11.06.2013 Views

Kutentha kwa thupi

Kutentha kwa thupi

Kutentha kwa thupi

SHOW MORE
SHOW LESS

You also want an ePaper? Increase the reach of your titles

YUMPU automatically turns print PDFs into web optimized ePapers that Google loves.

Kumwetsedwa poyizoni

Ana ambiri amamwalira akameza zinthu zomwe zili ndi poyizoni. Pofuna kuteteza

ana anu, tsatani njira zozitetezerazi:

Ikani zinthu zonse zokhala ndi

Poyizoni patali ndi ana.

Poyizoni woyenera kusamala naye:

• mankhwala ophera makoswe • fodya

• DDT kapena mankhwala aliwonse • chitedze

ophera tizilombo monga lindane ndi

sheep dip

• ayodini

mankhwala ochedwa Lye

machesi

mafuta anyali komanso agalimoto

• chakudya chowonongeka

• masamba, njere kapena zipatso

• mankhwala opaka matabwa

zokhala ndi poyizoni

• nyema za ntsatsi

• chakudya chowonongeka

• macheso

105

Musayike mafuta a galimoto

(petulo) kapena a nyali ndi

zina zonse za poyizoni

m’mabotolo a zakumwa

zoziziritsa kukhosi chifukwa

ana angathe kumwa.

Chitani izi msanga:

• Musankakamize kusanza munthu amene sakuzindikira chomwe chikuchitika

(wokomoka) kapena yemwe wamwa poyizoni wa m’mafuta a nyali, agalimoto

ngakhalenso asidi wina wa mphamvu kwambiri. Wodwalayo akakhala mwana

m’mwetseni madzi kapena mkaka maminitsi 15 aliwonse kuti usungunule

poizoniyo.

• Ngati mukuganizira kuti munthuyo wamwa poyizoni wa m’zinthu zina zake ndipo

munthuyo sali mtulo, m’thandizeni kuti asanze. Ikani chala chanu kukhosi

kwake kapena mupatseni supuni ya tiyi yodzadza ndi mankhwala a madzi a

silapu kapena ipekaki (ipecac)(tsamba 402) kenaka ndikum’mwetsa madzi.

Mukhozanso kum’patsa chakumwa chosakaniza makala opera. Akuluakulu

apatsidwe matambula awiri a madziwa (tsamba 402).

Ngati munthuyo akumva kuzizira, mfunditseni bulangeti koma apewe kutentha.

Ngati munthuyo wamwetsedwa poyizoni wambiri, pitani naye kuchipatala

msanga.

Hooray! Your file is uploaded and ready to be published.

Saved successfully!

Ooh no, something went wrong!