Ulendo wa Chiyembekezo - Popline

Ulendo wa Chiyembekezo - Popline Ulendo wa Chiyembekezo - Popline

dbpop1.popline.org
from dbpop1.popline.org More from this publisher
26.02.2013 Views

Ulendo wa Chiyembekezo Maphunziro Othandiza Kusankha Mwanzeru Polimbana ndi Mliri wa Edzi

Ulendo wa Chiyembekezo

Maphunziro Othandiza Kusankha Mwanzeru

Polimbana ndi Mliri wa Edzi

k

GAWO LOYAMBA: Kumvetsa bwino za HIV ndi EDZI

Mau Otsegulira

M’gawo ili muli zochita zokondweretsa zimene cholinga chake nkufuna kutiwuza momveka

bwino kuti HIV, Edzi komanso mankhwala a ARV ndi chiyani. Gawoli likufotokozanso m’mene

kachilombo koyambitsa Edzi ka HIV kamafalira ndi chimene chimachitika m’thupi la munthu

amene ali ndi kachilomboka. Zochita za m’gawoli ndizoti zimupangitse munthu kuganizira

mozama zinthu monga kulandira uphungu ndi kuyezetsa magazi komanso nkhani ya amene ali

ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi.

Uthenga Ofunika

• Aliyense amene amagonana ndi wina osadzitetedza adziwe kuti akhoza

kutenga HIV.

• Sizotheka kudziwa kuti munthu ali ndi HIV pongomuona maonekedwe

okha ayi. Samalani chifukwa maonekedwe amapusitsa.

• Nkotheka kuti munthu akhoza kukhala ndi kachilombo ka HIV

koyambitsa Edzi koma nkumamva m’thupi mwake kuti muli bwinobwino

komanso nkumaoneka wa thanzi.

• Limbikitsanani kupita kukayezetsa magazi kuti mudziwe ngati muli ndi

kachilomabo ka HIV kapena ayi. Izi zikuthandizani inu kupanga zisankho

zoyenera m’moyo wanu.

• Njira zofalitsira Edzi zilipo zochepa. Munthu sangatenge HIV chifukwa

cholumidwa ndi udzudzu, kukumbatirana, kugawana chakudya kapena

kugwiritsa ntchito chimbudzi chimodzi.

Chochita 1A: Moto Olusa

Cholinga

• Kuti ophunzira adziwe m’mene HIV komanso matenda ena obwera kamba ka kugonana

angafalikire.

• Kuwonetsa kuti nkhani ya HIV ndi yofunika kukambirana chifukwa zotsatira zake

n’zokhudza miyoyo yathuyi.

Kukonzekera

M’chochita ichi kupatsana chanza kukusonyeza mchitidwe wogonana popanda chitetezo ngati

njira imodzi imene imafalitsa kachilombo ka HIV. Ili ndi gawo limene liyenera kuwapangitsa

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

1

anthu kuti ayambe kukambirana za kafalidwe ka HIV ndi m’mene kachilomboka kakhoza

kuwonongera miyoyo yawo. Pemphani anthu awiri amene akuphunzitsa kapena amene

akuphunzira amene angafune kuti atsogolere monga anthu awiri otsegulira gawo la “kukhala

moyo ndi kachilombo ka HIV.”

Chochitachi chitenga mphindi 10 kapena 15.

Chochitachi chikugwirizana bwanji ndi zochita zina?

Chochita ichi chidzapangitsa ophunzira kuganizira mozama nkhani ya kuyezetsa magazi

mwakufuna kwawo, ndipo izi zikhoza kugwirizana ndi chochita 5D: Kupereka uphungu ndi

kuyezetsa magazi mosaumirizidwa.

Kachitidwe kake

1. Uzani ophunzira za zokambirana

Musanayambe uzani ophunzira za zokambirana pogwiritsa ntchito ndondomeko ya pa tsamba

xv: Kutsogolera zokambirana mu gawo la Malangizo kwa ophunzitsa.

2. Kugwirana chanza

Onetsani njira yosangalatsa yomwe mungaperekere moni kwa munthu wina. Mwachitsanzo:

Gwirani mphuno yanu ndi dzanja

lanu la manzere, kenaka ikani

dzanja lanu la manja mopingasa

kudzera pa m’pata womwe

wapangika ndi dzanja manzere lija

ndi kupatsa chanza nzanu yemwe

wachitanso chimodzimodzi,

monga mukuonera pa

chithunzichi:

Chithunzi 3: Chithunzichi

chikuonetsa m’mene okonza

bukhuli adayeserera chochitachi

pa zokambirana zomwe zidachitika

pa msika wa pa Mikute (Kambiri

Turn Off) ku Salima.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

2

3. Zungulirani bwalo

Funsani ophunzira kuyenda momasuka kuzungulira bwalo ndi kupatsa moni anthu enanso

okwanira atatu pogwiritsa ntchito moni watsopanoyu. Atamaliza kugwirana chanza ayenera

kubwelera kumbuyo kwa bwalo lophunzilirapoli.

4. Tanthauzirani chochitachi

Funsani anthu awiri odzipereka kubwera kutsogolo kwa bwaloli. Fotokozani kuti mu

masewerawa anthuwa tiwayerekeza kuti ali ndi HIV. Kenaka funsani omwe anagwirana

chanza ndi anthuwa kuti nawonso abwere kutsogolo.

Fotokozani kuti:

“Mu masewerowa, kugwirana chanza kwa njira imeneyi kukuyimira kugonana opanda chitetezo

ndi munthuyu komwe kungapangitse kutenga kachilombo ka HIV. Choncho aliyense yemwe

anagwirana chanza ndi anthuwa akhoza kutenga kachilomboka.”

Funsaninso omwe atsalira kumbuyo kwa bwaloli omwe anagwirana chanza ndi anthu omwe

angobwera kutsogolo kwa bwaloli kuti nawonso abwere kutsogolo. Fotokozerani kuti malingana

ndi chochitachi nawonso ali pam’ndandanda wa anthu omwe akhoza kutenga kachilombo ka

HIV. Pa nthawiyi ambiri ngati si onse ayenera kukhala atayima kutsogolo kwa bwaloli.

Funsani ndi kukambirana, molingana ndi chochitachi:

Ndi anthu angati omwe anali kale ndi kachilombo ka HIV?

Ndi angati tsopano omwe ali pangozi yotenga kachilomboka?

Kodi izi zikutiwuza chiyani pa za momwe HIV ingafalire m’dera lathu?

Pitirizani kufotokoza motere:

“Molingana ndi seweroli, mchitidwe ogonana omwe mwakhala nawo wakuikani pa ngozi

yotenga kachilombo ka HIV. Munthu siungadziwe kuti watenga kachirombo ka HIV nthawi

iliyonse yomwe wagonana ndi wina popanda chitetezo. Njira yokhayo mungathe kudziwira ndi

kudzera m’kuyezetsa magazi.”

Chochitachi chitha kukuthandizani kukambirananso zokhudza kulandira uphungu ndi kuyezetsa

magazi mosaumirizidwa. Onani Kulandira uphungu ndi kuyezetsa magazi mosaumirizidwa

omwe uli m’gawo la Zowonjera 1 kumapeto a bukhuli.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

3

Chochita 1B: Ndani ali ndi kachilombo ka HIV?

Cholinga

• Kufuna kukambirana za kuweruza komanso maganizo olakwika oti ndani ali ndi HIV

kapena alibe.

• Kufotokozera kuti maonekedwe a thupi sichizindikiro chodalirika pofuna kudziwa za

HIV.

• Kufuna kuthandiza anthu kuti amvetse bwino za nkhani za anthu omwe ali ndi HIV ndi

kutanthauza kwa kukhala m’chiyembekezo ndi HIV ndi Edzi.

• Kulimbikitsa ophunzira kupita kukayezetsa magazi kuti adziwe za moyo wawo

okhudzana ndi HIV.

Kukonzekera

Werengani ndi kudziwa bwino nkhani za anthu osiyanasiyana omwe ali pa zithunzi zomwe

mugwiritse ntchito.

Sankhani zithunzi za anthu omwe ananena poyera ndipo akukhala momasuka ndi HIV, chithunzi

chilichonse chikhale pa pepala la A4 ndi nkhani zawo.

Ngati nkotheka, funsani munthu yemwe ali ndi HIV kuti akhale nanu pa zokambiranazi, ndipo

perekani ndi kuyankha mafunso kuchokera kwa ophunzira anu. Onetsetsani kuti munthuyu

akhale wathanzi komanso amene akukhala momasuka ndi HIV.

Chochitachi chitenga mphindi 60 (kapena 90 ngati pali munthu yemwe ali ndi HIV kuti

alankhule)

Chochitachi chikugwirizana bwanji ndi zochita zina?

Chochitachi chikugwirizana ndi kafotokozedwe ka chochita 1C: Chimachitika ndi chiyani

m’thupi la munthu amene ali ndi HIV kapena ayi? Chochitachi chikugwirizananso ndi chochita

2B: Kuwoloka pa Timilato kwa anthu amene ali ndi HIV, chochita 5D: Kuyezetsa magazi ndi

kulandira uphungu mosaumirizidwa ndi chochita 5E: Zinthu zomwe anthu amene ali ndi HIV,

odwala Edzi, mabanja ngakhalenso anansi awo ayenera kudziwa ndi kuchita.

Kachitidwe kake

Ophunzira asankhe yemwe akuganizira kuti ali ndi HIV kapena ayi kuchokera pa zithunzi

zosiyanasiyana (zosakanizidwa kutengera mtundu, msinkhu ndi ngati ndi mkazi kapena

mwamuna). Zifukwa za kusankha kwawo zikambidwe mtsogoleri asanalongosole za mbiri zawo

ndi kuwatsimikizira kuti anthu onse ali pa zithunzizo ananena poyera ndipo amakhala momasuka

ndi HIV.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

4

1. Sankhani chithunzi cha amene mukuganiza kuti ali ndi HIV kapena ayi.

Sankhani ndi kuyala zithunzi za

anthu amene ananena poyera kuti

ali ndi HIV ndipo amakhala

momasuka: (monga mukuonera pa

chithunzi 4), kapena patsani

ophunzira ena kuti anyamule

chithunzi chimodzichimodzi

ndikuti aliyense athe kuona

bwinobwino. Funsani ophunzira

kuti aloze anthu omwe ali ndi HIV

ndinso omwe akuganizira kuti

alibe HIV. Afunseni kuti achotse

zithunzi za anthu omwe

akuganizira kuti ali ndi HIV ndi

kuziika pambali komanso za anthu

omwe alibe ndi kuziika mbali ina

ndi kusiya pakati zithunzi zomwe

sakudziwa mbali yake yeni yeni.

2. Zokambirana

Chithunzi 4: Ophunzira akuyang’ana zithunzi

zomwe zayalidwa.

Funsani ophunzira kuti afotokoze

zifukwa zomwe asankhira

zithunzizo. Mwachitsanzo, ngati

wina anganene kuti ali ndi HIV

chifukwa choti akuwoneka

osasangalala: ayankheni powafunsa ngati munthu aliyense owoneka osasangalala ali ndi HIV. Izi

zimapangitsa ophunzira kuganizira za kuweruza ndi maganizo awo olakwika omwe ali nawo pa

nkhani ya HIV.

3. Mau kuchokera kwa munthu yemwe ali ndi HIV (muli ndi ufulu kuchita gawoli

kapena ayi)

Ngati muli ndi munthu yemwe ananena poyera kuti ali ndi HIV komanso okhala momasuka

angakhale ali ndi HIV yemwe ali okondwa kugawana za mbiri ya moyo wake ndi gulu lanu

muwonetseni kugululo. Mupatseni nthawi yoti awalankhule, ayankhe mafunso ndi kukambirana

nawo ophunzira anuwo.

4. Yalani zinthunzi ndi nkhani zake

Zokambirana zikatha, ikani pamodzi zithunzi za nkhani zija za anthu amene ali muzithunziwo

kuti ophunzira aone komanso awerenge nkhanizo paokha ngati nthawi ilipo.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

5

Chochita 1C: Chimachitika ndi chiyani m’thupi la munthu amene

ali ndi HIV, Edzi kapena ayi?

Cholinga

• Kulongosola bwino kusiyana komwe kulipo pakati pa HIV ndi Edzi.

• Kufotokozera momveka chomwe chimamuchitikira munthu ndi chitetezo cha m’thupi

mwake ngati munthuyo ali ndi HIV ndi m’mene Edzi imayambira m’thupi la munthuyo.

• Kufotokozera kuti ndi zotheka kuti amene ali ndi HIV atha kuoneka wa thanzi kwambiri.

• Kufotokoza mosavuta ntchito ya ma ARV.

Kukonzekera

Chochitachi chimagwiritsa ntchito sewero ndi cholinga chofuna kufotokozera bwino za HIV,

Edzi, matenda opatsirana osiyanasiyana, komanso zomwe ma ARV amachita. Inu monga

mtsogoleri kapena owerenga, muyenera kupeza anthu anayi, kapena asanu kuti akuthandizeni

(kuphatikizapo ena mwa ophunzira anu), amene ayenera kutenga mbali ya asilikali a chitetezo

cha m’thupi, HIV, matenda ena, ndinso ARV.

Muchochitachi otenga mbali ayenera kusonyeza mbali yoimira thupi la munthu ndi kuchita

zinthu zosiyana potsatira izi.

1. M’thupi musadalowe tizilombo

Chitetezo cha mthupi (asirikali a m’thupi) ndi cha mphamvu komanso chimatha kulimbana ndi

matenda ali wonse.

2. Kukhala ndi HIV, popanda zizindikiro

HIV ikalowa m’thupi, asirikali achitetezso cha mthupi amagwira ndi kukankhira HIV pa kona.

Asirikaliwa akadali ndi mphamvu zakutha kulimbana ndi matenda ena monga malungo.

3. Kukhala ndi Edzi/ kulandira chithandizo cha mankhwala a ARV

HIV imafoola asirikali achitetezo cha thupi ndi kulola matenda osiyanasiyana kulowa m’thupi la

munthu.

Mankhwala a ARV akafika amathandiza asirikali kukhalanso ndi mphamvu ndipo amatha

kulimbana ndi matenda osiyanasiyana monga m’mene mukuonera pa chithunzi 5.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

6

Werengani kachitidwe kake ka chochitachi m’munsimu ndipo pangani ndondomeko ya momwe

mungaphunzitsire mu chilankhulo chomveka bwino, ndi chovomerezeka ndi gulu lanu.

Ngati muli ndi okuthandizani kuphunzitsa funsani m’modzi kepana awiri kuti atenge mbali

zofunikira kwambiri muchochitachi monga asirikali achitetezo cha thupi ndi HIV.

Pangani zobisira nkhope kapena zizindikiro zoyimira mbali imene munthu akuchita (izi mukhoza

kuchita kapena ayi).

Muchochitachi mugwiritsa ntchito Timilato tija, kapena chiri chonse chomwe mungayikire

malire a m’thupi monga kulemba pansi ndi mtengo kapena choko.

Chochitachi chitenga mphindi 15 kapena 30.

Chithunzi 5: Ma ARVs amathandiza msirikali wa m’thupi kukhalanso ndi

mphamvu zolimbana ndi matenda osyanasiyana

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

7

Kachitidwe kake

1. Konzani malo amene azifanizidwa ngati thupi la munthu

Konzani kapena jambulani bwalo lokwanira mamitala awiri mopingasa pogwiritsa ntchito

timitengo, zingwe, kapena choko.

2. Gawirani ntchito kwa anthu omwe apange seweroli

Funsani anthu asanu odzipereka kuti akuthandizeni kupanga sewero lanu (kuphatikizapo

okuthandizani kuphunzitsa aja). Perekani ntchito zosiyana kwa wina aliyense. Onetsetsani kuti

munthu yemwe akhale msirikali wachitetezo chathupi akhale wamtali ndi wamphamvu kuposa

onse pagulupo.

3. Pangani sewero lanu

Gwiritsani ntchito maganizo omwe ali kumamzere kwa bokosi liri pa tsamba lotsatirali, kapena

fotokozerani nkhaniyi m’mene mungakondere. Onetsetsani kuti opanga sewero akuonetsa

zomwe inu mukunena pochita zomwe zalembedwa kumanja kwa bokosiri. Pumani kwa mphindi

zingapo mukamaliza chigawo choyamba ndi kuyamba gawo lina pofuna kuonetsa kusiyana.

4. Mafunso ndi zokambirana

Athokozeni omwe amachita sewero ndipo funsani anthu kuti awawombere m’manja. Mufunse

ngati anthu ali ndi mafunso kapena zokamba pa sewereroli. Muwawuze kuti zithunzi zonse

zomwe anaziwona mu chochita 1B: Ndani ali ndi kachilombo ka HIV? ndi za wanthu amene ali

ndi kachilombo koyambitsa a matenda a Edzi.

Chochitachi chitha kulumikizana ndi Gawo Lachisanu: Zochitika pa njira yaku Chilumba cha

Tsogolo. M’gawoli muli zochitika zimene zikukhudza anthu amene ali ndi HIV komanso Edzi.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

8

Zomwe Aphunzitsi ayenera kunena Zomwe opanga seweroli ayenera kuchita

Gawo loyamba: asanatenge kachilombo koyambitsa matenda a Edzi

Mkati mwa bwalo ili mukuimira munthu wa thupi la thanzi. Msirikali wa chitetezo cha m’thupi kulowa

M’thupi limeneri muli mazanamazana a asirikali achitetezo m’bwalo, pa malo pakonzedwa kuti palowe

chathupi a pakati pa 600 kapena 1000 pa dontho liri lonse la m’malo mwa thupi la munthu paja.

magazi. Ntchito ya asirikaliwa ndi kuteteza komanso Akudzigwedezagwedeza, kuwoneka

kulimbana ndi matenda aliwonse olowa m’thupi la munthuyi. wadzimphamvu, wankhongono ndipo wayima

Iyi ndi mbali ya chitetezo cha thupi. Tiyeni timulandire

msirikaliyu ndi m’manja.

ngati chimunthu cha ndewu.

Ndichachidziwikire kuti asirikali a chitetezo cha mu thupi Kachilombo kulowa m’thupi. Msirikali wa

ndi amphamvu ndipo akhoza kulimbana ndi nthenda iri chitetezo cha m’thupi kulimbana ndi kachilombo

yonse imene ingabwere m’thupi la munthu. Onani

kachilombo koyambitsa kutsegula m’mimba ndi mphere

kakulowa m’thupi.

kaja ndi kukatulutsa kunja kwa thupi.

Pano tikuwonanso kachilombo kena koyambitsa matenda, Kachilombo kena kulowa m’thupi. Msirikali

mwina TB.

wachitetezo atamenyana nako kwa kanthawi

wakagonjetsa nkukaponyera kunja kwa thupi.

Chitetezo cha m’thupi ndi chokwanira kuthana ndi matenda Msirikali uja wachitetezoyu,

wamba ndi kuwagonjetsa mwamsanga.

nkudzigwedezagwedeza kuwonetsa ukali wake.

Gawo lachiwiri: Kukhala ndi HIV m’thupi mwako popanda zizindikiro.

Tsiku lina HIV yalowa m’thupi. Nthawi zambiri imalowa HIV yalowa m’thupi ndi kuyamba kulimbana ndi

kudzera m’kugonana opanda chitetezo, pamene munthu msirikali wa chitetezo cha thupi. Msirikaliyo

agonana ndi munthu amene ali ndi kachilomboka. Msirikali wakankhira HIV mbali imodzi kukona kwa thupi

wa chitetezo kumenyana nayo HIV ndikuyikankhira pakona.

Koma sangayigonjetseretu ndikuyipha.

ndipo wayikhazika pansi HIV.

Pamene asirikaliwa akhazika pansi HIV sikuti asiya Matenda alowa m’thupi ndipo msirikali wa

kumenya nkhondo ndi tizilombo tina tobwera mu thupi. chitetezo cha thupi uja walimbana nawo

Asirikaliwa akhoza kumenya nkhondo imeneyi kwa zaka

zambiri. Nthawi zambiri zimakhala zaka zokwanira zisanu

kapena khumi, nthawi zina zimatha kufika ngakhale zaka 20.

Kudya bwino, kukhala osadandawula, kumakhala ndi

chiyembeke zokomanso kumwa ma ARV zimathandiza kuti

ukhale moyo wawutali. Anthu ena pang’ono amene ali ndi

HIV mwina sadzadwala matenda a Edzi.

ndikuwakankhira kunja. Matenda ena alowanso.

Gawo lachitatu: Kukhala ndi matenda a Edzi komanso kumwa ma ARV

Nthawi zambiri kachilombo ka HIV kaja kamayamba Kachilombo ka HIV kayimilira ndi kuyamba

kuchuluka mphamvu ndipo kamagonjetsa asirikali ambiri a kumenyana ndi msirikali wa m’thupi uja.

chitetezo cha mthupi ndikuwatenga monga akapolo ake. Kachilombo kaja kamugwira msirikaliyo

Zikatero ndiye kuti chitetezo cha mu thupi chimachepa. ndikumuyika manja ake onse kumbuyo kuti

asamenyenso nkhondo.

Ndiye matenda ena akalowanso m’thupi, asilikali aja Matenda alowa m’thupi ndipo akungovina,

amalephera kumenyana nawo. Chitetezo cha m’thupi kuyenda m’mene angafunire ndipo pa nthawi

chacheperatu ndipo matenda ali onse angalowe m’thupimu imeneyi msirikali wa mu thupi uja adakali

akhoza kutakasuka kwambiri. Chitetezo chacheperatu ndipo

thupi likhoza kudwala nthenda zosiyanasiyana. Imeneyi

ndiyo Edzi.

m’manja mwa HIV ndipo sangathe kuyenda.

Munthu ukuyenera kuti ukayezetse kuti udziwe ngati ukhoza ARV alowa m’thupi nkuyamba kumenyana ndi

kuyamba kumwa ma ARV. Ma ARV amachepetsa

HIV, msirikali anagwida uja wawomboledwa

chiwerengero cha tizilombo ta HIV m’thupi, koma sikuti ndipo HIV wakankhidwiranso kukona kuja.

mankhwalawa angaphe tizilomboti ayi. Ma ARV

Msirikali uja watenganso mphamvu zina ndipo

amapatsanso nyonga asirikali achitetezo aja kuti abwerere

ku nkhondo.

wayambiranso kuchita nkhondo.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

9

Chochita 1D: M’mene HIV ingafalire

Cholinga

Kufotokoza njira zosiyanasiyana m’mene HIV imafalira.

Kukonzekera

Zithunzi za pa makadi zosonyeza anthu amene ali ndi kachilombo ka HIV zija zidzagwiritsidwa

ntchito ndi cholinga chofuna kuthandiza kukambirana pa nkhaniyi.

Werengani Zowonjezera 1 gawo lomwe likunena za Kachilombo ka HIV koyambitsa matenda a

Edzi.

Zoti mugwiritse ntchito ndi makadi ndipo kuchokera pa makadi paja musankhepo:

• Mayi ndi bambo m’modzi owoneka a zaka zofanana

• Mayi woyembekezera

• Sing’anga

Chochitachi chitenga mphindi 10 kapena 15.

Chochitachi chikugwirizana bwanji ndi zochitika zina?

Chochitachi chikhoza kugwiritsidwa ntchito pamodzi ndi chochita 2A: Kuwoloka pa Timilato

kapena 4A: Kugwiritsa ntchito makadi ndi mabwato a Ulendo wa Chiyembekezo pofuna

kufotokozera khalidwe limene lingamugwetse munthu m’madzi momwe muli zinyama zolusa,

kapena limene lingamupangitse munthu kuwoloka bwinobwino.

Kachitidwe kake

1. Chimene chikhoza kumugwetsera munthu m’madzi kapena ayi

Mutenge makadi awiri pamene pali mzimayi ndi mzibambo owoneka a zaka zofanana ndipo

mufotokoze kuti:

Anthu awiri awa anakumana posachedwapa ndipo kachibwenzi kakukula ndithu pakati

pawo. Asadakumane, aliyense mwa iwowa adalinso ndi chibwenzi chomwe amagonana

nacho. M’modzi wa iwowa akhoza kukhala ndi tizilombo ta HIV.

Funsani kuti:

Ngati zinthu izi zitachitika, kodi anthu amenewa angapatsirane kachilombo ka HIV?

• Atabwerekana zometera

• Atagwirana manja kapena kukumbatirana

• Atapsyopsyonana

• Udzudzu utaluma uyo ali ndi HIV nkukalumanso wopandayo.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

10

• Mzimayiyo atachita ngozi nkukalandira magazi ochokera kwa munthu amene ali ndi HIV.

• Mkaziyo atayetsemulira ku nkhope kwa bamboyo.

• Atagonana pogwiritsa ntchito kondomu

• Atagwirizana kuti adzakhala okhulupirika kwa wina ndi nzake ndi kuti adzgonana

opanda kondomu.

• M’modzi mwa iwo ali ndi matenda opatsirana pogonana koma akumagananabe popanda

kondomu.

• Bamboyo atagonana ndi mkazi amene mwamuna wake adamwalira ndi cholinga chofuna

kuyeretsa mkaziyo komanso azimu (kulowa kufa).

2. Kutenga mimba ndi nkhani ya HIV

• Mutenge khadi pali chithunzi cha

mzimayi wapakati chija.

• Muwafunse ophunzira kuti:

Ngati mayiyu ali ndi kachilombo koyambitsa

matenda a Edzi, munganenepo chiyani za

mwana yemwe akumuyembekezerayo?

Chithunzi 6: Mayi Wapakati Chithunzi 7: Singa’nga

3. Kubwerekana malezala ndi masingano

• Onetsani chithunzi cha sing’anga.

• Muwafunse ophunzira:

• Kodi atapita kwa sing’anga uyu, amene amagwiritsa ntchito maleza podzicheka,

ngakhalenso pocheka anzake mphini, akhoza kutenga kachilombo ka HIV?

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

11

Kodi chitetezo chilipo kapena ayi?

Zoti Aphunzitsi Adziwe

• Kugwiritsa ntchito limodzi zinthu ngati masupuni, makapu ndi zina za

kukhitchini. Chitetezo chilipo.

• Atagwirana manja kapena kukumbatirana. Chitetezo chilipo.

• Atapsopsonana. Chitetezo chilipo.

• Udzudzu utaluma uyo ali ndi HIV nkukalumanso wopandayo. Chitetezo

chilipo. Udzudzu ukakuluma umakuthira malovu amene amakhala ndi

kachilombo koyambitsa malungo. Udzudzu siuthira magazi amene amakhala

ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi.

• Mkaziyo atayetsemulira ku nkhope kwa mzibamboyo. Chitetezo chilipo.

• Atagonana pogwiritsa ntchito kondomu. Chitetezo chilipo.

• Atagwirizana kuti adzakhala okhulupirika kwa wina ndi mzake ndikuti

adzigonana opanda makondomu. Chitetezo palibe pokhapokha atakayesetsa

magazi awo.

• M’modzi mwa iwo ali ndi matenda opatsirana pogonana koma akumagonanabe

popanda kondomu. Chitetezo palibiretu, munthu akatenga matenda

opatsirana pogonana ndi chitsimikizo chakuti mwina adatenga kachilombo

koyambitsa matenda a Edzi. Matenda oterowo amabweretsanso tizilonda

kumaliseche ndipo izi zimapangitsa kuti pakhale mwayi wawukulu wakuti

kachilombo ka HIV kalowe m’thupi la munthu.

Mayi wapakati kupatsira mwana wake wakhanda.

• Kamwana ka khanda kakhoza kutenga kachilombo koyambitsa matenda a Edzi kwa

mayi ake kakadali m’mimba, kapena pobadwa, kapenanso kudzera mu mkaka wa

m’maere. Koma ndi ana atatu okha mwa ana khumi amene angatenge kachilombo

koyambitsa matendawa kwa kholo lawo. Izi zikhoza kuchepetsedwa ngati mayi wa

mwanayo angamalandire mankhwala okhudza HIV pa nthawi imene ali ndi pakati

komanso pamene mwanayo akubadwa.

Chitetezo kumatendawa pamene upita kwa asing’anga.

Popita kwa sing’anga muzitenga lezala lanulanu. Nthawi zina asing’anga amatema mphini pa

thupi la munthu.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

12

Zoti Aphunzisti Adziwe

Miyambo ina imene ikuwonjezera kuti kachilombo ka HIV kafalikire.

Pali miyambo ina imene ikupititsa patsogolo kufala kwa kachilombo ka HIV. Miyamboyo ndi

monga iyi.

ChokoloKulowa kufa. Kugonana ndi namfedwa wa mkazi mamuna wake atangomwalira

chakumene ndi cholinga chomuchotsera mizimu.

Kulowa mu uvuni. Izi zikuchulukirachulukira tsopano. Anthu amakhulupilira kuti

akamawotcha njerwa akuyenera kuti agonane ndi atsikana pa usiku umene akuwotcha

njerwawo ndi cholinga chakuti njerwazo zipse bwino.

Hlazi-kumupatsa mwamuna mng’ono wa mkazi wake ngati njira yomuthokozera kuti

akusamalira bwino mkazi wakeyo.

Fisi.

Magule awusiku. Awa ndi magule amene amavinidwa nthawi yachisangalalo. Anthu

amavina usiku onse. Magule ambiri otere amakhala owutsa mudyo ofuna kugonana ndipo

nthawi zambiri mowa umaphikidwa ndikumwedwa, zomwenso zimaonjezera kuti anthu akhale

osasamala.

Miyambo ina imene imapititsa patsogololo mchitidwe wa kugonana.

Mkazi sachepa.

Okawona nyanja anakawona ndi mvuu zomwe.

Mphongo ya chiwala sichepa.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

13

Mau Otsegulira

GAWO LACHIWIRI: Timilato

Uthenga wa m’mene tingapewere kutenga kachilombo koyambitsa matenda a Edzi komanso

matenda obwera kaamba kogonana ndi odziwika. Ndiyetu m’malo mongokambirana chabe za

nkhaniyi, m’gawo lino muli masewero osangalatsa zedi komanso osayiwalika. Masewerowa

akusonyeza m’mene tingapewere matenda opatsirana pogonana pogwiritsa ntchito njira zitatu

zodziwika zija: kudziletsa, kukhulupirika kapena kugwiritsa ntchito kondomu (kuwoloka pa

Timilato) kuti tisatenge HIV (kugwidwa ndi ng’ona) kuti tikafike bwino ku tsogolo lathu

(chilumba).

Uthenga Ofunika

• Munthu aliyense ali ndi udindo odziteteza komanso kuteteza ena ku

kachilombo ka HIV.

• Kachilombo ka HIV kamayambitsa matenda oopsya a Edzi omwe

pakali pano alibe mankhwala.

• Kusiya mchitidwe ogonana, kukhulupirika kwa bwenzi mmodzi,

mkazi kapena mwamuna wathu amene alibe kachilombo ka HIV

komanso kugwiritsa ntchito kondomu ndi njira zomwe

zingatithandize kudziteteza ku kachilombo ka HIV.

• Makolo akuyenera kukambirana ndi ana awo mosabisa zakufunikira

kodikira osagonana kufikira mwana atakhwima maganizo kuti

akhoza kupanga chisankho chopewa matendawa payekha.

• Anthu apabanja akuyenera kumasukirana pokambirana za m’mene

angadzitetezere komanso m’mene angatetezere ena ku kachilombo ka

HIV.

Aliyense amene amagonana ndi wina akuyenera kukambirana mosabisa komanso

mwatchutchutchu ndi bwenzi lakelo nkhani zokhudza HIV komanso Edzi.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

14

Chochita 2A: Kuwoloka pa Timilato

Cholinga

• Kuti tifotokoze bwinobwino za njira zimene ziripo zopewera kutenga kachilombo

komanso matenda opatsirana podzera m’kugonana.

• Kuwapatsa ophunzira chithunzithunzi chogwiritsa ntchito njira zitatu zija monga kupewa,

kukhulupirika kapena kugwiritsa ntchito kondomu popewa kachilombo ndicholinga

chakuti akhale ndi tsogolo labwino.

Kukonzekera

Mundimeyi ophunzira amayesera kuoloka

mtsinje pogwiritsa ntchito kamulatho kamodzi

kakang’ono kamene kamayimira kupewa

kugonana usadakwatiwe ndipo kutsogolo kwake

kukhala okhulupirika kwa mwamuna kapena

mkazi wako m’banja.

Timilatoti tiri pamwamba pa madzi omwe muli

ng'ona ndi nyama zina zolusa.

Ng'onazi zikuyerekezedwa ndi kachilombo ka

HIV komanso matenda opatsirana kudzera

m’kugonana.

Kwa omwe akulephera kuyenda pa kamlatho

kamodzi, kamlatho kena kamawonjezeredwa

pambali pa koyamba kaja (kamlathoka

kakuyimira kondomu) ndipo munthu amakhoza

kuwoloka bwinobwino

Zofunika pophunzitsa ndi izi:

• Timilato ta thabwa

• Zithunzi za ng’ona, njoka, mvuu komanso chilumba

• Chinsalu cha buluwu ngati mukufuna

• Malo okwanira osesa bwino ngakhale pa bwalo.

Chithinzi 8: Kamlatho kamodzi ndi

zilombo zolusa

Yeserani chochitachi ndipo muphunzire kupinda ndodo zatimilatoyi kuti musawononge lasitiki

wake.

Chochitachi chitenga mphindi 15 kapena 20.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

15

Chochitachi chikugwrizana bwanji ndi zochita zina?

Chochita cha m’gawo lino chikugwirizana

kwambiri ndi chochita cha m’gawo

lachinayi: Chilumba cha Tsogolo.

Komanso chigawochi chikugwirizana ndi

zokambidwa m’gawo lachisanu: Zochitika

m’jira ya ku Chilumba cha Tsogolo, lomwe

likukamba za zimene tingachite paulendo

wathu wa kuchilumba cha tsogolo.

Kachitidwe kake

1. Kukhazikitsa malo

Yalani chinsalu cha buluwu pansi

mozondotsa kuti ngalawa zikhale pansi.

Pamwamba pawoneke popanda kanthu.

Ngati pansi pali poyipa monga pali madzi

kapena matope musagwiritse ntchito

chinsaluchi monga momwe awonetsera mu

chithunzi 8.

Ikani zithunzi zolusa monga ng'ona, mvuu

ndi njoka pansi ngakhale pa chinsalu cha

buluwu.

Chithunzi 9: Kuwoloka pa ka mlatho kamodzi

Yalani pansi thabwa lokhala ndi utoto woyera mbali ina wabuluwu pakati pa zinyama zolusazo.

Ikani chithunzi cha chilumba kumapeto kwa thabwa limene liri ndi mtundu wabuluwu kapena

pansi (Onani chithunzi 8).

2. Kusonyeza kugwiritsa ntchito milato

Powawuza ophunzira za chochitachi, onetsetsani kuti mwawawuza mowapatsa chidwi.

Awuzeni motere:

Tiyeni tiyerekeze kuti patsogolo pathu pali mtsinje waukulu. Mu mtsinjemo muli ng'ona

komanso zilombo zina zolusa. Muyenera kuwoloka mtsinjewu pogwiritsa ntchito mulatho

uwu poyenda pang'onopang'ono kutsogoza phazi limodzi. Phazi lina litsalire pambuyo pa

chidendene cha phazi lomwe liri patsogolo. Pitirizani choncho mpaka mutaoloka'

Yambani mwasonyeza kuyenda pa kamlathoka inuyo kuyambira koyamba kwa thabwa loyeralo.

Mwadala dzigwetseni pa kamlathoka.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

16

3. Onetsani chizindikiro cha NDITHA!

Muwawuze ophunzira kuti munthu akakwaniritsa kuwoloka

mlatho onse akuyenera kumuthandiza kusangalala pokuwa kuti

“Nditha!” uku akusonyeza chizindikiro pokweza chala chawo

chachikulu.

4. Ophunzira ayese kuyenda pa timilato

Uzani ophunzira kuti, “Ine ndinalephera kuwoloka pa kamlathoka,

tsono amene akhoza kundiposa ine ndi yani?

Chithunzi 10: Chizindikiro cha “NDITHA!”

Uzani ophunzira amene akufuna kuti awoloke pa mlatho kuyambira kumene kuli mtundu woyera

kukalekeza kumene kuli mtundu wabuluwu.

Wina akakwaniritsa kuwoloka onse akuyenera kusangalala naye pamodzi pokuwa kuti

NDITHA!

5. Ophunzira amene analephera

kuwoloka pa kamulatho kamodzi

agwiritse ntchito timilato tiwiri.

Onse amene anadzipereka kuwoloka pa

timilatoti akamaliza, muwayamikire, maka

iwo amene anawoloka bwinobwino.

Olephera muwatsimikizire kuti asadandaule

pakuti muwonjezera mlatho wina kuti

awoloke bwino.

Muyike kathabwa kachikasu kaja pafupi ndi

kathabwa kena kaja ndipo timatabwato

titalikirane kwa phazi limodzi. Awonetseni

ophunzira m’mene angawolokere kukafika

kuchilumba pogwiritsa ntchito matabwa

onse awiri, kathabwa ka chikasu komanso

kamene kali ndi

mtundu woyera ndi wa buluwu kaja.

Chithunzi 11. Kuyenda pa Timilato

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

17

Amene anagwera m’madzi koyamba kaja, ayeserenso kachiwiri. Panopa amenewo akuyenera

kuti awoloke ndithu. Muwalimbikitse.

Munthu akawoloka bwinobwino onse akuyenera asangalale naye pamodzi pokuwa kuti

NDITHA! pamene ena akululutira ndi kuwomba m’manja.

6. Kukambirana tanthauzo la chochitachi komanso phunziro lake

Funsani ophunzira mafunso okhuza chochitachi. Munamva bwanji?

• Pamene munali pakati pa kamlatho?

• Pamene munawoloka bwinobwino?

• Pamene munalephera nkugwera m’madzi?

Mufotokozere zinthu izi:

Chilumba chija chikuyimira tsogolo labwino, lowala, komanso zinthu zimene inu mumazifuna

kuti mudzachite ndikukhala nazo mtsogolo. Kuyenda pa milato kuja kukusonyeza njira imene

inuyo mudzayendamo musadakafike ku tsogolo lanulo.

Funsani mafunso awa:

• Kodi mukuganiza kuti ng’ona, mvuu, komanso njoka zimene zinali m’madzi zija

zikuyimira chiyani?

Nyama zimenezi zikhoza kuyimira zinthu zambirimbiri zokhumudwitsa zimene munthu akhoza

kukumana nazo pamene m’moyo wake, zinthu monga matenda monga obwera kamba ka

kugonana komanso HIV.

Ophunzira wina akatchula kuti zilombo za m’madzizo zikhozanso kuyimira HIV kapena

matenda opatsirana pogonana mufunse funso lakuti:

• Kodi njira zimene munthu ungapewere HIV komanso matenda opatsirana pogonana ndi

monga ziti?

Ophunzira aja akakuwuzani njira zonse zitatu za m’mene munthu angapewere HIV komanso

matenda odza kamba kogonana, inuyo mufotokoze mwatsatanetsatane. (yang’anani zolembedwa

m’musimu):

• Kamlatho kamene kali ndi mtundu woyera komanso wabuluwu kuyimira kudziletsa,

osagonana kufikira utapeza banja (mtundu oyera) komanso kukhulupirika kwa mkazi

wako kapena mwamuna wako ukakhala m’banja (mtundu wabuluwu). Anthu ena

amakwaniritsa ndithu kukhala osagonana ndi munthu kufikira atalowa m’banja komanso

kukhulupirika akakhala m’banja kwa moyo wawo onse. Koma ambiri amalephera ndipo

amagwera m’madzi m’mene muli zilombo zolusa zija. Tsono kuti tisagwere m’madzimo

tikhoza kugwiritsa ntchito kamlatho kachiwiri kaja kachikasu kamene kakuyimira

kondomu.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

18

Pitirizani pofunsani mafunso awa:

• Zinatheka bwanji kuti muwoloke?

• Nanga izi zikutanthawuzanji ku moyo wathu wa tsiku ndi tsiku?

• Mwaphunzira chiyani?

Mutsogolere kukambirana pa mafunso ali pa mwambawa. Palinso maganizo ena pano akuti

mukhoza kuwonjezera ngati ophunzira akuvutika pokambiranapo.

7. Kugwiritsa ntchito chizindikiro cha NDITHA!

Pamene ophunzira akhala chete kukhala ngati akuganiza mozama, muwawuze kuti ayang’ane

m’mene nkhope za anzawo zikuwonekera.

Aliyense apange nawo chizindikiro cha NDITHA! Izi kawirikawiri zimabweretsa

chimwemwe komanso kumasuka pakati pa ophunzirawo pakuti zimawakumbutsa kuti ndi

zotheka kukafika pa chilumba chija.

Muwawuzenso ophunzira tsono kuti ayang’anenso nkhope za anzawo zija kuti awone

m’mene zasinthira.

Muwafunse ophunzira aja kuti anamva bwanji m’mene anakuwa kuti NDITHA!

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

19

Zokuthandizani kuti muwoloke bwino

Zoti Ophunzitsa Adziwe

• Nchofunika kuti pamene munthu afuna kuwoloka pa timilato, ayike mtima wake

pachilumba chimene akupitako. Ngati munthu akhala ndi nkhawa ndi

kumangolingalira za mavuto a m’moyo mwake akhoza kugwera m’madzi ndi

kugwidwa ndi ng'ona.

• Nkofunika kulimbikitsana powoloka pa timilatoti.

• Munthu akhoza kuwoloka mosavuta ngati atasiya katundu wake pansi komanso

kuchotsa nsapato. M’moyo mwathunso nthawi zina tiyenera kusintha makhalidwe athu

ena kuti tidziteteze. Mwachitsanzo, pali miyambo ina yamakolo athu monga mwambo

wa Chokolo, Kulowa kufa ndi ina yomwe tikamaitsatira tiyika miyoyo yathu pachiswe.

• Kusiya kuledzera - munthu woledzera komanso wogwiritsa ntchito mankhwala

ozunguza bongo monga chamba sangathe kuwoloka bwinobwino patimilathoti ndipo

akhoza kugwera m’madzi momwe muli ng'ona.

• Kathabwa kachikasu kakuimira njira yogwiritsa ntchito kondomu pamene tigonana ndi

anthu ena. Njira iyi ikhoza kuteteza munthu ku HIV.

• Anthu ambiri amanenadi kuti munthu kuti adziteteze ku kachilombo ka HIV, ayenera

kudziletsa, pokhala okhulupirika kwa bwenzi limodzi kapena kwa munthu amene tiri

naye pabanja. Alipodi anthu ena amene akhoza kutsatira njira izi mmoyo mwawo

onse. Koma alipo anthu ena amene sangathe kukwanitsa njira ziwiri zimenezi. Kwa

anthu oterewa, palibe njira ina yodzitetezera yoposa kugwiritsa ntchito kamlatho

kachikasu kamene kakuimira kondomu.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

20

Njira zitatu zopewera HIV

Kudziletsa

Zoti Aphunzitsi Adziwe

Uwu ndiye mlatho umene uli wotetezeka kwambiri kuposa yonse. Ndi njira yokhayi imene

munthu akhoza kukhala odzidalira kwathunthu kuti sangatenge kachilombo ka HIV kudzera

m’kugonana. Kwa ena, kudziletsa kapena kuti kupewa chiwerewere zimatanthawuza kuti

asakhale ndi chibwenzi. Ndi zotheka kukhala ndi chibwenzi koma osamagonana nacho.

Bwato limeneritu ndiye lotetezeka kwambiri. Mukhozatu kupsopsonana, kugwiranagwirana,

kaya kusisitana koma osagonana.

Kukhala okhulupirika kwa bwenzi limodzi limene liribe kachilombo komanso pabanja

Izi zimafunika abwenzi amene apanga chisankho chokhwima kuti sadzagonananso ndi wina

aliyense koma bwenzi lawolo limene liribe kachilombo. Ngati mukufuna kukwera bwato

limeneri choyamba ndikupita kaye kukayezetsa magazi ndipo muonetsetse kuti nonse mulibe

kachilombo koyambitsa matenda a Edzi. Ngati m’modzi wa inu adagonanapo ndi wina kapena

mwina adalandirako magazi kwa wena ndi zotheka kuti akhoza kukhala ndi kachilombo.

Mupite mukayezetse magazi anu komanso kulandira uphungu.

Kugwiritsa ntchito kondomu moyenerera nthawi imene mukugonana

Iyi ikhoza kukhala kondomu ya amuna kapena akazi. Kondomu yachimuna amavala ndi

amuna ndipo imatha kusunga umuna kuti usalowe mkati mwa chiwalo cha mkazi, kaya ndi

mkamwa kapena malo ochitira chimbudzi. Kondomu ya chikazi nayonso ndi yapulasitiki

ndipo imakhala ndi mkombero kumapeto kwake konse kuwiri. Imeneyi imalowetsedwa

kumaliseche kwa mkazi ndipo mkombero uja ndi umene umapangitsa kuti kondomuyo isavute

kukhala m’malo mwake.

Kondomu ya chikazi imapereka ufulu wambiri kwa amayi kuti agwiritse ntchito kondomu

kapena ayi? Kondomuyi imagwiritsidwa ntchito pofuna kupewa kupatsirana kachilombo ka

HIV, matenda opatsirana pogonana komanso kuteteza kutenga mimba. Njirayi ikhoza

kugwiritsidwa ntchito ndi anthu amene ali kale pa banja komanso amene angoyamba kumene

ubwenzi wawo.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

21

Chochita 2B: Kuwoloka pa Timilato kwa anthu omwe ali ndi HIV

Cholinga

• Kufuna kutsimikiza mfundo yonena kuti amene ali ndi kachilombo koyambitsa matenda

a Edzi akhoza kukhala ndi moyo nthawi yayitali komanso mosangalala.

• Kufuna kutsimikiza mfundo yakuti tisaganizire kwambiri za mavuto amene tiri nawo,

m’malo mwake tiziganizira zinthu zomwe tikufuna tidzakwaniritse m’moyo mwathu.

• Kufuna kufufuza njira za m’mene tingathandizire anthu amene ali ndi kachilombo ka

HIV koyambitsa matenda a Edzi.

Kukonzekera

Chochitachi chimagwiritsa ntchito timilato tomwe tija koma mwa mtundu wina. Cholinga chake

ndi chofuna kupatsa maganizo anthu kuti akambirane zokhudza amene ali ndi kachilombo ka

HIV. Chochitachi chimasonyeza njira zimene achibale, anzake a munthu, kaya ogwira nawo

ntchito akhoza kusamalira munthu amene ali ndi kachilombo ka HIV kapena matenda a Edzi.

Muwerenge mbuku lotchedwa: Kukhala m’chiyembekezo ndi HIV ndi matenda a EDZI lomwe

liri m’phukusi la Chiyembekezo.

Zipangizo zofunika ndi: ng’ona, mvuu, njoka, timilato, komanso chilumba.

Chochitachi chitenga mphindi 10 kapena 20.

Chochitachi chikugwirizana bwanji ndi zochita zina?

Chochitachi chikugwirizana ndi chochita 5E: Zomwe anthu amene ali ndi HIV ndi odwala Edzi,

mabanja ngakhalenso anasi awo yenera kudziwa ndi kuchita.

Kachitidwe kake

1. Kuyenda pa timilato pamene uli ndi kachilombo ka HIV

Ikani kamlatho kamodzi ndipo ikani zilombo zolusa zija m’madzi. Awuzeni ophunzira kuti,

pamene mukuwoloka pa kamlathoka.

“Mudzidzitenga ngati kuti ndinu munthu m’modzi amene adapezeka ndi kachilombo ka

HIV. Ndipo mukutha kuwona zipsinjo komanso zinthu zosawutsa mtima

zitakuzungulirani. Popeza muli ndi kachilombo koyambitsa Edzika ndiye kuti basi

mumwalira, choncho ndiye kuti tsogolo lanu mwalitaya basi. Kodi mavuto amene anthu

amene ali ndi kachilombo amakumana nawo ndi monga ati?”

Anthu akhoza kumatchula zinthu monga kusalidwa, kukanidwa ndi achibale, anzako, ndi zina

zambiri.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

22

2. Kuthandiza munthu amene ali ndi HIV

Funsani:

Kodi anthu ena angamuthandize bwanji munthu yemwe ali ndi HIV?

Ngati wina apereka ganizo lakuti munthu ali ndi kachilomboyu athandizike, inuyo mufunse

amene ali omasuka kukuthandizani kuwoloka pa kamlathoka.

Muwonetse m’mene angakuthandizireni kuwoloka kamlathoka powuza ena kuti akugwireni

dzanja, kaya ndi m’mapewa kuti muwoloke bwino mlathowu. Pamene muwoloka muwauze

ophunzira kuti tsopano chilumba chakutsogolo chija mukutha kuchiwonanso ndipo muuze wina

kuti ayike chilumbacho kutsogolo kwa mtsinje pothera pa kamlathopo.

Mukambiranebe njira zimene mukhoza kuthandizira munthu amene ali ndi kachilombo ka HIV

koyambitsa matenda a Edzi ndi njira zina za m’mene mungam’thandizire.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

23

GAWO LACHITATU: Chilumba cha Tsogolo

Mau Otsegulira

Kuti munthu apange chinthu monga kusintha khalidwe ndi chinthu chofunikira kwambiri kuti

iyeyo awone payekha kuti nkofunikira kutero. Munthu amasintha khalidwe akawona kuti

m’kusintha khalidwelo muli phindu monga tsogolo labwino. Tsono gawo ili lithandiza

ophunzira kuti akhale ndi masomphenya a tsogolo lawo. Gawoli likatero lipangitsa achinyamata

ndi anthu ena aja kuti aunikire moyo wawo ndi kuwona ngati zimene akuchita pakali pano

pokhudzana ndi nkhani yogonana zingawapatse tsogolo labwino.

Uthenga Ofunika

• Munthu aliyense aganizire moyo wabwino umene akufuna adzakhale

nawo mtsogolo.

• Pali chiyembekezo cha tsogolo labwino ngati munthu apanga chisankho

chogwiritsa ntchito mabwato achitetezo omwe akuyimira kudziletsa,

kukhulupirika m’banja kapena pa ubwenzi ngakhalenso kugwiritsa

ntchito kondomu

• Ndi chinthu chofunikira komanso cha phindu kuti anthu amene ali ndi

HIV aziganizira za tsogolo lawo ndi zimene akuzifuna m’moyo mwawo

osati azingoganizira za imfa kapena mavuto ena.

Chochita 3A: Chilumba cha Tsogolo

Cholinga

Kuthandiza ophunzira kuti:

• Aganizire za moyo wawo wa m’tsogolo.

• Aganizire za njira zopewera kachilombo koyambitsa matenda a Edzi zimene zikhoza

kuwathandiza kuti adzafike bwino kutsogolo limene akulifunalo.

Kukonzekera

Ophunzira aliyense aganizire za chilumba cha tsogolo lake, m’mene akufunira kuti moyo wake

udzakhalire mtsogolo. Ayike mtima pa chilumba cha tsogolo lakecho ndipo aganizire za njira

zopewera kachilombo, (kukhalabe pa timilato, kapena m’mabwato a chitetezo aja) ndi cholinga

chakuti akafike bwino pa chilumba cha tsogolo lake. Ganizirani komanso konzekerani za

chitsanzo chimene mungapereke cha chilumba chanu cha tsogolo.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

24

Onetsetsani kuti chilumba chanucho chikhale choona ndi kuti mutha kuchikwaniritsa. Izi ndi

zothandiza kuti phunziroli likhale la tanthauzo osati zongosewera ayi.

Zipangizo zofunika ndi izi:

• Timakadi tankhani

• Timilato ta thabwa

• Chilumba, ng’ona, mvuu ndi njoka

• Khadi la nkhani ya Fatsa ndi makadi ena amene mungagwiritse ntchito

• Chithunzi cha malo amene Fatsa amachitirapo bisinesi yake

• Chithunzi cha nyumba ndi banja la Fatsa

• Mapepala osalembedwa

• Zolembera

Chochitachi chitenga mphindi 30 kapena 45.

Chochitachi chikugwirizana bwanji ndi zochita zina?

Chochitachi chikhoza kukhala chopambana ndithu ngati chigwirizana ndi zochita za m’gawo

lachiwiri monga chochita 2A: Kuwoloka pa Timilato kapena 2B: Kuwoloka pa Timilato kwa

anthu amene ali ndi HIV. Chikhozanso kulumikizana ndi gawo lachinayi: Mabwato a Ulendo wa

Chiyembekezo.

Kachitidwe kake

1. Konzani malo

Ikani timilato tonse tiwiri pansi ndi zilombo zolusa zija (ng’ona, njoka ndi mvuu) komanso

chilumba cha tsogolo pothera pa timilatoti. Onetsetsani kuti chilumba chili kumapeto kwa mbali

ya buluwu kwa kathabwa ka mitundu iwiri kaja monga zawonetsedwa pa chithunzi 11.

2. Zimene mukuyenera kuganizirapo kwambiri powoloka milatoyi

Funsani ophunzira:

“Kodi pamene mumawoloka pa timilato paja chimene chinakuthandizani kuti

muwoloke bwino ndi chiyani?

Anthu ambiri amawoloka bwino ngati ayika maso awo pa chilumba chimene chili patsogolo pa

timilato chija. Akamayang’ana zilombo zimene ziri m’madzi zija amatha kugweramo.

Ophunzira akayankha muwawuze kuti:

“Mavuto osiyanasiyana omwe tingakumane nawo m’moyo mwathu asatipangitse kugonja

ndi kuiwaliratu za tsogolo lathu. Poyamba tidzikumbutse kawirikawiri za tsogolo lathu

kotero kuti tsogolo lathulo litipatse mphamvu zolimbana ndi mavuto omwe

angatilepheretse kukwaniritsa tsogolo lathulo.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

25

3. Perekani chitsanzo cha chilumba cha tsogolo

Mupereke chitsanzo chogwira mtima chimene munthu akhoza kukhala nacho cha tsogolo lake.

Ichi chikhoza kukhala:

a. Chitsanzo chochokera kwa inu aphunzitsi

Kufotokoza mothandizidwa ndi chithunzi chimene mwajambula chokhudzana ndi tsogolo lanu

m’mene mukufuna kuti lidzakhalire. Mufotokoze za tsogololo ngati kuti mwafikako kale,

mwachitsanzo: “Pano tsopano ndi chaka cha …... Ndiri okondwa kwambiri chifukwa cha zinthu

zomwe ndakwaniritsa. Ndine wamphamvu, wathanzi ndi osangalala m’moyo mwanga. Ndiponso

zinthu zikundiyendera kwambiri”.

b. Chitsanzo cha Fatsa ndi chilumba cha tsogolo lake

Fotokozani nkhani ya Fatsa kuchokera pa khadi paja

motere:

"Fatsa amakhala ndi makolo ake pamodzinso ndi

achimwene ndi achemwali ake. Makolo ake

akhala akuvutika kusamalira anawa ndiponso

kuwalipirira sukulu. Fatsa ali ndi chibwenzi ndipo

mnyamatayu dzina lake ndi Sewa. Sewa

amachokera kubanja losauka ndipo amalandira

ndalama zochepa. Pakati pa Fatsa ndi Sewa

palibe vuto lina lirilonse. Awiriwa agwirizana

kuti asayambe msanga kugonana koma iwo

amasangalala kukhalira limodzi nthawi zambiri,

kumacheza ndi kuseka".

Funsani ophunzira:

Kodi Fatsa akugwiritsa ntchito kamlatho kati?

Chithunzi 12: Fatsa

Pitirizani kufotokoza za Fatsa motere:

“Mayi a Fatsa akhala akudandaula kuti mtsikanayo sabweretsa ndalama ku

nyumba. Fatsa amazindikira kuti anzake amene amayenda ndi a chidyamakanda

amavala momuposa iye. Tsiku lina akuyenda chidyamakanda china chotchedwa Selo

chinaimika galimoto pafupi ndi Fatsa nkumuuza iye kuti am’patsa ndalama ngati

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

26

avomera kuti apite limodzi koyenda. Fatsa anakana izi monga momwe amachitira

m’mbuyo monsemu.

Fatsa amadziwa kuti kachilombo ka HIV ndikopatsirana pogonana ndipo anamva kuti

achidyamakanda ambiri amakana kugwiritsa ntchito kondomu, pogonana. Komabe Fatsa

watopa ndi umphawi akufuna kuthandiza makolo ndi abale ake ndiponso akufuna kugula

zovala zatsopano. Tsono iye akuganiza kuti mwina angoyesa kamodzi kokha.

Fatsa watsala pang’ono kulowa m’galimoto la Selo zomwe zotsatira zake zikakhale

kugonana kosadzitchinjiriza.”

Uzani ophunzira kuti:

Fatsa mu nkhaniyi watsala pang’ono kulumphira m’madzi momwe muli zoopsya zosiyanasiyana

monga ng’ona, njoka ndi zina. Atangotsala pang’ono kulowa m’galimoto lija masomphenya a

chilumba cha tsogolo lake anam’bwerera. Lozani chilumba chomwe chiri ku tsogolo kwa

timilato.

Onetsani ophunzira chinthunzi cha Fatsa ndi bizinesi yake ndipo chiikeni pa chilumba.

Pitirizani kufotokoza motere:

“Fatsa akuganiza ali ndi bizinesi yosoka zovala, iye m’maganizo mwake akuyiwona

bisinesiyi italembedwa. “Fatsa

Fashion Clothing” mwiniwake:

Fatsa Mwali. Iye m’maganizo

mwake, akuwonanso anthu

akumuyamikira kuti amasoka zovala

zabwino. Iye akuwona bizinesiyi

ikumubweretsera ndalama

zokwanira kudzisamalira pamodzi

ndi banja lake, ndipo zina amatha

kutumizira makolo ake. Izi

zimamupangitsa Fatsa kukhala

wokondwa. Wamaliza ntchito yake

ndipo akupita kunyumba yake

imene iri kuseri kwa malo ake a

bisinesi. Pachilumba cha tsogolo

lakeri, iye tsopano ali pa banja

ndipo iye ndi mwamuna wake Sewa

ali ndi ana awiri okongola athanzi.”

C

h

Chithunzi

13: Fatsa ndi malo ake a bisinesi

Ikaninso chithunzi cha nyumba ndi banja la Fatsa pa chilumbachi.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

27

Pitirizani kufotokoza motere:

“Fatsa akuyang’ananso m’madzi, akuganizira za chilumba chake chosangalatsachi. Iye

akuganiza kuti ndi tsogolo labwino ngati limeneri sibwinonso kuyenda ndi

chidyamakanda pakuti chikhoza kumuwonongera tsogolo lake.

Akumuyang’ana Selo ndipo anamuuza kuti: "Ine ayi, ndikumva chisoni kuti ine

ndine mwana ndipo inu ndinu achikulire, msinkhu woyenera kukhala bambo anga.

Muzipita ndipo musadzandivutitsenso. Bambo uja wachita manyazi nachoka.”

Funsani mafunso awa:

• Fatsa amachokera kubanja losauka ndipo amafuna ndalama, kodi iye anatha bwanji kukana

ndalama za Selo?

• Kodi mukuganiza kuti chinampangitsa Fatsa kuganiza kuti bizinesi yake ikhoza kuyenda

bwino ngakhale asanaiyambe nchiyani?

• Nanga chimene iye angachite kuti zimene akufunazo, zokhala ndi bizinesi komanso banja

labwino, zidzatheke ndi chiyani?

Onetsani chithunzi 15: Njira yomwe Fatsa anadutsa kuti afike tsogolo lake. Ngati muli ndi

zithuzi zochulukirapo za Fatsa muwapatse ophunzirawa kuti awone.

Chithunzi 14: Nyumba ndi banja za mtsogolo za Fatsa

Mokondwa Fatsa adakamufotokozera mzake za chilumba cha tsogolo lake komanso za buzinesi

yake yosoka zovala.

“Nawenso ukhale nacho chilumba cha tsogolo lako.”

“Komatu ine zosokasokazi sindingazithe,” mzakeyo adatero.

“Zimenezo ndi za ine osati za iwe,” Fatsa adamuwuza mzakeyo, “ Iwe chilumba

chatsogolo lako sichingafanane ndi changa. Chako ndi chako, aliyense aziganizira za

chilumba chake pa iye yekha.”

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira

kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

28

Chithunzi 15: Njira yomwe Fatsa anadutsa kuti afike tsogolo lake

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira

kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

29

4. Ganizirani za m’mene mukufunira kuti tsogolo lanu lidzakhalire

Muwawuze ophunzira kuti akhale momasuka, kaya akhala chogona, kaya akhala pansi, koma

akhale motakasuka. Muwafotokozere mtima uli m’malo izi:

Aliyense wa inu akhoza kupanga tsogolo lake. Sindikudziwa kuti tsogolo lanu ndi lotani.

Aliyense atakasuke ndipo aganizire za m’mene akufunira kuti tsogolo lake lidzakhalire.

Mwina zikhoza kukuthandizani mukatseka maso. Muganizire tsogolo lanu ngati chilumba.

Chilumba chatsogolo lanu chikuyimira zinthu zimene inu mukufuna kuti mudzachite

m’tsogolo muno. Pa chilumba cha tsogolo lanuchi mukhoza kuyikapo chilichonse chimene

mukufuna komanso chimene mukuganiza kuti nchotheka. Muziziwona ngati zachitikadi,

mwafikadi kutsogoloko. Muli ndi thanzi ndipo zonse zikukuyenderani. Mukuwona chiyani?

Amene ali ndi inu ndi yani? Mukumva chiyani? Kodi nanga anthu ena akunena chiyani za

inu? Mukumva bwanji? Mukuchita chiyani pa nthawiyi? Nanga luso limene muli nalo pa

nthawiyi ndi lotani?Chofunikira kwambiri m’moyo mwanu ndi chiyani? Nanga pa chilumba

chimenechi inuyo ndinu yan?

5. Pezani chinthu choyimira tsogolo lanu

Patsani ophunzira aliyense pepala kuti ajambulepo chilumba cha tsogolo lake. Muwafotokozere

kuti simukufuna kuti iwo ajambule zokongola ngati sangathe. Chofunika kwambiri nchakuti

iwowo amvetsetse za chimene ajambulacho.

Omwe sangathe kujambula kapena amene alibe zojambulira akhoza kutenga chithu china

chilichonse monga mwala kuti chiyimire tsogolo lawo. Izi zichitike mu mphindi 15 kapena 20.

6. Kuchita sewero lokhudza chilumba cha tsogolo lanu

Muwawuze ophunzira kuti akhale motayana ndipo aganizire za chilumba cha tsogolo lawo.

Ayike mwala wawo kapena kalikonse kamene kakuyimira tsogolo lawo pakati pa malo amene

awapeza. Ngati akufuna akhoza kugwiritsa ntchito zinthu zina monga mpando kuti asonyeze

tsogolo lawo. Ndiye muwawuze ophunzirawo kuti ayendere anzawo kuti akamve kuti tsogolo la

anzawolo ndi lotani ndipo nawonso akuyenera kufotokozera anzawo za tsogolo lawo.

7. Kugawana ndi anzanu za tsogolo lanu komanso kukonzekera kuti mungakafikeko

bwanji ku tsogolo lanulo

Mufunse amene angathe kuti afotokozere gulu za tsogolo limene akulifuna ndipo azifotokoza

ngati kuti wafikako kale ku tsogololo.

Ngati ajambula chinthunzi awonetse gulu chithunzicho ndipo afotokozere. Muwawuze kuti

akayime ku tsogolo kumene mwayika chilumba kuja ndipo azifotokoza ngati kuti afika kale ku

tsogolo lawolo.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

30

Muwafunse kuti:

Kodi izi zikuchitika m’chaka chanji? Ndinu ndani? Mukuwona chiyani? Mukumva

chiyani? Mukumva bwanji m’thupi mwanu?

Muwauze ophunzirawo kuti asiye tsogolo lawolo kapena zizindikiro za tsogolo lawozo

kutsogolo kwa timilato pa chilumba chija ndipo abwere koyambirira kwa timilato kuja.

Muwauzenso kuti:

Tsopano tiri kuno, osatinso kutsogolo lanu lija. Tsogolo lathu lija ndi ilo liri ukolo ndipo

nditsogolodi labwino zedi. Aliyense aganizire ndi kudzifunsa mafunso awa:

• Kodi mlatho umene ine ndikugwiritsa ntchito kapena umene ndikuyenera kuti ndigwiritse

ntchito ndi uti?

• Nanga mlatho odalilika umene ungandithandize kuti ndifike kutsogolo langalo ndi uti?

• Chinthu choyamba chimene ine ndingapange lero kapena sabata ino chakuti

chindithandize kukafika ku tsogololi ndi chiyani?

Mufunse amene akufuna kuti awoloke pa timilato paja kupita ku tsogolo lawo. Akawoloka

bwinobwino aloleni kuti atenge chomwe chikuimira tsogolo lawo ndi kuchita chizindikiro cha

NDITHA!

Chitani izi ndi anthu angapo amene anatha kugawana ndi anzawo za tsogolo lawo.

8. Zilumba zowonjezera

Fotokozani:

Ngati chilumba chanu chikuwoneka kuti chiri kutali komanso chovuta kufikira, mukhoza kufuna

kupanga chilumba china chimene chiri pafupi nanu komanso chimene chikuwoneka chosavuta

kuchifikira. Ndi bwino kumakhalanso ndi zinthu zofuna zimene ukhoza kuzikwaniritsa

pasanapite nthawi yayitali. Mukafika pa chilumba chinacho, onetsetsani kuti mukupitiriza

ulendo opitanso kuchilumba china.

Muwafunse ophunzira kuti:

• Kodi chilumba chawo chapafupi ndi chotani?

• Nanga patha nthawi yayitali bwanji asadafikeko?

Muwawonetsenso chinthunzi cha Fatsa ndi njira zake pamene akuganizira za tsogolo lake

komanso bizinesi yake yosoka.

9. Kugwiritsitsa masomphenya komanso zilumba za tsogolo zolumikizana

Ophunzira asunge zizindikiro zimene zikuyimira tsogolo lawo. Mupereke maganizo awa kwa

ophunzira.

• Chojambula chanuchi mukachisunge kunyumba kuti chizikakukumbutsani za tsogolo

limene inu mukulifuna.

• Mukhoza kusintha chilumba chanu ngati mukufuna ndipo mukhozanso kuwonjezera

zilumba zina.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

31

• Mugawane maganizo a zilumba zanuzo ndi okondedwa anu. Mukambirane kuti mukhale

ndi chilumba chimodzi ngati nkosowekera kutero. Mukhozanso kukambirana ndi ana anu

kuti muwone m’mene mungawayikire pa chilumba chimenechi.

• Mufufuze chimene mukuyenera kuchita pofuna kufika pa chilumbacho ndipo

muyambepo kuchita zimenezo.

Zoti Aphunzitsi Adziwe

Mbukhu ka Ulendo wa Chiyembekezo, timafuna ophunzira kuti aganizire za tsogolo lawo ndi

m’mene iwo akufunira kuti lidzakhalire ndipo tsogololi timaliwonetsa ngati chilumba.

Zinthu zina zomwe zingathandize anthu kuyerekeza za chilumba chawo ndi izi:

• Kuyerekezaku kumayenda bwino ngati munthu wakhazikitsa mtima wake pansi.

Choncho uzani ophunzira kuti akhazikitse mitima yawo pansi akamayerekeza za

momwe zinthu zingakhalire ali pa chilumba cha tsogolo lawo.

• Inu ngati aphunzitsi mungathandize pofewetsa mau anu ndi kuyankhula mosafulumira

mukamaunikira anthuwa m’mene angayerekezere za chilumba cha tsogolo lawo.

• Mphunzitsiyo akhonzanso kuthandiza pofotokoza zonse ngati kuti zikuchitika tsopano:

Kodi mukumva bwanji mthupi lanu? Mukuwona chiyani? Mukununkhiza chiyani?

Nanga mukumva chiyani pa malopo?

• Funsani mafunso ofuna kudziwa zotsatira monga awa:

o Mukufuna mutachita chiyani?

o Pali njira zingati zokafikira kumeneko?

o Mwasowa chithandizo chanji?

o Chinthu choyambirira choti mupange panopa ndi chiyani?

Mafunso ngati amenewa amawathandiza ophunzira kuti ayike maso awo pa tsogolo.

Zimapatsanso anthu maganizo abwino akuti achitepo kanthu. Mafunso ngati awa ali bwino

pamene mukukambirana za HIV kapena matenda a Edzi. Mafunso otere ndi abwino kusiyana

ndi amene amakhazikika pa zovuta monga: “Vuto lanu ndi chiyani?” “Analinayambitsa

ndani?”

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

32

GAWO LACHINAYI: Mabwato a Ulendo wa

Chiyembekezo

Mau Otsegulira

Gawoli likuyamba ngati m’mene linayambira gawo lachiwiri la timilatho pogwiritsa ntchito

mabwato ndi cholinga chofuna kuwoloka bwino nyanja kapena mtsinje momwe muli nyama

zolusa zomwe zikuimira HIV. Zithunzi za pa makadi zija zigwiritsidwanso ntchito kuti anthu

akambirane nkhanizo mozama.

Uthenga Ofunika

• Kachilombo ka HIV kakufala kwambiri muno m’Malawi monga

madzi osefukira. Munthu aliyense amene sadziteteza akhoza

kutenga matenda opatsirana pogonana komanso kachilombo ka

HIV.

• Munthu akhoza kudziteteza kuti asatenge kachilombo ka HIV

pochita izi:

o Kudziletsa

o Kukhulupirika pokhala ndi mkazi kapena mwamuna

m’modzi ogonana naye amene alibe kachilomboka

o Kugwiritsa ntchito Kondomu. Izi ziri ngati kugwiritsa

ntchito mabwato atatu.

• Munthu akuyenera kuti apeze bwato limene akwere. Bwatolo

likhale lakuti munthuyo wasankha yekha osati kukakamizidwa

potengerana ndi chikhalidwe, chipembedzo, komanso m’mene

akhalira m’moyo mwake.

• Ngati munthu awona kuti sangakwanitse njira ina mwa njira zomwe

tatchulazi akhoza kusintha ndikutenga njira ina.

Chochita 4A: Kugwiritsa ntchito makadi ndi mabwato a Ulendo wa

Chiyembekezo

Cholinga

Kuthandiza ophunzira kuti akambirane momasuka zokhudza HIV zimene zikuwakhudza

komanso zimene zikukhudza dera lawo.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

33

Kukonzekera

Kufala kwa kachilombo koyambitsa matenda a Edzi m’Malawi muno kukufanizidwa ndi

kusefukira kwa madzi (nsalu ya mtundu wa buluwu) ndi nyama zolusa zomwe ziri momwemo

(mavuto a moyo uno kuphatikizapo HIV, Edzi ndi matenda opatsirana pogonana). Mabwato

atatuwa akuyimira kudziletsa, kukhulupirika ndi kugwiritsa ntchito kondomu. Ophunzira

azifotokoza nkhani ya munthu amene ali pa khadi ndipo aziyika khadilo akatha kufotokoza

nkhaniyo mu bwato kapena m’madzi malingana ndi nkhani ya munthuyo. Ngati nkhani ya

munthu wa pa khadi lina pali mavuto ophunzira akambirane kuti munthuyo angamuthandize

bwanji.

Musanayambe chilichonse, sankhani makadi apakati pa khumi ndi awiri kapena khumi ndi

asanu. Makadi osankhidwawa akhale a anthu amene ophunzira anu akhoza kuwadziwa msanga.

Mwachitsanzo mukhoza kuyikapo mzimayi wapakati ngati mukufuna kukambirana za m’mene

mwana wakhanda angatengere kachilombo koyambitsa matenda a Edzi kwa kholo lake.

Zofunika kugwiritsa ntchito ndi izi:

• Makadi a anthu osiyanasiyana

• Chinsalu cha buluwu

• Malo opachikapo chinsaluchi kapena kuyala

• Ng’ona, njoka komanso mvuu

Chochitachi chitenga mphindi 30.

Chochitachi chikugwirizana bwanji ndi zochita zina?

Zimene ophuzira angakambirane apa zikhoza kugwirizana ndi zomwe ziri m’gawo lachisanu la

Kukambirana kudzera m’zisudzo (Forum Theatre).

Kachitidwe kake

1. Kukhazikitsa malo

Fotokozani:

“Nthano iyi ikufanizira madzi osefukira owopsya amene anafika kumalo ena ndi m’mene anthu

akudera limenelo anadzitetezera kumadziwo. Madziwo anasefukira kwa zaka zingapo ndipo

anaononga nyumba, midzi komanso matawuni”

Yalani chinsalu chabuluwu pansi kapena pakhoma.

Ikani ng’ona, njoka ndi mvuu pachinsalupo ndipo muyerekeze kuti zimenezi zili m’madzi.

Uzani ophunzira kuti ng’ona ndi zilombo zina za m’madzi zingafane ndi mavuto osiyanasiyana

amene timakumana nawo m’miyoyo yathu kuphatikizapo matenda opatsirana pogonana

komanso kachilombo ka HIV.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

34

Pitirizani kufotokoza motere:

“Anthu ambiri sakudziwa komwe madzi osefukirawa akuchokera. Ena akukwera pamadenga a

nyumba zawo, ena akuthawira kuntunda. Ena akungoyang’ana madziwo koma sakufuna kusiya

zinthu zimene iwo akuchita. Pali mabwato atatu omwe anthu angagwiritse ntchito podziteteza.

Mabwatowa akuimira Kudziletsa, Kukhulupirika ndi Kondomu.

Aliyense wa anthuwa malingana ndi chikhalidwe kapena chipembedzo chake, akhoza kusankha

kuti kodi akwera bwato lit. Aliyense amene sali pa mabwatowa ndiye kuti akusambira m’madzi

ndipo akhoza kugwidwa ndi zilombo zolusa zija. Anthu ena akuyesetsa kuti akwere limodzi mwa

mabwatowa koma akulephera.”

Chithunzi 16: Ophunzira akuyika khadi malingana ndi nkhani yake

2. Kuwadziwitsa ophunzira za anthu a pa khadi

Muwawonetse ophunzira makadi amene mwawasankha ndipo muwawuze kuti iwo akuyenera

kufotokoza nkhani za anthu amene ali pa makadiwo ndikuti amachita chiyani pa moyo wawo.

Mugawe makadiwo pakati pa ophunzirawo. Ngati nkotheka muwalole ophunzira kuti asankhe

okha makadi amene akuwafuna. Muwauze ophunzira amene ali ndi makadi kuti:

“Akambe za munthuyo ndi dzina lake. Akambe moyerekeza za mbiri ndi khalidwe

lamunthu wapakhadipo ngati kuti akumudziwa. Akambe zomwe akuganizira kuti

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

35

munthuyo akupanga pakali pano. Ayike khadilo pachinsalu cha buluwu m’malo

m’mene akuganizira kuti akuyenera kukhala. Ngati ophunzira akusowa pomuyika

munthu wa pakhadiyo amuyike m’madzi muja. Awayike pamene akuganizira kuti ali

panopa osati pamene akuganizira kuti akhoza kudzakhala.”

Muwawuze ophunzira kuti alumikize nkhani za anthu amene ali pa makadiwo. Mwachitsanzo,

ngati munthu wina wapakhadi watchulidwa kuti ndi mayi wa banja lake, mufunse ngati alipo

wina amene ali ndi mwamuna wake wa mayiwo pa khadi lina. Potero mukhoza kuwona kuti

kukambirana kwanu kukukhudzana mwambiri ndipo kudzera mwa anthu osiyanasiyana a pa

makadiwa mukhoza kukambirana zambiri ndithu.

Muwadziwitse ophunzira kuti anthu amakhoza kusintha mabwato awo achitetezo. Mufotokozere

izi ndi khadi limene liri ndi munthu amene akuwoneka ngati ndi wa bizinesi motere:

“Mkuluyu ndi wa bizinesi komanso ali pa banja ndipo nthawi zambiri amakhulupirika kwa

mkazi wake. Ndiye wanyamuka kupita kukachita bizinesi. Kumeneko wasankha kukwera

bwato la kudziletsa, koma patangotha sabata imodzi wakumana ndi mayi wina okongola.

Ngati aganiza zogonana ndi mayiyo, akuyenera kugwiritsa ntchito kondomu chifukwa ngati

satero ndiye kuti agwera m’madzi muli zilombo zolusa muja ngakhale iye wakhala

okhulupirika. Akagwera m’madzimo ndiye kuti akhoza kukakokeranso mkazi wake

m’madzimo. Anthutu amatha kusintha mabwato pamene ali mu njira ya moyo uno.

3. Mukambirane zimene zikhoza kuwathandiza anthu ali pamakadi aja

Funsani ophunzira kuti:

• Mungawathandize bwanji anthu ali pa makadi aja pa zinthu zomwe akukumana nazo?

• Nanga amene ali m’mabwato aja muwathandiza bwanji kuti akhale momwemo?

• Nanga amene ali m’madzi aja, akhoza kutani kuti akwere nawo?

Mugwiritse ntchito mafunsowa pokamba za anthu ali pamakadi aja, muzitenga khadi

limodzilimodzi. Muwafunse ophunzira kuti akhoza kumuthandiza bwanji munthu ali pa khadiyo

kuti athane ndi vuto limene akukumana nalo.

Ngati pali ena pakati pa ophunzirawa amene akukumanadi ndi mavuto ngati amene

mukukambiranawo ndiye kuti izi zikhoza kuwathandiza.

Zimene zakambidwa m’gawo linozi zikhoza kufikitsidwanso pa chiyindeyinde pogwiritsa

ntchito zisudzo zamgawo lotsatirali.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira

kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

36

Chithunzi

17: Mabwato a Ulendo wa Chiyembekezo

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira

kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

37

GAWO LACHISANU: Zitsanzo zochitika pa njira ya ku

Chilumba cha Tsogolo

Mau Otsegulira

Gawo lino cholinga chake ndikuti lithandize ophunzira kuti amange mfundo, luso, komanso njira

zimene zikhoza kuwathandiza pa nkhani zokhudza ubwenzi, kuyezetsa magazi komanso kukhala

ndi moyo wathanzi ngakhale uli ndi HIV.

Gawo ili likuyamba ndi malangizo amene mungagwiritsire ntchito Kukambirana kudzera

m’zisudzo (Forum Theatre). Kenako gawoli likufotokoza za zochitika zina zimene zikugwirizana

ndi Kukambirana kudzera m’zisudzo. Zokambirana zotsatirazo zikukhudzana ndi nkhani za

kudziletsa, kukhulupirika, kugwiritsa ntchito kondomu, kukayezetsa magazi komanso kulandira

uphungu mosaumirizidwa komanso kusamalira iwo amene ali ndi kachilombo koyambitsa

matenda a Edzi.

Cholinga

Kuthandiza ophunzira kuti apeze njira komanso nzeru zowathandiza zokhudzana ndi nkhani ya

kachilombo ka HIV koyambitsa matenda a Edzi ndi nkhani zina zokhudza matendawa.

Uthenga Ofunika

• Njira ya munthu yokafikira ku chilumba cha tsogolo sikuti imakhala

yowongoka, yopanda mavuto nthawi zonse. Imakhala ndi zokoma

komanso zoipa nthawi zina. Zimafunikira kuti munthu alimbe mtima

kuti akafike ku chilumba chake.

• Kuti tisatenge kachilombo ka HIV zidzafunikira kuti tipange mfundo

zathu komanso tikhale odzikhulupirira ndi omasuka kukambirana

nkhani zokhudza HIV ndi Edzi ndi abwenzi amene tili nawo.

Kukambirana kudzera m’zisudzo (Forum Theatre)

Kodi Kukambira kudzera m’zisudzo ndi chiyani?

Kukambirana kudzera m’zisudzo ndi njira imene imagwiritsa ntchito zisudzo. Ngakhale

owonera amatenga nawo mbali m’zisudzozi. Anthu amafunafuna njira zimene akhoza kuthana

ndi vuto lokambidwa m’zisudzomo. Njira iyi ikhoza kugwiritsidwa ntchito pokambirana pa mitu

yambiri.

Kugwiritsa ntchito Kukambirana kudzera m’zisudzo kwasiyana ndi m’mene anthu ambiri

amagwiritsira ntchito zisudzo pokamba nkhani ya matenda a Edzi ndi kachilombo koyambitsa

38

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

matendawa. Nthawi zambiri anthu amachita chisudzo kuti anthu awonere ndipo akatero

amakambirana pambuyo pake. Kukambirana kudzera m’zisudzo nkosiyana chifukwa chakuti

owonerera amachita nawo. Iwo amapeza njira zimene akhoza kuthetsera vuto limene

likukambidwa m’chisudzomo okha. Owonererawo amayenera alongosole bwino komanso

kuwonetsa m’mene akufunira kuti zinthu zikhalire. Izi zimapangitsa kuti zokambidwazo

zisayiwalike.

Kukonzekera kwake

Chimene chimachitika mu Kukambirana kudzera m’zisudzo ndi chakuti bwalo lokambirana

limapanga kasewero kakang’ono, kuyambira mphindi imodzi kulekeza zisanu, ndipo mwini

nkhani musewerolo amapanga zinthu zimene zimayika iye m’mavuto kapena pabwino.

Ochita chisudzowa amapanga kamodzi kokha mpaka kukalekeza chisudzochi kumapeto. Kenako

sewero lija limadzachitikanso kachiwiri koma ulendo uno sewerolo limayimitsidwa pamene

anthu akuwona kuti mwini nkhani musewerolo akukamba kapena kuchita zosayenera.

Akaliyimitsa chotero sewerolo amafunsana kuti “Tingatani kuti munthuyu timuthandize kuti

apange zinthu zoyenera?” Zikatero sewero lija limapitilira ndipo zija zatchulidwa zija

zimayikidwa mkati mwa sewerolo lija.

Sewero lija likayimitsidwa, amene akutsogolera zokambirana zija akhoza kufunsa munthu kuti

alowe m’seweromo nakachita zimene akuganiza kuti mwini nkhani m’sewerolo ayenera kuchita.

Izi zikhoza kuchitika kangapo ndithu. Kufunsa ophunzira kuti akufuna kuti mwini nkhaniyi

amalize bwanji sewerolo, angamuthandize bwanji? Akakambirana njira zoyenera kudzera mu

chisudzo chija, ophunzira aja amakhala awiriawiri kuti akambirane ndi kuzamitsa njira zomwe

akambirana zija.

1. Ganizirani za zimene mukufuna kukambirana komanso m’mene

mupangire

Kudzera mu zokambirana kudzera m’zisudzo inu mukhoza kukambirana nkhani zambiri.

Sankhani nkhani imene ingakhudze anthu amene akuwonerawo. Nkhaniyo ikhoza:

• Kuchokera pa mgwirizano umene ophunzira anafotokoza kuti ulipo pakati pa anthu ali pa

makadi aja.

• Kuchokera mu nkhani zolembedwa pa mapepala akuluakulu aja a A4.

• Kuchokera mu zitsanzo zoperekedwa m’gawo lino.

• Mukhoza kukonza nokha ngati nkhaniyo mukuyiwona kuti ndiyofunika kuti

mukambirane.

Seweroli:

• Akuyenera kuchita ndi anthu awiri okha basi kuti lisachuluke zochita.

• Lisadutse mphindi zisanu.

• Mwini nkhani mu sewerolo azilakwitsa dala zokamba kapena zochita ndipo mathero ake

azikhala oyipa.

• Lizikhala lokhudza nkhani yakuti ikhoza kuchitikadi.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

39

2. Awuzeni anthu awiri ochita chisudzo aja zimene ayenera kuchita ndipo ayesere

Zokambirana zisanayambe muwapemphe anthu awiri ochita chisudzo aja kuti ayeserere.

Muwonetsetse kuti m’modzi wa iwo akuchita dala zopanda pake koma zoti anthu owonera

azikhulupirire. Asapange mwachibwana kwambiri. Muwawuze m’mene Kukambirana kudzera

m’zisudzo kumakhalira ndipo muwonetsetse kuti nthawi imene azidzachitanso seweroli

kachiwiri lidzakhale chimodzimodzi ngati poyamba paja. Anthu owonera ndi amene akuyenera

kulisintha seweroli, osati momwe mwawapephera kuti achite sewerolo ayi.

Zofunika kugwiritsa ntchito ndi izi:

• Mlatho wa thabwa umodzi

• Ochita zisudzo awiri (ophunzira kapena aphunzitsi).

Kukambirana kudzera m’zisudzo kutenga mphindi 20 kapena 40 chitsuzo chilichose.

Kachitidwe kake

1. Dziwitsani anthu za chisudzocho

Muwawuze ophunzira kuti pali sewero limene awonetse anthu awiri. Muwafotokozere zomwe

chisudzocho chikukamba ndipo mulumikize nkhani ili mu chisudzoyo ndi zina zimene

mwakhala mukukambirana m’mbuyo, kaya ndi zapakhadi zija. Mukhoza kuyamba mwakamba

kaye nkhani zili pa mapepala akuluakulu aja musadayambe seweroli ngati nkoyenera.

2. Chitani chisudzocho ulendo oyamba

Anthu awiri aja achite seweroli mpakana kumapeto. Ngati mukufuna kuti anthu ochita sewero

aja ayambe kapena ayime, muzigwiritsa ntchito matabwa mumakonzera milatho aja.

Muziwamenyetsa matabwawo ngati m’mene amachitira akamajambula kanema. Sewero likatha

alimbikitseni owonera kuti awombe m’manja kuthokoza amene amachita aja. Afunseni kuti

sewerolo aliwona bwanji?

3. Panganinso sewero lija kachiwiri ndipo owonerera ayambe kuyikapo ndemanga

Afotokozereni owonera chimene chikuchitika kuti:

Sewero lija lichitidwanso kachiwiri ndipo kuchita kwake kukhala chimodzimodzi ndi

ulendo oyamba uja. Owonera azilowererapo tsopano ndi ndemanga zawo ndi cholinga

chofuna kukonza sewero lija kuti lithe bwino ndikuti mwini nkhani mu sewerolo

asalakwitsenso. Mwini nkhani musewerolo akachita chinthu cholakwikwa chimene

munthu wina akufuna kukonza, iye azikuwa kuti “dulani kaye.”

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

40

Chithunzi 18

Apa tikuwona ophunzitsa akuchita

sewero lofanizira zochitika za a

chidyamakanda. Ophunzitsa

m’modziyo watenga matabwa

m’manjamo akudikilira kuti

m’modzi wa anthu owonerera

akweze dzanja akawona kuti mwini

nkhani walakwitsa musewerolo,

amenyetse matabwawo. Wina

akakweza dzanja ophunzitsa

ayimitsa sewerelo kuti okweza

dzanjayo aperekepo ndemanga yake.

Chithunzi 19

Bambo ali kudzanja lamanjayo

anakweza dzanja ndipo sewero

linayimitsidwa kuti bamboyi

aperekepo maganizo ake. M’malo

mongofotokoza pamene

palakwikwa, bambo uja

amapemphedwa kuti awonetse

m’mene msungwana

onyengereredwa ndi

Chidyamakanda uja akuyenera

kuchitira mu sewero lija.

Bamboyitu watenga gawo la

msungwana uja ndipo ophunzitsa uja

adakachitabe mbali ya

uchidyamakanda uja.

Tsono inu monga mphunzitsi, mutenge matabwa aja amagwiritsidwa ntchito ngati milatho aja.

Wina owonera sewero akakweza dzanja inu muziwombanitsa matabwa aja nkunena kuti “dulani

kaye.” Akayimitsa chotero mumufunse munthu amene wapangitsa kuti sewerolo liyime kuti

akufuna kukonza pati.

Mumuwuze munthu walowa tsopanoyo ndi uja analowapo kale uja kuti abwerere m’buyo

pang’ono nalibwerezanso sewerolo. Owonera ali ndi ufulube kunena kuti “dulani kaye.”

Ayimitsebe ngati akuwona kuti amene walowa tsopanoyo akuchita zosayenera.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

41

Sewero likatha mukambirane zimene zimachitika museweromo ndikuwona ngati kusintha

sewero kuja kunathandiza. Ngati owonera aja adakali ndi maganizo ena, aloleni kuti achitenso

ndipo wina akhoza kutenga mbali ya mwini nkhani. Mukhoza kubwereza ndithu kufikira

owonera ndi gulu lonse litakhutitsidwa kuti sewerolo latha moyenera ndipo sewerolo likhale la

zinthu zakuti zikhoza kuchitikadi ngakhale ndi zopeka.

Ngati wina owonera wafotokozera bwino zedi m’mene akufunira kuti mwini nkhani asinthire

zochita zake mu sewerolo muwalimbikitse owonera kuti anene kuti “Nditha!” nkuonetsa

chizindikiro chake chija.

Dziwani ichi: Ngati anthu akuchita manyazi kapena sakufuna kuti apange nawo sewerolo

kachiwiri pamene mwasintha zina, muwawuze anthu awiri oyamba aja kuti apitirize kungoti

azisintha zinthu zimene anthuwo akufuna kuti zisinthidwe.

4. Muwone kuti njira zimene zikuyenda bwino ndi ziti

Mufunse kuti:

Kodi njira zimene zinamuyendera bwino mwini nkhani uja ndi zotani?

Nanga taphunzira chiyani mu chisudzo chimenechi?

5. Yesererani m’magulu a anthu awiriawiri

Muwagawe anthu m’magulu a anthu awiri kuti ayesere zinthu zimene aphunzira. Mugulu liri

lonse musankhe munthu A ndi munthu B.

• Munthu A atenge mbali ya mwini nkhani (mwachitsanzo msungwana wasukulu uja)

ndipo munthu B atenge mbali ya munthu wina uja.

• Munthu B azipereka maganizo ake kutengerana ndi m’mene achitira, (mwachitsannzo

kodi msungwana wasukulu uja adalolera zofuna za chidyamakanda chija mu njira yakuti

zikhoza kuchitikadi m’moyo uno?) Anthu aja asinthane mbali.

• Munthu A azipereka maganizo ake kutengerana ndi m’mene achitira.

Zoti Aphunzitzi Adziwe

Kukambirana kudzera m’zisudzo

Zochita zotsatirazi ndizitsanzo zomwe zikugwiritsa ntchito Kukambirana Kudzera m’Zisudzo.

Zitsanzozi ndi zokhuza:

• Kudziletsa kugonana

• Kukhala okhulupirika pa banja kapena pa ubwenzi

• Kugwiritsa ntchito kondomu

• Kulandira uphungu ndi kuyezetsa magazi mosaumirizidwa

• Zomwe anthu amene ali ndi HIV ndi odwala Edzi, mabanja, ngakhalenso anansi awo

ayenera kudziwa ndi kuchita

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

42

Chochita 5A: Kudziletsa kugonana

Cholinga

• Kulimbikitsa, makamaka achinyamata amene sadakwatire kapena kukwatiwa kuti akhale

ndi njira zonenera kuti “TOTO! kugonana.”

• Kuthandiza makolo komanso ana awo kuti akhale omasukirana kukambirana nkhani

zokhudza umoyo komanso kugonana.

Kukonzekera

Kugwiritsa ntchito Kukambirana kudzera m’zisudzo, (muwone koyambilira kwa gawo lino)

pokambirana nkhani makamaka zokhudza achinyamata amene sadakwatire, gawoli ndi

lothandiza kuti achinyamatawo apeze njira zowathandiza kukana kugonana komanso

kukambirana zinthu zoyenera kuchita kapena kusachita anthu akakhala pa ubwenzi.

Werengani m’Zowonjera 1 gawo limene likunena za Mkhalidwe Odzidalira, Wankhanza ndi

Osakhuzidwa ndi zinthu.Werenganinso pamene palembedwa za Kukambira kudzera m’zisudzo

koyambirira m’gawo lomwelino.

Musankhepo pa zimene zalembedwa m’kabokosimu zimene inu mukufuna kuti mukambirane

komanso molingana ndi zimene ophunzira anu akufuna. Mukhoza kusankha mutu wina

wapadera omwe sudatchulidwe m’kabokosimu.

Mupeze anthu awiri akuti achite seweroli ndipo muwafokozere m’mene limayendera.

Mutu Machitidwe a chisudzo

Chidyamakanda/ kukana kuti

TOTO! /njira zokanira

Sewero 1. Chidyamakanda chikufunsira mwana

wasukulu (mwana wa sukulu ndiye mwini nkhani

m’seweroli). Mwana wa sukuluyo amafuna akane

koma chidyamakanda chija chamunyengerera ndi

zinthu zambiri ndipo wavomera kuti agonane naye

mbamboyo mopanda chitetezo.

Kukambirana/kukana/kuvomereza Sewero 2. Ana asukulu awiri, mtsikana ndi mnyamata.

Wina akunkakamiza mzakeyo kuti agonane

mosagwiritsa ntchito chitetezo chilichonse. Winayo

Makolo ndi ana, kukambira nkhani

zokhudza umoyo komanso

kugonana

ndiwofooka ndipo avomerezadi kugonana osadziteteza.

Sewero 3. Kholo (mwini nkhani) likufuna kuti

likambirane ndi mwana nkhani zokhudza HIV,

ukhondo komanso chiwerewere ndi mwana wake

wachichepere, koma mwana uja poyamba nkhani ija

watchula liu lotukwana ndipo kholo lija lakanika kuti

likambirane nkhani ija ndi mwana uja.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

43

Zogwiritsa ntchito ndi izi:

• Thabwa limodzi lija limagwiritsidwa ntchito ngati mlatho lija

• Anthu awiri ochita sewero

• Pepala lalikulu lija la A4 limene likuwonetsa Chidyamakanda

Chichitachi chitenga mphindi 20 kapena 40.

Kachitidwe kake

1. Gwiritsani ntchito makadi

Ngati mukukambirana za a chidyamakanda mukhoza kufuna kuyamba ndi kuwonetsa khadi la

A4 limene pali chidyamakanda chikupereka makwacha kwa mtsikana.

Chithunzi 20: Ufulu okana

2. Gwiritsani ntchito Kukambirana kudzera m’zisudzo kuti mukambirane nkhani

yokhudza kukana kugonana

Werenganinso zolembedwa m’bukku lino zokhudza Kukambirana kudzera m’zisudzo pamene

mukuchita chisudzo chimene mwachisankha.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

44

Mukafika pamfundo nambala 5, yesererani m’magulu a anthu awiri ndipo muwawuze

ophunzira kuti apitirizebe mpaka atafika ponena kuti akhutitsidwa ndi “Toto!” wochokera kwa

nzawo amene akuchita naye sewero.

Chithunzi 21: Toto wochepa mphamvu ndi toto wamphamvu

Chochita 5B: Kukhala okhulupirika pa banja kapena pa ubwenzi

Cholinga

Kuthandiza anthu amene ali pa banja kapena iwo amene akhala pa ubwenzi ogonana kwa nthawi

yayitali.

Kukonzekera

Chochitika ichi chigwiritsabe Kukambirana kudzera m’zisudzo ndipo musankhe sewero limene

ndi logwirizana ndi anthu amene ali pa banja kapena amene akhala pa ubwenzi wogonana pa

nthawi yayitali.

Chochitachi chitenga mphindi 20 kapena 40.

Zogwiritsa ntchito ndi izi:

• Thabwa la mlatho limodzi

• Anyamata a zisudzo awiri

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

45

Mutu Machitidwe a chisudzo

Kukambirana kuti agwiritse kondomu

kapena apite kukayezetsa magazi ku VCT

centre.

Kachitidwe kake

Sewero 4. Amayi akuganiza kuti amuna awo

sakuyenda bwino. Ndiye iwo akufuna

kukambirana ndi amuna awowo kuti ayambe

kugwiritsa ntchiyo makondomu kepena

akayezetse magazi kuti adziwe ngati ali ndi HIV

kapena ayi. Koma amayiwo poyamba

zokambiranazi ndi amuna awowo ayamba

mokalipa ndipo mapeto ake anamenyana.

Gwiritsani ntchito chisudzo kuti mukambirane za kufunika kokambirana za ubwino wa

makondomu

Pangani sewero lomwe mwasankha pa mutu umenewu wa kukhulupirika.

Chochita 5C: Kugwiritsa ntchito Kondomu

Cholinga

• Kuti anthu adziwe za makondomu ndi komwe angawapeze.

• Kuti anthu aphunzire m’mene angakambirane kukabirana zokhudza makondomu ndi

mamuna wawo kapena bwenzi lawo komanso kulimbikitsa anzawo za ubwino ogwiritsa

ntchito makondomu.

• Kuti aphunzire kagwiritsidwe ntchito ka kondomu.

Kukonzekera

M’chochitachi mugwiritsa ntchito Kukambirana kudzera m’zisudzo kuti muunike nkhani zomwe

zimakhala pakati pa anthu m’banja kapena ubwenzi zokhudzana kugwrirtsa ntchito kondomu.

Mufufuze ngati anthu amene mukuwaphunzitsawo akhoza kupeza makondomu a chikazi

mwachidule, (alipo pafupi? Nanga mtengo wake ndi wotani?) ngati zili choncho

muwaphunzitse m’mene angagwiritsire ntchito kondomu yachikazi komanso yachimuna. Ngati

kondomu ya chikazi palibe basi ingophunzirani za kagwiritsidwe ntchito ka kondomu ya amuna.

Werengani zokhudzana Kukambirana kudzera m’zisudzo ndi Kukambirana za kondomu. Ngati

mukuwona kuti izi ndi zothandiza, muwapatse ophunzira anu mapepala a patsamba limeneri.

Pangani sewero lokhudza nkhani imeneyi ya kondomu. Pezani anthu awiri kuti achite seweroli

ndipo apatseni mpata wakuti ayesere asadafike polichita seweroli zenizeni.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

46

Mutu Machitidwe a chisudzo

Kudziwa za kondomu/chifukwa

chogwiritsira ntchito kondomu/kukambirana

za kugwiritsa ntchito kondomu.

Kuphuzira kagwiritsidwe ntchito ka

makondomu.

Sewero 5. Mnyamata, (yemwe ndi mwini

nkhani) akunyadira mzake kuti iye sagwiritsa

ntchito kondomu pakuti chiwalo chake ndi

chachikulu ndikuti makondomu amaphulika,

iye amafuna nyama ku nyama. Mnzake uja

akuyesera kuti amuwuze ubwino wa

makondomu koma sakufotokoza bwino

chifukwa chakuti alibe mfundo zokwanira

zomuuza mnzakeyo.

Sewero 6. Munthu wina (yemwe ndi mwini

nkhani) akuyesera kumulongosolera mnzake

kagwiritsidwe ntchito ka kondomu, koma

sakufotokoza bwino.

Zogwiritsa ntchito ndi izi:

• Thabwa la mlatho

• Anthu awiri ochita chisudzo

• Makondomu a chikazi, (imodzi aliyense) ngati makondomuwo alipo ndipo ngati

sangapezeke ingogwiritsani ntchito makondomu a abambo

• Maliseche abambo osema, oyerekezera chabe, (izi zimapezeka mu phukusi la ulendo wa

chiyembekezo)

• Zinthu monga nthochi kapena chisononkho ndi zina zomwe zingagwiritsidwe ntchito

ngati chokodzera cha abambo kuti anthu aziyeserera mavalidwe a kondomu m’magulu

awo

• Ma pepala ofewa a tishu.

• Kwa iwo amene akufuna muwapatse mapepala amene palembedwa Kagwiritsidwe

ntchito ka kondomu ya abambo, Kangwiritsidwe ntchito ka kondomu ya amayi ndi

Kukambirana za kondomu

Chochitachi chitenga mphindi 20 kapena 40.

Kachitidwe kake

1. Kodi makondomu mungawapeze kuti? Nanga mitundu yake ndi yotani?

Mufunse ophunzira mafunso otsatirawa ndipo inuyo mutsogolere kukambirana pa mafunso awa:

• Kodi m’dera lino makondomu amapezeka kuti?

• Mitundu ndi mitengo yake ndi yotani?

• Mavuto amene anthu angakumane nawo pofuna kupeza kondomu ndi otani?

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

47

2. Gwiritsani ntchito chisudzo kuti mukambirane za kufunika kokambirana za

ubwino wa kondomu

Pangani sewero lachisanu kapena lachisanu ndi chimodzi pa mutu umenewu wa kondomu. Ngati

nkotheka apatseni ophunzira Chithunzi 24: Kukambirana za kondomu.

3. Kufotokoza kagwiritsidwe ntchito ka kondomu ya chimuna kudzera mu zisudzo

Kuti mufotokoze bwino m’mene anthu angavalire komanso kugwiritsira ntchito kondomu

yachimuna, onetsani sewero la chisanu ndi chimodzi. Munthu amene ali mwini nkhani

museweroli azilakwitsa dala kuti owonera aliyimitse nakonza polakwikapo.

Ngati onse akulephera kuwonetsa bwino kagwiritsidwe ntchito ka kondomu koyenera, inuyo

mutenge mbali yowonetsa kagwiritsidwe ntchito ka kondomu koyenera.

4. Kagwiritsidwe ntchito ka kondomu yachikazi

Ngati ophunzira anu aja akutsimikizirani kuti akhoza kuwapeza makondomu achikazi

mosavutikira muwafotokozere m’mene angawagwiritsire ntchito.

5. Kuyeserera

Kuti anthu adziwe bwinobwino kagwiritsidwe ntchito ka kondomu akuyenera kuti ayesere

paokha. Kawirikawiri anthu amachita manyazi kuti atero, ndiye muwagawe m’magulu a anthu

ochepa ndipo akhale ndi anthu amene akhoza kumasuka nawo.

Amuna akhale kwaokha, chimodzimodzinso akazi. Achichepere akhoza kukhalanso m’magulu

awo. Ndiye kuti mukhoza kukhala ndi magulu anayi: atsikana, anyamata, abambo ndi amayi.

Perekani makondomuwo.

Aliyense (ngati nkotheka) akhale ndi makondomu awiri ya abambo ndi imodzi ya amayi.

Muwapatsenso zoyesezera maliseche a abambo. Muwalimbikitse kuti awone m’mene anzawo

akuchitira ndipo athandizane kuti aliyense adziwe kachitidwe kake.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

48

Zoti Aphunzitsi Adziwe

Kondomu ndi yolimba, ili ndi khoma lolimba ndithu mwakuti umuna, kapena kachilombo

ka HIV koyambitsa matenda a Edzi, kapena tizilombo toyambitsa matenda ena opatsirana

pogonana sitingadutse.

Ngati mungagwiritse bwino ntchito makondomu, chitetezo mukhoza kuchipeza.

Makondomu amatsitsa kotheratu mafalidwe akachilombo kusiyana ndi pamene munthu

akhala osagwiritsa ntchito kondomu. Amathandizanso kupewa matenda ena opatsirana

pogonana komanso mimba zosafunika zimapewedwa.

M’Malawi muno makondomu achimuna ndi amene amapezeka mosavuta. Makondomu

achikazi sapezeka wamba ndipo amakonda kukhala okwera mtengo. Kuti munthu agwiritse

bwino ntchito kondomu mpofunika kuti:

• Makondomuwo azipezeka ndipo azipezeka pa mtengo wabwino

• Muthu akhale ndi zifukwa zokwanira zomulimbikitsira kugwiritsa ntchito

kondomuyo, (mwachitsanzo, ngati munthuyo akufuna tsogolo labwino, kaya ngati

akufuna kukhala wa thanzi).

• Adziwe kukambirana ndi bwenzi lake za kagwiritsidwe ntchito ka kondomu.

• Akhale ozindikira m’mene kondomu ingagwiritsidwire ntchito.

Kondomu ya amuna

Kondomu ya abambo ndi ya labala monga ya amayi ndipo imatchinjiriza umuna kuti

usalowe kumaliseche kwa mnzimayi, mkamwa kapenanso kuthako. Makondomuwa

amagulitsa komanso amapezeka m’zipatala, m’malo a zaukhondo komanso m’zipatala

zing’onozing’ono.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

49

Kagwiritsidwe ntchito ka kondomu ya amuna

1. Gulani makondomu anu ku malo agulitrsira zinthu kapena ku zipatala zomwe zimagulitsa

makondomu ambiri ndiponso komwe amasunga makondomuwa m’mapakete awo

m’malo ozizira bwino osati padzuwa.

2. Yang’anitisitsani pakete ya makondomuwa ndipo onetsetsani kuti nthawi yake yogwiritsa

ntchito kondomuyo sidathe komanso ikhale yosabooka. Ngati mtundu wa kondomu

sukuoneka bwino, komanso ngati kondomuyi ikumata mukaikhudza, musaigwiritse

ntchito chifukwa ikhoza kung’ambika.

3. Valani kondomu pokhapokha ngati maliseche anu alimba musanayambe kugonana.

4. Muwonetsetse kuti nsonga ya kondomu iri kunja ndipo ikuloza kumwamba.

Mukamavala muzikhala ngati mukuyifunyukula kumayitsitsira m’musi kumene

maliseche anu adamerera. Kansonga ka kondomu kaja mukakoke pang’ono ndi dzanja

limodzi ndi cholinga chakuti pakhale mpata wakuti ukale (umuna) ugwere

m’kansongamo ndikutinso isaphulike.

5. Valani kondomuyo pogwiritsa ntchito dzanja linalo ndipo muyifunyukule kufikira

poyambira thupi.

6. Maliseche a mkazi akhale ndi chinyezi kupewa kuti kondomuyo ingaphulike komanso

kuti musangalale pogonana. Kumaliche kwa mkazi kumakhala konyowa ngati

tamukonzekeretsa mkaziyo kugonana. Khalani achikondi abwino, musanayambe

kugonana yambani mwagwiranagwirana, sewerani mpaka kumaliseche kwa mkazi

yemwe mukugonana naye kutanyowa.

7. Musagwiritse ntchito mafuta ngati Vaseline, mafuta a mtedza kapena mafuta a mtundu

wina uliwonse kunyowetsa kondomu. Mafuta amapangitsa kondomu kuphulika.

8. Makondonomu amadalirika mukawagwiritsa ntchito bwino.

9. Mukatha kugonana, chida cha abambo chisanafote kwambiri, vulani kondomuyi. Chitani

izi mutagwira kukamwa kwa kondomuyi ndi pepala lofewa mutalizunguza ku chida

chanu mosamala. Izi muchite kuti musataye umuna omwe uli mkondomuyi kapena

kudzitaila m’manja.

10. Chotsani kondomu ndipo mangani m’pepala ndipo katayeni m’chimbudzi chokumba

kapena otchani kapenanso kukwirira. Musagwiritse ntchito kondomu kawiri. Gwiritsani

ntchito kondomu yatsopano nthawi zonse pomwe mukugonana.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

50

Kondomu yachikazi

Zoti Aphunzitsi Adziwe

• Makondomu a mayi sapezeka wamba ndipo ngokwererapo mtengo. Ngati

makondomu amayi akuvuta kuwapeza kwake, basi ingophunzirani za kondomu

ya abambo.

• Kondomu ya amayi ndi yofewa ndiponso imawonekera mkati. Ntchito yake ndi

kupewa kukhala ndi pathupi posayembekezera, kupewa kutenga kachilombo ka

HIV ndiponso kupewa matenda opatsirana kudzera mkugonana. Kondomuyi ili

ndi mbali ziwiri zozungulira kumapeto ake.

• Mbali imodzi ndi yotsegula ndipo inayo ndiyotseka. Mbali yotsekayi ndikomwe

mungalowetsere kondomuyi ku malicheche ogonanirana a amayi. Mbaliyi

imathandizanso kuti kondomuyi isalowe mkati kwambiri.

• Mbali ina ya kondomuyi imakhala kunja kwa malisechewa ndipo imathandiza

kulimbitsa bwino kondomuyi popeza ndi yomwe imagwira nsonga ya

maliseche a abambo pogonana.

• Kondomuyi imakhala yonyowetsedwa kale kuti idzitha kulowa bwino ku

maliseche a amayi. Mungalowetse kondomuyi ku maliseche a amayi nthawi

iliyonse musanayambe kugonana. Mukatha kugonana chotsani kondomuyi.

• Kindomu ya amayi singalowe m’thupi la mayi nkusowera momwemo. Izi ndi

nkhamba kamwa chabe.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

51

Kagwiritsidwe ntchito ka kondomu ya akazi

Mugwiritse ntchito zafotokozedwa pa tsamba lotsatira.

Chithunzi 23. Kupiringiza nkombero wakunja polowetsa kondomu mkati

• Mutenge paketi imene muli

kondomu ya chikazi ndipo

mulongosole izi:

• Kuyitulutsa bwinobwino m’paketi

komanso kuwonetsetsa kuti

kondomuyo ndi yosang’ambika.

• Kulowetsa kondomuyo

kumaliseche kwa mnzimayi.

Mugundanitse chala cha chikulu

ndi cha m’komba phala ndipo

zipange dzenje ngati kumaliseche

kwa mzimayi. Ndi dzanja linalo

mulangize m’mene

angalowetserekondomuyo

kumalisecheko.

Chithunzi 24: Kulowetsa chiwalo cha mwamuna mkati mwakondomu

• Kulowetsa chiwalo cha

mwamuna m’kondomuyo:

Muwonetsetse kuti chilowe

bwino osati kulowera pambali

pa kondomu yomwe mayi

wavala. Mukhoza kugwiritsa

ntchito ziwalo za amuna zosema

zija mukamawasonyeza

ophunzira.

• Kupiringiza nkombero

(chingerengere) wakunja ndi

kuchotsa kondomu ku maliseche

aja munawakonza aja.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

52

Kavalidwe ka kondomu yachikazi

1. Tulutsani kondomu m’paketi bwino

Muwone papaketipo tsiku limene kondomuyo idzasiye

kugwira ntchto yake ndipo muwonetsetse ngati

kondomuyo ndi yosabowoka. Mung’ambe kondomuyo

kuchokera ku mtunda cha kudzanja la manzere.

Muyigwire bwino osang’amba ndi zikhadabo ayi.

Muwonetsetse kuti ndi yonyowetsedwa m’kati ndi

kunja komwe. Madzi kapena mafuta akhoza

kunyowetsa kondomuyo.

2. Finyani nkombero wa kunja

Chala chanu chachikulu ndi cha n’khala pakati chigwire

nkombero wamkatiwo ndi kuwufinya kuti utalike

komanso kuwonda.

3. Lowetsani nkombero

Sankhani malo ofewa. Mwendo wina uponde pa bedi,

kaya pa mpando, kapena nyonyomalani kapenanso

kukhala pansi koma miyendoyi mutayitayanitsa. Ndi

dzanja linalo kankhani milomo yomwe imaphimba

kumaliseche kwanuyo. Lowetsani nkomberowo

mkatikati mwa malisechewo.

Mukhoza kuvala kondomuyi nthawi iri yonse pamene

musadayambe kugonana.

4. Ikankhireni nkati ndipo ilowe kwathunthu

Mulowetse chala cha mkomba phala mkati mwa

kondomuyo ndipo ikankhireni mkati kwambiri.

Osadandawula, sikuti ikhoza kumira yonse ayi.

Muwonetsetse kuti yakhazikika bwino mosapiringizika.

Nkombero wa kunja uja ukhale kunja kwa maliseche.

5. Lowetsani chiwalo cha abambo

Mofewa bwino ndi moleza, lowetsani chiwalo cha

mwamuna kumaliseche anu ndi dzanja lanu kuti

muwonetsetse kuti chiwalocho chalowa bwino mu

kondomu kumaliseche anuwo.

6. Piringizani nkombero wa kunja, tulutsani

kondomuyo ndi kuyitaya

Potokolani nkombero wa kunja uja ndipo itulutseni

kondomuyo pang’onopang’ono musanadzuke.

Ikulungeni pa mapepala ofewa a tissue nkuyitaya.

Ikwirireni, kaya kutentha kumene, kapenanso

kuyiponya kudzala. Muzigwiritsa ntchito kondomu

yatsopano nthawi iri yonse imene mukugonana

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

53

Chithunzi 25: Kukambirana za kondomu

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

54

Chochita 5D: Kulandira uphungu ndi kuyezetsa magazi

mosaumirizidwa

Cholinga

• Kuwafotokozera anthu ndondomeko ya kulandira uphungu ndi kuyezetsa HIV ndi

komwe angapeze uphunguwu.

• Kuunikira anthu ubwino oyezetsa magazi mosakamizidwa.

Kukonzekera

Chochita ichi chikufotokozera bwinobwino za kulandira uphungu ndi kuyezetsa magazi

mosaumirizidwa (VCT). Kodi uphungu mungawupeze kuti? Nanga amene akufuna kuti

akayezetse kapena kulandira uphungu atani?

Werengani Zowonjezera 1 gawo likunena za Kulandira uphungu ndi kuyezetsa magazi

mosaumirizidwa kapena kawerengeni m’kabukhu komwe adalemba a National AIDS

Commission pa nkhani yomweyi.

Imvani zambiri kuchokera ku chipatala chomwe muli nacho pafupi za komwe anthu omwe

mukuwathandiza angapeze uphungu waulerere ndi kuyezetsa magazi.

Dziwani zambiri powerenga pa mutu okhudza Kukambirna kudzera m’zisudzo, imene ndi ndime

yoyambirira ya m’gawo lino.

Mungathe kugwiritsa ntchito sewero lalembedwa panoli kapena mukhoza kukonza lanu nokha

malingana ndi zimene ophunzira anu akufuna pokhudzana ndi nkhani yoyezetsa magaziyi.

Pezani anyamata awiri azisudzo ndipo muwafotokozere m’mene Kukambirana kudzera

m’zisudzo kumayendera.

Chochitachi chitenga mphindi 20 kapena 40.

Zogwiritsa ntchito ndi izi:

• Thabwa la mlatho limodzi

• Anyamata a zisudzo awiri

Mutu Machitidwe a chisudzo

Luso lokopa ena/ubwino odziwa m’mene

magazi ako aliri/wina kukhala ndi

kachilombo wina ayi pa banja.

Sewero 7. Mnyamata ndi mtsikana omwe

akuganizira zakuti amange banja. Mnyamatayo

akumuwuza mtsikanayo kuti akayezetse magazi,

(mnyamatayi ndi mwini nkhani). Mtsikana uja

sakufuna kutero ndipo ayamba kukangana.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

55

Chochitachi chikugwirizana bwanji ndi zochita zina?

Ubwino odziwa m’mene magazi ako aliri ndi wakuti munthu umatha kukonzekera za tsogolo

lako bwino komanso tsogolo la banja lako. Izi zikhoza kufaniziridwa ndi Chochita 3A: Chilumba

cha Tsogolo.

Chochita 1A: Moto Olusa, Chochita 1B: Ndani ali ndi HIV? Chochita 1C: Chimachita ndi

chiyani m’thupi la munthu amene ali ndi HIV, Edzi kapena ayi? Zimenezi zimapangitsa anthu

kufuna kukayezetsa magazi awo. Izi zimalimbikitsanso kuti anthu amene ali ndi HIV akhoza

kukhala moyo ndithu nthawi yayitali ndipo athanzi.

Chochita 1B: Ndani ali ndi HIV? Zikuphatikiziraponso chithunzi cha Bruce Radebe. Atapita

kukayezetsa magazi ake adamupeza kuti adali ndi kachilombo ka HIV koyambitsa matenda a

Edzi. Adamuwuza bwenzi lake poganizira kuti mwina bwenzi wakeyo amusiya. Koma ayi

ndithu, zimenezo zidangolimbikitsa chibwenzi chawo nkupititsa patgogolo chikhulupiriro chawo

pa wina ndi mzake. Adamanga banja m’chaka cha 2003, nthawi zonse akamagonana amagwiritsa

ntchito makondomu.

Kachitidwe kake

Choyamba

Muwafunse ophunzira anu kumene angapeze uphungu m’dera lawo kapena malo ena ozungulira.

Mukambirane za malo amenewo. Muwawuze mayina amalowo, dera lake, nthawi imene

amagwira ntchito kumaloko komanso mitengo yake ya kumene angapeze uphungu komanso

kukayezetsa magazi ngati amalipiritsa.

Kodi chimene chimachitika polandira VCT nchiyani?

Muwafunse ophunzira mafunso awa:

• Kodi kuyezetsa mapazi ku HIV ndi chiyani?

• Nanga chimene chimachitika polandira uphungu ndi kuyezetsa magazi ndi chiyani?

Muziwakonza ophunzirawo akalakwitsa.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

56

Chochita 5E: Zomwe anthu amene ali ndi HIV, odwala Edzi,

mabanja ngakhalenso anansi awo ayenera kudziwa

ndi kuchita

Cholinga

• Kuwathandiza kupeza njira zomwe zingawapangitse kukhala ndi moyo wautali anthu

amene ali ndi kachilombo ka HIV kapena amene akuganiza kuti ali nako.

• Kulimbikitsa njira zoyenera zomwe tingathandizire ndi kulimbikitsira anthu amene ali

ndi kachilombo ka HIV komanso omwe akudwala matenda a Edzi.

Kukonzekera

Gawo ili likukamba zambiri zokhudzana ndi m’mene munthu angakhalire m’chiyembekezo ndi

HIV. Ikukambanso za m’mene munthu angafotokozere banja lake kuti ali ndi kachilombo

koyambitsa matenda a Edzi. Tigwiritsanso ntchito sewero lomwe likukamba zambiri za zomwe

mungachite ngati nzanu kapena mbale wanu wakuuzani kut ali ndi HIV.

Werengani buku lomwe likupezeka m’phukusi la Chiyembekezo la Kukhala m’chiyemekezo ndi

HIV ndi matenda a Edzi. Werenganinso zokhudza Kukambirana kudzera m’zisudzo.

Sankhani limodzi mwa masewero amene mwapatsidwawa, kapena konzani lanulanu, malingana

ndi nkhani zimene mukufuna kukambirana.

Pezani anthu awiri ochita sewero ndipo muwafotokozere m’mene angachitire seweroli, kenaka

awuzeni kuti ayeserere.

Chichitachi chitenga mphindi 30 kapena ola limodzi.

Mutu Machitidwe a chisudzo

Kuvomereza, kumvetsetsa ndi luso

loperekera uphungu.

Kuwululira mwana zokhudza magazi ako,

muyang’ane mkabuku kaja ka Kukhala

m’chiyemekezo ndi HIV ndi matenda a

Edzi.

Sewero 8: Wina anakayezetsa magazi ndipo

wapezeka kuti ali ndi kachilombo. Anapita kuti

akafotokozere nzake (mwini nkhani) koma nzake

uja wamukana mwamwano ndipo wathetsa

ubwenzi. Owonera awonetse kuti chinthu

chabwino kuchita pa nthawi ngati imeneyi ndi

chiyani?

Sewero 9: Kholo limuwuza mwana kuti,

“ndisakubisire mwana wanga ine ndiri ndi HIV

ndipo ndifa!” Osamuuza mwanayo kuti Edzi ndi

chiyani, osakambirana naye bwinobwino

mwanayo kuti afunse mafunso ndikumvetsetsa

nkhaniyo ayi. Ndiye mwana uja posadziwa naye

akuti, “nanenso mundipatsire Edziyo, tifa tonse

basi.” Kenako mwana uja nkuyamba kulira.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

57

Zofunika kugwiritsa ntchito ndi izi:

• Milato

• Chilumba

• Zilombo zolusa monga ng’ona, mvuu ndi njoka

• Ochita zisudzo awiri

Chochitachi chikugwirizana bwanji ndi zochia zina?

Chochita 2A: Kuwoloka pa Timilato ndi chochita 3A: Chilumba cha Tsogolo, zikulimbikitsa kuti

anthu amene ali ndi kachilombo ka HIV akhoza kukhala nthawi yayitali ndipo akhoza kuchita

zinthu zikuluzikulu m’moyo uno. Chochita 2B: Kuwoloka pa Timolato kwa amene ali ndi HIV

chikhozanso kugwiritsidwa ntchito mu gawo lino.

Kachitidwe kake

1. Kodi zinthu zimene munthu amene ali ndi kachilombo ka HIV amakumana nazo

ndi monga chiyani?

Tulutsani khadi limodzi kuchokera, “m’kati mwa madzi,” lomwe likuyimira munthu yemwe ali

ndi HIV.

Muwafunse anthu mafunso awa:

• Kodi munthu uyu angamve bwanji ndipo angatani atazindikira kuti ali ndi kachilombo

koyambitsa matenda a Edzi.

• Nanga anthu awa angatani atamva kuti munthu ameneyi ali ndi kachilombo koyambitsa

matenda a Edzi?

- Anzake, mkazi wake, mwamuna wake, chibwenzi chake.

- Makolo.

- Ana ake.

- Abwenzi ake, ogwira nawo ntchito, abwana ake.

• Kodi ndi chilumba chiti cha tsogolo chimene chingamuthandize iyeyu?

• Amene akudwala matenda a Edzi, tingawasamalire bwanji?

2. Kuwoloka pa mlatho kwa anthu amene ali ndi HIV.

Pangani chochita 2B: Kuwoloka pa mlatho kwa anthu amene ali ndi HIV, pofuna kuwonetsa

m’mene tingawathandizire anthu amene ali ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi.

3. Gwiritsani ntchito Kukambirana kudzera m’zisudzo kuti nkhaniyi muyikambe

ndithu mozama.

Pangani chisudzo chimene mwachisankha chija. Werenganinso zokhudza Kukambirana kudzera

m’zisudzo.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

58

Zowonjezera 1: Zofunika kuti aphunzitsi adziwe

1. Matenda opatsirana pogonana

Pali matenda ena opatsirana kudzera m’njira yogonana. Ena mwa matenda amene anthu

angapatsirane mnjira imeneyi ndi monga: chinzonono, chindoko, mabomu, mawuka ndi ena

otere. Matenda amenewa atha kuchizidwa ndi chithandizo cha kuchipatala. Padakali pano palibe

mankhwala omwe angachize matenda a Edzi, komabe kuchiza matenda ena opatsirana pogonana

mwansanga kungachepetse kufala kwa kachilombo koyambitsa matenda a Edzi ka HIV.

Kupezeka ndi matenda opatsirana pogonana ndi chitsimikizo chakuti munthuyo adagonanapo ndi

wina mosadziteteza ndipo mwina akhoza kukhala ndi kachilombo ka HIV.

Mungadziwe bwanji ngati muli ndi matenda opatsirana pogonana?

Matendawa akamayamba samawonetsa zizindikiro zili zonse ndipo odwalayo amaonekabe

wathanzi. Tizilombo tamatendawa timafala nthawi imeneyi ngati munthu wagonana ndi wina.

Zizindikiro za matendawa

• Zilonda kumaliseche, m’milomo komanso kochitira chimbudzi. Zilondazi zimapweteka

kwambiri. Nthawi zina zilondazi zimakhalapo zambiri kapena chimodzi basi. Komanso

nthawi zina munthu amachita mwanabele m’mphechepeche ndipo zotupazo zimatha

kutupa ndi kuphulika.

• Ena mwa matendawa saonetsa zizindikiro ndipo munthu samamva kupweteka

kulikonse.

• Abambo omwe akudwala chinzonono amamva kupweteka pamene akukodza komanso

mafinya achikasu amatuluka kuchokera kumaliseche.

• Zizindikiro zamatendawa mwa amayi zimakhala zodabwitsa chifukwa zimatha kukhala

zosiyanasiyana monga mafinya omwe amatuluka kumaliseche ali onunkha, komanso

mafinyawa amatha kuwoneka m’mitundu iyi: achikasu, oyera komanso obiliwira

(green). Malisechenso amatha kukhala ndi zilonda kapena zotupa, kuyabwa kapenanso

kungopweteka chabe. Amathanso kumva kupweteka mmunsi mwa mimbamu, nsana,

komanso amamva kuphwanya thupi ndi kuzizira. Mayi otereyu ayenera kupita

kuchipatala msanga.

Kodi matenda opatsirana pogonanawa ndi oopsa?

Matenda ena a m’gulu limeneri monga Chinzonono angayambitse matenda ena omwe

angapangitse mayi kulephera kubereka. Matendawa akhoza kupangitsanso kuti mwana amene

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

59

angabadwe akhale wakhungu kapena kubadwa wakufa. Matendawa angapangitsenso kuti

abambo akhale osabereka.

Ndibwino kuthamangira ku chipatala kukawonana ndi a dotolo pamene munthu wadwala

matendawa kuti akalandire chitandizo mwamsanga ndiponso asapatsire anthu ena.

Onse omwe wodwalayu anagonana nawo ayenera kukalandiranso thandizo ku chipatala.

2. Kachilombo ka HIV koyambitsa matenda a Edzi

Kodi HIV ndi Edzi ndi chiyani?

Edzi m’chingelezi imayimira kuti Acquired Immune Deficiency Syndrome (AIDS). Edzi ndi

matenda omwe munthu amadwala akakhala ndi kachirombo ka HIV, ndipo mau oti HIV

amatanthauza Human Immuno-deficiency Virus.

HIV imachita ngati momwe chimachitira chiswe chikalowa m’denga la nyumba. Poyamba

kachilomboka kamalowa m’thupi ndipo kamaswana. Nthawi imeneyi palibe yemwe amadziwa

kuti m’thupi muli vuto liri lonse popeza munthu otereyu amawoneka bwinobwino ndiponso

wathanzi kwa zaka zingapo. Munthu otereyu ndiye kuti ali ndi HIV osati Edzi.

Monga takamba kale, chiswe chimatenga nthawi yaitali kuti chiyambe kudya denga lija.

Momwemonso munthu amatha kukhala ndi HIV kwa nthawi yayitali chitetezo cha thupili

chisanagonjetsedwe ndi tizilombo ta HIV.

Pakapita nthawi munthu amayamba kusonyeza zizindikiro zina monga zotupa m’malo

osiyanasiyana komanso kuwonda, kumva ngati malungo, kutsekula m’mimba, kutsokomola,

kutuluka zilonda m’thupi ndi zina zotero. Nthawi ikamapita munthuyo amayamba kudwala

kwambiri m’mapapo, mu ubongo, komanso matenda ena. Zikatero ndi pomwe amatha kunena

kuti munthu wayamba kudwala Edzi.

HIV ndi Edzi zakhala m’Malawi muno kuyambira m’chaka cha 1985.

Kodi pali mankhwala omwe angachize EDZI?

Pakali pano palibe mankhwala ochiza matenda a Edzi. Mankhwala ambiri omwe amamveka ndi

ongoletsa kuswana kwa kachilombo ka HIV m’thupi la munthu kuti kasayambitse msanga Edzi.

Mankhwala oterewa alipo koma ndi okwera mtengo. Palinso makhwala ena omwe amathandiza

kuchiza matenda ena kwa anthu omwe ali ndi Edzi.

Kodi HIV imafala bwanji?

Tizilombo ta HIV timatha kufala podzera mu magazi, umuna kapena ukazi, komanso kudzera

mu mkaka wa m’mawere wa amayi. Malovu, thukuta komanso misozi sizingamupatse munthu

kachilombo ka HIV pakuti sitikhalamo mu zinthu zimenezo kufikana pakuti mpakana munthu

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

60

akhoza kutenga HIV. Tizilombo tomwe timapezeka m’magazi, mu umuna kapena ukazi

timafalikira mwa munthu wina pochita zinthu izi:

Kudzera m’kugonana kosadziteteza (popanda kondomu)

Kachilombo ka HIV kamafala pa nthawi imene anthu agonana. HIV ikhozanso kufala ngakhale

pakati pa amuna okhaokha omwe amagonana kapena akazi okhaokhanso ogonana.

Kuchokera kwa mayi kupita kwa mwana

Mayi amene ali ndi HIV akhoza kupatsira mwana yemwe sanabadwe panthawi yomwe

akubereka komanso kudzera mu mkaka wa m’mawere omwe mwana akuyamwa kuchokera kwa

mayi wake. Mwa ana khumi aliwonse omwe amabadwa kwa amayi amene ali ndi kachilombo ka

HIV, ana atatu amatenga HIV kuchokera kwa mayi wawo. Ndiye kuti ana asanu ndi awiri

amakhalabe moyo opanda kachilombo ka HIV. Komabetu pali njira zimene zingathandizire kuti

ana ambiri asamatenge kachilomboka kwa mayi wawo. Njirazi ndi monga izi:

- Kupewa kupatsa kachilomboka kapena kuwonjezera kachilomboka kwa mayi wapakati

pogwiritsa ntchito kondomu.

- Kubeleka kudzera mu njira ya opaleshoni.

- Kupereka ma ARV kwa mwana wobadwayo ndi mayi wake.

- Kumupatsa mwana wobadwayo mkaka wa m’mawere okha kwa miyezi isanu ndi umodzi

kenako kumuletseratu mwanayo kuyamwa.

Munthu angathenso kutenga HIV kudzera m’magazi

Ngati munthu alandira magazi kwa munthu yemwe ali ndi HIV, olandirayo akhoza kutenga

kachilombo ka HIV. M’zipatala zambiri masiku ano amayesa kaye magazi kuti awone ngati

magaziwo alibe kachilombo ka HIV asanaperekedwe kwa munthu wina. Ngati apeza kuti ali ndi

kachilomboka, magaziwo amawataya.

Munthu angathenso kutenga HIV kudzera mu zipangizo zina

Kachilombo ka HIV kamatha kufala podzera mu kubwerekana malezala kapena jakisoni

zosanyikidwa m’makhwala kapena kuwiritsidwa bwino. Anthu omwe amagwiritsa mankhwala

ozunguza bongo pomadzibaya ndi jakisoni amathanso kutenga HIV m’njira imeneyi.

Nawonso asing’anga akuyenera kuyitanitsa ndi kugwiritsa lezala watsopano kwa munthu

aliyense yemwe akuchekera mphini.

HIV ikhozanso kufala podzera mu njira izi:

• Kugwiritsa ntchito chodulira chimodzi podula mchombo wa mwana pakubadwa pake.

• Mwambo wamdulidwe (jando) pamene mugwiritsa ntchito chida chimodzi.

• Pometa ndipo wina wadzicheka iwe nkugwiritsira ntchito lezalo lomwelo.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

61

Zinthu zomwe sizingafalitse kachirombo ka HIV

Kachilombo ka HIV kamapezeka mmagazi, mu umuna kapena mu ukazi komanso kachilomboka

kamayenera kulowa mmagazi a munthu kuti kafale. Nchifukwa chake HIV siifala podzera

m’kupsopsonana, kukumbaritana, kugwirana manja, kugwiritsa ntchito chimbudzi chimodzi,

kubwerekana zovala, kugawana zakudya, zakumwa, kutsokomolerana, kulumidwa ndi udzudzu

umodzi, kuphunzira nawo limodzi ku sukulu komanso kugwira ntchito limodzi ndi omwe ali ndi

EDZI. Simungatengenso kachilomboka popereka magazi ngati zipangizo zotengera magazizo zili

zotetezedwa bwino.

3. Kulandira uphungu ndi kuyezetsa magazi mosaumirizidwa

(Uthenga uwu wachokera m’kabukhu kotchedwa Kulandira uphungu ndi kuyezetsa magazi

mosakakamizidwa kolembedwa ndi a National AIDS Commission ndipo kabukhuka kalinso mu

thumba la Chiyembekezo)

Kodi kulandira uphungu ndi kuyezetsa magazi mosaumirizidwa kumatanthauza chiyani?

Uku ndi kulandira uphungu ndi kuyesetsa magazi mwa kufuna wekha kuti munthu udziwe ngati

uli ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi kapena ayi. Kulandira uphungu ndi kuyezetsa

magazi kumachitika mwachinsinsi kuti munthu wokayezetsayo akhale omasuka ndipo kuti anthu

ena asadziwe zotsatira zake.

Munthu wina aliyense sayenera kukakamizidwa kuti ayezetse magazi ake chifukwa kutero ndi

kuphwanya ufulu wa chibadwidwe wa munthuyo. Choncho abambo ndi amayi, makolo ndi ana

awo, atsogoleri ndi anthu awo kapenanso anthu pa ntchito sayenera kukakamizidwa kukayezetsa

magazi.

Kodi cholinga choyesetsera magazi ndi chiani?

Cholinga choyezetsera magazi ndi kuti munthu adziwe ngati ali ndi kachilombo koyambitsa

matenda a Edzi kapena ayi.

Kodi oyenera kuyesetsa magazi ndi ndani?

Wina aliyense amene akufuna kudziwa ngati ali ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi

kapena ayi. Nkofunika kwambiri kuti abambo kapena amayi amene akufuna kubereka ayezetse

magazi kuti apewe kupatsira mwana wodzabadwayo. Achinyamata amene akufuna kulowa

m’banja ayenera kuyezetsa magazi. Izi ziwathandiza kuti asapatsirane kachilomboka.

Ndondomeko ya uphungu ndi kuyezetsa magazi

1. Kukambirana musanayezetse magazi

Uku ndi kukambirana mwa chinsinsi pakati pa phungu ndi munthu ofuna kuyezetsa magazi.

Munthu woyezetsa magazi amaunikiridwa za ubwino oyezetsa magazi kwa iyeyo komanso kwa

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

62

anthu ena. Kukambiranaku kumathandiza kuti munthuyo avomereze kuti ayezetsa magazi ndipo

kuti avomereza zotsatira zake.

2. Kuyezetsa magazi

Apa woyesa magazi amatenga dontho lamagazi pachala cha munthuyo ndikuyesa ngati

m’magazimo muli kachirombo koyambitsa matenda a Edzi kapena ayi. Masiku ano izi

zimatenga kanthawi kochepa.

3. Kulandira uphungu mutayezetsa magazi

Uku ndi kukambirana pakati pa a dokotala kapena phungu ndi munthu amene wayezedwa

magazi. Cholinga chamalangizo amenewa ndi chofuna kumulimbikitsa munthuyo pa zotsatira za

magazi ake. Mumakambirana za m’mene mungakhalire ngati atakupezani ndi kachilombo

koyambitsa matenda a Edzi kapena mulibe. Uphunguwu umalimbikitsanso kuti anthu achepetse

makhalidwe omwe angachititse kuti atenge kachilombo ka HIV.

Ubwino olandira uphungu ndi kuyezedwa magazi

Uku ndi kukambirana pakati pa phungu ndi woyesetsa magazi uja. Apa ndi pamene phungu

amamuuza woyesedwayo zotsatira zake.

Mwa zina woyesedwa magaziyo amauzidwa za m’mene angadzisamalirire kuti kachilomboka

asakatenge ngati wapezeka kuti alibe; kapena za m’mene angadzisamalirire kuti asapatsire anthu

ena kachilomboka ngati ampeza nako. Kaya akupeza nako kapena ayi, kukambiranaku nkofunika

kwambiri.

Ubwino woyezetsa magazi nkupezeka kuti ulibe HIV

• Umachita chisankho choyenera posintha khalidwe lako kuti usatenge kachilomboka.

• Umakhala ndi mtendere wa mu mtima.

• Kwaiwo amene ali pa banja, kumalimbikitsa kukhulupirirana.

Ubwino oyezetsa magazi ndikupezeeka kuti uli ndi HIV

• Umaunikiridwa kufunika komathamangira kuchipatala ngati sukupeza bwino

kukalandira chithandizo choyenera.

• Umaunikiridwa ndondomeko zomwe ungatsatire kuti ukhale ndi moyo wathanzi

monga kupewa kumwa mowa ndi kusuta fodya.

• Umayesetsa kuti usapatsire anthu ena kachilomboka kapena kutenga matenda ena

opatsirana pogonana.

• Kumadya zakudya zakasinthasintha ndi cholinga choonjezera mphamvu m’thupi kuti

chitetezo chikhale chokwanira.

• Kumachita masewero olimbitsa thupi kuti lizikhala la mphamvu.

• Kupewa nkhawa makamaka kwa amene avomereza zotsatira zawo.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

63

• Kukonzeratu ndondomeko ya m’mene katundu wako adzagawidwire

ukadzakamwalira.

• Kulandira nawo mankhwala a ARV. Ndi anthu okhawo amene adakayesetsa magazi

ndipo adavomorezedwa ndi madotolo amene angalandire nawo mankhwalawa.

Komwe tingapite kukayezetsa magazi

• MACRO

• Zipatala zazikulu za boma ndi zina za zing’ono

• Zipatala za Mishoni

4. Mankhwala owonjezera chitetezo kwa omwe ali ndi HIV (ARV)

(Uthenga uwu wachokera mu kabukhu kotchedwa Mankhwala a ARV, kolembedwa ndi a

National AIDS Commission ndipo kabukhuka kalinso m’thumba la Chiyembekezo)

Kodi ma ARV ndi chiyani?

ARV ndi mankhwala omwe amathandiza kuchepetsa kuchulukana kwa tizilombo toyambitsa

matenda a Edzi m’thupi la munthu. Makhwalawa siochiritsa matenda a Edzi ayi.

Kodi oyenera kumwa mankhwala a ARV ndi ndani?

Munthu amene ali ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi ndipo adotolo atsimikiza kuti

ayambe kumwa makhwalawa. Sianthu onse omwe ali ndi kachilomboka amene angayambe

kumwa mankhwalawa. Munthu akayamba kumwa makhwalawa amamwa tsiku ndi tsiku pa

moyo wake wonse.

Ubwino wa mankhwala a ARV

• Munthu wakumwayo amakhala wathanzi.

• Munthu wakumwayo sadwala pafupipafupi matenda ena monga kutsekula m’mimba ndi

zibayo.

Ndondomeko zomwe zimatsatidwa munthu asanayambe kumwa mankhwala a ARV

Choyambirira munthu amalandira uphungu mosakakamizidwa kuchokera kwa akatswiri a

zachipatala. Cholinga cha uphunguwu ndi kukambirana ndi munthuyo za ubwino woyezetsa

magazi komanso kumulimbikitsa ndi kumuuza zomwe angachite atamva zotsatira za magazi ake.

Kenaka munthuyo amayezedwa magazi. Ndipo ngati wapezeka ndi kachilombo koyambitsa

matenda a Edzi, munthuyo amamuyeza kuchuluka kwa mphamvu ya chitetezo cha m’thupi lake

nthawi yomweyo komanso mobwereza patapita nthawi. Ndipo akapezeka kuti chitetezo chake

ndi chotsika kwambiri, munthuyo amauzidwa kuti atha kuyamba kumamwa makhwala a ARV.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

64

Munthu amene wavomerezedwa kumamwa a ARV amauzidwa zinthu izi:-

• Kuchuluka kwa makhwala amene ayenera kumamwa pa tsiku.

• Kodi ayenera kumwa kangati patsiku?

• Nanga ayenera kumwa nthawi yotalika bwanji?

• Amauzidwanso kuti sayenera kugawana makhwala ake ndi wina aliyense.

• Matenda ena omwe angayambe kudwala chifukwa cha mphamvu ya ma ARV kapena

chifukwa choti mankhwalawa sakuyanjana nawo.

• Kufunika kotsatira malangizo a akatswiri a zachipatala nthawi zonse pamene akumwa

mankhwalawa.

• Kufunika komadya zakudya zakasinthasintha.

Zoyenera kuchita ngati munthu akumamwa mankhwala a ARV

• Kukhala ndi wachibale amene ntchito yake ikhale yokumbutsa munthuyo kuti

azimwa ma ARV panthawi yake, mosalekeza komanso potsatira mulingo wake.

• Kukhala odziletsa zogonana kuopa kuonjezera tizilombo tina m’thupi kapenanso

kufalitsa kwa ena.

• Kugwiritsa ntchito makondomu moyenera nthawi zonse pamene mwafuna kugonana.

• Kumathamangira kuchipatala ngati munthuyo sakupeza bwino m’thupi mwake.

• Kumachita masewera olimbitsa thupi.

• Kumapemphera pafupipafupi ndi cholinga choti munthuyo alimbikitsidwe mu uzimu.

• Kupewa kumamwa mankhwala a zitsamba amene a sing’anga ena amanama uti ndi

wochiza Edzi.

• Kupewa kumwa mowa ndi kusuta fodya.

Anthu ena omwe angapatsidwe mankhwala a ARV ataonedwa ndi a chipatala

• Anthu amene agwiririridwa.

• Amayi ndi atsikana a pakati amene ali ndi kachilombo koyambitsa Edzi.

• Ana obadwa kwa amayi omwe ali ndi kachilomboka kale.

• Anthu amene akudwala chifuwa chachikulu cha TB.

• Anthu amene akhudzana kapena kugwira magazi a anthu ena makamaka pa ngozi.

Mankhwala a ARV tingawapeze kuti?

Ena mwa malo amene tingathe kupeza mankhwalawa ndi awa:

• Queen Elizabeth Central Hospital

• Kamuzu Central Hospital (Lighthouse)

• Mzuzu Central Hospital

• Chipatala cha Boma ku Thyolo

• Chipatala cha Boma ku Chiradzulu

• Blantyre Adventist Hospital

• African Bible College Clinic ku Lilongwe

• Chipatala cha Mishoni ku Ekwendeni

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

65

• Chipatala cha Mishoni ku Nguludi ku Chiradzulu

• Chipatala cha Mishoni cha Mulanje

• Chipatala cha Mwaiwathu ku Blantyre, ndi zipatala zina za Boma ndi za Mishoni.

5. Mkhalidwe Odzidalira, Wakhanza ndi Osakhuzidwa ndi zinthu

Kudzidalira

Makolo athu amatiphunzitsa chikhalidwe chawo tikanali ana aang’ono. Mu chikhalidwe chathu,

atsikana ndi amayi amaphunzitsidwa kukhala odzichepetsa makamaka kwa anyamata ndi

abambo.

Polankhula ndi abambo kapena anyamata, atsikana ndi amayi amayenera kugwetsa nkhope

zawo, kukhala chogwada komanso kulankhula mochepetsa mawu. Akakwatiwa, amayenera

kukwaniritsa zofuna za amuna awo kaye asanakwaniritse zawo, komanso za apongozi ndi alamu

awo ndiponso za ana a m’mbanjamo.

Khalidwe lodzidalira limaonekera ngati munthu anena kapena kuwuza ena zomwe akufuna

kapena kufuna kuchita, komanso kuganiza osachita mantha ndi kubisa. Khalidwe lotere

limathandiza munthu kukhala ndi mphamvu pa moyo wake. Anthunso amamulemekeza

makamaka ngati sakwiyitsa ena podzidalirapo.

Chithunzi 26: Nkhanza za abambo zimachepetsa mphamvu za amayi

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

66

Amayi ndi atsikana amaphunzitsidwa kukhala osadzidalira paokha. Apa tikutanthauza kuti:

• Amayenera kusiyira amuna kapena anyamata kuti aganize zochita

• Sapereka maganizo awo pa nkhani zokhuza iwo eni

• Saganizira zodzitukula pa moyo wao

• Amabisa maganizo awo ndizowawa zawo mumtima kuti pakhale bata ndi mtendere.

Anyamata ndi abambo amaloledwa kuchita zamphulupulu, kusonyeza kukwiya pokalipa

ngakhale mokuwa kapena kumenya zinthu ngakhalenso kuwopsyeza anzawo.

Chithunzi 27: Kudzidalira kwa amayi kumalimbikitsa ubwenzi ngakhale banja

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

67

Ndondomeko yothandiza kuti munthu athe kuvomera kapena kukana

• Mudziwawuza anthu m’mene mukumvera mu mtima mwanu. Mukhonza kuwawuza kuti,

'Ine m’mene ndikuganizira ndi mwakutimwakuti’ kapena kuwawuzanso kuti, “ Ine

ndikufuna chakutichakuti’’.

• Mudziyimitsa mutu wanu, khalani pansi kapena imilirani motakasuka.

• Mudzimuyang’ana munthu m’maso nthawi zonse ndipo zimene mukukamba

zidzigwirizana ndi zimene zikuwoneka pa nkhope panu.

• Mudzikamba mokweza kuti anthu amve zimene mukukambazo.

• Muphunzire kuti ndi ufulu wa munthu aliyense kunena kuti TOTO! ndipo inuyo

muphunzire kunena choncho panokha.

• Anthu akakuyamikirani kapena kukulangizani mudzimvera ndipo pa inu nokha

mudzimva bwino.

• Muzidzilemekeza nokha ndipo mudzichita zimene inuyo mukuwona kuti ndi zabwino ndi

zothandiza.

• Muphunzire kunena moleza mtima mukakwiya kuti musakhumudwitse ena.

• Osachita mantha kutsutsana ndi anthu.

Kufotokoza zimene mukufuna pogonana.

Matupi athuwatu ndi athuathu. Ifeyo tikhoza kusankha tokha nthawi imene tikufuna kuti

tigonane ndi munthu wina kapena ayi. Ndi chinthu cha nzeru kuti ifeyo tidzifotokoza momveka

bwino m’mene tikufunira kuti zinthu zikhalire pamene tikufuna kugonana ndi wina. Ndi ufulu

wa munthu wina aliyense kugonana ndi wina komanso kukana.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

68

Zowonjezera 2: Kuwunikanso momwe maphunziro a

Ulendo wa Chiyembekezo ayendera

Tikufuna kumva kuchokera kwa inu!

Tumizani fomuyi ku: BRIDGE Project, Johns Hopkins Bloomberg School of Public Health,

Centre for Communication Programs, P.O. Box 303782, Lilongwe 3, Malawi.

1. Chongani gulu la anthu omwe mwagwiritsa nawo ntchito maphunziro a Ulendo wa

Chiyembekezo

Magulu achinyamata

Magulu a m’midzi

Omwe ali ndi kachilombo ka HIV ndi odwala Edzi

Ana opemphapempha m’misewu

Atsogoleri azipembedzo zosiyanasiyana

Asing’anga

Ana asukulu

Alangizi opereka uphungu

Ogwira ntchito zogonana mwa malonda

Anthu ena

2. Mukuwona kuti maphunziro a Ulendo wa Chiyembekezo akusintha bwanji chikhalidwe

ndi zochita za ophunzirawo?

3. Kodi ophunzira anu achita kapena anena chiyani kuti mutsimikize kuti pali kusintha?

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

69

4. Pogwiritsa ntchito bukhu la Ulendo wa Chiyembekezo, ndi zinthu ziti zomwe zinayenda

bwino?

5. Ndi zovuta zotani zomwe mwakumana nazo pogwiritsa ntchito buku la Ulendo wa

Chiyembekezo?

6. Kodi munasinthapo kapena kuonjezera zinthu zina pogwiritsa ntchito buku la Ulendo wa

Chiyembekezo? Ngati munatero, kodi zomwe munawonjezerazo kapena munasinthazo

zinathandiza bwanji?

7. Ndi zinthu ziti zomwe mungakonde kuti tizisinthe kapena kuziwonjezera kuthandiza kuti

bukhuli limveke bwino?

8. Kodi mukuwona kuti inuyo kapena bungwe lanu lingafunenso maphunziro ena

owonjezera kapena thandizo lina lirilonse pogwiritsa ntchito bukuli la Ulendo wa

Chiyembekezo?

a. Inde kukufunika kutero

b. Ayi sikofunika kutero

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

70

9. Ngati muyankha kuti inde, mukufuna maphunzirowo kuti akayang’ane mbali ziti

kwenikweni? Komanso maphunzirowo akakhale a yani?

10. Mukuganiza kuti maphunzirowa akuyenera kupindulira yani?

13. Perekani ndemanga zina ngati ziripo.

Dzina lanu: .......................................................................………………………………………….

Bungwe lanu: ......................................................................………………………………………..

Keyala yanu: .......................................................................………………………………………..

Telefoni yanu: ……………………………………………………………………………………...

Fax yanu: ...........................................................................................................................................

E-mail yanu: ………………………………………………………………………..........................

Zikomo Kwambiri!

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

71

Zowonjera 3: Mabuku Owonjezera

1. Boal, A. et al (1984) Theatre of the Oppressed Pluto Press Ltd.

2. Charvet, S. (1997) Words that Change Minds Kendall/Hunt Publishing Company.

3. Gordon, G (1999) Choices – A Guide for Young People by Gill Gordon (1999) Published

by Macmillan Education.

4. Holland, R (1999) How to run the human bio-computer.

5. Hubley, J. (1993) Communicating Health Macmillan Education.

6. McDermott, I. & O’Connor, J. (1996) Neuro Lingusitic Programming and Health

Thorsens.

7. Joinet, B., Rivas C., Mugolola, T. (1995) The Fleet of Hope Association Flotille de

l'espoir, 103 av de Villiers, 75017 Paris.

8. Labouchere, P., Tweedie, I. & Fiagbey, E. (2001) Journey of Hope Ghana Users’ Guide

Johns Hopkins University/ Center for Communication Programs/ Population

Communication Services.

9. Labouchere, P. (2003a) Outcome Focus or Problem Focus Available from:

http://www.comminit.com/changetheories/ctheories/changetheories-45.html

10. Labouchere, P. (2004) Bridges of Hope Users Guide – May 2004.

11. Lusaka Interfaith Networking Group Treasuring the Gift – How to handle God’s gift of

sex – Sexual Health learning activities for religious youth groups Published by project

concern International (Zambia).

12. Malawi National HIV/AIDS Policy - A CALL TO RENEWED ACTION, 2003.

13. Malawi Bridge Project (2004) Message Harmonisation for HIV and AIDS – Message

Guide.

14. Orr, N. (2003) Positive Health – Revised and Expanded 2003 Edition Empowerment

Concepts E-mail: neil_orr@yebo.co.za.

15. Orr, N. & Patient, D. (1999) PsychoNeuroImmunology Empowerment Concepts.

16. Parker, W. et al. (2000) Living Openly: Stories and Images of HIV Positive South

Africans Beyond Awareness Campaign, HIV/AIDS and STD Department, Department of

Health, Pretoria, available on http://www.cadre.org.za/BAC/BACpdf/LivingOpenly.pdf

17. Welbourn, A. (1995) Stepping Stones Action Aid.

18. Shone, R. (1992) Creative Visualisation.

19. Witte, K. (2002) The Use of 'Fear Appeals' in Public Health Campaigns and in

Patient/Provider Encounters Available from www.comminit.com/st2001/sld-3135.html

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

72

20. Association of Christian Educators in Malawi, (2004) HIV/AIDS Communication and

Life Skills-A Teacher’ Training Manual, Domasi, Malawi Institute of Education.

21. Ministry of Education (2004), Life Skilss for HIV/AIDS A Training Manual for Secondary

Schools in Malawi, Domasi, Malawi Institute of Education.

22. Ministry of Youth, Sports and Culture Malawi, (1996), Family Life Edication Program:

Focus on Youth, A resource Guide, Lilongwe.

23. National Family Planning Council of Malawi (1999), Life Planning Skills: A Training

Manual for Young People in Malawi, Lilongwe.

24. Peace Corps Malawi, (1996) The Life Skills Manual, A Guide to Behaviour Change

Programming for Teachers, Health Worker, Facilitators and Peer Educators, Lilongwe.

25. PEACE Corps (2000) Life Skills Manual, Washington DC.

26. Population Services International, Malawi, (2002) Youth Alert Magazine, Lilongwe.

27. Light on Learning: Using PRA to explore school going Adolescents’ Views on their

Sexual and Reproductive Health.

28. Love! You can really Feel it, you know- Talking about sexuality and personal

relationships in School. Liber Distribution-Publication Stjanst, S-162 89 Stocklholm,

Sweden.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

73

ULENDO wa CHIYEMBEKEZO

Maphunziro Othandiza Kusankha

Mwanzeru Polimbana

ndi

Mliri wa Edzi

Bukhu Lophunzitsira Kudziteteza ku Edzi

m’Malawi

Olemba

Peter Labouchere, Glory Mkandawire ndi Kirsten Böse.

“NDITHA!”

… kunena mosabisa za Edzi, kudziletsa

kugonana, kukana zogonana,

kukhala ndi ukhondo, kukhala opanda mantha,

kukhala m’chiyembekezo nkudzakwaniritsa

tsogolo langa.

ZA MBIRI YA BUKHULI

Bukhuli linalembedwa ndi sukulu ya ukachenjede ya Johns Hopkins Bloomberg School of Public

Health Centre for Communication Programs ku America.

Bukhu la Ulendo wa Chiyembekezo ndi chida champhamvu chothandiza a Malawi kusankha

mwanzeru polimbana ndi mliri wa Edzi ndi kukhala ndi thanzi kuti adzathe kukwaniritsa zolinga za

m’moyo mwawo.

Bukhuli lakonzedwa ndi chithandizo chochokera ku United States Agency for International

Development (USAID).

Bukhuli lidalembedwa ndi kusindikizidwa ndi Johns Hopkins Bloomberg School of Public Health

Centre for Communication Programs (CCP): M’chaka cha 2005.

Mukhoza kusindikiza bukhu lino ndikumaligwiritsa ntchito mutafuna, koma musachite malonda ndi

mabukhu omwe mwasindikizawo, muwagawe mwaulere. Posindikiza mabukhu anuwo vomerezani

kuti maganizo ali mabukhuwo analembedwanso ndi a CCP, a Peter Labouchere komanso a Bernard

Joinet.

Ndemanga pa bukhuli zikhoza kutumizidwa kwa:

The Country Representative

John Hopkins Bloomberg School of Public Health Centre for Communication Programs

PO Box 30782

Lilongwe, Malawi

Tel. : (265) 01 750 733 / 750 553

Fax : (265) 01 750 496

E-mail : kbose@malawibridge.org

Ngati mukufuna kudziwa zambiri zokhudza zipangizo ndi kaphunzitsidwe pogwiritsa ntchito bukhuli

mukhoza kufunsa awa:

1. Peter Labouchere

HIV/AIDS Training Consultant

P.O Box 131

Victoria Falls

Zimbabwe

Tel: (263) 13 43254

Fax: (263) 13 43254

E-mail: petrel@mweb.co.zw

2. The Director for Africa Division

Johns Hopkins Bloomberg School of Public Health Centre for Communication Programs

111 Market Place, Suite 310

Baltimore, Maryland 21202 – 4012

USA

Tel: (410) 659 6300

Fax: (410) 659 6266

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

ii

ZA M’KATIMU

Masomphenya a BRIDGE Project pa za Togolo la Malawi. ………….…………………… …......v

Mau Oyamba………………………………………………………………………………………… vi

Mau Othokoza………………………………………………………………………………………..vii

Ulendo wa Chiyembekezo: Mau Otsogolera……………………………........................................viii

Malangizo kwa phunzitsi……………..……………………………………………………………...xii

Nthabwala ndi masewero ochotsa tulo...…………....................…….. ……………………………xix

Gawo Loyamba: Kumvetsa bwino za HIV ndi Edzi……………………………...…………………1

Chochita 1A: Moto Olusa……………………………………………………………………………....1

Chochita 1B: Ndani ali ndi kachilombo ka HIV?.……………..……...………………………………..4

Chochita IC: Chimachitika ndi chiyani m’thupi la munthu amene ali ndi HIV kapena ayi? …...……..6

Chochita 1 D: M’mene HIV ingafalikire…….......................................................................................10

Gawo Lachiwiri: Timilato………...…………………………………………………………………14

Chochita 2A: Kuwoloka pa milato ………………………………………..………………………….15

Chochita 2B: Kuwoloka pa timilato kwa anthu omwe ali ndi HIV...……….……..………………….22

Gawo Lachitatu: Chilumba cha Tsogolo……………….....………………………………………..24

Chochita 3A: Chilumba cha Tsogolo………………………….…………………………………........24

Gawo Lachinayi: Ulendo wa Chiyembekezo…………………………………………………….....33

Chochita 4A: Kugwiritsa ntchito makadi ndi mabwato a Ulendo wa Chiyembekezo………………...33

Gawo Lachisanu: Zochitika m’njira ya ku Chilumba cha Tsogolo……………………………....38

Kukambirana Kudzera m’Zisudzo (Forum Theatre).…………………………………………............38

Chochita 5A: Kudziletsa kugonana.…………………………………………………………………..43

Chochita 5B: Kukhulupirika m’banja kapena pa bwenzi……………………………………..............45

Chochita 5C: Kugwiritsa ntchito kondomu……………………………………………………….......46

Kagwiritsidwe ntchito ka kondomu ya amuna…..………………………………………………….....50

Kagwiritsidwe ntchito ka kondomu ya akazi.…....................................................................................52

Kukambirana za kondomu……………………………………………….…………………………....54

Chochita 5D: Kuyezetsa magazi ndi kulandira uphungu mosaumirizidwa................………………...55

Chochita 5E: Zomwe anthu amene ali ndi HIV ndi odwala Edzi, mabanja, ngakhalenso anansi awo

ayenera kudziwa ndi kuchita………………………………………………………………………......57

Zowonjezera 1: Zofunika kuti Aphunzitsi adziwe………………………………………………....59

Matenda opatsirana pogonana …………………..………………………………………………….....59

Kachilombo ka HIV ndi matenda a Edzi………………………………………………………..….....60

Kulandira uphungu ndi kuyezetsa magazi mosaumirizidwa………………………………………......62

Mankhwala owonjezera chitetezo kwa omwe ali ndi HIV (ARV)………………………………….....64

Mkhalidwe Odzidalira, Wankhanza ndi Osakhuzidwa ndi zinthu………………………………….....66

Zowonjezera 2: Kuwunika ntchito yogwiritsa phukusi la Chiyembekezo (HopeKit) …………...69

Zowonjezera 3: Mabuku Owonjezera……...……………………………………..………………...72

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

iii

Masomphenya a BRIDGE Project pa za Tsogolo la

Malawi

AMalawi tonse tigwirane manja pokonza tsogolo labwino limene

aMalawi onse:

• Akhale ndi ufulu ndi mphamvu zosankha pankhani zokhudzana ndi

kugonana molingana ndi zikhulupiriro zawo.

• Akhulupirire ndi kukhala ndi chiyembekezo kuti akhoza kukhala ndi

tsogolo labwino ngakhale nthawi ino ya mliri wa EDZI.

• Adziwe kuti mliri wa EDZI ukukhudza aliyense.

• Akhale ndi udindo otengapo mbali polimbana ndi mliri wa EDZI.

• Akambe poyera zokhudza HIV ndi EDZI osawopa kusalidwa ndi ena.

• Agwire limodzi ntchito yothandiza kuthetsa kusiyana pakati pa

atsikana ndi anyamata popereka mphamvu kwa atsikana ndi amayi.

• Akhale ndi chiyembekezo m’miyoyo yawo komanso m’madera awo

polimbana ndi kuthetsa EDZI.

• Akhale ndi chikondi ndi kuthandiza anthu omwe ali ndi HIV kapena

EDZI.

• Akondwere kuti atengapo mbali pothandiza kukwaniritsa tsogolo la

Malawiri.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

iv

MAU OYAMBA

Powona m’mene HIV ikufalira kuno ku Africa komanso m’mene ikusakazira miyoyo ya anthu,

pakufunika kuchitapo kanthu kuti tigonjetse matenda amenewa. Bukhu la Ulendo wa

Chiyembekezo ndi chimodzi mwa zida zomwe mabungwe ngakhalenso anthu angathe kugwiritsa

ntchito potengapo mbali kufalitsa uthenga odziteteza ku mliriwu komanso posamalira amene ali

kale ndi matendawa.

Ulendo wa Chiyembekezo ndi mbali imodzi yomwe Malawi BRIDGE Project akugwiritsa ntchito

poyesa kuthandiza anthu kuti adziteteze ku kachilombo ka HIV. Ntchito ya BRIDGE Project

ikulimbikitsa m’mene anthu angapewere HIV. Ntchito ya pulojekitiyi ikugwiridwa ndi Johns

Hopkins Bloomberg School of Public Health Centre for Communication Programs mogwirizana

ndi Save the Children US. Cholinga cha BRIDGE Project ndi kuchepetsa kufala kwa

kachilombo ka HIV pothandiza a Malawi kuonjezera pa zomwe akudziwa za Edzi kuti akhalenso

anthu amene akuchitapo kanthu kupewa matendawa; kuthandizana ndi mabungwe ena kuti

akwaniritse mfundo zimene adakhazikitsa polimbana ndi matenda a Edzi; kuthandiza anthu kuti

akhale ndi khumbo loyembekezera tsogolo labwino.

Atsogoleri a ndale, mafumu komanso ena osiyanasiyana tsopano akuzindikira ndipo akutengapo

mbali kuwuza anthu kuti adzikamba zamliriwu mosabisa, potero tidzathandizana kulimbana ndi

mliriwu. Mabungwe osiyanasiyana komanso magulu ena a anthu ali nawo pankhondo imeneyi,

kuwuza anthu makamaka achinyamata kuti asinthe khalidwe lomwe lingatitengere HIV

kupyolera m’maphunziro osiyanasiyana.

Cholinga cha bukhu la Ulendo wa Chiyembekezo ndi kulimbikitsa ntchito zomwe zikuchitika kale

ndi mabungwe komanso magulu a anthu polimbana ndi mliri wa EDZI muno m’Malawi. Bukhuli

likugwiritsa ntchito njira zina zosangalatsa pophunzitsa kuti kufala kwa mliriwu kuchepe. Pakali

pano anthu oposa 70,000 amatenga kachilombo ka HIV m’chaka chilichonse muno m’Malawi.

Bukhuli likukamba za “Mabwato a Ulendo wa Chiyembekezo”, mfundo yomwe Bambo

Benard Joinet wa Katolika pamodzi ndi a Jose Cantal, a Theodore Mugolola ndi ena analemba

ndipo lagwiritsidwa ntchito m’mayiko osiyanasiyana. Bukhu la Ulendo wa Chiyembekezo

lagwiritsa ntchito njira zina zatsopano zophunzitsira poyerekeza Timilatho ndi Chilumba cha

Tsogolo. A Peter Labouchere ndiwo amene anamasulira njirazi ndi kuzilemba bwinobwino

m’bukhuli.

Bukhu la Ulendo wa Chiyembekezo la Malawi lalembedwa potengera bukhu la mtundu omwewu

lomwe linalembedwa ku Ghana.

Bukhuli layesedwa muno m’Malawi ndi anthu komanso mabungwe osiyanasiyana kuti likhaledi

loyenera kwa a Malawi. Zomwe anthu amene analiyesa bukhuli anena zasonyeza kuti ndi

losavuta, ndi lomveka bwino, ndipo lingagwiritsidwe ntchito ndi magulu osiyanasiyana pa nkhani

za HIV ndi matenda a EDZI.

Bukhu la Ulendo wa Chiyembekezo ndi chida cha mphamvu chothandiza anthu ndi magulu

osiyanasiyana kukambirana mwakuya zokhudza mliri wa Edzi. Tiri ndi chikhulupiriro kuti

bukhuli lithandiza kuti anthu azindikire za mliri wa EDZI ndiponso kuti asinthe makhalidwe

omwe angaike miyoyo yawo pachiswe. Tikutsimikiza kuti bukhuli ndi lothandiza kwa onse

amene akukhuzidwa ndi miyoyo ya anthu a m’Malawi komanso m’mayiko ena pa dziko lonse.

Kirsten Böse

Country Representative

Johns Hopkins Centre for Communication Programs.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

v

MAU OTHOKOZA

Alembi a bukhu la Ulendo wa Chiyembekezo akuthokoza kwambiri anthu awa: a Evelyn Lemani, katswiri

amene adatanthauzira buku loyamba la Ulendo wa Chiyembezo kuti ligwirizane ndi chikhalidwe cha a Malawi

lomwe lidayesedwa ku Kambiri m’boma la Salima; a George Alufandika (Save the Children/BRIDGE) ndi a

Edward Chakhwana (MANASO) potengapo gawo lalikulu kuwongolera zomwe zalembedwa m’bukuli; a Jane

Brown, a Ketan Joshi, a Isabelle Sanche ndi a Lisa Folda ogwira ntchito ku CCP ndiponso a Kent Mphepo, a

Patrick Phoso, a Telina Matabwa ndi a Towera Kachingwe ogwira ntchito ku BRIDGE Project pothandizira zina

ndi zina pa ntchito yolemba bukhuli; a Shadreck Chikoti pothandiza kutanthauzira bukhuli mu Chichewa.

Alembi a bukhuli akuthokozanso Gill Gordon powavomereza kuti agwiritse ntchito bukhu lawo la Choices;

Petra Rohr-Rouendaal popereka zojambula ziri mbuku lino ndipo a Macmillan Education Ltd pololeza kuti

tikhoza kugwiritsa ntchito zithunzizi. Alembiwa akuthokozanso a Augusto Boal chifukwa cha luso lomwe

adalipanga ku Latin America lotchedwa “ Theatre of the Oppressed” lomwe ndi maziko a zokambirana

kudzera m’dzisudzo “Forum Theatre”.

Anthu ambiri athandiza kwambiri kuti bukhu lino lifike pamene lafikapa ndipo anthuwo ndi awa:

Bambo Bernard Joinet omwe adali oyambirira kubweretsa chiganizo cha Mabwato a pa Ulendo wa

Chiyembekezo chomwe chiri m’gawo lachinayi m’bukhuli ndipo iwo adavomerezanso kuti chiganizo chawocho

chikhoza kugwiritsidwa ntchito m’bukhuli; a Cantal Rivas amene adabweretsa maganizo ogwiritsa ntchito

chinsalu ndi makadi; ojambula a Theodore Mugolola a ku Tanzania, a Solomon Titus-Glover a ku Ghana ndi a

Rodgers Chilemba a ku Malawi pojambula anthu a pamakadi komanso Ike Kwamena Essilfie-Essel a ku Ghana

amene adajambula chithunzi chomwe chili pachikuto cha bukhuli.

Alembi akuthokoza mabungwe ena popereka zida zina za m’phukusi la chiyembekezo “Hope Kit”: a PSI

Malawi-Pakachere popereka mabuku a Kukhala m’Chiyembekezo ndi HIV ndi Edzi ndi a National AIDS

Commission popereka timabukhu ta Mankhwala a ARV ndi Kulandira uphungu ndi kuyezetsa magazi

mosaumirizidwa. Alembiwa akuthokozanso a Society for Women and AIDS in Malawi - Africa Division, a

Family Planning Association of Malawi ndi a PSI Malawi-Youth Alert pololeza kugwiritsa ntchito ma poster

awo; akuthokozanso omwe adalemba bukhu la Positive Living pololeza kugwiritsa ntchito zinthunzi ndi nkhani

za m’bukhu lawo za anthu a ku South Africa omwe ali ndi HIV.

Akuthokozanso anthu amene adatenga mbali yayikulu pa nthawi imene bukhuli linkayesedwa kugwiritsidwa

ntchito kwa nthawi yoyamba; a Peter Labouchere, a Glory Mkandawire (CCP/BRIDGE), a Joyce Wachepa

(Save the Children/Umoyo Network) , a Akuzike Tasowana (MANASO) komanso omwe amaphunzira

kugwriritsa ntchito bukhuli pa nthawi yoyesayo omwe ndi awa:

Joseph Sambaudye (Maphunziro Foundation); Timothy Bonyonga (Banja La Mtsogolo); Levson Phiri (Save the

Children/ BRIDGE); William Jiya (ICOCA); Thembi Thadzi (Counseling of Adolescent & Youth

Organization); Solomon Nyirenda (MANASO); Barton Kafanikhale (Kasungu AIDS Support Organization);

Machilika Matemba (Tsogolo la Ana); Steve R Ndiwo (REFORD); Margaret Sibale (Nkhotakota AIDS Support

Organization); Harold Chilikutali (Nzama Parish HBC); Violet Sichinga (Friends of Mzuzu Community);

Edward Chakhwana (MANASO); George Alufandika (Save the Children/BRIDGE); Blandina Tauzi

(Tikoleraneko); Jacob Kambemba (NAPHAM); Maggie Kambalame (Save the Children); Saiti Jambo

(Muslim Association of Malawi) ndi Steve Mfune (Salima AIDS Support Organization).

Zinthunzi zambiri mbukhuli ndi za anthu amene tawatchulawa ndipo zidatoledwa pa misonkhano

yosiyanasiyana nthawi imene bukhuli linkayesedwa ku Salima.

Potsiriza tithokoze Johns Hopkins Bloomberg School of Public Health Centre for Communication Programs

(CCP) omwe anathandiza kulemba bukhuli komanso United States Agency for International Development

(USAID) omwe adapereka ndalama zogwiritsira ntchito polemba bukhuli.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

vi

ULENDO wa CHIYEMBEKEZO: Mau Otsogolera

Bukhu la Ulendo wa Chiyembekezo ndi chida champhamvu chomwe chingathandize aliyense

kutenga mbali popewa mliri wa matenda a Edzi. Njirayi imathandiza onse ogwiritsa ntchito

kulimbikitsa mtima wofunitsitsa kuthana ndi mabvuto a mtundu uli onse mu njira yoyenera.

Dziko la Malawi ndi limodzi mwa mayiko ambiri pa dziko lapansi amene akhudzidwa

kwambiri ndi mliri wa matenda a Edzi. Mliri wa Edzi watenga kale miyoyo ya anthu oposa

555,000 m’dziko la Malawi kuyambira pamene matendawa anazindikiridwa m’dziko lino

m’chaka cha 1985.

Ulendo wa Chiyembekezo ukusonyeza njira zopatsa a Malawi mphamvu zosankha moyenera

poganizira zogonana. Njirazi zikulingana ndi zomwe achinyamata ngakhalenso akulu

amakumana nazo m’moyo mwawo pankhani yogonanayi.

Ulendo wa Chiyembekezo wayerekezedwa ndi izi:

Madzi kapena mtsinje m’mene muli nyama zolusa monga ng'ona, njoka ndi zina zomwe

zikuimirira kachilombo ka HIV koyambitsa matenda a Edzi ndi matenda ena ndi zovuta zina

m’moyo wa munthu.

Mabwato atatu ndi timilato tamitundu itatu – zimenezi zikuyimira njira zitatu zothandiza

kupewera matenda a Edzi za:

� Kudziletsa

� Kukhulupirika kwa mkazi kapena mwamuna m’modzi.

� Kugwiritsa nchito Kondomu.

Cholinga cha bukhu la Ulendo wa Chiyembekezo

• Kuthandiza achinyamata m’dziko lino kuthetsa matenda a Edzi.

• Kuthandiza anthu onse amene afuna kukhala pa ubwenzi ndi mkazi kapena

mwamuna kuti asatenge matenda a Edzi.

• Kulimbikitsa achinyamata komanso akuluakulu kusankha njira zopewera

matenda a Edzi popewa kugonana, pokhulupirika kwa mkazi kapena

mwamuna m’modzi komanso pogwiritsa ntchito Kondomu.

M’mene Cholingachi chingakwaniritsidwire

Kuti cholingachi chikwaniritsidwe, bukhu la Ulendo wa Chiyembekezo likusonyeza izi:

• Kulola kukamba poyera komanso mwatchutchutchu zokhudza umoyo waubereki ndi

za matenda a EDZI ndi kachilombo ka HIV.

• Polola ophunzira kutengapo mbali mosangalala ponena nthano ndi pochita masewero

ena osiyanasiyana.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

vii

• Posonyeza ophunzira njira zosiyanasiyana zopatsa mphamvu yodzitetezera ku

matenda a Edzi (kudziletsa, kukhuluprika kwa mwamuna kapena mkazi mmodzi, ndi

kugwiritsa nchito kondomu).

• Kulimbikitsa a Malawi kusankha njira zoyenera zosamalirira miyoyo yawo kuti

akwaniritse zolinga zawo.

• Kugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana zothandiza anthu kusintha khalidwe lomwe

lingawatengere kachilombo ka HIV.

• Kuthandiza anthu kukhala ndi mphamvu zomakambirana pa nkhani zogonana

pachibwenzi komanso pabanja.

• Kulongosola mwatsatanetsatane zoyezetsa magazi ndi kulandira uphungu pa za

matenda a Edzi.

• Kupitiriza kukumbutsa anthu kuti awonetse chikondi kwa anthu omwe ali ndi

kachilombo ka HIV kapenanso omwe akuvutika ndi matenda a Edzi.

Amene adagwiritsapo ntchito bukhu lino ndi zomwe akukamba

Bukhu la Ulendo wa Chiyembekezo lakhala likugwiritsidwa ntchito m’mayiko ena monga

Zambia, Ghana, South Africa, Sri Lanka, France ndi Britain. Tsopano tiri ndi mwayi kuti eni

bukhu loyambirirawo adatilola kuti tikhoza kusintha zina ndi zina kuti zomwe zili m’bukhu

loyambalo zigwirizane ndi kuno ku Malawi.

Ku Malawi kuno msonkhano woyambirira wa Aphunzitsi udachitika mu January 2005 ndipo

udathandiza kuwunikira kuti bukhuli likhale m’mene lilirimu.

Chithunzi 1: Msonkhano oyamba wa Aphunzitsi a Ulendo wa Chiyembekezo ku Malawi

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

viii

Ndemanga zokhudza bukhuli

Pa nthawi yoyesa bukhuli kuno ku Malawi ndi pomwe adagwiritsa ntchito mabuku

oyamba ku mayiko ena anthu adapereka ndemanga zawo zokhudza zochitika m’bukhu la

Ulendo wa Chiyembekezo.

Ndemanga zina za ku Malawi zidali motere:

“Anthu anakhudzidwa kwambiri ndi zochitika zimene ziri mphukusi la Ulendo wa

Chiyembekezo kotero kuti ambiri asintha mfundo zimene adamanga. Ulendo

wa Chiyembekezo wabweretsadi kusintha khalidwe losayenera. Ulendo wa Chiyembekezo

ukuthandiza anthu kukhala m’chiyembekezo ndi HIV ndi Edzi”

Magaret Sibale, Nkhotakota AIDS Support Organization, Nkhotakota.

“Ine ndikuganiza kuti kukamba za tsogolo ndi chinthu chomupangitsa munthu kuzindikira za

udindo wake komanso kumudziwitsa kuti ndichinthu cha nzeru kuti adziteteze kumatenda a

Edzi. Zochitika za m’bukhu la Ulendo wa Chiyembekezo ndizosavuta kuzitsata.”

George Alufandika, Save the Children US, Salima.

“Ine ndinakhudzidwa kwambiri ndi zochitika za m’mbukhu limeneri makamaka zokhuza

Chilumba cha Tsogolo kotero kuti tsopano ndinapanga chiganizo kuti ndikwaniritse tsogolo

langa. Bukhuli ndi labwino kwambiri ndipolosavuta kuligwiritsa ntchito.”

Thembi Thadzi, Counseling of Adolescent & Youth Organization, Lilongwe.

“Ine ndimaganiza kuti ndidzakhala oyitanira ma mini basi mpaka kalekale koma nditapanga

nawo sewelo la Chilumba cha Tsogolo ndaona kuti nditha kisitha tsogolo langa ndi

kulikwaniritsa bwinobwino.”

Mnyamata oitanira ma mini basi ku Balaka.

Ndemanga zina za ku mayiko ena zidali motere:

"Bukhu la Ulendo Wa chiyembekezo ndi chida cha mphamvu chophunzitsira za kuwopsya

kwa

kachirombo ka HIV ndi matenda a EDZI. Limathandiza anthu kumvetsa bwino za mliri

umenewu ndiponso kusintha mkhalidwe. Ophunzira amaphunzira kudzera m’masewero

osiyanasiyana mosangalala. Ndi bukhu losangalatsa ndithu”

Maurice Acquaye, AIDS Co-ordinator, salvation Army, Ghana.

“Sindinagwiritsepo ntchito kondomu koma m’mene ndamveramu kuti ikhoza kunditeteza

monga mmene mlatho uchitira, ndili okonzeka kukagula makondomu asanu lero masana”

Mayi wochokera ku Begoro, Ghana.

“Mafunde ndi zilumba zomwe zatchulidwa m'bukhuli ndi zinthu zomveka bwino ndithu

makamaka pamene tikhala ndikulangiza anthu ofuna chithandizo. Ndagwiritsa ntchito

Chilumba Cha Chiyembekezo ndi anthu amene anali ndi nkhawa komanso otaya mitima”

Theresa Matafwali, Wopereka Uphungu, Zambia.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

ix

Phukusi la Ulendo wa Chiyembekezo (Hope Kit)

Pali phukusi lomwe muli zinthu zosiyanasiyana kuphatikizapo zomwe zimagwiritsidwa

ntchito mothandizira bukhu lino. Phukusiri liri ndi zinthu izi:

1. Bukhu la Ulendo wa Chiyembekezo.

2. Bukhu la Mauthenga a HIV ndi Edzi.

3. Timatabwa topinda (milingo yake 22mmx 22mm x 1.8mm mulitali) Kathabwa kena ndi

koyera (white) mbali ina ndi yabuluwu (blue). Pamene kathabwa kena ndi kachikasu

(yellow) konse.

4. Nsalu yayikulu yabuluwu yojambulidwa mabwato atatu a mtundu oyera, buluwu ndi

chikasu.

5. Pepala lalikulu mulingo wa A4 losonyeza nyanja momwe muli anthu, mabwato, ng'ona

ndi zilumba.

6. Makadi 10 osiyanasiyana okhudza za HIV ndi matenda ena opatsirana pogonana oti anthu

akambirane.

7. Makadi awiri a ng’ona, awiri a mvuu ndi khadi limodzi la njoka.

8. Khadi limodzi la Chilumba.

9. Zithunzi zodulidwa zokwana 25 pomwe pali anthu osiyanasiyana komanso a zaka

zosiyana.

10. Makadi 10 a A4 okamba za anthu amene ali ndi HIV.

11. Bukhu lotchedwa “Kukhala m’Chiyembekezo ndi HIV ndi matenda a Edzi”.

12. Timapepala tokamba za Mankhwala a ARV ndi Kulandira uphungu ndi kuyezetsa magazi

mosaumirizidwa.

13. Zikwama ziwiri za pulasitiki zoyikamo zinthu zimene zatchulidwa pa 7 kulekeza 12.

14. Chifanizo cha maliseche aamuna (Mbolo) chosema.

Powonjezera zinthu zomwe zili m’phukusiri, ophunzitsa ayeneranso kukhala ndi zinthu izi:

• Mapepala okwanira munthu aliyense pomwe adzajambulepo Chilumba cha Tsogolo.

• Zolembera.

• Makondomu ndi zina zomwe angaphunzilirepo kugwiritsa ntchito kondomu monga

maliseche a bambo osema.

• Mafomu olembapo m’mene maphunziro akuyendera.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

x

MALANGIZO KWA OPHUNZITSA

Ndani angaphunzitse pogwiritsa ntchito bukhu la Chiyembekezo?

Bukhu limeneli angagwiritse ntchito anthu monga awa:

• Ophunzitsa achinyamata

• Aphunzitsi a sukulu

• Anamwino ndi Alangizi a zaumoyo

• Aphunzitsi a zachitukuko

• Opereka uphungu

• Alangizi a zamalimidwe

• Aphunzitsi a Sukulu za Kwacha

• Ndi ena omwe angaone kuti bukhuli lingawathandize

Zomuyenereza munthu kuti aphunzitse mwadongosolo pogwiritsa ntchito

bukhu la Ulendo wa Chiyembekezo

• Luso lophunzitsa pogwiritsa njira zoti anthu amasuke

• Kudziwa za kachilombo ka HIV ndi matenda a Edzi

• Kudziwa chilankhulo cha ophunzira onse

• Kudziwa kuthandiza ophunzira munjira zoti aphunzilire

M’malo amene bukhuli lingagwiritsidwe ntchito

Bukhu la Ulendo wa Chiyembekezo lalembedwa ndi kugwiritsidwa ntchito m’malo osiyanasiyana:

m’misonkhano, pophunzitsa akuluakulu, achinyamata, komanso amipingo. Mukhozanso kuligwiritsa

ntchito ndi anthu omwe sadziwa kulemba kapena kuwerenga. Nazi zitsanzo zamagulu osiyanasiyana

momwe bukhuli lingagwiritsidwe ntchito:

• M’misonkhano yosiyanasiyana

• M’magulu a achinyamata

• M’sukulu

• M’magulu a chipembedzo

• M’magulu a ana osowa mabanja owasamalira ndipo amayendayenda m’misewu ndi

mmatawuni

• M’magulu ophunzitsa za Edzi

• M’magulu othandiza anthu omwe ali ndi kachilombo ka HIV kapena matenda a Edzi

• Magulu a asing'anga azitsamba kapena azamba kuti awuze anthu zowona za kachilombo ka

HIV ndi matenda a Edzi

• M’malo momwe mumapezeka galimoto, maminibasi ndi anthu oyenda maulendo awo

• Popereka uphungu kwa munthu kapena mabanja amene ayezetsa magazi awo pankhani za

Edzi

• Pabanja pokambirana za matenda a Edzi

• Pocheza ndi anzathu m’sukulu ngakhale ku ntchito pa nkhani za matenda a Edzi

• M’malo omwera mowa

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

xi

Kugwiritsa ntchito bukhuli ndi anthu omwe ali ndi HIV kapena EDZI

Bukhuli ndi chida champhamvu chomwe chingagwiritsidwe ntchito ndi anthu omwe ali ndi

kachilombo ka HIV. Gawo la Chilumba cha Chiyembekezo ndi lomwe liri lofunika kwambiri

chifukwa ndi lopereka chilimbikitso kwa munthu amene ali ndi HIV kuti akhoza kukhala ndi

moyo wabwino popanga zinthu zoyenera komanso pokhala ndi chikhulupiriro poganizira za

tsogolo lake. Kudziteteza pogwiritsa ntchito kondomu ndi njira yomwe anthu awa

angadzitetezere kuti asatenge tidzilombo tina ta HIV komanso kuteteza ena kuti asatenge

kachilombo ka HIV.

Kuganizira zokhudza akazi ndi amuna (Gender)

Nkofunika ndithu kuganizira zovuta ndi zofuna amayi komanso abambo zokhudza matupi

awo komanso moyo wawo okhudza zogonana. M’mayiko ambiri ngakhalenso muno

m’Malawi, abambo amapezeka kuti akukhala ndi mphamvu zolamulira azimayi. Pachifukwa

ichi, amawoneka ochepa mphamvu ndipo sadziwa kusamalira ndi kuteteza matupi awo. Izi

zimaonekeranso makamaka pamene pali nkhani yofuna kugonana. Ichi nchifukwa chake

amayi ambiri akupezeka ndi kachilombo ka HIV kuposa abambo. Izi ziri chomwechi

makamaka m’mayiko akum’mwera kwa Africa m’mayiko monga Malawi. Pa nkhani

yomweyi, Ripoti ya ofesi ya UNAIDS la Global Epidemic 2000 linasonyezanso kuti atsikana

ambiri a zaka zapakati pa 15 mpaka 19 ali ndi kachilombo ka HIV kuposa anyamata a

misinkhu yomweyi.

Choncho pamene mukukambirana musaiwale kuti zofuna, zochita, udindo ndi khalidwe la

akazi ndi losiyana ndi amuna. Mphunzitsi alimbikitse akazi ndi amuna kuti azikambirana

momasuka nkhani yokhudza zogonana akakhala pabanja kapena paubwenzi.

Kagwiritsidwe ntchito ka zigawo m’bukhuli

Zigawo ndi zochitika za m’bukhu lino zayikidwa m’ndondomeko yake yomwe mukhoza

kuitsatira. Koma gawo ndi chochita chilichonse ndi choima pachokha. Ngati inu mukuwona

kuti mungathe kuchita bwino lomwe potsatira ndondomekozi, muli omasuka kutero ngati

zikugwirizana ndi zokhumba zanu. Chochita chilichonse chikhoza kuyima pa chokha.

Choncho mukhoza kusankha gawo kapena chochita mosatsatira ndondomeko ija malingana

ndi zosowa za gulu lanu kapena nthawi yomwe muli nayo.

Kukula kwa gulu

Pogwiritsa ntchito bukhuli, ndibwino kuti magulu asakhale aakulu kupyolera anthu makumi

atatu(30) kuti ophunzira onse athe kutengapo mbali. Magulu ochepera monga a anthu awiri

mpaka asanu zithunzi zochepera za mulingo wa A4 ndizo zoyenera kugwiritsa ntchito

kusiyana ndi nsalu yabuluwu. Zithunzi zimenezi zingagwiritsidwenso ntchito ngati malo

ophunzirira ndi ochepa.

Bukhuli ndilongokutsogolerani, Sibukhu la malamulo

ayi!

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

xii

Mungakhale bwanji mphunzitsi wabwino?

Anthu ambiri amaganiza kuti akayima pakati pa anthu ndi kuwatsogolera m’zochitika ndiye

kuti iwo ndi aphunzitsi abwino. Izi sizowona. Pali zinthu zingapo zofunikanso kudzitsa

kuwonjezera pa kutsogolerako. Zinthuzi zafotokozeredwa mu chithunzi chotsatirachi.

Unikani

maphunziro

Kodi njira kamanso

nthawi imene

ndingawunike ngati

maphunziro

akuyenda bwino ndi

iti?

Tsogolerani

maphunziro

Kodi ndipannge

bwanji kuti

maphunzirowa

ayende bwino?

Funsani zosowa

zamaphunziro za

ophunzira

Kodi zosowa za

maphunziro za

ophunzira ndi ziti?

Kalondolondo-

kuwonetsetsa kuti

maphunziro

akutsatidwa

Kodi ndingathe

bwamji kuti ndidziwe

ngati maphunzirowo

akuyenda bwino?

Konzani

ndondomeko/njira

konzekerani

Kodi ndikwanitsa

bwanji zolinga za

pamapmaphunzirozi?

Zolinga za

maphunziro

Kodi ophunzira

adziwe ndipo athe

kuchita ziti pakutha pa

maphunziro?

Chithunzi 2: Ndondomeko yoti Aphunzitsi atsatire potsogolera maphunziro

Monga m’mene mwawoneramu ndondomekoyi imakhala yozungulira ngati chingerengere,

kotero kuti zimene umaphunzira kuchokera ku zomwe unawunika m’mbuyo zimakuthandiza

kuti ukonze bwino phunziro lako la mtsogolo.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

xiii

1. Fufuzani zosowa za maphunziro za ophunzira

Musadakumane ndi gulu lanu mufufuze kaye zinthu izi:

� Kodi pali kale zinthu zokhudza HIV ndi matenda a Edzi zimene ophunzira anga

akufuna kuti adziwe?

� Nanga zimene akuzidziwa kale iwowo ndi zotani? Ali ndi luso lamtundu uliwonse?

Nanga maganizo awo ndi otani?

� Ndichiyani chimene chingawapangitse iwo kuti asamvetse zimene ndi kuphunzitsa?

� Chimene iwo akuyembekezera pa maphunziro amenewa ndi chiyani?

Ndi chinthu cha nzeru kuti inu mucheze ndi akuluakulu ena a m’gulu lanu. Mukhoza

kuwafunsa mafunso kuti mudziwe zina za iwo.

Pofuna kufufuza luso la anthuwo muzindikire kuti pali kusiyana pakati pa kuzindikira kuti

munthu akhoza kuchita chinthu ndi kuchichitadi chinthucho. Mwachitsanzo, anthu ambiri

amanena kuti amadziwa kugwiritsa ntchito kwa kondomu pamene chilungamo chake ndi

chakuti anthu ambiri sadziwa kagwiritsidwe ntchito ka kondomu.

Pofunsa mafunso osamafunsa mafunso amene munthu akhoza kuyankha ndi “EYA” kapena,

“AYI.” Anthu azikhala ndi mwayi ofotokozera akapatsidwa funso.

Zochita zina m’bukhu lino, monga chochita 4A, zikhoza kuthandiza kuti mudziwe bwino

lomwe zinthu zimene zimachitika m’dera limene inuyo mukuphunzitsalo. Chochita 4A

chikukakamiza anthu a m’dera limene mukuphunzitsalo kuti akambe zimene zimachitika

m’dera lawo.

2. Zolinga za maphunziro

Muzidziwa zenizeni zimene mukufuna kuphunzitsa pa phunziro limene mukukonzekera

kuphunzitsa. Kodi pamapeto ake aphunziro lanu mukufuna ophunzira adziwe chiyani?

Zimenezi muzidzidziwiratu musadayambe kuphunzitsa.

3. Kukhazikitsa ndondomeko, ndi kukonzekera

Muzidziwiratu njira imene mugwiritse ntchito pophunzitsa. Koyambirira kwa phunziro liri

lonse m’bukhuli kuli malangizo a m’mene mungaphunzitsire.

a. Musadayambe kuphunzitsa

• Werengani kaye zonse zimene mukuyenera kuphunzitsa.

• Kodi ndi zochita ziti zimene mukufuna kuchita, nanga ndondomeko yake ndi

yotani? Zigwirizana bwanji ndi zosowa za ophunzira anu?

• Panokha yeserani m’mene muzikachitira pophunzitsa.

• Muyeserenso panokha m’mene mukuganizira kuti ophunzira akhoza

kuyankhira mafunso.

b. Kukonza zipangizo ndi malo

• Onetsetsani kuti muli ndi zonse zofunikira pophunzitsa.

• Ngati pali mapepala ena akuti ophunzira awerenge kapena kuwona,

mukonzeretu zoonjezera.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

xiv

• Ngati mugwiritse ntchito fomu yowunikira m’mene maphunziro ayendera,

muyikonzeretu fomuyo anthu asadayambe kuphunzira kuti mukawapatse.

Mukhoza kukonza fomu yanuyanu kapena kugwiritsa ntchito imene iri pa

Zowonjezera 2 kumapeto kwa bukhuli.

• Mufike pa malo ochitirako maphunziro patatsala mphindi 15 kuti maphunziro

ayambe.

4. Kutsogolera maphunziro

Gawo lanu inuyo ndi kutsogolera phunziro kuti ophunzira adziwe okha nkhani ya HIV ndi

Edzi ndi kuti akhoza kupewa bwanji kapena kudzisamalira motani pa nkhani yokhudza

matenda a Edzi.

Kutsogoleratu sikuphunzitsa ayi. Mukhoza kuphunzitsako pang’ono ngati pali zina zimene

ophunzirawo sadziwa. Koma maphunzirowa akhoza kukhala aphindu ngati mungavomere

kuti ophunzirawo azitengapo gawo lalikulu pokambirana ndi kuchita mwa iwo okha

zochitika zimene ziri m’maphunzirowa. Azipeza mayankho pa iwo wokha, pokhudzana ndi

nkhani imeneyi ya HIV ndi Edzi. Inu ntchito yanu ndi kutambasula/kuwonjezera ngati ena

afotokoza kapena ayankha mwachidule kwambiri.

Luso la utsogoleri woterewu mukhoza kuliphunzira, sikuti ndi zinthu zovuta ayi. Pano pali

zinthu zina zakuti zikuthandizeni inu kukhala mtsogoleri wabwino.

a. Pa chiyambi pa maphunziro

• Landirani ndi kupereka moni kwa ophunzira anu. Awuzeni dzina lanu.

• Khalani a nsangala ndi omweturira.

• Ngati nkotheka, chitani kanthabwala kuti anthu akhale ndi chidwi.

Tikupatsirani zitsanzo za zimene inu mukhoza kunena kuti anthu akhale

ndi chidwi ndi phunziro limene inu mukuphunzitsa. Ndi bwino

kumayamba motere, “Dzina langa ndine… ndipo ndimakonda ku…”

Chitani izi ngati ophunzirawo ali ochuluka.

• Muwafunse ophunzira zimene akuyembekeza kuphunzirolo.

b. Fotokozani cholinga cha phunziro lanu

• Tsindikani kuti cholinga cha maphunziro a Ulendo wa Chiyembekezo

ndikuti anthu akhale a ukhondo, akhale ndi moyo wautali, ndi kuti

akwaniritse zolinga zawo ndi maloto awo pa moyo wawo. Kambiranani

zokhudza HIV ndi Edzi.

• Ngati mukuchita phunziro lotsatira, yambani mwakumbutsana kaye

zimene mudaphunzira nthawi yopitayo kuti muwakumbutse amene akhoza

kuyiwala.

• Onetsetsani kuti anthu akumvetsetsa chilankhulo chimene inu

mukugwiritsa ntchito.

• Mugwirizane ndondomeko ya m’mene maphunziro anu aziyendera,

monga:

� Nthawi yoyambira ndi kutsirizira maphunziro anu.

� Kulemekeza maganizo a mzako.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

xv

� Asamangoyankhula anthu amodzimodzi.

� Kupereka mpata kwa munthu aliyense kuti alankhulepo.

Alimbikitseni anthu amanyazi kuti atengepo gawo.

� Muzisunga zinsinsi za anthu amene akufuna kuti muwasungire

zinsinsi zawo.

c. Panthawi imene mukuphunzitsa

• Mvetserani anthu akamalankhula.

• Onetsetsani kuti anthu akutsatira mutu umene mukukambirana.

• Munthu asamangolankhula yekhayekha nthawi zonse.

• Limbikitsani anthu ofatsa kutengapo nawo mbali.

• Fotokozeraninso bwinobwino zokambiranazo mozifupikitsa.

• Gawanani ntchito yophunzitsa ndi anzanu.

• Gwiritsani ntchito chiyankhulo chomveka kwa gulu.

• Mvetserani bwinobwino zimene ophunzira akunena ndipo alimbikitseni

kuti nawo azimvetsera zimene anzawo akuyankhula.

• Alimbikitseni ophunzira anu kuti akambe maganizo awo, m’mene

akumvera kapena zomwe akukumana nazo m’moyo mwawo m’malo

momangowawuza chochita.

• Onetsani chidwi ndi ulemu pa maganizo a anthu ena ngakhale inuyo

mutakhala kuti simukugwirizana nawo maganizowo.

• Onetsetsani nkhope za anthu amene mukuwaphunzitsawo ndi zochita

zawo kuti zikufotokoza chiyani osangodalira zomwe akuyankhula.

• Pezani chochita china anthu akatopa kuti muchotse kutopako.

• Yankhani mafunso mowona mtima, ngati yankho la funso lakusowani,

awuzeni ophunzirawo kuti panthawiyo mulibe yankho ndipo mufufuza

kapena awunikireni kumene angathe kukapeza yankho.

Funsani mafunso akuti munthu

afotokozere, monga awa:

1. Tingawathandize bwanji amene ali

ndi HIV kapena amene akudwala

Edzi?

2. Kodi ndi ziti zimene

zingakuthandizeni inu kugwira

ntchito ngati gulu limodzi?

d. Pa mapeto pa phunziro

Osafunsa mafunso amene

angayankhidwe mwachidule, monga

EYA kapena AYI, monga awa:

1. Kodi ndi bwino kuthandiza anthu

amene ali ndi HIV kapena Edzi?

2. Nkotheka kugwira ntchito ngati

gulu limodzi?

• Tsenderani pomangirira zonse zimene mwakambirana mwachidule.

• Fotokozani zimene mudzachite mukadzakumananso.

• Awuzeni ophunzira m’mene angakupezereni ndi kuti angadziwe bwanji

zambiri zokhudza HIV ndi Edzi.

• Ophunzira akuwuzeni m’mene awonera zokambiranazo ndi m’mene

mwatsogolerera (onani nfundo ili m’munsimu).

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

xvi

5. Kuwunika maphunziro.

Kuwunika m’mene maphunziro anu ayendera ndi chinthu chofunikira kwambiri, choncho…

• Sinkhasinkhani njira yophunzitsira imene ikuyenda bwino yoti mukhoza kuyigwiritsa

ntchito thawi zina.

• Fufuzani zimene sizikuyenda bwino ndikupeza njira yomwe mungakonzere mukhoza

kuzikonza bwanji.

• Unikani zosowa za maphunziro zimene zikadalipobe pakati pa ophunzira anu.

• Unikani zomwe zingathandize kupitiriza maphunziro kapena kusintha njira

zophunzitsira.

Kuwunikanso phunziro kukhoza kuchitika pa mapeto pa maphunziro. Nthawi zina

kuwunikaku kukhoza kuchitika patapita nthawi ophunzira atakhala ndi mwayi ogwiritsa

ntchito zomwe adaphunzira.

Kapena

a. Mapeto a phunziro

Aphunzitsi aloleni ophunzira kuti akuwuzeni mwatchutchutchu maganizo awo pa

m’mene awawonera maphunziro. Mphunzitsi wabwino amafunika kumvera zimene

ophunzira ake akunena pokhudza m’mene maphunziro ayendera. Pa nthawi imene

inu mukuphunzitsa onani m’mene maphunziro akuyendera. Pomaliza pa

maphunzirowo funsani maganizo a ophunzira anu kuti awawona bwanji

maphunzirowo. Ophunzira akhoza kulemba maganizo awo kapena kukuwuzani

pakamwa. Funsani ophunzira mafunso monga awa:

• Chinthu chaphindu chimene inu mwaphunzira pa inu nokha ndi chiyani?

• Nanga zimene mwaziphunzirazi mukazigwiritsa ntchito bwanji?

• Chimene chinakusangalatsani pa phunziroli ndi chiyani?

• Chimene sichinakusangalatseni ndi chiyani? Nchifukwa chiyani

sichinakusangalatseni?

• Takambanipo za m’mene mwayiwonera ndondomeko ya maphunzirowa.

Chabwino chimene chinalipo ndi chiyani? Nanga chimene tikhoza

kusintha ndi chiyani?

• Kodi mukadali ndi mafunso ena okhudza nkhani ya HIV ndi matenda a

Edzi?

• Afunseni amene amatha kulemba kuti alembe maganizo awo pa mapepala ndipo

akupatseni akamaliza. Mukhoza kugwiritsa ntchito fomu imene ili Mzowonjezera 2:

“Kuwunika ntchito yogwiritsa phukusi la Chiyembekezo” pa tsamba 69 kapena imene

ili mu phukusi la Ulendo wa Chiyembekezo.

• Mukhoza kuwasiyira ma fomuwo kuti azilemba pang’onopang’ono kwa masabata

angapo.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

xvii

. Maphunzirowo akangotha

Ena akuthandizeni kuwunikanso phunzirolo. Muwonetsetse zimene ophunzira aja

akuwuzani. Mukambirane za njira zimene zinayenda bwino ndi zimene sizinayende

bwino ndikuchita kafukufuku kuti mungatani mukamadzachitanso maphunzirowo.

Chitani kalondolondo pa zinthu monga:

• Fufuzani zina ndi zina zimene zinakuvutani kuwafotokozera ophunzira

pokambirana.

• Ngati padakali zinthu zina zimene ophunzira ena akufuna kuti adziwe

pawokha apatseni mpata oti mukambirane nao.

c. Patapita nthawi maphunziro atatha

Kuti mudziwedi ngati anthu akupindula ndi maphunzirowo, ndi bwino kuti

mumverebe maganizo kuchokera kwa iwo za m’mene akuwonera maphunzirowo

ndikuti maphunzirowo akuwapindulira bwanji pa moyo wawo. Ngati nkotheka,

maphunzirowa akatha, mudzakumanenso ndi ophunzirawa, kapena atsogoleri awo

kuti adzakufotokozereni m’mene maphunzirowa akuwathandizira pa moyo wawo

patatha masabata angapo. Kodi maphunzirowa akuwagwiritsa ntchito bwanji

m’moyo mwawo. Kambiranani mozama ndi ophunzirawo.

6. Kalondolondo-kuonetsetsa kuti maphunziro akutsatidwa

Pa ndime iri yonse imene muliri nthawi ya maphunziro onetsetsani kuti mukutsatira

komanso kuwunika m’mene maphunziro akuyendera, m’mene inu munafunira

kuchokera pa chiyambi.

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

xviii

NTHABWALA NDI MASEWERA OCHOTSA TULO

Pali masewera osiyanasiyana omwe mphuzitsi ngakhalenso ophunzira angachite kuti achotse

tulo pa nthawi imeme akuphunzira. M’munsimu muli zitsanzo za masewerawa.

1. Sunthani ngati…

Anthu wonse akhala pansi ndipo akhala mozungulira, munthu m’modzi yemwe akusowa

pokhala, (oyitana) ali pakati pagulu lija.

Woyitana uja aziti: “Suthani ngati uli... nkumatchula chimene akufuna.

Chitsanzo: Sunthani ngati mwavala chofiira. Aliyense amene apezeke m’gulu

lotchulidwalo akuyenera kusuntha pokhala. Munthu amene azikhala yekhayekha ali choyima

ndi amene tsopano azitenga ntchito ya oyitana, chifukwa oyitana oyamba uja azikhala

atapeza mpando okhala.

2. Bwato lomira.

Mufunse ophunzira kuti angoganiza kuti pali bwato limene likumira mwamsangamsanga.

Tsono kuti anthu akwere bwato lina limene labwera kuti liwapulumutse akuyenera kukhala

m’magulu a anthu owerengeka.

Awuzeni ophunzira kuti angokhala pachigulu chimodzi, kenako mukuwe kuti, “bwato

likumira, khalani atatu atatu.” Anthu akhala m’magulu a anthu atatu atatu koma pakhoza

kupezeka munthu m’modzi kapena awiri amene alibe gulu, amenewo ndiye kuti amira

limodzi ndi bwato ndipo awuzeni kuti akhale pansi.

Mubwereze chochitachi potchula manambala osiyanasiyana, monga “bwato likumira, seveni,

kaya faifi, choncho.”

Ulendo wa Chiyembekezo: Bukhu lophunzitsira kudziteteza ku Edzi m’Malawi.

xix

Hooray! Your file is uploaded and ready to be published.

Saved successfully!

Ooh no, something went wrong!