28.07.2013 Views

FROM CHINAMWALI TO CHILANGIZO:

FROM CHINAMWALI TO CHILANGIZO:

FROM CHINAMWALI TO CHILANGIZO:

SHOW MORE
SHOW LESS

You also want an ePaper? Increase the reach of your titles

YUMPU automatically turns print PDFs into web optimized ePapers that Google loves.

MWACHIDULE

Chimangiriro ichi chikufufuza mwadongosolo chilangizo m'mipingo ya Konveshoni ya

Babatist m'Malawi (BACOMA), ndikuona kufunikira kwache pakati pa mtundu wa

Achewa. Mu mbiri ya chiKhristu, zaonetsa kuti poyambirira mipingo imakana ndi

kutsutsana ndi miyambo ya makolo. Koma pang'ono ndi pang'ono, mipingo inayamba

kubvomereza ndi kulandira za miyamboyo pokhazikitsa mwambo wa chiKhristu

m'malo mwake. M'mipingo yathu ya Babatist, nkhani ya chilangizo ndi chinamwali

yakhala bvuto leni leni kutchito ya ubusa ndi yofalitsa Uthenga wa Yesu. Izi zakhala

tero chifukwa chakulephera kwa BACOMA kumvetsetsa ndi kutanthauzira chinamwali

kuchokera m'Mau a Mulungu muchinenero cha anthu.

Ndicholinga cha chimangiriro ichi kuthandiza BACOMA, komanso mipingo yonse mu

Afrika, kuti ikhale yomasuka kuphunzira za chikhalidwe ndi miyambo ya anthu.

Cholinga ndi kuti mipingo imvetsetse mozama ndikukhoza kutanthauzira mwambo uli

wonse pakugwiritsa ntchito Mau a Mulungu.a muchinenero chawo. Chimangirirochi ndi

chiyambi chakulimbikitsa BACOMA pandondomeko yakukambirana, kulingirira, ndi

kuphunzitsa anthu ake zokhuzana ndi chikhalidwe ndi miyambo ya makolo poyang'ana

matanthauzo ache m'Bukhu Lopatulika.

Chitatha chigawo chamayambo mu chimangirirochi, chigawo chachiwiri chayang'ana

mbiri, chikhalidwe, ndi zikhulupiriro za mtundu wa Achewa. Chigawo chachitatu

chaonetsa kukhazikitsidwa kwa mipingo wa Babatist kuchokera kumbali ziwiri.

Poyamba kuchokera ku moyo wachipembezo ndi chikhalidwe cha azungu aBabatist

akuAmerika, amene anabweretsa Uthenga Wabwino ku Afirika. Mbali yachiwiri

yayang'ana zinthu zingapo zimene zinapangisa aMalawi kulandira ndi kufalitsanso

Uthengawo kwa aMalawi anzawo. Popeza chilangizo ndi gawo la chikhalidwe chathu,

chigawo chachinayi chalongosola mwatsatane-tsatane mwambo wa chinamwali cha

Achewa cha ndakula. Chigawo chachisanu chapereka mbiri ya chilangizo makamaka

mu BACOMA. Chigawo chachisanu ndi chimodzi chalongosola ndi kufufuza m'mene

chilangizo chikuyendera m'mipingo ya Babatist. Kafukufuku waonetsa kuti chilangizo

sichikukwaniritsa zosowa zeni-zeni za anthu pakulingirira zolinga zimene chinamwali

chimakwaniritsa kwa Achewa. Chomwecho chigawo chotsiriza chapereka malingiriro

ndindomeko yofunika kuti BACOMA iyambe kukambirana, kulingirira, ndi kuphu­

nzitsa akhristu za m'mene Mau a Mulungu amatanthauzira miyambo yamakolo athu.

Chitsanzo cha chinamwali cha Chikhristu chaperekedwa potsirizira pa chimangirirochi.

IV

Hooray! Your file is uploaded and ready to be published.

Saved successfully!

Ooh no, something went wrong!