FROM CHINAMWALI TO CHILANGIZO:
FROM CHINAMWALI TO CHILANGIZO:
FROM CHINAMWALI TO CHILANGIZO:
Create successful ePaper yourself
Turn your PDF publications into a flip-book with our unique Google optimized e-Paper software.
Anamkungwi amuonetse mtsikana kabvalidwe ka mwele bwino-bwino. Amupatse nayenso

achite monga waonera mpakana akhonze ndipo anthu alulutire. Amuonetsenso kachapidwe

ndi kasungidwe kache pamene nyimbo ikuimbidwabe. Potsiriza abwereze kumulongosolela

kuti:

While still singing, the instructresses should demonstrate and teach her well how to wear the menses linen and

how to clean and take care ofthem. They should then explain the following to her:

Tsopanotu iye ayenera kudzisamalira thupi lake koposa kale. Akhale waukhondo nthawi

zonse ndi thupi ndi zobvala zake. Mtsikana adzisamalire kwenikweni thupi lake ndi nsaru

zake panthawi imene ali mumsambo kuti asapezeke akutulutsa fungo loipa. Komanso

asakhetsere paliponse mwazi wamsambo, popeza zimachititsa manyazi kuti ena aone mwazi

umenewu. Kuyimba kupitirire.

Now she must take care ofher body more than before. She needs to keep her body and her clothes clean at all

times, particularly when she is menstruating so that no bad smell comes out. She needs to make sure that no

blood stains remain anywhere for is it a shameful thing for people to see the stains. The singing continues.

12. Kumana, kumana mtsikana x 2

Mmati undipatse

Wabvundikira

13. Mulungu adawauza Adamu nda aHava

Muberekane, muchurukane

Refuse, refuse the girl

I wanted you to give me

You have covered

God told Adam and Eve

Be fruitful, and increase in number

Longosolani kuti njira imene amatipatsira ana Mulungu ndi yakugonana mwamuna ndi

mkazi amene ali pabanja. Kugonana kwa mwamuna ndi mkazi amene sali pabanja ndi

chimo la chigololo pamaso pa Mulungu ('Usachite chigololo' Eksodo 20:14; 1 Akorinto

6:13, 19).

Explain that God gives us children through sexual activity in a marriage. Therefore sex outside marriage is

adultery to God ('Do not commit adultery' Exodus 20:14; 1 Corinthians 6:13,19).

14. Kodi lamulo la Mulungu likuti chiani?

Likuti Usachite chigololo

Thupiri si/ili la chigololo

15. Kodi abale simudziwa eel

Simudziwaaa eel

Kodi abale simudziwa eel

Simudziwaa eel

Thupi lanu liri kachisi, liri kachisi

Wa Mzimu Woyeraaa!

What does God's law say?

It says do not commit adultery

The body is not for adultery

Friends, do you not know eh!

Do you not know eh!

Friends, do you not know eh!

Do you not know eh!

Your body is a temple, is a temple

Ofthe Holy Spiritiii!

Onse azibvina akugwira thupi lao ndikusonyeza kumwamba kokhala Mzimu Woyera.

They should be dancing while touching their bodies and pointing towards heaven where the Holy Spirit is.

16. Mwendo, mwendo nkuyendera

Maso, maso nkupenyera

Chimodzimodzi, ziwalo zachinsinsi

Ntchito yake m 'banja

Leg, leg is for walking

Eyes, eyes are for looking

Similarly, private parts

Their job is in marriage

209