito yobwezeretsa” (Restoration Movement). Komatu atsogoleri antchito imeneyi analibe maganizondi zolinga zofuna kuyambitsa mpingo winanso ayi. Iwo anangofuna kuti magulu onse olekana aja akhaleamodzi monga thupi la Khristu motsamira pa malembo. Komabe ngakhale anthu ambiri anabvomerezapempho limeneli, anthu ambiri m’mipingo yambiri anakana, ndipo “Osinthitsa zinthu aja” kapena“obwezeretsa zinthu aja” pamodzi ndi owatsatira awo anangopitiriza monga gulu chabe. Choncho konse kuAmerica ndi ku Britain anthu a m'gulu limeneli ankatchedwa “Akhristu”, ndipo mpingo wa pamalounkatchedwa “mpingo wa Khristu,” “mpingo wa Chikhristu,” kapena “Ophunzira a Khristu.” Koma ndimaina amenewa sanatanthauze kuti iwo okha ndi amene anali anthu ake a Khristu. Sanali kuyesererakutenga malo a Mulungu ndi kuweruza zotsatira zake za okhulupirira enawo. Koma anangokhulupirira kutingati mpingo uli wake wa Khristu, uyenera kumlemekeza pobvalanso dzina lake, monganso momwemkwatibwi amabvalira dzina la womkwatira wake. Sanafune dzina lomwe silinachokere m’mawu aMulungu, ndipo anakhulupirira kuti maina oikidwa ndi anthu osiyanasiyana amangolimbikitsa kusiyanakomwe kulipo pakati pathu.9. Bungwe limeneli lobwezeretsa silinakwaniritse zomwe limayembekeza ndi zolinga zake monga momwezikanakhalira. Panabukanso kugalukirana kwakukulu mzaka za m ma 1900. Pankhani ya nyimbozoimbidwa pogwiritsira ntchito zida munthawi yachipembedzo ndi kukhazikitsa bungwe la a mishonare.Kugawikanaku kunapitirirabe pamene mpingo tsopano unasowa ndi kutaya masomphenya a zolinga zakezoyamba zija. Ena omwe anali kugulu lopanda ukali mubungwe limeneli anayamba kusalemekeza ndikukhulupirira mphamvu ndi ulamuliro wa malemba. Nawo oumirira za miyambo aja anasokonekeransokumbali inayo, nayamba timagulu tina tambirimbiri, namadzitcha kuti iwo okhawo ndiwo ali mpingoweniweni wopulumutsidwa. Zolinga zenizeni zomwe zinatsogolera ntchito imeneyi zinali za kufunika kwamphamvu ndi ulamuliro wa malemba ndi kuipa kogawanikana chifukwa chosiyana maganizo ndikumvetsana pa nzeru zina ndi zikhulupiriro zina. Mipingo ya Khristu inapitiriza ganizo loyambalo komaUmodzi 39

unalephera kumvetsetsa ndi kukumbukira cholinga cha ganizo lachiwiriro. Tinalepherakusiyanitsazinthuzenizeni zotumikira ndi maganizo chabe. Tinali monga gulu limodzi la palokha, logawikam'timagulu tambiri mwa magulu a chipembedzo ku America, logawikana m’magulu opitirira 25. Gulu lathulotchedwa ‘mipatuko’ ndipo kenako tinawapitirira mu njira yolekanitsa, moyo wa mpatuko.Monga momwe kusintha ndi kubwezeretsa kumafunikira nthawi zina, komanso kuli nako kuopsa kwakekomwe kuli kwa mitundu iwiri: Pa momwe amatengera machitidwe a m’Chipangano Chatsopano, angathekunyalanyaza chiphunzitso cha m’Baibulo pazakusinthika mtima kwa mumtima (komwenso umodziumatsamira). Ndipo angayambe kukhala ndi moyo woyang’ana ndi kudalira malamulo, kukhulupiriro kutiMulungu amatilandira chifukwa cha kusunga malamulo kuposa chifukwa cha chisomo cha ulere chapamtanda wa Khristu. Ntchito yosintha ndi kubwezeretsa imeneyi nthawi zambiri yakhala ikugwera mmisampha yonse iwiri. Ngakhale panthawi yomwe ntchitoyi inali pa kaindeinde, sikunatheke kubwezeretsachiphunzitso cha m’Chipangano Chatsopano, machitidwe ndi moyo wabwino sizinatheke kufika pomwezinali kufunikirapo. Iyi ndi ntchito yoti imangopitirira.Wolemba ameneyu akukhulupirirabe kuti “mfundo yobwezeretsa” ndi yofunikirabe yoyenera kupitirira,makamaka kusiya miyambo ndi zizolowezi zopangidwa ndi anthu ndi kupitiriza kuyanjanitsa okhulupiriraonse mwa kutsamira pa mphamvu ndi ulamuliro wa mawu a Mulungu basi. Palibe yemwe angatsutsemfundo imeneyi. Ngakhale mfundoyi yakhala ikulephera m’magawo ena, ntchito yobwezeretsayi yalalikandi kufalitsa uthenga wamtengo wapatali ndi wofunikira kwambiri wonena za kutsamira ndi kudalira pamphamvu ndi ulamuliro wa malembo, ndiponso waturutsa atumiki a Mulungu ambiri omwe agwira ntchitoyotamandika kwambiri. Ndipo sionse a atsogoleri a gulu limeneli omwe anakhala ndi mtima wampatuko.Abambo anga a ine anakana kulowa m’gulu la mpatukolo ndipo zotsatira zake ndi zoti anazunzidwakwambiri. M’masiku atsopanowa, magulu ena omwe anachoka mogalukira analapa ndipo analandiridwam’chiyanjano chathu.10. Mpingo uyenera kumayendetsedwa mwa ulamuliro ndi mphamvu za malemba okha m’chikhulupiriro ndim’machitidwe wokha basi, chifukwa:A. Miyambo ndi ziphunzitso zongoonjezeredwa ndi anthu zimagawanitsa Akhristu – Aroma 16:17.B. Akhristu ayenera kumvera mawu a Khristu Ambuye wawo ndipo ayenera kumachita chifuniro chawomonga momwe chinaululidwa m’Baibulo. Iwo alibe mphamvu ndi ulamuliro wosintha chimenechinalamulidwa ndi Ambuye kapena atumwi awo. Onse okonda Khristu ayenera kumalakalakakumukondweretsa pomvera ndikudzipereka ku mawu ake – Yohane 14:21,23; Luka 6:46.C. Mulungu sakondwera ndi mapemp0hero athu pamene tilowetsa miyambo ndi zizolowezi zopangidwandi anthu m’malo mwa malamulo a Mulungu – Mateyu 15:3-9.D. Sitingathe kupeza nzeru za mtundu woposa nzeru za Mzimu Woyera zomwe zifotokozedwam’malamulo a atumwi ndi zitsanzo za mumpingo woyamba.11. Atsogoleri oyamba a gulu la kubwezeretsa aja, anali okhudzidwa kwambiri ndi nkhani ya umodzi pakati paAkhristu. Iyi ndi nkhani ya Baibulo. Mu Aefeso 4:4-6 Paulo akutiuza wapereka mndandanda waziphunzitso zisanu ndi ziwiri (7) za zoonadi zake zomwe mipingo yonse pamodzi ndi Akhristu onseayenera kugwiritsa ndi kukhala nazo mofanana ngati afuna kukhala ndi “umodzi wa Mzimu Woyera” mwaKhristu. Iye akutchula thupi limodzi, Mzimu mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, Ambuye mmodzi, ubatizoumodzi, ndi Mulungu mmodzi. Awa ndiwo maziko enieni a chiphunzitso cha umodzi.Komabe kungomvana ndi kugwirizana pa chiphunzitso chokha sikungayanjanitse Akhristu. Koyambirirakwa ndime yomweyo ya umodzi, pa Aefeso 4:1-3, Paulo akutiuza za mtima womwe Akhristu ayenerakukhala nawo kuti asunge ndi kusamalira umodzi pakati pawo. Iye akutchula, kudzichepetsa konse,chifatso, chipiriro ndi kulolerana mwachikondi. Malingana ndi Pauloyo, umodzi ndi chinthu cha Mzimu,ndipo zoyeneretsa zomwe zasanjidwa pamenepazi ndizo chipatso cha Mzimu Woyera – Agalatiya 5:22,23.Kulikonse komwe Paulo anapita, iye amaphunzitsa kuti Akhristu sayenera kuweruzana wina ndi mnzakekapena kulekana chifukwa cha mfundo zazing’ono, zomwe angathe kukambirana ndi kusankha maganizoomwe afuna ponena za m’Baibulo ndi ziphunzitso zake, koma ayenera kungosiyira nkhani zimeneziUmodzi 40

Mulungu pamene iwo apitiriza kugwira ntchito pamodzi. – Aroma 14:1-15:7. Kugawanikana pa zinthuzimenezi pakokha ndiko kusamvera malemboko. Baibulo litiphunzita kuti ife timayanjanitsidwa ndikukhala amodzi chifukwa choonadi chenicheni cha chilungamo osati chifukwa choti tagwirizana ndikufanana maganizo pa mfundo zina zazing’ono. Ndipo kupatukana kwambiri sikumabwera chifukwachosamvana pa ziphunzitso koma chifukwa mtima wofuna kudziganizira wekha, ndinso makani chabe –Agalatiya 5:19-21; Aroma 16:17,18. Nthawi zambiri nkhani za chiphunzitso ndi chikhulupirirozimaperekako mwayi wa ulemu; zoterezi zikanatha kukonzedwa ngati pakanakhala mtima wabwino ndikulakalaka kwenikweni kwa umodzi. Titha kukhalabe okhulupirira ndi kudalira malemba pa chiphunzitsondi chikhulupiriro chathu ndi machitidwe athu, koma ndi kulekanabe maganizo ndi kumagawikanabe,kumapitirirabe kupikisana kufikira mitima yathu itasinthika ndipo umulungu utabadwa mwa ife mwaMzimu Woyera ndi mawu. Nthawi zambiri kupatulana chifukwa cha zipembedzo, sichifukwa ayi, komakungofuna kulimbana kudzifunira kutchuka, kudziyeretsa pobvala mwinjiro wa chipembedzo. Ngakhalentchito yobwezeretsa inachita gawo lalikulu pobwerera ku kudalira ku maziko a chiphunzitso ndimachitidwe a malemba, sunathe kupitiriza mpaka pa ndime yokonzanso za bvuto la kufunika kwa kusinthakwenikweni kwa uzimu ndi kusinthika kwenikweni kwa mkati mwa mtima.Choncho pofuna kukhala ndi umodzi wachipembedzo, chiphunzitso chathu chiyenera kupitirirabe kusinthikapogwiritsa ntchito malemba, ndipo mitima yathu nayonso isinthike pogwiritsa ntchito Mzimu Woyera. Zonsezikuti zitheke pamafunika kudzichepetsa. Munthu wodzitukumula ndi wonyada sangathe kusiya ndi kuiwalazikhulupiriro ndi zizolowezi zake za umunthu pamodzi ndi moyo wake wozolowera zolimbana ndi zotsutsana.Ndipo kudzichepetsa kumeneku kumatheka pokhapokha pamene tibadwanso mkatikati mwa mtima wathu mwaMzimu Woyera ndi kupatsidwa umoyo watsopano wa Yesu Khristu. Tiyeni tidzipereke kumoyo womvera ndikukhulupirira malemba ndi Mzimu Woyera. Pakutero tidzakwaniritsa pemphero la Ambuye Yesu: “[Ine ndipemhera] kuti onsewa akakhale amodzi … kuti dziko lapansi likakhulupirire kuti inu munandituma ine” –Yohane 17:20,21.Mutu 7: Mpingo wa Khristu ndi Zipembedzo Zina za Chikhristu.Ngati umodzi uli wofunikira kwambiri mu ntchito yofalitsa uthenga wabwino, ndi koyenerera kuti tionensobwino pa za momwe timaganizira magulu omwe analowa nawo mu gulu losintha sintha zija. Nkhani zina zaziphunzitso zomwe zimatigawanitsa pakati pathu zimakhala zokulirapo. Komanso mwa chiyero, timayenerakuyamikira ndi kuthokoza pa zinthu zomwe anthu achita bwino, poonjezera pakudzudzula ngati alakwitsa.Ndiri wokondwa chifukwa ambiri pakati pa abale alibenso mtima wofuna kutenga udindo wa Mulunguwoweruza ena omwe ali mu “zipembedzo zina.” Tingathe kukhala okhulupirika m’malembo popanda kutero.Ndimasanalatsidwa ndi mawu amphamvu omwe ena a abale m’mipingo ina amanena, “osati Akhristu okhawo,koma Akhristu okha.” Yesu analangiza ophunzira ake kuti asaletse iwo omwe anali kutumikira m’dzina lakengakhale sanali nawo m’gulu limodzi. Paulo anali wokondwera chifukwa Yesu analalikidwa ngakhale ena aolalikawo sanali ndi zolinga zowona.1. Mipingo ya Khristu mzaka zatsopanozi, zaposachedwapa inayamba kudziwika mona yokhulupirira kuti ndiyekhayo yodziwika kuti ndi yopulumutsidwa. Ndiri wokondwa chifukwa tsopano pali kusintha, chifukwaizi si zomwe abale athu omwe amayamba ntchitoyi anakhulupirira. Abale omwe anayambitsa kuti Mulunguanali nawo anthu ake omwe anali m'zipembedzo zosiyanasiyana. Anapempha Akhristu onse kuti asiyeziphunzitso ndi zikhulupiriro ndi kugwirizana mwa kumangiririka pa malemba basi. Bambo wangaanandiphunzitsa kuti munthu aliyense yemwe wabadwanso kawiri, nalandiridwa ndi Mulungu, ali gawo lathupi la Khristu ngakhale mipingo yathu isamdziwe kaya imdziwe. Tikanakomana nako kuzunzidwamwadzidzidzi, maganizo athu onse akadasinthika tsiku limodzi pa umodzi wathu. Tikanayamikirakwambiri aliyense yemwe alemekeza Yesu monga Ambuye ndi kuyeserera kumumvera.2. Gulu lathu lachita ndi ziphunzitso zina zofunikira zomwe enawo amazifuna. Mwa chitsanzo, AlexanderCampbell anali mmodzi wa anthu omwe anayambirira kuona ndi kulalikira za kusiyana kwa pakati pamapangano akale ndi atsopano, ganizo iri tsopano likuvomerezedwa ndi kulandiridwa ndi zipembedzo zinazomwe zimakana kusintha mwa chisawawa. Ndimakhulupirira kuti tiri nazo nzeru zofunikira pa za ubatizondi utsogoleri mu mpingo.3. Anthu adzatimvera ngati tiwalemekeza ndi kuwakonda. Kwa zaka zambiri, ndakhala ndi kuganizira kutingati tifuna kuti anthu amvetse bwino zikhulupiriro zathu, kunali bwino tikanakhala nayo njira yabwinoyochitira zimenezi. Kudzichepetsa ndi chikondi kungatithandize kukalowa m’mitima yomwe kuuma moyoUmodzi 41

ndi chipongwe, ndi kupikisana sikungalowe (2 Timoteo 2:24-26). Mmodzi wa ophunzira anga, mkuluwampingo, anandiuza kuti sanakhulupirira kuti mipatuko ingadzathetsedwe kufikira pamene anakhala ndikuphunzira mu maphunziro a SHBI ndi kuona anthu ochokera ku mipingo yosiyanasiyana mwa chidwiakubvomereza chiphunzitso cha Baibulo. Mkulu wina anadabwanso Poona momwe anthu amenewaanachita pokhalabe m’maphunziro ake omweo amfundo za kubwezeretsa omwe takhala tikuphunzitsanthawi zonse.Tsiku lina madzulo ndinali kuphunzitsa pofotokozera chiphunzitso cha Calvinistic chomwe chimatichirichonse chimatsogoleredwa ndi Mulungu ndipo palibe mwayi wopanga chisankho chifukwa Mulungundiye amaoneratu zonse. Wina anathirira ndemanga yoti “zimenezi ndiye zitinso?” Ife timakhulupirira kutiMulungu amatipatsa mwayi wosankha chifuniro chathu.” Tsiku lina usiku ndinafotolozera za nkhani yaNamani wakhate yemwe chikhulupiriro chake chinayesedwa polamulidwa kuti akasambe mu mtsinje waYordano. Ndinafotokoza kuti nthawi zambiri Mulungu amafuna muyezo wina wake wa chikhulupiriromonga njira yoonera chikhulupiriro chathu. Mkulu wina wopuma pa ntchito monga mphunzitsi wamkuluyemwe anali ndi zaka 80, wampingo wa Baptist, wa nzeru zake ndithu, anafunsa kuti, kodi nawonsoubatizo ungakhalenso njira yoyesera chikhulupiriro? Nthawi zonse ndimafotokoza kuti ubatizo ndi gawondi nthawi yomwe chikhulupiriro chathu chimakumana ndi chisomo cha Mulungu ndi kubweretsachikhulupiriro. Ndi kukhulupirira kuti kupambana kwathu kungathe kufanizidwa bwino ndi kwa winaaliyense pamene tifika pa ndime yolandira ulemu pa maganizo a chiphunzitso ndi chikhulupiriro chathu.4. Ine ndimakhulupirira kwambiri monga ndakhala ndi kuchitira nthawi zonse pa za ubatizo, ngakhalendimaganizanso kuti pena pakenso sitinaganizire bwino ndipo tinasokoneza chiphunzitsochi chifukwachochita nacho mopitirira. Ngati mwana analandira ubatizo wa pamutu ali mwana, ndingamulimbikitse kutiakwaniritse ndithu chiphunzitso cha Ambuye cha ubatizo ndipo achite zimenezi ndi chikhulupirirochakechake. Ngakhale kuti asanatulukire ndi kuona kufunika kwa zimenezi, sikuti ndikanakhala naye ndiubale wofanana ndi womwe ndingakhale ndi wina yemwe amakaniratu Yesu kukhala Ambuye wake.5. Nimakhulupirira kuti kulakwitsa kumodzi kuopsa komwe kunachitika mu mbiri ya nthawi zosinthayi, pambali yogawanitsa thupi la Khristu, kunali kukhulupirira kuti, “kuti ubatizo ukhale waphindu,wobatizidwayo ayenera kumvetsa kuti ubatizowo umachotsa machimo. Maganizo amenewa amafalitsidwandi mzaka za 1900 ndi Austin Mc Garry, yemwe anali mlembi woyamba wa bukhu lotchedwa “mazikoolimba” (Firm foundation). Chifukwa chenicheni cholembera bukhu limenelo chinali choti anthu aunikirendi kuona ngati kubatizidwa kawiri ndi kwabwino malingana ndi maganizo a David Lipscomb, mlembi wabukhu lotchedwa “kuyankhula mogwirizana ndi uthenga” (Gospel advocate) ku Tennessee ku America.A. A Baptist ambiri akhala akuphunzitsa kuti chikhululukiro chimabwera panthawi yomwe munthuakhala ndi chikhulupiriro mwa Khristu monga mpulumutsi, ndipo kuti ubatizo umangoonetserakuyeretsedwa komwe kwa chitika kale. Mbale Lipscomb anali mmodzi wa atsogoleri omwe anagwirantchito pakati pa mipingo ya Khristu kumwera kwa America. Iye anakhulupirira monganso ambiri a ifetichitira, kuti ubatizo ndi nthawi yomwe ife timalandira chikhululukiro cha machimo. Koma iyeanakhulupirira kuti sikwabwino kubatizanso kawiri mbaptist yemwe anafuna kulowa m’misonkhanoyathu. Iye anafotokoza kuti popeza anthu omwe anatembenuka mwa a Baptist amakhulupiriransompulumutsi yemweyo amene ifenso timkhulupirira, anamva chisoni chifukwa cha machimo awo,ndipo anafunitsa kukhululukira machimo ndi kubwera kwa Khristu monga mpulumutsi wawo ndiAmbuye wawo, ndipo popeza ambiri a iwo ndi cholinga choti akadzichepetse ndikudzipereka kucholinga cha Mulungu, onse omwe anachita zimenezi analandira ubatizo woyenera ndi wolondola.Lipscomb anakhulupirira kuti ngati panali chikhulupiriro chodzichepetsa mwa Mulungu, sikunalinsokofunikira kwenikweni kuti munthu amvetse bwino machitidwe a nthawi yomwe iye anayeretsedwa,kapena kutsatira mwatsatanetsatane lemba lirilonse lofotokozera za dongosolo la ubatizo. M’Njira ina,amanena kuti, ife tomwe tinabatizidwa popanda kumvetsetsa bwino za mphatso ya Mzimu Woyeratinayenera kubatizidwanso kawiri kuti tilandire Mzimu Woyera. Nkhani yonse iri mu bukhuLolembedwa ndi Jimmy Allen lothedwa “kubatizidwanso” (Rebaptism).B. Alaliki athu oyambirira aja a m'gulu losintha zinthu aja sanabatiza kawiri a Baptist aja ayi komaanangowatenga iwo ngati ziwalo za thupi la Khristu. Mipingo yambiri ya Khristu ya ku mmawa kwamtsinje wa Mississippi ku America anachitanso mogwirizana ndi maganizo a Lipscomb, ndipo paUmodzi 42

mafika mzaka za m'ma 1980 iwo ochitira umboni uthenga anali kugwirizanabe ndi maganizo aLipscomb obatizanso kawiri. Mipingo yambiri ku Texas ku America, kumbali inayi, inakopedwa ndiMc Garry ndipo anayamba kuwatenga onse obatizidwa ndi a Baptist ngati osapulumutsidwa. Ine ndikukhulupirira kuti Lipscomb amalondola. Panalibenso njira ina yomwe tikanagwirizana kapenakuganizira monga momwe taganizira kapena kugwirizanira pa ubatizo. Mwa chitsanzo, ngati malamuloa boma lathu akanakhala kuti amafuna zonse, malumbiro a akwatiwo ndinso ………. Kuti apangeukwati weniweni wobvomerezeka, ndipo ngati akwatiwo adachita zonsezo koma ndi kuganiza iwoanalowa kale banja pochita malumbiro awo basi, ndani wa ife angathe kuwachititsa kuti abwererensonakayambenso ukwati wawo? Kodi sitikanakwanitsidwa popeza cholinga chawo chenicheni chinalichofuna kulowa banja ndipo anachita zinthu zonse zofunikira? Ine ndi kuona njira ya Mc Garryyobatizanso kawiri ngati gawo limodzi pa zochitika zoloza ku magawano ndi kulekana maganizo pamalamulo, ndiponso losagwirizana ndi mtima kapena Mzimu wa uthenga. Ndipo ngati Lipscomb analiwolondola ndi wokhoza, ndiye kuti tiri ndi abale ndi alongo ochuruka koposa momwe timaganizira.6. Poonjezera pa kuononga komwe kumabwera chifukwa cha kugawanikana ku uthenga, munayambamwaganizira za momwe timachimwira pamene tikana abale ndi alongo omwe Mulungu anawalandira?Kumbukirani wamkulu uja anamutcha mwana wolowerera uja kuti “mwana wanu uja” m’malo moti“mbale wanga.” Kodi ife mwa kusadziwa kwathu sitinanenepo zinthu zina zonyoza anthu ena omwe ndiodzadza ndi chikhulupiriro ndi odzipereka kwambiri kwa Khristu ndiponso ali a nzeru ndi odziwa malembamonga ife tiriri? Mzaka zanga zoyamba ntchito yanga yotumikira ngati m’mishonare, ndinalemba nkhaniza ubatizo zomwe ndimaika kunja ana a Mulungu ambiri. Ndiri wodzadzidwa ndi manyazi ndipo ndikupempha chikhululukiro kwa Mulungu ndi kwa inu a mumpingo.A. Ngati Mulungu amagwiritsa ntchito chizindikiro cha Mzimu Woyera monga chomdziwitsa za anthuake, kodi ife tingathe kunyalanyaza chipatso chobadwa chifukwa cha Mzimu Woyera wopezekam’miyoyo ya okhulupirira odziperekawa?B. Kodi ife tokha tiri ndi choonadi chonse? Tiri ife kodi olungama, kapena tidalira pa chisomo? Ngatitidalira chisomo, kodi ndiye kuti chisomocho chimangogwira ntchito pa kuperewera kwathu kokha,kapenanso ngakhale zolakwika zosiyanasiyana ndi zofooka za anthu ena? Kodi tikudziwa ntchitoyaikulu yomwe chisomo chimagwira pamene anthu alemekeza Khristu monga Ambuyemokhulupirika? Kodi tidayamba tapanga chisankho pakati pa chisomo ndi lamulo?7. Tinasochera kuchoka pa kumvetsa bwino zomwe malemba anena za umodzi womwe unaphunzitsidwa ndiomwe anayambitsa ntchito yobwezeretsa. Tiyenera kulapa ndi kupempha chikhululukiro cha Mulunguchifukwa chokaniza ana ambiri a Mulungu powatcha akunja, osapulumutsidwa. Ntchito ya gulu lathuliyakhala ikutsutsa ena chifukwa chogawikana ndi kulowa m'mpitatuko. Komanso pamene nafenso tiri nditchimo longa lomwelo. Mau oti “mpatuko” satanthauza “munthu yemwe amaphunzitsa kuti kudzilekanitsawekha podzitengera dzina la padera lakolako. Nakhale dzina loti mpingo wa Khristu ndi dzina labwinongati cholinga chathu chiri chongofuna kulemekeza Khristu, nkotheka kusagwiritsa ntchito dzinalimoyenera wampatuko ngati cholinga chathu ndi chodzilekanita ndi anzathu monga mpingo wokhawowokhulupirika woyenera kumasonkhana wokha. Baibulo limapereka maina ambiri ampingo, koma mipingoyambiri yomwe tipembezako singalole kutchulidwa “mpingo wa Mulungu,” kapena “Banja la Mulungu,”“ana a Mulungu.” Izi zikungoonetsa momwe ambiri a ife takhalira amipatuko pa za dzina loti “mpingo waKhristu.”Tikukhala m’masiku oyipa ndipo kuipitsitsa kungabwerebe. Tiyenera kufikira ambiri a osochera mongamomwe tingathere. Ndi kovuta kukonza zofooka ndi zotchinjiriza zomwe zimasokoneza uthengazoyambitsidwa ndi malekano osafunika osabvomerezeka ndi Baibulo. Posachedwapa tidzaima pamaso paMulungu. Tiyenera kuopa Mulungu koposa zinthu zomwe munthu sadzibvomereza. Tiyenerakudzichepetsa ndikachita ndi pemphero la Ambuye lija la umodzi ndi chidwi chonse. Tiyenera kugwiranadzanja ndi okhulupiria ena omwe anabadwanso mwatsopano kuzipembedzo zinazo, ndi anthu omwe mwaiwo Mzimu Woyera akuchita nawo mwa chionekere. Kuti tichite izi sikuti tiyenera kutaya chimodzi chazikhulupiriro zathu za m’Baibulo. Pamene ubale pakati pathu ndi iwo ukukula, ndipo pamene akuonaKhristu mwa ife, adzayamba kulemekeza kwambiri Khristu pa china chirichonse chomwe KhristuUmodzi 43

adzawaphunzitsa kudzera mwa ife. Ndipo ngakhale atapitirira kulekana maganizo pa zina zazing’onom’malemba, izi siziwachititsa kuti akhale anthu osochera ayi. Anthu sapulumutsidwa chifukwakukhulupirira bwino za mphamvu za Mulungu pozifanizira ndi chifuniro chake cha munthu, kapena pa zaBaibulo lotanthauziridwa bwino, kapena pa za mphatso za Mzimu Woyera kapena pa za makhalidwe ake apakutha pa zaka chikwi. Chomwe chimafunikira kwambiri ndi ubale wathu ndi Khristu. Ngati ena a ifeadzapulumutsidwe, chidzakhala chifukwa cha mphatso ya mwazi wa Khristu, osati chifukwa choti tinaliolondola ndi ochita bwino pankhani zonse za malemba ayi.Malekano akufa pang’onopang’ono m’malo ambiri. Anthu tsopano akukhala ndi chidwi chofuna kuiwalakusinjirirana za mipatuko ndikuyamba kungomvera chiphunzitso cha Baibulo chosavuta. Mipingo yambirim’dera la kwathu posachedwapa yasiya maina odzipatsa chifukwa cha kupatukana. Mipingo yambiri yaganiza zomatsogoleredwa ndi akulu a mpingo kaya kuti oyang’anira – Abusa. Anthu a m’zipembedzozambiri akuitanitsa ziphunzitso zotsamira ndi kudalira Baibulo. Anthu mazana anayi (400) ochokera kuzipembedzo zosiyanasiyana m’dera la Houston amalembetsa kuti alowe m’maphunziro ochitika pa sukuluya Baibulo ya South Houston chaka chiri chonse. Ife timaphunzitsabe zomwe tikhulupirira za Baibulo,ndipo popeza timawaphunzitsa anthuwa mwa ulemu ndi modekha mwa Mzimu ndi moyo wa Khristu, iwoamakondweretsedwa kubwera ndi kudzaphunzira.Ngakhale mu Chikatolika mulinso kubwerera kumachitidwe a mpingo woyamba; mpingo uliwonse womwendi womangidwa m’masiku ano ku Houston udzakhala nalo damu lobatizira pobiza thupi lonse. Mkuluwina wachinyamata wa mpingo wa Hispanic anabwera ku ofesi kwanga sabata yathayo ali wosangala ndiwotengeka chifukwa anali wofuna kuyamba maphunziro. Iye amachokera ku mpingo womwe unasankhakudzitcha kuti “mpingo wobwezeretsa”. Iye amafulumiza kuzindikira za malingaliro athu obwerera kuBaibulo. Sikuchokera zaka mazana awiri (200) zapitazo pamene takhala ndi mwayi wothandiza anthu kutiakhale amodzi mwa kudzichepetsa kwa malemba.Zoonjezera: Zothandizira Zina pa Phunziro la UmodziMafunso Othandizira Phunziro la Aroma 14:1-15:131. Kodi anthu onse a mumpingo amamva mofanana, kapena ali ndi chidziwitso cha chikhulupirirochofanana? 14:1.2. Kodi “nkhani zazing’ono” ndi chiyani? (14:1). Kodi mawu amenewa a masuliridwa motani m’mabukuenawo?3. Kodi mfundo zonse za choonadi cha chipembedzo zimamveka mofanana m’malemba? Kodi mfundo zonsendi zofunikira monga maziko a chipulumutso?4. Kodi alipo Mafunso ena okhudza za chipembedzo kapena makhalidwe a Chikhristu omwe kungatheke kutiAkhristu awiri okhulupirika angathe kusiyana maganizo?5. Kodi ndi nkhani ziwiri ziti zazing’ono zomwe Paulo apereka mona zitsanzo mu Aroma 14:2-8? Kodimuganiza kuti kusiyana maganizo kumeneku kunachokera m’maganizo ati?6. Kodi chikhulupiriro chofooka (kapena chidziwitso cha choonadi cha chikhulupiriro) chidampangitsabwanji kukhala ndi moyo wolimbikira kukana zina?7. Kodi ndi zinthu zinanso ziti zomwe timaonetsa kulekana kwathu (zazing’ono) zomwe ziriponso pakati paAkhristu lero?8. Kodi Mkhristu wolimbayo (wosabvutika ndi chikumbumtima chodziletsa) anayesedwa pokhala ndi moyowotani kwa mbale wake wofookayo? Kodi mbale wofookayo anayesedwa ndi moyo wotani kwa mbalewake wosamangikayo? 14:3,10.9. Kodi Paulo anamlamulira chiyani mbale wolimbayo? Nanga wofookayo, womangikayo? 14:3,10.Umodzi 44

10. Kodi pamenepa ndiye kuti Paulo akunena kuti anthu angathe kukhala ndi zikhulupiriro zosiyana ndinsomachitidwe osiyana munkhani zimenezi komabe ndi kumakhalirana bwino mwa mtendere mumpingoumodzi?11. Kodi ziripo mfundo zina zofunikira ndinso choonadi chomwe tonse tiyenera Kudzibvomereza ndikuzilandira ngati tifuna kuti tikhale amodzi? Aefeso 4:1-6; 1 Akorinto 15:3-8; 1 Timoteo 3:16.12. Nchifukwa chiyani payenera kukhala kulolerana ndi kugonjerana pokhudza nkhani zazing’ono ngati tifunatigwire ntchito ngati mpingo?13. Nchifukwa chiyani kuli kobvuta kugwiritsa ntchito chiphunzitso ichi cha kulolerana ndi kugonjera pamfundo zokhudza kupembedza kwa gulu lonse osati pa mfundo zokhudza kungosintha chabe?14. Kodi tilipire yani nkhani za zolimbana zazing’ono zing’onozi? 14:10-12.15. Kodi abale omwe asiyana maganizo ayenera asachite chiyani? Ayenera alimbikire chiyani? 14:13.16. Ngati munthu akayika ndi china kapena mfundo ina, kodi iye mwini ayenera kuchita chiyani? 14:14,23.17. Ngati mbale wofookayo womangika m'chikumbumtima ali pomwepo kapena zimkhudza, kodi mbalewolimbayo wosakaikayo asachite chiyani? 14:13-21.18. Nanga naye mbale wofookayo, kumbali yake asachite chiyani? 14:3,13.19. Kodi ndi kulakwa kuti mbale wofookayo odzudzula ufulu wa mbale wake wolimbayo monganso momwembale wolimbayo kuchita zinthu zomwe zikhumudwitse mbale wofookayo? Kodi machitidwe awirionsewa amalimbikitsa kulakwirana ndi magawano pakati pa Akhristu?20. Kodi tiyenera kuika umodzi ndi moyo wabwino ndinso kuchita bwino kwa mpingo patsogolo pa chiyani?21. Kodi olimba ayenera kumachita chiyani? Nanga sayenera kumachita chiyani ngati atsata chitsanzo chaKhristu? 15:1-3.22. Nchifukwa chiyani kumakhala kosabvuta kuti mbale wolimba azindikire kuti nkhani iyi ndi yaing’onokusiyana ndi mbale wofooka? Kodi zingatheke kuti mfundo ina iwoneke ngati lamulo koma ndi kuthekakuti ine ndizindikirebe kuti pali mpata woti ndi sagwirizane nazo mokhulupirika?23. Tiyenera kumalolerana wina ndi mnzake m'njira yomweyo yonga ndani analandira ndani?15:7.24. Kodi zimene zija zinangochitika chifukwa cha kuchita bwino kwathu, kapena chifukwa cha chisomo?25. Ngati mbale wolimba uja ndi wofooka uja analibe chidwi chochita ndi kulekana maganizo kwawomogwirizana ndi maganizo a Paulo aja mundimeyi, koma kulimbikira pa kudzudzulana kapenakunyozana, kapena kulakwirana mwadala kotero kuti kulekana kukanayambika, kodi mpingoukadatani nawo? 16:17,18.26. Yemwe anachita motere sanatumikire Khristu kapena kukonda koma anali kutumikira chiyani?27. Kodi 1 Akorinto 8:1-13 ndi 10:23-33 akulozera chiyani munkhani imeneyi?28. Sititaya kwakukulu ngati titaya nyama ndi cholinga chofuna kupewa choyambitsa kupunthwa. Koma nangabwanji ngati palinso china chomwe mpingo ukanapindula nacho ndi kufikira mizimu yambiri, komachikhumudwitsa m’modzi kapena awiri mumpingo? Kodi nthawi zina timathawitsa abale kapenakufooketsa abale ambiri ndi cholinga chofuna kupewa kukhumudwitsa ochepa? Kodi Paulo amatanthauzazimenezi pa chiphunzitso chake cha m’misonkhano chija?Umodzi 45

Zothandiza Powerenga Aroma 14:1-15:7Mu Aroma 14:1-15:13 Paulo akupitiriza kuphunzitsa za machitidwe akhalidwe ndi moyo wa Mkhristumalingana ndi chifundo chomwe Mulungu wationetsera. Gawo limeneli likuona mwapadera momwetingakhalire ndi umodzi mumpingo ndinso monga abale ndi alongo mwa Khristu, ngakhale timakhala nakokusiyana m’maganizo ndi zikhulupiriro pa nkhani zina “zazing’ono.” Iri ndi bvuto lomwe limakhalapochifukwa cha umunthu wathu wauchimo kuchokera mu zifukwa zosiyansiyana ndi masiyanidwe a makulidwem'nzeru ndi kukhwima.Zoyenera kuyang’ana mu Aroma 14:1-15:1314:1: Yemwe chikhulupiriro chake chiri chofooka mumlandire. Yemwe ali womangika malinga ndichikumbumtima chake ndipo “amangosiya” zinthu zambiri zomwe Mulungu sanaletse; yemwe sanakhwimem’chikhulupiriro ndi chidziwitso cha Khristu kokwanira kuti amvetse ufulu womwe tiri nawo mwa Khristu.Popanda kuweruza pa zinthu zazing’ono [NASB: osati ndi chifukwa chofuna kuweruza malingana ndimaganizo ake; RSV: koma osati chifukwa cholimba pa maganizo.]Mawu a Mulungu anazindikira kuti chifukwa cha kufooka kwathu kwa umunthu, mfundo zonse zolondolakapena zolakwika zimamveka bwino kwa ife, choncho zina ndi zoti titha “kulekana maganizo.” Komansom’malembo sananenemo zambiri za Mafunso ena koposa enanso. Mpata ulipo kwa anthu okhulupirika, oopaMulungu wosiyana maganizo munkhani ngati zimenezi.Malembonso amazindikira kuti sinkhani zonse za chikhulupiriro cha Chikhristu chachikulu mofanana kapenamofunikira – Mateyu 5:19; 23:23. Alipo malemba omwe ali ndi mndandanda wa ziphunzitso ndi zikhulupirirozazikulu – Aefeso 4:4=6; 1 Akorinto 15:3=4; Aroma 14:17; Mateyu 22:35-40. Ziphunzitso zazikulu zimenezizomwe ziri monga maziko zimaphunzitsidwa m’malemba kawirikawiri komanso mwadongosolo kuposa zinazazing’ono zija. Palibe mwayi waukulu wololedwa kulimbana pa ziphunzitso zazikuluzi.Mulungu amvetsa mwangwiro, koma amadziwa kuti ife sitiri choncho ayi. Gawo limeneli likuonetsa poyerakuti titha kukhalirana pamodzi ndi kumagwira ntchito pamodzi mumpingo popanda kugwirizana pa mfundozina zazing’ono, zomwe pa umunthu wathu mwayi ulipo woti titha kutsutsana mokhulupirika. Palibe wina waife yemwe amaona zinthu mwangwiro, kapena yemwe amamvera mwangwiro. Chisomo chiyenera kutchinjirizakusamvetsa kwathu monga momwe chimatchinjirizira kusachita mwangwiro kwathu. Ndipo tiyenera kuchitirachifundo iwo omwe timalekana nawo maganizo monga momwe Mulungu amapatsiranso ife chisomo. Tiyenerakukana yemwe akana chiphunzitso ndi chikhulupiriro chachikulu, chofunikira chenicheni cha Chikhristu – 2Yohane 9-11. Koma tiyenera kulandira, osati kukana, yemwe tasiyana naye mu nkhani ndi mfundo“zazing’ono.”Kodi tingadziwe bwanji zomwe ziyenera kutengedwa ngati nkhani zazing’ono?14:2-12: Kuchokera mu mpingo wa ku Roma, Paulo akupereka zitsanzo ziwiri za nkhani zazing’ono zomweAkhristu angathe kusiyana maganizo komabe ndi kumagwira ntchito pamodzi mwa Khristu. Chikhulupiriro chamunthu wina chimlola kudya chirichonse (iye akudziwa kuti Yesu “anayeretsa zakudya zonse” – Marko 7:19 –ndi kutinso “fano sirili kanthu” – 1 Akorinto 8:4) – Koma munthu wina, amene chikhulupiriro chake chirichofooka, adya masamba okha. Iye akhulupirira kuti ndi kuchimwa kapena kungakhale kuchimwa kudyanyama. Omasulira ena amaganiza kuti yemwe akumangikabe ndi lamulo la Chipangano Chakale la zakudyalindi Myuda. Ena amaganiza kuti ndi wa amitundu yemwe wangotembenuka kumene kuchokera ku kupembedzamafano yemwe tsopano ali wosamala kwambiri pa za chakudya chomwe chikuperekedwa ku mafano poyambandipo kenako kugulitsidwa ku misika yakunja. Atha kuganiza kuti chakudyacho chaipitsidwa mwa uzimuchifukwa chinaperekedwa kwa mafano m’mbuyomo. Myudanso angaganize mwa mtundu womwewo.Chikhulupiriro cholimba chingamuthandize munthu ameneyu kuti aone kuti chakudya ndi chakudya ndiponsokuti fano liribe uzimu weniweni. Fano ngakhale mdierekeze wokhala pambuyo pa fanolo alibe mphamvu ya pamunthu wina aliyense kupatula munthu yekhayo amene aopa fanolo m’maganizo mwake. Koma ngati fanoloalilumikiza m’maganizo ake mwa uzimu ndi chakudyacho pamenepo ndiye kuti chakudyacho chirichosayeretsedwa kwa iyeyo.Umodzi 46

Mwa chitsanzo china, mundime 5, munthu wina atenga tsiku lina monga loyera kuposa linzake; winaangotenga masiku onsewo monga chimodzimodzi. Kusunga tsiku loyamba la Sabata monga “tsiku la Ambuye”pokumbukira kuukanso kwa Khristu sinkhani yomwe iri mumtima ayi. Tsiku limeneli linalandiridwa ndiAkhristu onse oyamba aja ngakhale anali ndi maganizo osiyanasiyana pa za masiku enawo. Pano Pauloakunena za masiku achipembedzo a padera, a munthawi za Chipangano Chakale ndi malamulo ake aChiyuda:masabata kapena masiku opumula Mulungu uliwonse, kulemekeza “kutuluka kwa mwezi uliwonse”, ndimiyambo yina yachipembedzo yochitika chaka ndi chaka mwa chitsanzo paska, Pentekoste, kumasulidwa ndizina zoteroChikhulupiriro cha uthenga wabwino chidawamasula Akhristu, kaya Ayuda, kaya amitundu ku kudalira pazinthu zimenezi (Akolose 2:13-17), koma ngati china chinali cholinga cha Mulungu, nkobvuta kuti tichisiyendikuyamba choonadi chinanso chatsopano. Choncho tiri ndi Akhristu ena mumpingo wa ku Roma omweakudya nyama pamene ena sadya; ena akusungabe mwambo wakale cha Chiyuda wosunga ndi kulemekezamasiku ena pamene ena satero ayi.M’masiku ano tiribe bvuto limeneli kwenikweni mumpingo koma tiri ndi mabvuto ena olekana maganizo pankhani zina “zazing’onozing’ono”. Pali nkhani za khalidwe labwino, lobvomerezeka: Kodi kubvala kwabwinondikuti? Kodi amuna ndi akazi asambe malo amodzi kunyanja? Kodi Mkhristu abvine dansi? Kodi ndi zithunziziti zomwe Mkhristu sayenera kuona? Kodi nyimbo zonse za magatala ndi zachabe? Kodi Mkhristu achite ndifodya? Kodi kungolawa pang’ono ndi kwachabe, popeza munthu saledzera nako? Kodi pa nthawi yochezeranamwamuna ndi mkazi, khalidwe lobvomerezeka ndi liti?Palinso Mafunso ena a chipembezo ndi ntchito za mpingo, zomwe zina za izo zitsatidwa ndi kuchitidwa ndimaganizo osiyana pakati pathu mobwerezabwereza: Kodi tikhale ndi mgonero wa Ambuye kangati? Koditiyenera kukhala ndi kalasi mumpingo? Kodi tikhale ndi zikho zingati zomwera chipatso cha mpesa munthawiya mgonero? Kodi nyimbo zoimbira ndi zida ndi zobvomerezeka m'chipembedzo? Kodi mwamuna ameneanalekana ndi mkazi wake mwa malemba angathe kukhala woyang’anira/mbusa? Kodi nchoyenera kuikaatumiki achikazi? Kodi mipingo ingathe kugwirizana kudzera mu utsogoleri wa mpingo womwe wayambitsantchitoyo pa ntchito zina zazikulu? Kodi ndi chobvomerezeka kuomba m’manja mumpingo? Kodi zisudzozimaloledwa mumpingo? Komanso pali Mafunso ena a ziphunzitso ndi zikhulupiriro: Kodi Khristu adzabwerapatapita zaka chikwi kapena pasanapite zaka chikwi? Kodi mphatso za zozizwitsa zikuchitikabe mumpingolero? Kodi zimatheka kuti Mkhristu agwe kuchoka m’manja mwa Khristu ndi kutayika?Pamene Akhristu asiyana maganizo “pankhani zazing’ono,” machimo awiri amayenera kufika: mbale wolimbayemwe mwa chikhulupiriro chake amadya nyama anganyoze mbale wofooka yemwe chikumbumtima chakechimletsa; ndipo mbale wofookayo angadzudzule mbale yemwe ali ndi ufulu uja. Paulo akuletsa zonsezi.Munthu yemwe adya zonseyo asanyoze (NASB): tiganizirane mosanyozana; RSV: osanyoza) iye amene sadya;ndipo munthu amene sadya chirichonse asadzudzule (NASB: asaweruze; RSV: asaike chiweruzo pa) munthuyemwe amadya. Chifukwa chiyani? Popeza Mulungu amulandira iye. Mulungu angalandire munthu yemwekwa ine aoneka monga wolakwa.Munthu yemwe ali ndi chikumbumtima cha choonadi, yemwe adziwe zambiri za chikhulupiriro, nthawi zonseamakhala pa mayeso odzitukumula podziona ngati wapamwamba kuposa wina yemwe sanadziwe kwambiriuja, pomutenga ngati wosafunikira kwa Mulungu ndi mpingo. Chidziwitso chimatukumula, koma chikondichimamangirira. Munthu yemwe aganiza kuti adziwe zambiri alinakonso kuperewera kwina” – 1 Akorinto 8:1-2. Kudzitukumula ndi dzenje la anthu omwe amaganiza kuti iwo ndiye odziwa kuposa ena onse. Munthuwomangidwa ndi chikumbumtima uja, ngakhale kuti kwenikweni zimachitika chifukwa cha kusakhwima muuzimu, nayenso amakhala pa mayeso oganiza kuti mbale wake wokhala ndi ufulu uja, ngati wosasamaliramalamulo a Mulungu ndi kumudzudzula. Kumakhala kobvuta kwa iye kuti azindikire “nkhani zazing’ono”monga momwe ziriri ndi kusiyira zina zonsezo kuti Mulungu ndiye aweruze pamene iye apitiriza kutumikiraMulungu.Bvuto la maganizo a mbale wolimbayo lingathe kuononga ubale ndi kubvulaza umodzi wampingo. Kudzudzulakomwe mbale wofooka uja amachita mwa chisawawa kwa ena kungathenso kuononga ubale ndi umodzi. Ngatimmodzi wa onsewa achita zimenezi mpaka kufika poti pakhale kulekana ndi kugawikana, Paulo akulamuliraAkhristu kuti tisamale naye ndi kupatuka pa iye. Munthu woteroyo angodzisangalatsa ndi zomkondweretsa iyemwini (kukakamira kufuna kutchedwa wochita bwino mwa yekha kapena chakudya, kapena kuchitamwangwiro). Iyeyo sakutumikira Khristu – Aroma 16:17,18.Umodzi 47

Bvuto la maganizo a mbale wolimbayo lingathe kuononga ubale ndi kubvulaza umodz wampingo. Kudzudzulakomwe mbale wofooka uja amachita mwa chisawawa kwa ena kungathenso kuononga ubale ndi umodzi. Ngatimmodzi wa onsewa achita zimenezi mpaka kufika poti pakhale kulekana ndi kugawikana, Paulo akulamuliraAkhristu kuti tisamale naye ndi kupatuka pa iye. Munthu woteroyo angodzisangalatsa ndi zomkondweretsa iyemwini (kukakamira kufuna kutchedwa wochita bwino mwa yekha kapena chakudya, kapena kuchitamwangwiro). Iyeyo sakutumikira Khristu – Aroma 16:17,18.Ndi kulakwa kuti mbale aliyense aweruze mbale wake (kumtsutsa kapena kumtenga ngati wopanda pake). Kodindiwe yani woti ukaweruze wantchito wa mwini wake? Mbale aliyense amayang’aniridwa ndi kuyankha zonsekwa Mulungu poyambirira. Sindiyenera kutenga udindo wa Mulungu wakuweruza. Munthu amaima kapenakugwa kwa Ambuye wake (yemwe ndi Mulungu). Ndipo adzatha kuimanso, chifukwa Ambuye angathekumthandizanso kuti aime, ngakhale atakhala ndi zomwe zioneka ngati zolakwika, malingana ndi zomwe inendiganiza ndi kukhulupirira pa nkhani zina zazing’ono.Paulo atipatsa mitu itatu yoti ititsogolere pa khalidwe lathu mu ndime imeneyi:1. Aliyense akhale wokhutitsidwa mumtima mwake (v5c). Aliyense wa ife ali ndi udindo womvetsa ndikuganizira mosamala kwambiri chomwe akukhulupirira kuti ndicho cholinga ndi chifuniro cha Mulungu pankhani kapena mfundo iriyonse. Ngakhale sitingathe kumva mvemvemve monga amachitira Mulungu,tiyenera kukhala ndi njala ya kumva malembo monga momwe tingathere. Tiri ndi udindo wophunzitsachikumbumtima chathu. Ife sitiri oweruza maganizo a wina aliyense ayi.2. Ngati wina aliyense aona chinthu china monga chodetsedwa (choipa) ….. kwa iyeyo ndi chodetsedwa ……munthu yemwe akaika achimwa ngati adya, chifukwa sadya ndi chikhulupiriro (vv. 14b,23). Ngatindilakalaka kuchita chinthu chomwe ndi kuchikaikira kapena kukhulupirira kuti ndi choipa, ndiye kuti ndirindi mzimu wa wochimwa wa chilakolako ngakhale kuti Mulungu saletsa chinthu chomwe ndikuchitacho.Ndiyenera kumalolera maganizo a ena pa nkhani ndi mfundo zazing’ono, koma ndiyenera kumveramosamalitsa chomwe chikumbumtima changa chindiuza kuti ndi chobvomerezeka.3. Ganizirani kuti musaike chopunthwitsa kapena cholepheretsa chirichonse m’njira ya mbale wanu.Malingana ndi kukhwima kwa chikumbumtima chanu, chingathe kukulolani kuchita zinthu zina zomwe enaamaziona ngati zoipa ndi zolakwika, komabe musamangochita zimenezi nthawi iriyonse kapena pamalopena paliponse pomwe zingabvutitse ndi kuyambitsa mabvuto kwa mbale kapena mlongo wanu.Iye yemwe aona tsiku limodzi ngati lofunika kuposa linzake, atero kwa Ambuye. Iye yemwe adya nyama kwaAmbuye, chifukwa ayamikira Mulungu, ndipo iye yemwe sadya, atero kwa Mulungu. Ndi chinthu chofunikakudziwa ndi kuchita chifuniro cha Mulungu molondola monga momwe tingathere, koma koposa zonse, ndikofunikira kuchita zonse zomwe timachita ndi cholinga cholemekeza Mulungu. Ngakhale sitimvetsabwinobwino, Mulungu amazindikira cholinga chathu chofuna kumulemekeza ndi kumumvera. Kaya moyokaya imfa, ife ndife ake a Ambuye. Ife tiri m’manja ake mu zonse, pa zonse ndipo timayankha china chirichonse kwa iye, tiri pansi pa ulamuliro wake m’zonse, koposa wina aliyenseyo, ndipo tiyenera kuchita chinachirichonse chomwe tingathe kuti timkondweretse.Uweruziranji mbale wako ….. upepusiranji mbale wako? Popeza tonse tidzaima pampando wachiweruzo waMulungu. Ngati ndiweruza mbale wanga yemwe “ali womasuka” kusiyana ndi ine munkhani zazing’ono, ndiyekuti ndi kutenga malo ndi udindo wa Mulungu wakuweruza. Ngati ndinyoza ndi kupepusa mbale wangawomangiririka ku chikumbumtima chake, chimodzimodzinso ndiye kuti ine ndi kudzikweza koposa iyeyo,chinthu chomwe ndi Mulungu yekha angathe kuchichita mwa mphamvu yake. Podziwa kuti tonsefe tidzaimapampando wachifumu ndi kunena ntchito zathu zonse kwa Mulungu tiyenera kukhala odzichepetsa pochita ndianzathu pamene pabuka kusamvana. “Musaweruze pakuti inunso mungaweruzidwe. Popeza m’njira yomweyomuweruzira ena, inunso mudzaweruzidwa nayo.” – Mateyu 7:1,2. “Choncho aliyense wa ife adzafotokozayekha ntchito zake kwa Mulungu. Choncho ziripotu zinthu zina zomwe ndiribe ufulu woweruza. Ndithakungozisiyira pakati pa Akhristu anzanga ndi Mulungu.Izitu sizitanthauza kuti sitiyenera kuweruza pa chirichonse chabwino kapena choipa. Mu Aroma 14, Paulosakunena za zinthu zazikulu, zodziwikiratu za zabwino ndi zoipa, koma iye akunena za zinthu zazing’onozomwe tiri nawo mpata wokambirana. Akhristu pamodzi ndi atsogoleri, nthawi zina amapatsidwa mwayiUmodzi 48

woweruza zina zazing’ono – 1 Yohane 4:1-3; 1 Akorinto 5; Mateyu 18:15-20; Machitidwe 17:11. Tiyenerakukhala ndi luntha pamodzi ndi nzeru zotithandiza kusiyanitsa mfundo zazikulu zosayenera kusewera nazomwa uzimu ndi mfundo zazing’ono zomwe tingathe kuweruza. Kufooka kwathu pa mfundo imeneyi ndikokuwalowetsa “libolonje” m’mbiri ya mpingo.14:13-23: Choncho (popeza tonse tidzaweruzidwa ndi Mulungu), tiyeni tisiye kumaweruzana (kaya ndi mbalewamphamvu kunyoza mbale wofooka, kapena wofooka kudzudzula ndi kuweruza wamphamvu ndiwolimbayo) m’malo mwake sankhani kusaika chopunthwitsa kapena chokhumudwitsa, m’njira ya mbale wako.Ngati ine mwa ufulu wanga, ndichita chomwe chioneka cholakwika ndi chosabvomerezeka kwa wofooka uja,ndiye kuti ndingamupunthwitse munjira ziwiri:1). Ndimupangitsa kuti kukhale kobvuta kwa iye kuti iye ndi ine tikhale “amodzi” – angathenso kusiyakusonkhana ndi kupembedza;2). Ndimupangitsa kupitiriza kuchita zomwe inenso ndi chitazo ngakhale zioneka zolakwika kwa iyeyo ndipopotero adzaswa maganizo a chikumbumtima chake pochita zimenezi. 1 Akorinto 8:1-13 ndi 10:23-33 ndiwomaziko a chaputala chimenechi omwe ayenera kuwerengedwa ndi mavesi omwe alembedwawo. Inendikhulupirira kuti palibe chakudya chomwe ndi chodetsedwa mwa chokha. Koma ngati wina aona chinthuchina ngati chodetsedwa, ndiye kuti chinthucho ndi choipa kwa iyeyo ndipo zidzakhala chomwecho mpakapomwe chikumbumtima chake chidzamasuke chifukwa cha kukula mu chikhulupiriro. Taonani vesi 23 ndipomufanizire. Munthu yemwe akaikira aweruzidwa ngati adya, chifukwa sadya ndi chikhulupiriro; ndipo chinachirichonse chomwe sichichokera ku chikhulupiriro chiri tchimo.Chikondi chenicheni sichikondwera kubvutitsa anthu ena. Ngati mbale wako akhumudwa ndi chomwe iweukudya, ndiye kuti iwe suchita mwa chikondi. Chakudya chanu (kaya china chirichonse) pamenepa ndiye kutichafika pa ndime yofunikira koposa mtendere wa mbale kapena mlongo wanu komanso ndi ubale wanu.Khristu anafa, anapereka moyo wake, kupulumutsa mbale wanuyo. Simaganizo abwino ngati simudzalolerakusiya nyama ya nkhumba (kaya china chirichonse) ndi cholinga chofuna kupewa kumutengera kukuonongeka.Taonaninso ndime 20: Musaononge ntchito ya Mulungu (Mzimu wa mbale wanu ndi ntchito yonse yomweMulungu anachita kuti aipulumutse) chifukwa cha chakudya.Musalole kuti chomwe muchiona ngati chabwino anthu anene kuti ndi choipa. Paulo sakunena kuti “musalolembale wanu wofooka kukuletsani chomwe chikumbumtima chanu chikulolani kuchita.” Koma akunena kutichomwe muchiona ngati choyenera ndi chabwino chingathe kukhala chodetsedwa ngati muchigwiritsa ntchitoyoti muvulaze moyo wa uzimu wa mbale wanuyo. Ngati khalidwe lanu limadalira kapena lilingana ndi ufumuwakumwamba, chiyero, ufulu, chimwemwe ndi zokhazo zomwe mudzakhala mukuganizira kwambiri, osatikaya mudya kaya mumwa chomwe mumakonda, kaya kubvala chirichonse, kaya kupita kuzikondwerero zina.Ngati tiika chiyero, ufulu, chimwemwe ndi mtendere wa abale anthu ndi alongo athu patsogolo koposa zonsezodzikondweretsa tokha, ndiye kuti tikukondweretsa Mulungu ndipo tiri kubvomerezedwa ndi anthu.Choncho tiyeni tiyesetse kulimbika ndithu kuchita chirichonse chomwe chikapherezere ku mtendere ndi kukulakoyenera. Ngati ichi chitanthauza kusiya zinthu zina zomwe ziri zobvomerezeka nane koma zokhumudwitsakwa mbale wanga wofookayo, zikhale chomwecho. Chakudya chonse ndi choyeretsedwa, koma sibwino kutimunthu adye china chirichonse chomwe chingapunthwitse winayo.Chirichonse chomwe mukhulupirira zinthu zimenezi (zakudya, masiku ndi zina zotero) zikhale pakati pa inueni ndi Mulungu wanu. Paulo sakutanthauza kuti nkosayenera kukambirana za zimenezi ndi mzimu wabwinopakati panu ndi iwo omwe tisiyana nawo maganizo, kapena kuphunzira nawo pamodzi ndi cholinga chofunakuchepetsako kusamvanako. Iye akutanthauza kuti kaya maganizo anga “ndi omasuka” kaya omangika,sindiyenera kumangoumirira pa maganizo anga omwewo ndi kulimbikitsa makangano. Maganizo athuasadzadze ndi moyo wongofuna kulimbana pa mfundo zazing’ono koma adzadze ndi mfundo zazikulu ndizofunikira za Khristu. Paulo afuna kuti tonse tigwirire ntchito pamodzi ngakhale timasiyana m’maganizo ndimfundo zazing’ono ndikuti tisiyire kuweruza komaliza pa mfundo zazing’ono kwa Mulungu mwini.15:1-3: kumbukirani kuti panalibe kulekanitsa machaputala ndi mavesi pamene Paulo anali kulemba kalataimeneyi. Iye akupitirizabe kufotokozera maganizo ake pa bvuto limodzi lomweli mu chaputala 15. Ndipo ifeamene tiri olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu ndi kusadzikondweretsa tokha - podyakapena kuchita chirichonse chomwe chitikondweretsa. Ndi zoona kuti mbale wofooka womangidwa ndiUmodzi 49

chikumbumtima akulamulidwa kuti akhale wololera anzake ndi wosaweruza chimodzimodzi mbale wakewamphamvu uja ndi wosamangika uja yemwe alamulidwanso kuti ataye ufulu wake chifukwa cha mbale wakewofooka uja. Koma popeza mbale wolimbayo ndiye ali nazo mphamvu, ntchito yaikulu yosunga ndi kusamaliramtendere ndi kupewa kulakwa iri kwa iyeyo. Thupi lathu lakale la uchimo lodzikonda silifuna kunyamulantchito imeneyi. Iyi ndi ntchito yotheka kwa munthu watsopano wopulumutsidwa. Munthu wakale uja ayenerakupachikidwa ndi Yesu.Yesu anati, “ngati wina afuna kunditsata ine, iye ayenera kudzikana yekha ndi kunyamula mtanda wake tsikundi tsiku ndi kunditsata ine. Pakuti aliyense wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya, koma yense wotayamoyo wake chifukwa cha ine adzaupeza – Luka 9:23-24. Mtanda uyimirira moyo wobvuta ndi wopweteka kwaife koma wobweza ndi kupulumutsa ena. Moyo wathu wakale umafuna kudzikondweretsa okha, osatikukondweretsa enawo mwa kutaya ufulu wathu. Ichitu ndi chifukwa chake “kudzikana” liri monga gawoloyamba pa ulendowu monganso anamchitira Yesu. Aliyense wa ife akondweretse mbale wake kutizimuyendere bwino, kuti amlimbikitse akule bwino.Paulo anasiya ufulu wake wolandira thandizo lochokera kwa abale ampingo wa ku Korinto ndi cholinga chotintchito yofalitsa uthenga ikhale ndi mphamvu – 1 Akorinto 9:12. Iye anangokhala “chirichonse kwa anthuamitundu ulionse,” kusiya zina zomwe iye anali kudzikonda koposa mu nkhani za miyambo yake ndichipembedzo kuti akathe kugwirizana bwino ndi gulu liri lonse lomwe iye akapezeke akugwirako ntchito yaMulungu – 1 Akorinto 9:19-23. Kuchotsa zizolowezi za miyambo yamakolo ake zomwe zikanakhozakulepheretsa uthenga kufika kwa anthu kunali kofunikira kwambiri kwa iye koposa kungochita zomsangalatsaiye kumbali yake. Paulo anali wokonzeka “kuononga chirichonse chomwe anali nacho ngakhale kudziperekaiye mwini kuphatikizaponso Akorinto aja mu uzimu – 2 Akorinto 12:15. Iye sanachite zimenezi chifukwazimamukondweretsa iye mwini, koma chifukwa anasamalira kwambiri za chipulumutso cha ena koposa zinthuzina zodzikondweretsa nazo yekha mwini.Paulo anafotokoza zikhulupiriro zake mu 1 Akorinto 10:31-33:1 “Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitanizonse kuulemerero wa Mulungu”2 “Musachimwitse wina aliyense, kaya ndi Myuda, Mhelene kapena mpingo wa Mulungu.”3 “Ndimayeserera kukondweretsa aliyense m’zonse, chifukwa sindifuna kuti wopindula ndikhale ine komaunyinjiwo, kuti apulumutsidwe. Ndiponso anati, “mutengere chitsanzo changa monganso ine nditsanziraKhristu.” 11:1.Popeza ngakhale Yesu sanadzikondweretsa yekha. Iye sanasiye malo ake abwino ndi ufulu wokhalam’ulemerero wakumwamba chifukwa pansipano panali pomkomera, koma chifukwa chakuti Iye analiwamphamvu ife tinali ofooka, ndipo sitikanatha kudzithandiza tokha. Khristu anali “Mulungu m’zonse,” koma“anadzichepetsa kotheratu nakhala wapansipansi” (RSV: “anadzikhuthula yekha”) – Afilipi 2:5-8. Iye anakhalakapolo wathu, potiganizira ife, osati yekha. (Ndi chifukwa chake timsirira koposa) Iye anatinyamulira machimoathu ndi zolemetsa zathu. Ndipo mfundo yaikulu ya ife Akhristu m'moyo ndi makhalidwe athu ikhale yofunakufanana ndi Khristu munjira zomwe tichitira ndi anthu onse.15:4-7: Pakuti zonse zomwe zinalembedwa kale, zinalembedwa ndi cholinga choti ife tiphunzire. PamenepaPaulo anangotenga malembo amenewa kuchokera mu Chipangano Chakale. Ife Akhristu sitiri omangidwa ndilamulo la m’Chipangano Chakale, koma malembo a m’Chipangano Chakale ali odzala ndi umulungu ndimfundo zake. Ife timaphunzira zambiri za Mulungu ndi makhalidwe ake kuchokera mu malemba amenewa.Ndipo kuti tithe kumvetsa bwino Chipangano Chatsopano tiyenera kukumba kuchokera ku maziko aChipangano Chakale.Mulungu yemwe amapereka chipiriro ndi chilimbikitso (zofunika ziwiri pa umodzi wa abale) akupatseni inuMzimu wa umodzi pakati panu pamene muli kutsata Yesu Khristu. Umodzi ndi chinthu cha uzimu mongansocha chikhulupiriro. Mzimu wa umodzi ndi wofunikira monga kufunikiranso kwa kugwirizana pa zikhulupiriroza mfundo zazikulu zikulu.Umodzi 50

Anthu atha kumabvomerezana pa zikhulupiriro ndi ziphunzitso komabe kumapezeka osiyana maganizom'zambiri chifukwa cha mtima wa makani ndi wodzitukumula. Malekano ambiri omwe anthu amati amayambachifukwa cha kusamvetsa bwino ziphunzitso ndi zikhulupiriro, ponena zoona amayambira pa uzimuwodzikondweretsa makani ndi kulimbanira kupambana – “ndikhale wamkulu.” Nkhani ya ziphunzitso ndizikhulupiriro imangopangitsa kuti kulekanako kukhale ngati ndi kwabwino. Pakanakhala kuti panali chikondindi kudzichepetsa kwa mzimu, ndiye kuti abale akanatha kupeza njira yothetsera bvuto la kukhala ndiziphunztso ndi zikhulupiriro zosiyana yomwe ikanatha kuwathandiza kugwirira ntchito pamodzi.Theka lamachimo omwe asanjidwa “m’ntchito za thupi” – Agalatiya 5:19-21 – nthawi zonse zimapezekam'kugawanika kwa mpingo. Kumbali inayi, “chipatso cha Mzimu ‘Woyera” – Agalatiya 5:22-23) ndichochenicheni chomwe chimapangitsa kuti abale ndi alongo athe kugwirira ntchito pamodzi ngakhale ali nazozofooka zawo aliyense payekha.Mwa chidziwikirenso, choncho, umodzi mumpingo umadalira kwambiri pa “kufa kwa munthu wakale wauchimo, kubadwanso mwa uzimu, moyo watsopano monga momwe zimakhalira ndi momwe timveraziphunzitso ndi zikhulupiriro. “Mu chaputala chonena za umodzi” cholembedwa ndi Paulo Aefeso 4, Paulowatenga nthawi m'mavesi atatu oyamba pofotokoza za mmodzi wa uzimu, ndipo mavesi ena atatu otsatiranawoPaulo wafotokozera za ziphunzitso ndi zikhulupiriro.Kuti ndi mtima umodzi ndi mawu amodzi mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.Izi sizitanthauza kumangobvomerezana pa mfundo zirizonse zazing’ono; zitanthauza kukhala ‘amodzi’ mwaYesu ngakhale pakhale kusiyanako. Milomo yathu iyankhule mosasintha pa zinthu zazikulu zosayenerakusinthidwa zofunikira. Timalemekeza ndi kutumikira Ambuye mmodzi yemweyo.Choncho mulandirane wina ndi mnzake, monganso momwe Khristu analandira inu. Kodi Khristuanakulandirani inu pokha pamene munaona ndi kubvomereza za choonadi chake chonse? Ngati kudali tero,bwenzi pakali pano mu kudikirabe kuti mulandiridwe. Ayi iye anatifera ife pamene tinali ochimwabe ndipoanatilandira ife ku thupi lake pamene tinali tiri makanda pa momwe tinali kumvetsera malemba ndikudzipereka kwathu. Ngati anatilandira mwa chisomo pamene tinali ochimwa kopambana, ifenso tiyenerakulandira abale ndi alongo athu omwe ali osachita mwangwiro.Ndi cholinga chofuna kuti Mulungu atamandidwe. Pamene Akhristu achitana mwa chisomo, Mulunguadzatamandidwa chifukwa cha magwero a chisomocho pamene dziko liona momwe Akhristu akondaniranangakhale pamakhala kupunthwa ndi kulephera, dziko lidzadziwa kuti pali china chake choona ndi chamtengowapatali chomwe chikuchitika mumpingo. Pali munthu wina yemwe anadzacheza pa msonkhano wampingo laMulungu anati, “Ine ndi kuona ndinso kumva mumtima mwanga kuti kuno kuli mtendere ndi chikondi.”15:8-13: Khristu wakhala kapolo wa Ayuda – Anabwera monga Myuda natumikira pakati pa Ayuda – m’malomwa choonadi cha Mulungu = kuti abweretse uthenga wa chipulumutso ku dziko lonse ndi kutionetsa ife Atate– kukwaniritsa malonjezano operekedwa kwa makolo oyamba a m’Chipangano chakale kuti mafuko onseadziko lapansi adzadalitsidwa kudzera mwa obadwa wochokera mwa iwo – Genesis 12:1-3 – kuti amitunduakalemekeze Mulungu chifukwa cha chifundo chake.Asanabwere Khristu, Israyeli yekha ndiye anali ndi phangano ndi Mulungu. Amitundu analibe gawo opandachiyembekezo – Aefeso 2:11,12. Koma Khristu anafera anthu onse natumiza uthenga wake kwa amitundu ndiAyuda omwe. Paulo anagwiritsa ntchito malemba anayi a m’Chipangano Chakale omwe anali kulosera zachifundo cha Mulungu chomwe analandira nacho amitundu.Kunakhala kobvuta kwambiri kubweretsa ndi kusunga umodzi pamene mpingo wapangidwa ndi anthuochokera ku zikhulupiriro ziwiri zosiyana za miyambo ya makolo, zipembedzo, chikhalidwe, mitundu kapenakapezedwe kachuma. Nkhani zambiri zazing’ono mumpingo woyamba uja zinalimonso, ndipo izi zinalichomwecho chifukwa kusiyana kwa zikhulupiriro ndi ziphunzitso kuja kumawatengera ku Mafunsoochokeranso ku zikhulupiriro zosiyana. Izi zimaoneka kwambiri makamaka pakati pa Ayuda ndi amitunduomwe anayamba kukhulupirira aja, monga afotokozera mu Aroma 14. Pa kuphunzitsa kwake, Paulo analimbikakufotokoza cholinga cha Mulungu pa Ayuda ndi amitundu kuti akhale ogwirizana napanga munthu mmodziwatsopano mwa Khristu. Anthu okhulupirika akukumanabe ndi mabvuto mumpingo amenewa lero, mabvutoUmodzi 51

amenewa olephera kuona zinthu mofanana chifukwa chakusiyana m’chikhalidwe, miyambo, zaka, maphunziro,ndi zina zambiri.Pali chinthu chimodzi chomwenso tiyenera kuchiona: Paulo akutitsimikizira ndi chiphunzitso choti pa mbalendi mbale, tiyenera tidzikhala okonzeka kusiya zathu zina monga nyama pa nthawi yomwe tikuona kutitingapunthwitse mbale wina yemwe ali womangidwa ndi chikumbumtima chake. Nthawi zambirinso takhalatikuganiza kuti tiyenera kusiya mchitidwe kapena njira ya kapembezedwe mumpingo kapena ntchito ina yamumpingo yomwe ikhumudwitsa mtima wa mbale aliyense mumpingo kuti mwina tingapangitse kuti winaachimwe.Izi zimachitika chifukwa cha chikondi cha kwa anthu chilakolako choonadi chofuna kupewa kulakwiranakapena kupatukana. Chikondi chidzayesetsa kupewa kukhumudwitsa monga momwe chingathere. Komatutiyenera kusamalira kwambiri pogwiritsa ntchito mfundo za Paulozi pa nkhani za pa mpingo; sizikhalazosabvuta monga momwe zikhalira pakati pa aliyense payekha, m'modzimodzi.Mwa chitsanzo, ngati mpingo ukuganizira za ntchito yofalitsa uthenga ndi kutembenuza mizimu 50, ndipopafupifupi mpingo wonse ukukhulupirira kuti ntchitoyo ikugwirizana ndi malemba ndipo ndi yokhoza, kodimpingo usiye kugwira ntchitoyi chifukwa m’[bale mmodzi kapena akukhulupirira kuti ntchitoyi ikulakwiramawu a Mulungu? Kodi nkwabwino kupunthwitsa osakhulupirira 50 (kuwalepheretsa kulandira ndikukhulupirira uthenga wabwino) ndi cholinga chofuna kupewa kukhumudwitsa mmodzi kapena awirimumpingo? Kodi ndi chifuniro cha Mulungu kuti chikumbumtima chofunikira cha abale ofookam’chikhulupiriro chidzingololedwa kulamulira njira zomwe mpingo udzigwirira ntchito zake? Kodi kusiyantchito yofunikira kwambiri mumpingo kukhala kosabvuta monga momwe zikhalira ndi kusiya kudya nyama?Ngati mu Aroma 14 timaphunzira kuti mbale wolimba asachite china chirichonse chomwe chingapunthwitsembale wofooka, kodi pameneponso sakuphunzitsa mwa chimvekere kuti mbale wofookayoasaweruze/asadzudzule iwo omwe chikumbumtima chawo chiwapatsa ufulu? Kodi kupembeza pa mpingokutanthauza kuti tibvomereze zonse zomwe mpingowo umachita? Kodi Aroma 14 sitiphunzira kuti tingathekugwira ntchito ndi mpingo, koma pewani kuchita nokha chirichonse chomwe chikumbumtima chanuchikutsutsani, ndipo siyirani kuweruza pa zinthu zina kwa Mulungu?Nkhani zina zazing’ono zimakhudza zochitika pa kupemphera mwangwirizano. Chikumbumtima cha winasichimlola kukhala nawo pa chipembedzo chosonkhana m'nyumba imodzi monga zikhalira masiku ano.Pamenepa munthuyu angathe kuchoka pa mpingo umodzi ndi kukayamba kusonkhana kumpingo wina komwemapembezedwe ali obvomerezedwa ndi chikumbumtima chake. Komabe ngakhale ziri chomwechi, mipingoiwiri ija itha kutsatira moyo wololerana wa mu Aroma 14 pakati pawo, kugwirizana mu zinthu zomwe afananam’maganizo ndi kusiyira zina zonsezo kwa Mulungu kuti aweruze. Mipingo isatayenso Chiyanjano chawochifukwa cha nkhani zazing’ono zoti angasankhe kukambirana kapena kungosiyira Mulungu kuti aweruzekoposa Mkhristu payekha payekha/m'modzimodzi.Mafunso Othandiza Pokambirana:1. Kodi malemba amaphunzitsa zotani pakulimbana kosatha chifukwa cha nkhani zazing’ono zachipembedzo? 2 Timoteo 2:14; Tito 3:9-12.2. Tchulani zina za zitsanzo za masiku ano za “nkhani zazing’ono” zokhudza khalidwe la Mkhristu? Ntchitoya mpingo ndi mapembedzedwe?3. Kodi tidzalolera motani ngati wina apempha kumasonkhana nafe komanso nafuna kulemekeza Sabata(Loweruka) pa iye yekha, kwinaku namasunga ndi kulemekeza tsiku la Ambuye Lamulungu, mongansokunalili ndi Aroma aja?4. Taganizirani mfundo, nkhani kapena chinthu china chirichonse chomwe abale anu a Chikhristuamakhulupirira kuti ndi chobvomerezeka koma inu mumachikaikira?5. Taganiziraninso china chirichonse chomwe mukhulupirira koma ena a Akhristu anzanu amakhulupirira kutindi cholakwika?Umodzi 52

6. Kodi ndi chifukwa chiyani nthawi zambiri kumakhala kobvuta kwa basi kwa munthu yemwe amaumirirazimene anazidziwa zokhazo, wokhala womangiririka pa chikumbumtima chake kuona nkhani yaing’onoyoti mutha kukambirana ndi kusankha maganizo amodzi, ngati yoyenera kutero?7. Nanga ndi zinthu ziti zomwe mumaziika pa mndandanda wanu wa zenizeni zomwe mumakhulupirira paChikhristu chanu, zomwe kaya zitani simungalole kuzisintha mokambirana? Kodi ndi ziphunzitso ndizikhulupiriro ziti zomwe tiyenera kugwirizana nazo pasanakhale umodzi? Kodi kapena nkhani yake ndiyomwe iri pa Aefeso 4:4-6.8. Kodi nthawi zina timatenga nkhani zazing’ono kukhala zofunikira koposa “Chiyero,” mtendere, ndichimwemwe mwa Mzimu Woyera?” Nanga tingapewe bwanji moyo umenewu?9. Nanga tingachite chiyani kuti zitheke kumvera chiphunzitso cha Paulo chakulolerana mu Aroma 14 ndipopanthawi yomweyo kusamalira ndi kusunga mzimu womvera malangizo onse a Mulungu aang’ono ndiaakulu omwe? Kodi kungatheke kukhala wosalolera kusiya zomwe ukhulupirira iwe mwa wekha ndikukhala wololera za ena panthawi imodzi?10. Ndi chiyani chomwe munayamba mwa chisiyapo m’nthawi ina yake pofuna kupewa kulakwira maganizo awina?11. Kodi zimatheka kukhala kumbali yolondola “pankhani yomwe pali maganizo awiri” komabe ndi kukhalawoweruzidwa ndi Mulungu chifukwa akuonetsa kugawanitsa malinga ndi njira yomwe akutengerankhaniyo?12. Nchifukwa chiyani umodzi uli wofunika? Yohane 17:20,21; 13:35.MBALI ZOBVUTA POTANTHAUZIRA MALEMBAMawu oyamba: Matanthauzidwe a gulu lija lakubwezeretsa:1) Ponena za chikhulupiriro ndi machitidwe athu onse, malembo ndiwo atitsogolera ndi kutilamulira.2) Baibulo limalamulira popereka lamulo pomwepo, chitsanzo chobvomerezeka ndi maganizooyenera.3) Pamene Baibulo linena, ifenso timanena ndipo pamene Baibulo likhala chete ifenso tikhala chete.Ndi kukhulupirira kuti maganizo onsewa ndi omveka ndi obvomerezeka ndiponso kuti tonse tingathekugwirizana nawo. Komatu Sali osabvuta kuwagwiritsa ntchito m’machitidwe athu. Tamvani ndemanga yakatwiri wina wotchedwa Dr. Bill Humble:Nkosabvuta kungonena mfundo ya gulu lobwezeretsa lija yoti – mpingo uliwonse mumbadwouliwonse ukhale pafupifupi wofanana ndi mpingo wa m’Chipangano Chatsopano. Ndi chinthuchobvuta kuti tizindikire ndi kuganizira zomwe Chipangano Chatsopano chifuna mu nthawi iriyonse pa yokha. Mpingo uyenera kumafunsa, kodi ndi ziti zomwe ziri zoyenereka kutsatidwamalinga ndi dongosolo la Chipangano Chatsopano? Nanga ndi ziti zomwe tingazichotse popezazinangokhala monga gawo la chikhalidwe ndi miyambo ya nthawi zakale ndipo kuti ndizosamangiririka ku mpingo mu m’badwo uliwonse? Iri ndi bvuto lokhudzana ndikatanthauziridwe ka Baibulo ….. bvuto la njira ya kamasuliridwe ka malemba ndipo mayankhoake sakhala okhweka nthawi zonse.Ntchito yobwezeretsa inagawanikana chifukwa chabvuto lakamasuliridwe kamalembo. Phunziroli likhalalikuunika Madera a ena a mabvuto amenewa.1. Kodi kukhala chete kwa malemba kumatiletsa kapena kumatiloleza?A. Mu nthawi zakusintha ndi kukonzanso zinthu zija Martin Luther anakhulupirira kuti chirichonseUmodzi 53

chomwe sichinaletsedwa mwatchutchutchu m’malemba chiri chololedwa, pamene Ulrich Zwinglianakhulupirira kuti chirichonse chomwe sichilamulidwa mwatchutchutchu nchosaloledwa. Munthawiyakubwezeretsa, Barton W. Stone anabvomera kunyema ndikumwa pa mgonero pamodzi ndiosabatizidwa mobizidwa chifukwa sanapeza lemba lenileni loletsa zimenezi. Koma AlexanderCampbell anatsutsa zimenezi, ponena kuti panalibe lemba lolamulira machitidwe amenewa Palinsokusiyana kwa maganizo ngati komweku pokhudza za kugwiritsa ntchito zida poyimba nyimbo.B. Zitsanzo za zochita zina zomwe gulu limodzi kapena gawo lina la anthu obwezeretsa aja anatsutsachifukwa sanazipeza m’malemba: amasiye Akhristu, makoleji Achikhristu, mgwirizano wodzera mumpingo umodzi wothandizira, mabungwe a amishinale, zikho zambiri pa mgonero wa Ambuye,thumba la chuma cha mpingo, nyumba za mpingo, mabuku a nyimbo, mgonero wa madzulo(wachiwiri) alembi ampingo, alaliki oyang’anira za achinyamata, alaliki a uthenga wabwino,misonkhano ya achinyamata, anthu oyendetsa ntchito, makalasi ochitidwa m’nthawi zofanana, malaudisipikala, mabukhu ophunzitsira Baibulo, maholo achitira mafeloshipi, ndi zina zotero.C. Ambiri akhulupirira kuti pamene Mulungu afotokoza mwapadera njira yochitira chinthu china, ichichitanthauza kuti pasachitikenso njira za mtundu winanso osakhala umenewu.Zitsanzo:1) Ubatizo wobiza sulola wina monga wotsira madzi pamutu, kapena kungowaza.2) Mnjale, mtengo womwe anapangira chombo cha Nowa osati mkungudza kapena mitengo ina –Genesis 6.3) Moto woyera wokha pa guwa, osati miyoyo ina wamba – Levitiko 10.4) Mkate ndi chipatso cha mpesas pa mgonero wa Ambuye osati chakudya china chirichonse kapenachakumwa.5) Akulu pa mpingo uliwonse osati utsogoleri wamtundu wosiyana ndi umenewu.6) Mapembedzedwe a padera a m’Chipangano Chatsopano osatinso monga ena ali onsewo.Ngati kukhale chete kwa malemba sikutiletsa, ndiye kuti machitidwe ena onse achilendoadzakhalanso obvomerezedwa. Komanso palibe yemwe akhulupirira kuti machitidwe onse omwesitilamulidwa mwapadera kuchita ndi oletsedwa. Ambiri a ife timagwiritsa ntchito timakaputing’onoting’ono tayekha tayekha pa mgonero ngakhale Khristu anagwiritsa ntchito chikho chimodzi.Ambiri timakhulupirira kuti zothandizira zina kuti lamulo lina likwaniritsidwe ngakhale sizinachitekutchulidwa kapena kufotokozedwa m’malemba, zimalamulidwa ndi chilamulo chongoganizira, komapokhapokhapo ngati chachita kuletsedwa mwapadera penapake.Komanso, palibe yemwe amakhulupirira kuti machitidwe alionse omwe sanaletsedwe mwa dongosolondi ololedwa. Mipingo yomwe imangwiritsa ntchito zida mu nyimbo zawo imatsutsa ponena kuti zidazizimaloledwa m’Chipembedzo chifukwa siziletsedwa mwapadera; koma amakana ubatizo wowazamadzi pamutu ngakhale siziletsedwa mwapadera.D. Dr. J.D. Thomas anapereka maganizo oti, “kukhala chete pamene malemba akhale chete” si mfundoyaikulu ayi, koma amagwiritsidwa ntchito m’malo okhawo omwe malemba afuna kuti machitidwekapena m'chitidwewo usachitike. Naye Clinton Lockhart analemba kuti, “kutsimikizira pa choonadikumachotsadi chomwe chikutsutsana nacho basi.2 Kodi ndi zitsanzo ziti zomwe zatimanga lero?A. Pamene tiona atumwi kapena mpingo woyamba uja ukuchita kanthu, mwina uwu ungakhale umboniwa atumwiwo pa lamulo lomwe iwo analamulidwa nalo ngakhale kuti lamulolo silifotokozedwa bwinokwa ife m’malemba. Chitsanzo:Umodzi 54

1) Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu – Machitidwe 5:28,29.2) Woyang’anira wa ndende yaku Filipi anatembenuka nthawi yomweyo – Machitidwe 16:33.3) Paulo anamtumiza Onesimo, kapolo wathawa uja Filimoni mbuye wake.4) Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku iwo omwe anali kupulumutsidwa – Machitidwe 2:47.5) Paulo anakhala “chili chonse kwa anthu onsewo”, ndi cholinga chofuna kuti afalitse bwinouthenga – 1 Akorinto 9:19-22.6) Antchito ampingo anali kudzodzedwa “powaika manja” – Machitidwe 6:1-6.7) Ophunzira oyamba anali kutchedwa Akhristu – Machitidwe 11:26.8) Anthu omwe ubatizo wawo woyamba sanali watanthauzo anabatizidwanso – Machitidwe 19:1-6.B. Koma ndi anthu ochepa omwe amakhulupirira kuti chitsanzo chirichonse mumpingo woyambachipereka lamulo lomwe tiyenera kulitsata m’masiku ano.1) Alaliki ankapita awiriawiri – Luka 10:1-4.2) Paulo anafotokozera chiphunzitso ndi ndakatulo ya osapembedza – Machitidwe 17:28.3) Paulo analalika mu kachisi wa Ayuda – Machitidwe 13; 14:1; 17:1,2.4) Analalika miyezi itatu m'kachisi mmodzi – Machitidwe 19:8.5) Anali kuphunzitsa tsiku ndi tsiku pa “sukulu ya ku Turano” – Machitidwe 19:9,10.6) Anasonkhana pa mgonero wa Ambuye usiku m’chipinda chapamwamba – Luka 22:7-20;Machitidwe 20:7,8.7) Paulo analalika mpaka usiku ndi kupitiriraponso – Machitidwe 20:7,11.8) Mgonero wa Ambuye unachitika pogwiritsa ntchito chikho chimodzi – Mateyu 26:27.9) Mpingo wa ku Yerusalemu unasankha atumiki 7 kuti athandize pa chakudya – Machitidwe 6:1-6.10) Nthawi zambiri Paulo ankayenda pa ngalawa pokalalika.C. Kuganizira chitsanzo chomwe chiri chomangirira inali ntchito yaikulu m’nthawi yobwezeretsa.Zitsanzo:1) Iwo omwe anatsutsa anaunikira pempho la alaliki ku chitsanzo cha Paulo chosalalikira kumalokomwe Khristu akudziwidwa kale – Aroma 15:20.2) Omwe amatsutsa kugwirira ntchito kwa mipingo pamodzi amati mumpingo woyamba uja,chithandizo chimachokera kuchokera ku mpingo umodzi kupita ku winawo pa nthawi zamabvutozokha ndiponso kuchokera ku mpingo wopeza bwino kupita kumpingo wosauka.3) Gawo lina la zitsanzo zomwe chithandizo chinali kupita kwa a mishonale osadzera ku mpingowomwe unali kumthandiza – Afilipi 4:15,16; 2 Akorinto 11:8.4) Omwe amatsutsa za Sunday sukulu amati chitsanzo chomwe timaona cha maphunziro a gulu ndichokhacho chomwe timaona mpingo wonse uli pamodzi, ndipo amati chimenechi ndichochimaletsa malasi otsatana – Machitidwe 11:26; 1 Akorinto 14:23.Umodzi 55

5) Dr. J.D. Thomas amapereka maganizo oti “pokhapokhapo ngati pali chisonyezo choonadi ndichomveka bwino choti machitidwewa anali oyenera kuchitidwa, [ndi Akhristu oyamba, ndiulamuliro wa atumwi]. Ifenso tidzachita koma mwa ufulu wosankha m’masiku ano. (mawu alim'mikutirowo ndi anga).3 Ndi maganizo ati omwe ndi ofunikira?A. Malembo ndi malamulo ena amphamvu opezeka, ngakhale sanafotokozeredwe mwatchutchutchu,akhoza kungoganiziridwa mwa chilungamo kuchokera ku zonenedwa ndi mfundo zina. Zitsanzo:1) Kaini ndi Abele anauzidwa mtundu wansembe yomwe Mulungu anafuna, - Genesis 4:3-5; Ahebri11:4.2) “Kulalikira Yesu” kunaphatikizana ndi kulalikira ubatizo – Machitidwe 8:36-39.3) Ubatizo siwamakanda ayi – Marko 16:16, Machitidwe 2:38.4) Kusiyana pakati pa mwamuna ndi mkazi chifukwa cha chigololo kumaloledwa kwa mwamunangakhalenso mkazi – Mateyu 19:9; Marko 10:11,12.5) Mpingo uliwonse wa pamalo udzikhala woima paokha monganso iriri mipingo ina yonse –Machitidwe 14:23; Tito 1:5.6) Kulibenso Atumwi padziko lapansi masiku ano – Machitidwe 1:21,22.7) Munthu wathupi la uchimo sikuti ndiwongotaikiratu – Luka 8:15.8) Oyang’anira ayenera ayambe ayesedwa ndi kubvomerezedwa asanaikidwe manja – 1 Timoteo3:10.9) Anthu ofuna ntchito ya oyang’anira ayenera asankhidwe ndi mpingo – Machitidwe 6:1-6.B. Komabe pali kusiyana pakati pa ganizo lofunikira, ndi losatsimikizika kapena looneka ngati ndi loona.1) Poti Ayuda patsiku la Pentekoste (Machitidwe 2) anauzidwa kuti alape nabatizidwe, ndi ganizolofunika kuti anthu amenewa anali achikulire kuti anatha kukhulupirira ndi kubatizidwa.2) Likuoneka ngati ganizo loona koma losatsimikizika loti popeza anthu analipo zikwi zitatu ndiyekuti mmaiwe ndi m'malo osamba anthu mu mzinda wa Yerusalemu.3) Likuoneka kuti ndi ganizo loona ndipo lingatheke loti atumwi onse anagwira ntchito yobatizaanthu zikwi zitatu aja mothandizana.C. Nthawi zambiri pakhala pali bvuto pofuna kumvana ngati ganizo la anthu pa mfundo ina ndi lofunikakapena losatsimikizika kapena ndi lotheka. Zitsanzo:1) Mpingo wa ku Trowa unasonkhana pa tsiku loyamba la Sabata kunyema mkate – Machitidwe20:7. Atsogoleri antchito yobwezeretsa anali naonso maganizo amenewa oti mipingo yonse,kulikonse m’Chipangano Chatsopano amanyema lamulungu lirilonse. Komabe ena amafunsangati limeneli liri ganizo lofunikira potengera pa ndime yake yokhayi.2) Ganizo linanso likutengedwa mu 1 Timoteo 3:2, loti mwamuna mmodzi sangakhale mkulupamalo. Koma enanso amatsutsa zimenezi.Umodzi 56

3) Mkate womwe unkagwiritsidwa ntchito pa Pasika unali wopanda chotupitsira. Yesuanagwiritsa ntchito mkate wapa Pasika pamene anali kuyambitsa mgonero wa Ambuye.Pakhala ganizo loti mkate wa pamgonero wa Ambuye ueyenera udzikhala wopandachotupitsa.D. Tomasi Campbell, m’chikalata cha dongosolo lake analemba:Ngakhale zoganizira chabe ndi zochotsedwa ku malemba, ngati zaganiziridwamwabwinoko, zingathe kumatchulidwa kuti ziphunzitso za mau opatulika a Mulungu,koma kodi sizikumangiriridwa mmaganizo a Akhristu kopitirira. Komwe akanayenerakuunika ndi kulumikiza bwino mgwirizano wake, ndipo mwaumboni natsimikizira kutiziri chonchodi; popeza chikhulupiriro chawo chisasamire pa nzeru za anthu, koma mumphamvu ndi ulamuliro wa Mulungu. Choncho palibe kuchotsa zinthu kwa mtunduumenewu kungatengedwe monga choyanjanitsa, koma zimakhala ku zotsatira ndikumangirika kwa mpingo.Iye analankhula zimenezi chifukwa anaona kuti panali kutsamiranso pa maganizo a munthupotenga maganizo a choonadi cha m’malemba.4. Kusiyanitsa pakati pa zofunikiradi ndi zongochitika.Ngakhale chitsanzo cha mpingo woyamba uja chingakhale molingana ndi malamulo a atumwiaja, zichitika zawo zina zitha kungokhala monga zochitika chabe zomwe ziribe gawo lirilonsendi chifuniro cha Mulungu mu mpingo wake. Mwachitsanzo, cholinga, kutanthauza ndimagawo ena a mgonero wa Ambuye monga tionera mmalemba akuonetsa chifuniro chaMulungu kwa ife lero, koma malo kapena nthawi yochitira mgonerowo (m’chipindachapamwamba usiku) ndi zinthu zoti zinangochitika basi.5. Kusiyanitsa zochitika mdziko lathu kapena dera lathu, zokhala kanthawi kochepa ndinsozachikhalidwe, ndi ziphunzitso zapadziko lonse ndi magwiritsidwe ntchito achikhalire.A. Malamulo ngakhale zitsanzo zina zinaoneka ngati tanthauzo lake ndi cholinga chake kwakanthawi kochepa ndi malo ake. Zitsanzo:1) Akazi kubveka mitu yawo popemphera – 1 Akorinto 11.2) Kupsopsonana kopatulika – 1 Akorinto 16:203) Kusamba mmapazi – Yohane 13; 1 Timoteo 5:10.4) Kupewa banja chifukwa cha masutso alinkudza – 1 Akorinto 7:25-31.Izi siziri zotimanga ife lero ponena zoona, ngakhale kuti malamulowo akutero. Enasamasiyanitsa ndipo akadagwiritsidwabe ntchito malamulowa lero.B. Anthu a mgulu lobwezeretsa lija ndinso ena omwe sanali mgululi anatsutsa kuti mfundo yam’Chipangano Chatsopano yoletsa akazi kutsogolera mmisonkhano yachipembedzo ndintchito za mpingo linali monga mwambo ndi chikhalidwe komanso malinga ndi nthawiyo,osati ndiyogwira ntchito padziko lonse mpaka kale ayi. Koma Paulo watengera malamulo akepa chilengedwe ndi kuchimwqa kwa munthu – 1 Akorinto 14:34-35; 1 Timoteo2:11-15.C. Payenera kukhala kuganizira mozama bwino kuti tithe kusiyanitsa zofunikira kwambiri, ndiUmodzi 57

zongochitika chabe ndi zachikhalidwe, komanso ndi zogwira ntchito konsekonse.6. Kusiyanitsa zoyambirira ndi zopitirira nazo pa chifuniro cha Mulungu.Malamulo ndi zitsanzo zina zimakhazikika ndi kukhuza kwambiri ku nthawi zoyambirira ndizokhazikitsa mpingo, osati ku nthawi zonse. Zitsanzo: “Zizindikiro za mtumwi” – 2 Akorinto12:12; udindo wa atumwi; Bungwe la ku Yerusalemu – Machitidwe 15.7. Kusiyanitsa mawu okuluwika ndi oona.A. Baibulo liri ndi mau ena omwe analembedwa kuti amveke monga momwe aliri mosabvutandipo ena akamveke mokuluwika. Timasokoneza zomwe Baibulo litanthauza pamene titengamau olembedwa moona ngati mkuluwiko ndi olembedwa monga mkuluwiko ngati oona.B. Mafunso ena okhudza chipembedzo omwe amafunsidwa pa nkhani imeneyi ndi aja a zaulamuliro wa zaka chikwi (mileniamu) wa Khristu (Chibvumbulutso 20) ndinso zogwiritsantchito zikho zambiri pamgonero wa Ambuye.C. Maganizo othandiza kuti tizindikire mau okuluwika (olembedwa ndi J.R. Duncan):1) Momwe nkhaniyo ikumvekera.2) Ngati zonenedwazo zinena zachinthu choti sichingatheke mwachilengedwe.3) Ngati tanthauzo lenileni la nkhaniyo litsutsana ndi malemba ena.4) Ngati tanthauzo lake lenileni lidzafuna machitidwe omwe ali olakwika kapena oletsazinthu zoona.5) Ngati tiuzidwa kuti ndi mau ophiphiritsa.6) Ngati zotsimikizika ndi zokhazikika zilowa m’malo osatsimikizika ndi osakhazikika.7) Ngati zinenedwa mongoseweretsa.8) Kuona wekha momwe zinthu ziriri panthawiyo ndi nkhaniyo.9) Malamulo amaperekedwa mmau omveka bwino.7. Kodi zoyankhula za Yesu mnthawi za utumiki wake zikutilamula ife mumpingo lero?A. Anthu ena amati ziphunzitso za Yesu pankhani za kulekana m’banja ndi kukwatiranso ndinsozomwe anayankhula pa chiphunzitso cha paphiri zinali za kwa mbadwo wapansi pa chilamulocha Mose omwe unatha panthawi yomwe Yesu anafa, ndipo sizigwiranso ntchito mumpingolero.B. Pamene zina za ziphunzitso za Yesu zinkagwirizana ndi momwe Ayuda ankamvererachilamulo cha Mose (pita ukadzionetsere kwa ansembe; “Alembi ndi Afarisi amakhalapampando wa Mose; choncho mverani ndikuchita zomwe akuuzani”), zambiri za ziphunztsozakezi ndi za ufumu/mpingo ndipo ndi zokonzedwera mpingowo. Chiphunzitso cha paphirichinena za chiyero cha ufumu – Mateyu 5:20ff. Pankhani ya banja kulekana ndi kukwatiranso,Yesu akusiyanitsa chiphunzitso chake ndi cha Mose – Mateyu 19:3-9.Umodzi 58

Mitu yofunika potsiriza:1. Ambiri akufufuza matanthauzo ena atsopano pakati pa mipingo yonse yomwe iri mgawolobwezeretsa lija. Iwo amadzudzula kusagwiritsa bwino ntchito ndinso kusiyana maganizomugululi pamomwe anamvera ndikutanthauzira machitidwe akale aja (malamulo, zitsanzo,kuganizira kofunika). “Mamasuliridwe amasiku ano” amafunika kuti ife tisiye kufufuza zazoonadi za nkhaniyo kuchokera kunkhani yomwe siikhudza nkhaniyo ndipo tiganiziremosamala zankhaniyo, mbiri ya nkhaniyo yalembedwera. Alangizi abwino ndinso omasuliramalemba okhwima akhala akulimbikitsa zimenezi. Mamasuliridwe atsopano amakana zitsanzondi zoganizira kuti zisakhale zamphamvu yolamulira ndipo amangobvomereza malamulookhawo olembedwa mosakuluwika ndi mwwachindunji. Izi zakhala chomwechi chifukwa chamabvuto omwe takomana nawo pofuna kuzindikira kuti kodi ndi zitsanzo ziti kapenazoganizira ziti zomwe ziri zomangirira. Koma mabvuto onsewa akatha, anthu adzakhalabeakuyang’ana pa zotsanzo ndi zoganizira kuti apeze muuni wowaunikira kuti mpingoukhulupirire ndi kuchita ziti.2. Zolimbana zathu zambiri za momwe tingagwirire ntchito ya mpingo zimabwera chifukwachokakamira dongosolo kapena machitidwe, zomwe zotsatira zake zimayamba kulamulidwandi moyo wopendekera ku chilamulo. Mpingo woyamba womwe unachita potsatira utsogolerindi malangizo a atumwi sunayenere kukhala chitsanzo chathu, koma timaona dongosolo lakachitidwe mmalo monse momwe Mulungu analibe nawo dongosololo. Timachita izichifukwa cha khalidwe lathu lomwelija lopendekera pa malamulo lofuna kukhala odziwitsitsa.Pamene tisiya moyo ndi khalidwe lopendekera ku malamulo ndikuyamba kumvera pansi pachisomo, pamenepo tidzatha kulemekeza chitsanzo cha m’Chipangano Chatsopano popandakupitirira ndi kumasulira moonjezera.3. Malembo amazindikira zambiri zomwe ndi mfundo zazing’ono zomwe zimatchedwa “mfundo,kapena nkhani zazing’ono zoti titha kusiyana pa momwe tiziganizira” – Aroma 14,15 – nkhanizomwe mpata umakhalapo anthu atha mwachilungamo, ndimokhulupirika kulolerana kusiyanamaganizo pakumasulira kwake. Tiyenera kulemekeza chikumbumtima chathu pazomwe ife enitichita, koma Baibulo litiphunzitsa kuti tingathe ndipo tiyenera kugwira ntchito pamodzi ndiiwo omwe maganizo awo ndi athu asiyana kwambiri pa zinthu zina zazing’ono. Koma palimfundo za choonadi zina zazikulu za uthenga wabwino zomwe tiyenera kugwirizana kutitikhale amodzi (onani ndikuwerenga Aefeso 4:1-6). Mfundo zazikulu zachoonadi zimenezizalembedwa momveka bwino m’Baibulo. Choncho pamene tiri ofunikira kulimbikirabentchito yofufuza zomwe Mulungu atilamulira m’malemba, sikuti tidzipeza mayankho onsekapena kugwirizana pa mfundo zofunikira zazikulu kuti tithe kugwira ntchito pamodzi.--B. ShelburneSouth Texas Leader’ MeetingSeptember 30, 1989Kusiyanitsa Malemba ndi Miyambo M’chipembedzo.Mawu oyamba: Werengani Marko 7:1-13. Ayuda anadzipangira miyambo yaumunthu yambirinaipanga kukhala yamphamvu ndi ulamuliro kotero kuti anaika pambali chilamulo cha Mulunguchifukwa cha miyambo yaoyo. Kodi nafenso tingachite zimenezi? Mipatuko yambiri mntchitoyobwezeretsa ija inabweramo chifukwa cholemekeza kwambiri miyambo ndi kuitenga ngati yofunikakwambiri kuposa malemba.Malemba ndi mau a Mulungu. Sitingathe kumasula chomwe iwo amanga mwaqchimvekere. Miyambondi mau a munthu. Imapangidwa ndi nzeru za munthu ndi zikhalidwe za makolo zosiyirana. Tiri ndiufulu wosintha miyambo ndi zizolowezizi.Umodzi 59

1. Kodi miyambo imayamba bwanji? Nanga imachokera kuti? Inayamba kudzera m’njira ziwiri:ABPamene Mulungu wapereka lamulo lomwe sanafotokoze bwino momwe lamulololigwirira ntchito, iye watisiyira mwai woti tisankhe njira yabwino yogwirizana ndi nthawiyathu komanso momwe zinthu ziriri panthawiyo.1) Izi ziyenera kutero popeza uthenga waperekedwa ku mitundu yosiyanasiyana mzakamazana-mazana.a) Ife timagwiritsa ntchito njira zosiyana siyana zofalitsira uthenga mosiyana ndimpingo woyamba uja.b) Timasonkhana mmalo osiyanasiyana koc) Machitidwe ena a kapembedzedwe kathu ndi osiyana kwambiri ndi ampingowoyamba uja.2) Pamene malembo safotokozera bwinobwino njira ya machitidwe ake, ife timayang’anapa zofunikira za munthawi zathu zino ndi malo athu ndinso poganizira zomwezingachitikedi kuchokera mmalemba, ndipo kenako timasankha njira yoyenera ndiyabwino. Zizolowezi ndi zikhalidwe zimenezi, kaya njira zimenezi zoyambika kalezi,ndizo zimapanga miyambo.3) Miyambo imatha kuyambanso posonkhanitsa nzeru zochokera kwa atsogoleri athuomwe timawalemekeza ndinso anzeru ena amakedzana.4) Sinkhani zonse zopezeka mmalemba zimamveka bwino. Mu zomwe sizimvekabwinozo, mwai ulipo wololera mokhulupirika kusiyana kwa maganizo ndikutanthauzira. Kutanthauzira kwa mfundozi ndikosiyirana kuchokera ku mbadwoumodzi kupita ku mbadwo winawo, ndipo sitimaphunziranso nkhanzo kwa ife tokha.5) Malembo satchula pachokha mwachimodzichimodzi cha zonse zomwe tikumana nazomunthawi zathu zalero (monga mankhwala ozunguza bongo). Tiyenera kumaona zoonazenizeni za malemba pa zinthu zimenezi ndikuzigwiritsa ntchito pa zochitika ndizobvuta moyo wathu wa masiku amakono. Aphunzitsi athu ndi atsogoleri athuamagwiritsa ntchito njira imeneyi poweruza zina ndi zina ndipo nafenso timasiyira ena.Zonse zosonkhanitsidwa kuchokera ku maweruzo akalewo zimakhala miyambo yathukapena zizolowezi zathu ndi ziphunzitso zathu mumpingo. (kumbukirani, kutisitikunena za zinthu zolembedwa momveka bwino m’Baibulo, koma za maganizoathupi la munthu lopanda ungwiro.)6) Izi zingathandize kupeza chifukwa chomwe gulu lathu lagawanika.a. Chipangano Chatsopano chinalibe cholinga choti chikhale monga bukhula dongosolo la malamulo monga chinali Chipangano Chakale (ngakhaletiyenera kulemekeza malamulo omwe chitipatsa)b. Kwakukulu Chipangano Chatsopano chiri ndi mfundo zazikulu zachoonadi zomwe zingagwiritsidwe ntchito pa bvuto liri lonse muchikhalidwe chiri chonse. Ndipo Mulungu ayembekezera kuti ife tikulemonga Khristu mu umunthu wathu kuti tithe mwaumunthu wathukuchita zinthuUmodzi 60

Umodzi 61zobvomerezeka – Yeremiya 31:33; Aroma 13:10.c. Koma thupi lathu lauchimo limakonda malamulo ooneka olembedwamofotokozedwa bwino monga a m’Chipangano Chakale aja.1. Kuti titsimikizire zaungwiro wathu poona momwe tichitirabwino potsatira malamulo ena.2. Kuti tisamaganizire ndikugwiritsa ntchito malamulo.3. Kuti tisasinthike mkatimo.d. Choncho tayesetsa kuika “mosamveka bwinomo” m’ChipanganoChatsopano pongoganizira, kuchotsera, kuika maganizo athundikumasulira malingana ndi zomwe tikuyembekezera. Timafunalamulo lapa chirichonse. Dongosolo lirimo m’Chipangano Chakalelakayendetsedwe kampingo ndi ntchito zake, koma nthawi zina tatengandikugwiritsa ntchito moyo wopendekera pa dongosolo lodziwika,ndikufuna dongosolo la malamulo ena oti m’Chipangano Chakalemulibe ata. Ndipo kuyambira pamene maganizo ndi nzeru zina zamunthu zinayamba kugwiritsidwa ntchito kuti zitseke mmipata momwesimumamveka bwino ndikuti apeze dongosolo lakayendetsedwe kantchito zina, nthawi zonse sitinakhala ndi maganizo ofanana mumchitidwe umenewu. Choncho tangokhala ogawikana mtimagulu,kagulu kali konse ndikumaganiza kuti ndikokhako komwe kayendetsantchito zampingo mogwirizana ndi dongosolo la malemba.e. Tikanatha kupewa kugawikanaku ngati tikanazindikira kuti kutsutsanakwathu kulipo chifukwa cha mbali ya maganizo athu ndikutanthauzirakwa umunthu wathu, osati chifukwa cha malemba omveka bwino.Ndiyenera kumvera chikumbumtima changa, koma ndisamangirirechikumbumtima changacho kwa ena ngati njira yoyesera Chiyanjanochathu. Makolo athu am’ntchito yobwezeretsa ija anati,”mchikhulupiriro,k umodzi; mmaganizo, ufulu; mzinthu zonse,chikondi.”2. Ndikofunikira kudziwa ndiikumvetsa kuti mmitundu yonse ya miyambo muli maganizo ena aumunthu.A. Miyambo ingathe kufaniziridwa ndi mau a Mulungu, koma ndi maganizo a munthu. (Miyamboina ingathe kukhala ndi maziko ake ochokera ku malemba kuposa ina.)B. Nkhani zomveka bwino ndi zofunikira za mau a Mulungu sizingaikidwe pambali kapenakukaikiridwa. Ngati sitilemekeza mphamvu ya mau a Mulungu, ndiye kuti basi, tataya zonse.Tasokonekera.C. Koma kusiyana maganizo pa miyambo kumafuna kulolerana chifukwa ife pamodzi ndiamphunzitsi athu tonsefe ndi anthu omwe tingathe kuchimwanso. Choncho ndikofunikirakwambiri kumadziwa kuti kodi ndi nkhani ziti zomwe ziri zammalembo ndipo ndiziti zomwesiziri zammalembo koma zamiyambo chabe.D. Miyambo ndi zizolowezi za chikhalidwe ndi mamvedwe a zinthu angathe kusiyidwa pambalindikusinthidwa ngati akusokonezandikulepheretsa ntchito ya Mulungu.

(Zitsanzo: ganizo loti akazi samakhala pamodzi pophunzira Baibulo mwapadera; kugwiritsantchito Baibulolotanthauziridwa kamodzi kokha basi; kusagwirizana ndi nyumba zopembezereramo;maganizo oti mlaliki sangalalike mmalo oposera amodzi pa nthawi imodzi; ganizo loti munthummodzi ndiye adzilalika nthawi zambiri mumpingo;p ndi zina zotere.)3. Zoona zina zomwe tiyenera kuzizindikira zokhudza kusintha mmiyambo yathu.A. Tiri ndi miyambo monganso ena amachitira.B. Tiyenera kumadziwa kusiyana pakati pa miyambo ndi malembo kuti tisalimbane chifukwa chamiyambo monga momwe tingachitire chifukwa cha malemba. Akhristu ena olemekezekaakupha mipingo yawo chifukwa chosadziwa za kusiyana kumeneku. Tidzalandira mphotochifukwa choima nji! Pa malemba; tidzaweruzidwa chifukwa chogawanitsa kapena kutchingampingo chifukwa cha miyambo ndi zizolowezi.C. Kawirikawiri kusintha sikukhala kwa phindu ngati kungokhala kapena kuchitika chifukwachongofuna kusintha basi (pokhapokha kukhale chifukwa chofuna kutidzutsa ndikutipangitsakuti tiganize zomwe tikuchitazo).D. Ngati njira kapena maganizo omwe tazolowera kuchitira zinthu akulepheretsa ntchito yaMulungu, tiyenera kukonzekera ndikukhala ndi chidwi chofuna kusintha. Iripo mizimu yomweikapezeka kumwamba pokhapokha ngati titasintha magwiridwe athu antchito kuti ikhaleyamphamvu. Paulo mtumwi anali wokonzekera kusintha chirichonse chomwe sichinalichomangiririka ku mau ngati chinali choti chikapulumutse mizimu yotayika – 1 Akorinto 9:19-23 – ndipo sakanakondwera ndi mitima yathu yosalola kusunthika koma kuumirira miyambondi zizolowezi yomwe ikulepheretsa kufikira mizimu yotayika yomwe iri kunja.E. Inde ndikobvuta kwambiri kusiyiratu mwambo wogwirira ntchito kapena kamasuliridwe,ngakhale kuti kutero kuli kulimbana ndi mau a Mulungu kapena kulepheretsa ntchito yaMulungu. Komatu dziwani kuti sipakhala kukula muuzimu kapena kukula kwa mpingo ngatipalibe kusintha kwabwino.F. Zambiri zomwe tichita mumpingo kuti tiyang’anitsitse tidzaona kuti ndi zizolowezi chabekaya miyambo chabe zosati zofotokozeredwa mu malemba. Zitsanzo:Mapemphero a Lachitatu madzulo.Misonkhano iwiri yamapemphero Lamulungu.Mapemphero a Lamulungu mmawa pa 10:30Mgonero wa Lamulungu usiku.Pemphero lalikulu limodzi.Nyimbo zitatu tisanapemphere kenako nyimbo litatha pemphero.Kusiya vesi yachitatu ya nyimbo.Bukhu la nyimbo.Otsogolera nyimbo.Madododo a nyimbo mmabuku a nyimbo.Mayimbidwe okhala ndi magawo anayi onse a mau.Kuimba mokoma monga momwe tidziwira.Chikho chakechake pamgonero.Madzi a chipatso champesa.Kudutsitsa chifaniziro chamgonero mmizere.Umodzi 62

Kutenga kochepa kwambiri ka mkate ndi chikho.Pagome.Nyumba zopemphereramo.Maofesi a nyumba zopemphereramo.Zizindikiro za mpingo.Dzina loti “Mpingo wa Khristu” monga dzina lokhalo lobvomerezeka ndi lopambana.Nyumba zosonkhanirana.Mobatizira.Malaudi sipikala.Zida za kanema ndi kanema.MaBaibulo olembedwa ndi alembi osiyanasiyana.Kagawidwe ka mitu ndi ndime m’Baibulo.Othandizira ntchito zina.Ulaliki wotenga mphindi wakumi atatu (30 mins)Nyimbo zoitana.Misonkhano yofalitsa uthenga yotenga sabata yatunthu.Munthu mmodzi yekha wolalikira nthawi zambiri.Alaliki a achinyamata, misonkhano ya achinyamata kuperekera mbale ya chopereka.1) Miyambo yambiri yomwe tawerengayi inayamba yakanidwapo pamene inalikungoyambidwa kumene. Ina yaiyo mpaka lero ikuoneka ngati yabwino ndiyobvomerezeka munthawi zathu zino. Inayo ingafune kuonedwansondikusinthidwa apa ndi apo. Mbali yaikulu kwambiri ya dongosolo la momwetichitira mumpingo lingathe kusinthidwa koma ndikumapitirirabe kumverandikulemekezabe zomwe malemba amaphunzitsa.Zofotokozera:• Kukhala mozungulira gome ndikumalandira mgonero monga tichitirapakudya chakudya.• Zosakhala ndi woyendetsa ntchito kutsogolo kapena ulaliki wokonzedwa.• Kuwernga malembo ambiri.• Alaliki osiyanasiyana pa misonkhano yosiyana.• Msonkhano kugawidwaq mtimagulu khumi ting’ono ting’ono.• Msonkhano wotenga maola awiri.• Mapemphero asanu kapena khumi.• Aliyense kupita kutsogolo kukalandira mgonero.• Kumangoimba ndi mau amodzi ofanana osagawa mmau anayi aja ngatikwayala.• Kuyamba ndi mgonero ulaliki usayambe.• Akazi kukhala kwaokha mosiyana ndi amuna.• Kukumana kwa kumidzi.Izi sikuti ndiye zobvomerezekazo, koma zikusonyeza zomwe zinayenerakuchitidwa malingandi ndi malemba.2) Tikanabvutika kwambiri polandira ndikupembedza potengera dongosolo lampingo woyamba uja, ngakhale posanena za mphatso zao za Mzimu Woyera:• Analibe nyumba yawoyawo yopembedzera.• Oyankhula ambiri pamsonkhano – aliyense yemwe anali ndi choyankhula.• Aliyense yemwe analindi nyimbo yakeUmodzi 63

ankaimba osatinso zotokonzekera.• Nthawi zambiri ankakweza manja mmwamba popemphera.• Akazi ankabvala maduku, osangoti monga chipewa chabe.• Kulibe kukonzekera ngakhale dongosolo lenileni.• Kupembeza kwawo kumatenga nthawi yaitali kwambiri.3) Akhristu ampingo woyamba uja nawonso akanabvutika kwambiri ndi miyamboyathu.• Kutsiriza ikamafika 12 koloko.• Zinthu zabwino, zamakono monga nyumba etc.• Akazi osabvala maduku, obvala zobvala zionetsa mikono yawo.• Amuna ndi akazi kukhala pamodzi (kumaiko ena)• Nyimbo zoyimbidwa mokoma, ndinso mamvekedwe anayi munyimbomonga mau onse aakulu, aang’ono, apakati ndi ena okometsera.• Misonkhano yokhala ndi ndondomeko, yochepetsedwa mwina chifukwacha zina (?)4) Mipingo yathu imene, yasintha zambiri mzaka zapitazi osazindikira kuti tasiyamalemba.• Kusintha kuchokera ku Baibulo Lolembedwa m’chichewa chakale kupitaku chichewa chamakono.• Misonkhano ya achinyamata.• Magulu ogwira ntchito zina.• Kuyenderana pakati pa amayi.• Madongosolo a mautumiki.• Magulu apadera oyimba.• Mautumiki a mapemphero apadera.• Nkhani za mumpingo m’manyuzi.• Kugwiritsa ntchito vidiyo ndi zithunzi zake.• Kugwiritsa ntchito ndalama zampingo pogulira chakudya ndimmisonkhano.• Matimu a mpira a mpingo.• Nyumba zochitira masewera olimbitsa thupi ndi zina za anthu abanjalonse.• Alaliki achigawo kapena pamalo.• Misonkhano yokonzedweratu.• Ubatizo wochitika mmadamu okonza osati ku mtsinje kapena dziwe.• Kugwiritsa ntchito malaudi sipikala ochokera ku “misonkhano ina” mumpingo wa Khristu.• Kuwawerengera ana nthano ya m’Baibulo nthawi yamapemphero aLamulungu.G. Miyambo ingathe kukhala ndi nzeru. Nthawi zina zimaonetsa kuphunzira ndi umulungu waatsogoleri anzeru, komabe miyamboyi ndi ya anthu basi.H. Miyambo kawirikawiri imangothandiza kuti munthu adziwike mtundu wake. Kusinthamiyambo ndi zizolowezi sikulakwira Mulungu, komatu kwa ife kumaoneka ngati kusinthampingo. Koma kusintha kwambiri kopanda tanthauzo kwa miyambo ndi zizoloweziUmodzi 64

kungasokoneze mpingo ndikubweretsa kusamvana.I. Bvutoli pamenepa sikukhala ndi miyambo, koma kuilola kuti ikhale monga mfumuyotilamulira ndikumabvutika kusamala monga momwe tikanachita ndi mau a Mulungu.J. Miyambo imasonkhanitsa ndipo imafuna kuti tidziilemekeza. Njira yekhayo yomweingatithandize kupewa kulowerera ndi kuyamba kulamuliriridwa ndikufooketsedwa ndimiyambo ndi zizolowezi zimenezi, ndi younikanso miyambo yathuyo m’mibadwo yonsepogwiritsa ntchito kuunika kwabwino kwa mau a Mulungu powerenga liwulo ngati kutisitinamveponso zamiyambo yathu. Izitu zimafuna kulimba mtima ndikupirira zedi. Miyamboiyenera kumaunikidwa ndi malemba, osati malemba kumawaunika ndi miyambo.Mau otsiriza: Tayesani kufufuza ndikuzindikira momwe maganizo anu amangiriridwa ku miyambo.Tapezani nthawi yoti muganizire mozama zazinthu, ndipo mosadzinyenga nokha muonemo zinthuzangokhala monga miyambo chabe. Izi zidzakuthandizani ndipo mudzaona kusiyana pamomwemudzayambire kubvomera momwe mungalandirire kusintha. Nditha kukhala ndi zinthu zanga zomweziri zokondedwa ndipo ndimazitenga ngati zofunika kwambiri, komanso ndiyenera kulemekezandikuonetsetsa kuti thupi la Ambuye likulandira zonse zofunikira zake ndiponso ndiyenerakulemekeza zosowa ndi zofunikira poyamba za ena. Tiyenera “kumverana wina ndi mnzakemkumvera Mulungu” – Aefeso 5:21.--- B. Shelburne, West Tate Seminar, Brownfield, TX, Apr. 1992.Mndandanda wa zothandiza zina pa zotsutsana.Ngati mutapezana ndi wina wokutsutsani muntchito ya Mulungu, nawa Mafunso ena oti mudzifunsenokha.1. Kodi ine ndikuonjesera gawo liti ku makanganowa chifukwa cha kufooka kwanga, kupusakwanga, kusakhala ndi maganizo abwino kapena machimo?2. Kodi kusayankha bwino kwanga kwaonjezera bwanji pakulimbanaku? Ndingathekudziletsa pamomwe ndichitira wina akandikwiyitsa.3. Kodi yemwe akunditsutsayu walakwitsa komabw ali wokhulupirika, kapena ndiwochimwakwenikweni? Izi zimathandiza mayankhidwe anga.4. Kodi ndikupemphera motsimikiza chifukwa cha wonditsutsayo ndinso kuti papezeke njiraya chilungamo ndi yachiyero yothetsera bvutoli? Kodi ndayesapo kusala pamodzi ndimapemphero? Kodi ndikufunsa nzefu, kudzichepetsa ndichizindikiritso cha zolakwazakumbali yanga? Chithandizo cha Mzimu Woyera.5. Ngati pali kulakwirana, kodi ndapitapo kwa m’bale wangayo kapena mlongoyo momverabwino malinga ndi dongosolo losanjidwa ndi Yesu mu Mateyu 18:15-20; 5:23-24?6. Kodi ndapita ndi mtima wodekha (Agalatiya 6:1-2)? Kodi ndakonda mtendere wokwanirakuti nditha kuchitadi dongosolo lopitalo mmalo modikira kuti koma winayo ndiyeandipeze?7. Kodi ndayesetsa kusunga chinsinsi choti makanganowo asakhudze anthu ena? Izizimateteza umodzi wa mpingo ndi banja.Umodzi 65

8. Kodi ndikuyesetsa kugonjetsa choipa ndi chabwino? (Aroma 12:21) kapena kodindikubwezera choipa ndi choipa chinzake? Kodi ndalola kuti wotsutsana nayeyo anditsitsempaka ndifike pakufanana ndi khalidwe lakelo?9. Kodi ndakumbukira kuti kubvutika chifukwa chikhala ndi moyo wofanana ndi Yesundicho chiphunzitso chachikulu chomwe ndiyenera kupereka?10. Kodi ndiri ndimantha kuti ndikambirane zobvuta ndi wonditsutsayo? Mutha kukambiranapa chirichonse, chingakhale chobvuta chotani, ngati muyankhulana munjira yoyenera.Kodi ndabwera munjira zoti zimupangitsa woyambana nayeyo kudziteteza m’malomololera? Kodi ndikuoneka ngati ndifuna kumuputa?11. Kodi ndafufuza njira zina zocchitira zomwe ndiyenera kuchita, zomwe woyambana nayeyoangathe kubvomereza? Nthawi zonse njira imapezeka ngati tikondweretsedwandikufufuzako.12. Kodi ndikuyankhulayankhula za woyambana nayeyo ndi ena mmalo moyankhula kwa iye?Izi zimangosonkhezera moto wa kulimbanako.13. Kodi ndikuyesetsa kudandaulira pagawo lomwe wotsutsana nayeyo ndi inetingagwirizane? Kodi ndikuyesetsa kukonza ubale wathu?14. Kodi ndakhala ndi nthawi yophunzira momwe Yesu pamodzi ndi ophunzira akeanamchitira pamene panabuka kusamvana?15. Kodi ndikuweruza zolinga za mkati a wotsutsana nayeyo pamene sindingathe kuona zamumtima kapena kudziwa zonse zachitika? (Yohane 7:24; Mateyu 7:1-5; Yakobo 2:12,13).Kodi ndingakondwere ndi muyezo womwewo wachiweruzo utaperekedwa kwa ine?16. Kodi ndayesa kupempha malangizo ndi uphungu kuchokera kwa achikulire, anzeru ndiodalilika?17. Kodi ndakhala nayo nthawi yoganizira ngatidi ndikubvutika chifukwa cha ine mwinikapena chifukwa cha Mulungu? Kumbukirani kuti ife sitimuona Yesu akubvutikachifukwa cha iye mwini, popeza anali atadzikhutula nali wofafa ku thupi. Ifensotikufunsidwa kuchita chimodzimodzi.18. Ngati wotsutsana nayeyo salola kusintha, kodi ndiri wokonzeka kutula nkhani yonseyi kwaMulungu mwini? 1 Yohane 4:4; 1 Petro 2:23; Masalmo 23:5. Kodi ndiri wokonzekakusiyira Mulungu kuti abwezere zonse? Aroma 12:19. Kodi ndiri ndi mzimu wokhululuka,pozindikira kuti nanenso ndilakalaka kukhululukidwa – Mateyu 6:12,14,15.19. Ngati ndichoka ndikusiya malo kapena chinthu chifukwa chakulimbana ndikutsutsana,kodi ndayesetsa kuchita mbali yanga yosiya ubale uli wosaonongeka?Zochokera ku maphunziro okonzedwa ndi a Shelburneotchedwa “Moyo ndi ntchito ya Mlaliki”Ndondomeko ya Moyo wa MpingoMipingo ina imalowa pansi chifukwa cha chiwerengero cha anthu ndi mabvuto ndi maganizo.Umodzi 66

1. Kodi tikumuika Khristu ndi mtanda monga potsamira penipeni pa uthenga wathu? 1 Akorinto2:2.2. Kodi abusa akuwetadi mwauzimu, kapena angopanga maganizo ongoti bola ziziyenda malingandikukonda kwawo? 1 Petro 5:1-4; Yohane 10:1-18; Ahebri 13:17.3. Kodi alaliki sanasiyitsidwe ntchito yawo yeniyeni yolalika malembo ku mizimu yosowa?Machitidwe 6:1-6.4. Kodi alaliki ndi atsogoleri ndi zitsa zokwanira za zomwe alalika? 1 Timoteo 3:1-13; 4:12.5. Kodi tikukopa anthu kulowa mumpingo ndi mau a Mulungu, kapena ndi ntchito zina zathupizosangalatsa thupi ndi zina zadziko? 1 Akorinto 3:10-13.6. Kodi timawakonda osochera kotero kuti titha kudzichepetsa molingana ndi momwe angalolereMulungu kuti tikawafikire, kapena timayembekezera kuti iwo ndiwo ayenera kutsatira zomweife tifuna basi? 1 Akorinto 9:19-23.7. Kodi timalimbika posamala otembenuka mwatsopano ndi anthu omwe anagwa naukanso,kapena timangowasiya akumangodzigwera okha? Mateyu 28:19-20; 1 Atesalonika 5:14;Aroma 15:1; Aefeso 4:11-=16; Ahebri 5:11; 6:3.8. Kodi tikugwiritsa ntchito mphatso ndi maluso a azimayi mokwanira ndi mogwirizana ndimalemba? Aroma 16:1-3,6,12; Afilipi 4:2,3; 1 Timoteo5:3-16.9. Kodi tiri ndi chidwi chofuna kuthandiza anthu “kupachika umunthu wao wakale” ndikukhalaobadwa mwatsopano ngati ife kuti abatizidwe? Kodi tikuthandiza anthu, kuphatikizapoatsogoleri kuti athane ndi kudzitukumula ndi kudzikondweretsa okha komwe kumagawanitsamipingo ndi mabanja? Aroma 6:1-14; 7:7-25; 8:1-17; Aefeso 4:22-24; Agalatiya 5:19-23.10. Kodi timalimbikira chiphunzitso cha m’Chipangano Chatsopano pa zakusinthika kwa mkatimonganso momwe tichitira ndi chiphunzitso cha “kutsatira dongosolo labwino?” 2 Timoteo3:5; Mateyu 18:1-3; 2 Akorinto 3:6.11. Kodi tikati kumvera timachit mogwirizana ndi uphungu wa Mulungu watunthu kapenachifuniro cha Mulungu, kapena timangochita pongotsata ziphunzitso zotikondweretsa –Machitidwe 20:27; Mateyu 23:23,24.12. Kodi timawakonda otayika koti mpaka tingalolere kusiya miyambo yathu ina ngatiingatisokoneze ndikulepheretsa kuti tikawafikire?Kodi timasokoneza miyambo ndi zizolowezi za chikhalidwe chathu ndi zofunikira zamalemba? Mateyu 15:1-9.13. Kodi Akhristu ena onse omwe tisonkhana nawo amasamala kwambiri mizimu ya otayikakoposa zowakondweretsa iwo eni ndi zosawakondweretsa? Aroma 15:1-3.14. Kodi pali maubale oipa mumpingo kapena pakati pa atsogoleri omwe chifukwachakudzitukumula sitingathe kuwathetsa, ngakhale akulepheretsa ntchito ya mpingo? Kodiiripo njira yomwe mukupanga pakali pano yoti muthandize kukonza ndi kuchotsa kuwawiranamitima komwe kwakhalapo kuyambira kale mumpingomo komwe kukufoketsa mpingo?Mateyu 18:15; 5:23,24; Afilipi 2:14-16.Umodzi 67

15. Kodi pali machimo ena omwe angobisidwa mmitima ya Akhristu kapena atsogoleri omweakulepheretsa kuti chisomo cha Mulungu chichite nawo mpingo ndikuthandiza? Yoswa 7; 2Akorinto 6:14-7:1; 2 Timoteo 2:19-22.16. Kodi atsogoleri akupitirizabe kuphunzira ndikukula kuti athe kutsogolera osati kuti mpingouwapitrire? 2 Timoteo 2:15; 2 Petro 3:18; Kodi alipo atsogoleri ena omwe akulephera kugwirantchito chifukwa cha mantha? Mateyu 25:14-30; Chibvumbulutso 21:8.17. Kodi kusala pamodzi ndi mapemphero kumakonzekera njira zabwino zopanga maganizo ndimachitidwe abwino? Machitidwe 13:1-3; 14:23.18. Kodi tikuphunzitsa mnjira yoti imapherezera mkusinthika kwa miyoyo? Kodi anthuakuthandizidwa kutuluka muuchimo ndi moyo wachionongeko? Luka 4:18,19; Aroma 12:1,2.(miyoyo yosinthika imakhala ndichikoka)19. Kodi utumiki wathu wophunzitsa umalingana bwanji ndi utumiki wa mapemphero owirikiza?Kodi kapena tikuyeserera kuchita ndi utumiki ulionse popanda unzake? Machitidwe 6:4; 13:3.Maganizo khumi ndi atatu (13) omwe Thomas Campbell analemba ndi kunena poyera.Ganizo 1: Kuti mpingo wa Khristu pano pa dziko lapansi mofunikira, mwacholinga komansomwalamulo langwirizano ndi umodzi; wokhala ndi iwo onse opezeka ku malo konse omwechikhulupiriro chawo chimatsamira pa Khristu ndikumumvera mu zonse molingana ndi malemba,ndikuonetsera zomwezonso pa khalidwe lawo lodziletsa, osati kwa wina aliyenseyo; pakuti siwinaaliyenseyo amene angatchulidwe kuti ndi Mkhristu woona ndi wolongosoka.2. KutiKuti ngakhale Mpingo wa Khristu pa dzikoli ufunikira kukhalabe pakati pa anthuosiyanasiyana, mosiyana ndi wina, koma sipayenera kukhala kusiyananso ndi magawanopakati pake. Ayenera kumalandirana wina ndi mnzake monganso momwe Yesu Khristuwawalandirira ku ulemerero wa Mulungu. Choncho ndicholinga chimenechi onse anayenerakumayendera lamulo limodzi, kusamalira ndikumayankhula chinthu chimodzi; ndi kukhalansoolumikizidwa pamodzi mu mtima umodzi, ndinso muchiweruzo chimodzi.3. Kuti izi zitgheke, pasakhale chirichonse chomwe chikidwe ndikukakamiza Akhristu mongamfundo zolembedwa zoti Akhristu azizilemekeza monga chikhulupiriro chawo, kapenachomwe ayener kulamulidwqa nacho mona malamulo a mgonero, koma zokhazo zomwezaphunzitsidwa molongosoledwa bwino ndikuikidwa mwa iwo kuchokera mmawu a Mulungu.Zosaloleranso china chirichonse, kutengedwa ngati lamulo la Mzimu Woyera, mu malamulooyendetsera mpingo wawo ndi ntchito zina zapakati pawo, koma zokhazo zomwezafotokozedwsa bwino ndi kuperekedwa kwa iwo mwa ulamuliro wa Ambuyathu YesuKhristu pamodzi ndi Atumwi ake pa Mpingo wa m’Chipangano Chatsopano; kaya pakulongosolera kaya pakutsimikizira pa zomwe zinachitika kale.4. Kuti ngakhale malemba am’Chipangano Chakale ndi Chatsopano ndi ogwirizana mosalekana,pamodzi ndikupanga bvumbulutso limodzi langwiro la chifuniro cha umulungu, lomangirirandikupulumutsa mpingo, choncho chifukwa chachimenechi sungagawanitsidwe; koma pa zachomwe chiri cha pacholinga chawo cha panthawi yomweyo, Chipangano Chatsopano chirichangwiro monga Bukhu la malamulo a chipembedzo, khalidwe labwino, ndi kayendetsedwekampingo wa Chipangano Chatsopano, ndinso monga lamulo langwiro lapakagwiridwekantchito zina za anthu ake, monganso popeza Chipangano Chakale chinali mapembedzedwe,kusunga khalidwe labwino, ndiponso kayendetsedwe kabwino ka ntchito za mpingowaChipangano Chakale ndi ntchito zinanso zosankhikia za anthu ake.Umodzi 68

5. Kuti ndikulemekeza malamulo ndi zoikika za Ambuye wathu Yesu Khristu, pamene malemboakhala chete pa za nthawi kapena machitidwe, ngati zoterozo ziripo, palibe ulamulirowamunthu womwe uli ndi mphamvu yoikapo maganizo ake, ndicholinga chofuna kukwaniritsazooneka zoperewerazo podzipangira malamulo ampingo; kapena pasapezeke kuwaikiraAkhristu madongosolo ena munkhani ngati zimenezi, koma iwo ayenera kugwiritsa ntchitomalamulo ndi zoikika za Ambuye Yesu monga momwe zingagwirizanire mwachidziwikire ndikuyankha cholinga cha mpingo wawo. Munthu alibe mwai waukulu woika ulamulo ndizoikika zake mu mpingo, zomwe Ambuyathu Yesu Khristu sanaike. Palibe chirichonsechomwe chiyenera kulandiridwa mu chikhulupiriro kapena chipembedzo champingo, kapenakupangidwa mona mfundo yoyanjanitsa pakati pa Akhristu, chomwe sichinakhalapo munthawiya Chipangano Chatsopano.6. Kuti ngakhale zoganizira ndi zochotsedwa ku malemba, ngati ziganiziridwa mwabwino,zingathe kutengedwa monga chiphunzitso cha malembo oyera a Mulungu, koma pamenepandiye kuti sakumangirika ku chikumbumtima cha Akhristu kopitirira momwe amalandirirachoonadicho, ndikumaona ngati ndimmwne ziyenera kukhalira malinga ndi zomweakuwerengazo; popeza chikhulupiriro chawo sichiyenera kuima pa nzeru ya anthu, komamumphamvu ndi ulemerero wa Mulungu. Choncho, kuchotsera koteroko kusapangidwekukhala monga lamulo loyanjanitsira, koma akhalapo zonse zoyeretsa, kukonza chimangirirocha mpingo. Choncho apa nchachidziwikire kuti kuchotserako zina za mmalemba kotereku,ndikuganizira ndikuikirira maganizo ena omaoneka ngati oona sikuyenera kuchitika munkhanizonse zampingo.7. Kuti ngakhale ziphunzitso za choonadi cha umulungu, ndi maumboni odzitetezera kuzolakwikazi, akhale oti mwina tingataye nawo moyo, ndipo pamene ali okwanira ndi oyenerazolinga zimenezi, ndiye kuti ziri bwino; komabe, popeza zambiri za zimenezi zichitikam’maganizo aumunthu, ndiponso zambiri zake zichokera ku zoganizira za munthu, siziyenerakutengedwa ngati malamulo oyendetsera Chiyanjano cha Akhristu; pokhapokhapo tiganizirazomwe ziri zotsutsana ndi zoonazo, zakuti palibe yemwe ali ndi ufulu pa zachiyanjano champingo, koma zokhazo zokhala ndi chiweruzo chokhala ndi maganizo omveka, kapena afikirapa kudziwitsitsa za ziphunzitso; pamene mpingo unadziwa ndikukhala nazo kuyambira kalelomwe, ndipo udzakhala nazo, zokhala ndi ana, ang’ono ndi achinyamata pamodzi ndiabambo.8. Kuti monga kuli kosafunikira kuti anthu ayenera kudziwa kapena kumvetsa bwino zoonadi zaumulungu zonse zobvumbulutsidwa kuti ziwayeneretse kukhala ndi udindo mumpingo;pachifukwa chomwechi, asabvutike ndikukhala ndi luso la ntchito mwapadera koposa momweangadziwire; koma kuti posiyana ndi zimenezi, mwakuzindikira za moyo wao mwauzimu,kusochera ndikuonongeka kwa moyo wao mwa chikhalidwe ndi zochita, ndinso za njira yachipulumutso mwa Yesu Khristu, kuphatikizira pa luso la pa chikhulupiriro chawo ndikumvera iye mu zinthu zonse, molingana ndi mau ake, ndizomwe ziri zofunikira kwa iwokuwayenereza kulandiridwa ku Mpingo wake.9. Kuti osne amalandira luso limeneli chifukwa cha chisomo, ndipo amachitira umboni zonsezikudzera momwe achitira ndi khalidwe lawo ndi zopsetsa mtima zawo, aonane wina ndimnzake oyeretsedwa amtengo wapatali a Mulungu, akondane wina ndi mnzake ngati abale,ana am’banja limodzi ndi atate mmodzi, akachisi a mtima umodzi, anthu a mtchupi limodzi,achisomo chimodzi, ziwalo za chikondi chimodzi cha umulungu, ogulidwa ndi dipo lamtengoumodzi, ndiponso oyembekezera mwaumodzi kulowa cholowa chimodzi. Choncho omweMulungu wawamanga pamodzi munthu wina asyeserere kuwalekanitsa.Umodzi 69

Kuti malekano pakati pa Akhristu ndichinthu chipitsitsa, chodzala ndi machimo enaambirimbiri. Malekano ndi chinthu chotsutsana ndi Chikhristu, popeza chimaononga umodiwooneka wa thupi laKhristu; ngati kuti iye anagawanika, kuchotsa ndikudula magawo enaathupi lake. Malekano ndi kutsutsana ndi malemba, monga amaletsedwa ndi ulamuliro waMulungu, kuphwanya lamulo lake. Malekano siumunthu, popeza amautsa Akhristu kutiazidzudzulana, adzizondana kapena kudana, omwe ali omangiriridwa ku lamulo lalikulu,loposa, lokondana wina ndi mnzake ngati abale, makamaka monga momwe Khristunsoanawakondera. Mwachidule, malekano ndi chipatso cha kusokonekera maganizo ndinso chantchito iriyonse yachoipa.10. Kuti kunyalanyaza ndikusiyako zina za bvumbulutso la choonadi cha Mulungu, ndinsokungoonjezera ulamuliro wina wopangitsa kuti maganizo a anthu ndizopeka zina kukhala njirayoyanjanitsira, poziika mu malamulo, chikhulupiriro, kapena chipembedzo cha mpingo, ziri,komanso zakhala zodziwika zomwe zayambitsa ndikubweretsa, kuyambitsa zonsezachinyengo ndinso kugawanikana zomwe sizinachitikeponso mu Mpingo wa Mulungu.11. Kuti zonse zomwe ndi zotumikira kwambiri ku ungwiro woposa ndi zoyeretsedwa za mpingopano pa dziko ziri, choyamba, kuti palibe womwe ukalandiridwe ngati woyanjana nafe, komamonga wokhala ndi muyezo wa chidziwitso cha malemba chomwe chanenedwa pamwambapa,ngakhale, chachiwiri, kuti uliwonse ukhale pachiyanjano chake kopotirira koposa ngakhalezoona za luso lake pa momwe achitira ndi zopsetsa mtima ndi khalidwe lake. Chachitatu, kutioyang’anira ake okhala nazo zoyeneretsa monga mwa malemba, ogwiritsa ntchito mfundozokhazo zachikhulupiriro ndi chiyero zobvumbulutsidwa ndikuikidwa mmau a Mulungu osatizina ziri zonsezo zopangidwa ndi munthu. Potsiriza kuti mmagwiridwe ao onse a ntchito zawoamakhala pafupi ndikusunga zonse zoikika ndi umulungu, chitatha chitsanzo cha mpingowakalekale, kuonetseredwa m’Chipangano Chatsopano; popanda zoonjezera zina ziri zonse zamaganizo a munthu kapena zongotulukiridwa ndikuikidwa ndi anthu.12. Potsiriza. Ngati pali zina zochitika malingana ndi nthawi zofunikira kuti zithandizane pochitandi zoikikika za umulungu zisapezeke mmasamba a bvumbulutso la Mulungu, koma, zokhazozomwe ziri zofunikira pachifukwa chimenechi ziikidwa pansi pa gulu za anthu, popandakukometsera kwa mtundu wina uliwonse kuti zioneke ngati gwero lake ndilopatulika, koterokuti kusinthika kulikonse komwe kungachitike kapena kusiyana pa masungidwe a zinthuzimenezi kusabweretse kulimbana kapena kugawanikana mumpingo.Translated from English by Rhodes Maluwa. © by G.B. Shelburne, III (except for any graphics and scripture quotations). May be reproduced for nonprofit,non-publishing instructional purposes provided this entire copyright notice is included and document content is not altered. South Houston BibleInstitute, PO Box 891246, Houston, TX 77289-1246 USA, tel. 281-990-8899, Email shbi@shbi.org, web site . Scriptures, unlessothewise noted, are taken from theBukhu Loyera, lopangidwa ndi The Bible Society of Malawi, P.O. Box 740, Blantyre, Malawi, copyright @ 1999.Umodzi 70

Hooray! Your file is uploaded and ready to be published.

Saved successfully!

Ooh no, something went wrong!