Create successful ePaper yourself
Turn your PDF publications into a flip-book with our unique Google optimized e-Paper software.
Zilonda zofika m’mimba

Chilonda chilichonse chofika m’mimba kapena m’matumbo ndi chowopsa.

Zikatero pitani kuchipatala msanga. Koma poyamba chitani izi:

Mangani chilondacho ndi bandeji labwino.

Ngati matumbo ali kunja kwa chilonda, amangeni ndi

nsalu yonyikidwa m’madzi owiritsidwa komanso a mchere.

Musayesere kubwezera matumbowo m’kati. Onetsetsani

kuti nsaluyo ndi yonyowa nthawi zonse.

Musam’mwetse wodwalayo mankhwala

kapena kumupatsa chakudya chilichonse

pokhapokha ngati kungatenge masiku awiri kuti

mukafike kuchipatala. Kenaka mpatseni madzi

akumwa pang’onopang’ono.

Ngati wovulalayo sakuzindikira

chomwe chikuchitika, nyamulani

miyendo yake kuti ipitirire pang’ono

mutu wake.

Ngati wovulalayo ali ndi ludzu, muwuzeni kuti ayamwe madzi akukansalu

koviikidwa m’madzi.

Mpatseni jekeseni wopha tizilombo

toyambitsa matenda.

Musapereke mankhwala othandiza kuchita

chimbudzi (enima) ngakhale mimba itupe

kapena ngati wovulalayo akulephera kuchita

chimudza kwa masiku angapo. Mimba

ikang’ambika, musapereke enima chifukwa

akhoza kupha wovulalayo.

MUSADIKIRE WAZAUMOYO.

PITANI KUCHIPATALA NDI

MUNTHU WOVULALAYO

MWACHANGU. Ayenera

kukachitidwa opaleshoni.

93