Create successful ePaper yourself
Turn your PDF publications into a flip-book with our unique Google optimized e-Paper software.
102

Mmene munthu wovulala kwambiri

anganyamulidwire

Mosamala kwambiri, m’nyamuleni

munthu wovulala mosampinda

paliponse. Samalitsani kuti mutu ndi

khosi zisakhotetsedwe. Munthu

m’modzi agwire khozi mowongoka

molingana ndi thupi ndipo

asasunthesunthe.

Mothandizana, muikeni wovulalayo

mosamala pa machira.

matumba

a chenga

Muuzeni munthu wina abweretse

machira.

Ngati khosi lathyoka, ikani

matumba a mchenga kapena zovala

zopindidwa kwambiri m’mbali zonse

za mutu wa wodwalayo kuti

usayendeyende.

Pomunyamula, yesetsani kuti mapazi akhale m’mwamba ngakhale pa phiri.