Create successful ePaper yourself
Turn your PDF publications into a flip-book with our unique Google optimized e-Paper software.
83

M’mene mungaleketsere kutayika kwa magazi pachilonda

1. Kwezani m’mwamba mbali yovulalayo.

2. Ikani nsalu kapena dzanja lanu pachilondapo.

Mopsinya muzikhazika dzanja pachilondapo

mpakana magazi ataleka kutayika/kutuluka. Izi

zikhoza kutenga mphindi 15 kapena ola limodzi

kapena kuposerapo. Njirayi ingasiyitsiretu magazi

kutayika/kutuluka pa chilonda chilichonse.

3. Ngati magazi sakuleka kutayika ngakhale muike dzanja kapena nsalu

pachilondapo ndipo ngati munthuyo akutayabe magazi ambiri koti akhoza kufa,

chitani zinthu zotsatirazi:

• Pitirizani kuphimba mosindikira

pachilondapo.

• Kwezani m’mwamba mbali yovulalayo.

• Mangani mkono kapena mwendo pafupi

ndi pachilondapo. Mangani kwambiri kuti

magazi asatayikenso.

• Pomanga pachilonda musagwiritsire

ntchito waya kapena chingwe

chopyapyala. M’malo mwake gwiritsirani

ntchito nsalu yopinda bwino kapena

lamba wamkulu.

Malangizo akasamalidwe:

• Mangani mwendo/dzanja pokhapokha ngati magazi akutuluka kwambiri ndipo

ngati sangaleketsedwe pophimba pachilondapo

• Masulaniko pang’ono mphindi makumi atatu aliwonse kuti muwone ngati chomwe

mwamangacho chikufunikabe komanso pofuna magazi kuti ayende bwino.

Chilonda chikamangidwa kwa nthawi yaitali, zikhoza kuwononga mwendo/dzanja.

Kotero kuti zikhoza kufunkira kuti zidulidwe.

• Musagwiritsire ntchito dothi, parafini, lime kapena coffee pofuna kuleketsa

magazi kutuluka pachilonda.

• Ngati magazi akutuluka kwambiri, kwezani mapazi ndi kutsitsa mutu powopa kuti

thupi lichititsidwa shoko kapena kuchititsidwa mantha akulu (onani tsamba 78).